Yehova—Mulungu Amene Amaphunzitsa
“Adzakhala onse ophunzitsidwa ndi [Yehova, NW].”—YOHANE 6:45.
1. Kodi Yesu tsopano akuchitanji ku Kapernao?
YESU KRISTU wangochita kumene zozizwitsa ndipo tsopano akuphunzitsa m’sunagoge ku Kapernao, pafupi ndi Nyanja ya Galileya. (Yohane 6:1-21, 59) Ambiri akudabwa pamene iye akunena kuti: “Ndinatsika kumwamba.” Iwo akung’ung’udza kuti: “Si Yesu uyu, mwana wa Yosefe, atate wake ndi amayi wake tiwadziŵa? Anena bwanji tsopano kuti, Ndinatsika kumwamba?” (Yohane 6:38, 42) Powadzudzula, Yesu akuti: “Kulibe mmodzi akhoza kudza kwa ine koma ngati Atate wondituma ine amkoka iye; ndipo ine ndidzamuukitsa iye tsiku lomaliza.”—Yohane 6:44.
2. Kodi pali chifukwa chotani chokhulupirira lonjezo la Yesu la chiukiriro?
2 Ndi lonjezo labwino chotani nanga limenelo—kuukitsidwa tsiku lomaliza, pamene Ufumu wa Mulungu ulamulira! Tingakhulupirire lonjezo limeneli chifukwa chakuti likuchirikizidwa ndi Atate, Yehova Mulungu. (Yobu 14:13-15; Yesaya 26:19, NW) Inde, Yehova, yemwe amaphunzitsa kuti akufa adzauka, ali “mphunzitsi wamkulu pa onse.” (Yobu 36:22, Today’s English Version) Posumika maganizo pa chiphunzitso cha Atate, Yesu kenako akunena kuti: “Chalembedwa mwa aneneri, Ndipo adzakhala onse ophunzitsidwa ndi [Yehova].”—Yohane 6:45.
3. Kodi tidzalingalira mafunso otani?
3 Kunena zoona, ungakhale mwaŵi kukhala pakati pa aja amene mneneri Yesaya analemba za iwo kuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.” (Yesaya 54:13) Kodi tingakhale otero? Kodi ndani amene akhala ngati ana kwa iye nalandira ziphunzitso zake? Kodi ziphunzitso za Yehova zofunika kwambiri zimene tiyenera kudziŵa ndi kutsatira kuti tilandire dalitso lake nzotani? Kodi Yehova anaphunzitsa motani kale, ndipo kodi akuphunzitsa mwanjira imodzimodziyo lerolino? Ameneŵa ndi mafunso amene tidzalingalira.
Atate, Mphunzitsi, Mwamuna
4. Kodi ndani mwa ana a Yehova anayamba kulandira chiphunzitso chake?
4 Yehova anayamba kukhala Atate ndi Mphunzitsi pamene analenga Mwana wake wobadwa yekha, Yesu asanakhale munthu. Ameneyu amatchedwa “Mawu” chifukwa chakuti ndiye Wolankhulira Yehova Wamkulu. (Yohane 1:1, 14; 3:16) Mawuyo anatumikira “pambali pa [Atate] ngati mmisiri,” ndipo anaphunzira zambiri pa chiphunzitso cha Atate wake. (Miyambo 8:22, 30) Kwenikweni, anakhala Mtumiki, kapena njira, mwa amene Atate analengera zinthu zina zonse, kuphatikizapo “ana a Mulungu” auzimu. Iwo ayenera kuti anakondwera kuphunzitsidwa ndi Mulungu! (Yobu 1:6; 2:1; 38:7; Akolose 1:15-17) Pambuyo pake, munthu woyamba, Adamu, analengedwa. Nayenso anali “mwana wa Mulungu,” ndipo Baibulo limasonyeza kuti Yehova anamlangiza.—Luka 3:38; Genesis 2:7, 16, 17.
5. Kodi Adamu anataya mwaŵi wamtengo wapatali wotani, komabe ndani amene Yehova anaphunzitsa, ndipo chifukwa ninji?
5 Nzachisoni kuti, Adamu, mwa kusamvera kwake kwadala, anataya mwaŵi wa kupitiriza kukhala mwana wa Mulungu. Chotero, mbadwa zake sizikananena kuti zinali ndi unansi ndi Mulungu wa kukhala ana ake chifukwa chabe cha kubadwa kwawo. Komabe, Yehova anaphunzitsa anthu opanda ungwiro amene anayang’ana kwa iye kaamba ka chitsogozo. Mwachitsanzo, Nowa anakhala “munthu wolungama” yemwe “anayendabe ndi Mulungu,” choncho Yehova analangiza Nowa. (Genesis 6:9, 13–7:5) Mwa kumvera kwake, Abrahamu anasonyeza kuti anali “bwenzi la Mulungu,” chotero nayenso anaphunzitsidwa ndi Yehova.—Yakobo 2:23; Genesis 12:1-4; 15:1-8; 22:1, 2.
6. Kodi ndani amene Yehova anayamba kuona monga “mwana” wake, ndipo iye anali mphunzitsi wotani kwa mwanayo?
6 Patapita zaka zambiri, m’tsiku la Mose, Yehova analoŵa mu unansi wa pangano ndi mtundu wa Israyeli. Chotero, mtunduwo unakhala anthu ake osankhika ndipo anauona ngati “mwana” wake. Mulungu anati: “Mwana wanga . . . ndiye Israyeli.” (Eksodo 4:22, 23; 19:3-6; Deuteronomo 14:1, 2) Chifukwa cha unansi wa pangano umenewo, Aisrayeli anakhoza kunena zimene zinalembedwa ndi mneneri Yesaya kuti: “Inu Yehova ndinu Atate wathu.” (Yesaya 63:16) Yehova anasenza thayo lake lautate naphunzitsa ana ake, Israyeli, mwachikondi. (Salmo 71:17; Yesaya 48:17, 18) Kwenikweni, pamene iwo anakhala osakhulupirika, iye mwachifundo anawadandaulira kuti: “Bwerani, ananu obwerera.”—Yeremiya 3:14.
7. Kodi Israyeli anali ndi unansi wotani ndi Yehova?
7 Chifukwa cha unansi wa panganowo ndi Israyeli, Yehova mophiphiritsira anakhalanso Mwamuna wa mtunduwo, ndipo uwo unakhala mkazi wake wophiphiritsira. Ponena za iye, mneneri Yesaya analemba kuti: “Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wamakamu ndiye dzina lake.” (Yesaya 54:5; Yeremiya 31:32, NW) Ngakhale kuti Yehova anachita mbali yake bwino lomwe monga Mwamuna, mtundu wa Israyeli unakhala mkazi wosakhulupirika. “Monga mkazi achokera mwamuna wake monyenga,” anatero Yehova, “chomwecho mwachita ndi ine monyenga, inu nyumba ya Israyeli.” (Yeremiya 3:20) Yehova anapitiriza kuchonderera ana a mkazi wake wosakhulupirikayo; anapitiriza kukhala “Mlangizi [wawo] Wamkulu.”—Yesaya 30:20, NW; 2 Mbiri 36:15.
8. Ngakhale kuti Israyeli monga mtundu anakanidwa ndi Yehova, kodi ndi mkazi wophiphiritsira uti wochitiridwa chithunzi amene iye adakali naye?
8 Pamene Israyeli anakana Mwana Wake, Yesu Kristu ndi kumupha, Mulungu potsirizira pake anamkaniratu Israyeli. Chotero mtundu Wachiyuda umenewu sunakhalenso mkazi wake wophiphiritsira, ndiponso iye sanalinso Atate ndi Mphunzitsi wa ana ake opulupudza. (Mateyu 23:37, 38) Komabe, Israyeli anali chabe mkazi wongochitira chithunzi. Mtumwi Paulo anagwira mawu Yesaya 54:1, amene amalankhula za “[mkazi, NW] wouma” wosiyana ndi “mkazi wokwatibwa ndi mwamuna,” mtundu wa Israyeli wakuthupi. Paulo akusonyeza kuti Akristu odzozedwa ali ana a “chumba,” amene akumutcha “Yerusalemu wakumwamba.” Mkazi wophiphiritsira wochitiridwa chithunzi ameneyu wapangidwa ndi gulu lakumwamba la Mulungu la zolengedwa zauzimu.—Agalatiya 4:26, 27.
9. (a) Kodi Yesu anali kunena za yani pamene analankhula zakuti ‘ana ako adzaphunzitsidwa ndi Yehova’? (b) Kodi ndi pachifukwa chotani pamene anthu amakhalira ana auzimu a Mulungu?
9 Chotero, m’sunagoge wa ku Kapernao, pamene Yesu anagwira mawu ulosi wa Yesaya wakuti: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova,” anali kulankhula za aja amene anali kudzakhala “ana” a “Yerusalemu wakumwamba,” gulu la Mulungu lakumwamba longa mkazi. Mwa kulandira ziphunzitso za Yesu Kristu, woimira Mulungu wochokera kumwamba, Ayuda omvetserawo anakhoza kukhala ana a mkazi wa Mulungu wakumwamba yemwe kale anali chumba napanga “mtundu woyera mtima,” “Israyeli wa Mulungu” wauzimu. (1 Petro 2:9, 10; Agalatiya 6:16) Pofotokoza mwaŵi waukulu kwambiri umene Yesu anapereka wa kukhala ana a Mulungu auzimu, mtumwi Yohane analemba kuti: “Anadza kwa zake za iye yekha, ndipo ake a mwini yekha sanamlandira iye. Koma onse amene anamlandira iye, kwa iwo anapatsa mphamvu yakukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake.”—Yohane 1:11, 12.
Ziphunzitso za Yehova Zofunika Kwambiri
10. Chipanduko cha m’Edene chitangochitika, kodi Yehova anaphunzitsanji ponena za “mbewu,” ndipo ndani anakhala Mbewu imeneyo?
10 Yehova, pokhala Atate wachikondi, amauza ana ake za zifuno zake. Chotero, pamene mngelo wopanduka anasonkhezera anthu aŵiri oyamba kusamvera, Yehova nthaŵi yomweyo ananena za chimene adzachita kuti akwaniritse chifuno chake cha kupanga dziko lapansi kukhala paradaiso. Ananena kuti adzaika udani pakati pa “njoka yokalambayo,” amene ali Satana Mdyerekezi, “ndi mkaziyo.” Ndiyeno anafotokoza kuti “mbewu” ya mkazi idzalalira “mutu” wa Satana, kumupha. (Genesis 3:1-6, 15; Chivumbulutso 12:9; 20:9, 10) Monga momwe taonera, mkazi—wodziŵika pambuyo pake monga “Yerusalemu wakumwamba”—ndi gulu lakumwamba la Mulungu la zolengedwa zauzimu. Koma kodi “mbewu” yakeyo ndani? Ndiye Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, amene anatumidwa kuchokera kumwamba ndi amene adzawononga Satana potsiriza pake.—Agalatiya 4:4; Ahebri 2:14; 1 Yohane 3:8.
11, 12. Kodi Yehova anafutukula motani chiphunzitso chake chofunika kwambiri cha “mbewu”?
11 Yehova anafutukula chiphunzitso chofunika kwambiri chimenechi cha “mbewu” pamene analonjeza Abrahamu kuti: “Ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi zakumwamba, . . . m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa.” (Genesis 22:17, 18) Yehova anagwiritsira ntchito mtumwi Paulo kufotokoza kuti Yesu Kristu ndiye Mbewu yolonjezedwa ya Abrahamu ndi kuti enanso adzakhala mbali ya “mbewu” imeneyo. “Ngati muli a Kristu,” analemba motero Paulo, “muli mbewu ya Abrahamu, [oloŵa, NW] nyumba monga mwa lonjezano.”—Agalatiya 3:16, 29.
12 Yehova anavumbulanso kuti Kristu, Mbewuyo, adzachokera mumbadwo wachifumu wa Yuda ndi kuti “anthu adzamvera iye.” (Genesis 49:10) Ponena za Mfumu Davide wa fuko la Yuda, Yehova analonjeza kuti: “Ndidzakhalitsanso mbewu yake chikhalire, ndi mpando wachifumu wake ngati masiku a m’mwamba. Mbewu yake idzakhala kunthaŵi yonse, ndi mpando wachifumu wake ngati dzuŵa pamaso panga.” (Salmo 89:3, 4, 29, 36) Pamene mngelo Gabrieli analengeza kubadwa kwa Yesu, anafotokoza kuti mwanayo anali Wolamulira woikidwa ndi Mulungu, Mbewu ya Davide. “Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu,” anatero Gabrieli, “ndipo [Yehova, NW] Mulungu adzampatsa iye mpando wachifumu wa Davide atate wake: . . . ndipo ufumu wake sudzatha.”—Luka 1:32, 33; Yesaya 9:6, 7; Danieli 7:13, 14.
13. Kuti tilandire dalitso la Yehova, kodi tiyenera kuchita motani ndi chiphunzitso chake?
13 Kuti tilandire dalitso la Yehova, tiyenera kudziŵa ndi kuchitapo kanthu pa chiphunzitso chofunika kwambiri chimenechi cha Ufumu wa Mulungu. Tiyenera kukhulupirira kuti Yesu anatsika kumwamba, kuti ndiye Mfumu yoikidwa ndi Mulungu—Mbewu yachifumu imene idzayang’anira kubwezeretsedwa kwa Paradaiso pa dziko lapansi—ndi kuti adzaukitsa akufa. (Luka 23:42, 43; Yohane 18:33-37) Ku Kapernao pamene Yesu analankhula za kuukitsa akufa, Ayuda ayenera kukhala ataona kuti iye analankhula choonadi. Eya, milungu ingapo yokha zimenezo zisanachitike, mwinamwake m’Kapernao mmenemo, iye anali ataukitsa mwana wamkazi wazaka 12 wa mkulu wa sunagoge! (Luka 8:49-56) Ndithudi nafenso tili ndi chifukwa chokhulupirira ndi kuchita mogwirizana ndi chiphunzitso cha Yehova cha Ufumu wake chopatsa chiyembekezo!
14, 15. (a) Kodi Ufumu wa Yehova ngwofunika motani kwa Yesu? (b) Kodi nchiyani chimene tifunikira kumvetsa ndi kuchifotokoza ponena za Ufumu wa Yehova?
14 Yesu anapereka moyo wake wa pa dziko lapansi pa kuphunzitsa za Ufumu wa Yehova. Anaupanga mutu wa utumiki wake, ndipo analangiza ngakhale otsatira ake kuupempherera. (Mateyu 6:9, 10; Luka 4:43) Ayuda akuthupi anali pamzera wokhala “anawo a ufumu,” koma chifukwa cha kusoŵa chikhulupiriro, ambiri a iwo anataya mwaŵi umenewo. (Mateyu 8:12; 21:43) Yesu anasonyeza kuti ndi “kagulu ka nkhosa” kokha kamene kamalandira mwaŵi wa kukhala “ana a ufumuwo.” “Ana” ameneŵa akhala “oloŵa anzake a Kristu” mu Ufumu wake wakumwamba.—Luka 12:32; Mateyu 13:38; Aroma 8:14-17; Yakobo 2:5.
15 Kodi ndi oloŵa ufumu angati amene Kristu adzatengera kumwamba kukalamulira naye dziko lapansi? Ndi 144,000 okha, malinga ndi kunena kwa Baibulo. (Yohane 14:2, 3; 2 Timoteo 2:12; Chivumbulutso 5:10; 14:1-3; 20:4) Koma Yesu anati anali ndi “nkhosa zina,” zimene zidzakhala nzika za pa dziko lapansi mu ulamuliro wa Ufumuwo. Zimenezi zidzakhala ndi thanzi langwiro ndi mtendere kosatha pa dziko lapansi laparadaiso. (Yohane 10:16; Salmo 37:29; Chivumbulutso 21:3, 4) Tifunikira kumvetsa chiphunzitso cha Yehova chonena za Ufumuwo ndi kuchifotokoza.
16. Kodi ndi chiphunzitso chiti cha Yehova chofunika kwambiri chimene tifunikira kudziŵa ndi kutsatira?
16 Mtumwi Paulo anasonyeza chiphunzitso china cha Yehova chofunika kwambiri. Iye anati: “Wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzake.” (1 Atesalonika 4:9) Kuti tikondweretse Yehova, tifunikira kusonyeza chikondi chimenecho. “Mulungu ndiye chikondi,” limatero Baibulo, ndipo tiyenera kutsanzira chitsanzo chake cha kusonyeza chikondi. (1 Yohane 4:8; Aefeso 5:1, 2) Nzachisoni kuti, anthu ambiri alephereratu kuphunzira kukonda anthu anzawo monga momwe Mulungu amatiphunzitsira. Bwanji nanga za ife? Kodi talabadira chiphunzitso cha Yehova chimenechi?
17. Kodi tiyenera kutsanzira mkhalidwe wa yani?
17 Kuli kofunika kwambiri kwa ife kulandira ziphunzitso zonse za Yehova. Mkhalidwe wathu ukhaletu wonga uja wa amasalmo a Baibulo omwe analemba kuti: “Mundidziŵitse njira zanu, Yehova; mundiphunzitse mayendedwe anu. Munditsogolere m’choonadi chanu, ndipo mundiphunzitse.” “Ndiphunzitseni malemba anu. Mundiphunzitse chisiyanitso ndi nzeru . . . Ndiphunzitseni maweruzo anu.” (Salmo 25:4, 5; 119:12, 66, 108) Ngati mukumva mofanana ndi mmene amasalmowo anamvera, mungakhale pakati pa chikhamu cha ophunzitsidwa ndi Yehova.
Khamu Lalikulu la Ophunzitsidwa
18. Kodi mneneri Yesaya ananeneratu za chiyani chimene chidzachitika m’tsiku lathu?
18 Mneneri Yesaya ananeneratu zimene zidzachitika m’nthaŵi yathu kuti: “Padzakhala masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pa nsonga ya mapiri . . . Ndipo anthu ambiri adzamka, nati, Tiyeni tikwere kumka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake.” (Yesaya 2:2, 3; Mika 4:2) Kodi anthu ophunzitsidwa ndi Yehova ameneŵa ndani?
19. Kodi ndani amene akuphatikizidwa pa ophunzitsidwa ndi Yehova lerolino?
19 Amaphatikizapo ena kuwonjezera pa aja amene adzalamulira ndi Kristu kumwamba. Monga momwe taonera kale, Yesu anati anali ndi “nkhosa zina”—nzika za pa dziko lapansi za Ufumuwo—kuwonjezera pa “kagulu ka nkhosa” ka oloŵa Ufumu. (Yohane 10:16; Luka 12:32) A “khamu lalikulu” lopulumuka “chisautso chachikulu,” ali a gulu la nkhosa zina, ndipo ali ndi kaimidwe kovomerezeka pamaso pa Yehova chifukwa cha chikhulupiriro chawo m’mwazi wokhetsedwa wa Yesu. (Chivumbulutso 7:9, 14) Ngakhale kuti a nkhosa zina sakuphatikizidwa mwachindunji pa “ana” otchulidwa pa Yesaya 54:13, iwo ali odalitsidwa mwa kuphunzitsidwa ndi Yehova. Chotero, iwo moyenera amatcha Mulungu “Atate” chifukwa adzakhaladi Gogo wawo kupyolera mwa “Atate Wosatha,” Yesu Kristu.—Mateyu 6:9; Yesaya 9:6.
Mmene Yehova Amaphunzitsira
20. Kodi Yehova amaphunzitsa m’njira zotani?
20 Yehova amaphunzitsa m’njira zambiri. Mwachitsanzo, amatero mwa zolengedwa zomwe zili ntchito ya manja ake, zimene zimapereka umboni wa kukhalako kwake ndi nzeru zake zazikulu. (Yobu 12:7-9; Salmo 19:1, 2; Aroma 1:20) Ndiponso, amaphunzitsa mwa kulankhula ndi munthu mwachindunji, zimene anachita polangiza Yesu asanakhale munthu. Mofanana ndi zimenezo, panthaŵi zitatu zolembedwa, iye analankhula mwachindunji kwa anthu pa dziko lapansi ali kumwamba.—Mateyu 3:17; 17:5; Yohane 12:28.
21. Kodi ndi mngelo uti amene Yehova anagwiritsira ntchito kwambiri monga woimira wake, koma tidziŵa bwanji kuti anagwiritsiranso ntchito ena?
21 Yehova amagwiritsiranso ntchito oimira ake aungelo kuphunzitsa, kuphatikizapo Mwana wake Woyamba, “Mawu.” (Yohane 1:1-3) Ngakhale kuti Yehova angakhale atalankhula mwachindunji kwa Adamu, mwana wake wangwiro m’munda wa Edene, mwina iye anagwiritsira ntchito Yesu asanakhale munthu kumlankhulira Iye. (Genesis 2:16, 17) Mwinamwake ameneyu ndiye ‘mthenga wa Mulungu, amene anatsogolera ulendo wa Israyeli’ ndi amenenso Yehova anawalamulira kuti: ‘Mverani mawu ake.’ (Eksodo 14:19; 23:20, 21) Mosakayikira Yesu asanakhale munthu analinso “kazembe wa ankhondo a Yehova” yemwe anaonekera kwa Yoswa kumlimbikitsa. (Yoswa 5:14, 15) Yehova amagwiritsiranso ntchito angelo ena kupereka ziphunzitso zake, monga aja amene anagwiritsira ntchito kupereka Chilamulo kwa Mose.—Eksodo 20:1; Agalatiya 3:19; Ahebri 2:2, 3.
22. (a) Kodi ndani amene Yehova wagwiritsira ntchito kuphunzitsa pa dziko lapansi? (b) Kodi njira yaikulu imene Yehova akuphunzitsira anthu lerolino njotani?
22 Ndiponso, Yehova Mulungu amaphunzitsa mwa kugwiritsira ntchito oimira ake aumunthu. Makolo mu Israyeli anayenera kuphunzitsa ana awo; aneneri, ansembe, akalonga, ndi Alevi anaphunzitsa mtunduwo Chilamulo cha Yehova. (Deuteronomo 11:18-21; 1 Samueli 12:20-25; 2 Mbiri 17:7-9) Yesu anali Wolankhulira Mulungu wamkulu pa dziko lapansi. (Ahebri 1:1, 2) Kaŵirikaŵiri Yesu ananena kuti zimene anaphunzitsa zinalidi zimene anaphunzira kwa Atate, chotero, mwanjira imeneyo, omvetsera ake anali kuphunzitsidwa ndi Yehova. (Yohane 7:16; 8:28; 12:49; 14:9, 10) Yehova anachititsa mawu ake kulembedwa, ndipo m’tsiku lathu iye akuphunzitsa anthu makamaka mwa kugwiritsira ntchito Malemba ouziridwa ameneŵa.—Aroma 15:4; 2 Timoteo 3:16.
23. Kodi ndi mafunso otani amene adzalingaliridwa m’nkhani yotsatira?
23 Tikukhala m’nthaŵi yofunika, pakuti Malemba amalonjeza kuti ‘masiku otsiriza [amene tikukhalamo] anthu ambiri adzaphunzitsidwa njira za Yehova.’ (Yesaya 2:2, 3) Kodi malangizo ameneŵa akuperekedwa motani? Kodi tiyenera kuchitanji kuti tipindule ndi programu yaikulu yakuphunzitsa ya Yehova imene ikuchitika tsopano limodzinso ndi kutengamo mbali? Mafunso amenewo tidzawalingalira m’nkhani yotsatira.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Yehova anakhala motani Atate, Mphunzitsi, ndi Mwamuna?
◻ Kodi Yehova amaphunzitsanji za “mbewu”?
◻ Kodi chiphunzitso chofunika kwambiri chimene tiyenera kutsatira chimene Mulungu watiphunzitsa nchotani?
◻ Kodi Yehova amaphunzitsa motani?
[Chithunzi patsamba 10]
Kuukitsa mwana wamkazi wa Yairo kunapereka chifukwa chokhulupirira lonjezo la Yesu la chiukiriro