Kodi Ukwati Ndiwo Mfungulo Yokha ya Chimwemwe?
“Ali womasuka, kuti akwatiwe naye amene afuna, koma mwa Ambuye. Koma akhala wokondwera koposa ngati akhala monga momwe ali.”—1 AKORINTO 7:39, 40.
1. Kodi Malemba amamfotokoza motani Yehova, ndipo kodi iye wazichitira chiyani zolengedwa zake?
YEHOVA ndiye “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Monga Wogaŵira Wowoloŵa Manja wa ‘mphatso iriyonse yabwino, ndi chininkho chirichonse changwiro,’ amapatsa zolengedwa zake zonse zaluntha—zaumunthu ndi zauzimu—zinthu zenizenizo zimene afunikira kuti akhale achimwemwe muutumiki wake. (Yakobo 1:17) Chifukwa cha chimenecho, mbalame yoimba nyimbo, nkhanda yothamangathamanga mokondwa, kapena nsomba ya dolphin yoseŵera, zonsezi zimachitira umboni wakuti Yehova analenga nyama kuti nazonso zisangalale ndi moyo m’malo awo okhala oyenerera. Wamasalmo amapitiriza kunenadi mwandakatulo kuti “mitengo ya Mulungu yadzala ndi madzi; mikungudza ya ku Lebano imene anaioka.”—Salmo 104:16.
2. (a) Kodi nchiyani chikusonyeza kuti Yesu amapeza chimwemwe pochita chifuniro cha Atate wake? (b) Kodi ophunzira a Yesu anali ndi zifukwa zotani zokhalira ndi chimwemwe?
2 Yesu Kristu ndiye ‘chizindikiro chenicheni cha chikhalidwe cha Mulungu mwiniyo.’ (Ahebri 1:3) Pamenepa, nkosadabwitsa kuti Yesu ayenera kutchedwa “Mwini Mphamvu wodala.” (1 Timoteo 6:15) Iye amatipatsa chitsanzo chabwino kwambiri cha mmene kuchita chifuniro cha Yehova kungakhalire kokhutiritsa koposa chakudya, kukumapereka chisangalalo chowona. Yesu amatisonyezanso kuti pangakhale chisangalalo pochita zinthu mowopa Mulungu, ndiko kuti, ndi ulemu waukulu ndi kuwopa kusamkondweretsa Iye. (Salmo 40:8; Yesaya 11:3; Yohane 4:34) Pamene ophunzira 70 anabwerera “mokondwera” pambuyo pa ulendo wolalikira Ufumu, Yesu mwiniyo ‘anakondwera ndi mzimu woyera.’ Atalankhula za chikondwerero chake kwa Atate wake m’pemphero, anatembenukira kwa ophunzirawo naati: ‘Odala masowo akuwona zimene muwona. Pakuti ndinena ndi inu kuti aneneri ndi mafumu ambiri anafuna kuwona zimene inu muziwona, koma sanaziwona; ndi kumva zimene mukumva, koma sanazimva.’—Luka 10:17-24.
Zifukwa Zokhalira Achimwemwe
3. Kodi nzifukwa zina zotani zokhalira ndi chimwemwe?
3 Kodi maso athu sayenera kukhala odala kuwona zinthu zimene tikuwona m’kukwaniritsidwa kwa Mawu ndi zifuno za Yehova m’nthaŵi ino yamapeto? Kodi sitiyenera kukondwera kwambiri kuti tikuzindikira maulosi amene aneneri ndi mafumu okhulupirika onga ngati Yesaya, Danieli, ndi Davide sanawamvetsetse? Kodi sitiri osangalala kutumikira Mulungu wachimwemwe, Yehova, pansi pa utsogoleri wokangalika wa Mwini Mphamvu wodala, Mfumu yathu Yesu Kristu? Ndithudi tiri osangalala!
4, 5. (a) Kodi tiyenera kupeŵa chiyani kuti tikhalebe achimwemwe muutumiki wa Yehova? (b) Kodi nzinthu zina zotani zimene zimapangitsa chimwemwe, ndipo kodi zimenezi zimadzutsa funso lotani?
4 Komabe, ngati tikufuna kukhalabe achimwemwe muutumiki wa Mulungu, sitiyenera kuzika zofunikira zathu zopezera chimwemwe pa malingaliro akudziko. Malingalirowa angaphimbe kuganiza kwathu chifukwa amaphatikizapo chuma chakuthupi, umoyo wodziwonetsera, ndi zina zotero. ‘Chimwemwe’ chirichonse chozikidwa pa zinthu zoterozo chidzakhala chakanthaŵi kochepa, popeza kuti dzikoli lipita.—1 Yohane 2:15-17.
5 Atumiki ambiri odzipereka a Yehova amazindikira kuti kufikira zonulirapo zakudziko sikudzabweretsa chimwemwe chowona. Atate wathu wakumwamba yekha ndiye amapereka zinthu zauzimu ndi zakuthupi zomwe zimabweretsa chimwemwe chenicheni kwa atumiki ake. Ndife oyamikira chotani nanga kaamba ka chakudya chauzimu chimene amatipatsa kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”! (Mateyu 24:45-47) Tirinso oyamikira chifukwa cha chakudya chakuthupi ndi zinthu zina zakuthupi zimene timalandira kuchokera kudzanja lachikondi la Mulungu. Ndiyeno, palinso mphatso yabwino koposa ya ukwati ndi zosangalatsa za moyo wa banja. Nkosadabwitsa kuti chikhumbo chamtima wonse cha Naomi kwa apongozi ake amasiye chinafotokozedwa m’mawu aŵa: ‘Yehova [akupatseni mphatso, NW] mupeze mpumulo yense m’nyumba ya mwamuna wake.’ (Rute 1:9) Chotero ukwati ndiwo mfungulo imene ingatsegule khomo lopezera chimwemwe chachikulu. Koma kodi ukwati ndiwo mfungulo yokha yotsegulira chipata choloŵera kumoyo wachimwemwe? Makamaka achichepere ayenera kusanthula mosamalitsa ngati ziri tero.
6. Malinga ndi Genesis, kodi chifuno chenicheni cha ukwati chinali chiyani?
6 Pofotokoza chiyambi cha ukwati, Baibulo limati: ‘Mulungu ndipo adalenga munthu m’chifanizo chake, m’chifanizo cha Mulungu adamlenga iye; adalenga iwo mwamuna ndi mkazi, Mulungu ndipo anadalitsa iwo, ndipo adati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse.’ (Genesis 1:27, 28) Pamene Yehova anakhazikitsa ukwati, Adamu anagwiritsiridwa ntchito kubala zolengedwa zowonjezereka za umunthu, mwakutero kufutukula fuko la anthu. Koma ukwati umatanthauza zoposa zimenezi.
“Mwa Ambuye”
7. Kodi ndi chiyeneretso chaukwati chotani chimene kholo lina lokhulupirika linapanga zoyesayesa zazikulu zakuchikwaniritsa?
7 Popeza kuti Yehova Mulungu ndiye Woyambitsa ukwati, tikayembekezera kuti akakhazikitsa miyezo ya ukwati umene ukabweretsera atumiki ake chimwemwe. M’nthaŵi za makolo akale, kukwatirana ndi awo amene sanali olambira Yehova kunaletsedwa mwamphamvu. Abrahamu analumbiritsa mtumiki wake Eliezere pali Yehova kuti sakatengera mwana wa kholo lakalelo, Isake, mkazi kwa Akanani. Eliezere anapanga ulendo wautali ndipo analabadira mosamalitsa malangizo a Abrahamu kotero kuti akapeze ‘mkazi amene Yehova amsankhira mwana wa mbuyake.’ (Genesis 24:3, 44) Chotero Isake anakwatira Rebeka. Pamene mwana wawo Esau anasankha akazi pakati pa Ahiti achikunja, akazi ameneŵa “anapweteka mtima wa Isake ndi wa Rebeka.”—Genesis 26:34, 35; 27:46; 28:1, 8.
8. Kodi pangano la Chilamulo linaika chiletso chotani pa ukwati, ndipo nchifukwa ninji?
8 Pansi pa pangano la Chilamulo, kukwatira amuna kapena akazi a mitundu yakutiyakuti Yachikanani kunali koletsedwa. Yehova analangiza anthu ake kuti: ‘Musakwatitsane nawo; musampatse mwana wake wamwamuna mwana wanu wamkazi, kapena kutenga mwana wake wamkazi akhale wa mwana wanu wamwamuna. Popeza adzapatutsa mwana wanu aleke kunditsata ine, kuti atumikire milungu ina; potero Yehova adzapsa mtima pa inu, ndipo adzakuwonongani msanga.’—Deuteronomo 7:3, 4.
9. Kodi Baibulo limapereka uphungu wotani kwa Akristu ponena za ukwati?
9 Nkosadabwitsa kuti ziletso zofananazo za kusakwatira awo amene salambira Yehova ziyenera kugwira ntchito mu mpingo Wachikristu. Mtumwi Paulo anachenjeza okhulupirira anzake kuti: ‘Musakhale omangidwa m’goli ndi osakhulupira osiyana; pakuti chilungamo chigawana bwanji ndi chosalungama? Kapena kuunika kuyanjana bwanji ndi mdima? Ndipo Kristu avomerezana bwanji ndi Beliyali? Kapena wokhulupira ali nalo gawo lanji pamodzi ndi wosakhulupira?’ (2 Akorinto 6:14, 15) Uphungu umenewo umagwira ntchito m’njira zambiri ndipo umakhudzadi ukwati. Malangizo achindunji a Paulo kwa atumiki onse odzipereka a Yehova ngakuti ayenera kulingalira kukwatira winawake “kokha ngati iye ali muumodzi ndi Ambuye.”—1 Akorinto 7:39, NW, mawu amtsinde.
Wosakhoza Kukwatira “mwa Ambuye”
10. Kodi Akristu ambiri osakwatira akuchitanji, ndipo ndifunso lotani lomwe limabuka?
10 Akristu ambiri osakwatira asankha kulabadira chitsanzo cha Yesu Kristu mwakukulitsa mphatso ya umbeta. Ndiyeno, chifukwa chokhala osakhoza kupeza munthu wowopa Mulungu ndipo kuti akwatire “mwa Ambuye,” Akristu ambiri okhulupirika aika chidaliro chawo mwa Yehova ndipo akhala mbeta m’malo mokwatira wosakhulupirira. Mzimu wa Mulungu umawabweretsera zipatso zonga chimwemwe, mtendere, chikhulupiriro, ndi kudziletsa, zowatheketsa kusungabe umbeta woyera. (Agalatiya 5:22, 23) Pakati pa awo amene akulaka mwachipambano chiyeso chimenechi cha kudzipereka kwa Mulungu pali chiŵerengero chachikulu cha alongo athu Achikristu, omwe timawalemekeza kwambiri. M’maiko ambiri, chiŵerengero chawo chimaposa cha abale ndipo chotero amachita mbali yaikulu ya ntchito yolalikira. Ndithudi, ‘[Yehova, NW] anapatsa mawu: akazi akulalikira uthengawo ndiwo khamu lalikulu.’ (Salmo 68:11) Kwenikweni, atumiki ambiri a Mulungu osakwatira, ponse paŵiri amuna ndi akazi, akusunga umphumphu wawo chifukwa chakuti ‘akukhulupirira Yehova ndi mtima wawo wonse, ndipo iye akuwongola mayendedwe awo.’ (Miyambo 3:5, 6) Koma kodi amene panthaŵi ino sangakwatire “mwa Ambuye” adzakhala opanda chimwemwe?
11. Kodi Akristu amene amakhala mbeta chifukwa cha malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo angatsimikiziridwe za chiyani?
11 Tiyeni tikumbukire kuti ndife Mboni za Mulungu wachimwemwe, Yehova, tikutumikira pansi pa Mwini Mphamvu wodala, Yesu Kristu. Chotero ngati kulemekeza kwathu ziletso zomvekera bwino zoikidwa m’Baibulo kutipangitsa kukhala mbeta chifukwa chosapeza wokwatirana naye “mwa Ambuye,” kodi nkwanzeru kuganiza kuti Mulungu ndi Kristu akatisiya opanda chimwemwe? Ndithudi ayi. Chifukwa chake, tiyenera kutsimikiza kuti nkotheka kukhala achimwemwe monga Akristu pamene tiri mumkhalidwe wosakwatira. Yehova angatipangitsedi kukhala achimwemwe kaya ndife okwatira kapena mbeta.
Mfungulo ya Chimwemwe Chowona
12. Kodi nkhani ya angelo opanduka imasonyeza chiyani ponena za ukwati?
12 Ukwati sindiwo mfungulo yokha ya chimwemwe kwa atumiki onse a Mulungu. Mwachitsanzo, talingalirani za angelo. Chigumula chisanadze, angelo ena anakhala ndi zikhumbo zosakhala zachilengedwe chawo monga zolengedwa zauzimu, sanakhutire ndi chenicheni chakuti sakakhoza kukwatira, ndipo anavala matupi aumunthu kuti adzakwatire akazi. Chifukwa chakuti angelo ameneŵa ‘sanasunga chikhalidwe chawo choyamba,’ Mulungu ‘adawasunga [iwo] m’ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.’ (Yuda 6; Genesis 6:1, 2) Momvekera bwino, Mulungu sanalinganize konse kuti angelo akwatire. Chotero ukwati sungakhale konse mfungulo ya chimwemwe chawo.
13. Kodi nchifukwa ninji angelo oyera ali achimwemwe, ndipo kodi ichi chimasonyeza chiyani kwa atumiki onse a Mulungu?
13 Komabe, angelo okhulupirikawo ali achimwemwe. Yehova anayala maziko a dziko lapansi “kugulu losangalala la nyenyezi za m’maŵa ndi kuomba m’manja kwachimwemwe kwa ana [aungelo] a Mulungu.” (Yobu 38:7, The New Jerusalem Bible) Kodi nchifukwa ninji angelo opatulikawo ali achimwemwe? Chifukwa chakuti amatumikira Yehova Mulungu mosalekeza, ‘akumamvera liwu la mawu ake’ kuti awachite. Amakondwera ‘kuchita chomkondweretsa.’ (Salmo 103:20, 21, NW, mawu amtsinde) Inde, chimwemwe cha angelo opatulikawo chimadza chifukwa chotumikira Yehova mokhulupirika. Imeneyo ndiyo mfungulo ya chimwemwe chowona kwa anthunso. Pachifukwa chimenecho, Akristu odzozedwa okwatira omwe akutumikira Mulungu mwachimwemwe tsopano sadzakwatira akadzaukitsidwa ku moyo wakumwamba, koma adzakhala achimwemwe monga zolengedwa zauzimu zochita chifuniro cha Mulungu. Pamenepo, kaya ngokwatira kapena mbeta, atumiki okhulupirika onse a Yehova angakhale achimwemwe chifukwa chakuti maziko enieni a chimwemwe ndiwo utumiki wokhulupirika kwa Mlengi.
‘Kanthu Kena Kabwino Kwambiri Koposa Ana Aamuna ndi Aakazi’
14. Kodi ndilonjezo laulosi lotani lomwe linaperekedwa kwa mifule yaumulungu mu Israyeli wakale, ndipo kodi nchifukwa ninji lingawoneke kukhala lachilendo?
14 Ngakhale ngati Mkristu wokhulupirika sakwatira, Mulungu angampatse iye chimwemwe. Akhoza kupeza chilimbikitso ku mawu amene molosera ananenedwa kwa mifule ya mu Israyeli wakale: ‘Pakuti atero Yehova kwa mifule imene isunga masabata, nisankha zinthu zimene zindikondweretsa ine, nigwira zolimba chipangano changa, kwa iyo ndidzapatsa m’nyumba yanga ndi mkati mwa makoma anga malo, ndi dzina [kanthu kena kabwino kwambiri koposa, NW] ana aamuna ndi aakazi; ndidzawapatsa dzina lachikhalire limene silidzadulidwa.’ (Yesaya 56:4, 5) Munthuwe ungayembekezere kuti iwo akalonjezedwa mkazi ndi ana kuti apititse patsogolo dzina lawo. Koma analonjezedwa dzina ‘loposa ana aamuna ndi aakazi’—dzina lachikhalire m’nyumba ya Yehova.
15. Kodi tinganenenji ponena za kukwaniritsidwa kwa Yesaya 56:4, 5?
15 Ngati mifule imeneyi ilingaliridwa kukhala chithunzithunzi cha ulosi cha “Israyeli wa Mulungu,” iwo amaimira odzozedwa amene amalandira malo osatha mkati mwa nyumba yauzimu, kapena kachisi wa Yehova. (Agalatiya 6:16) Mosakaikira, ulosi umenewu udzagwiranso ntchito m’lingaliro lenileni kwa mifule yowopa Mulungu ya Israyeli wakale imene idzaukitsidwa. Ngati alandira nsembe ya dipo ya Kristu ndi kupitirizabe kusankha zimene zimakondweretsa Yehova, adzalandira ‘dzina lachikhalire’ m’dziko latsopano la Mulungu. Zikagwiranso ntchito kwa awo a “nkhosa zina” amene m’nthaŵi yamapeto ino amalepa ukwati ndi ukholo kuti adzipereke kotheratu kuutumiki wa Yehova. (Yohane 10:16) Ena a ameneŵa angafe ali osakwatira ndi opanda ana. Koma ngati ali okhulupirika, m’chiukiriro adzalandira ‘kanthu kena kabwino kwambiri koposa ana aamuna ndi aakazi’—dzina limene ‘silidzadulidwa’ m’dongosolo latsopano.
Ukwati Sindiwo Mfungulo Yokha ya Chimwemwe
16. Kodi nchifukwa ninji tinganene kuti ukwati sumabweretsa chimwemwe nthaŵi zonse?
16 Anthu ena amaganiza kuti chimwemwe chimapezeka mu ukwati nthaŵi zonse. Komabe, tiyenera kuvomereza kuti ngakhale pakati pa atumiki a Yehova lerolino, ukwati sumabweretsa chimwemwe nthaŵi zonse. Umathetsa mavuto ena koma kaŵirikaŵiri umachititsa ena amene angakhale ovuta kuwalaka kuposa amene amayang’anizana ndi anthu osakwatira. Paulo ananena kuti ukwati umabweretsa ‘chisautso m’thupi.’ (1 Akorinto 7:28) Pamakhala nthaŵi zina pamene munthu wokwatira amakhala ndi “nkhaŵa” ndi “wogawanika.” Kaŵirikaŵiri amakupeza kukhala kovuta “kutsata chitsatire Ambuye opanda chocheukitsa.”—1 Akorinto 7:33-35, NW.
17, 18. (a) Kodi oyang’anira oyendayenda ena asimba chiyani? (b) Kodi Paulo anapereka uphungu wotani, ndipo nchifukwa ninji uli wopindulitsa kuugwiritsira ntchito?
17 Ukwati ndi umbeta womwe ndizo mphatso zochokera kwa Mulungu. (Rute 1:9; Mateyu 19:10-12) Komabe, kuti mupambane mumkhalidwe uliwonse wa iŵiriyo, nkofunika kulingalira mwapemphero. Oyang’anira oyendayenda akusimba kuti Mboni zambiri zikukwatira ziri zachichepere kwambiri, kaŵirikaŵiri kukhala makolo asanakonzekere kusenza mathayo otulukapo. Ena a maukwati ameneŵa amasweka. Okwatirana ena amachita ndi mavuto awo, koma ukwati wawo sunawabweretsere chimwemwe. Monga momwe wolemba maseŵero wina Wachingelezi William Congreve analembera, amene amafulumira kukwatira “angamve chisoni potsirizira pake.”
18 Oyang’anira dera akusimbanso kuti abale ena achichepere amapeŵa kufunsira utumiki wa pa Beteli kapena kudzipereka mwaufulu ku Sukulu Yamaphunziro Autumiki chifukwa cha kuwopa chiyeneretso cha kukhala mbeta kwa kanthaŵi. Koma Paulo akupereka uphungu wakuti munthu asakwatire ‘asanapitirire unamwali wake,’ kutanthauza kuti afunikira kudikirira kufikira chisonkhezero chakugonana choyambirira chitachepa. (1 Akorinto 7:36-38) Zaka zokhala wekha monga mbeta yachikulire zimapatsa munthuwe kuzoloŵera ndi chidziŵitso chamtengo wake, kukuika pamalo abwino akusankha mnzako wamuukwati kapena kupanga chosankha cholingaliridwa bwino chakukhala mbeta.
19. Ngati tiribe chosoŵa chenicheni chakukwatira kodi tingailingalire motani nkhaniyo?
19 Enafe tinapitirira unamwali, wokhala ndi zisonkhezero zamphamvu zakugonana. Nthaŵi zina tingalingalire za madalitso a ukwati koma kwenikweni tiri ndi mphatso ya umbeta. Yehova angawone kuti timamtumikira mogwira mtima mumkhalidwe waumbeta ndipo tiribe chifuno chenicheni chakukwatira, chomwe chingatipangitse kuleka mathayo ena muutumiki wake. Ngati ukwati suli chosoŵa chathu chaumwini ndipo sitinakhale ndi mwaŵi wakupeza mnzathu wamuukwati, Mulungu angakhale watisungira kenakake kutsogolo. Chotero tiyeni tisonyeze chikhulupiriro kuti adzapereka zosoŵa zathu. Chimwemwe chachikulu timachipeza mwakuvomereza modzichepetsa zimene zimawoneka kukhala chifuniro cha Mulungu kwa ife, monga momwedi abale Achiyuda ‘anakhala du, nalemekeza Mulungu’ pamene anazindikira kuti anapatsa Akunja mwaŵi wakulapa kotero kuti akakhale ndi moyo.—Machitidwe 11:1-18.
20. (a) Kodi ndiuphungu wotani wonena za umbeta umene waperekedwa pano kwa Akristu achichepere? (b) Kodi ndimfundo yaikulu yotani yonena za chimwemwe yomwe ikhalabe yowona?
20 Pamenepo, ukwati ungakhale mfungulo yopezera chimwemwe, ngakhale kuti ungatsegulenso khomo ku mavuto. Chinthu chimodzi nchotsimikizirika: Ukwati sindiwo njira yokha yopezera chimwemwe. Chotero, mutalingalira zinthu zonse, kukakhala kwanzeru, makamaka kwa Akristu achichepere, kuyesa kupereka mpata kukhala mbeta kwa zaka zingapo. Zaka zimenezo zingagwiritsiridwe ntchito kutumikira Yehova ndi kupita patsogolo mwauzimu. Komabe, mosasamala kanthu za msinkhu kapena chidziŵitso chauzimu, mfundo yaikulu imene imakhalabe yowona kwa onse odzipereka kotheratu kwa Mulungu ndi iyi: Chimwemwe chowona chimapezeka muutumiki wokhulupirika kwa Yehova.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji atumiki a Yehova ali achimwemwe?
◻ Kodi nchifukwa ninji ukwati suli mfungulo ya chimwemwe chachikulu koposa?
◻ Posankha mnzawo wamuukwati, kodi nchiyani chimafunikira kwa anthu a Yehova?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kwanzeru kukhulupirira kuti Akristu amene amakhalabe mbeta angakhale achimwemwe?
◻ Kodi tiyenera kuvomereza chiyani ponena za ukwati ndi chimwemwe?