Kodi Mudzanena Kuti,“Ndine Pano! Munditumize Ine”?
“Yehova [anati]: ‘Ndidzatumiza yani, ndipo ndani adzatimukira ife?’ Ndipo ine ndinati: ‘Ndine pano! Munditumize ine.’”—YESAYA 6:8.
1, 2. Ndi chifukwa chapadera chotani cha chimwemwe chimene okwatirana aŵiri anali nacho?
“TIRI achimwemwe kutumiza kalata yathu ya chivomerezo kupita ku Colombia. Tasangalala ndi mwaŵi wathu wautumiki muno mu Ecuador mochuluka koposa ndi mmene taipilaita iyi ingalongosolere.” Inayamba motero kalata yochokera kwa Mboni za Yehova ziŵiri zomwe zinapita ku Ecuador kumene ofesi ya nthambi yatsopano ya Watch Tower Society inali kumangidwa.
2 Atumiki amenewa anapita ku Ecuador kukachita zoposa kuthandiza chabe pa kumanga; iwo anathandizanso monga aphunzitsi Achikristu. Iwo analemba kuti: “Tapeza kuti utumiki wa m’munda uli umodzi wa zinthu zofunika koposa. Kokha milungu itatu yapitayo, asanu ndi atatu a ife tinapita kunja pa msika ndi kugawira mabukhu 73 ndi magazini oposa 40. Mlungu umodzi pasadakhale tinali, tinayamba maphunziro aŵiri a Baibulo atsopano. Mowonadi tingawone kufunika kwa nthambi yatsopano. Mkazi wanga ndi ine tingakonde kukuyamikani kaamba ka mwaŵi wa kupitiriza mu mtundu wapadera umenewu wa utumiki wa nthaŵi zonse” tsopano mu Colombia.
3. Ndimotani mmene ambiri asonyezera mzimu wofanana ndi uja umene Yesaya anasonyeza?
3 Okwatirana aŵiri amenewa, ndi mazana ambiri a ena omwe adzipereka kutumizidwa ku dziko la chilendo, amawunikira mzimu wofanana ndi wa mneneri Yesaya. Pamene iye anamva Yehova akunena kuti: “Ndidzatumiza ndani, ndipo ndani adzatimukira ife?” Yesaya anayankha kuti: “Ndine pano! Munditumize ine.” Mulungu kenaka analamulira: “Kauze anthu awa, ‘Imvani inu ndithu, koma osazindikira; yang’anani inu ndithu, koma osadziŵitsa.’” (Yesaya 6:8, 9) Kodi Yesaya anali kudzipereka kutumizidwa kaamba ka chiyani, ndipo nchiyani chimene chinatulukapo kuchokera pamenepo? Ndipo nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera ku mbiri imeneyi mu mkhalidwe wa kufanana nako kwa makono ndi maphunziro ena aliwonse a umwini kaamba ka ife?
Ntchito ya Yesaya Yokalalikira
4, 5. (a) Ndi mkhalidwe wotani umene unalipo pamene Yesaya analandira masomphenya olembedwa mu mutu 6? (b) Nchiyani chimene Yesaya anawona m’masomphenyawo?
4 Yehova Mulungu anafunsa Yesaya, “Ndidzatumiza yani?” m’chaka chimene Mfumu Uziya anafa. (Yesaya 6:1) Mmenemo munali mu 777 B.C.E., kapena chifupifupi zaka zana limodzi ndi makumi asanu ndi aŵiri mphambu zisanu Ababulo asanawononge Yerusalemu ndi kulikhalitsa bwinja dziko la Yuda. Yehova anawona kuti mikhalidwe yoipa inali kudza, ndipo iye anatumiza Yesaya kukapereka uthenga ponena za icho. Nchiyani chimene tingaphunzire kuchokera ku ntchito yake yolalikira?
5 Monga mmene tikanakhalira, chotero Yesaya angakhale anasonkhezeredwa mokakamiza ndi malo amene iye analandira ntchito yake. Iye analemba: “Ine . . . ndinawona Yehova, atakhala pa mpando wachifumu wautali, ndi wotukulidwa, ndi zovala zake zinadzala m’kachisi. Pamwamba pa iye panaima aserafi; yense anali ndi mapiko asanu ndi limodzi; aŵiri anaphimba nawo nkhope yake, aŵiri naphimba nawo mapazi ake, aŵiri nauluka nawo. Ndipo wina anafuula kwa mnzake nati: ‘Woyera, woyera, woyera, Yehova wa makamu. Dziko lonse lapansi ladzala ulemerero wake.’”—Yesaya 6:1-3.
6. Nchifukwa ninji unali mwaŵi kwa Yesaya kuwona zimene anawona?
6 Yesaya anadziŵa kuti Uziya anali atakanthidwa ndi khate pamene iye, wosakhala wa fuko la ansembe, modzikweza analowa m’kachisi Wopatulika kukapereka chonunkhiza. Chotero, ndi mwaŵi wotani nanga kwa Yesaya kuwona kukhalapo kwenikweni kwa Mulungu! Yesaya, munthu wopanda ungwiro, m’lingaliro lenileni sanamuwone Yehova, koma iye analoledwa kumuwona Iye m’masomphenya. (Eksodo 33:20-23) Ukulu wa ichi unawunikiridwa ndi angelo a malo apamwamba (aserafi) amene anatumikira pa mpando wachifumu wa Yehova. Iwo, akuzindikira kuyera kwa Mulungu, mwaulemu anaphimba ‘nkhope zawo.’ Kupyolera m’kachitidwe ka ulemu kameneka, iwo mogogomezera akulengeza kuyera kwa Yehova. Ndi chotulukapo chotani chimene mukulingalira kuti zonsezo zingakhale nacho pa munthu?
7. Ndimotani mmene Yesaya anachitira, ndipo ndimotani mmene tingadzimverere mofananamo?
7 Lolani Yesaya ayankhe. “Ndipo ine ndinati: ‘Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndiri munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga awona Mfumu, Yehova wa makamu!’” (Yesaya 6:5) Yesaya anadziŵa kuti iye anali mlankhuli wa Mulungu, koma masomphenya amenewa anasindikiza pa iye kuti iye anali wonyansa, wosakhala ndi milomo yoyera yomwe ikayenerera mlankhuli wa Mfumu ya ulemerero ndi yoyera imeneyo. Ena a ife, nafenso, nthaŵi zina tingakanthidwe ndi kuchimwa kwathu, osadzimva kukhala oyenera kum’fikira Mulungu m’pemphero, ndipo mocheperapo kukhala ndi dzina lake likutchedwa pa ife. Chokumana nacho chowonjezereka cha Yesaya, chiyenera, kukhala cholimbikitsa.
8. Mngelo anachita utumiki wotani, ndi chotulukapo chotani?
8 Mmodzi wa aserafi otumikirawo anauluka kwa iye ndi makala amoto ochokera pa guwa lansembe za nyama. Akukhudza ndi khalalo kukamwa kwa Yesaya, mngeloyo anati: “Tawona! ichi chakhudza milomo yako; ndipo mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zawomboledwa.” (Yesaya 6:6, 7) M’masiku a Solomo, moto wochokera kumwamba unatsimikizira kuti Yehova anali atalandira nsembe za pa guwa, ngakhale zoperekazo sizikanapanga ansembe kukhala oyera kotheratu pamaso pa Mulungu. (2 Mbiri 7:1-3; Ahebri 10:1-4, 11) Komabe, pamene Yesaya anachotseredwa zoipa zake ndi khala lamoto, iye anakhoza kulandira chiweruzo cha Yehova chakuti kuchimwa kwake kunalipiridwa ku utali wofunikira kulandira ntchito yapadera yolalikira. Ndi zitsanzo zosangalatsa zotani zimene ichi chimalingalira ponena za mtsogolo?
9. Nchiyani chimene chinali nsonga ya uthenga wa Yesaya?
9 Chokumana nacho chosangalatsa chimenechi chinatsogoza mneneriyo kulandira ntchito yolalikira yotchulidwayi. (Yesaya 6:8, 9) Koma nchifukwa ninji Yesaya anayenera kunena kuti anthu mobwerezabwereza anamva koma osapeza chidziŵitso? Mawu a Mulungu akuwonjezera: “Nenepetsa mtima wa anthu awa, lemeretsa makutu awo, nutseke maso awo, kuti asawone . . . nakabwerenso nachiritsidwe.” (Yesaya 6:10) Kodi chimenechi chikutanthauza kuti Yesaya, mogonthetsa kapena mopanda luso, akayenera kukana Ayuda kotero kuti iwo akhalebe pa udani ndi Yehova? Ayi. Ichi chinali kokha chisonyezero chabe cha mmene Ayuda ambiri adzavomerezera mosasamala kanthu kuti ndi mokhulupirika chotani ndiponso ndi mokwanira chotani mmene Yesaya anakwaniritsira ntchito yolalikira kaamba ka imene anadzipereka mwakunena kuti, “Ndine pano! Munditumize ine.”
10. (a) Kodi vuto linali pati m’kukhala kwa anthuwo monga akhungu ndi ogontha? (b) Nchiyani chimene Yesaya anatanthauza mwa kufunsa kuti, “Kufikira liti?”
10 Kulakwa kunali ndi anthuwo. Mosasamala kanthu za kuwalola kwa Yesaya kuti “amve,” iwo sakatenga chidziŵitso kapena kupeza kuzindikira. Mulungu ananeneratu pasadakhale kuti ambiri, chifukwa cha kuuma khosi kwawo ndi kawonedwe kawo kopanda uzimu, sadzavomereza. Ochepa koposa angadzatero. Koma ochulukira adzakhala monga akhungu monga ngati maso awo anatsekedwa ndi utoto wamphamvu koposa, ngati mungalingalire chimenecho. Ndi kuutali wotani kumene mkhalidwe woipa umenewu ukapitirira? Chimenecho, m’malo mwa kutchula ndi zaka zingati zimene iye adzatumikira, ndi chimene Yesaya anafunsa ndi mawu awa: “Mpaka liti, Yehova?” Mulungu anayankha: “Mpaka midzi ikhala bwinja, yopanda wokhalamo.” Ndipo chotero chinachitika, ngakhale kuti pambuyo pa nthaŵi ya moyo ya Yesaya. Ababulo anachotsa anthu a padziko lapansi, kusiya Yuda “wosakazidwa kukhala bwinja.”—Yesaya 6:11, 12; 2 Mafumu 25:1-26.
11. Ndimotani mmene kulalikira kwa Yesaya kunaperekera chitonthozo?
11 Pomalizira, ngakhale kuli tero, Yehova anatsimikizira Yesaya kuti zonse sizinali zopanda chiyembekezo. “Ndipo likatsala limodzi la magawo khumi mmenemo.” Inde, ilo linali ‘ngati mtengo waukulu umene, pakugwetsedwa iwo, padzakhala tsinde, mbewu yopatulika.’ (Yesaya 6:13) Pambuyo pa zaka 70 za kukhala mu ukapolo ku Babulo, mbewu, kapena otsalira, anabwerera kudzikolo, ngati kuti inali mphukira yatsopano yochokera pa tsinde la mtengo waukulu. (2 Mbiri 36:22, 23; Ezara 1:1-4; yerekezani ndi Yobu 14:7-9; Danieli 4:10, 13-15, 26.) Chotero, pamene kuli kwakuti uthenga wa Yesaya unali womvetsa chisoni, unali ndi mbali yotonthoza. Pali chifukwa cha m’Malemba, ngakhale kuli tero, kwa ife kuwona Yesaya monga chitsanzo kaamba ka zochitika za mtsogolo. Motani?
Kukwaniritsidwa Kokulira
12. Ndi maziko a m’Malemba otani amene alipo a kuitanira Yesu monga Yesaya Wamkulu?
12 Zaka mazana angapo pambuyo pa imfa ya Yesaya, wina anabwera amene tingamutche Yesaya Wamkulu—Yesu Kristu. Mu kukhalapo kwake asanakhale munthu, iye anadzipereka kutumizidwa ndi Atate wake kudziko lapansi, kumene iye akaphatikiza m’kulalikira kwake zinthu zimene Yesaya analemba. (Miyambo 8:30, 31; Yohane 3:17, 34; 5:36-38; 7:28; 8:42; Luka 4:16-19; Yesaya 61:1) Mwachindunji kwambiri, Yesu anadziphatikiza iyemwini ndi Yesaya mutu 6 pamene anali kulongosola chifukwa chimene Iye anaphunzitsira monga mmene Anachitira. (Mateyu 13:10-15; Marko 4:10-12; Luka 8:9, 10) Chimenecho chinali choyenera, popeza Ayuda ambiri omwe anamva Yesu sanali ofunitsitsa kulandira uthenga wake ndi kuchita pa iwo monga mmene awo amene anamva mneneri Yesaya sanali ofunitsitsa kulandira uthenga wake. (Yohane 12:36-43) Ndiponso, mu 70 C.E. Ayuda omwe anadzipanga iwo eni kukhala ‘akhungu ndi ogontha’ ku uthenga wa Yesu anakumana ndi chiwonongeko chofanana ndi chija cha mu 607 B.C.E. Chochitika chimenechi mu zana loyamba chinali chisautso pa Yerusalemu ‘chonga chimene sichidakhale chotero kuyambira chiyambi cha dziko lapansi ndipo sichidzachitikanso.’ (Mateyu 24:21) Komabe, monga mmene Yesaya ananeneratu, otsalira, kapena “mbewu yopatulika,” anasonyeza chikhulupiriro. Awa anapangidwa kukhala mtundu wauzimu, “Israyeli wodzozedwa wa Mulungu.”—Agalatiya 6:16.
13. Nchifukwa ninji tingayembekezere kukwaniritsidwa kwina kwa Yesaya mutu 6?
13 Tsopano tifika ku kukwaniritsidwa kwina kozikidwa pa Baibulo kwa Yesaya mutu 6. Monga mfungulo kukumvetsetsa ichi, lingalirani mawu a mtumwi Paulo chifupifupi chaka cha 60 C.E. Iye analongosola chifukwa chimene Ayuda amene anamva iye mu Roma sakanalandira “umboni wake ponena za ufumu wa Mulungu.” Chifukwa chake chinali chakuti Yesaya 6:9, 10 anali kukwaniritsidwanso. (Machitidwe 28:17-27) Kodi ichi chikutanthauza kuti pambuyo pa kuchoka kwa Yesu pa chiwonetsero cha dziko lapansi, ophunzira ake odzozedwa anayenera kupitiriza ntchito yofanana ndi ya Yesaya? Inde, ndithudi!
14. Ndimotani mmene ophunzira a Yesu anayenera kuchitira ntchito yonga ya Yesaya?
14 Yesaya Wamkuluyo asanakwere kumwamba, ananena kuti ophunzira ake adzalandira mzimu woyera ndipo pambuyo pa chimenecho “adzakhala mboni za [iye] ponse paŵiri m’Yerusalemu ndi m’Yudeya monse ndi m’Samariya ndi kufikira malekezero ake adziko.” (Machitidwe 1:8) Mofanana ndi mmene guwa loperekerapo nsembe linaperekera chimene chinafunikira kaamba ka kuchotsa zolakwa za Yesaya, mofananamo nsembe ya Yesu inali maziko kaamba ka ophunzira ake kukhala ndi ‘machimo awo atakhululukidwa.’ (Levitiko 6:12, 13; Ahebri 10:5-10; 13:10-15) Chotero, Mulungu akawadzoza iwo ndi mzimu woyera, womwe ukawapatsanso iwo mphamvu kukhala ‘mboni ku malekezero a dziko lapansi.’ Ponse paŵiri mneneri Yesaya ndi Yesaya Wamkulu anatumizidwa kulengeza uthenga wa Mulungu. Mofananamo, atsatiri odzozedwa a Yesu “anatumizidwa kuchokera kwa Mulungu . . . m’chigwirizano ndi Kristu.”—2 Akorinto 2:17.
15. Nchiyani chimene chakhala yankho la chisawawa ku kulalikira konga kunja kwa Yesaya m’nthaŵi yathu, kuloza ku m’tsogolo motani?
15 M’nthaŵi zamakono, makamaka kuyambira pa mapeto a Nkhondo ya Dziko I, Akristu odzozedwa awona kufunika kwa kulengeza uthenga wa Mulungu. Ichi chimaphatikizapo nsonga yotonthoza yakuti “tsiku la kubwezera la Mulungu wathu” liri pafupi. (Yesaya 61:2) Kusakaza kwake kudzakhala nkhonya makamaka kwa Dziko la Chipembedzo, limene kwanthaŵi yaitali ladzinenera kukhala anthu a Mulungu, monga mmene anachitira Israyeli wakale. Mosasamala kanthu za zaka makumi angapo a kulalikira kokhulupirika kwa mboni zodzozedwa za Mulungu, ambiri m’Dziko la Chipembedzo ‘alemeretsa mitima yawo ndi kutseka makutu awo; ndi maso awo atsekedwa.’ Ulosi wa Yesaya umasonyeza kuti ichi chidzapitiriza kukhala tero “kufikira midzi idzakhala bwinja, yopanda wokhalamo, ndi nyumba zopanda anthu ndi dziko likhala bwinja ndithu.” Ichi chidzasonyeza kutha kwa dongosolo loipa la zinthu iri.—Yesaya 6:10-12.
“Munditumize Ine”
16. Nchifukwa ninji chinganenedwe kuti “khamu lalikulu” likugawanamo m’ntchito yofanana ndi ija ya Yesaya?
16 Lerolino, pali mamiliyoni a Akristu odzipereka omwe ali ndi chiyembekezo cha m’Baibulo cha kukhala kosatha mu paradaiso padziko lapansi. Pa maziko ansembe ya mwazi wa Yesu, “khamu lalikulu” limeneli lingakhululukidwe machimo awo kumlingo woyenera tsopano. Iwo nawonso amalandira mphamvu ndi chichirikizo kupyolera mwa mzimu wa Mulungu pamene agwirizana ndi chiŵerengero chotsalira cha Akristu odzozedwa m’kunena kuti, “Ndine pano! Munditumize ine.” Kuwatumiza kukachita chiyani? Paulo akunena pa Aroma 10:13-15: “‘Amene aliyense adzaitanira pa dzina la [Yehova, NW] adzapulumuka.’ Komabe, iwo adzaitana bwanji pa iye amene sanamkhulupirira? Ndipo, adzakhulupirira bwanji iye amene sanamva za iye? Ndipo, adzamva bwanji popanda wolalikira? Ndipo adzalalikira bwanji ngati satumidwa? Monganso kwalembedwa [pa Yesaya 52:7]: ‘Okometsetsa ndithu ali mapazi a iwo akulalikira uthenga wabwino wa zinthu zabwino!’”—Chivumbulutso 7:9-15.
17. Kuyerekeza ndi ulosi wa Yesaya, nchiyani chimene chiri mbali ya uthenga wathu?
17 Kumbukirani kuti iye anayankha asanadziŵe zinthu zonse za uthenga pamene Yesaya ananena kuti, “Ndine Pano! Munditumize ine.” Mosiyanako, timadziŵa chimene Mulungu akufuna kuti chilalikidwe tsopano ndi awo amene akuvomereza kuchiitano chake: “Ndidzatumiza yani, ndani adzatimukira ife?” Chimaphatikizapo chenjezo lapasadakhale lonena za “tsiku la kubwezera la Mulungu wathu.” Komabe, uthengawo umaphatikizanso “mbiri yabwino ya zinthu zabwino.” Mwachitsanzo, awo amene “akutumizidwa” amagawana m’kulalikira “ufulu kwa awo omangidwa msinga ndi kutsegulidwa maso kwa andende.” Kodi kuchita chimenechi sikuyenera kukhala magwero a chikhutiritso chokulira?—Yesaya 61:1, 2, NW.
18, 19. Ndi m’njira zapadera zotani m’zimene ambiri akunena kuti, “Munditumize ine”?
18 Ngati inu mukulalikira kale “mbiri yabwino ya zinthu zabwino,” kubwereramo uku kwa Yesaya mutu 6 kungakufulumizeni inu kufunsa kuti: Kodi ndingavomereze motani mokulira koposa mu mzimu wa Yesaya 6:8? Mofanana ndi anthu aŵiri otchulidwa poyambirirapo m’nkhaniyi, mazana agawanamo mu programu ya Ogwira Ntchito Yomanga Odzipereka a Dziko Lonse. Ambiri owonjezereka, amene alibe maluso akumanga, apita ku malo kumene chifuno kaamba ka alaliki a Ufumu chiri chokulira. Ichi chimachitidwa bwino koposa mwakufunafuna thandizo kuchokera ku ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society. Ndithudi, kukonzekera kuli kofunika koposa, kaamba ka chinenero, mikhalidwe ya kakhalidwe, ziyembekezo za ntchito, ndi zinthu zina zimene zingakhale zosiyana kwambiri m’dziko lachilendo. Komabe, musataye kuthekera kuchoka m’manja mwanu kokha chifukwa chakuti masinthidwe okulira angafunikire kuchitidwa. Ambiri amene akhala ndi kawonedwe ka “Ndine pano! Munditumize ine” apanga machitidwe oterowo ndipo akhala odalitsidwa molemerera ndi Mulungu kaamba ka kuchita tero.—Yerekezani ndi Miyambo 24:27; Luka 14:28-30.
19 Ndipo enabe—abale kapena alongo osakwatira, anthu okwatira, ndipo ngakhale mabanja athunthu—apita ku malo ena m’dziko lawo kapena dera kumene kufuna kaamba ka alaliki a Ufumu kapena oyang’anira Achikristu kuli kokulira. (Machitidwe 16:9, 10) Kuchita tero kungafunikire kupanga kudzipereka kwina, monga ngati kupeza mtundu wina wa ntchito yakuthupi, mwinamwake ina yokhala ndi malipiro ochepa. Ena afunsira kuleka kugwira ntchito mwamsanga mwa kukhala ndi ndalama za penshoni zochepera ndi kupeza ntchito ya pa kanthaŵi kotero kuti akhale ndi nthaŵi yochuluka mu utumiki. Chiri chosangalatsa chotani nanga pamene banja lonse linena kuti, “Ndife pano! Titumizeni ife.” Ichi, nachonso, chimawonetsera mkhalidwe wa Yesaya. Mkazi wake mokangalika anagawanamo m’kuchita chifuniro cha Mulungu monga mneneri wachikazi, ndipo ana ake anakhudzidwa mu uthenga wa ulosi.—Yesaya 7:3, 14-17; 8:3, 4.
20. Ndi Yesaya 6:8 m’maganizo, nchiyani chimene muyenera kulingalira?
20 Ngakhale ngati mikhalidwe yanu sikulolani kuchita masinthidwe a akulu oterowo, mungalingalirepo, ‘Kodi ndikuchita chirichonse chimene ndingathe kumene ndiri, kutsanzira kuvomereza kwa Yesaya?’ Dzikakamizeni inu eni kulengeza uthenga wa Mulungu, ngakhale m’mikhalidwe yoipa kapena m’kuyang’anizana ndi kusiyana kwa unyinji; mwachidziŵikire, Yesaya anachita mofananamo. Khalani achangu m’kulankhula kwa ena ponena za “mbiri yabwino ya zinthu zabwino!” Yehova wanena kuti, “Ndidzatumiza yani?” Tsimikizirani kuti, mofanana ndi Yesaya wakale, yankho lanu liri lakuti, “Ndine pa-no! Munditumize ine” kukalalikira uthenga Wake.
Nsonga za Kubwereramo
◻ Ndi m’mikhalidwe yotani mmene Yesaya analandira masomphenya a mutu 6, ndipo nchiyani chimene iye anawona?
◻ Ndi ntchito ya mtundu wanji imene Yesaya analandira?
◻ Nchifukwa ninji Yesu angatchedwe Yesaya Wamkulu, ndipo ndimotani mmene ophunzira ake akukhudzidwira m’ntchito yonga ya Yesaya?
◻ Ndimotani mmene mungasonyezere mzimu wonga uja wa Yesaya?
[Chithunzi patsamba 17]
Yesaya anayeretsedwa ndi kutumizidwa kukalalikira
[Chithunzi patsamba 18]
Ambiri ayankha, kunena kuti “Ndine pano! Munditumize ine”