Hagai
2 Pa tsiku la 21 la mwezi wa 7, Yehova analankhula ndi mneneri Hagai+ kuti: 2 “Chonde, kafunse Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli bwanamkubwa wa Yuda,+ Yoswa+ mwana wa Yehozadaki+ mkulu wa ansembe ndiponso anthu ena onse kuti: 3 ‘Kodi pakati panu pali aliyense amene anaona ulemerero umene nyumbayi* inali nawo poyamba?+ Kodi panopa mukuiona bwanji? Kodi simukuona kuti ilibiretu ulemerero tikayerekeza ndi poyamba?’+
4 ‘Koma tsopano limba mtima iwe Zerubabele. Limba mtima iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe,’ watero Yehova.
‘Limbani mtima anthu nonse amʼdzikoli+ ndipo gwirani ntchito,’ watero Yehova.
‘Pakuti ine ndili ndi inu,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 5 ‘Kumbukirani zimene ndinakulonjezani pamene munkatuluka mʼdziko la Iguputo.+ Panopa mzimu wanga udakali ndi inu.*+ Choncho musachite mantha.’”+
6 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Posachedwapa ndigwedezanso kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi mtunda.’+
7 ‘Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa mʼnyumba imeneyi.+ Ndipo ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemerero,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
8 ‘Siliva ndi wanga, golidenso ndi wanga,’ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
9 ‘Ulemerero wa nyumba yatsopanoyi udzakhala waukulu kuposa wa nyumba yoyamba ija,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
‘Ndipo ndidzakupatsani mtendere pamalo ano,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”
10 Pa tsiku la 24 la mwezi wa 9, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova analankhula ndi mneneri Hagai+ kuti: 11 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Funsa ansembe zokhudza Chilamulo.+ Uwafunse kuti: 12 “Ngati munthu atanyamula nyama yopatulika pachovala chake, ndiyeno chovalacho nʼkukhudza mkate, kapena msuzi, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chilichonse, kodi chinthu chokhudzidwacho chingakhale chopatulika?”’”
Ansembewo anayankha kuti: “Ayi!”
13 Ndiyeno Hagai anafunsanso kuti: “Ngati munthu amene wadetsedwa chifukwa chokhudza mtembo atakhudza chilichonse mwa zinthu zimenezi, kodi chingakhale chodetsedwa?”+
Ansembewo anayankha kuti: “Inde, chingakhale chodetsedwa.”
14 Choncho Hagai anati: “‘Mmenemutu ndi mmene anthu awa alili ndipo ndi mmene mtunduwu ulili pamaso panga. Ndi mmenenso ntchito yonse ya manja awo ndi chilichonse chimene amapereka nsembe chilili. Ndi zodetsedwa,’ watero Yehova.
15 ‘Koma tsopano, chonde ganizirani izi mofatsa kuyambira lero mpaka mʼtsogolo: Asanasanjikize mwala pamwala unzake mʼkachisi wa Yehova,+ 16 kodi zinthu zinali bwanji? Munthu ankati akapita pamulu wa zokolola umene ukanakwana miyezo 20, ankapeza kuti ndi wongokwana miyezo 10. Ndipo munthu ankati akapita moponderamo mphesa kuti akatunge miyezo 50 ya vinyo, ankapeza kuti muli wongokwana miyezo 20.+ 17 Ine ndinakulangani ndipo ndinawononga ntchito za manja anu pobweretsa mphepo yotentha, matenda a mbewu a chuku+ ndi matalala, koma palibe aliyense amene anabwerera kwa ine,’ watero Yehova.
18 ‘Lero, pa tsiku la 24 la mwezi wa 9, pamene maziko a kachisi wa Yehova ayalidwa,+ kuyambira lero kupita mʼtsogolo, chonde ganizirani izi mofatsa: 19 Kodi mbewu zilipobe mʼnyumba yosungiramo mbewu?*+ Kodi mitengo ya mpesa, ya mkuyu, ya makangaza* ndi ya maolivi yabereka zipatso? Kuyambira lero ndikupatsani madalitso.’”+
20 Yehova analankhulanso ndi Hagai kachiwiri pa tsiku la 24 la mweziwo+ kuti: 21 “Uza Zerubabele bwanamkubwa wa Yuda kuti, ‘Ine ndigwedeza kumwamba ndi dziko lapansi.+ 22 Ndidzagonjetsa maufumu ndi kuchotsa mphamvu za maufumu a anthu a mitundu ina.+ Ndidzawononga magaleta* ndi okwera pamagaletawo. Mahatchi* ndi okwera pamahatchiwo adzaphedwa ndipo aliyense adzaphedwa ndi mʼbale wake ndi lupanga.’”+
23 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo ndidzakutenga iwe Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli,+ mtumiki wanga,’ watero Yehova. ‘Ndipo ndidzachititsa kuti ukhale ngati mphete yodindira chifukwa iwe ndi amene ndakusankha,’ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”