Mlandu wa Bwalo la Milandu la Chilengedwe Chonse Womwe Umakuyambukirani
“‘Onetsani mlandu wanu,’ ati Yehova. ‘Tulutsani zifukwa zanu zolimba.’”—YESAYA 41:21.
1, 2. (a) Ndani amene akukhudzidwa ndi mlandu wowopsya wa bwalo la milandu womwe udzazengedwa? (b) Nchiyani chimene chiri pa nkhani?
KUZUNGULIRA m’mbiri yakale pakhala milandu yosaŵerengeka ya m’bwalo la milandu. Mu iyi, mboni zinabweretsedwa ndipo umboni unaperekedwa kaamba ka kutsutsa mbali imodzi kapena inzake. Yambiri ya milandu imeneyi inakhudza munthu aliyense payekha, pamene ina inayambukira unyinji wokulira wa anthu. Koma milandu yonse yoteroyo simawoneka monga kanthu itayerekezedwa ndi mlandu wa bwalo la milandu la chilengedwe chonse womwe tsopano ukuzengedwa. Iwo uli mlandu wa bwalo la milandu waukulu kwambiri m’mbiri. Zotulukapo zake zidzayambukira munthu aliyense pa dziko lonse lapansi, kaya asankha kukhudzidwa ndi iwo kapena ayi.
2 Munthu wowonekera m’mlandu umenewu ali munthu wapamwamba kwambiri m’chilengedwe chonse, Yehova Mulungu, “amene Analenga thambo, nalifutukula, nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka mmenemo, Iye amene amapatsa anthu a mmenemo mpweya, ndi mzimu kwa iwo amene ayenda mmenemo.” (Yesaya 42:5) Kodi ndi iti imene iri nkhani imeneyi? Umulungu wake uli pa nkhani—kulungama kwa ulamuliro wake pa chilengedwe chonse, kuphatikizapo dziko lapansi ndi nzika zake. Iyi ingatchedwe nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse.
3. Ndi mafunso otani amene ali achindunji ku nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse?
3 Ogwirizana ndi nkhaniyo ali mafunso awa: Ndi iti ya milungu yonse yolambiridwa imene yatsimikizira kukhala yodalirika kwakuti mungapereke moyo wanu ndi mtsogolo mwanu kwa iyo? Ndi iti imene m’chenicheni inakhalako, ndipo ndi iti imene iri chabe yopangidwa ndi anthu? Kodi palidi Mulungu wamkulu, wowona, wamoyo yemwe angapulumutse mtundu wa anthu kuchokera ku mkhalidwe womwe ulipowu wosowa chochita ndi kubweretsa mtundu wowongoka wa boma lomwe lingatsimikizire za mtendere weniweni, chisungiko, kupita patsogolo, ndi umoyo wabwino?
4. Nchiyani chimene chinganenedwe za awo omwe amadzimva kuti palibe nkhani, popeza iwo amanena kuti amakhulupirira kale mwa Mulungu?
4 Anthu ambiri amamva kuti palibe nkhani kaamba ka iwo, popeza iwo amanena kuti amakhulupirira kale mwa Mulungu. Koma kodi iwo angapereke chitsimikiziro chakuti mulungu amene iwo amamlambira alidi Mulungu wowona, kuti malonjezo ake ali odalirika, ndi kuti zifuno zake ndi malamulo ake zimatsogoza miyoyo yawo? Ngati anthu otero ayankha kuti inde, chotero iwo ayeneranso kukhala okhoza kuyankha mafunso awa: Kodi nchiyani chimene chiri chitsimikiziro chakuti pali Mulungu wowona amene malonjezo ake ali odalirika? Nchiyani chimene chiri chifuno cha Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu ndi dziko lapansi? Ndi kuti kumene tiri m’nyengo ya nthaŵi ya Mulungu, ndipo nchiyani chimene mtsogolo mwaposachedwapa mwasunga? Nchiyani chimene iye akufuna kuti ife tichite monga munthu payekha ngati tikafuna kumusungirira iye?
5. Ndi kwandani kumene anthu angayerekezedwe pamene iwo satulutsa chitsimikiziro cha kuchirikiza chikhulupiriro chawo mwa Mulungu?
5 Anthu ambiri amene amanena kuti amakhulupirira mwa Mulungu ali osakhoza kuyankha mafunso amenewo mwaulamuliro. Oterowo angayerekezedwe ndi awo omwe anadzinenera kukhala akukhulupirira mwa Mulungu m’zana loyamba koma amene ntchito zawo zinasonyeza kunyenga kwa kudzinenera kwawo. Za iwo mawu a Mulungu amanena kuti: “Avomereza kuti adziŵa Mulungu, koma ndi ntchito zawo amkana iye.” Inde, “chikhulupiriro chopanda ntchito chiri chakufa.” (Tito 1:16; Yakobo 2:26) Chotero, awo amene amanena kuti amakhulupirira mwa Mulungu koma sangatulutse chitsimikiziro cholimba cha kuchirikiza icho m’njira iriyonse iwo sali osiyana ndi anthu a m’mazana apita omwe anakhulupirira mwa milungu yonyenga yomwe kuyambira pa nthaŵiyo inazimiririka monga zinthu za kulambira.
Milandu Yoyesa
6, 7. (a) Longosolani chipembedzo cha Aigupto akale. (b) Ndimotani mmene Aisrayeli analoŵetsedwera m’nkhani pakati pa Yehova ndi milungu ya Igupto?
6 Chitsanzo cha ichi chinali mlandu womwe unabweretsedwa motsutsana ndi milungu ya Igupto wakale chifupifupi zaka 1,500 isanafike Nyengo Yathu. Aigupto ankalambira unyinji wa milungu, kuphatikizapo nyama monga ngati ng’ombe, mphaka, ng’ombe yaikazi, ng’ona, mphamba, chule, nkhandwe, mkango, njoka, mulimba, ndi m’mbulu. Zambiri za zinyama zimenezi zinali kulingaliridwa kukhala kudziveka thupi la nyama kwa mulungu kapena mulungu wachikazi, ndipo kupha imodzi ya iyo mwadala kunabweretsa chilango cha imfa. Nyama zopatulika zinali kukonzedwa bwino pambuyo pa imfa yawo ndipo zinali kupatsidwa kuikidwa kwapadera.
7 Mosiyana ndi milungu yonseyo anali Mulungu amene Israyeli wakale anamulambira, Yehova. Woimira wake, Mose, anatumizidwa kukafunsa Farao kumasula anthu a Yehova, omwe panthaŵiyo anali mu ukapolo, popeza Yehova anali atawalonjeza iwo ufulu wawo. (Eksodo 3:6-10) Koma Farao ananena kuti: “Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake ndi kulola Israyeli apite? Sindimdziŵa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite.” (Eksodo 5:2) Farao anadzimva wachidaliro kuti milungu ya Igupto inali yapamwamba kuposa Yehova.
8, 9. (a) Ndimotani mmene Yehova anatsimikizirira upamwamba wake pa milungu ya Igupto? (b) M’chiyang’aniro cha zimene zinachitika, nchiyani chimene chiyenera kunenedwa ponena za milungu ya Igupto?
8 Kodi ndi ndani amene akatsimikizira kukhala Mulungu wowona yemwe anali wokhoza kusunga malonjezo ake ndipo wokhoza kuchinjiriza anthu ake? Yankho linayenera kufika mwamsanga. Yehova ananeneratu kuti: “Ndidzachita maŵeruzo pa milungu yonse ya Aigupto.” (Eksodo 12:12) Kodi iye anakwaniritsa ulosi umenewo? Inde! Yehova anabweretsa miliri yosakaza khumi yokonzekeretsedwa kuchititsa manyazi milungu ya Igupto. Palibe ndi mmodzi yense wa milungu imeneyo anatha kuchinjiriza Aigupto. Ndipo mliri wa 10 unali wodziŵika mwapadera, popeza unapha woyamba kubadwa wa Igupto, kuphatikizapo wa Farao. Uwu unali mliri wachindunji kwa mulungu wawo wamkulu Ra (Amon-Ra), popeza atsogoleri Aigupto anadzilingalira iwo eni kukhala milungu, ana a Ra. Kwa Aigupto, imfa ya mwana woyamba kubadwa wa Farao inatanthauza imfa ya mulungu.
9 Ngakhale kuli tero, palibe ndi mmodzi yense wa ana oyamba kubadwa a Aisrayeli anaphedwa, popeza iwo anali ndi chinjirizo la Yehova. Kachiŵirinso, Mulungu anapatsa anthu ake ufulu umene iye anawalonjeza iwo. Ndipo monga kukantha komalizira ku milungu yonyenga ya Igupto, Farao ndi gulu lake la nkhondo—aliyense wa iwo—anawonongedwa m’Nyanja Yofiira. Chotero, Yehova anatsimikizira kukhala Mulungu wowona. Malonjezo ake anali amene anakwaniritsidwa, ndipo alambiri ake anali amene anatetezeredwa. (Eksodo 14:21-31) Kumbali ina, milungu ya Igupto inali yopanda mphamvu kuthandiza alambiri awo. Milungu imeneyo kunalibe m’chenicheni koma inali kokha zopanga za anthu.
10. Ndi nkhani yotani imene inayang’anizana ndi alambiri a Yehova ndi Asuri?
10 Nkhani ina yokhudza umulungu inawonekera zaka mazana asanu ndi atatu pambuyo pake, m’nthaŵi ya Mfumu Hezekiya.a Alambiri a Yehova anali kuwopsyezedwa ndi Mphamvu Yadziko yowopsya ya Asuri yomwe inali italaka mitundu yonse pa njira yake. Tsopano inalamulira kugonjera kwa Yerusalemu, mzinda umene unali ndi “mpando wachifumu wa Yehova,” kuimira kulambiridwa kwake pa dziko lapansi. (1 Mbiri 29:23) Mfumu ya Yuda, Hezekiya, anazindikira kuti Asuri ‘anasakaza maiko ena onse ndipo kuti anawononga milungu ya m’maiko amenewo mwa kuwatentha ndi moto chifukwa iwo sanali milungu, koma ntchito za manja a munthu.’—Yesaya 37:18, 19.
11. Ndimotani mmene Yehova anapulumutsira alambiri ake, ndipo kodi ichi chinachitira chitsanzo chiyani?
11 Hezekiya wokhulupirika kenaka anapemphera kwa Yehova, kupempha kaamba ka chinjirizo lake. Yehova analonjeza kuti palibe chida cha Asuri chomwe chidzakantha Yerusalemu. (Yesaya 37:33) Mowonadi ku ulosi umenewo, palibe n’chimodzi chonse chinakantha. M’malo mwake, “[m’ngelo NW] wa Yehova anatuluka, naphaipha m’zitando za Asuri, zikwi zana ndi makumi asanu ndi atatu ndi zisanu.” Pambuyo pa kugonjetsedwa kosakaza kumeneko, mfumu ya Asuri, Sanakeribu, anabwerera. Pambuyo pake, pamene iye anali kulambira mulungu wake Nisiroki, ana ake anamupha iye. (Yesaya 37:36-38) Chotero Yehova kachiŵirinso anatsimikizira kukhala Mulungu wa ulosi wowona yemwe angapulumutse alambiri ake. Milungu ya Asuri ndi mitundu yowazinga inatsimikizira kukhala yonyenga, yosakhalako, yosakhoza kutetezera atsatiri awo.
12. Ndi mwanjira yotani mmene Belisazara anasekera Yehova?
12 Chifupifupi zaka mazana aŵiri pambuyo pake, Mulungu analola anthu ake, omwe anakhala osakhulupirika, kutengedwa mu ukapolo ndi mphamvu ya dziko yotsatira, Babulo. Mbali yake yowonekera yaikulu inali unyinji wa milungu, milungu yachikazi, ndi akachisi olambirira. Koma ndi kudzimva kodzikweza, mfumu ya Babulo Belisazara anaseka Yehova. Pa phwando lalikulu, iye analamulira kuti zotengera zopatulika zomwe zinagwidwa kuchokera m’kachisi wa Yerusalemu zibweretsedwe. “Mfumu ndi akulu ake, akazi ake ndi akazi ake ang’ono, amweremo. Anamwa vinyo, nalemekeza milungu ya golidi, ndi ya siliva, ya mkuwa, ya chitsulo, ya mtengo, ndi ya mwala.”—Danieli 5:1-4.
13. Nchiyani chimene Yehova anapangitsa Danieli kunena kwa Belisazara?
13 Ichi chinali chitonzo chachindunji kwa Yehova, chitokoso kwa iye m’dzina la milungu ya Babulo. Yehova kenaka analola mneneri wake Danieli molimba mtima kuchitira umboni kwa Mfumu Belisazara ndi kwa onse omwe analipo pa phwandolo. Danieli anasungilira umulungu wa Yehova ndi kuuza mfumu Belisazara kuti: “Simunadzichepetsa mu mtima mwanu, . . . koma munadzikweza kutsutsana naye Ambuye wa Kumwamba; . . . mwalemekezanso milungu ya siliva, ndi ya golidi, ya mkuwa, ya chitsulo, ya mtengo, ndi ya mwala, imene siiwona, kapena kumva, kapena kudziŵa; ndi Mulungu amene m’dzanja mwake muli mpweya wanu, ndi njira zanu zonse, yemweyo simunamchitira ulemu.”—Danieli 5:22, 23.
14. Ndimotani mmene Yehova anachitira chitsanzo kuti iye anali Mulungu wowona?
14 Kenaka Danieli anapereka uthenga wa Yehova, umene unali wakuti: Mfumu yodzikweza Belisazara ndi Babulo adzagwetsedwa ndi Amedi ndi Aperisi usiku umenewo! (Danieli 5:24-27) Kodi ulosi umenewo unakhala wowona? Inde. “Usiku womwewo Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa. Ndipo Dariyo Mmedi analandira ufumuwo.” (Danieli 5:30, 31) Kachiŵirinso, mofanana ndi Igupto ndi Asuri, Yehova anatsimikizira kukhala Mulungu wowona, Mulungu amene amakwaniritsa malonjezo ake. Atumiki a Mulungu anapindula, popeza iwo anamasulidwa kuchokera ku ukapolo ndi kubwezeretsedwa ku dziko lawo. Awo amene anawumirira kutsatira milungu yonyenga anafika ku tsoka.
Maulosi a Nthaŵi Yathu
15. (a) Ndi mbali yotani imene maulosi ambiri a Baibulo ali nayo? (b) Kodi nkuchiyaninso kumene timalozera pamene tigwiritsira ntchito liwu lakuti “mulungu”?
15 Mneneri Yesaya anauziridwa kulemba maulosi omwe anakwaniritsidwa m’mbuyomo m’nthaŵi zakale. Koma kaŵirikaŵiri mu ulosi wa Baibulo, pamakhala kukwaniritsidwa kwina kwakukulu koyenera kuchita ndi nthaŵi yathu. Iyi inali nkhani ndi zinthu zambiri zimene Yesaya analemba. Mbali ya uthenga wake iri ndi ulosi wonena za chitokoso chamakono cha Yehova kwa mitundu yonse ndi milungu yawo. Ndipo ndi liwu lakuti “milungu” timalozera osati kokha kwa milungu yolambiridwa mwachindunji ndi anthu m’mbali zonse zadziko, kuphatikizapo mitundu yotchedwa yachikunja lerolino, komanso kwa zinthu zomwe zimayenerera tanthauzo la liwu limenelo. Kutanthauzira kumodzi kwa bukhu lotanthauzira mawu kwa liwu lakuti “mulungu” kuli: “Mmodzi wolamulira mbali yapadera kapena mbali ya chenicheni; munthu kapena chinthu chokhala ndi phindu lapamwamba.”
16. Ndi milungu yotani imene anthu amitundu, kuphatikizapo Chikristu cha Dziko amalambira lerolino?
16 Awo amene amawonedwa monga milungu lerolino amaphatikizapo mamiliyoni a milungu yolambiridwa ndi a Hindu, limodzinso ndi iyo yolambiridwa ndi Abuddah, Ashinto, animists, ndi anthu a zipembedzo zina. Imaphatikizaponso mulungu wa kukondetsa zinthu za kuthupi, chomwe chiri chinthu chaphindu lapamwamba kwa anthu ambiri pa dziko lapansi, chisonkhezero chenicheni cha miyoyo yawo. Chimaphatikizaponso milungu ya mphamvu za nkhondo ndi sayansi imene mitundu imayang’anako kaamba ka chisungiko ndi chipulumutso. Kachiŵirinso, anthu ambiri ngakhale m’Chikristu cha Dziko amene amanena kuti amakhulupirira mwa Mulungu iwo m’chenicheni samakhulupirira iye kapena mokhulupirika kutumikira iye, koma m’malo mwake iwo amakhulupirira ndi kutumikira anthu kapena zinthu monga zinthu za kukhulupirika koyambirira.
17. Ndikuti kumene kukwaniritsidwa kokulira kwa uthenga wa Yesaya kumaloza?
17 Kukwaniritsidwa kokulira kwa Yesaya kukulozeredwa kwa milungu yonse yoteroyo m’nthaŵi yathu. Yehova akuuza magulu a mitundu kuzisonkhanitsa iwo pamodzi ndi “kulankhula.” Iye akuwatokosa iwo kuti: “Tiyeni tiyandikire pamodzi kuchiŵeruziro.” (Yesaya 41:1) Lerolino, tikukhala m’nthaŵi ya “chiŵeruzo” kaamba ka dziko lino. Ilo liri “m’masiku ake otsiriza” monga kunanenedweratu pa 2 Timoteo 3:1-5 ndi Mateyu 24:1-14. Pa nthaŵi ino Yehova akutokosa milungu yamitundu kuneneratu molongosoka za mtsogolo ndipo chotero kutsimikizira kuti iyo iri milungu. Iye akuitokosanso iyo kuchinjiriza atsatiri awo ngati ingatero. “Onetsani mlandu wanu,” iye akutero. “Tulutsani zifukwa zanu . . . tiwonetseni ife zinthu zimene zirinkudza.”—Yesaya 41:21, 22.
18. Ndimotani mmene Mulungu wamphamvuyonse amadzizindikiritsira iyemwini, ndipo nchiyani chimene iye akulonjeza alambiri ake?
18 Mulungu wamphamvuyonse akudzizindikiritsa amene iye ali: “Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.” (Yesaya 41:8) Ndipo akuuza awo amene amamusungilira iye kuti: “Usawope, pakuti Ine ndiri pamodzi ndi iwe; usawopsyedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako. Ndidzakulimbitsa, inde, ndidzakuthangata.” Iye akuwalonjeza iwo kuti: “Onse amene akukwiira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa. Iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati chabe, nadzawonongeka.” “Palibe chida chosulidwira iwe chidzapindula . . . Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova.”—Yesaya 41:10, 11; 54:17.
19, 20. (a) Ndimotani mmene Yesaya akusonyezera kuti pali nthaŵi yoikika kaamba ka Yehova ya kulungamitsa zinthu? (b) Ndi ndani amene Yehova akubweretsa kutsogolo “m’masiku otsiriza” ano, ndipo ndimotani mmene iwo akuimira iye?
19 Kwa nthaŵi yaitali, kwa zaka mazana, Yehova walola mitundu kupita m’njira yawoyawo. Komabe, nthaŵi yake yoikidwiratu kaamba ka kulungamitsa zinthu pa dziko lapansi yafika. Chotero iye akulengeza kuti: “Ndakhala nthaŵi yambiri wosalankhula. Ndakhala chete ndi kudzithungata ndekha.” Koma tsopano, “Yehova adzatuluka ngati munthu wamphamvu. Adzautsa nsanje ngati munthu wa nkhondo. Iye adzafuula, inde adzakuwa zolimba; adzachita zamphamvu pa adani ake.” (Yesaya 42:13, 14) M’maulosi a Yesaya ndi olemba Baibulo ena, limodzinso ndi awo a Yesu, Yehova akuneneratu za kuutsa anthu “m’masiku otsiriza” ano kuchitira umboni mwachangu kwa iye, ngati kuti anali mboni m’mlandu wa bwalo la milandu.
20 Anthu amene Yehova amabweretsa kumtumikira iye amapereka chitsimikiziro chakuti iye ali Mulungu wowona, Mpulumutsi wa alambiri ake ndi Msakazi wa milungu yonyenga ndi atsatiri awo. Anthu a Yehova lerolino ‘amaimba chitamando kuchokera ku malekezero a dziko, kuchokera ku mitundu yonse ndi zisumbu, kuchokera pamwamba pa mapiri.’ (Yesaya 42:10-12) Ichi chimakwaniritsa ulosi winanso wa Yesaya umene unaneneratu kuti: “Ndipo padzakhala masiku otsiriza, [m’nthaŵi yathu] . . . kuti phiri la nyumba ya Yehova, [kulambira kwake kowona] lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri, [pamwamba pa mitundu ina yonse ya kulambira]; mitundu yonse [anthu ochokera ku mitundu yonse] idzasonkhana kumeneko.” Ndipo nchiyani chimene iwo akufulumiza ena kuchita? Iwo akuuza owona mtima kuti: “Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, . . . ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira yake, ndipo tidzayenda m’mayendedwe ake.”—Yesaya 2:2-4.
21. Ndi mafunso otani amene akudzutsidwa ndi chitokoso cha Yehova kwa milungu ya mitundu?
21 Chotero, monga ngati kuti akulankhula ku bwalo la milandu, Yehova akunena kuti: “Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane pamodzi. . . . Atenge mboni zawo, kuti avomerezeke [kukhala NW] olungama, pena amve, nanene ‘Nzowonadi!’” (Yesaya 43:9) Ichi ndi chitokoso chachindunji kwa milungu ya mitundu. Kodi iriyonse ya iyo inganene za zimene ziri mtsogolo? Kodi iyo inali yokhoza kunena tero m’nthaŵi zapita? Kodi iyo ingapeze wina aliyense kuchitira umboni ndi chitsimikiziro cholimba chakuti milungu yoteroyo yatsimikizira kukhala yowona, yoyenera chimvero chathu? Ndi mbiri yotani imene milungu ya mitundu, ndi atsatiri awo, yatulutsa m’nthawi yathu? Kodi yakhala yabwinopo kuposa imene milungu ya Igupto wakale, Asuri, ndi Ababulo inatulutsa? Kumbali ina, kodi awo amene achitira umboni kwa Yehova atulutsa chitsimikiziro champhamvu chakuti Yehova ali Mulungu wowona, mmodzi yekha woyenera kulambira kwathu? Nkhani yotsatira idzalongosola nkhani zimenezi.
[Mawu a M’munsi]
a Kope la January 15 la Nsanja ya Olonda linalongosola mmene Yehova anafupira kukhulupirira mwa Iye kwa Hezekiya. Zochitika za chitsanzo zimenezo zinakhudzanso umulungu.
Mafunso Akapendedwe
◻ Ndi iti imene iri nkhani ya ulamuliro wa chilengedwe chonse?
◻ Ndi milungu iti ya mitundu imene ikuloŵetsedwa m’nkhaniyo lerolino?
◻ Ndi chotulukapo chotani cha milandu itatu yoyesa chimene chimasonyeza upamwamba wa Yehova pa milungu yonyenga?
◻ Ndimotani mmene Yesaya akusonyezera kuti Yehova adzalungamitsa zinthu m’tsiku lathu?
◻ Ndi mafunso otani amene akufunikira kuyankhidwa onena za atsatiri a zipembedzo zonse lerolino?
[Chithunzi patsamba 11]
Milungu ya Igupto inali yopanda mphamvu pamaso pa Mulungu wowona, Yehova
[Chithunzi patsamba 12]
Milungu ya Asuri ndi atsatiri awo anasakazidwa ndi Mulungu wowona
[Chithunzi patsamba 13]
Danieli anapereka uthenga wa Yehova kwa alambiri a milungu yonyenga ya Chibabulo