Zidakwa Zauzimu—Kodi Ndizo Yani?
“Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efraimu.”—YESAYA 28:1.
1. Kodi ambiri akhala ndi chidaliro chotani, koma kodi ziyembekezo zawo zidzakwaniritsidwa?
TIKUKHALA m’nthaŵi zosangalatsa. Anthu ambiri asangalatsidwa ndi masinthidwe andale zadziko padziko lonse ndi kuwona anthu owonjezereka akuloŵetsedwamo ndi Mitundu Yogwirizana. Mu December 1989 magazini a Detroit Free Press ananena kuti: “Pamene pulaneti likuloŵa m’ma 1990, mtendere wafalikira.” Magazini a ku Soviet Union analengeza kuti: “Tikukonzeka kusula malupanga athu kukhala anangwape,” pamene kuli kwakuti mlembi wamkulu wa Mitundu Yogwirizana analengeza kuti: “Sitirinso m’nkhondo yoputana ndi mawu.” Indedi, pakhala ziyembekezo zazikulu, ndipo mosakaikira, dziko likusintha. Posachedwapa, nkhondo ya ku Gulf yasonyeza mmene masinthidwe angachitikire mofulumira. Koma kodi dziko liripoli lidzakhalapo ndi nthaŵi ya mtendere weniweni ndi chisungiko, ndi mapindu ake onse otsatirapo? Yankho n’lakuti ayi. Kwenikweni, tsoka lalikulu likutukusira limene lidzagwedeza dziko ndi maziko ake! Ndilo tsoka limene chipembedzo ncholoŵetsedwamo mozama.
2. Kodi mkhalidwe wamakono unafanizidwa motani m’Israyeli ndi Yuda wakale?
2 Tsoka limeneli linachitiridwa chithunzi ndi zochitika m’Israyeli ndi Yuda wakale mkati mwa zaka za zana lachisanu ndi chitatu ndi lachisanu ndi chinayi B.C.E. Kalelo, anthu analingalira kuti anaupeza mtendere. Koma Mulungu, kupyolera mwa mneneri wake Yesaya, anachenjeza kuti chiyembekezo chawo cha mtendere chinali chinyengo, chomwe chikavumbulidwa posachedwa. Mofananamo lerolino, Yehova, kupyolera mwa Mboni zake, akuwachenjeza anthu kuti iwo akunyengedwa ngati ayembekezera kupeza mtendere wokhalitsa kudzera mwa zoyesayesa za anthu. Tiyeni tiŵerenge chenjezo laulosi la Yehova ndikuwona mmene limagwirira ntchito lerolino. Ilo likupezeka m’mutu 28 wa Yesaya ndipo linalembedwa isanafike 740 B.C.E., mwachiwonekere mkati mwa kulamulira kwa Peka Mfumu yoipa ya Israyeli ndi Ahazi Mfumu yopanduka ya Yuda.
“Oledzera a Efraimu”
3. Kodi nkukanidwa kodabwitsa kotani kumene Yesaya anakulengeza?
3 Mu vesi 1 ya mutu 28, tikudzidzimuka ndi ndemanga yodabwitsa yakuti: ‘Tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efraimu, ndi kwa duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene liri pamutu paiwo, amene agwidwa ndi vinyo, m’chigwa cha nthaka yabwino.’ Ha, Aisrayeliwo ayenera kukhala anadabwa chotani nanga kumva kukanidwa kwamphamvu koteroko! Kodi “oledzera a Efraimu” ameneŵa anali yani? Kodi “korona wakunyada” wawoyo anali chiyani? Ndipo kodi ‘chigwa cha nthaka yabwino’ nchiyani? Chofunika koposa, kodi mawu ameneŵa amatanthauzanji kwa ife lerolino?
4. (a) Kodi Efraimu anali yani ndipo chigwa cha nthaka yabwino chinali chiyani? (b) Kodi nchifukwa ninji Israyeli anadzimva kukhala wosungika?
4 Popeza kuti Efraimu linali fuko lalikulu koposa la mafuko khumi a Israyeli, liwu lakuti “Efraimu” nthaŵi zina linalozera ku ufumu wonse wakumpoto. Chotero “oledzera a Efraimu” analidi zidakwa za Israyeli. Likulu la Israyeli linali Samariya, yemwe anali pamalo apamwamba pa chigwa cha nthaka yabwino. Chotero mawu akuti ‘chigwa cha nthaka yabwino’ amalozera kwa Samariya. Pamene mawuŵa analembedwa, ufumu wa Israyeli unali woipa kwenikweni, mwachipembedzo. Ndiponso, unali unagwirizana mwa ndale zadziko ndi Suriya motsutsana ndi Yuda ndipo tsopano unadzimva kukhala wosungika. (Yesaya 7:1-9) Zonsezi zinali pafupi kusintha. Tsoka linkayandikira, limene linali chifukwa chake Yehova analengeza “tsoka kwa korona wakunyada wa oledzera a Efraimu.”
5. (a) Kodi nchiyani chimene chinali korona wakunyada wa Israyeli? (b) Kodi ndani anali zidakwa za Efraimu?
5 Kodi “korona wakunyada” anali chiyani? Korona nchizindikiro cha ulamuliro wachifumu. Mwachiwonekere, “korona wakunyada” anali kaimidwe ka Israyeli monga ufumu wa pawokha, wolekana ndi Yuda. Chinachake chinali pafupi kuchitika kuwononga kaimidwe kachifumu ka Israyeli kodzidalira. Pamenepa, kodi ndani anali “oledzera a Efraimu”? Mosakaikira, panali zidakwa zenizeni m’Israyeli, popeza kuti Samariya anali malo ochitirako kulambira koipa kwachikunja. Komabe, Baibulo limalankhula za mtundu woipitsitsa wa uchidakwa. Pa Yesaya 29:9, timaŵerenga kuti: ‘Iwo aledzera, koma si ndi vinyo, ali dzandi dzandi; koma si ndi chakumwa chaukali.’ Uwu unali uchidakwa wauzimu, chakumwa choledzeretsa chodetsedwa, chakupha. Atsogoleri a Israyeli—makamaka atsogoleri ake achipembedzo—mwachiwonekere anavutika ndi kuledzera kwauzimu koteroko.
6. Kodi nchiyani chimene chinaledzeretsa Israyeli wakale?
6 Kodi nchiyani chinachititsa uchidakwa wauzimu wa Israyeli wakale? Kwakukulukulu, kunali kugwirizana kwake ndi Suriya motsutsana ndi Yuda, kumene kunapatsa atsogoleri a mtunduwo lingaliro labwino la chisungiko. Uchidakwa wauzimuwu unapatutsa Israyeli pa kuzindikira kwenikweni. Mofanana ndi chidakwa chenicheni, iye anali wachidaliro chinkana kuti panalibe chifukwa chirichonse chokhalira tero. Ndiponso, Israyeli anavala duwa laulemerero la kugwirizana kwake koledzeretsa ndi Suriya monyada, mofanana ndi duwa lokongola. Koma, monga momwe Yesaya akunenera, linali duwa lakufota limene silikakhalitsa.
7, 8. Mosasamala kanthu za malingaliro ake abwino, kodi Israyeli wakale anali pafupi kukumana ndi chiyani?
7 Yesaya akugogomezera zimenezi m’mutu 28, vesi 2 motere: ‘Tawonani, [Yehova, NW] ali ndi wina wamphamvu wolimba; ngati chimphepo cha matalala, mkuntho wakuwononga, ngati namondwe wa madzi amphamvu osefukira, adzagwetsa pansi ndi dzanja lamphamvu.’ Kodi ndani anali “wamphamvu wolimba” ameneyu? M’nthaŵi ya Israyeli wakale, unali Ufumu wamphamvu wa Asuri. Ufumu wadziko wankhalwe, woipawu ukagwera Israyeli mofanana ndi mkuntho wa kuwononga, namondwe wa madzi amphamvu osefukira. Ndi chotulukapo chotani?
8 Yesaya akupitiriza kunena motere: ‘Korona wakunyada wa oledzera a Efraimu adzaponderezedwa; ndi duwa lakufota la ulemerero wake wokongola, limene liri pamutu pa chigwa cha nthaka yabwino, lidzakhala ngati nkhuyu yoyamba kucha malimwe asanafike; poiwona wakupenya imeneyo, amaidya iri m’dzanja lake.’ (Yesaya 28:3, 4) Likulu la Israyeli, Samariya, linali lofanana ndi nkhuyu yoyamba kucha kwa Asuri, yokonzekera kuthotholedwa ndi kudyedwa. Kugwirizana kwa Israyeli ndi Suriya konga duwa kudali pafupi kuponderezedwa. Kukakhala kopanda phindu pamene tsiku lakubwezera likadza. Choipa kuposapo, ulemerero wake wonga korona wa kudziimira pawokha ukaphwanyidwa pansi pa mapazi a adani Aasuri. Ha, nditsoka lotani nanga!
‘Ansembe ndi Aneneri Asochera’
9. Kodi nchifukwa ninji Yuda anayembekezera uthenga wabwinopo wochokera kwa Yehova kuposa umene Israyeli wakale anaulandira?
9 Inde, kuŵerengera koipitsitsa kunayembekezera Israyeli, ndipo monga momwe Yehova Mulungu anachenjezera, kuŵerengera kumeneko kunadza m’chaka cha 740 B.C.E. pamene Samariya anawonongedwa ndi Asuri ndipo ufumu wakumpoto unaleka kukhalapo monga mtundu wodziimira pawokha. Chimene chinachitika kwa Israyeli wakale chikukhala chenjezo lowopsa ku chipembedzo chonyenga chosakhulupirika lerolino, monga momwe tidzawonera. Koma bwanji ponena za mbale wa Israyeli, ufumu unzake wokhala kum’mwera, Yuda? M’nthaŵi ya Yesaya kachisi wa Yehova ankagwirabe ntchito m’Yerusalemu, likulu la Yuda. Unsembe unkagwirabe ntchito kumeneko, ndipo aneneri onga Yesaya, Hoseya, ndi Mika analankhula m’dzina la Yehova. Pamenepo, kodi ndiuthenga wotani umene Yehova anaupereka kwa Yuda?
10, 11. Kodi ndimkhalidwe wonyansa wotani umene unalipo m’Yuda?
10 Yesaya akupitirizabe kutiuza kuti: ‘Iwonso [ndiwo, ansembe ndi aneneri a Yerusalemu] adzandima ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, wansembe ndi mneneri adzandima ndi chakumwa chaukali.’ (Yesaya 28:7a) Mwachiwonekere, atsogoleri achipembedzo a Yuda analinso oledzera. Ndiponso, monga mu Israyeli, ena anali zidakwa m’lingaliro lenileni, ndipo ngati ndichoncho, ichi chinali chamanyazi. Lamulo la Mulungu mwachindunji linaletsa zakumwa zaukali kwa ansembe pamene ankatumikira m’kachisi. (Levitiko 10:8-11) Uchidakwa weniweni m’nyumba ya Mulungu ukakhala kulakwira Lamulo la Mulungu kowopsa kwenikweni.
11 Angakhale kuli choncho, chowopsa koposa nchakuti, m’Yuda munali uchidakwa wauzimu. Monga momwe Israyeli anadziphatikira ndi Asuriya motsutsana ndi Yuda, chotero Yuda anafuna chisungiko kupyolera m’chigwirizano ndi Asuri. (2 Mafumu 16:5-9) Mosasamala kanthu za kukhalapo kwa kachisi wa Mulungu ndi aneneri ake, Yuda anaika chikhulupiriro mwa anthu pamene anayenera kudalira Yehova. Kuwonjezerapo, pokhala atapanga chigwirizano cholangizidwa moipa choterocho, atsogoleri ake anakhala ndi malingaliro osasamala mofanana ndi anansi awo oledzera mwauzimu a kumpoto. Kaimidwe kamaganizo kawo kosasamala kanamnyansa Yehova.
12. Kodi nchiyani chimene chikakhala chotulukapo cha uchidakwa wauzimu wa Yuda?
12 Yesaya akupitirizabe kunena kuti: ‘Iwo amezedwa ndi vinyo, nasochera ndi chakumwa chaukali, adzandima popenya, napunthwa poweruza. Pakuti magome onse adzazidwa ndi masanzi ndi udio, palibe malo okonzeka.’ (Yesaya 28:7b, 8) Mwachidziŵikire, mumkhalidwe wawo woledzera weniweniwo, ena anasanza m’lingaliro lenileni m’kachisimo. Koma choipa kuposapo, ansembe ndi aneneri omwe adayenera kupereka chitsogozo chakulambira anasanza zonyansa zauzimu. Ndiponso, kusiyapo okhulupirika oŵerengeka, ziweruzo za aneneri zinakhotetsedwa, ndipo iwo analosera zinthu zonyenga kaamba ka mtunduwo. Yehova akalanga Yuda chifukwa cha chidetso chauzimuchi.
Zidakwa Zauzimu Lerolino
13. Kodi mkhalidwe m’Israyeli ndi Yuda unafanana motani ndi m’zaka za zana loyamba C.E., ndiponso umafanana motani ndi umene ulipo lerolino?
13 Kodi maulosi a Yesaya anakwaniritsidwa kokha pa Israyeli ndi Yuda wakale? Kutalitali. Onse aŵiri Yesu ndi mtumwi Paulo anagwira mawu ake ponena za uchidakwa wauzimu ndi kuwagwiritsira ntchito pa atsogoleri achipembedzo a m’nthaŵi yawo. (Yesaya 29:10, 13; Mateyu 15:8, 9; Aroma 11:8) Lerolinonso, mkhalidwe wofanana ndi wa m’nthaŵi ya Yesaya wabuka—tsopano uli m’Chikristu Chadziko, gulu lachipembedzo lapadziko lonse limene limanena kuti limaimira Mulungu. Mmalo mwakutenga kaimidwe kolimba kaamba ka chowonadi ndi kudalira pa Yehova, Chikristu Chadziko, Chikatolika ndi Chiprotestanti, chimaika chikhulupiriro chake m’dziko. Mwakutero icho chikudzandiradzandira mosakhazikika, mofanana ndi zidakwa za Israyeli ndi Yuda. Zidakwa zauzimu za mitundu yakale ija zinachitira chithunzi bwino lomwe atsogoleri auzimu a Chikristu Chadziko lerolino. Tiyeni tiwone mmene ziriridi motero.
14. Kodi ndimotani mmene atsogoleri achipembedzo a Chikristu Chadziko aliri oledzera mofanana ndi mmene adaliri atsogoleri a Samariya ndi Yerusalemu wakale?
14 Mofanana ndi Samariya ndi Yerusalemu, Chikristu Chadziko chaledzera kotheratu ndi vinyo wa zigwirizano zandale zadziko. Mu 1919 icho chinali pakati pa ochirikiza oyambirira a Chigwirizano cha Amitundu. Pamene kuli kwakuti Yesu anati Akristu sakakhala mbali ya dziko, atsogoleri a Chikristu Chadziko amapititsa patsogolo maunansi ndi atsogoleri andale zadziko. (Yohane 17:14-16) Vinyo wophiphiritsira wa kachitidwe koteroko ngwotsitsimula kwa atsogoleri achipembedzo. (Yerekezerani ndi Chibvumbulutso 17:4.) Iwo amasangalala pamene atsogoleri andale zadziko afunsira uphungu kwa iwo ndi kumayanjana ndi akuluakulu a dziko lino. Monga chotulukapo, iwo alibe chitsogozo chauzimu chenicheni chochipereka. Iwo amasanza zonyansa mmalo molankhula uthenga woyera wa chowonadi. (Zefaniya 3:9) Pokhala akuwona mwachimbuuzi ndi mosokonezeka, iwo sali atsogoleri abwino a anthu.—Mateyu 15:14.
“Langizo Ndi Langizo”
15, 16. Kodi ndimotani mmene anthu a m’nthaŵi ya Yesaya anachitira ku machenjezo ake?
15 M’zaka za zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., Yesaya anavumbula mwapadera njira yolakwika ya atsogoleri auzimu a Yuda. Kodi iwo anachitapo motani? Iwo anakuda kuvumbulako! Pamene Yesaya anaumirira m’kulengeza machenjezo a Mulungu, atsogoleri achipembedzowo anayankha mwaukali motere: ‘Kodi iye adzamvetsa yani uthengawo? Iwo amene aletsedwa kuyamwa, nachotsedwa pamabere?’ (Yesaya 28:9) Inde, kodi Yesaya anaganiza kuti ankalankhula kwa makanda? Atsogoleri achipembedzo a Yerusalemu anadzilingalira kukhala anthu akulu msinkhu, okhozadi kudzipangira zosankha. Iwo sanadziwone kukhala ofunikira kumvetsera zokumbutsa zamphamvu za Yesaya.
16 Akatswiri achipembedzo amenewo anaiyesa njerengo ntchito yolalikira ya Yesaya. Iwo anamseka nati: “Pakuti pali langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang’ono, uko pang’ono.” (Yesaya 28:10) ‘Yesaya amangobwerezabwereza zinthu,’ iwo anatero. ‘Iye amapitiriza kunena kuti: “Ichi nchimene Yehova walamula! Ichi nchimene Yehova walamula! Iyi ndi miyezo ya Yehova! Iyi ndi miyezo ya Yehova!”’ Mu Chihebri choyambirira, Yesaya 28:10 analembedwa ndi mawu amodzimodzi obwerezabwereza, kapena monga nyimbo yolerera mwana. Ndipo umu ndimmene atsogoleri achipembedzo anamuwonera mneneriyo, wobwerezabwereza ndi wachibwana.
17. Kodi ndimotani mmene ambiri lerolino amachitira ku uthenga wopereka chenjezo wolengezedwa ndi Mboni za Yehova?
17 M’zaka za zana loyamba C.E., kulalikira kwa Yesu ndi ophunzira ake kunamveka kobwerezabwereza ndi kokhweka mofananamo. Amene anatsatira Yesu anawonedwa ndi atsogoleri achipembedzo Achiyuda kukhala otembereredwa, abulutu opulukira, anthu wamba osaphunzira. (Yohane 7:47-49; Machitidwe 4:13) Mboni za Yehova lerolino kaŵirikaŵiri zimalingaliridwa mwanjirayo. Izo sizinapite ku maseminale a Chikristu Chadziko, ndipo sizimagwiritsira ntchito maina apamwamba aulemu kapena mawu a maphunziro azaumulungu monga momwe amachitira atsogoleri achipembedzo. Chotero akuluakulu m’Chikristu Chadziko amazipeputsa, akumaganizira kuti ziyenera kudziŵa malo awo ndi kupatsa atsogoleri achipembedzo ameneŵa ulemu waukulu.
18. Kodi nchiyani chimene atsogoleri achipembedzo amanyalanyaza lerolino?
18 Komabe, pali chinachake chimene atsogoleri achipembedzo amenewo amanyalanyaza. Chinkana kuti akuluakulu a m’tsiku la Yesaya anakana uthenga wake, iye ankalankhula chowonadi, ndipo machenjezo ake anakwaniritsidwadi! Mofananamo, machenjezo amene Mboni za Yehova zimalankhula lerolino ngowona, ozikidwa molimba pa Mawu a Mulungu a chowonadi, Baibulo. (Yohane 17:17) Chifukwa chake, iwo adzakwaniritsidwa.
Kuŵerengera
19. Kodi ndimotani mmene Yuda anakakamizidwira kulabadira kwa alendo olankhula chinenero chachilendo?
19 Pa Yesaya 28:11, timaŵerenga kuti: ‘Koma ndi anthu a milomo yachilendo, ndi a lilime lina, iye adzalankhula kwa anthu awa.’ Kuphunzitsa kwa Yesaya kunamvekera kukhala mafotokozedwe achilendo kwa Yuda. Chinkana kuti Yuda anapulumuka chiŵembu cha Asuri chomwe chinasesa Israyeli, m’kupita kwa nthaŵi Yehova anamlanga Yuda kupyolera mwa mlendo wina, Nebukadinezara. (Yeremiya 5:15-17) Chinenero cha Chibabulo chinamveka chankhalwe ndi chachilendo kwa Ahebri amenewo. Koma anakakamizika kuchimvetsera pamene Yerusalemu ndi kachisi wake anawonongedwa mu 607 B.C.E. ndipo nzika zake zinatengeredwa kuukapolo ku Babulo. Mofananamo lerolino, Chikristu Chadziko posachedwapa chidzavutika chifukwa chakuti, mofanana ndi Yuda wakale, chanyalanyaza kuchonderera kwa Yehova.
20, 21. Kodi Mboni za Yehova zikulengezanji mosalekeza, koma kodi nchiyani chimene atsogoleri a Chikristu Chadziko akukana kuchita?
20 Ponena za oterowo ulosiwo umati: ‘Amene ananena nawo, Uku ndikupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva. Chifukwa chake mawu a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang’ono, uko pang’ono; kuti ayende ndi kugwa chambuyo, ndi kuthyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.’—Yesaya 28:12, 13.
21 Mosalekeza, monga momwe Yesaya ananenera za uthenga wa Mulungu, Mboni za Yehova zimauza Chikristu Chadziko kuti chiyenera kuika chikhulupiriro chake m’mawu a Yehova. Koma icho chimakana kumvetsera. Kwa icho, Mboni zikuwoneka kukhala zikubwebweta m’lilime lachilendo. Izo zimalankhula chinenero chimene icho sichingamve. Chikristu Chadziko chimakana kupereka mpumulo kwa olema mwakunena za Ufumu wa Mulungu ndi dziko latsopano likudzalo. Mmalomwake, icho ncholedzera ndi vinyo waunansi wake ndi dziko lino. Chimakonda kuchirikiza zothetsera mavuto a anthu zandale zadziko. Mofanana ndi Ayuda a m’tsiku la Yesu, icho sichinafune malo opumira a Ufumu, ndipo sichidzauza ena ponena za uwo.—Mateyu 23:13.
22. Kodi Yehova akudziŵitsa atsogoleri a Chikristu Chadziko za chiyani?
22 Motero, mawu aulosi a Yesaya akudziŵitsa atsogoleri achipembedzo kuti Yehova sadzalankhula nthaŵi zonse mwa Mboni Zake zosavulaza. Posachedwapa, Yehova adzapangitsa “langizo ndi langizo, lamulo ndi lamulo” kugwira ntchito, ndipo chotulukapo chake chidzakhala changozi kwa Chikristu Chadziko. Atsogoleri ake achipembedzo ndi nkhosa zawo ‘adzathyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.’ Inde, mofanana ndi Yerusalemu wakale, dongosolo lachipembedzo la Chikristu Chadziko lidzawonongedwa kotheratu. Ha, icho chidzakhala chochitika chosayembekezereka, nchodabwitsa chotani nanga! Ndipo chotulukapo chake nchowopsa motani nanga kaamba kakuti atsogoleri achipembedzo akonda uchidakwa wauzimu mmalo mwa zokumbutsa za Yehova!
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi zidakwa za Efraimu zinali yani, ndipo kodi izo zinaledzera nchiyani?
◻ Kodi akorona akunyada a zidakwa za Efraimu anaponderezedwa motani?
◻ Kodi ndimkhalidwe wochititsa manyazi wotani m’Yuda umene Yesaya anauvumbula?
◻ Kodi nkuti lerolino kumene tikuwona uchidakwa wauzimu?
◻ Kodi nchifukwa ninji Chikristu Chadziko chiyenera kulabadira chimene chinachitika ku mtundu wakale wa Yuda?