Kutumikira Yehova Mwachimwemwe
‘Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumyimbira mokondwera.’—SALMO 100:2.
1, 2. (a) Kodi ndimotani mmene tsankho laufuko linawonetsedwera poyera m’Berlin, Jeremani, koma kodi nkhondo ya mtanda ya “Ulamuliro wa Zaka Chikwi” inatha motani? (b) Kodi ndikusiyana kotani ndi 1936 kumene kunawonedwa mu Olympia Stadium mu July 1990, ndipo kodi chimwemwe cha gulu lamitundu yonse lomwe linasonkhana pamenepo chinachilikizidwa ndi chiyani?
MALOWO ndi Olympia Stadium, ku Berlin. Zaka makumi asanu mphambu zinayi kuchiyambiyambi, bwalo labwino limeneli linali malo apakati a mtsutsano pamene wolamulira wa Nazi wotsendereza ufulu, Adolf Hitler ananyoza wothamanga wakuda wa ku Amereka amene anapata mamedulo anayi a golidi. Kunalidi kupeputsidwa kwa kudzitukumula kwaufuko kwa Hitler kwa “upamwamba wa fuko la Aryan”!a Koma tsopano, pa July 26, 1990, akuda, oyera, achikasu—anthu ogwirizana ochokera m’magulu amitundu 64, onse pamodzi 44,532—anasonkhana pano kaamba ka Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova wa “Chinenero Choyera.” Padali kusefukira kwa chimwemwe kotani nanga masana a Lachinayi amenewo! Pambuyo pa nkhani yaubatizo, onka ku ubatizo okwanira 1,018 anafuula kuti “Ja!” nafuulanso kuti, “Ja!” povomereza kudzipereka kwawo kwa Yehova Mulungu, kuchita chifuniro chake.
2 Chinatengera Mboni zatsopanozi mphindi 19 kuti zituluke m’bwaloli kunka ku dziŵe laubatizo. Ndipo mkati mwa mphindi zonsezo, kuwomba m’manja kwamphamvu kunamveka m’bwalo lalikululo. Opambana pa Maseŵera a Olympic sanapatsidwepo konse kuwomba m’manja konga kumene analonjeredwa nako mazana ameneŵa, ochokera m’mitundu yambiri, amene akusonyeza chikhulupiriro chimene chimalaka dziko. (1 Yohane 5:3, 4) Chimwemwe chawo nchozikidwa zolimba m’chidaliro chakuti Ufumu wa Mulungu wolamulidwa ndi Kristu udzabweretseradi anthu zaka chikwi za madalitso aulemerero.—Ahebri 6:17, 18; Chibvumbulutso 20:6; 21:4, 5.
3. Kodi nchowonadi chotani chimene chikugogomezeredwa ndi chidaliro cha osonkhanawo, ndipo motani?
3 Panopa palibe udani waufuko kapena wautundu, popeza kuti onse akulankhula chinenero choyera cha Mawu a Mulungu, mwakutero kugogomezera kuwona kwa mawu a Petro akuti: ‘Zowona ndizindikira kuti Mulungu alibe tsankho; koma m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.’—Machitidwe 10:34, 35; Zefaniya 3:9.
4. Kodi anthu ambiri osonkhanawo anakhala akhulupiriri pansi pa mikhalidwe yotani, ndipo kodi mapemphero awo ayankhidwa motani?
4 Mbali yaikulu ya anthu omwe anasonkhana m’Berlin ameneŵa anakhala akhulupiriri mkati mwa zaka zambiri za chitsenderezo, zokuta nyengo ya Nazi (1933-45) ndi nyengo ya sosholizimu yomwe inatsatirapo ku Jeremani Yakum’mawa, kumene chiletso pa Mboni za Yehova changochotsedwa kumene mwalamulo pa March 14, 1990. Chotero, ambiri a iwo ‘analandira mawuwo m’chisautso chambiri, ndi chimwemwe cha mzimu woyera.’ (1 Atesalonika 1:6) Iwo tsopano ali ndi ufulu waukulu wa kutumikira Yehova, ndipo chimwemwe chawo chiribe malire.—Yerekezerani ndi Yesaya 51:11.
Nthaŵi Zachimwemwe
5. Kodi Israyeli anakondwerera motani chipulumutso cha Yehova pa Nyanja Yofiira?
5 Kumasulidwa kwa abale athu Kum’mawa kwa Yuropu, ndiponso posachedwapa m’mbali zina za Afirika ndi Asiya, kumatikumbutsa chipulumutso chochitidwa ndi Yehova m’nthaŵi zakale. Timakumbukira ntchito zamphamvu za Yehova pa Nyanja Yofiira, ndi mmene nyimbo yachiyamiko ya Israyeli inafikira pachimake ndi mawu awa: ‘Afanana ndi inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi inu ndani, wolemekezeka, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?’ (Eksodo 15:11) Lerolino, kodi sitimapitiriza kukondwera ndi zinthu zozizwitsa zimene Yehova akuchitira anthu ake? Ndithudi timatero!
6. Kodi tingaphunzirenji m’kufuula kwachimwemwe kwa Israyeli mu 537 B.C.E.?
6 Chimwemwe chinasefukira mu 537 B.C.E. pamene Israyeli anabwezeretsedwa ku dziko lake pambuyo pa ukapolo m’Babulo. Mtundu wa Yehova ukalengeza tsopano, monga momwe analoserera Yesaya kuti: ‘Tawonani, Mulungu ndiye chipulumutso changa; ndidzakhulupira, sindidzawopa; pakuti Yehova Mwini ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, iye ndiye chipulumutso changa.’ Nchitamando chotani nanga! Ndipo kodi mtunduwo ukachisonyeza motani chimwemwe chimenecho? Yesaya akupitiriza kuti: ‘Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muyimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero.’ Iwo tsopano akakhoza ‘kufuula mokuwa m’kudziwikitsa m’dziko lonse’ machitidwe ake amphamvu, monga momwe atumiki owomboledwa a Yehova amachitira lerolino.—Yesaya 12:1-6.
Chimwemwe m’Ntchito ya Yehova
7. Kodi ndi zipulumutso zotani zimene zinadzetsa chikondwerero mu 1919?
7 M’nthaŵi zamakono atumiki a Yehova anayamba kufuula mwachimwemwe pamene iye anawapulumutsa mozizwitsa mu 1919. Pa March 26 m’chaka chimenecho, ziŵalo za Bungwe Lolamulira zinamasulidwa m’ndende ya ku United States, kumene zinatsekeredwa kwa miyezi isanu ndi inayi pansi pa milandu yachinyengo ya kupandutsa anthu. Ndichikondwerero chachikulu chotani nanga chimene chinachitika powalandiranso ku Beteli ya Brooklyn! Kuwonjezerapo, otsalira odzozedwa onse akanasangalala tsopano ndikumasulidwa mwauzimu kutuluka m’Babulo Wamkulu, dongosolo la chipembedzo limene Satana wayanga nalo dziko lonse.—Chibvumbulutso 17:3-6; 18:2-5.
8. Kodi nchotulutsidwa chozizwitsa chotani chimene chinalengezedwa pa Msonkhano wa ku Cedar Point mu 1919, ndipo ndichiitano cha ntchito yotani chimene chinapangidwa?
8 Zochitika za m’mbiri za 1919 zinakometseredwa ndi msonkhano wa anthu a Mulungu wochitidwa pa Cedar Point, Ohio, U.S.A., pa September 1-8. Tsiku lachisanu la msonkhanowo, “Tsiku la Antchito Anzathu,” pulezidenti wa Watch Tower Society, J. F. Rutherford, analankhula kwa anthu 6,000 m’nkhani yochititsa chidwi yokhala ndi mutu wakuti “Kulengeza Ufumu.” Pambuyo polongosola Chibvumbulutso 15:2 ndi Yesaya 52:7, iye anauza amvetseri ake kuti magazini atsopano, The Golden Age (tsopano odziŵika monga Galamukani!), akafalitsidwa milungu iŵiri iriyonse, makamaka kaamba ka kuwagaŵira m’munda. Pomaliza iye anati: “Anthu amene ngodzipereka kotheratu kwa Ambuye; awo amene ngwopanda mantha, amene mitima yawo njoyera, amene amakonda Mulungu ndi Ambuye Yesu ndi maganizo awo onse, nyonga, moyo ndi thupi, adzakondwera kukhala ndi phande m’ntchito imeneyi pamene mwaŵi wapezeka. Pemphani Ambuye kaamba ka chitsogozo ndi chilangizo chake kuti akupangeni kukhala m’thenga weniweni, wokhulupirika, ndi wokhutiritsa. Pamenepo, ndinyimbo yachimwemwe mumtima mwanu, pitani patsogolo kukamtumikira iye.”
9, 10. Kodi Yehova wapititsa patsogolo motani kufalitsidwa kwa magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!?
9 “Nyimbo yachimwemwe” imeneyo yamvedwa padziko lonse lapansi! Mosakaikira, aŵerengi athu ambiri akhala ndi phande m’kukweza kugaŵira kwa magazini a Galamukani! kufika ku makope 12,980,000 a kope lirilonse m’zinenero 64. Monga chiwiya champhamvu chotsogozera anthu okondwerera ku chowonadi, Galamukani! imatumikira monga inzake ya Nsanja ya Olonda. M’dziko lina la Kummawa, mlongo wachipainiya, pamene ankagwirira ntchito paulendo wa magazini wanthaŵi zonse, anadabwitsidwa kupeza kuti nthaŵi iriyonse pamene anapereka magazini atsopano, mwininyumbayo anapereka ndalama zokwanira $7 (U.S.) ku ntchito yadziko lonse ya Mboni za Yehova—kusonyezadi chiyamikiro chabwino kaamba ka ntchito Yaufumu!
10 Tsopano lino poyamba chaka cha 112 cha kufalitsidwa kwake, magazini a Nsanja ya Olonda amafalitsidwa makope okwanira 15,290,000 m’zinenero 111, zinenero 59 za makope ameneŵa zimatulutsidwa panthaŵi imodzi padziko lonse zokhala ndi zamkati mwake zofanana. Monga mdindo wokhulupirika, otsalira odzozedwa akupitirizabe kupatsa aŵerengi oyamikira ‘phoso lawo [lauzimu] pa nthaŵi yake.’ (Luka 12:42) Mu 1990, Mboni za Yehova zinasimba kuti zinalembetsa masabusikripishoni atsopano okwanira 2,968,309 a magazini aŵiriwo, chiwonjezeko cha 22.7 peresenti kuposa 1989.
Chimwemwe Chichuluka
11. (a) Kodi ndichiitano chotani chimene chinaperekedwa kwa anthu a Mulungu mu 1922 pa Cedar Point? (b) Kodi kufuula kwachimwemweku kwafutukulidwa motani?
11 Chimwemwe chinachulukanso pamene anthu a Mulungu, tsopano okwanira 10,000 anasonkhana kaamba ka msonkhano wachiŵiri pa Cedar Point, mu September 1922, ndi obatizidwa 361. M’nkhani yake yakuti “Ufumu Wakumwamba Wayandikira,” yozikidwa pa Mateyu 4:17, Mbale Rutherford anafikira mapeto odzutsa maganizo awa: “Dziko liyenera kudziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu ndikuti Yesu Kristu ndiye Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye. Ili ndi tsiku la masiku onse. Tawonani, Mfumu ilamulira! Inu ndinu athenga ake olalikira. Chotero, lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake.” Awo amene anafuula ndi chimwemwe pamsonkhano umenewo awonjezeka m’chiŵerengero kufikira mu 1989 pamene anthu oposa 6,600,000 anasonkhana pamisonkhano ya Mboni za Yehova yokwanira 1,210 padziko lonse, kumene anthu okwanira 123,688 anabatizidwa.
12. (a) Kodi anthu a Mulungu amakhala ndi phande m’chimwemwe chosayerekezeka chotani lerolino? (b) Kodi timalinganiza motani utumiki wathu wa kwa Yehova ndi chimvero chathu ku ‘maulamuliro aakulu’?
12 Mboni za Yehova zimasangalala ndi ufulu wawo. Kuposa zonse, zimasangalala ndikukwaniritsidwa kwamakono kwa mawu awa a Yesu: ‘Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.’ Nchosangalatsa chotani nanga kumasulidwa ku zinsinsi ndi malaulo a chipembedzo chonyenga! Nchodzetsa chimwemwe chosayerekezeka chotani nanga kudziŵa Yehova ndi Mwana wake ndikukhala antchito anzawo, ndichiyembekezo cha moyo wosatha! (Yohane 8:32; 17:3; 1 Akorinto 3:9-11) Atumiki a Mulungu amachiyamikiranso pamene ‘maulamuliro aakulu’ adzikoli, omwe ali pansi pawo, alemekeza ufulu wawo wakulalikira chiyembekezo chaulemerero cha Ufumu wa Yehova pansi pa Kristu. Iwo mofunitsitsa ‘amapereka zake za Kaisara kwa Kaisara,’ pamene panthaŵi imodzimodziyo akupereka ‘zake za Mulungu kwa Mulungu.’—Aroma 13:1-7; Luka 20:25.
13. Kodi Mboni za Yehova zasonyeza motani chimwemwe chawo pomasulidwa ku chitsenderezo?
13 Komabe, ngati ulamuliro wa anthu uyesera kuletsa thayo limeneli la kwa Mulungu, Mboni za Yehova zimayankha monga mmene anachitira atumwi kuti: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa anthu.” Panthaŵi imeneyo, pambuyo pakuti olamulirawo anamasula atumwiwo, iwo “anapita . . . nakondwera.” Kodi iwo anachisonyeza motani chimwemwe chimenecho? ‘Masiku onse, m’kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.’ (Machitidwe 5:27-32, 41, 42) Mofananamo, Mboni za Yehova zamakono zimakondwera pamene zipeza ufulu wokulirako wakulondola uminisitala wawo. M’maiko ambiri kumene Yehova watsegula njira, amasonyeza chimwemwe chachikulu mwakupereka umboni wotheratu ku dzina la Yehova ndi Ufumu ukudzawo mwa Kristu Yesu.—Yerekezerani ndi Machitidwe 20:20, 21, 24; 23:11; 28:16, 23.
Kupirira Ndi Chimwemwe
14. Kodi chimwemwe chimenechi chomwe nchipatso cha mzimu chimapambana bwanji chija cholongosoledwa m’dikishonale?
14 Kodi chimwemwe chachikulu chimenechi chomwe Akristu owona amakhala nacho nchiyani? Nchozama koposa ndi chokhalitsa kwambiri kuposa chimwemwe chapakanthaŵi cha wopambana pa Maseŵera a Olympic. Nchipatso cha mzimu woyera wa Mulungu, umene Mulungu amapereka kwa ‘omumvera iye monga wolamulira.’ (Machitidwe 5:32) Dikishonale ya Webster imalongosola chimwemwe kukhala ‘chakuya kwenikweni kuposa kusangalala, chopenyeka kapena kusonyezedwa kuposa chikondwerero.’ Kwa Mkristu, chimwemwe chiri ndi tanthauzo lakuya kwenikweni. Pokhala chochilikizidwa m’chikhulupiriro chathu, icho ndi mkhalidwe wamphamvu, wolimbikitsa. ‘Chimwemwe cha Yehova ndicho mphamvu yanu.’ (Nehemiya 8:10) Chimwemwe cha Yehova, chimene anthu a Mulungu amakulitsa, chimaposa kwenikweni chisangalalo chapamwamba chimene anthu amakhala nacho kuchokera ku zosangulutsa zakuthupi, zakudziko.—Agalatiya 5:19-23.
15. (a) Kodi kupirira kwagwirizana motani ndi chimwemwe m’zokumana nazo za Akristu okhulupirika? (b) Tchulani malemba ena amene amapereka chitsimikizo cholimbikitsa ponena za kusunga chimwemwe.
15 Talingalirani za abale athu a ku Ukraine. Pamene ‘maulamuliro aakulu’ anathamangitsira zikwi za iwo ku Siberia kuchiyambiyambi kwa ma 1950, iwo anavutika kwambiri. Pambuyo pake, pamene ulamuliro unawapatsa ufulu, iwo anayamikira, koma sionse amene anabwerera kwawo. Chifukwa ninji? Ntchito yawo ya Kummawa inawakumbutsa za Yakobo 1:2-4: ‘Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, mmene mukugwa m’mayesero a mitundu mitundu; pozindikira kuti chiyesedwe cha chikhulupiriro chanu chichita chipiriro.’ Iwo anafuna kupitirizabe kupirira m’kututa kosangalatsa kumeneko, ndipo chinalidi chodzetsa chimwemwe chotani nanga pamisonkhano yaposachedwapa ya Mboni za Yehova m’Poland kulandira Mboni zochokera kumidzi yakutali kwambiri kummawa kwa Pacific. Chipiriro ndi chimwemwe zayendera pamodzi kutulutsa chipatso chimenechi. Ndithudi, tonsefe amene tapirira mosangalala muutumiki wa Yehova tinganene kuti: ‘Koma ndidzakondwera mwa Yehova, ndidzasekerera mwa Mulungu wa chipulumutso changa. Yehova, Ambuye, ndiye mphamvu yanga.’—Habakuku 3:18, 19; Mateyu 5:11, 12.
16. Kodi zitsanzo zabwino za Yeremiya ndi Yobu ziyenera kutilimbikitsa motani m’ntchito yathu yakumunda?
16 Komabe, kodi ndimotani mmene tingasungire chimwemwe chathu pamene tikuchitira umboni kwa otsutsa owuma mutu? Kumbukirani kuti aneneri a Mulungu anakhalabe achimwemwe m’mikhalidwe yofananayo. Yeremiya analongosola motere pamene anali pansi pa chiyeso: ‘Mawu anu anapezeka, ndipo ndinawadya; mawu anu anakhala kwa ine chikondwero ndi chisangalalo cha mtima wanga; pakuti ndatchedwa dzina lanu, Yehova Mulungu wa makamu.’ (Yeremiya 15:16) Ndimwaŵi wotani nanga kutchedwa ndi dzina la Yehova ndikuchitira umboni dzina limenelo! Kuphunzira kwathu kwakhama kwaumwini ndi kukhalamo ndiphande mokulira m’misonkhano Yachikristu kumatimangirira kupitirizabe kusangalala ndi chowonadi. Chimwemwe chathu chidzasonyezedwa m’mkhalidwe wathu m’munda ndi m’kusangalala kwathu ndi Ufumu. Ngakhale pansi pachiyeso chowawa, Yobu anakhozabe kunena motere za adani ake: “Ndinawaseka akapanda kulimbika mtima; ndipo sanagwetsa kusangalala kwa nkhope yanga.” (Yobu 29:24) Mofanana ndi Yobu wokhulupirika, sitifunikira kugwetsa nkhope pamene otsutsa atiseka. Pitirizanibe kumwetulira! Nkhope yathu ingasonyeze chimwemwe chathu ndipo mwakutero kutipezetsa amvetseri.
17. Kodi chipiriro ndi chimwemwe zingabale bwanji chipatso?
17 Pamene tikulifola gawo kwa nthaŵi ndi nthaŵi, kupirira kwathu ndi chimwemwe zingadabwitse anthu olungama ndikuwalimbikitsa kusanthula chiyembekezo chaulemerero chimene tiri nacho. Nchodzetsa chimwemwe chotani nanga kuchititsa maphunziro Abaibulo ndi iwo mokhazikika! Ndipo pamene akuchilandira chowonadi chamtengo wake cha Mawu a Mulungu, timakhala achimwemwe chotani nanga pamene iwo pomalizira pake akhala atsamwali athu muutumiki wa Yehova! Pamenepo timakhala okhoza kunena, monga momwe mtumwi Paulo anauzira akhulupiriri atsopano a m’tsiku lake kuti: ‘Pakuti chiyembekezo chathu, kapena chimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nchiyani? Sindinu nanga, pamaso pa Ambuye wathu Yesu m’kufika kwake? Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi chimwemwe chathu.’ (1 Atesalonika 2:19, 20) Zowonadi, chimwemwe chokhutiritsa chiyenera kupezeka m’kutsogoza achatsopano ku chowonadi cha Mawu a Mulungu ndikuŵathandiza kukhala Mboni zodzipereka, zobatizidwa.
Chimwemwe Chimene Chimachilikiza
18. Kodi chidzatithandiza nchiyani kulaka ziyeso zosiyanasiyana zamakono?
18 M’moyo wathu watsiku ndi tsiku, mikhalidwe yambiri ingafunikire chipiriro. Matenda akuthupi, kuchita tondovi, ndi mavuto azachuma nzoŵerengeka zokha. Kodi ndimotani mmene Mkristu angasungire chimwemwe chake kotero kuti alake ziyeso zoterozo? Ichi chingachitidwe mwakupita ku Mawu a Mulungu kaamba ka chitonthozo ndi chitsogozo. Kuŵerenga kapena kumvetsera kuŵerengedwa kwa masalmo kungapereke chitsitsimulo m’nthaŵi zachiyeso. Ndipo onani uphungu wanzeru wa Davide uwu: “Umsenze Yehova nkhawa zako, ndipo Iye adzakugwiriziza; Nthawi zonse sadzalola wolungama agwedezeke.” (Salmo 55:22) Yehova alidi “Wakumva pemphero.”—Salmo 65:2.
19. Mofanana ndi Davide ndi Paulo, kodi tingakhale ndi chidaliro chotani?
19 Gulu la Yehova, kupyolera m’zofalitsidwa zake ndi akulu a mumpingo, nlokonzeka nthaŵi zonse kutithandiza, anthu ofookafe, kulimbana ndi mavuto athu. Davide anapereka uphungu wachikondi uwu: ‘Pereka njira yako kwa Yehova; khulupiriranso iye adzachichita.’ Iye adanenanso kuti: ‘Ndinali mwana ndipo ndakalamba: ndipo sindinapenya wolungama wasiyidwa, kapena mbumba zake zirinkupempha chakudya.’ Mwakugwirizana ndi mpingo Wachikristu, tidzazindikira kuti ‘chipulumutso cha olungama chidzera kwa Yehova, iye ndiye mphamvu yawo m’nyengo ya nsautso.’ (Salmo 37:5, 25, 39) Tiyeni titsatire nthaŵi zonse uphungu wa Paulo uwu: ‘Chifukwa chake sitifooka; . . . popeza sitipenyerera zinthu zowoneka, koma zinthu zosawoneka; pakuti zinthu zowoneka ziri za nthaŵi, koma zinthu zosawoneka ziri zosatha.’—2 Akorinto 4:16-18.
20. Kodi timawonanji ndi maso achikhulupiriro, ndipo kodi ichi chimatisonkhezera motani?
20 Tingaliwone dongosolo latsopano la Yehova limene liri kutsogoloku ndi maso athu achikhulupiriro. Ha, ndichimwemwe ndi madalitso osayerekezeka otani nanga amene adzakhala kumeneko! (Salmo 37:34; 72:1, 7; 145:16) Pokonzekera nthaŵi yaulemerero imeneyo, tiyeni tilabadire mawu a Salmo 100:2 awa: ‘Tumikirani Yehova ndi chikondwerero: Idzani pamaso pake ndi kumyimbira mokondwera.’
[Mawu a M’munsi]
a Ponena za “upamwamba wa fuko la Aryan,” The New York Times ya pa February 17, 1940, inagwira mawu woyang’anira Wachikatolika wa pa Yunivesite ya Georgetown kukhala akunena kuti “anamva Adolf Hitler akunena kuti Ufumu Woyera Waroma, womwe unali ufumu Wachijeremani, uyenera kukhazikitsidwanso.” Koma katswiri wambiri yakale William L. Shirer akufotokoza motere zotulukapozo: “Hitler anadzitama kuti Ulamuliro Wachitatu umene unabadwa pa January 30, 1933, ukapirira kwa zaka chikwi, ndipo m’kalankhulidwe ka Chinazi unali kusonyedwako monga ‘Ulamuliro wa Zaka Chikwi.’ Unakhalapo zaka khumi ndi ziŵiri ndi miyezi inayi.”
Pobwereramo:
◻ Kodi nchigonjetso chatsankho laufuko chotani chimene chikuwonedwa lerolino?
◻ Kodi nchiyani chimene chinapangitsa anthu a Mulungu akale kuimba ndi kufuula mokondwera?
◻ Kodi chimwemwe chenicheni chawo- njezeka motani m’nthaŵi zamakono?
◻ Kodi chipiriro ndi chimwemwe zimayendera limodzi motani?
◻ Kodi chimwemwe chathu tingachichilikize motani?