Kodi Mumalidziŵa Bwino Gulu la Yehova?
“Atero Yehova, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga.”—YESAYA 66:1.
1, 2. (a) Kodi ndi umboni wooneka uti umene mungapereke wokhudza gulu la Yehova? (b) Kodi Yehova amakhala kuti?
KODI mumakhulupirira kuti Yehova ali ndi gulu? Ngati mumakhulupiriradi, kodi nchifukwa ninji mumatero? Mwina mungayankhe kuti: ‘Inde, tili ndi Nyumba ya Ufumu. Tili ndi mpingo wolinganizidwa bwino wokhala ndi bungwe la akulu. Tili ndi woyang’anira dera woikidwa mwalamulo amene amatichezera nthaŵi ndi nthaŵi. Timachita misonkhano yaikulu yolinganizidwa bwino. Tili ndi ofesi yanthambi ya Watch Tower Society m’dziko mwathu. Ndithudi, zitsanzo zonsezi ndi zitsanzo zinanso zambiri zili umboni wakuti Yehova ali ndi gulu logwira ntchito.’
2 Zochitika zonsezi zimachitira umboni kuti pali gulu. Komatu ngati timangolingalira za gulu lapadziko lapansi, ndiye kuti sitikulidziŵa bwino gulu la Yehova. Yehova anauza Yesaya kuti dziko lapansi ndicho choikapo mapazi Ake chabe, koma kumwamba ndiwo mpando Wake wachifumu. (Yesaya 66:1) Kodi Yehova anali kunena za “kumwamba” kuti? Kodi anali kunena za mumlengalenga mwathumu? Kuthambo? Kapena za mtundu wina wa moyo? Yesaya akunena za ‘pokhala poyera ndi paulemerero’ pa Yehova, ndipo wamasalmo akufotokoza kuti kumwamba kumeneku ndiko “m’malo akhalamo Iye.” Choncho, “kumwamba” kumene Yesaya 66:1 akunena kukutanthauza malo osaoneka a mizimu kumene Yehova ali ndi mpando wapamwamba, kapena kuti wokwezeka.—Yesaya 63:15; Salmo 33:13, 14.
3. Kodi tingathetse bwanji zikayikiro?
3 Choncho, ngati tikufunadi kuzindikira ndi kudziŵa bwino gulu la Yehova, tiyenera kuyang’ana kumwamba. Ndipotu limeneli ndilo vuto limene anthu ambiri ali nalo. Popeza kuti gulu la Yehova lakumwamba nlosaoneka, kodi tingadziŵe bwanji kuti lilipodi? Mwina ena angakayikirenso kwambiri akumanena kuti, ‘Tingatsimikize bwanji zimenezo?’ Chabwino, kodi ndi motani mmene chikhulupiriro chingagonjetsere kukayikira? Njira ziŵiri zofunika kwambiri ndizo phunziro laumwini lozama la Mawu a Mulungu ndi kupezeka pamisonkhano yachikristu mokhazikika ndi kutengamo mbali. Tikatero tidzayamba kuzindikira choonadi ndi kuchotsa kukayikira. Atumiki ena a Mulungu anakayikiranso. Tiyeni tilingalirepo zomwe anachita mnyamata wa Elisa pamene mfumu ya Aramu inali kuchita nkhondo ndi Israyeli.—Yerekezerani ndi Yohane 20:24-29; Yakobo 1:5-8.
Amene Anaona Makamu a Kumwamba
4, 5. (a) Kodi mnyamata wa Elisa anali ndi vuto lotani? (b) Kodi Yehova anayankha motani pemphero la Elisa?
4 Mfumu ya Aramu inatumiza khamu lalikulu lankhondo usiku ku Dotana kuti akagwire Elisa. Pamene mnyamata wa Elisa analaŵirira mmamaŵa natuluka, mwina ncholinga chokapitidwa mphepo padenga lathyathyathya la nyumba yawo ya ku Middle East, iye anazizwa chotani nanga! Khamu lonse lankhondo la Aramu lokhala ndi akavalo ndi magaleta ankhondo linazinga mudziwo, kuyembekezera kugwira mneneri wa Mulungu. Mnyamatayo anafuulira Elisa nati: “Kalanga ine, mbuye wanga! Tichitenji?” Mwachionekere, modekha ndiponso mwachidaliro, Elisa anayankha kuti: “Usaopa, pakuti okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” Mnyamatayo ayenera kuti anazizwa nafunsa kuti, ‘Nanga iwo ali kuti? Ine sindikuwaona!’ Limenelo lingakhalenso vuto lathu nthaŵi zina—kulephera kuona ndi maso athu achidziŵitso, kapena kuzindikira, makamu a kumwamba.—2 Mafumu 6:8-16; Aefeso 1:18.
5 Elisa anapemphera kuti maso a mnyamata wake atseguke. Kodi kenaka chinachitika nchiyani? “Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.” (2 Mafumu 6:17) Inde, iye anaona makamu a kumwamba, angelo ankhondo akuyembekezera kutetezera mtumiki wa Mulungu. Tsopano iye anazindikira chimene Elisa anali kudalira.
6. Kodi tingalidziŵe motani gulu lakumwamba la Yehova?
6 Kodi nthaŵi zina timalephera kuzindikira monga momwe anachitira mnyamata wa Elisa? Kodi timangoona mbali yooneka ndi maso yokha ya zinthu zimene zikutilepheretsa kapena kulepheretsa ntchito yachikristu m’maiko ena? Ngati timatero, kodi tingayembekezere masomphenya apadera kuti atiunikire? Ayi, chifukwa chakuti tili ndi chinthu china chimene mnyamata wa Elisa analibe—buku lathunthu lokhala ndi masomphenya ambiri, Baibulo, limene lingatiphunzitse za gulu lakumwamba. Mawu ouziridwa amaperekanso malangizo otitsogolera omwe amawongola kalingaliridwe kathu ndi njira yathu ya moyo. Komabe, tiyenera kuyesetsa kuti tikhale ndi kuzindikira ndi kukulitsa chidziŵitso cha makonzedwe a Yehova. Ndipo tingachite zimenezo mwa phunziro laumwini, pamodzi ndi pemphero ndiponso kusinkhasinkha.—Aroma 12:12; Afilipi 4:6; 2 Timoteo 3:15-17.
Kuphunzira Kuti Tizindikire
7. (a) Kodi ndi vuto lotani limene ena angakhale nalo ponena za phunziro laumwini la Baibulo? (b) Kodi nchifukwa ninji phunziro laumwini lili lopindulitsa kwambiri?
7 Phunziro laumwini silosangalatsa kwenikweni kwa anthu ambiri, makamaka amene anali kudana ndi maphunziro kusukulu kapena amene analibe mwayi wopita kusukulu. Komabe, ngati tikufuna kuzindikira ndi kudziŵa bwino gulu la Yehova ndi maso athu achidziŵitso, tiyenera kukulitsa chilakolako cha kuphunzira. Kodi chakudya chokoma chingakhalepo popanda kuchiphika mwakhama? Aliyense wodziŵa bwino kuphika adzakuuzani kuti pamakhala ntchito yaikulu kuti aphike chakudya chokoma. Komabe, mwina mungachidye patheka la ola kapena kucheperako. Komatu mapindu a phunziro laumwini tingakhale nawo moyo wathu wonse. Phunziro laumwini lingakhale losangalatsa ngati tikuona mmene tikupitira patsogolo. Mtumwi Paulo ananena molondola kuti tiyenera kudzipenyerera tokha ndi chiphunzitsocho ndi kupitiriza kuchita khama kuŵerenga poyera. Timafunikira kuchita khama nthaŵi zonse, koma mapindu amene tingapeze angakhale kosatha.—1 Timoteo 4:13-16.
8. Kodi buku la Miyambo likulimbikitsa khalidwe lotani?
8 Munthu wina wanzeru wakale anati: “Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziŵadi Mulungu.”—Miyambo 2:1-5.
9. (a) Kodi mtengo wa golidi umasiyana motani ndi “kumdziŵadi Mulungu”? (b) Kodi ndi ziŵiya ziti zomwe timafunikira kugwiritsira ntchito kuti tipeze chidziŵitso cholongosoka?
9 Kodi mwaona kuti umenewu ndi udindo wa ndani? Taonani kubwerezabwereza kwa mphatikiri wakuti ‘Uka.’ Ndipo taonaninso mawu akuti, ‘Ukaipwaira ngati chuma chobisika.’ Talingalirani za okumba migodi amene anakumba siliva ndi golidi kwa zaka mazana ambirimbiri ku Bolivia, Mexico, South Africa, ndi maiko ena. Iwo anagwira ntchito mwakhama, pogwiritsira ntchito mapiki ndi mafosholo, kufukula miyala kuti apezemo zitsulo zamtengo wapatalizo. Anaona kuti golidi ngwofunika kwambiri kotero kuti mumgodi wina ku California, U.S.A., iwo anaboola migodi yotalika makilomita 591, yozama makilomita pafupifupi 1.5—ncholinga chopeza golidi chabe. Komabe, kodi mungadye golidi? Kumwa golidi? Kodi angakuthandizeni m’chipululu mutamva njala ndi ludzu? Ayi, amangopezetsa chuma ndipo mtengo wake sukhazikika, umasintha tsiku ndi tsiku monga momwe misika yapadziko lonse imasonyezera. Ngakhale zili choncho, anthu ambiri aferapo. Nangano nkoyenerera chotani kugwira ntchito yaikulu kuti tipeze golidi wauzimu, “kumdziŵadi Mulungu”? Tangolingalirani zimenezo, kumdziŵadi Ambuye Mfumu yachilengedwe chonse, gulu lake, ndi zifuno zake! Kuti tichite zimenezo, tiyenera kugwiritsira ntchito mapiki ndi mafosholo auzimu. Zimenezo ndizo zofalitsa zozikidwa pa Baibulo zomwe zimatithandiza kukumba Mawu a Yehova ndi kuzindikira tanthauzo lake.—Yobu 28:12-19.
Kukumba Nzeru
10. Kodi Danieli anaonanji m’masomphenya ake?
10 Tiyeni tikumbe mwauzimu kuti tiyambe kulidziŵadi gulu la Yehova lakumwamba. Kuti tipeze nzeru yotitsogolera, tiyeni tilingalirepo za masomphenya a Danieli okhudza Nkhalamba yakale lomwe itakhala pampando wake wachifumu. Danieli analemba kuti: “Ndinapenyerera mpaka anaikapo mipando yachifumu, nikhalapo Nkhalamba yakale lomwe, zovala zake zinali za mbuu ngati chipale chofeŵa, ndi tsitsi la pamutu pake ngati ubweya woyera, mpando wachifumu unali malaŵi amoto, ndi njinga zake moto woyaka. Mtsinje wamoto unayenda wotuluka pamaso pake, zikwizikwi anamtumikira, ndi unyinji wosaŵerengeka unaima pamaso pake, woweruza mlandu anakhalapo, ndi mabuku anatsegulidwa.” (Danieli 7:9, 10) Kodi zikwizikwi amene anali kutumikira Yehova ameneŵa ndayani? Malifalensi a m’Baibulo la New World Translation, ogwiritsiridwa ntchito monga “mapiki” ndi “mafosholo,” amatifikitsa pa malifalensi monga Salmo 68:17 ndi Ahebri 1:14. Inde, amene anali kutumikira anali angelo akumwamba!
11. Kodi masomphenya a Danieli angatithandize motani kuti timvetsetse tanthauzo la mawu a Elisa?
11 Nkhani ya Danieli sinena kuti iye anaona angelo onse okhulupirika amene Mulungu amawalamulira. Mwina pangakhalenso angelo ena mamiliyoni ambiri. Koma kunena zoona, tsopano tikuona chifukwa chake Elisa anati: “Okhala pamodzi ndi ife achuluka koposa aja okhala pamodzi ndi iwo.” Khamu lankhondo la mfumu ya Aramu, ngakhale kuti linachirikizidwa ndi angelo osakhulupirika, ziŵanda, linali laling’ono kwambiri mosiyana ndi makamu a Yehova akumwamba!—Salmo 34:7; 91:11.
12. Kodi zambiri ponena za angelo mungazidziŵe motani?
12 Mwina mukufuna kudziŵa zambiri ponena za angelo ameneŵa, monga ntchito imene amagwira potumikira Yehova. Kuchokera kumawu achigiriki otanthauza mngelo, tingaone kuti iwo ali amithenga chifukwa chakuti mawuwo amatanthauzanso kuti “mthenga.” Komabe, iwo ali ndi ntchito zambiri. Komatu kuti mudziŵe ntchito zimenezi muyenera kukumba. Ngati muli ndi buku la Insight on the Scriptures, mungaphunzire nkhani yakuti “Angels” (Angelo), kapena mungaone nkhani zakale za mu Nsanja ya Olonda zonena za angelo. Mudzazizwa ndi zinthu zambiri zimene mudzadziŵa ponena za atumiki akumwamba ameneŵa a Mulungu ndi kuzindikira bwino za chichirikizo chawo. (Chivumbulutso 14:6, 7) Komabe, m’gulu la Mulungu lakumwamba, zolengedwa zina zauzimu zili ndi ntchito zapadera.
Zimene Yesaya Anaona
13, 14. Kodi Yesaya anaonanji m’masomphenya, ndipo kodi zimenezi zinamkhudza motani?
13 Tsopano tiyeni tikumbe masomphenya a Yesaya. Pamene muŵerenga chaputala 6, vesi 1 mpaka 7, mudzachita chidwi kwambiri. Yesaya akunena kuti iye ‘anaona Ambuye [“Yehova,” NW] atakhala pampando wachifumu,’ ndipo “pamwamba pa Iye panaima aserafi.” Iwo anali kufuula ponena za ulemerero wa Yehova, kutamanda chiyero chake. Inunso mudzakhudzidwa ngakhale mwakuŵerenga chabe nkhani imeneyi. Kodi Yesaya anatani? “Ine ndinati, Tsoka kwa ine! chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wamilomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.” Iye anachita chidwi chotani nanga ndi masomphenya amenewo! Kodi inunso mwachita chidwi?
14 Choncho, kodi Yesaya anachirimika motani pamene anaona ulemerero wotere? Iye akufotokoza kuti mserafi wina anamtonthoza nati: “Mphulupulu zako zachotsedwa, zochimwa zako zawomboledwa.” (Yesaya 6:7) Yesaya anakhulupirira kwambiri kuti Mulungu ali ndi chifundo ndipo anamvetsera mawu a Yehova. Tsopano, kodi simukufuna kudziŵa zambiri ponena za zolengedwa zauzimu zapamwamba zimenezi? Nanga muyenera kuchitanji? Kumbani chidziŵitso chowonjezereka. Chimodzi mwa ziŵiya zogwiritsira ntchito ndicho Watch Tower Publications Index, mungaone malifalensi ake onena za nkhani zambiri zofotokozedwa mwatsatanetsatane.
Kodi Ezekieli Anaonanji?
15. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti masomphenya a Ezekieli ngodalirika?
15 Tsopano tiyeni tilingalirepo za mtundu wina wa zolengedwa zauzimu. Ezekieli anali ndi mwayi woona masomphenya ochititsa chidwi asanatulukebe m’ndende ku Babulo. Tsegulani mabaibulo anu pa Ezekieli chaputala 1, mavesi atatu oyambirira. Kodi nkhaniyo ikuyamba motani? Kodi ikunena kuti, ‘Kalekale, m’dziko lina lakutali . . . ’? Ayi, imeneyi si nthano yofotokoza zimene sizinachitikepo. Vesi 1 likuti: “Ndipo kunali chaka cha makumi atatu, mwezi wachinayi, tsiku lachisanu la mwezi, pokhala ine pakati pa andende kumtsinje [wa] Kebara, kunatseguka kumwamba, ndipo ndinaona masomphenya a Mulungu.” Kodi mwaonaponji pavesi limeneli? Likutchula tsiku limene zinthuzo zinachitika ndi malo ake. Zimenezi zikusonya ku chaka chachisanu cha undende wa Mfumu Yoyakini, chaka cha 613 B.C.E.
16. Kodi Ezekieli anaonanji?
16 Yehova anatambasula dzanja lake kwa Ezekieli, ndipo iye anayamba kuona masomphenya ochititsa chidwi ndipo anaona Yehova ali pampando wachifumu m’galeta lalikulu lakumwamba limene linali ndi mikombero ikuluikulu yokhala ndi maso kuzungulira mkombero wonse. Nkhani yotichititsa chidwi pano njakuti panali zamoyo zinayi, chilichonse choimirira pafupi ndi mkombero. “Ndipo maonekedwe awo ndiwo anafanana ndi munthu, ndi yense anali nazo nkhope zinayi, ndi yense wa iwo anali nawo mapiko anayi. . . . Mafaniziro a nkhope zawo zinali nayo nkhope ya munthu; ndi izi zinayi zinali nayo nkhope ya mkango pambali ya ku dzanja lamanja; ndi izi zinayi zinali nayo nkhope ya ng’ombe pambali ya ku dzanja lamanzere; izi zinayi zinali nayonso nkhope ya chiombankhanga.”—Ezekieli 1:5, 6, 10.
17. Kodi nkhope zinayi za akerubi zimaimiranji?
17 Kodi zamoyo zinayi zimenezi zinali chiyani? Ezekieli iyemwini akutiuza kuti anali akerubi. (Ezekieli 10:1-3, 14) Nanga nchifukwa ninji anali ndi nkhope zinayi? Kuimira mikhalidwe yaikulu ya Ambuye Mfumu Yehova. Nkhope ya chiombankhanga inali chizindikiro cha nzeru zakuya. (Yobu 39:27-29) Nanga nkhope ya ng’ombe inaimiranji? Pokhala ndi khosi ndi mapeŵa amphamvu kwambiri, ng’ombe imatha kunyamula kavalo pamodzi ndi wokwerapo wake pomenyana. Ndithudi, ng’ombe ndiyo chizindikiro cha mphamvu zopanda malire za Yehova. Mkango umagwiritsiridwa ntchito monga chizindikiro cha kuŵeruza molimba mtima. Pomaliza, nkhope ya munthu moyenerera imaimira chikondi cha Mulungu, popeza kuti munthu ndiye chamoyo chokha cha padziko lapansi chimene chingasonyeze mkhalidwe umenewu mwanzeru.—Mateyu 22:37, 39; 1 Yohane 4:8.
18. Kodi mtumwi Yohane akuwonjezera motani chidziŵitso chathu cha gulu lakumwamba?
18 Palinso masomphenya ena amene angatithandize kuzindikira bwino zimenezi. Ameneŵa amaphatikizapo masomphenya a Yohane ofotokozedwa m’buku la m’Baibulo la Chivumbulutso. Iye, mofanana ndi Ezekieli, anaona Yehova ali pampando waulemerero motsagana ndi akerubi. Kodi akerubiwo anali kuchitanji? Iwo anali kubwereza mawu a aserafi a pa Yesaya chaputala 6, akumati: “Woyera, woyera, woyera, Ambuye Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali, amene ali, ndi amene alinkudza.” (Chivumbulutso 4:6-8) Yohane anaonanso mwanawankhosa ali pafupi ndi mpando wachifumuwo. Kodi ameneyo anaimiranji? Mwanawankhosa weniweniyo wa Mulungu, Yesu Kristu.—Chivumbulutso 5:13, 14.
19. Kodi mwazindikiranji ponena za gulu la Yehova m’phunziro lino?
19 Choncho, kupyolera m’masomphenya onsewa, kodi tazindikiraponji? Tazindikira kuti gulu lakumwamba lili ndi Yehova Mulungu monga mtsogoleri wake yemwe amakhala pampando wake wachifumu motsagana ndi Mwanawankhosa, Yesu Kristu, amene ndiye Mawu, kapena kuti Logos. Ndipo taonanso khamu lakumwamba la angelo, kuphatikizapo aserafi ndi akerubi. Onsewa ali m’gulu limodzi lalikulu, gulu logwirizana pochita zifuno za Yehova. Ndipo chimodzi mwa zifuno zimenezo ndicho kulalikira uthenga wabwino padziko lonse lapansi m’masiku ano otsiriza.—Marko 13:10; Yohane 1:1-3; Chivumbulutso 14:6, 7.
20. Kodi ndi funso liti lomwe lidzayankhidwa m’nkhani yotsatira?
20 Pomaliza, tili ndi Mboni za Yehova padziko lapansi zomwe zimasonkhana m’Nyumba zawo za Ufumu pofuna kuphunzira mmene zingachitire chifuniro cha Ambuye Mfumu. Zoonadi, tsopano tadziŵa bwino kuti pali ambiri amene ali nafe kusiyana ndi amene ali ndi Satana ndi adani a choonadi. Tsopano funso nlakuti, Kodi gulu lakumwambalo limakhudzidwa bwanji ndi ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu? Nkhani yotsatira idzayankha funso limeneli ndi mafunso ena ambiri.
Mafunso Obwereza
◻ Kodi tiyenera kuzindikiranji kuti tilidziŵe bwino gulu la Yehova?
◻ Kodi ndi chokumana nacho chotani chimene mnyamata wa Elisa anayang’anizana nacho, ndipo kodi mneneriyo anamlimbikitsa motani?
◻ Kodi phunziro laumwini tiyenera kuliona motani?
◻ Kodi Danieli, Yesaya, ndi Ezekieli akupereka motani tsatanetsatane wa gulu lakumwamba?
[Chithunzi patsamba 13]
Mapindu a phunziro laumwini amaposeratu mapindu a chakudya chophikidwa bwino
[Chithunzi patsamba 15]
Masomphenya a makamu akumwamba linali yankho la Yehova ku pemphero la Elisa