Kodi Mukukhalabe Osadetsedwa m’Njira Iriyonse?
“Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.”—YESAYA 52:11.
1. (a) Kodi ndimotani mmene lamulo lachifumu linavomerezera zotengera za Yehova kubwezeretsedwa ku Yerusalemu? (b) Kodi ndimotani mmene zina za zotengera zimenezi zinadetsedwera?
MWADZIDZIDZI iwo anali omasuka—pambuyo pa zaka 70 za ukapolo! Lamulo la chifumu chifupifupi 538 B.C.E. linalola mtundu wa Ayuda kubwerera “ndi kumanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Israyeli.” (Ezara 1:2, 3) Kenaka, chochitika china chodabwitsa: “Mfumu Koresi [wa Perisiya] iyemwini anabweretsa zotengera za nyumba ya Yehova, zimene Nebukadinezara adazitulutsa mu Yerusalemu.” (Ezara 1:7, 8) Pakati pa izi panali zotengera zopatulika zimene Belisazara ndi akulu ake ananyazitsa pa usiku wa kugwa kwa Babulo monyansa kuzigwiritsira izo ntchito kulemekeza milungu yonyenga! (Danieli 5:3, 4) Tsopano omwe anali otuluka kudziko la kwawo akabwezeretsa zotengera zimenezi ku Yerusalemu ndi kuzigwiritsira ntchito ku chilemekezo cha Yehova!
2. (a) Ndi ulosi uti wa Yesaya umene obwererawo adzakumbukira? Ndi kwa ndani kumene ukagwira ntchito? (b) Nchifukwa ninji iwo anachenjezedwa kusakhudza kanthu kalikonse kodetsedwa?
2 Pamene iwo motenthedwa maganizo anali kukonzekera kaamba ka ulendo, Ayuda obwererawo anakumbukira mawu a mneneri Yesaya: “Chokani inu, chokani, tulukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.” (Yesaya 52:11) Alevi, ndithudi, ndi amene anachita kutumizidwa kwenikweni kwa zotengerazo. (Numeri 1:50, 51; 4:15) Ngakhale kuli tero, Yesaya anali ataneneratu kuti obwezeretsedwa amenewa adzakhala onyamula zotengera zolemekezeka. Onse chotero anali ndi thayo la kukhala oyera. Iwo sanayenera kulanda Ababulo zinthu za mtengo wake monga mmene anachitira Aisrayeli pamene anali kuchoka mu Aigupto. (Yerekezani ndi Eksodo 12:34-38.) Iwo anayenera kukhala omasuka ku chikhoterero chirichonse cha kukondetsa zinthu zakuthupi kapena chadyera pobwerera. Ponena za “zosema zochitidwa manyazi” za Babulo, kungokhudza kokha limodzi kunali kodetsa.a (Yeremiya 50:1, 2) Kokha mwakukhala oyera m’njira iriyonse Ayuda akanayenda “m’Njira Yopatulika” kubwerera ku Yerusalemu.—Yesaya 35:8, 9.
3. Ndi ndani lerolino amene ali onyamula “zotengera” za Yehova? Nchifukwa ninji icho chiri chitokoso chotero kwa iwo kukhalabe osadetsedwa?
3 Mboni za Yehova lerolino ziyenera kukhala mofananamo zopatulika monga zonyamula “zotengera” za Yehova. Mtumwi Paulo anagwira mawu a Yesaya ndi kuwagwiritsira ntchito kwa Akristu a m’tsiku lake, akumanena kuti: “Okondedwa tidzikonzere tokha kuleka chodetsa chonse cha thupi ndi cha mzimu, ndi kutsiriza chiyero m’kuwopa Mulungu.” (2 Akorinto 6:17–7:1) Pambali pa kukhala m’dziko lodetsedwa, tiyenera kuchita ndi zikhoterero zathu zoipa za cholowa. (Genesis 8:21) Yeremiya 17:9 amatikumbutsa ife kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika. Ndani angathe kuudziŵa?” Ena amadzinyenga iwo eni ndi ena m’kukhulupirira kuti miyoyo yawo iri yosadetsedwa ndipo yolandiridwa kwa Mulungu, pamene m’chenicheni zimenezo siziri tero. Iwo amachita mtundu wa kunyenga. Chotero aliyense wa ife ayenera kufunsa, ‘Kodi ndikuika kuyesetsa kothekera kwa kukhala wosadetsedwa pamaso pa Yehova m’njira iriyonse?’ Kutithandiza ife kuchita tero, tiyeni ife tsopano tilunjikitse chidwi pa mbali zinayi za kuyera.
Kuyera Kwakuthupi: Chinthu Choyambirira
4. (a) Nchifukwa ninji kusadetsedwa kwakuthupi kuli koyambirira pakati pa anthu a Yehova? (b) Nchifukwa ninji chingakhale chovuta nthaŵi zina kusunga mkhalidwe wapamwamba wa chiyero?
4 Kuyera kwakuthupi kuli chinthu choyambirira pakati pa anthu a Yehova lerolino monga mmene kunaliri m’nthaŵi zakale. (Eksodo 30:17-21; 40:30-32) Ndiko nkomwe, kodi tingakhale tikuchita ndi “zotengera za Yehova” ndi ulemu ngati tsitsi lathu, manja, nkhope, mano, kapena zikhadabo zinali zakuda, kapena ngati timatulutsa fungo lathupi loipa? Chiri chapafupi, ngakhale kuli tero, kulola kaimidwe kotsika ka dziko kutisonkhezera ife.—Aroma 12:2.
5. (a) Nchifukwa ninji chiri chofunika chotero kuti tisunge makhalidwe athu a chiyero kukhala apamwamba? Perekani zitsanzo za kumaloko za mmene uphungu umenewu ungagwiritsiridwire ntchito. (b) Kodi ndimotani mmene akulu angathandizire?
5 Kodi tingakhale bwanji osiyana ndi dziko ngati tikhala ndi mkhalidwe wapansi wa dziko? Kodi nyumba yakuda kapena malo onyansa olambirira sangapangitse ‘mawu a Mulungu kuchitidwa mwano’? (Tito 2:5) Koma pamene tisonyeza ukhondo waumwini wabwino, kutola zinyalala pamalo a msonkhano, kuthandiza kukonza Nyumba ya Ufumu, ndi kusunga nyumba zathu—ngakhale nyumba zosawoneka bwino koposa—zaudongo ndi zoyera, timabweretsa ulemerero kwa Mulungu! (Yerekezani ndi 1 Petro 2:12.) Akulu, perekani chitsanzo chabwino chaumwini m’kukhala osadetsedwa. “Musabweze” kupereka uphungu woyenerera pamene kuli koyenera.—Machitidwe 20:20.
6. Nchiyani chimene chiyenera kukhala kaimidwe kathu ka kavalidwe popita ku misonkhano ndi mu utumiki wa m’munda?
6 Bwanji ponena za chovala chimene timavala pamene tikulambira pa misonkhano ndi pamene tiri mu utumiki wa m’munda? Kodi icho sichiyenera kukhala ‘chodekha ndi chabwino’? (1 Timoteo 2:9; Ahebri 10:23-25) Musalingalire kuti tiri ndi thayo la kuvala bwino kokha pamene tiri ndi mbali pa msonkhano. Zovala za nthaŵi zonse zopambanitsa ziri zosadekha ndipo zosayenerera kaamba ka kulambira. Zola zonyamulira mabukhu zong’ambika ndi maBaibulo oduka mungodya zake kapena akuda zingachotsenso chikondwerero ku uthenga wa Ufumu.
Kupewa Kuipitsa kwa Maganizo
7. Nchiyani chimene chiri mfungulo ku chiyero cha maganizo, molingana ndi Afilipi 4:8?
7 Pa Afilipi 4:8 Paulo anapereka uphungu wakuti: “Chotsalira, abale, zinthu ziri zonse zowona, ziri zonse zolemekezeka, ziri zonse zolungama, ziri zonse zoyera, ziri zonse zokongola, ziri zonse zimveka zokoma; ngati kuli chokoma mtima china, kapena chitamando china, zilingirireni izi.” Mosasamala kanthu za chimenecho, kulikonse tiri okanthidwa ndi ziyesero za kusunzumira mu “‘zinthu zozama za Satana.’”—Chivumbulutso 2:24.
8. Kodi ndimotani mmene matsoka operekedwa ndi mitundu yosiyanasiyana ya kusangulutsa angachitiridwe chitsanzo? Perekani zitsanzo za kumaloko.
8 Mwachitsanzo, kukhalapo kopepuka kwa zithunzi za maliseke ndi zinthu za chiwawa zatulukamo m’mavuto akulu kwa ena ogwiritsira ntchito ma rekorda a video kaseti. Mu Europe, mbale wokwatira ankawonera matepi onyansa pamene mkazi wake anapita kukagona. Mbewu ya cholakwa inabzyalidwa mwa iye mwamphamvu kutulukamo mu chigololo. (Yerekezani ndi Yakobo 1:14, 15.) Mu dziko limodzi la ku Africa, gulu la Mboni zachichepere zinabwereka matepi onyansa kuchokera kwa mabwenzi awo a kusukulu ndipo anawonerera iwo pamene makolo awo anali kunja. Mkulu mu Nigeria, ngakhale kuli tero, akuwona kuti: ‘Ngozi yaikulu kaŵirikaŵiri iri mu maprogramu a pa TV anthaŵi zonse amene mofananamo amasonyeza chiwawa, upandu, nkhondo, ziwonetsero za kugonana, ndi kunyodola kwa kusunga umphumphu wa mu ukwati.’ Manyuzipepala ofupikitsidwa a mtengo wotsika, magazini osonyeza zithunzi za maliseke, mabukhu odzutsa chilakolako cha kugonana, makanema, ndi nyimbo zonyansa zirinso zoyambitsa ngozi.
9. (a) Nchifukwa ninji tiyenera kukhala osankha ponena za zimene timvetsera, kupenyerera, ndi kuŵerenga? (b) Kodi ndimotani mmene tingachitire ngati tiyang’anizana ndi zinthu zokaikiritsa?
9 Sitingakhoze kudetsa maganizo athu ndi zinthu “zochititsa manyazi kuzilankhula.” (Aefeso 5:12) Chotero khalani osankha ponena za zimene mumvetsera, kuwonerera, ndi kuŵerenga. Dzichinjirizeni ndi kuchitapo kanthu mwamsanga kukana zinthu zosayenera. (Masalmo 119:37) Ichi chidzafunikira kudziletsa kwenikweni kwaumwini, mwinamwake mophiphiritsira ‘kupumphuntha thupi lanu ndi kulitsogoza monga kapolo.’ (1 Akorinto 9:27) Nthaŵi zonse kumbukirani, ngakhale kuli tero, kuti zimene timawonerera mwachinsinsi zimawonedwa ndi “Mmodzi wosawonekayo.” (Ahebri 11:27) Chotero pewani zimene ziri zokaikiritsa. “Pitirizani kutsimikizira zomwe ziri zolandirika kwa Ambuye.”—Aefeso 5:10, NW.
“Kukhala Ogalamuka” kuti Tikhale Oyera mwa Makhalidwe
10. (a) Nchifukwa chimodzi chiti chimene ambiri amadzudzulidwira kapena kuchotsedwera chaka chirichonse? (b) Ndi prinsipulo la Baibulo liti limene liyenera kuwongolera mkhalidwe wathu pa tchuthi ndi pa ntchito?
10 Pa Aefeso 5:5 Paulo anachenjeza kuti: “Pakuti ichi muchidziŵe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa m’ufumu wa Kristu ndi Mulungu.” Komabe, zikwi chaka chirichonse zimadzudzulidwa kapena kuchotsedwa chifukwa cha mkhalidwe woipa wa chisembwere—‘kuchimwira thupi.’ (1 Akorinto 6:18) Kaŵirikaŵiri, icho chiri kokha chotulukapo cha “kusasamalira monga mwa mawu a [Mulungu].” (Masalmo 119:9) Abale ambiri, mwachitsanzo, amachotsa kudzichinjiriza kwawo kwa makhalidwe mkati mwa nthaŵi ya tchuthi. Kunyalanyaza mayanjano a teokratiki, iwo amayambitsa ubwenzi ndi anthu a patchuthi a kudziko. Akumalingalira kuti awo ‘alidi anthu abwino,’ Akristu ena agwirizana nawo m’machitachita okaikiritsa. Mofananamo, ena akhala aubwenzi kwambiri ndi ogwira nawo ntchito. Mkulu mmodzi Wachikristu anakhala wodzilowetsamo kwambiri ndi mkazi wogwira naye ntchito kotero kuti iye anasiya banja lake ndi kuyamba kukhala ndi iye! Kuchotsedwa kunatulukapo. Ali mowona chotani nanga mawu a Baibulo, “Mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma”!—1 Akorinto 15:33.
11. Nchifukwa ninji kusonkhana kwa Chikristu kuyenera kuwongoleredwa moyenerera?
11 Kuchokera ku South Africa kukubwera ripoti iri: “Chowopsya china chomwe chikuwopsyeza kuwongoka kwa makhalidwe kwa ambiri kuli mapwando a akulu . . . ena a amene amachitidwa pambuyo pa magawo a msonkhano wa chigawo.” Komabe, kusonkhana kochepa kwa Akristu komwe kumawongoleredwa bwino kaŵirikaŵiri sikumagwera mu “m’chezo.” (Agalatiya 5:21) Ngati zakumwa zoledzeretsa zikuperekedwa, chitani tero pansi pa chitsogozo ndipo modziletsa. “Vinyo achita chiphwete,” ndipo pansi pa chisonkhezero chake, abale ena ataya chinjirizo lawo la makhalidwe abwino kapena kudzutsa zofooka zosinza. (Miyambo 20:1) Chotero, atumiki aŵiri achichepere anadzilowetsa mu machitidwe a kugonana kwa ofanana ziwalo pambuyo pa kumwa mopambanitsa zakumwa zoledzeretsa.
12, 13. (a) Ndimotani mmene ena alungamitsira mkhalidwe woipa? Nchifukwa ninji kulingalira koteroko kuli koipa? (b) Ndimotani mmene tingakhalire ogalamuka molimbana ndi ziwopsyezo za makhalidwe abwino?
12 Pamene muyesera kuchita cholakwa, kumbukirani kuti, mosasamala kanthu kuti ndife oyera motani mmene tingawonekere kunja, chiri chimene tiri mkati chomwe chimaŵerengera. (Miyambo 21:2) Ena mwachiwonekere amadzimva kuti Mulungu adzakhululukira kugwera kwawo kobwerezabwereza mu mkhalidwe woipa chifukwa iwo ali ofooka. Koma kodi uku sikukakhala “kusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa”? (Yuda 4) Ena amalingalira kuti “Yehova satipenya.” (Ezekieli 8:12) Kumbukirani, ngakhale kuli tero, kuti “palibe cholengedwa chosawonekera pamaso pake, koma zonse zikhala pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.”—Ahebri 4:13.
13 Chotero dzichinjirizeni motsutsana ndi ziwopsyezo za makhalidwe abwino! “Lolani dama ndi chidetso chonse kapena chisiriro zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima.” (Aefeso 5:3, 4) “Danani nacho choipa,” mosasamala kanthu kuti ndi chosangalatsa chotani mmene chiriri kuthupi.—Aroma 12:9.
Kukhala Osadetsedwa Mwauzimu
14, 15. (a) Kodi ndimotani mmene ena adzivumbulutsira iwo eni ku kusakaza kwauzimu? (b) Kodi ndimotani mmene ampatuko amagwiritsira ntchito ‘pakamwa pawo kusakaza anthu anzawo’? (c) Ndi mwanjira zotani mmene ampatuko aliri odetsedwa, ndipo nchiyani chimene iwo aiwala?
14 Ena adzivumbula iwo eni ku kuwononga kothekera kwauzimu mwa kutsegula ku zoulutsidwa za chipembedzo pa wailesi kapena pa wailesi ya kanema. M’dziko limodzi la ku Africa, ena anawonerera madrama a pa TV omwe anawonetsera kukhulupirira malaulo kwa zipembedzo za mwambo zokhulupirira mu zinthu za chilengedwe m’chiwunikiro chabwino. Mtumwi Paulo, ngakhale kuli tero, anachenjeza ponena za tsoka la kupha koposa—anthu ampatuko omwe anali “kupasula chikhulupiriro cha ena.” (2 Timoteo 2:16-18) Anthu onga amenewo adakalipo! (2 Petro 2:1-3) Ndipo nthaŵi zina anapambana m’kukhotetsa kulingalira kwa ena. Monga mmene Miyambo 11:9 imanenera: “Wonyoza Mulungu awononga mnzake ndi m’kamwa mwake.”
15 Ampatuko kaŵirikaŵiri amapempha mphamvu za kulingalira, kudzinenera kuti talandidwa maufulu athu, kuphatikizapo ufulu wa kutanthauzira Baibulo kaamba ka ife eni. (Yerekezani ndi Genesis 3:1-5) M’chenicheni, awo omwe akakhala osakaza samapereka chirichonse koposa kubwerera ku ziphunzitso zochititsa nselu za “Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 17:5; 2 Petro 2:19-22) Ena amachitengera kuthupi, kusonkhezera anansi akale “kusadera nkhaŵa” chifukwa ntchito yodzichepetsa ya kuchitira umboni kunyumba ndi nyumba iri “yosayenerera” kapena “yopanda malemba.” (Yerekezani ndi Mateyu 16:22, 23.) Zowona, olankhula mosyasyalika oterowo angawoneke oyera kunja m’njira ya kuthupi ndi makhalidwe. Koma mkati iwo ali odetsedwa mwauzimu, ogonjera ku kulingalira konyada, kodzidalira. Iwo aiwala zonse zimene anaphunzira ponena za Yehova, dzina lake lopatulika ndi mikhalidwe. Iwo samazindikiranso kuti zonse zimene anaphunzira ponena za chowonadi cha Baibulo—chiyembekezo chaulemerero cha Ufumu ndi dziko lapansi la paradaiso ndi kuthetsedwa kwa ziphunzitso zonyenga, zonga ngati Utatu, kusafa kwa moyo wa munthu, chizunzo chosatha, ndi purigatoriyo—inde, zonse za izi zinabwera kwa iwo kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.”—Mateyu 24:45-47.
16. Kodi ndimotani mmene olungama amapulumutsidwira ndi “chidziŵitso”?
16 Mosangalatsa, woyang’anira wadera mu France anawona kuti: “Abale ena amanyengedwa chifukwa amasowa chidziŵitso cholongosoka.” Chimenechi chiri chifukwa chake Miyambo 11:9 imanena kuti: “Koma olungama adzapulumuka pakudziŵa.” Ichi sichimatanthauza kumvetsera kwa ampatuko kapena kuŵerenga zolemba zawo. M’malo mwake, icho chimatanthauza kufika ku “chidziŵitso cholongosoka cha chinsinsi chopatulika cha Mulungu” kupyolera mu phunziro laumwini losamalitsa la Baibulo ndi zofalitsidwa za Sosaite zozikidwa pa Baibulo. Kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka chimenechi, ndi ndani amene angakhale wofunitsitsa kupereka chisamaliro ku zotuluka m’kamwa mwa ampatuko? Lolani kuti munthu aliyense “asakukopeni inu ndi mawu okopakopa”! (Akolose 2:2-4) Kusatsa konyenga kwa chipembedzo kochokera ku magwero alionse kuyenera kupewedwa monga ululu! Ndithudi, popeza Mbuye wathu wagwiritsira ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kufikitsa kwa ife “zonena za moyo wosatha,” nchifukwa ninji tidzafuna kuyang’ana kulikonse?—Yohane 6:68.
Kodi Mudzakhalabe Osadetsedwa?
17, 18. Nchifukwa ninji chiri chofunika koposa kukulitsa (a) kuyera kwakuthupi, (b) kuyera kwa maganizo, (c) kuyera kwa makhalidwe, ndi (d) kuyera kwauzimu?
17 Chotero zambiri zikulowetsedwamo m’kukhalabe osadetsedwa pamaso pa Yehova Mulungu. Kusunga matupi athu, nyumba zathu, zovala zathu, ndi Nyumba zathu za Ufumu kukhala zoyera mwakuthupi kumalemekeza uthenga wathu wa Ufumu. Kukhala oyera mwamaganizo kumatithandiza ife kukhala oyera mwa makhalidwe ndi mwauzimu. Ichi chimaitanira pa kulabadira kwathu uphungu wa Paulo pa Afilipi 4:8, kusunga maganizo athu pa zinthu zomwe ziri zowona, zoyera, ndi zolemekezeka.
18 Tingayamikirenso mokulira koposa kuti timakhala oyera mwa makhalidwe ponse paŵiri m’mawu ndi m’zochita. Yehova mosabisira amatichenjeza ife kuti awo amene amadzilowetsa mu mtundu wina uliwonse wa mkhalidwe woipa sadzaloŵa mu Ufumu wa Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Mosasamala kanthu kuti ndi mosangalatsa chotani mmene zinthu zoipa zingawonekere, ngati tifesa kuthupi, tidzatuta chivundi kuchokera kuthupi. (Agalatiya 6:8) Pomalizira, pali nkhani ya kukhalabe oyera mwauzimu, oyera mu ziphunzitso. Kuyera koteroko kumatithandiza ife kusunga ungwiro wa mitima yathu ndi maganizo. Ife chotero timafulumizidwa nthaŵi zonse kufunafuna malingaliro a Mulungu pa nkhanizo—osati athu.
19. Nchiyani chimene chingathandize ponse paŵiri odzozedwa ndi “nkhosa zina” kukhala oyera m’njira zonse?
19 Posachedwapa wopititsa patsogolo weniweni wa zodetsedwa—Satana Mdyerekezi—adzaponyedwa, limodzi ndi ziwanda zake, m’phompho lakuya. Kufikira panthaŵi imeneyo, lolani onse a atumiki a Yehova—odzozedwa ndi “khamu lalikulu”—akhalebe oyera monga onyamula zotengera za Yehova. (Chivumbulutso 7:9, 13-15; 19:7, 8; 20:1-3) Nkhondoyo iri yosagonjetseka ndi yamphamvu. Kumbukirani, ngakhale kuli tero, kuti Yehova amapereka kwaulere “mzimu wa chiyero.” (Aroma 1:4) Gulu lake loyera, ndi akulu ake, limaimanso lokonzekera kutithandiza ife mwakupereka uphungu wanzeru, wa m’Malemba. Ndi thandizo loterolo limodzi ndi kugamulapo kwathu, tingakhalebe oyera m’njira iriyonse!
[Mawu a M’munsi]
a Liwu la Chihebri kaamba ka zosema zochitidwa manyazi gil·lu·limʹ, linali liwu lonyodola limene poyambirira linatanthauza “mibulu ya tudzi”—chinachake chonyansa kwa Ayuda.—Deuteronomo 23:12-14; 1 Mafumu 14:10; Ezekieli 4:12-17.
Mafunso Akubwereramo
◻ Nchifukwa ninji Ayuda obwerera kuchokera ku Babulo anayenera kukhala oyera?
◻ Kodi ndimotani mmene tingaperekere chisamaliro ku chiyero chakuthupi?
◻ Kodi ndimotani mmene tingatetezere malingaliro athu kuchokera ku kuwonongedwa?
◻ Kodi ndimotani mmene tingakhalire odzichinjiriza ku ziwopsyezo za makhalidwe abwino?
◻ Kodi ndimotani mmene tingasungire ku chiyero chathu chauzimu?
[Chithunzi patsamba 16]
Nyumba zathu ziyenera kukhala zitsanzo za chiyero
[Chithunzi patsamba 17]
Akristu ayenera kugwiritsira ntchito chiweruzo chabwino m’kupewa matepi a video ndi maprogramu a pa TV omwe angawononge maganizo awo
[Chithunzi patsamba 18]
Kusonkhana kwa magulu ochepa kungakhale komangirira mwa makhalidwe
[Chithunzi patsamba 19]
Mboni zachangu zimakhala zoyera mwauzimu ndipo zimapeza chitetezero ndi chimwemwe kupyolera mu phunziro la Baibulo losamalitsa