Kodi Maulosi Abaibulo Ngodalirika Motani?
LEROLINO kuli mabuku ambiri a mbiri yakale. Kaŵirikaŵiri zolembedwa zimenezi za zinthu zimene zinachitika kale zimakhala zosangalatsadi. Pamene tikuziŵerenga, timadziyerekezera kukhala tili m’zochitika zamakedzana zimenezo. Kuyerekezera kwathuko kungakule pamene tiwona anthu, malo, ndi zochitikazo pamasamba opanda zithunzithunziwo.
Baibulo ndibuku limenelo—lodzaza ndi zochitika zosangalatsa za mbiri yakale. Kupyolera m’masamba ake, timadziŵa amuna ndi akazi onga Abrahamu, mkazi wake Sara, Mfumu Davide, Mfumukazi Estere, ndi Mphunzitsi Wamkulu, Yesu Kristu. Kwenikwenidi, tingayende nawo, kumva zimene ananena, ndi kuwona zimene anawona. Koma ambiri samawona Baibulo kukhala buku la mbiri yakale yokha. Iwo amakhulupirira kuti lili ndi zimene zatchedwa mbiri yolembedwa pasadakhale. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Baibulo nlodzaza ndi maulosi.
Komabe, kodi maulosi a Baibulo ngodalirika motani? Ngati maulosi Abaibulo anakwaniritsidwa m’zochitika zakale, kodi sitiyenera kuyembekeza kuti maulosi oterowo onena za zochitika za mtsogolo adzakwaniritsidwa? Tsopano tiyeni tipende zina za zitsanzo zimenezo kuwona ngati maulosi Abaibulo ali odalirika.
Israyeli ndi Asuri m’Zochitika za Dziko
Yesaya, mneneri wa Mulungu, amene anayamba kulosera pafupifupi 778 B.C.E., ananeneratu kuti: “Korona wakunyada wa oledzera a Efraimu [Israyeli] adzaponderezedwa; ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene lili pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiwona wakupenya imeneyo, amaidya ili m’dzanja lake.” (Yesaya 28:3, 4) Monga kunaloseredwa, pofika pakati pa zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., Samariya, likulu la Israyeli, linakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha yokonzeka kuthyoledwa ndi kudyedwa ndi magulu ankhondo a Asuri. Zimenezo ndizo zinachitika pamene Samariya anagonjetsedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E.—2 Mafumu 17:6, 13, 18.
M’kupita kwanthaŵi inafika nthaŵi yakuti Asuri alembedwe m’mbiri. Likulu lake linali Nineve, wokhala ndi mbiri yoipa ya kuchitira nkhanza akapolo kotero kuti anatchedwa “mudzi wa mwazi.” (Nahumu 3:1) Yehova Mulungu iyemwini analamula za kuwonongedwa kwa Nineve. Mwachitsanzo, kudzera mwa mneneri Nahumu, Mulungu anati: “Tawona, nditsutsana nawe, . . . [ndidza]kuchititsa manyazi, ndi kukuika chopenyapo. Ndipo kudzali kuti onse akupenyerera iwe adzakuthaŵa, nadzati, Nineve wapasuka.” (Nahumu 3:5-7) Nayenso Zefaniya ananeneratu za chiwonongeko cha Asuri ndi kupasulidwa kwa Nineve. (Zefaniya 2:13-15) Maulosi ameneŵa anakwaniritsidwa mu 632 B.C.E., pamene, modabwitsa, magulu ankhondo ophatikizana a Nabopolassar mfumu ya Babulo ndi a Cyaxares Mmedi anafunkha ndi kupasula Nineve—kotheratu kotero kuti ngakhale malo a mzindawo anakhala osadziŵika kwa zaka zoposa 2,000. Ufumu wa Babulo unali wotsatira m’zochitika za dziko.
Kuwonongedwa kwa Babulo Kuloseredwa
Baibulo linalosera kuti ufumu wa Babulo ukagwetsedwa ndipo linaneneratu mmene mzinda wake waukulu, Babulo, ukagwera. Pafupifupi zaka mazana aŵiri pasadakhale, mneneri Yesaya anachenjeza kuti mtsinje wa Firate ukaphwa. Mtsinjewo unkadutsa mkati mwa Babulo, ndipo zipata za m’mphepete mwa mtsinjewo zinali mbali yofunika ya chitetezo cha mzindawo. Ulosiwo unatchula Koresi monga wogonjetsayo ndipo unanena kuti “zitseko” za Babulo sizidzatsekedwera oukirawo. (Yesaya 44:27–45:7) Motero, Mulungu anatsimikizira kuti zitseko za Babulo zokhala m’mphepete mwa Firate zinasiyidwa zotsegula mkati mwa phwando pa usiku umene magulu ankhondo a Koresi Wamkulu anaukira. Chotero, iwo analoŵa mumzindamo mosavutika mwakuoloka mtsinjewo ndipo analanda Babulo.
Wolemba mbiri yakale Herodotus anati: “Koresi . . . anaika mbali ina ya gulu lake lankhondo pamalo amene Firate amaloŵera mu [Babulo] ndiyeno gulu lina kumbali ina kumene umatulukira, atalamula magulu aŵiri onsewo kuoloka mtsinjewo mwamsanga madziwo ataphwa. . . . Mwakukumba ngalande iye anapatutsira mtsinjewo ku nyanja (yomwe panthaŵiyo inali thaŵale) ndipo mwanjirayi anachepetsa kwambiri kuya kwa madzi amene anali m’mtsinjewo kotero kuti unakhala wokhoza kuolokeka, ndipo gulu lankhondo la Perisiya, limene linatsala ku Babulo kaamba ka chifuno chimenecho, linaloŵa mumtsinjemo, womwe tsopano unali ndi madzi ongofika m’ntchafu za munthu, ndipo, akumayenda m’mphepete mwake, anakaloŵa m’tauniyo. . . . Phwando linali mkati, ndipo ngakhale pamene mzindawo unali kugwa iwo anapitiriza kuvina ndi kusangalala, kufikira pamene anazindikira zimene zinali kuchitika.”—Herodotus—The Histories, lotembenuzidwa ndi Aubrey de Selincourt.
Usiku umenewo, mneneri wa Mulungu Danieli anachenjeza wolamulira wa Babulo za tsoka loyandikiralo. (Danieli, chaputala 5) Babulo wopanda mphamvu kwenikweni anakhalako kwa zaka mazana angapo pambuyo pake. Mwachitsanzo, mtumwi Petro analemba kalata yake yoyamba youziridwa ali kumeneko m’zaka za zana loyamba C.E. (1 Petro 5:13) Koma ulosi wa Yesaya udanena kuti: “Babulo . . . adzakhala monga momwe Mulungu anapasula Sodomu ndi Gomora. Anthu sadzakhalamo konse.” Mulungu ananenanso kuti: “[Ndidza]wononga ku Babulo dzina ndi otsala, ndi mwana wamwamuna, ndi chidzukulu chachimuna.” (Yesaya 13:19-22; 14:22) Monga kunaloseredwa, pomalizira pake Babulo anakhala bwinja. Kuyesayesa kuumanganso mzinda wamakedzanawo kungakope alendo koma kungausiyebe wopanda “mwana wamwamuna ndi chidzukulu chachimuna.”
Danieli—mneneri wa Yehova amene analipo pamene Babulo anagwa—anawona masomphenya onena za Amedi ndi Aperesi olakikawo. Iye anawona nkhosa yamphongo yanyanga ziŵiri ndi tonde amene anali ndi nyanga yaikulu pakati pa maso ake. Mbuziyo inaukira nkhosa yamphongoyo niikantha, nithyola nyanga zake ziŵirizo. Ndiyeno nyanga yaikulu ya mbuziyo inathyoka, ndipo nyanga zinayi zinamera m’malo mwake. (Danieli 8:1-8) Monga momwe Baibulo linaloserera ndipo mbiri yakale yatsimikizira nkhaniyo, nkhosa yamphongo yanyanga ziŵiriyo inaimira Mediya ndi Perisiya. Tondeyo anaimira Girisi. Ndipo bwanji za “nyanga . . . yaikulu” imeneyo? Imeneyi inatsimikizira kukhala Alexander Wamkulu. Pamene nyanga yaikulu yophiphiritsirayo inathyoka, nyanga zinayi zophiphiritsira (kapena, maufumu) zinailoŵa m’malo. Mogwirizanadi ndi ulosiwo, Alexander atafa, anayi a akazembe ake anadzitengera okha ulamuliro—Ptolemy Lagus analamulira Igupto ndi Palestina; Seleucus Nicator ku Mesopotamiya ndi Suriya; Cassander ku Makedoniya ndi Girisi; ndipo Lysimachus ku Thrace ndi Asia Minor.—Danieli 8:20-22.
Maulosi a Mtsogolo Mwabwino
Maulosi Abaibulo onena za zochitika zoterozo monga kupasulidwa kwa Babulo ndi kugwetsedwa kwa Mediya ndi Perisiya ali kokha zitsanzo za maulosi ambiri Amalemba amene anakwaniritsidwa kalelo. Baibulo lilinso ndi maulosi a mtsogolo mwabwino amene angakwaniritsidwe chifukwa cha Mesiya, Wodzozedwa wa Mulungu.
Maulosi ena Aumesiya a Malemba Achihebri anagwiritsiridwa ntchito pa Yesu Kristu ndi olemba Malemba Achikristu Achigiriki. Mwachitsanzo, olemba Mauthenga Abwino anasonyeza kuti Yesu anabadwira ku Betelehemu, monga kunanenedweratu ndi mneneri Mika. (Mika 5:2; Luka 2:4-11; Yohane 7:42) Pakukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yeremiya, ana anaphedwa pambuyo pa kubadwa kwa Yesu. (Yeremiya 31:15; Mateyu 2:16-18) Mawu a Zekariya (9:9) anakwaniritsidwa pamene Kristu analoŵa m’Yerusalemu atakwera mwana wa bulu. (Yohane 12:12-15) Ndipo pamene asilikali anagaŵana zovala za Yesu pambuyo pa kupachikidwa kwake, zimenezi zinakwaniritsa mawu a wamasalmo akuti: “Agaŵana zovala zanga, nalota maere pa malaya anga.”—Salmo 22:18.
Maulosi ena Aumesiya amasonya ku nthaŵi yachimwemwe ya mtundu wa anthu. M’masomphenya, Danieli anawona “wina ngati mwana wa munthu” akulandira “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu” kuchokera kwa Yehova, “Nkhalamba ya kale lomwe.” (Danieli 7:13, 14) Ponena za ulamuliro Waumesiya wa Mfumu yakumwamba imeneyo, Yesu Kristu, Yesaya analengeza kuti: “Adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere. Za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha pa mpando wachifumu wa Davide, ndi pa ufumu wake, kuukhazikitsa, ndi kuuchilikiza ndi chiweruziro ndi chilungamo kuyambira tsopano ndi kumkabe nthaŵi zonse. Changu cha Yehova wa makamu chidzachita zimenezi.”—Yesaya 9:6, 7.
Ulamuliro wolungama wa Mesiya usanayambe kulamulira kotheratu, chinachake chofunika koposa chiyenera kuchitika. Chimenechinso chinaloseredwa m’Baibulo. Ponena za Mfumu Yaumesiyayo, wamasalmo anaimba kuti: “Dzimangireni lupanga lanu m’chuuno mwanu, wamphamvu inu . . . Ndipo pindulani, m’ukulu wanu yendani, kaamba ka chowonadi ndi chifatso ndi chilungamo.” (Salmo 45:3, 4) Posonya ku tsiku lathu, Malemba ananeneratunso kuti: “Ndipo masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiyidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.”—Danieli 2:44.
Salmo 72 limaneneratu za mikhalidwe ya muulamuliro Waumesiya. Mwachitsanzo, “masiku ake wolungama adzakhazikika; ndi mtendere wochuluka, kufikira sipadzakhala mwezi.” (Vesi 7) Pamenepo sikudzakhala kupondereza kapena chiwawa. (Vesi 14) Palibe amene adzakhala ndi njala, popeza kuti “m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.” (Vesi 16) Ndipo tangoyerekezerani! Mungasangalale ndi zimenezi ndi madalitso ena padziko lapansi laparadaiso pamene dongosolo lazinthu lilipoli lidzaloŵedwa m’malo ndi dziko latsopano lolonjezedwa la Mulungu.—Luka 23:43; 2 Petro 3:11-13; Chivumbulutso 21:1-5.
Pamenepotu, mufunikira kusanthula maulosi Abaibulo. Chifukwa chake, bwanji osafunsa Mboni za Yehova kuti mudziŵe zochuluka? Kusanthula maulosi Abaibulo kungakuthandizeni kuzindikira nthaŵi imene tikukhalamo. Kungakulitsenso mumtima mwanu chiyamikiro chakuya kaamba ka Yehova Mulungu ndi kakonzedwe kake kabwino koposa ka madalitso amuyaya kwa onse amene amamkonda iye ndi kumumvera.
[Chithunzi patsamba 5]
Kodi mumadziŵa tanthauzo la masomphenya a Danieli onena za tonde ndi nkhosa yamphongo?
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi mudzakhalapo kuti mudzasangalale ndi kukwaniritsidwa kwa maulosi Abaibulo onena za moyo wachimwemwe padziko lapansi laparadaiso?