Kuphunzitsidwa ndi Yehova Mpaka Lero
“Yehova wandipatsa ine lilime la ophunzira.”—YESAYA 50:4.
1, 2. (a) Kodi Yehova anakonzekeretsera wophunzira wake wapamtima kaamba ka chiyani, ndipo chotulukapo chinali chotani? (b) Kodi Yesu anasonyeza motani Magwero a ziphunzitso zake?
YEHOVA MULUNGU wakhala Mphunzitsi chiyambire pamene anakhala Atate. Patapita nthaŵi kuchokera pamene ana ake ena anapanduka, iye anakonzekeretsa wophunzira wake wapamtima, Mwana wake Woyamba, kaamba ka utumiki pa dziko lapansi. (Miyambo 8:30) Yesaya chaputala 50 akusonyeza mwaulosi wophunzira ameneyu kukhala akunena kuti: “Ambuye Yehova wandipatsa ine lilime la ophunzira, kuti ndidziŵe kunena mawu akuchirikiza iye amene ali wolema.” (Yesaya 50:4) Chifukwa cha kugwiritsira ntchito chiphunzitso cha Atate wake pamene anali pa dziko lapansi, Yesu anali wotonthoza kwa onse amene anali “akulema ndi akuthodwa.”—Mateyu 11:28-30.
2 Yesu anachita zamphamvu zambiri m’zaka za zana loyamba. Anatsegula maso a akhungu ndi kuukitsanso akufa, komabe iye anadziŵika kwambiri monga mphunzitsi kwa anthu apanthaŵiyo. Otsatira ake limodzinso ndi omtsutsa anamutcha motero. (Mateyu 8:19; 9:11; 12:38; 19:16; Yohane 3:2) Yesu sanadzitame ndi zimene anaphunzitsa koma anati modzichepetsa: “Chiphunzitso changa sichili changa, koma cha iye amene anandituma ine.” “Monga anandiphunzitsa Atate, ndilankhula izi.”—Yohane 7:16; 8:28; 12:49.
Unansi Wabwino wa Mphunzitsi ndi Wophunzira
3. Kodi ulosi wa Yesaya umasonyeza motani chidwi cha Yehova mwa aja amene iye amaphunzitsa?
3 Mphunzitsi wabwino koposa amasonyeza chidwi chaumwini, chamtima wonse, ndi chachikondi mwa ophunzira ake. Yesaya chaputala 50 amasonyeza kuti Yehova Mulungu ali ndi chidwi chotero mwa aja amene amaphunzitsa. “Andigalamutsa mmaŵa ndi mmaŵa,” umatero ulosiwo, “nagalamutsa khutu langa kuti limve monga ophunzira.” (Yesaya 50:4) Panopa mawu ake akusonyeza mlangizi amene amagalamutsa ophunzira ake mmamaŵa kuti awaphunzitse. Pothirira ndemanga pa tanthauzo la ulosiwo, katswiri wina wa Baibulo anati: “Lingaliro lake nlakuti, Momboliyo adzakhala . . . munthu amene anali pasukulu ya Mulungu, titero kunena kwake; ndi amene adzakhala wokhoza kupereka malangizo kwa ena. . . . Mesiya anali wokhoza kwambiri, mwa kuphunzitsidwa ndi Mulungu, kukhala mlangizi wa anthu.”
4. Kodi Yesu analabadira motani chiphunzitso cha Atate wake?
4 Ophunzira amalabadira bwino lomwe chiphunzitso cha mphunzitsi wawo. Kodi Yesu analabadira motani chiphunzitso cha Atate wake? Kulabadira kwake kunali kogwirizana ndi zimene timaŵerenga pa Yesaya 50:5 kuti: “Ambuye Yehova watsegula khutu langa, ndipo sindinakhala wopanduka ngakhale kubwerera m’mbuyo.” Inde, Yesu anali wofunitsitsa kuphunzira. Anali wotchera khutu kwambiri. Ndiponso, anali wokonzekera kuchita zonse zimene Atate wake anampempha. Sanali wopanduka; m’malo mwake, anati: “Sikufuna kwanga ayi, komatu kwanu kuchitike.”—Luka 22:42.
5. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Yesu anadziŵa pasadakhale mavuto omwe anadzakumana nawo pa dziko lapansi? (b) Kodi ulosi wa Yesaya 50:6 unakwaniritsidwa motani?
5 Ulosiwo umasonyeza kuti Mwanayo anauzidwa za zotulukapo zomwe zikanakhalapo pa kuchita kwake chifuniro cha Mulungu. Zimenezi zikusonyezedwa ndi zimene wophunzirayo akunena: “Ndinapereka msana wanga kwa omenya, ndi masaya anga kwa iwo amene anakudzula tsitsi langa; sindinabisira nkhope yanga manyazi ndi kulavulidwa.” (Yesaya 50:6) Monga momwe ulosiwo ukusonyezera, Yesu anachitiridwa nkhanza pa dziko lapansi. “Anathira malovu pankhope pake,” analemba motero mtumwi Mateyu. “Ena anampanda khofu.” (Mateyu 26:67) Amene anachita zimenezi anali atsogoleri achipembedzo pa usiku wa Paskha wa 33 C.E. Tsiku lotsatira Yesu anapereka msana wake kwa omenya, pamene asilikali Achiroma anampanda mwankhalwe asanampachike pamtengo kuti afe.—Yohane 19:1-3, 16-23.
6. Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti Yesu sanataye chidaliro mwa Mphunzitsi wake, ndipo chidaliro chake chinafupidwa motani?
6 Mwanayo, wophunzitsidwa bwino pasadakhale, sanataye chidaliro mwa Mphunzitsi wake. Zimenezi zikusonyezedwa ndi zimene akunenanso malinga ndi ulosiwo: “Ambuye Yehova adzandithangata ine; chifukwa chake sindinasokonezedwa.” (Yesaya 50:7) Chidaliro cha Yesu mwa thandizo la Mphunzitsi wake chinafupidwa kwakukulu. Atate wake anamkweza, kumdalitsa ndi malo apamwamba kuposa aja a atumiki onse a Mulungu. (Afilipi 2:5-11) Nafenso madalitso aakulu akutiyembekezera malinga ngati timamatira momvera ku chiphunzitso cha Yehova ndi ‘kusabwerera m’mbuyo.’ Tiyeni tipende mmene chiphunzitso chimenecho chaperekedwera kufikira tsiku lathu.
Programu Yofutukuka ya Kuphunzitsa
7. Kodi Yehova waperekabe motani chiphunzitso chake pa dziko lapansi?
7 Monga momwe taonera kale, Yehova anagwiritsira ntchito Woimira wake wa pa dziko lapansi, Yesu Kristu, kupereka chiphunzitso chaumulungu m’zaka za zana loyamba. (Yohane 16:27, 28) Yesu nthaŵi zonse anasonyeza Mawu a Mulungu monga ulamuliro wa chiphunzitso chake, akumaikira chitsanzo aja omwe anaphunzitsa. (Mateyu 4:4, 7, 10; 21:13; 26:24, 31) Pambuyo pake, chiphunzitso cha Yehova chinaperekedwabe pa dziko lapansi mwa utumiki wa ophunzitsidwa amenewo. Kumbukirani kuti Yesu anawalamulira kuti: “Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu a mitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.” (Mateyu 28:19, 20) Pamene anapanga ophunzira, iwo anakhala mbali ya “nyumba ya Mulungu . . . [mpingo, NW] wa Mulungu wamoyo.” (1 Timoteo 3:15) Mwa iwonso mipingo yosiyanasiyana inapangidwa kumene anaphunzitsidwa ndi Yehova. (Machitidwe 14:23; 15:41; 16:5; 1 Akorinto 11:16) Kodi chiphunzitso chaumulungu chapitiriza mwanjira imeneyo mpaka tsiku lathu?
8. Kodi Yesu anasonyeza motani njira imene ntchito yolalikira idzatsogozedwera pa dziko lapansi mapeto asanadze?
8 Inde, chatero! Masiku atatu Yesu asanafe, iye ananeneratu kuti mapeto a dongosolo ili la zinthu asanafike, padzakhala ntchito yaikulu yolalikira. “Uthenga uwu wabwino wa ufumu udzalalikidwa pa dziko lonse lapansi, ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse; ndipo pomwepo chidzafika chimaliziro.” Yesu anapitiriza kufotokoza bungwe limene lidzatsogolera programu ya padziko lonse yolalikira ndi ya kuphunzitsa imeneyi. Analankhula za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amene adzakhala njira, kapena chiŵiya, choperekera chakudya chauzimu kwa atumiki Ake. (Mateyu 24:14, 45-47) Yehova Mulungu wagwiritsira ntchito “kapolo” ameneyu kuyang’anira zinthu za Ufumu pa dziko lonse lapansi.
9. Kodi amene amapanga kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ndani?
9 Lerolino, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru wapangidwa ndi otsalira a oloŵa Ufumu. Ameneŵa ndi Akristu odzozedwa, otsalira pa dziko lapansi a 144,000, amene ‘ali a Kristu,’ amenenso ali mbali ya “mbewu ya Abrahamu.” (Agalatiya 3:16, 29; Chivumbulutso 14:1-3) Kodi mungamdziŵe motani kapolo wokhulupirika ndi wanzeru? Makamaka mwa ntchito imene amachita ndi kumamatira kwawo zolimba ku Mawu a Mulungu, Baibulo.
10. Kodi ndi ziŵiya ziti zimene zikugwiritsiridwa ntchito ndi kagulu ka kapolo kuchirikiza ziphunzitso za Yehova?
10 Yehova akugwiritsira ntchito “kapolo” ameneyu monga njira yake yophunzitsira anthu lerolino. Akagulu ka kapolowo anatenga dzina lakuti Mboni za Yehova mu 1931. Chiyambire pamenepo anthu mamiliyoni ambiri agwirizana nawo ndipo alandira dzinalo nagwirizana nawo pa kulengeza Ufumu wa Mulungu. Magazini ano, a Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova, ali chiŵiya chachikulu chogwiritsiridwa ntchito ndi “kapolo” pa ntchito yophunzitsa. Komabe, zofalitsa zinanso zikugwiritsiridwa ntchito, kuphatikizapo mabuku, timabuku, mabrosha, matrakiti, ndi magazini a Galamukani!
11. Kodi ndi sukulu zotani zimene “kapolo” wakonza, ndipo iliyonse ya sukulu zimenezi ili ndi cholinga chotani?
11 Ndiponso, “kapolo” ameneyo amakonza sukulu zosiyanasiyana. Zimenezi zimaphatikizapo Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower, imene ili kosi ya miyezi isanu imene imakonzekeretsa atumiki achinyamata kaamba ka utumiki waumishonale kumaiko akutali, ndi kosi ya miyezi iŵiri ya Sukulu Yophunzitsa Utumiki, imene imaphunzitsa akulu ndi atumiki otumikira osakwatira ntchito zapadera zateokrase. Palinso Sukulu Yautumiki Waufumu, imene nthaŵi ndi nthaŵi imalangiza akulu Achikristu ndi atumiki otumikira za mathayo awo ampingo, ndi Sukulu Yautumiki Waupainiya, imene imakonzekeretsa alaliki anthaŵi yonse kukhala ogwira mtima kwambiri pantchito yawo yolalikira.
12. Kodi mbali ya mlungu ndi mlungu ya programu ya kuphunzitsa njotani?
12 Mbali ina ya programu ya kuphunzitsa ndiyo misonkhano isanu ya mlungu ndi mlungu yochitika m’mipingo yoposa 75,500 ya anthu a Yehova padziko lonse. Kodi mumapindula kwambiri ndi misonkhano imeneyi? Mwa kutchera khutu kwanu ku malangizo operekedwa, kodi mumasonyeza kuti mumakhulupiriradi kuti mophiphiritsira muli pasukulu ya Mulungu? Kodi kupita kwanu patsogolo kumasonyeza ena mosavuta kuti muli ndi “lilime la ophunzira”?—Yesaya 50:4; 1 Timoteo 4:15, 16.
Kuphunzitsidwa pa Misonkhano ya Mpingo
13. (a) Kodi njira yaikulu imene Yehova akuphunzitsira anthu ake lerolino njotani? (b) Kodi tingasonyeze motani chiyamikiro chathu kaamba ka Nsanja ya Olonda?
13 Yehova makamaka amaphunzitsa anthu ake kupyolera m’phunziro la Baibulo lamlungu ndi mlungu mwa kugwiritsira ntchito Nsanja ya Olonda monga chothandizira kuphunzira. Kodi mumaona msonkhano umenewu kukhala malo kumene mungaphunzitsidwe ndi Yehova? Ngakhale kuti Yesaya 50:4 amanena makamaka za Yesu, angakhudzenso onse amene amagwiritsira ntchito makonzedwe a Mulungu olandirira “lilime la ophunzira.” Njira imene mungasonyezere kuti mumayamikira Nsanja ya Olonda ndi mwa kuŵerenga kope lililonse mutangolilandira. Ndiyeno, pamene Nsanja ya Olonda iphunziridwa pampingo, mungasonyeze chiyamikiro chanu kwa Yehova mwa kupezekapo ndiponso mwa kukhala wokonzekera kupereka chilengezo chapoyera cha chiyembekezo chanu.—Ahebri 10:23.
14. (a) Kodi nchifukwa ninji kuyankha pamisonkhano yotero kuli mwaŵi waukulu kwambiri? (b) Kodi ndi mayankho otani a achichepere amene ali olimbikitsa koposa?
14 Kodi mumazindikira kuti mwa mayankho anu pamisonkhano, mungakhale ndi mbali m’programu yaikulu ya kuphunzitsa ya Yehova? Ndithudi, kuyankha pamisonkhano kuli njira yaikulu imene tingafulumizirane “ku chikondano ndi ntchito zabwino.” (Ahebri 10:24, 25) Kodi nawonso ana angakhale ndi mbali m’programu ya malangizo imeneyi? Inde, angatero. Kaŵirikaŵiri mayankho ochokera mumtima operekedwa ndi ana amalimbikitsa achikulire. Nthaŵi zina, achatsopano opezeka pamisonkhano yathu asonkhezeredwa ndi mayankho a ana kukhala ndi chidwi chachikulu cha choonadi cha Baibulo. Achichepere ena amakonda kuŵerenga mayankho awo m’ndime kapena kubwereza zimene wachikulire awanong’oneza m’khutu. Komabe, kumakhala kolimbikitsa kwambiri pamene mayankho awo awakonzekera bwino. Kuyankha koteroko kumalemekezadi Mlangizi wathu Wamkulu ndi programu yake yokwezeka ya kuphunzitsa.—Yesaya 30:20, 21.
15. Kodi makolo angachitenji kuthandiza ana kuyankha mogwira mtima?
15 Kumasangalatsa kuona ana akufuna kutamanda Mulungu wathu. Yesu anayamikira mawu achitamando ochokera kwa ana. (Mateyu 21:15, 16) Mkulu wina Wachikristu akuti: “Pamene ndinali mwana, ndinafuna kuyankha pa Phunziro la Nsanja ya Olonda. Atandithandiza kukonzekera yankho, atate anali kundiuza kuyeseza yankholo kosachepera kasanu ndi kaŵiri.” Mwinamwake paphunziro lanu labanja la Baibulo, makolonu mungathandize ana anu kukonzekera mayankho m’mawu awoawo pa ndime zosankhidwa mu Nsanja ya Olonda. Athandizeni kuyamikira mwaŵi waukulu umene ali nawo wa kukhala ndi phande m’programu ya kuphunzitsa ya Yehova.
16. Kodi phindu la Sukulu Yautumiki Wateokratiki lakhala lotani, ndipo ndani ayenera kulembetsa sukuluyo?
16 Chiphunzitso pamisonkhano ina Yachikristu chiyeneranso kuonedwa kukhala chofunika kwambiri ndi aja okhala ndi mwaŵi wakupereka chidziŵitsocho ndiponso omvetsera malangizo operekedwawo. Kwa zaka zoposa 50 tsopano, Yehova wagwiritsira ntchito Sukulu Yautumiki Wateokratiki kuphunzitsa amuna ndi akazi mamiliyoni ambiri kulalikira uthenga wa Ufumu mogwira mtima kwambiri. Awo amene akugwirizana mokangalika ndi mpingo angalembetse, kuphatikizapo anthu amene angoyamba posachedwapa kupezeka pamisonkhano, malinga ngati ali ndi moyo wogwirizana ndi malamulo Achikristu.
17. (a) Kodi Msonkhano Wapoyera unakhazikitsidwa makamaka ndi cholinga nchotani? (b) Kodi ndi zinthu zotani zimene alankhuli apoyera ayenera kukumbukira?
17 Mbali ina ya programu ya kuphunzitsa imene yakhalako kwa nthaŵi yaitali ndiyo Msonkhano Wapoyera. Malinga ndi dzina lake, msonkhanowu unakhazikitsidwa makamaka kuthandiza osakhala Mboni kudziŵa ziphunzitso za Baibulo. Chotero, wopereka nkhaniyo afunikira kupereka chidziŵitsocho mwanjira yomveka kwa omvetsera uthengawo nthaŵi yoyamba. Zimenezi zikutanthauza kufotokoza mawu ena, monga akuti “nkhosa zina,” “abale,” ndi “otsalira,” mawu amene anthu omwe sali Mboni sangawadziŵe. Popeza kuti opezeka pa Msonkhano Wapoyera angakhale ndi zikhulupiriro kapena makhalidwe osiyana kwambiri ndi Malemba—ngakhale kuti ali olandirika m’dziko lamakono—mlankhuliyo ayenera kusamala nthaŵi zonse ndipo sayenera kunyoza zikhulupiriro kapena makhalidwe otero.—Yerekezerani ndi 1 Akorinto 9:19-23.
18. Kodi ndi misonkhano ina iti ya mlungu ndi mlungu imene ilipo, ndipo zolinga zake nzotani?
18 Phunziro Labuku Lampingo uli msonkhano pamene zofalitsa zokonzedwa pansi pa chitsogozo cha kapolo wokhulupirika ndi wanzeru zimaphunziridwa mlungu uliwonse pamodzi ndi Baibulo. Buku lakuti Revelation—Its Grand Climax At Hand! ndilo limene likuphunziridwa pakali pano m’maiko ambiri. Msonkhano Wautumiki wakonzedwera kukonzekeretsa anthu a Yehova kuchita mokwanira ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi kupanga ophunzira.—Mateyu 28:19, 20; Marko 13:10.
Kuphunzitsidwa pa Misonkhano Yaikulu
19. Kodi ndi misonkhano iti yaikulu imene “kapolo” amakonza chaka ndi chaka?
19 Kwa zaka zoposa zana limodzi, “kapolo wokhulupirika” wakonza misonkhano yachigawo ndi yadera yophunzitsa Akristu oona ndi kuwapatsa chilimbikitso chapadera. Misonkhano itatu yotero imachitika chaka chilichonse tsopano. Pali msonkhano wa tsiku limodzi umene mipingo ingapo yopanga dera imapitako. M’chaka chimodzimodzicho, dera lililonse limakhala ndi msonkhano wa masiku aŵiri wotchedwa msonkhano wadera. Ndiponso, pali msonkhano wina wotchedwa msonkhano wachigawo, umene madera angapo amapitako. Zaka zina pamakhala misonkhano ya mitundu yonse. Misonkhano yaikulu imeneyi yokhala ndi Mboni zachilendo za kumaiko ambiri imalimbitsadi chikhulupiriro cha anthu a Yehova!—Yerekezerani ndi Deuteronomo 16:16.
20. Kodi nchiyani chimene chagogomezeredwa nthaŵi zonse pamisonkhano yaikulu ya Mboni za Yehova?
20 Mu 1922, pamene pafupifupi anthu 10,000 anasonkhana ku Cedar Point, Ohio, U.S.A., nthumwi zinasonkhezeredwa ndi chilimbikitso cha mlankhuli kuti: “Lino ndilo tsiku la masiku onse. Taonani, Mfumu ikulamulira! Inu ndinu oimira ake olengeza. Chifukwa chake lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake.” Misonkhano yaikulu yotero nthaŵi zonse yagogomezera ntchito yolalikira. Mwachitsanzo, pamsonkhano wa mitundu yonse ku New York City mu 1953, panaperekedwa chilengezo cha kuyamba kwa programu yophunzitsa ulaliki wa kunyumba ndi nyumba m’mipingo yonse. Kuitsatira kunathandizira kwambiri kulalikidwa kwa Ufumuwo m’maiko ambiri.
Kuphunzitsidwa ndi Mulungu Kuti Tiphunzitse Ena
21. Kodi ndi mwaŵi wotani umene tiyenera kulandira, mosaphonya cholinga chake?
21 Ndithudi, Yehova ali ndi programu yabwino kwambiri ya kuphunzitsa pa dziko lapansi lerolino! Onse amene amaigwiritsira ntchito bwino angaphunzitsidwe ndi Mulungu, inde, angakhale pakati pa amene apatsidwa “lilime la ophunzira.” Ndi mwaŵi wotani nanga kukhala pasukulu yophiphiritsira ya Mulungu! Komabe, polandira mwaŵi umenewu, sitiyenera kuphonya cholinga chake. Yehova anaphunzitsa Yesu kuti iye aphunzitse ena, ndipo Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti iwo achite ntchito imodzimodziyo imene iye anali kuchita komano pamlingo wokulirapo. Mofanana ndi zimenezo, Yehova akutiphunzitsa paprogramu yaikulu ya kuphunzitsa ndi cholinga chakuti tiphunzitse ena.—Yohane 6:45; 14:12; 2 Akorinto 5:20, 21; 6:1; 2 Timoteo 2:2.
22. (a) Kodi Mose ndi Yeremiya anali ndi vuto lotani, koma linatha bwanji? (b) Kodi tingakhale ndi chidaliro chotani chakuti Mulungu adzatsimikizira kuti kulalikidwa kwa Ufumu kwachitika?
22 Kodi mumanena monga Mose kuti, “Ndine munthu wosoŵa ponena,” kapena monga momwe Yeremiya ananenera kuti, “Sindithayi kunena”? Yehova adzakuthandizani monga momwe anawathandizira iwo. Iye anauza Mose kuti, “Ine ndidzakhala m’kamwa mwako.” Ndipo kwa Yeremiya anati: “Usawope . . . ine ndili ndi iwe.” (Eksodo 4:10-12; Yeremiya 1:6-8) Pamene atsogoleri achipembedzo anafuna kuletsa atumwi ake kulankhula, Yesu anati: “Ngati aŵa akhala chete miyala idzafuula.” (Luka 19:40) Koma miyalayo sinafuule nthaŵiyo, ndipo siiyenera kutero lero chifukwa Yehova akugwiritsira ntchito lilime la ophunzira ake kupereka uthenga wake wa Ufumu.
Kodi Mungayankhe?
◻ Kodi ndi unansi wabwino wotani wa Mphunzitsi ndi wophunzira wake umene ukusonyezedwa mu chaputala 50 cha Yesaya?
◻ Kodi Yehova wapereka motani programu yaikulu ya kuphunzitsa?
◻ Kodi mbali zina za programu ya kuphunzitsa ya Yehova nzotani?
◻ Kodi nchifukwa ninji uli mwaŵi waukulu kukhala ndi phande m’programu ya kuphunzitsa ya Yehova?
[Chithunzi patsamba 16]
Kaŵirikaŵiri mayankho a ana ochokera mumtima amalimbikitsa achikulire