‘Nyumba Yakupemphereramo Anthu a Mitundu Yonse’
“Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse?”—MARKO 11:17.
1. Kodi Adamu ndi Hava anali ndi unansi wotani ndi Mulungu poyamba?
PAMENE Adamu ndi Hava analengedwa, anali ndi unansi wapafupi ndi Atate wawo wakumwamba. Yehova Mulungu analankhulana nawo ndi kuwafotokozera chifuno chake chabwino kwambiri kaamba ka mtundu wa anthu. Ndithudi, iwo kaŵirikaŵiri anali kusonkhezereka kutamanda Yehova chifukwa cha ntchito zake zazikulu za chilengedwe. Ngati Adamu ndi Hava akanafuna chitsogozo pamene anali kulingalira za mbali yawo monga atate ndi amayi amtsogolo a banja la munthu, akanatha kufikira Mulungu kulikonse m’mudzi wawo wa Paradaiso. Sanafunikire mautumiki a wansembe m’kachisi.—Genesis 1:28.
2. Kodi ndi kusintha kotani kumene kunachitika pamene Adamu ndi Hava anachimwa?
2 Mkhalidwewo unasintha pamene mngelo wina wopanduka ananyenga Hava kuyamba kuganiza kuti mkhalidwe wake m’moyo udzawongokera ngati akana ulamuliro wa Yehova, akumati ‘adzakhala ngati Mulungu.’ Motero Hava anakhulupirira bodza la Satana nadya chipatso cha mtengo umene Mulungu anauletsa. Ndiyeno Satana anagwiritsira ntchito Hava kuyesa mwamuna wake. Mwatsoka, Adamu anamvetsera mkazi wake wochimwayo, akumasonyeza kuti anaŵerengera kwambiri unansi wake ndi mkaziyo kuposa unansi wake ndi Mulungu. (Genesis 3:4-7) Kwenikweni, Adamu ndi Hava anasankha Satana kukhala mulungu wawo.—Yerekezerani ndi 2 Akorinto 4:4.
3. Kodi zotulukapo zoipa za kupanduka kwa Adamu ndi Hava zinali zotani?
3 Pochita zimenezo, anthu aŵiri okwatirana oyambawo sanangotaya unansi wawo wamtengo wapatali ndi Mulungu komanso chiyembekezo chawo cha kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wa padziko lapansi. (Genesis 2:16, 17) M’kupita kwa nthaŵi matupi awo ochimwa anayamba kufooka mpaka anafa. Mbadwa zawo zinalandira mkhalidwe wa choloŵa chauchimo umenewu. “Chotero,” limalongosola motero Baibulo, “imfa inafikira anthu onse.”—Aroma 5:12.
4. Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene Mulungu anapereka kwa anthu ochimwa?
4 Kanthu kena kanafunika kuti anthu ochimwa ayanjanitsidwe ndi Mlengi wawo woyera. Pamene anali kupereka chilango kwa Adamu ndi Hava, Mulungu anapereka chiyembekezo ku mbadwa zawo zamtsogolo mwa kulonjeza za “mbewu” imene idzapulumutsa anthu pa ziyambukiro za chipanduko cha Satana. (Genesis 3:15) Pambuyo pake, Mulungu anavumbula kuti Mbewu ya dalitso idzadzera mwa Abrahamu. (Genesis 22:18) Pokhala ndi chifuno chachikondi chimenechi m’maganizo, Mulungu anasankha mbadwa za Abrahamu, Aisrayeli, kukhala mtundu wake wosankhidwa.
5. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala ndi chidwi ponena za mfundo za pangano la Chilamulo cha Mulungu ndi Israyeli?
5 Mu 1513 B.C.E., Aisrayeli analoŵa mu unansi wa pangano ndi Mulungu ndipo anavomera kuti adzamvera malamulo ake. Pangano la Chilamulo limenelo liyenera kusonkhezera chidwi chachikulu kwa onse amene akufuna kulambira Mulungu lerolino chifukwa linasonya ku Mbewu yolonjezedwa. Paulo anati linali ndi “mthunzi wa zokoma zilinkudza.” (Ahebri 10:1) Pamene Paulo ananena mawu ameneŵa, anali kufotokoza za utumiki wa ansembe a Israyeli pachihema chonyamulika cha kulambira. Chinatchedwa kuti “kachisi wa Yehova” kapena “nyumba ya Yehova.” (1 Samueli 1:9, 24) Mwa kupenda utumiki wopatulika umene unachitidwa panyumba ya Yehova ya padziko lapansi, tingathe kuzindikira bwino kwambiri makonzedwe achifundo mwa amene anthu ochimwa lerolino angayanjanitsidwe ndi Mulungu.
Malo Opatulikitsa
6. Kodi nchiyani chimene chinali m’Malo Opatulikitsa, ndipo kukhalapo kwa Mulungu kunaimiridwa motani mmenemo?
6 “Wa[m’]mwambamwambayo sakhala m’nyumba zomangidwa ndi manja,” limatero Baibulo. (Machitidwe 7:48) Komabe, kukhalapo kwa Mulungu m’nyumba yake ya padziko lapansi kunaimiridwa ndi mtambo mkati mwa chipinda chotchedwa kuti Malo Opatulikitsa. (Levitiko 16:2) Mwachionekere, mtambo umenewu unaŵala kwambiri, ukumaunikira Malo Opatulikitsa. Unali pamwamba pa bokosi lopatulika lotchedwa “likasa la mboni,” limene linali ndi miyala yosemedwa yozokotedwapo malamulo ena amene Mulungu anapatsa Israyeli. Pachotetezerapo cha Likasa panali akerubi aŵiri agolidi okhala ndi mapiko otambasulidwa, amene anachitira chithunzi zolengedwa zauzimu zokhala ndi malo apamwamba m’gulu lakumwamba la Mulungu. Mtambo wozizwitsa wa kuunika unali pamwamba pa chotetezerapo ndipo pakati pa akerubi. (Eksodo 25:22) Zimenezi zinachitira chithunzi Mulungu Wamphamvuyonse wokhala pa mpando wachifumu m’galeta lakumwamba lochirikizidwa ndi akerubi amoyo. (1 Mbiri 28:18) Zimenezi zikusonyeza chifukwa chake Mfumu Hezekiya anapemphera kuti: “Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, amene mukhala pa akerubi.”—Yesaya 37:16.
Malo Opatulika
7. Kodi m’Malo Opatulika munali ziŵiya zotani?
7 Chipinda chachiŵiri cha chihema chinatchedwa kuti Malo Opatulika. Mkati mwa chipinda chimenechi, kumanzere kwa khomo kunali choikapo nyali chokongola cha mphanda zisanu ndi ziŵiri, ndipo kulamanja kwake kunali gome la mkate woonekera. Kutsogolo kwa chipindacho kunali guwa la nsembe pamene panachokera fungo la zofukizapo kumka kumwamba. Linali kumaso kwa nsalu yotchinga imene inasiyanitsa Malo Opatulika ndi Malo Opatulikitsa.
8. Kodi ansembe anachita ntchito zotani nthaŵi zonse m’Malo Opatulika?
8 Mmaŵa uliwonse ndi madzulo alionse, wansembe anali kuloŵa m’chihema ndi kufukiza zofukiza pa guwa la nsembe lofukizapo. (Eksodo 30:7, 8) Mmaŵa, pamene zofukizazo zinali kupsa, nyali zisanu ndi ziŵiri zimene zinali pa choikapo nyali cha golidi anali kuzidzaza mafuta. Nyalizo zinali kuyatsidwa madzulo kuti ziunikire Malo Opatulika. La Sabata lililonse wansembe anali kuika mikate 12 yatsopano pa gome la mkate woonekera.—Levitiko 24:4-8.
Bwalo
9. Kodi nchiyani chimene chinali chifuno cha mkhate wa madzi, ndipo ndi phunziro lotani limene tingapeze pamenepa?
9 Chihema chinalinso ndi bwalo, lokwetezedwa ndi mpanda wa nsalu za hema. M’bwalo limeneli munali mkhate waukulu mmene ansembe anali kusambiramo manja ndi mapazi awo asanaloŵe m’Malo Opatulika. Anafunikiranso kusamba asanapereke nsembe pa guwa la nsembe limene linali m’bwalo. (Eksodo 30:18-21) Chofunika chimenechi cha chiyero chili chikumbutso champhamvu kwa atumiki a Mulungu lerolino chakuti ayenera kuyesayesa kukhala oyera mwakuthupi, m’makhalidwe, m’maganizo ndi mwauzimu ngati akufuna kuti Mulungu avomereze kulambira kwawo. (2 Akorinto 7:1) M’kupita kwa nthaŵi nkhuni za moto wa pa guwalo ndi madzi a m’mkhate zinaperekedwa ndi akapolo akukachisi osakhala Aisrayeli.—Yoswa 9:27.
10. Kodi ndi nsembe zina ziti zimene zinaperekedwa pa guwa la nsembe?
10 Mmaŵa uliwonse ndi madzulo alionse, anali kupsereza nsembe ya mwana wa nkhosa pa guwa pamodzi ndi chopereka ndi nsembe yothira. (Eksodo 29:38-41) Nsembe zina zinaperekedwa pamasiku apadera. Nthaŵi zina nsembe inaperekedwa chifukwa cha tchimo lina la munthu mwini. (Levitiko 5:5, 6) Panthaŵi zina Mwisrayeli anali kupereka nsembe yaufulu ya chiyanjano imene mbali zake zina zinali kudyedwa ndi ansembe ndi mwini nsembeyo. Zimenezi zinatanthauza kuti anthu ochimwa akanatha kukhala pamtendere ndi Mulungu, akumadya naye chakudya, titero kunena kwake. Ngakhale mlendo anatha kukhala wolambira wa Yehova ndi kukhala ndi mwaŵi wa kupereka nsembe zaufulu panyumba Yake. Koma kuti asonyeze ulemu wofunika kwa Yehova, ansembe anali kulandira nsembe zangwiro zokhazokha. Ufa wansembe unafunikira kuperedwa kukhala wosalala, ndipo nyama za nsembe zinafunikira kukhala zopanda chirema.—Levitiko 2:1; 22:18-20; Malaki 1:6-8.
11. (a) Kodi anachita motani ndi mwazi wa nyama za nsembe, ndipo unali kusonyezanji? (b) Kodi Mulungu amaona motani mwazi wa munthu ndi wa nyama womwe?
11 Mwazi wa nsembe zimenezi unabweretsedwa pa guwa la nsembe. Zimenezi zinakhala chikumbutso chatsiku ndi tsiku ku mtunduwo chakuti iwo anali ochimwa ofunikira momboli amene mwazi wake wokhetsedwa ungatetezere kosatha machimo awo ndi kuwapulumutsa ku imfa. (Aroma 7:24, 25; Agalatiya 3:24; yerekezerani ndi Ahebri 10:3.) Kugwiritsira ntchito mwazi kopatulika kumeneku kunakumbutsanso Aisrayeli kuti mwazi umaimira moyo ndi kuti moyowo mwini wake ndi Mulungu. Nthaŵi zonse Mulungu waletsa anthu kugwiritsira ntchito mwazi mwa njira yosiyana ndi imeneyo.—Genesis 9:4; Levitiko 17:10-12; Machitidwe 15:28, 29.
Tsiku Lotetezera
12, 13. (a) Kodi Tsiku Lotetezera linali la chiyani? (b) Mkulu wa ansembe asanabweretse mwazi m’Malo Opatulikitsa, kodi ayenera kuchitanji?
12 Kamodzi pachaka, mtundu wonse wa Israyeli kuphatikizapo alendo amene analambira Yehova, anafunikira kuleka kugwira ntchito zonse ndi kusala kudya. (Levitiko 16:29, 30) Patsiku lofunika limeneli, mtunduwo unali kuyeretsedwa patchimo mophiphiritsira kuti ukhalenso ndi unansi wamtendere ndi Mulungu kaamba ka chaka china. Tiyeni tiyerekezere chochitikacho ndi kulingalira mfundo zake zina zazikulu.
13 Mkulu wa ansembe ali m’bwalo la chihema. Pokhala atasamba mu mkhate wa madzi, akupha ng’ombe yamphongo ya nsembe. Mwazi wa ngo’mbewo autsanulira m’mbizi; udzagwiritsiridwa ntchito mwapadera kutetezera machimo a fuko la ansembe la Levi. (Levitiko 16:4, 6, 11) Koma tisananene zambiri pa nsembe, pali kanthu kena kamene mkulu wa ansembe ayenera kuchita. Iyeyo akutenga zofukizira mwinamwake m’chipande ndi makala amoto paguwa la nsembe m’chotengera moto. Tsopano iye akuloŵa m’Malo Opatulika napita cha kunsalu yotchinga ya Malo Opatulikitsa. Akudutsa pang’onopang’ono kuloŵa kuseri kwa nsalu yotchingayo naima patsogolo pa likasa la chipangano. Kenako, mosaonekera kwa munthu aliyense, akuthira zofukizazo pamakala amotopo, ndipo Malo Opatulikitsawo akudzazidwa ndi mtambo wa fungo lokoma.—Levitiko 16:12, 13.
14. Kodi nchifukwa ninji mkulu wa ansembe anafunikira kuloŵa m’Malo Opatulikitsa ndi mwazi wa nyama ziŵiri zosiyana?
14 Tsopano Mulungu ali wokonzekera kusonyeza chifundo ndi kupemphedwa chitetezero m’njira yophiphiritsira. Pachifukwa chimenechi chotetezerapo cha Likasa chinatchedwa “mpando wa chifundo” kapena “chivundikiro chopembedzera.” (Ahebri 9:5, NW, mawu amtsinde.) Mkulu wa ansembe akutuluka m’Malo Opatulikitsa, atenga mwazi wa ng’ombe, naloŵanso m’Malo Opatulikitsa. Monga momwe Chilamulo chinanenera, akunyika chala chake m’mwaziwo nauwaza kasanu ndi kaŵiri pachotetezerapo cha Likasa. (Levitiko 16:14) Ndiyeno akupitanso m’bwalo napha mbuzi, imene ili nsembe yamachimo “ndiyo yophera anthu.” Akuloŵa ndi mwazi wina wa mbuziyo m’Malo Opatulikitsa nachita nawo mofanana ndi mmene anachitira ndi mwazi wa ng’ombe. (Levitiko 16:15) Utumiki wina wofunika unali kuchitikanso pa Tsiku Lotetezera. Mwachitsanzo, mkulu wa ansembe anali kuika manja ake pamutu wa mbuzi yachiŵiri ndi kuvomereza pa iyo “mphulupulu zonse za ana a Israyeli.” Pamenepo mbuzi imeneyi yamoyo anali kuitumiza kuchipululu itasenza machimo a mtunduwo mophiphiritsira. Mwa njira imeneyi anatetezera “ansembe, ndi anthu onse a msonkhanowo” chaka chilichonse.—Levitiko 16:16, 21, 22, 33.
15. (a) Kodi kachisi wa Solomo anafanana motani ndi chihema? (b) Kodi buku la Ahebri limanenanji za utumiki wopatulika umene unachitidwa ponse paŵiri pachihema ndi pakachisi?
15 Kwa zaka 486 zoyamba za mbiri ya Israyeli monga anthu apangano la Mulungu, chihema chonyamulika chinatumikira monga malo awo olambirirapo Mulungu wawo, Yehova. Ndiyeno, Solomo wa Israyeli anapatsidwa mwaŵi wa kumanga nyumba yachikhalire. Ngakhale kuti kachisiyu anali kudzakhala wokulirapo ndi wokongola kwambiri, pulani yake yoperekedwa ndi Mulungu inali yolingana ndi ija ya chihema. Monga momwe chinalili chihema, anali phiphiritso la makonzedwe okulira ndi amphamvu kwambiri a kulambira amene Yehova ‘adzamanga, si munthu ayi.’—Ahebri 8:2, 5; 9:9, 11.
Kachisi Woyamba ndi Wachiŵiri
16. (a) Kodi ndi pempho lachikondi lotani limene Solomo anapereka pamene anali kupatulira kachisi? (b) Kodi Yehova anasonyeza motani kuti anavomereza pemphero la Solomo?
16 Popatulira kachisi waulemerero ameneyo, Solomo anaphatikizapo pempho louziridwa ili: “Kunena za mlendo wosakhala wa anthu anu Israyeli, akafumira ku dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu, . . . akadza iwowa ndi kupemphera kuloza ku nyumba iyi; pamenepo mumvere inu m’mwamba mokhala inumo, nimumchitire mlendoyo monga mwa zonse akuitanirani; kuti mitundu yonse ya anthu apadziko lapansi adziŵe dzina lanu, nakuopeni, monga amatero anthu anu Aisrayeli; ndi kuti adziŵe kuti nyumba iyi ndamangayi itchedwa ndi dzina lanu.” (2 Mbiri 6:32, 33) Mwanjira yotsimikizirika, Mulungu anasonyeza kuti anavomereza pemphero la Solomo lopatulira. Laŵi la moto linatsika kuchokera kumwamba ndi kunyeketsa nsembe zanyama zimene zinali pa guwa la nsembe, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza kachisiyo.—2 Mbiri 7:1-3.
17. Kodi nchiyani chimene chinachitikira kachisi womangidwa ndi Solomo pambuyo pake, ndipo chifukwa ninji?
17 Mwachisoni, Aisrayeli anataya mantha awo abwino a Yehova. M’kupita kwa nthaŵi, ananyoza dzina lake lalikululo mwa kukhetsa mwazi, kupembedza mafano, chigololo, kugonana pachibale, ndi mwa kuzunza ana amasiye, akazi amasiye, ndi alendo. (Ezekieli 22:2, 3, 7, 11, 12, 26, 29) Motero, m’chaka cha 607 B.C.E., Mulungu anapereka chiweruzo mwa kubweretsa magulu a nkhondo a ku Babulo kudzawononga kachisi. Aisrayeli otsalira anatengedwa ukapolo kumka ku Babulo.
18. Pakachisi wachiŵiri, kodi ndi mwaŵi wotani umene unatsegukira amuna ena amene sanali Aisrayeli amene anachirikiza kulambira Yehova ndi mtima wonse?
18 Patapita zaka 70 Ayuda otsalira olapa anabwerera ku Yerusalemu ndipo anapatsidwa mwaŵi wa kumanganso kachisi wa Yehova. Chochititsa chidwi nchakuti, panali kupereŵera kwa ansembe ndi Alevi oti atumikire m’kachisi wachiŵiri ameneyu. Chotero, Anetini, amene anali mbadwa za akapolo apakachisi osakhala Aisrayeli, anapatsidwa mwaŵi wowonjezereka kukhala atumiki a nyumba ya Mulungu. Komabe, sanakhale olingana ndi ansembe ndi Alevi.—Ezara 7:24; 8:17, 20.
19. Kodi ndi lonjezo lotani limene Mulungu anapanga lonena za kachisi wachiŵiri, ndipo lonjezo limeneli linakwaniritsidwa motani?
19 Poyamba kunaoneka ngati kuti kachisi wachiŵiriyo sadzafanana konse ndi woyamba. (Hagai 2:3) Koma Yehova analonjeza kuti: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero . . . Ulemerero wotsiriza wa nyumba iyi udzaposa woyambawo.” (Hagai 2:7, 9) Monga momwe ananeneradi, kachisi wachiŵiriyo anali ndi ulemerero wokulirapo. Anakhalako kuposa woyambayo ndi zaka 164, ndipo olambira ambiri ochokera m’maiko ambiri anafika m’mabwalo ake. (Yerekezerani ndi Machitidwe 2:5-11.) Kukonzedwa kwa kachisi wachiŵiri kunayamba m’masiku a Mfumu Herode, ndipo mabwalo ake anakuzidwa. Pokhala wokwezeka pathanthwe lalikulu ndi wokwetezedwa ndi makumbi okongola, analingana mu ulemerero ndi kachisi woyambirira amene anamangidwa ndi Solomo. Anaphatikizapo bwalo lakunja lalikulu la anthu a mitundu amene anafuna kudzalambira Yehova. Khoma lamwala linalekanitsa Bwalo la Akunja limeneli ndi mabwalo amkati a Aisrayeli okha.
20. (a) Kodi ndi chinthu chapadera chotani chimene chinasiyanitsa kachisi womangidwansoyo? (b) Kodi nchiyani chimene chinasonyeza kuti Ayuda anaona kachisiyo molakwa, ndipo Yesu anachitanji pa zimenezo?
20 Kachisi wachiŵiri ameneyu anali wapadera kwambiri chifukwa cha kukhala ndi Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, akumaphunzitsa m’mabwalo ake. Koma monga momwe zinalili ndi kachisi woyamba, Ayuda ambiri analibe lingaliro loyenera la mwaŵi wawo wa kukhala osunga nyumba ya Mulungu. Eetu, iwo analoladi amalonda kuchita malonda awo m’bwalo la Akunja. Ndiponso, anthu analoledwa kugwiritsira ntchito kachisiyo monga njira yachidule atanyamula zinthu kumka nazo kumbali ina ya Yerusalemu. Patatsala masiku anayi imfa yake isanachitike, Yesu anayeretsa kachisi kuchotsa machitachita adziko otero, akumapitiriza kunena kuti: “Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.”—Marko 11:15-17.
Mulungu Asiya Nyumba Yake ya Padziko Lapansi Kosatha
21. Kodi Yesu anasonyezanji ponena za kachisi wa Yerusalemu?
21 Chifukwa cha mchitidwe wolimba mtima wa Yesu pochirikiza kulambira Mulungu koyera, atsogoleri achipembedzo achiyuda anatsimikiza zomupha. (Marko 11:18) Podziŵa kuti adzaphedwa msanga, Yesu ananena kwa atsogoleri achipembedzo achiyuda kuti: “Nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” (Mateyu 23:37, 38) Motero iye anasonyeza kuti posapita nthaŵi Mulungu sadzavomerezanso mtundu wa kulambira umene iwo anauchita pakachisi woonekayo mu Yerusalemu. Sadzakhalanso “nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse.” Pamene ophunzira ake anasonyeza Yesu nyumba zokongola za kachisiyo, iye anati: “Simuona izi zonse kodi? Indetu ndinena kwa inu, Sipadzakhala pano mwala umodzi pa unzake, umene sudzagwetsedwa.”—Mateyu 24:1, 2.
22. (a) Kodi mawu a Yesu onena za kachisi anakwaniritsidwa motani? (b) M’malo mwa kuzika ziyembekezo zawo pa mudzi wapadziko lapansi, kodi Akristu oyambirira anafunafuna chiyani?
22 Ulosi wa Yesu unakwaniritsidwa patapita zaka 37 m’chaka cha 70 C.E., pamene magulu a nkhondo achiroma anawononga Yerusalemu ndi kachisi wake. Zimenezo zinapereka umboni wamphamvu wakuti Mulungu anali atasiyadi nyumba yake yooneka. Yesu sananeneretu za kumangidwanso kwa kachisi wina mu Yerusalemu. Ponena za mzinda wa padziko lapansi umenewo, mtumwi Paulo analembera Akristu achihebri kuti: “Pano tilibe mudzi wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.” (Ahebri 13:14) Akristu oyambirira anayembekezera kudzakhala mbali ya “Yerusalemu wakumwamba”—Ufumu wa Mulungu wonga mudzi. (Ahebri 12:22) Motero, kulambira Yehova koona sikulinso kozikidwa pa kachisi wina wooneka padziko lapansi. M’nkhani yathu yotsatira, tidzafotokoza za makonzedwe apamwamba amene Mulungu wakonza kaamba ka onse amene akufuna kumlambira “mumzimu ndi m’choonadi.”—Yohane 4:21, 24.
Mafunso a Kupenda
◻ Kodi Adamu ndi Hava anataya unansi wotani ndi Mulungu?
◻ Kodi nchifukwa ninji mbali za chihema ziyenera kusonkhezera chidwi mwa ife?
◻ Kodi timaphunziranji m’zochitika za m’bwalo la chihema?
◻ Kodi nchifukwa ninji Mulungu analola kachisi wake kuwonongedwa?
[Zithunzi pamasamba 10, 11]
Kachisi Womangidwanso ndi Herode
1. Malo Opatulikitsa
2. Malo Opatulika
3. Guwa la Nsembe Yopsereza
4. Thawale Lamkuwa
5. Bwalo la Ansembe
6. Bwalo la Israyeli
7. Bwalo la Akazi