Khulupirirani ya Yehova!
“Khulupirirani Yehova anthu inu, nthaŵi zamuyaya, pakuti mwa Ya Yehova muli Thanthwe lachikhalire.”—YESAYA 26:4, NW.
1, 2. Ndi nyimbo yokwezeka ya chitamando iti imene yayambidwa pa Yesaya 26:1-6, ndipo nchifukwa ninji?
KUGWETSEDWA kwa ‘mudzi wa mitundu ya akuwopsya’ kumaitanira nyimbo ya chipambano! (Yesaya 25:3) Chotero, moyenerera, ulosi wa pa Yesaya mutu 26, versi 1 mpaka 6, umayambitsa nyimbo yokwezeka ya chitamando kwa Mfumu Ambuye Yehova. Iyo kufikira tsopano ikuimbidwa “m’dziko la Yuda,” Yuda kutanthauza “Wotamandidwa.” Pano, kachiŵirinso, King James Version imagwiritsira ntchito mawu akuti “AMBUYE YEHOVA” kumene dzina laumulungu latchulidwa kaŵiri. Koma ali osangalatsa chotani nanga mawu a nyimbo imeneyo monga momwe amawonekera mu New World Translation, kumene kupezekaku ndi kwina konse kwa dzina laumulungu kwaikidwa molondola!
2 Mvetserani tsopano ku nyimbo yosangalatsa imeneyo: “Ife tiri ndi mudzi wolimba. Iye [Yehova] adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga. Tsegulani pazipata, kuti mtundu wolungama, umene uchita zowonadi ulowemo. Inu mudzasunga mtima wokhazikika mu mtendere weniweni, chifukwa ukukhulupirirani inu. Khulupirirani Yehova anthu inu, nthaŵi zamuyaya, pakuti mwa Ya Yehova muli Thanthwe lachikhalire. Chifukwa iye watsitsira pansi iwo amene anakhala pamwamba, mudzi wa pamsanje. Iye wautsitsa, wautsitsira pansi, waugwetsa pansi pa fumbi. Phazi lidzaupondereza pansi, ngakhale mapazi a aumphaŵi, ndi mapondedwe a osowa.” Ndi chimwemwe chotani nanga kukhala pakati pa okhulupirira amene tsopano akugawanamo m’kuimba nyimbo imeneyi—Mboni za Yehova!
3. (a) Nchiyani chimene chiri “mtundu wolungama,” ndipo ndani amene akulowa kupyola “zipata” zake zotseguka? (b) Ndimotani kuti gulu la Yehova limapita patsogolo mogwirizana mosasamala kanthu za zoyesayesa za adani kuliphwanya ilo?
3 Ambuye Yehova—Ya Yehova—ndithudi adzatsitsa onyada ndi kupulumutsa awo amene amakhulupirira mwa iye nthaŵi zonse. Ngakhale kuti iwo poyamba anali “ochepa,” Israyeli wauzimu anadzakhala “mtundu wamphamvu.” “mtundu wolungama.” Kuchokera mu “zipata” zotseguka m’gulu longa mzinda la Yehova, palowanso makamu ambiri a oyanjana nawo ochita chifuno chabwino omafika ku chiŵerengero choposa mamiliyoni atatu. Onse pamodzi amapanga ubale wa dziko lonse, umene chiŵerengero chake chimaposa pa chifupifupi mitundu 57 yopanga chotchedwa Mitundu Yogwirizana. Koma “mtundu” wa Mulungu ndi awo amene akuyanjana nawo ali ogwirizana mowonadi. Kuzungulira padziko lonse, chikhoterero chawo chiri kumvera maprinsipulo ake olungama. “Makoma” a gulu la “mtundu” wa Mulungu amapereka linga lochinjirizira motsutsana ndi zoyesayesa za Satana za kuseŵera ndi khalidwe lawo lokhulupirika m’kuchirikiza chowonadi. Mdaniyo sangaphwanye kuyenda kopita patsogolo komvera kwa anthu a Mulungu! Chikhulupiriro chathu nthaŵi zonse chimadalira pa ‘Ya Yehova, thanthwe la nthaŵi ya muyaya.’—Yesaya 54:17; 60:22.
4, 5. (a) Nchiyani chimene chiri “mzinda wokwezeka,” ndipo ndimotani mmene anthu a Yehova apondera iwo m’njira yophiphiritsira? (b) Ndi liti pamene ulosi wa Yesaya 26:10 umakhala ndi kukwaniritsidwa kokulira, ndipo ndimotani? (c) Ndi kugwira ntchito kwina kotani kumene ulosi umenewu uli nako?
4 Pamene tikufuula chenjezo lakuti Yehova ali pafupi kugwetsa “mzinda wokwezeka,” “Babulo Wamkulu” chiri chosangalatsa kuwona aumphaŵi ndi osowa a dziko lapansi akukupatira mbiri yabwino ya Ufumu. (Chivumbulutso 18:2, 4, 5) M’njira yophiphiritsira iwo, nawonso, amapondereza “mzinda wokwezeka” umenewo, osati mwa kugawanamo m’ntchito yosakaza, koma mwakutengamo mbali m’kulalikira tsiku la kubwezera la Yehova pa dongosolo loipa limenelo. (Yesaya 61:1, 2) Kwa zaka makumi angapo tsopano, Mboni za Yehova zakhala zikusonyeza kukoma mtima ngakhale kwa oipa mwakuitanira pa makomo awo ndi uthenga wopulumutsa moyo wa Ufumu. Koma zotulukapo zakhala monga momwe zasonyezedwera pa Yesaya 26:10: “Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo, m’dziko la machitidwe owongoka, iye adzangochimwa, sadzawona chifumu cha Yehova.”
5 Ulosi wa kubwezeranso umenewo uli ndi kukwaniritsidwa kwake kokulira lerolino. Ngakhale kuti amayanjidwa ndi mwaŵi, anthu ochepa amafuna kusintha miyoyo yawo ndi cholinga cha kulandira chiyanjo cha Yehova “m’dziko la machitidwe owongoka.” Awo amene amatonza Yehova ndi mboni zake zokhulupirika “sadzawona chifumu cha Yehova,” popeza iwo sadzapulumuka kudzasangalala ndi madalitso ozizwitsa omwe adzabwera kwa mtundu wa anthu pambuyo pakuti dzina la Yehova layeretsedwa. (Yesaya 11:9) Ulosiwo ungagwirenso ntchito, kachiŵirinso, m’dziko lapansi la Paradaiso pakati pa awo amene adzaukitsidwa kuchokera ku manda. Aliyense amene adzakana kugwirizana ndi zifuno za Yehova, monga mmene zamveketsedwera mu “mabukhu” aumulungu a nthaŵi imeneyo, sadzakhala ndi maina awo atalembedwa mu “bukhu la moyo.”—Chivumbulutso 20:12, 15; yerekezani ndi Ezekieli 33:11.
Yehova Akhazikitsa Mtendere
6. Ndi mawu otani amene anthu omvera a Yehova mwachimwemwe amafuula, ndipo nchifukwa ninji tero?
6 Anthu okhulupirika a Mulungu, ngakhale kuli tero, ali okondweretsedwa kotheratu kuwona Ya Yehova akukwezedwa, kulemekezedwa. Iwo amaitanira pa iye “kukhazikitsa mtendere” kwa anthu ake, ndipo mwachimwemwe amafuula kuti: “Mwachulukitsa mtundu, Yehova, mwachulukitsa mtundu. Inu mwalemekezeka, mwakuza malire onse a dziko.” (Yesaya 26:12, 15) M’maiko 210 kuzungulira dziko lapansi, Yehova akupitiriza kuwonjezera anthu onga nkhosa ku mtundu wake wauzimu. Mazana a zikwi a oyanjana nawo achatsopano akubatizidwa. Loposa theka la miliyoni la apainiya apadera, okhazikika, ndi othandizira amatumikira m’miyezi ya ziŵerengero zapamwamba. Nyumba za Ufumu zowonjezereka ndi Maholo a Misonkhano zikumangidwa. Nthambi za Watch Tower zikufutukula Nyumba zawo za Beteli ndi mafakitale ndipo akuwonjezera ziwiya zosindikizira. Kukulako kuli kopitirizabe!
7. Nchiyani chimene chimaŵerengera kaamba ka kufutukuka kwa gulu longa mizinda la Yehova?
7 Kufutukuka kumeneku kumabwera chifukwa chakuti “Kalonga wa Mtendere” akutsogoza zinthu za anthu a Mulungu padziko lapansi. Monga mmene Yesaya ananenera poyambirira mu ulosi wake: “Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchirikiza ndi chiweruzo ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kunkabe nthaŵi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.” (Yesaya 9:6, 7) Ndi mokulira chotani nanga mmene mawu amenewo akwaniritsidwira lerolino! Awo amene amakhulupirira mwa Yehova akukumana kale ndi mtendere, chiweruzo, chilungamo, cha ulamuliro wa ukalonga umenewo. Kwawabweretsa iwo pamodzi mu umodzi wachikondi womwe ukusangalalidwa kokha ndi ophunzira owona a Yesu. (Yohane 13:34, 35) M’kuwonjezerapo, iwo amayang’ana kutsogolo ndi chidwi chosamalitsa ku nthaŵi yomayandikira mofulumiranso pamene ulamuliro wa Ufumu wa Yesu ndi “chidziŵitso cha Yehova” chidzadzaza dziko lonse lapansi.—Yesaya 11:9; Danieli 2:35, 44, 45.
8. Nchiyani chimene chikusonyezedwa ndi mawu a Yehova pa Yesaya 26:20, ndipo kodi “zipinda za mkati” zikugwirizanitsidwa ndi chiyani?
8 Pamene kufutukuka kwa Ufumu kufika pachimake, kuitana kwa Yehova pa Yesaya 26:20 kumalira mofuula: “Idzani, anthu anga, lowani m’zipinda mwanu, nimutseke pamakomo panu; nimubisale kanthaŵi kufikira mkwiyo utapita.” Mosakaikira “zipinda za mkati” za ulosi umenewu zikugwirizana mwathithithi ndi mipingo yonga mizinda yoposa 54,000 yomwe imatumikira Mboni za Yehova kuzungulira dziko lonse lapansi lerolino. Chimene Yehova ali nacho m’maganizo chikutsalira kudzawonedwa. Koma tingakhale otsimikizira kuti pamene iye awononga oipa, iye adzachinjiriza anthu ake okhulupirira, monga mmene iye anachitira m’tsiku la Yesaya mwakubweza Asuri ankhanza.—Yesaya 10:24-26.
Chipulumutso Chatsimikiziridwa!
9. (a) Ndimotani mmene Mfumu Hezekiya anasonyezera kukhulupirira kwake mwa Yehova? (b) Pamene tikuzunzidwa kapena kutonzedwa ndi adani a Yehova, nchiyani chimene chimakhala chivomerezo chathu choyenera?
9 Atumiki a Yehova lerolino amakhulupirira mwa iye kaamba ka chifukwa chimodzimodzi chimene Mfumu Hezekiya anachitira. Iye anadalira kotheratu pa Yehova monga Mbuye wake Wolamulira. Chotero, pamaso pa chiwopsyezo cha Asuri, iye anapemphera kwa Yehova m’mawu awa: “Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi, inu ndinu Mulungu, inu nokha, wa maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Tcherani makutu anu, Yehova, nimumve. Tsegulani maso anu, Yehova nimuwone; ndi kumva mawu onse a Sanakeribu, amene watumiza kumtonza Mulungu wamoyo.” (Yesaya 37:16, 17) Pamene muzunzidwa, kusekedwa, kapena kutonzedwa ndi adani a Yehova, kodi pemphero lofananalo silimabwera mu mtima mwanu? Ndi chidaliro chotheratu mwa Yehova, kodi simumam’pempha iye kuchotsa chitonzo pa dzina lake? Imeneyo ndi njira imene Yesu anamverera pamene anali pafupi kufa pa mtengo wozunzirapo. Iye anapempha ngakhale kuti chikhocho chimene anali pafupi kumwa “chimpitirire” chifukwa cha chitonzo chachikulu kwa Atate wake.—Mateyu 26:39-44.
10. (a) Nchiyani chimene pemphero la Hezekiya linavumbulutsa ponena za kudera nkhaŵa kwake kwakukulu? (b) Ndimotani mmene ife mofanana ndi Hezekiya tingayang’anizirane ndi ziyeso isanafike Armagedo?
10 Pemphero la Hezekiya linasonyeza kuti iye analibe chisonkhezero chadyera m’kufuna chipulumutso kuchokera kwa Asuri. Iye sanali kokha kuyesera kudzipulumutsa iyemwini. M’mwalomwake, iye anali wodera nkhaŵa kuti dzina la Yehova liyeretsedwe ndi kuti ulamuliro wake ulemekezedwe. Chotero, pemphero lake linatha ndi mawu akuti: “Chifukwa chake, Yehova, Mulungu wathu, mutipulumutse ife m’manja mwake, kuti maufumu onse a dziko adziŵe, kuti inu ndinu Yehova, inu nokha.” (Yesaya 37:20) Mofananamo, pamene tikuyang’anizana ndi ziyeso zomwe ziri kutsogolo kwa nkhondo yomalizira ya Armagedo, lolani tisunge m’maganizo kuti chipulumutso chathu chaumwini chiri chachiŵiri ku kuyeretsa dzina la Yehova. Monga mmene Mbuye wathu Wolamulira analengezera nthaŵi 60 mwa mneneri wake Ezekieli: “Adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.”—Ezekieli 38:23.
11. (a) Ndi cholakwa chotani chimene Sanakeribu anapanga, ndipo nchiyani chimene Yehova ananena m’chigwirizano ndi ichi? (b) M’chiyang’aniro cha chotulukapo kwa Sanakeribu, ndi chikhulupiriro chotani chimene tingakhale nacho?
11 Pambuyo pa kupemphera kwa Hezekiya, Yesaya anadziŵitsa mfumu ponena za mawu amene Yehova analankhula motsutsana ndi Sanakeribu. Ndi cholakwa chotani nanga chimene wotonza wa Asuri ameneyo anapanga m’kutonza Mulungu wamoyo! Kupyolera mwa Yesaya, Yehova anati ponena za Sanakeribu: “Ndani amene iwe wamtonza ndi kumlalatira? Ndani amene iwe wakwezera mawu ako ndi kutukulira maso ako kumwamba? Ndiye Woyera wa Israyeli.” Ndipo anali Woyera wa Israyeli amene anachitapo kanthu usiku umenewo! Chinatenga kokha mngelo mmodzi wa Yehova kukantha ndi kupangitsa “mitembo” ya ankhondo a Asuri 185,000, gulu lamphamvu la Sanakeribu. Mfumu yonyada imeneyo inabwerera m’manyazi ku Nineve ndipo zaka zingapo pambuyo pake inaphedwa ndi ana ake amuna pamene inali kupitirizabe m’kulambira kwake mafano. Tingakhulupirire Yehova, kudalira kuti Iye adzapereka chilango chofananacho kwa Satana ndi achirikizi ake onse amene monyoza amatonza ndi kuzunza Mboni za Yehova.—Yesaya 37:23, 36-38.
Kubwezera “Ophedwa”
12. (a) Ndimotani mmene Yesaya 26:21 akulongosolela kuŵerengedwa komwe kudzachitika pa Armagedo? (b) Ndani amene ali “ophedwa” omwe adzayenera kubwezeredwa ngakhale isanafike Armagedo, ndipo tero motani?
12 Chinali chochitika cha nkhondo yochititsa mantha kubwerera m’mbuyo mmenemo, koma chinthu chowopsya kwambiri chidzachitika mkati mwa “chisautso chachikulu.” (Mateyu 24:21) Yehova akutiitana ife kuwona ukulu wa kupha kumeneko: “Pakuti tawonani! Yehova adza kuchokera ku malo ake kudzazonda okhala pa dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwawo; dziko lidzavumbulutsa mwazi wake, ndipo silidzavundikiranso ophedwa ake.” (Yesaya 26:21) Choyamba, Yehova adzapangitsa mphamvu za ndale kupereka chiweruzo pa opititsa patsogolo kulakwa kwa chipembedzo. Milungu yawo yonyenga sidzawapulumutsa iwo m’tsiku limenelo! Lolani papa wa Roma apitirizebe kusonkhanitsa zipembedzo zonse za “Babulo Wamkulu” kaamba ka mapemphero a zikhulupiriro zambiri. Palibe ndi mmodzi yemwe wa atsogoleri osakaniza zipembedzo amenewa amene amalemekeza Mulungu wowona ndi wamoyo, Yehova. Ziphunzitso zawo ziri zonyenga, zosazikidwa pa Baibulo, ndipo chotero zirinso njira zawo. Iwo aphana wina ndi mnzake mkati mwa zaka mazana. Iwo akhetsa mwazi wa Akristu opanda chiwawa. M’zana lino la 20, ambiri a olakwa amenewa achirikiza olamulira ankhalwe omwe anapha Mboni za Yehova m’ndende ndi misasa ya chibalo mwa kuwomba mfuti ndi nkhwangwa. Monga mmene Yehova mwachimvekere akulengezera kupyolera mwa aneneri ake, “ophedwa” amenewo ayenera kubwezeredwa.—Deuteronomo 32:41, 43; Yesaya 1:24; 63:4; Chivumbulutso 17:15-18; 18:21, 24.
13. Nchiyani chimene Yesaya akuneneratu ponena za “tsiku la Yehova,” ndipo ndi kwa ndani kumene mawuwo amagwira ntchito?
13 Pambuyo pakuti chipembedzo chonyenga chawonongedwa, Yehova adzachitapo kanthu mwamsanga motsutsana ndi atsutsi otsalira a Ufumu wa Kristu. Kwa otsutsa onse oterowo, limodzinso ndi “Babulo Wamkulu,” mawu a Mulungu pa Yesaya 13:6, 9 amagwira ntchito: “Kuwani inu, pakuti tsiku la Yehova liri pafupi! Lidzafika monga chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse. Tawonani! Tsiku la Yehova lidza, lankhanza, ndi mkwiyo ndi kukalipira kwaukali, kupasula dziko, ndi kudzawonongamo akuchimwa psyiti.” Chidzakhala monga mmene wamasalmo Davide ananeneratu kuti: “Yehova asunga onse akukondana naye, koma oipa onse adzawaononga.”—Masalmo 145:20; Chivumbulutso 19:11-21.
14. Ndi mawu owonjezereka a Yesaya ati amene mitundu idzachita bwino kulabadira, ndipo nchifukwa ninji?
14 Mitundu ya padziko lapansi ingachite bwino kulabadira mawu owonjezereka a Yesaya pa mutu 34, maversi 1 mpaka 8: “Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve, mvetserani anthu inu. . . . Pakuti Yehova akwiira amitundu onse, nachitira ukali khamu lawo lonse. Iye wawaononga psyiti, wawapereka kukaphedwa. Ophedwa awonso adzataidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yawo kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wawo. . . . Pakuti liri tsiku la kubwezera la Yehova.” M’mabwalo a ndale zadziko, mabizinesi a akulu, ndi chipembedzo chonyenga lerolino, kuwononga ndi mkhalidwe woipa wa chisembwere ziri zofala. Koma Yehova akukonzekera kuyeretsa dziko. Ku mapeto awa, iye akusonkhanitsa kuchokera ku mitundu yonse—kaamba ka chipulumutso—anthu awo amene ali ofunitsitsa kusintha miyoyo yawo kumtumikira iye m’chilungamo. Ena onse ayenera kutha psyiti m’tsiku lake lakubwezera.—Yeremiya 25:31-33.
Paradaiso wa Mtendere
15. Nchiyani chimene Yesaya akulongosola m’mutu 35 m’chigwirizano ndi (a) lerolino? (b) mtsogolo?
15 Mu Yesaya mutu 35, mneneri wa Mulunguyo akupitiriza, m’chinenero chabwino kwambiri chokhala ndi chithunzithunzi, kulongosola mkhalidwe wa anthu obwezeretsedwa a Yehova, awo amene lerolino amaika chikhulupiriro chawo nthaŵi zonse mwa iye. Pokhala atasonkhanitsidwa m’paradaiso wauzimu, amenewa “amawona ulemerero wa Yehova, ukulu wa Mulungu wathu.” Iye amayang’ananso kutsogolo ku paradaiso wa kuthupi ndi kukwaniritsidwa kwa lonjezo lakuti: “Pamenepo maso a akhungu adzatsegulidwa, ndi makutu a ogontha adzatsegulidwa. Pamenepo wopunduka adzatumpha ngati nswala, ndi lilime la wosalankhula lidzaimba. Pakuti m’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.” (Yesaya 35:1, 2, 5, 6) Kodi mumasangalala pa chiyembekezo choterocho? Kodi mumakhulupirira mwa Yehova, kudalira kuti iye adzakwaniritsa malonjezo amenewo?
16, 17. (a) Ndi chisonkhezero chofulumira chotani chimene Yesaya akupanga pamene akulongosola Paradaiso? (b) Ndimotani mmene anthu a Yehova afunikira kuvomerezera ku chisonkhezero chimenechi?
16 Mwa kukhulupirira mwa Yehova, mungagawanemo m’kulimbikitsa achatsopano, limodzinso ndi ena amene chikhulupiriro chawo chingafunikire kulimbikitsidwa. Pakati pa kulongosola Paradaiso, mneneri Yesaya akuwonjezera chisonkhezero chachangu ichi: “Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa mawondo a gwedegwede. Nenani kwa a mitima ya chinthenthe: ‘Limbani, musawope. Tawonani! Mulungu wanu adza ndi kubwezera chilango, ndi mphotho ya Mulungu. Iye adzafika ndi kukupulumutsani.’” (Yesaya 35:3, 4) Inde, tikufuna kuwona onse amene mitima yawo iri yolungama akumangirira chikhulupiriro mwa Yehova, ndi cholinga cha kupambana kulowa m’Paradaiso wa padziko lapansi.
17 Chotero, lolani ife tichirikize manja olefuka aliwonse kotero kuti apitirizebe “kugwiritsitsa mawu a moyo.” Lolani ife tilimbitse mawondo a gwedegwede, kuwapatsa iwo thandizo pamene akafunikira “kuyenda moyenera Yehova kukamkondweretsa monsemo.” (Afilipi 2:16; Akolose 1:10) Inde, lolani ife titonthoze onse amene angakhale opsyinjidwa mtima, ndipo lolani kuti tilimbikitsane wina ndi mnzake, pamene tikuyang’anizana ndi ziyeso kapena chizunzo, kuti tisonyeze “kulimba mtima konse kulankhula mawu a Mulungu mopanda mantha.” (Afilipi 1:14; 1 Atesalonika 5:14; Aefeso 5:15, 16) Kenaka, pamene tsiku lobwezera la Yehova likantha, tingakhale otsimikiziridwa za dalitso lake pamene ‘iye abwera kupulumutsa anthu ake.’ M’tsiku limenelo, kodi mudzakhala pakati pa awo okhulupirira mwa Yehova kaamba ka chipulumutso?
18. Ndi chiyembekezo cholemekezeka chiti chimene chiri kutsogolo kwa awo amene amakhulupirira mwa Yehova, ndipo nchiyani chimene chiri chigamulo chawo?
18 Kwa awo amene nthaŵi zonse amakhulupirira mwa Yehova, ndi chiyembekezo chowala chotani nanga chimene chiri kutsogolo kwa tsiku limenelo! Atsenderezi ochimwa adzakhala atatha! M’dziko latsopano, okonda Ya Yehova adzabwezeretsedwa ndi Mwana wake ku ungwiro wopanda uchimo! Kodi inu simulakalaka kaamba ka nthaŵi imeneyo? Kukhulupirira kwanu mwa Yehova kudzakubweretsani inu ku tsiku losangalatsa limenelo. Inde, khulupirirani Yehova nthaŵi zonse, anthu inu, popeza ichi chitanthauza chipulumutso!
Mafunso Akubwereramo
◻ Nchiyani chimene nyimbo ya chipambano ya Yesaya 26 ikutilimbikitsa ife kuchita?
◻ Ndi “mudzi wokwezeka” uti umene Yehova adzautsitsa, ndipo ndimotani mmene ife timaupondera iwo?
◻ Nchiyani chimene tikuphunzira kuchokera ku pemphero la Hezekiya pamaso pa chiwopsyezo cha Sanakeribu?
◻ Ndimotani mmene “ophedwa” a Yesaya 26:21 akubwezeredwera?
◻ Nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo ngati tikhulupirira mwa Ya Yehova?
[Bokosi patsamba 19]
Kupatsa Mlandu Mdindo Woyera?
M’kufupikitsa nkhani ya Umberto Siniscalchi mu Il Giornale ya Milan, World Press Review inanena kuti: “Bwalo Lalikulu la Apilu la Italy liri pansi pa kusulizidwa kwakukulu chifukwa linaletsa, mu July [1987], chilolezo chogwira nduna za banki zitatu za Vatican zolowetsedwa mu Mlandu wa Kugwiritsira Ntchito Molakwa Chuma cha Tchalitchi.” Chosankhacho, chozikidwa pa pangano lakale pakati pa Vatican ndi boma la Italy, chinapereka lamulo la chipatula kwa tcheyamani wa bankilo, yemwe ali bishopo wamkulu, ndiponso manenjala wotsogoza wa bankilo ndi woŵerengera ndalama wamkulu. Kubwereramoko kukuwonjezera kuti: “Asulizi ena, ngakhale kuti iwo sakupereka liwongo pa oweruzawo kaamba ka chosankhacho, akusungilira kuti panganolo likutsutsana ndi lamulo la dziko la Italy chifukwa cha kupereka lamulo la kupatula kwa awo amene analowetsedwa mu upandu m’dziko la Italy. Okonza malamulo a boma ena akukakamiza kaamba ka chivomerezo kulola dongosolo la chiweruzo la Italy kuzenga mlandu Mdindo Woyera kaamba ka milandu yochitidwa mu Italy.”