Nkhosa Zina ndi Pangano Latsopano
“Alendonso . . . , yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba chipangano changa; nawonso ndidzamka nawo ku phiri langa lopatulika.”—YESAYA 56:6, 7.
1. (a) Malinga ndi masomphenya a Yohane, kodi chikumalizidwa nchiyani pamene mphepo ya Yehova yachiweruzo yagwidwa? (b) Kodi ndi khamu lochititsa chidwi liti limene Yohane anaona?
M’MASOMPHENYA achinayi a m’buku la Chivumbulutso, mtumwi Yohane anaona mphepo yowononga ya chiweruzo cha Yehova itagwidwa pamene anali kumaliza kusindikiza chizindikiro onse a “Israyeli wa Mulungu.” Awa ndiwo oyambirira kulandira madalitso kudzera mwa Yesu, mbewu ya Abrahamu yaikulu. (Agalatiya 6:16; Genesis 22:18; Chivumbulutso 7:1-4) M’masomphenya omwewo, Yohane anaona “khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, . . . afuula ndi mawu akulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.” (Chivumbulutso 7:9, 10) Pamene anena kuti, “Chipulumutso kwa . . . Mwanawankhosa,” a khamu lalikulu akusonyeza kuti nawonso adalitsidwa mwa Mbewu ya Abrahamu.
2. Kodi khamu lalikulu linaoneka liti, ndipo kodi likuzindikiridwa motani?
2 Khamu lalikulu limeneli linazindikiridwa kalelo mu 1935, ndipo lerolino lili ndi chiŵerengero choposa mamiliyoni asanu. Pokhala olembedwa chizindikiro kuti ndiwo odzapulumuka pachisautso chachikulu, mamembala ake adzapatulidwira ku moyo wosatha pamene Yesu adzamaliza kulekanitsa “nkhosa” ndi “mbuzi.” Akristu a m’khamu lalikulu ali m’gulu la “nkhosa zina” zonenedwa m’fanizo la Yesu la makola a nkhosa. Iwo ali ndi chiyembekezo cha kukhala ndi moyo kosatha m’paradaiso wa padziko lapansi.—Mateyu 25:31-46; Yohane 10:16; Chivumbulutso 21:3, 4.
3. Kodi Akristu odzozedwa ndi a nkhosa zina ali osiyana motani m’nkhani ya pangano latsopano?
3 A 144,000 amalandira madalitso a pangano la Abrahamu kudzera m’pangano latsopano. Monga otengamo mbali m’pangano limeneli, iwo amakhala “a chisomo” ndi ‘omvera lamulo kwa Kristu.’ (Aroma 6:15; 1 Akorinto 9:21) Choncho, mamembala 144,000 okha a Israyeli wa Mulungu ndiwo amadya moyenerera zizindikiro za pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu, ndipotu ndi okhawa amene Yesu anapangana nawo pangano la Ufumu. (Luka 22:19, 20, 29) A khamu lalikulu satengamo mbali m’pangano latsopanoli. Komabe, iwo amagwirizana ndi Israyeli wa Mulungu ndipo amakhala nawo “m’dziko” lawo. (Yesaya 66:8) Nchifukwa chake kuli koyenerera kunena kuti nawonso ali ndi chisomo cha Yehova ndiponso ali omvera lamulo kwa Kristu. Ngakhale kuti satengamo mbali m’pangano latsopanolo, iwo amapindula nalo.
“Alendo” ndi “Israyeli wa Mulungu”
4, 5. (a) Malinga nkunena kwa Yesaya, kodi ndi gulu liti limene lidzatumikira Yehova? (b) Kodi Yesaya 56:6, 7 akukwaniritsidwa motani kwa a khamu lalikulu?
4 Mneneri Yesaya analemba kuti: “Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire Iye, ndi kukonda dzina la Yehova, akhale atumiki ake, yense amene asunga sabata osaliipitsa, nagwira zolimba chipangano changa; nawonso ndidzamka nawo ku phiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo zidzalandiridwa pa guwa lansembe langa.” (Yesaya 56:6, 7) Mu Israyeli, zimenezi zinatanthauza kuti “alendo,” osakhala Aisrayeli, anali ndi mwaŵi wolambira Yehova—kukonda dzina lake, kutsatira zofunika m’pangano la Chilamulo, kusunga Sabata, ndi kupereka nsembe pakachisi, ‘nyumba yopemphereramo’ ya Mulungu.—Mateyu 21:13.
5 M’tsiku lathu, “alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova” ndiwo a khamu lalikulu. Amenewa amatumikira Yehova mogwirizana ndi Israyeli wa Mulungu. (Zekariya 8:23) Iwo amaperekanso nsembe zolandiridwa monga momwe amachitira Israyeli wa Mulungu. (Ahebri 13:15, 16) Amalambirira m’kachisi wauzimu wa Mulungu, “nyumba [yake] yopemphereramo.” (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 7:15.) Kodi iwo amasunga Sabata mlungu uliwonse? Odzozedwa ngakhalenso a nkhosa zina sanalamulidwe kuchita zimenezo. (Akolose 2:16, 17) Komabe, Paulo ananena kwa Akristu achihebri odzozedwa kuti: “Momwemo utsalira mpumulo wa Sabata wa kwa anthu a Mulungu. Pakuti iye amene adaloŵa mpumulo wake, adapumulanso mwini wake ku ntchito zake, monganso Mulungu ku zake za Iye.” (Ahebri 4:9, 10) Ahebri amenewo analoŵa mu “mpumulo wa Sabata” umenewu pamene anagonjera ku “chilungamo cha Mulungu” ndi kupumula pa kuyesayesa kwawo kukhala mogwirizana ndi ntchito za Chilamulo. (Aroma 10:3, 4) Akristu Akunja Odzozedwa amasangalala ndi kupumula kofananako mwa kugonjera ku chilungamo cha Yehova. A khamu lalikulu amapumulanso pamodzi nawo.
6. Kodi a nkhosa zina amagonjera motani pangano latsopano lerolino?
6 Ndiponso, a nkhosa zina amagonjera pangano latsopano mongadi momwe alendo akale anagonjera pangano la Chilamulo. Motani? Osati mwa kukhala otengamo mbali ayi koma mwa kugonjera ku malamulo ogwirizana nalo ndi kupindula ndi makonzedwe ake. (Yerekezerani ndi Yeremiya 31:33, 34.) Monga anzawo odzozedwawo, a nkhosa zina ali ndi lamulo la Yehova lolembedwa ‘m’mtima mwawo.’ Iwo amamkonda kwambiri Yehova ndipo amatsatira malamulo ndi mapulinsipulo ake. (Salmo 37:31; 119:97) Mofanana ndi Akristu odzozedwa, iwo amamdziŵadi Yehova. (Yohane 17:3) Nanga bwanji ponena za mdulidwe? Zaka pafupifupi 1,500 pangano latsopano lisanakhazikitsidwe, Mose analimbikitsa Aisrayeli kuti: “Dulani khungu la mitima yanu.” (Deuteronomo 10:16; Yeremiya 4:4) Pamene kuli kwakuti mdulidwe wokakamiza wakuthupi unathera pamodzi ndi Chilamulo, odzozedwa ndi a nkhosa zina omwe ayenera ‘kudula’ mitima yawo. (Akolose 2:11) Pomaliza, Yehova amakhululukira machimo a nkhosa zina pamaziko a ‘mwazi wa pangano’ wokhetsedwa wa Yesu. (Mateyu 26:28; 1 Yohane 1:9; 2:2) Mulungu sawatenga iwo kukhala ana ake auzimu, monga momwe amachitira ndi a 144,000. Koma a nkhosa zina amayesedwa olungama ndi iye, mofanana ndi mmene Abrahamu anayesedwera wolungama monga bwenzi la Mulungu.—Mateyu 25:46; Aroma 4:2, 3; Yakobo 2:23.
7. Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene chatsegukira a nkhosa zina lerolino, amene ayesedwa olungama monga momwe analili Abrahamu?
7 Kuyesedwa olungama kwa a 144,000 kumatsegula njira yawo yokhalira ndi chiyembekezo cha kukalamulira pamodzi ndi Yesu mu Ufumu wakumwamba. (Aroma 8:16, 17; Agalatiya 2:16) Kuyesedwa olungama kwa a nkhosa zina mwa kutchedwa mabwenzi a Mulungu kumatsegula njira yawo yokhalira ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’dziko lapansi la paradaiso—kaya mwa kupulumuka Armagedo monga mbali ya khamu lalikulu kapena mwa “kuuka kwa olungama.” (Machitidwe 24:15) Ndi mwaŵi waukulu chotani nanga kukhala ndi chiyembekezo chimenecho ndiponso kukhala bwenzi la Mfumu ya chilengedwe chonse, kukhala ‘wogonera m’chihema mwake’! (Salmo 15:1, 2) Ndithudi, odzozedwa ndi a nkhosa zina omwe anadalitsidwa modabwitsa kudzera mwa Yesu, Mbewu ya Abrahamu.
Tsiku la Chitetezo Lalikulu
8. Kodi nsembe za Tsiku la Chitetezo za m’Chilamulo zinali kusonya ku chiyani?
8 Pamene anali kufotokoza za pangano latsopano, Paulo anakumbutsa oŵerenga ake za Tsiku la Chitetezo limene linali kuchitika chaka chilichonse m’pangano la Chilamulo. Patsikulo, anali kupereka nsembe zosiyana—ina ya fuko la ansembe la Levi ndipo ina inali ya mafuko 12 amene sanali ansembe. Zimenezi zafotokozedwa kwa nthaŵi yaitali kuti zinali kusonya ku nsembe yaikulu ya Yesu imene inali kudzapindulitsa a 144,000 amene ali ndi chiyembekezo cha kumwamba ndiponso anthu mamiliyoni ambiri amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi.a Paulo anasonyeza kuti m’kukwaniritsidwa kwake, mapindu a nsembe ya Yesu amaperekedwa kudzera m’Tsiku la Chitetezo lalikulu la m’pangano latsopano. Monga Mkulu wa Ansembe wa tsiku lalikulu limeneli, Yesu anapereka moyo wake wangwiro monga nsembe yachitetezo kuti apeze “chiombolo chosatha” kaamba ka anthu.—Ahebri 9:11-24.
9. Pokhala a m’pangano latsopano, kodi Akristu odzozedwa achihebri anakhala ndi mwaŵi wotani?
9 Akristu ambiri achihebri a m’zaka za zana loyamba anapitirizabe kukhala ndi ‘changu cha pa Chilamulo [cha Mose].’ (Machitidwe 21:20) Choncho, moyenerera, Paulo anawakumbutsa kuti: “[Yesu] ali Nkhoswe ya chipangano chatsopano, kotero kuti, popeza kudachitika imfa yakuombola zolakwa za pa chipangano choyamba, oitanidwawo akalandire lonjezano la zoloŵa zosatha.” (Ahebri 9:15) Pangano latsopano linamasula Akristu achihebri ku pangano lakale, limene linavumbula zochimwa zawo. Chifukwa cha pangano latsopano limeneli, iwo anatha kulandira “lonjezano la zoloŵa zosatha [zakumwamba].”
10. Kodi nchiyani chimene chimapangitsa odzozedwa ndi a nkhosa zina kuyamika Mulungu?
10 “Iye” amene “akhulupirira Mwanayo” adzapindula ndi nsembe ya dipo. (Yohane 3:16, 36) Paulo anati: “Kristunso ataperekedwa nsembe kamodzi kukasenza machimo a ambiri, adzaonekera pa nthaŵi yachiŵiri, wopanda uchimo, kwa iwo amene amlindirira, kufikira chipulumutso.” (Ahebri 9:28) Lerolino, awo amene akulindirira Yesu mofunitsitsa amaphatikizapo Akristu otsalira odzozedwa a Israyeli wa Mulungu ndi mamiliyoni ambiri amene amapanga khamu lalikulu, amenenso ali ndi choloŵa chosatha. Magulu onse aŵiriwo amayamika Mulungu chifukwa cha pangano latsopano ndiponso chifukwa cha madalitso opatsa moyo otsagana nalo, kuphatikizapo Tsiku la Chitetezo lalikulu ndi utumiki wa Mkulu wa Ansembe, Yesu, m’malo Opatulikitsa akumwamba.
Otanganitsidwa mu Utumiki Wopatulika
11. Pokhala ndi chikumbumtima choyeretsedwa mwa nsembe ya Yesu, kodi odzozedwa ndi a nkhosa zina omwe amachitanji mosangalala?
11 M’kalata yake yolembera Ahebri, Paulo anagogomezera za mtengo waukulu wa nsembe ya Yesu m’makonzedwe a pangano latsopano poyerekezera ndi nsembe za machimo za m’pangano lakale. (Ahebri 9:13-15) Nsembe yabwino kwambiri ya Yesu ingathe ‘kuyeretsa chikumbumtima chathu kuchisiyanitsa ndi ntchito zakufa, kukatumikira Mulungu wamoyo.’ Kwa Akristu achihebri, “ntchito zakufa” zinaphatikizapo “zolakwa za pa chipangano choyamba.” Kwa Akristu a lerolino, zimaphatikizapo machimo amene anachita kumbuyoku koma analapa moonadi ndipo Mulungu anawakhululukira. (1 Akorinto 6:9-11) Pokhala ndi chikumbumtima choyera, Akristu odzozedwa ‘amatumikira Mulungu wamoyo.’ Ndipo a khamu lalikulu amachitanso chimodzimodzi. Pokhala atayeretsa chikumbumtima chawo “m’mwazi wa Mwanawankhosa,” iwo ali m’kachisi wauzimu wamkulu wa Mulungu, ‘kumtumikira Iye usana ndi usiku.’—Chivumbulutso 7:14, 15.
12. Kodi timasonyeza motani kuti tili “m’chikhulupiriro chokwanira”?
12 Kuwonjezera pamenepo, Paulo anati: “Tiyandikire ndi mtima woona, m’chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera.” (Ahebri 10:22) Kodi tingasonyeze motani kuti tili “m’chikhulupiriro chokwanira”? Paulo anauza Akristu achihebri kuti: “Tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu [cha kumwamba], pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika; ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:23-25) Ngati chikhulupiriro chathu chilidi chamoyo, ifenso ‘sitidzaleka kusonkhana kwathu pamodzi.’ Tidzakhala osangalala kufulumiza abale athu ndi kufulumizidwa ndi iwo ku chikondano ndi ntchito zabwino ndi kulimbikitsidwa kaamba ka ntchito yofunika ya kulalikira poyera chiyembekezo chathu, kaya chikhale cha padziko lapansi kapena cha kumwamba.—Yohane 13:35.
“Chipangano Chosatha”
13, 14. Kodi pangano latsopano lili losatha m’njira ziti?
13 Kodi chidzachitika nchiyani pamene onse a 144,000 adzalandira chiyembekezo chawo cha kumwamba? Kodi pangano latsopano lidzaleka kugwira ntchito? Panthaŵi imeneyo, padziko lapansi sipadzakhala wotsalira aliyense wa Israyeli wa Mulungu. Onse otengamo mbali m’panganolo adzakhala ndi Yesu “mu Ufumu wa Atate [wake].” (Mateyu 26:29) Koma tikukumbukira mawu a Paulo m’kalata yake yolembera Ahebri akuti: ‘Mulungu wa mtendere . . . anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wa nkhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha.’ (Ahebri 13:20; Yesaya 55:3) Kodi pangano latsopano lili losatha motani?
14 Choyamba, mosiyana ndi pangano la Chilamulo, ilo silidzaloŵedwa m’malo ndi lina lililonse. Chachiŵiri, zotsatirapo za ntchito yake nzosatha, mongadi momwe ulili ufumu wa Yesu. (Yerekezerani Luka 1:33 ndi 1 Akorinto 15:27, 28.) Ufumu wakumwamba uli ndi malo osatha m’zifuno za Yehova. (Chivumbulutso 22:5) Ndipo chachitatu, a nkhosa zina adzapitirizabe kupindula ndi makonzedwe a pangano latsopano. Mu Ulamuliro wa Zaka Chikwi wa Kristu, anthu okhulupirika adzapitirizabe ‘kutumikira [Yehova] usana ndi usiku m’Kachisi mwake’ mongadi momwe akuchitira tsopano lino. Yehova sadzakumbutsiranso machimo awo akale amene anakhululukidwa pamaziko a ‘mwazi wa pangano’ wa Yesu. Iwo adzapitirizabe kuyesedwa olungama monga mabwenzi a Yehova, ndipo lamulo lake lidzakhala lolembedwabe m’mitima mwawo.
15. Fotokozani za unansi wa Yehova ndi olambira ake a padziko lapansi m’pangano latsopano.
15 Kodi Yehova panthaŵiyo adzanenabe kwa atumiki aumunthu ameneŵa kuti: ‘Ndine Mulungu wawo, ndipo iwo ndi anthu anga’? Inde. ‘Adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nawo.’ (Chivumbulutso 21:3) Iwo adzakhala “tsasa la oyera mtima,” nthumwi za padziko lapansi za “mudzi wokondedwawo,” mkwatibwi wakumwamba wa Yesu Kristu. (Chivumbulutso 14:1; 20:9; 21:2) Zonsezi zidzatheka chifukwa cha kukhulupirira kwawo ‘mwazi wa pangano’ wokhetsedwa wa Yesu ndi kumvera kwawo mafumu ndi ansembe akumwamba, amene anali Israyeli wa Mulungu pamene anali padziko lapansi.—Chivumbulutso 5:10.
16. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene oukitsidwa padziko lapansi akuyembekezera? (b) Kodi ndi madalitso otani amene adzadza pamapeto a zaka chikwi?
16 Nanga bwanji ponena za akufa amene adzaukitsidwa padziko lapansi? (Yohane 5:28, 29) Iwonso adzaitanidwa kuti ‘adzidalitse’ mwa Yesu, Mbewu ya Abrahamu. (Genesis 22:18) Iwo adzayeneranso kukonda dzina la Yehova, kumtumikira, kupereka nsembe zolandiridwa, ndi kumtumikira m’nyumba yake yopemphereramo. Awo amene amachita zimenezo adzaloŵa mu mpumulo wa Mulungu. (Yesaya 56:6, 7) Chakumapeto kwa zaka chikwizo, okhulupirika onse adzakhala atasandulizidwa kukhala anthu angwiro mothandizidwa ndi Yesu Kristu ndi ansembe anzake a 144,000. Iwo adzakhala olungama, osati kungoyesedwa olungama monga mabwenzi a Mulungu chabe. Iwo ‘adzakhala ndi moyo’ popeza kuti adzakhala atamasuka kotheratu ku uchimo ndi imfa ya Adamu. (Chivumbulutso 20:5; 22:2) Amenewo adzakhala madalitso otani nanga! Monga momwe tionera lerolino, zikuoneka kuti ntchito yaunsembe ya Yesu ndi a 144,000 idzakhala itamalizidwa panthaŵiyo. Madalitso onse a Tsiku la Chitetezo lalikulu adzakhala ataperekedwa. Ndiponso, Yesu “adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate.” (1 Akorinto 15:24) Kudzakhala chiyeso chomaliza choperekedwa kwa mtundu wa anthu, ndipo kenaka Satana ndi ziŵanda zake adzasakazidwa ku nthaŵi za nthaŵi.—Chivumbulutso 20:7, 10.
17. Polingalira za chimwemwe chimene tikuyembekezera, kodi aliyense wa ife ayenera kufunitsitsa kuchitanji?
17 Kodi ndi ntchito yanji, ngati idzakhalapo, imene idzachitidwa ndi “chipangano chosatha” m’nyengo imene idzayambika panthaŵiyo? Ifeyo sitinganene kalikonse. Zimene Yehova wavumbula kufikira tsopano nzokwanira. Zimatipangitsa kukhala ndi mantha aulemu. Tangolingalirani—moyo wosatha monga mbali ya “miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano”! (2 Petro 3:13) Pasakhaletu chilichonse chofooketsa chikhumbo chathu cha kulandira lonjezano limenelo. Kuchirimika kungakhale kovuta. Paulo anati: “Pakuti chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.” (Ahebri 10:36) Komabe, kumbukirani kuti mavuto alionse amene tingafunikire kuwagonjetsa, chitsutso chilichonse chimene tingafunikire kuchilaka, sizingafanane mpang’ono pomwe ndi chimwemwe chimene tikuyembekezera. (2 Akorinto 4:17) Choncho, pasakhaletu aliyense wa ife amene ali “a iwo akubwerera kuloŵa chitayiko.” M’malo mwake, tikhaletu “a iwo a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo.” (Ahebri 10:39) Tonsefe tikhaletu ndi chikhulupiriro chokwanira mwa Yehova, Mulungu wa mapangano, kaamba ka madalitso osatha a aliyense wa ife.
[Mawu a M’munsi]
a Onani buku lakuti Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano, mutu 13, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mwamvetsetsa?
◻ Kuwonjezera pa Akristu odzozedwa, kodi ndaninso amene akudalitsidwa mwa Mbewu ya Abrahamu?
◻ Pokhala odalitsidwa mwa pangano latsopano, kodi a nkhosa zina ali ofanana motani ndi otembenuka a m’chipangano chakale?
◻ Kodi a nkhosa zina amadalitsidwa motani m’makonzedwe a Tsiku la Chitetezo lalikulu?
◻ Nchifukwa ninji Paulo anatcha pangano latsopano kuti ndi “chipangano chosatha”?
[Bokosi patsamba 21]
Utumiki Wopatulika m’Kachisi
A khamu lalikulu amalambirira pamodzi ndi Akristu odzozedwa m’bwalo lapadziko lapansi la kachisi wamkulu wauzimu wa Yehova. (Chivumbulutso 7:14, 15; 11:2) Palibe chifukwa chimene tinganenere kuti iwo ali m’Bwalo lakwalokha la Akunja. Pamene Yesu anali padziko lapansi, m’kachisi munali Bwalo la Akunja. Komabe, m’mamangidwe ouziridwa ndi Mulungu a akachisi a Solomo ndi Ezekieli, panalibe makonzedwe alionse a Bwalo la Akunja. M’kachisi wa Solomo munali bwalo lakunja mmene Aisrayeli ndi otembenuka, amuna ndi akazi, anali kulambiriramo pamodzi. Amenewa ndi makonzedwe aulosi a bwalo lapadziko lapansi la kachisi wauzimu, mmene Yohane anaonamo khamu lalikulu likuchita utumiki wopatulika.
Komabe, ansembe ndi Alevi okha ndiwo anali kuloŵa m’bwalo lamkati, mmene munali guwa lalikulu; ansembe okha ndiwo anali kuloŵa m’malo Opatulika; ndipo mkulu wa ansembe yekha ndiye anali kuloŵa m’malo Opatulikitsa. Bwalo lamkati ndi malo Opatulika amazindikiridwa kuti anali kuchitira chithunzi mkhalidwe wapadera wauzimu wa Akristu odzozedwa padziko lapansi. Ndipo malo Opatulikitsa amachitira chithunzi kumwamba kwenikweniko, kumene Akristu odzozedwa amalandira moyo wosakhoza kufa pamodzi ndi Mkulu wawo wa Ansembe wakumwamba.—Ahebri 10:19, 20.
[Chithunzi patsamba 23]
Polingalira za chimwemwe chimene tikuyembekezera, tiyeni tikhale “a chikhulupiriro cha ku chipulumutso cha moyo”