‘Kufunafuna Mawu Okondweretsa, Mawu Owongoka’
‘MLALIKIYO anasanthula akapeze mawu okondweretsa, ndi zolemba zowongoka ngakhale mawu owona.’ (Mlaliki 12:10) Ayenera kukhala amtengo wapatali chotani nanga ‘mawu okondweretsa, owongoka’ ozikidwa pa Malemba ouziridwa! Iwo amayerekezeredwa ndi “zipatso za golidi m’nsengwa za siliva,” aluso ndi olemekezeka pa nthaŵi iriyonse ndi amtengo wapatali m’mikhalidwe yopsinja iriyonse.—Miyambo 25:11.
M’tsiku lathu Mlaliki Wamkulu, Yesu Kristu, wapereka chuma chauzimu choposeratu chija chosangalalidwa ndi anthu a Mulungu okhala pansi pa mafumu akale Achiisrayeli. (Mateyu 12:42) Kwa zana zoposa zana limodzi, mawu okondweretsa, owongoka a chowonadi ochita ndi mbali iriyonse ya moyo aperekedwa m’zofalitsidwa za Watch Tower Society ndikugaŵiridwa mofala m’zinenero zambiri. Motero mabanja ambiri ndi munthu payekha akhoza kusonkhanitsa m’nyumba zawozawo laibulale ya mabuku azilozero odalirika amene amasumika pa Baibulo. Kuwonjezerapo, mipingo yambiri ya Mboni za Yehova iri ndi malaibulale ogwiritsiridwa ntchito pa Nyumba Zaufumu zawo.
Komabe, kupeza mawu okondweretsa, owongoka ofunikira kaamba ka mkhalidwe wakutiwakuti kumafunabe kufufuza. Pozindikira chimenechi, kuyambira kale m’mbiri yake, Watch Tower Society yafalitsa zosonyezera zoloza ku zofalitsidwa zake.—Onani bokosi pamasamba 28 ndi 29.
Lamulo Latsopano
Chaka cha 1985 chinayambitsa mutu watsopano m’mbiri ya ma Watch Tower Publications Index. Ma Index asanu ndi anayi oyambirira anaphatikizidwa pamodzi ndikugwirizanitsidwa m’volyumu imodzi yokuta 1930 mpaka 1985, projekiti imene inatenga zaka 14 za kuyesayesa kwamphamvu kwa amuna. Motero, mapindu a Index ya volyumu imodzi yoteroyo yokuta zaka zambiri anatsogolera ku lamulo latsopano, lafalitsa ma Index ophatikiza. Chaka ndi chaka, kaŵirikaŵiri mkati mwa zaka zinayi zotsatizana, brosha ya Index yophatikiza idzakuta chaka chimodzi, ziŵiri, zitatu, ndiyeno zinayi. Zaka zisanu zirizonse Index yachikuto cholimba idzaphatikiza ma Index onse kuchokera 1986 kunka mtsogolo, monga ngati 1986-90, 1986-95, namanka choncho. Motero, sikufunikira kufufuza ma Index oposa atatu: 1930-1985 Index, Index yatsopano yachikuto cholimba, ndi brosha yatsopano.
Index Yokonzedwa Mokulingalirani
Gawo loyamba mu Index iriyonse ndilo chosonyezera nkhani. Pokonza chosonyezera nkhani, mafunso aŵiri amakumbukiridwa: (1) Kodi nchidziŵitso chotani chimene chiyenera kuiikidwa pa chosonyezera? (2) Kodi munthu angachifunefune kuti chidziŵitsocho?
Monga woŵerenga, simungakhale mukufuna kupeza ndemanga yaing’ono iriyonse yokhala m’nkhani. Popeza kuti mwachisawawa mumakhala mukufuna chidziŵitso chofunika kwambiri kapena chimene chiri chothandizadi, ichi ndicho chimasankhidwa kuikidwa pa chosonyezera. Koma mawu oterowo satofunikira kukhala ochuluka. Mawu olembedwa pa Index angasonye ku mawu ochepa monga mzera umodzi, monga ngati ndemanga ya Sosaite pa lamulo la nkhani yakutiyakuti. Kapena ikhoza kukuta nkhani yonse, ngakhale bukhu lonse. Komabe, kaŵirikaŵiri, mawu olembedwawo amatsogolera ku ndime zingapo za kukambitsirana.
Funso lakumene zilozero ziyenera kupezeka mu Index nlofunika mofananamo, popeza kuti oŵerenga amaganiza mosiyana ndipo adzayang’ana pansi pa mitu yosiyana. Mwachitsanzo, chidziŵitso chonena za Nsanja ya Babele chimapezeka pansi pa TOWER OF BABEL. Koma oŵerenga ena angayang’ane pansi pa BABYLON, ARCHAEOLOGY, kapena LANGUAGE(S), kudalira pa mfundo ya nkhaniyo imene akuifuna. Motero, kuyesayesa kumapangidwa kubwerezanso zilozerozo pansi pa mitu yosiyanasiyana yoyenerera, tikumakumbukira kuti oŵerenga ngamisinkhu ndi makulidwe osiyanasiyana, ndipo ali ndi zifuno zosiyanasiyana.
Mmene Index Ingakuthandizireni
Mofanana ndi mapu Index ingakutumikireni kokha ngati mumaigwiritsira ntchito. Kodi mumayembekezera kupeza chiyani kaya m’chosonyezera nkhani kapena m’chigawo chosonyezera Malemba chimene chimatsatira?
Zilozero m’chigawo chosonyezera Malemba ndizo mawu olongosola vesi limodzi ndi limodzi. Mungapeze malongosoledwe a mkhalidwe umene mawu a lembalo analankhulidwiramo, chifukwa chake analembedwa, anthu kwa amene anagwira ntchito, kapena tanthauzo la liwu lirilonse kapena mawu. Chitsanzo chingakhale pempho la m’pemphero lachitsanzo la Yesu lakuti: “Musatitengere kokatiyesa.” (Mateyu 6:13) Kodi nchifukwa ninji linanenedwa mwanjirayo? Chosonyezera Malemba chidzakuthandizani kudziŵa.
Chosonyezera nkhani, monga mwadzina lake, n’chosonyezera kwakukulukulu nkhani mmalo mwa liwu kapena mawu. Pofuna kupeza nkhani moifuna ndimutu wake, oŵerenga ena akhala ndi vuto lakuipeza. Vutoli lingakhalepo ngati palibe liwu m’mutuwo lodziŵikitsa kwenikweni nkhaniyo. Chitsanzo chingakhale nkhani yakuti “How Much Is Too Much?,” imene inafotokoza ziyambukiro za zakumwa zolezeretsa. Pokumbukira zamkati mwa nkhaniyo, mungapite ku ALCOHOLIC BEVERAGES kapena DRINKING mu Index, ndipo mudzapeza kuti yalozeredwako pamenepo.
Index ingakhale yothandiza mwapadera m’kupeza chidziŵitso pa mavuto amene mungayang’anizane nawo. Mwachitsanzo, ngati ndinu kholo, kodi nthaŵi zina mumamva kugwiritsidwa mwala m’zoyesayesa zanu zakulanga ndi kutsogoza ana anu? Pansi pa CHILDREN mudzapeza zilozero zambiri zopereka chidziŵitso cha kuganiza, malingaliro, ndi zosoŵa zawo. Komabe, pansi pa mutu wakuti CHILD TRAINING, mudzapeza zilozero za kuphunzitsa ndi kulanga m’mbali zonse za moyo wawo.
Watch Tower Society panthaŵi zina imalandira mapempho olembedwa ofuna thandizo pakuthetsa mavuto a muukwati kapena mafunso onena za maunansi a muukwati akutiakuti. Pamene kuli kwakuti Sosaite ingakhoze kuyankha, uphungu wamphamvu wothandiza umodzimodziwo, ungapezedwe mwakupita ku mutu wakuti MARRIAGE, ndi mitu yake yaing’ono yakuti “problems” ndi “sex” kapena “sexual relations,” ndikuyang’ana zilozero zondandalitsidwa.
Makalata amalandiridwanso kuchokera kwa ovutika ndikuchita tondovi kapena kupsinjika maganizo. Chitonthozo ndi thandizo zoperekedwa mwa makalata zingapezedwe mofulumira kwambiri m’laibulale yanuyanu kapena yokhala pa Nyumba Yaufumu yakwanuko mwakufufuza mitu yakuti DEPRESSION ndi MENTAL ILLNESS mu Index. Nkhani zofotokoza mmene wina angalakire mavuto a maganizo, kuchiritsa komwe kulipo, ndi zokumana nazo zothandiza za amene anachitapo tondovi zasonyedwako.
Kodi ndinu wachichepere? Mungakhale ndi nkhaŵa za ukwati, moyo wa banja, sukulu, unansi wanu ndi makolo anu, ndi zina zotero. Mutu waukulu wakuti YOUTHS uli ndi zilozero zopezeka pansi pa mitu yaing’ono yonseyi ndi ina yowonjezereka. Kuwonjezerapo, mitu yonga ngati RELATIONSHIPS, SCHOOLS, CAREER, ndi COURTSHIP imapatsa zambiri. Kaamba ka kupanga lipoti la kusukulu, Index ingakutsogolereni ku nkhani zabwino pa chilengedwe, sayansi, mankhwala, zachuma, ndi nkhani zina zambirimbiri.
Imapindulitsa Amisinkhu Yonse
Mkazi wina wazaka 81 zakubadwa analemba kuti: “Mabuku ndi magazini ali mgodi wa golidi wa chidziŵitso ndi nyonga yauzimu—ndipo Index imatulutsira golidiyo kunja.” Nakubala yemwe ana ake ngamisinkhu ya zaka zisanu ndi zitatu ndi wina zisanu ndi zinayi zakubadwa anati: “Tsopano ndimazizwa mmene ndikanachitira popanda iyo. Yanditsogolera ku mayankho a mafunso ambiri amene anandizizwitsa kwa nthaŵi yaitali ndipo ndapanga kufufuza pokonzekera misonkhano ya mpingo mopepuka kwambiri. . . . Ndikufuna kukuuzaninso mmene chofalitsidwachi chathandizira phunziro lathu Labaibulo labanja. . . . Pamene mwamuna wanga apatsa asungwanawo chosankha cha zimene angafune kuchita, iwo kaŵirikaŵiri amafuna kupanga kufufuza mwakugwiritsira ntchito Index imeneyi. Amakondweretsedwa kusankha nkhani imene amaikonda, monga ngati nyama zowasangalatsa kapena maiko osiyanasiyana, ndipo amakhoza kupeza chidziŵitsocho mongothandizidwa pang’ono basi. Izi zawaphunzitsanso kuti phunziro Labaibulo nlosangulutsa.”
Kufunafuna mawu okondweretsa ndi mawu owongoka a chowonadi kuli ndi mapindu amtengo wapatali. Zoyesayesa za Mlalikiyo zinapereka mapindu opitirira kotheratu pa chifuno chake choyambirira, popeza kuti mawu oterowo atumikira kulimbikitsa ndi kutsogoza atumiki a Yehova kufikira lerolino. Zoyesayesa zathu zofananazo zimadzetsanso dalitso la Yehova, ndi zotulukapo zokhala kwamuyaya.—Miyambo 3:13-18, 21-26.
[Bokosi/Chithunzi pamasamba 28, 29]
Zosonyezera Zoyambirira
Mu 1902 bukhu lapadera la Holman Parallel Edition Bible linatulutsidwa kaamba ka Watch Tower Society, ndipo linali ndi zothandiza zochuluka zokonzedwa ndi Sosaite. Mbali yake ya zowonjezeredwa inali ndi zonse ziŵiri chosonyezera nkhani ndi chosonyezera Malemba zochita ndi mpambo wa mabuku a Millennial Dawn (pambuyo pake odzatchedwa Studies in the Scriptures), timabuku tatikulu tiŵiri, ndi Zion’s Watch Tower ya 1879-1901.
Mabaibulo a Berean a 1907 ndi pambuyo pake anapereka zosonyezera zofananazo. Awawa analoŵedwa m’malo mu 1922 ndi zosonyezera zazikulu zokhudza zofalitsidwa zonse za Sosaite. Zosonyezera zimenezi zinapezeka m’mavolyumu otsirizira asanu ndi aŵiri a zosindikizidwanso za Watch Tower (1879-1919). Kufikira lerolino zotsirizirazi ndizo maziko aakulu opezera nkhani zoperekedwa m’zofalitsidwa zoyambirira za Watch Tower Society.
Komabe, kwa zaka 40 zotsatira, panafunikira kupanga kufufuza m’zofalitsidwa zotulutsidwa pambuyo pa 1919 mwakugwiritsira ntchito zosonyezera zosiyanasiyana zopezedwa kumbuyo kwa mabuku ndi m’kope lotsirizira la magazini la chaka ndi chaka. Koma mu 1959 Sosaite inayamba projekiti yaikulu yoika chosonyezera nkhani ndi cha Malemba m’volyumu imodzi zochita ndi zofalitsidwa Zachingelezi. Gulu linasonkhanitsidwa limene linaphatikizapo ziŵalo za ogwira ntchito pa malikulu, ndi omaliza Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, ndipo ngakhale oyang’anira oyendayenda ochokera ku New York City. Pambuyo pa kuyesayesa kwamphamvu kwa chaka chimodzi ndi theka kwa ogwira ntchito odzipereka 18, Watch Tower Publications Index yoyamba, yokhala ndi magawo a nkhani zokambitsiridwa ndi malemba olongosoledwa, yokuta zaka 31 kuchokera 1930 mpaka 1960, inatulutsidwa. Iyo inatulutsidwa choyamba kwa omvetsera osangalatsidwa pa Misonkhano ya Olambira Ogwirizana mu 1961.
Kuyambira pamenepo, Watch Tower Publications Index yafalitsidwa m’chingelezi chaka chirichonse, ndi Index yophatikiza yachikuto cholimba pambuyo pa zaka zisanu zirizonse.