Mutu 13
Nthaŵi ya Kubadwanso
KUPULUMUKA mapeto a dziko lovunda liripoli ndiko chiyembekezo chokondweretsa. Tikulakalaka kuwonjoka ku zoipa, umbombo ndi chiwawa za dziko. Koma kanthu kenanso kamakuchititsanso kukhala kokhumbika kwambiri kuti tipulumuke. Kodi nkotani? Chenicheni chakuti onse amene akukhala mbali ya “dziko lapansi latsopano” adzakhalanso ndi mwaŵi wa kumasulidwa ku machimo awo, ku matenda ndi moyo wa kudwala, inde ngakhale ku imfa. (Chivumbulutso 21:1-5) Komabe, kuti zimenezi zichitike, uchimo weniweniwo uyenera kuchotsedwa kotheratu. Kodi zimenezo nzotheka motani? Nzogwirizanitsidwa ndi zimene Yesu Kristu analongosola kukhala “kubadwanso.”
2 Kwa atumwi ake, Yesu anati: “M’kubadwanso, pamene Mwana wa munthu adzakhala pachimpando chaulemerero wake, inunso mudzakhala pamipando khumi ndi iŵiri, kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.” (Mateyu 19:28) Kubadwanso idzakhala nthaŵi ya “kubadwa kachiŵiri,” nthaŵi “pamene zonse zipangidwa zatsopano,” monga momwe matembenuzidwe ena a Baibulo amakunenera. (The Emphasized Bible, lotembenuzidwa ndi Rotherham; The Jerusalem Bible) Mwa njira ya kubadwanso kumeneku, kudzakhala kotheka kwa anthu kukhalanso ndi ungwiro umene mtundu wa anthu unali nawo pachiyambi.
3 Chifukwa cha uchimo wolandiridwa kuchokera kwa Adamu, mbadwa zake zonse zinafunikira kufa, ndipo zochuluka zavutika ndi matenda omvetsa chisoni otsogolera ku imfa. (Aroma 5:12) Palibe kukhuthulidwa ku imfa kukanagulidwa ndi ndalama. Palibe ntchito zimene munthu wopanda ungwiro anali wokhoza kuchita zikanapeza chimasuko kaamba ka iyemwini kapena wina aliyense. Chiweruzo cholungama cha Mulungu chinafuna kuti ngati anthu ati apeze mwaŵi wa kukhala ndi moyo wamuyaya, nsembe iyenera kuperekedwa yolingana mu mtengo ndi chimene Adamu anataya, ndiko kuti, moyo waumunthu wangwiro. Palibe aliyense wa mbadwa za Adamu anali ndi moyo woterowo kuti apereke.—Salmo 49:7-9; Mlaliki 7:20.
4 Mwachifundo, Yehova mwiniyo anapanga makonzedwe ofunika mwa kutumiza Mwana wake wobadwa yekha, Yesu, kudziko lapansi monga munthu wangwiro kudzapereka moyo wake monga “dipo lolinganira.” (1 Timoteo 2:5, 6, NW) Ha ndichisonyezero cha kukoma mtima kwapadera ndi chachikondi cha Mulungu chotani nanga kwa anthu! Moyo umene uli wotheka monga chotulukapo suuli kanthu kamene tingapeze monga malipiro koma ndiwo mphoto yochokera kwa Mulungu. Komabe, umaperekedwa kokha kwa awo amene amazindikira mowonadi kufunikira kwawo makonzedwe a Mulungu amenewa, nasonyeza chikhulupiriro mwa iwo ndi kusonyeza chikhulupiriro chimenecho mwa kumvera Mwana wa Mulungu. (Aroma 6:23; Yohane 3:16, 36) Koma kodi ndiliti pamene mapindu a nsembe imeneyo adzalandiridwa ndi anthu?
MAPINDU AMENE TSOPANO ACHOKERA KU NSEMBE YA KRISTU
5 Mapindu anayamba kuyambukira miyoyo ya anthu mwamsanga Yesu Kristu (m’ntchito yake monga Mkulu wa Ansembe wamkulu wa Mulungu) atapereka mtengo wansembe yake pamaso pa Mulungu kumwamba. Choyamba, kuyambira pa Pentekoste wa 33 C.E., mapindu amenewa anayamba kulandiridwa ndi awo amene, oitanidwa kukhala oloŵa nyumba limodzi ndi Kristu, amene akatumikira monga mafumu ndi ansembe limodzi naye m’mwamba. (Machitidwe 2:32, 33; Akolose 1:13, 14) Ndiyeno, mwapadera mu 1935, anthu amene analandira chiyembekezo cha moyo wamuyaya padziko lapansi anayamba kudziwonetsera. Nawonso, chiyembekezo chawo, chinatheketsedwa ndi nsembe ya Kristu. (1 Yohane 2:1, 2) Kuperekedwa kopita patsogolo kumeneku kwa mtengo wa nsembe imeneyo kunasonyezedwa ndi zochitika zimene zinachitika pa Tsiku Lachitetezero la Israyeli wakale.
6 Wotsogoza pachihema chopatulika cha Israyeli, ndipo pambuyo pake pakachisi, anali mkulu wa ansembe amene anali chiŵalo cha banja la Levi la Aroni. Amuna ena a banja la Aroni anali ansembe aang’ono, ndipo amuna onse otsala a fuko la Levi anatumikira monga othandiza. Kuti apereke chotetezera machimo, mkulu wa ansembe anapereka nsembe nyama ziŵiri, zimene mwazi wake wa iriyonse unaperekedwa mosiyana m’Malo Opatulikitsa, monga momwe Yehova analamulira. Yoyamba inali likonyani yoperekedwa ndi mkulu wa ansembe Wachiaroni kaamba ka “iye yekha, ndi mbumba yake,” imene inaphatikizapo fuko lathunthu la Levi. (Levitiko 16:11, 14) Yachiŵiri inali mbuzi imene inaperekedwa monga nsembe ya machimo “kaamba ka anthu,” mafuko ena khumi ndi aŵiri. (Levitiko 16:15) Ndiponso, machimo a Israyeli yense anaululidwira pamutu pa mbuzi yamoyo, ndipo inatayiridwa m’chipululu. (Levitiko 16:21, 22) Kodi zonsezi zinathanthauzanji?
7 Mtumwi Paulo akulongosola kuti kukwaniritsidwa kwake kuli pansembe imodzi ya Yesu Kristu. “Kristu sanaloŵa m’malo opatulika omangika ndi manja, akutsanza owonawo; komatu m’mwamba momwe, kuwonekera tsopano pamaso pa Mulungu chifukwa cha ife . . . kuchotsa uchimo mwa nsembe ya iye yekha.” (Ahebri 9:24-26) Pamenepa kodi nchifukwa ninji mwazi wa nyama yoposa imodzi unaloŵetsedwa m’Malo Opatulikitsa pa Tsiku Lachitetezero la Israyeli? Kumeneku kunali kusonyeza mbali zosiyana za chimene nsembe yaumunthu yangwiro ya Yesu ikuchita. Ndipo mbali inanso inasonyezedwa mwa kuululira machimo a mtunduwo pamutu wa mbuzi yamoyo ndiyeno nkuitayira m’chipululu.
8 Monga momwedi mwazi wa ng’ombe yoperekedwera nsembe mbumba ya Aroni unaloŵetsedwa choyamba m’chipinda Chopatulikitsa, momwemonso mapindu a nsembe ya Yesu anagwiritsiridwa ntchito choyamba pa awo amene akakhala ogwirizana ndi Kristu mu unsembe wakumwamba. Zimenezi zinachitidwa kuyambira mu 33 C.E. kumkabe mtsogolo. Yesu Kristu analibe machimo amene anayenera kutetezeredwa, monga momwe anachitira Aroni, koma awo amene akakhala ansembe aang’ono limodzi ndi Kristu anali nawo. Amenewa anaphiphiritsiridwa ndi fuko la Levi. (1 Petro 2:4, 5) Kuperekedwa kwa mwazi wochokera m’nsembe yachiŵiri, mbuzi yansembe ya machimo “kaamba ka anthu,” kunasonyeza kuti ena mwa mtundu wa anthu akapindula ndi nsembe ya Kristu pambuyo pa kagulu kakumwamba. Amenewa akakhala anthu amene akapeza moyo padziko lapansi m’Paradaiso wobwezeretsedwa. Anaphiphiritsiridwa ndi “mafuko khumi ndi aŵiri [osakhala aunsembe] a Israyeli” pa Tsiku Lachitetezero. (Mateyu 19:28; Salmo 37:29) Yesu sanafere kokha onsewa, koma kwenikweni amachotsa machimo a awo amene anawafera mwansembe, akumapereka chimasuko kwa iwo. Zimenezi zinasonyezedwa ndi chenicheni chakuti, potsirizira pake, machimo a Israyeli ataululidwira pambuzi yamoyo, inatayiridwa m’chipululu, yosadzawonekanso.—Salmo 103:12; Yesaya 53:4-6.
9 Kwa onse amene akusonyeza chikhulupiriro m’makonzedwe achikondi a Yehova kupyolera mwa Kristu, kukhululukidwa kwenikweni kwa machimo, kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu, nkothekera tsopano mosasamala kanthu za kakhalidwe kawo kakale. Angalandire madalitso amtengo wapatali a kupereka utumiki wopatulika kwa Mulungu ndi chikumbu mtima choyera. (1 Akorinto 6:9-11; Ahebri 9:13, 14) Koma zimenezi sizitanthauza kuti iwo panthaŵi ino akupatsidwa moyo wopanda ziyambukiro zonse za uchimo. (1 Yohane 1:8-10; Aroma 7:21-25) Kwa awo amene adzalamulira kumwamba limodzi ndi Kristu, moyo woterowo udzapezedwa kokha pamene atsiriza njira yawo yapadziko lapansi ndipo akuukitsidwira ku kusafa kumwamba. Kwa ena amtundu wa anthu, chimasuko chotheratu ku uchimo chidzatheketsedwa mwa kubadwanso.
“M’KUBADWANSO”
10 Monga momwe Yesu adanenera, kubadwanso ndiko “pamene Mwana wa munthu [Yesu Kristu] adzakhala pachimpando chaulemerero wake.” (Mateyu 19:28) Ndithudi, sichirichonse chimene chinachitika nthaŵi yomweyo pamene anaikidwa pampando wachifumu. Pambuyo pa kuikidwa pampando wachifumu kwa Yesu mu 1914 C.E., choyamba anayeretsa miyamba, akumachotsako Satana ndi ziŵanda zake. Ndiyeno anayamba kuukitsira otsatira ake odzozedwa ku ulemerero wakumwamba. (Chivumbulutso 12:5, 7-12; 1 Atesalonika 4:15-17) Sikokha kuti atumwi okhulupirika a Kristu anapatsidwa “mipando khumi ndi iŵiri” yolonjezedwa kwa iwo, koma mopita patsogolo ena onse a 144 000 akuikidwa pampando wachifumu kumwamba pa chiukiriro chawo kwa akufa.—Chivumbulutso 3:21.
11 Pamene kusankhidwa kwa anthu opanga kagulu kakumwamba kunatha, kusonkhanitsidwa kwa khamu lalikulu la “nkhosa zina” kunayamba, makamaka kuyambira mu 1935 kumkabe mtsogolo. Limeneli, nalonso, linayamba kulandira mapindu ochokera m’nsembe ya Kristu likumatsuka miinjiro yawo ndi kuiyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa. Lirinkuthandizidwa “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo chenicheni ndi kukhulupirika.” (Chivumbulutso 7:9, 10, 14; Aefeso 4:20-24, NW) M’ziŵerengero zowonjezerekawonjezereka likupindula ndi makonzedwe a Mulungu kupyolera mwa Kristu amene angatsogolere ku kukhala kwawo ndi moyo kosatha m’Paradaiso wobwezeretsedwa.—Chivumbulutso 7:17; 22:17.
12 Mwamsanga, tsopano, dziko loipa lidzawonongedwa. Satana ndi ziŵanda zake adzaikidwa m’phompho. Tsiku Lachiweruzo la zaka chikwi la anthu lidzayamba. Yesu Kristu adzakhala mkulu wa Oweruza, ndipo adzatsimikizira kuti onse akupatsidwa mpata wokwanira ndi chithandizo chachikulu kotero kuti aphunzire njira zolungama za Yehova ndi kugwirizana nazo. Otsatira Kristu odzozedwa amenewo amene anadzitsimikizira kukhala osunga umphumphu kufikira imfa adzagwirizana naye m’ntchitoyo, ‘kuweruza mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli.’ (Luka 22:28-30; Chivumbulutso 20:4, 6) Zimenezi sizitanthauza kuti iwo adzaweruza kokha mbadwa zakuthupi za Israyeli. Mmalo mwake, adzaweruza onse amene anaphiphiritsiridwa ndi “mafuko khumi ndi aŵiri [osakhala aunsembe] a Israyeli” pa Tsiku Lachitetezo. Zimenezi zikuphatikizapo dziko lonse la anthu owomboledwa. (1 Akorinto 6:2) Opulumuka chisautso chachikulu adzakhala oyamba kupindula ndi programu imeneyi yotukula anthu. Koma mabiliyoni owonjezereka adzakhalanso ndi phande, chifukwa chakuti awo oti aweruzidwe akuphatikizapo “amoyo ndi akufa.” (2 Timoteo 4:1; Machitidwe 24:15) Kudzakhala kokondweretsa chotani nanga pamene akufa amene aphatikizidwa m’nsembe ya dipo ya Kristu abwerera! Ha ndimisozi yachisangalalo yotani nanga pamene okondedwa agwirizanitsidwa!
13 Imeneyi idzakhala nthaŵi pamene, potsirizira pake, anthu achotseredwa zopinga zakuthupi ndi maganizo zochititsidwa ndi uchimo. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anachiritsa nthaŵi yomweyo anthu amene anali amanjenje, awo amene anali akhungu kapena ogontha kapena amene sanathe kulankhula, ndi anthu amene thupi lawo linapundulidwa kapena amene nyonga yawo inathetsedwa ndi nthenda. Ntchito zamphamvu zimenezo zinali kokha kulaŵidwiratu kwa zimene adzachitira anthu onse mkati mwa Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi. Pokhala ndi chifukwa chabwino, aliyense amene awona kapena kulandira umboni wodabwitsa wotero wa kukoma mtima kwa Yehova ndi amene kenako akunyoza ulamuliro wake adzawonongedwa kosatha. Koma mwa kuphunzitsidwa njira zolungama za Yehova ndi kuganiza zisonkhezero za awo amene akusonyeza chikhulupiriro ndi kumvera kwenikweni zidzawongokera mwapang’onopang’ono kufikira atafika ku ungwiro wokwanira. Okonda Yehova amenewo adzakhala atalandiradi kubadwa kwatsopano, kubadwanso. Kudzakhala monga ngati kuti anapatsidwa chiyambi chatsopano m’moyo ndi atate watsopano, Atate Wosatha, Yesu Kristu.—Yesaya 26:9; 9:6.
14 Pamenepo, pambuyo pa kupambana chiyeso chotsiriza pamapeto a zaka chikwi, iwo adzalandiridwa ndi Yehova Mulungu kupyolera mwa Kristu kukhala ana enieni a Mulungu, monga mbali yabanja Lake langwiro la m’chilengedwe chonse. Chimenechi nchiyembekezo cholimbikitsa chotani nanga—osati kokha kwa opulumuka chisautso chachikulu komanso kwa akufa onse amene akuukitsidwa kudzaloŵa m’chisangalalo cha moyo m’dziko lapansi Laparadaiso!—Aroma 8:20, 21.
[Mafunso]
1. (a) Kodi ndimwaŵi wodabwitsa wotani umene udzayembekezera opulumuka kuloŵa mu “dziko lapansi latsopano”? (b) Koma kodi zimenezo zidzafunikira chiyani?
2. Kodi nchiyani chimene chiri “kubadwanso” kotchulidwa pa Mateyu 19:28?
3. (a) Kodi nchiyani chimene chatuluka mu uchimo wa Adamu? (b) Kodi nchifukwa ninji palibe mbadwa za Adamu zimene zakhoza kudzionjola ku ziyambukiro zauchimo wa choloŵa?
4. (a) Kodi ndimotani mmene dipo lofunikalo linaperekedwera? (b) Kodi ndimotani mmene tingapindulire nalo?
5. (a) Kodi ndani amene anali oyamba kupindula ndi nsembe ya Kristu? (b) Kodi ndikagulu kena kati kamene kapindula, ndipo makamaka kuyambira liti?
6. Mwachidule longosolani zimene zinachitika pa Tsiku Lachitetezo.
7. (a) Kodi ndinsembe imodzi iti imene inaphiphiritsiridwa pamenepo? (b) Kodi nchifukwa ninji panali nyama yansembe yoposa imodzi imene inagwiritsiridwa ntchito?
8. (a) Kodi ndimotani mmene zochitika za Tsiku Lachitetezo zinasonyezera amene akapindula choyamba ndi nsembe ya Kristu? (b) Kodi ndikuperekedwa kotani kwa nsembe ya Yesu kumene kunasonyezedwa mwa nsembe yamachimo “kaamba ka anthu”? (c) Kodi ndichinthu china chiti chimene chinalongosoledwa mwa fanizo mwa kutayira mbuzi m’chipululu?
9. (a) Kodi ndimadalitso otani amene awo amene akusonyeza chikhulupiriro m’nsembe ya Kristu akulandira tsopano? (b) Kodi ndimapindu ena otani amene adzadza pambuyo pake?
10. (a) Kodi ndiliti pamene kubadwanso kunayamba? (b) Kodi alionse apatsidwa mipando yachifumu m’kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yesu?
11. Kodi ndim’njira iti imene “nkhosa zina” zikuwonera kufikira tsopano ziyambukiro za kubadwanso?
12. (a) Kodi ndani amene anaphiphiritsiridwa ndi “mafuko khumi ndi aŵiri a Israyeli” amene Yesu panopa anasonyako? (b) Kodi ndani kuwonjezera pa opulumuka amene adzapindula ndi kubadwanso?
13. Kodi ndimotani mmene ziyambukiro za Tsiku Lachiweruzo la zaka chikwi lidzakhaliradi kubadwanso?
14. Kodi ndiunansi wamtengo wapatali wotani umene onse opambana chiyeso chotsiriza adzapatsidwa kukhala nawo?