MUTU 16
‘Muzichita Chilungamo’ Poyenda ndi Mulungu
1-3. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kumuchitira chinachake Yehova? (b) Kodi Yehova, yemwe anatipulumutsa, amafuna kuti tizichita chiyani?
TAYEREKEZANI kuti muli musitima yapamadzi yomwe ikumira. Pamene mukuona kuti palibenso zopulumuka, pakufika munthu kudzakupulumutsani. Ndiye kodi mungamve bwanji munthu wokupulumutsaniyo atakufikitsani kumtunda n’kukuuzani kuti: “Musadandaule mwapulumuka”? N’zosachita kufunsa kuti mungafune kumuchitira chinachake posonyeza kumuthokoza chifukwa choti wapulumutsa moyo wanu.
2 Zimenezi zikufanana ndi zimene Yehova anatichitira. Kunena zoona, timafunika kuchita zinazake pomuthokoza. Iye anapereka dipo lomwe limathandiza kuti tipulumutsidwe ku uchimo ndi imfa. Timaona kuti ndife otetezeka podziwa kuti tikamakhulupirira nsembe yamtengo wapataliyi, machimo athu amakhululukidwa komanso tidzakhala ndi moyo wosatha. (1 Yohane 1:7; 4:9) Monga tinaonera m’Mutu 14, dipo ndi umboni wamphamvu wakuti Yehova ndi Mulungu wachilungamo ndiponso wachikondi. Ndiye kodi tingasonyeze bwanji kuyamikira?
3 Njira yabwino ndi kuganizira zimene Yehovayo amafuna kuti tichite. Kudzera mwa mneneri Mika, Yehova akutiuza kuti: “Iye anakuuza munthu iwe zimene zili zabwino. Kodi Yehova akufuna kuti uzichita chiyani? Iye akungofuna kuti uzichita chilungamo, uziona kuti kukhulupirika n’kofunika, ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (Mika 6:8) Onani kuti chimodzi mwa zinthu zimene Yehova amafuna ndi chakuti ‘tizichita chilungamo.’ Kodi tingachite bwanji zimenezi?
Muziyesetsa “Kuchita Zimene Zilidi Zolungama”
4. Kodi timadziwa bwanji kuti Yehova amayembekezera kuti tizitsatira mfundo zake zolungama?
4 Yehova ndi amene amatiuza kuti ichi n’chabwino, ichi ndi choipa ndipo amayembekezera kuti tizitsatira mfundo zake. Popeza mfundo zakezo ndi zolungama, tikamazitsatira timakhala kuti tikuchita chilungamo. Lemba la Yesaya 1:17 limati: “Phunzirani kuchita zabwino, muzichita chilungamo.” Mawu a Mulungu amatilimbikitsanso kuti: “Yesetsani kukhala olungama.” (Zefaniya 2:3) Amatiuzanso kuti: “Muvale umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Mukachita zimenezi mudzatha kuchita zimene zilidi zolungama.” (Aefeso 4:24) Munthu amene amachita zimene zilidi zolungama amapewa zachiwawa, zachiwerewere komanso zinthu zodetsa chifukwa zimenezi zimaipitsa zinthu zoyera.—Salimo 11:5; Aefeso 5:3-5.
5, 6. (a) N’chifukwa chiyani kutsatira mfundo za Yehova si mtolo wolemetsa kwa ife? (b) Kodi Baibulo limasonyeza bwanji kuti kuchita chilungamo ndi ntchito yopitirira?
5 Kodi kuchita zimene Yehova amafuna ndi chimtolo cholemetsa? Ayi. Munthu amene amakonda Yehova saona kuti zimene Yehovayo amafuna n’zovuta kuzichita. Chifukwa choti timakonda Mulungu wathu ndiponso makhalidwe ake, timafuna kuti tizichita zinthu zomusangalatsa. (1 Yohane 5:3) Kumbukirani kuti Yehova “amakonda ntchito zolungama.”’ (Salimo 11:7) Ngati tikufunadi kumatsanzira Mulungu pa nkhani yochita chilungamo, tiyenera kuphunzira kukonda zimene Mulungu amakonda n’kumadana ndi zimene iye amadana nazo.—Salimo 97:10.
6 Anthu omwe si angwirofe zimativuta kuchita zinthu mwachilungamo. Tiyenera kuvula umunthu wakale ndi ntchito zake zauchimo n’kuvala umunthu watsopano. Baibulo limanena kuti umunthu watsopano ‘umapangidwa’ chifukwa chodziwa Mulungu molondola. (Akolose 3:9, 10) Mawu akuti ‘umapangidwa’ akusonyeza kuti kuvala umunthu watsopano ndi ntchito yopitirira yomwe imafuna khama. Komabe ngakhale titayesetsa kwambiri kuchita zoyenera, nthawi zina timaganiza, kulankhula komanso kuchita zinthu zolakwika chifukwa choti si ife angwiro.—Aroma 7:14-20; Yakobo 3:2.
7. Kodi tiyenera kumaona bwanji zimene timalakwitsa pamene tikuyesetsa kuchita chilungamo?
7 Kodi tiyenera kumaona bwanji zimene timalakwitsa pamene tikuyesetsa kuchita chilungamo? N’zoona kuti sitiyenera kuchepetsa kuopsa kochita machimo. Komabe sitiyenera kugwa ulesi n’kumaona kuti si ife oyenera kutumikira Yehova chifukwa choti timalakwitsa zinthu zina. Mulungu wathu wokoma mtima anakonza zoti anthu omwe alapa mochokera pansi pa mtima azitha kukhala nayenso pa ubwenzi. Taganizirani mawu olimbikitsa amene mtumwi Yohane ananena. Iye anati: “Ndikukulemberani zinthu izi kuti musachite tchimo.” Koma kenako ananenanso kuti: “Komabe, wina akachita tchimo, tili ndi wotithandiza wolungama, Yesu Khristu, amene ali ndi Atate.” (1 Yohane 2:1) Yehova anapereka nsembe ya dipo ya Yesu kuti tizitha kumutumikira movomerezeka ngakhale kuti ndife ochimwa. Zimenezitu zikuyenera kutilimbikitsa kuti tizifunitsitsa kusangalatsa Yehova.
Uthenga Wabwino Ndi Wogwirizana Ndi Chilungamo cha Mulungu
8, 9. Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino imasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wachilungamo?
8 Njira ina yomwe tingasonyezere kuti timachita chilungamo komanso kutsanzira Yehova pa nkhaniyi, ndi kuchita zonse zimene tingathe pa ntchito yolalikira. Kodi ntchito yolalikira uthenga wabwino imasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wachilungamo?
9 Yehova sadzawononga dziko loipali asanachenjeze anthu. Pamene Yesu ankanena ulosi wofotokoza zimene zidzachitike munthawi ya mapeto, ananena kuti: “Choyamba uthenga wabwino ukuyenera kulalikidwa kwa anthu amitundu yonse.” (Maliko 13:10; Mateyu 24:3) Mawu akuti “choyamba,” akusonyeza kuti zinthu zina zidzachitika pambuyo poti ntchito yolalikira yagwiridwa padziko lonse. Zinthu zimenezi zikuphatikizapo chisautso chachikulu chimene chidzawononge oipa n’kubweretsa dziko latsopano. (Mateyu 24:14, 21, 22) Sizidzakhala zoona kunena kuti Yehova sanachitire chilungamo anthu oipa. Pochenjeza anthuwa, iye akuwapatsa mpata wokwanira woti asinthe zochita zawo kuti asadzawonongedwe.—Yona 3:1-10.
10, 11. Kodi timasonyeza bwanji kuti Mulungu ndi wachilungamo tikamagwira nawo ntchito yolalikira?
10 Tikamalalikira uthenga wabwino, kodi timasonyeza bwanji kuti Mulungu ndi wachilungamo? Choyamba, n’zoyenera kuti tizichita zonse zomwe tingathe pothandiza ena kuti adzapulumuke. Taganiziranso chitsanzo chopulumutsidwa musitima yomwe ikumira ija. Pamene mwapulumutsidwa ndipo muli m’boti, n’zosachita kufunsa kuti mungakhale ofunitsitsa kuthandiza ena omwe adakali m’madzi. Mofanana ndi zimenezi, tili ndi udindo wothandiza anthu omwe tingati ali m’madzi m’dziko loipali. N’zoona kuti ambiri safuna kumvetsera uthenga wathu. Koma popeza Yehova akulezabe mtima, tili ndi udindo wowapatsa mwayi woti “alape” n’kudzapulumuka.—2 Petulo 3:9.
11 Tikamalalikira uthenga wabwino kwa anthu onse amene timakumana nawo, timasonyeza chilungamo m’njira inanso yofunika kwambiri. Timasonyeza kuti tilibe tsankho. Kumbukirani kuti “Mulungu alibe tsankho. Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.” (Machitidwe 10:34, 35) Kuti timutsanzire pa nkhani yosonyeza chilungamo, sitiyenera kuweruziratu anthu. Koma tiyenera kuuza anthu onse uthenga wabwino posatengera mtundu wawo, mmene anthu amawaonera komanso kaya ndi olemera kapena osauka. Tikamachita zimenezi, timapatsa anthu mwayi woti amve uthenga wabwino komanso kuchita zomwe akuphunzira.—Aroma 10:11-13.
Zimene Timachitira Ena
12, 13. (a) N’chifukwa chiyani sitifunika kufulumira kuweruza ena? (b) Kodi malangizo a Yesu akuti “siyani kuweruza ena” ndiponso akuti “siyani kutsutsa ena” amatanthauza chiyani? (Onaninso mawu a m’munsi.)
12 Tingasonyezenso chilungamo pochitira ena zinthu mofanana ndi zimene Yehova amatichitira. N’zosavuta kuweruza ena, kumangoganizira zolakwa zawo ndiponso kukayikira zolinga zawo. Koma ndi ndani angafune kuti Yehova azingokayikira zolinga zake komanso kumangomuimba mlandu pa zimene walakwitsa? Yehova satichitira zimenezi. Wolemba masalimo wina ananena kuti: “Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndi ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?” (Salimo 130:3) Kodi sitikuyamikira kuti Mulungu wathu wolungama ndiponso wachifundo anasankha kuti asamangoganizira zolakwa zathu? (Salimo 103:8-10) Ndiye kodi tizichita bwanji zinthu ndi anthu ena?
13 Anthu ena akalakwitsa zinazake, tingatsanzire chilungamo komanso chifundo cha Yehova posafulumira kuwaweruza makamaka pa nkhani zazing’ono komanso zomwe sizikutikhudza. Pa ulaliki wake wa paphiri, Yesu anachenjeza kuti: “Siyani kuweruza ena kuti inunso musaweruzidwe.” (Mateyu 7:1) Mogwirizana ndi zimene Luka analemba pa nkhaniyi, Yesu anawonjezera kuti: “Siyani kutsutsa ena ndipo inunso simudzatsutsidwa.”a (Luka 6:37) Yesu anasonyeza kuti amadziwa zoti anthu omwe si angwirofe tili ndi chizolowezi choweruza ena. Aliyense wa anthu omwe ankamumvetserawo, yemwe anali ndi chizolowezi choweruza ena, ankafunika kusiya.
14. Kodi tiyenera ‘kusiya kuweruza ena’ pa zifukwa ziti?
14 N’chifukwa chiyani tiyenera ‘kusiya kuweruza ena’? Chifukwa chimodzi n’chakuti si udindo wathu kuchita zimenezi. Yakobo, yemwe anali wophunzira wa Yesu, anatikumbutsa kuti: “Wopereka Malamulo komanso Woweruza alipo mmodzi yekha” amene ndi Yehova. Choncho Yakobo anafunsa mosapita m’mbali kuti: “Iwe ndiwe ndani kuti uziweruza mnzako?” (Yakobo 4:12; Aroma 14:1-4) Kuwonjezera pamenepa, n’zosavuta kuweruza mopanda chilungamo chifukwa ndife ochimwa. Makhalidwe monga tsankho, kunyada, nsanje ndiponso kudzilungamitsa angachititse kuti tiziona ena molakwika. Komanso anthufe sitidziwa zonse ndipo kuganizira mfundo imeneyi kuyenera kutithandiza kuti tisamafulumire kupezera ena zifukwa. Sitingadziwe za mumtima mwa munthu ndiponso sitingadziwe zonse zokhudza mmene zinthu zilili pa moyo wake. Tikaganizira mfundo zimenezi, ndife ndani kuti tizinena Akhristu anzathu kuti sakuchita zokwanira potumikira Mulungu kapena alibe zolinga zabwino? Ndi bwino kuti tizitsanzira Yehova n’kumaona zabwino zimene abale ndi alongo athu amachita m’malo moganizira kwambiri zimene amalakwitsa.
15. Kodi Akhristu sayenera kulankhula komanso kuchita zinthu ziti?
15 Nanga kodi tiyenera kuchita bwanji zinthu ndi anthu a m’banja lathu? Anthu ayenera kumakhala mwamtendere komanso motetezeka m’banja. Koma n’zomvetsa chisoni kuti masiku ano nthawi zambiri anthu amachitiridwa nkhanza ndi anthu a m’banja lawo. Si zachilendo kumva zokhudza amuna, akazi ndiponso makolo amene amalalatira komanso kuchitira nkhanza anthu a m’banja lawo. Komatu Akhristu sayenera kuchitira ena nkhanza komanso kulankhula mawu okhadzula kapena onyoza. (Aefeso 4:29, 31; 5:33; 6:4) Malangizo a Yesu akuti ‘tisiye kuweruza ena’ komanso ‘tisiye kutsutsa ena’ amagwiranso ntchito panyumba. Kumbukirani kuti tingasonyeze chilungamo pochitira ena zinthu mofanana ndi zimene Yehova amatichitira. Ndipo Mulungu wathu satichitira zinthu mouma mtima kapena mwankhanza. Koma amakonda kwambiri anthu amene amamukonda. (Yakobo 5:11) Chimenechitu ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa ife.
Akulu Amagwira Ntchito Yawo “Mwachilungamo”
16, 17. (a) Kodi Yehova amayembekezera kuti akulu azichita chiyani? (b) Kodi akulu amayenera kuchita chiyani ngati wochimwa sakusonyeza kuti walapa kuchokera pansi pa mtima, ndipo n’chifukwa chiyani?
16 N’zoona kuti tonsefe tili ndi udindo wochita zinthu mwachilungamo. Komabe akulu mumpingo wa Chikhristu ali ndi udindo waukulu pa nkhaniyi. Taonani zimene Yesaya analosera zokhudza “akalonga,” kapena kuti akulu. Iye anati: “Taonani! Mfumu idzalamulira mwachilungamo, ndipo akalonga adzalamuliranso mwachilungamo.” (Yesaya 32:1) Zoonadi, Yehova amayembekezera kuti akulu azigwira ntchito yawo mwachilungamo. Kodi akuluwo angachite bwanji zimenezi?
17 Amuna oyenerera amenewa amadziwa mfundo yakuti, kuti achite chilungamo cha Yehova, ayenera kuthandiza mpingo kukhala woyera. Nthawi zina akulu amafunika kuweruza nkhani zokhudza tchimo lalikulu. Poweruzapo, iwo amakumbukira kuti Yehova amafuna kuti achitire munthuyo chifundo ngati zingatheke kutero. Choncho amayesetsa kuthandiza wochimwayo kuti alape. Koma bwanji ngati munthuyo sakusonyeza kuti walapadi ngakhale kuti ayesetsa kumuthandiza? Zikatere, akulu amayenera kuchita zinthu molimba mtima ndipo amatsatira malangizo a Yehova osonyeza chilungamo chenicheni akuti: “M’chotseni munthu woipayo pakati panu.” Zimenezi zikutanthauza kumuchotsa mumpingo. (1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11) Akulu amamva chisoni kuti akufunika kuchita zimenezi, koma amazindikira kuti n’zofunika poteteza mpingo kuti ukhalebe woyera. Koma iwo amakhulupirirabe kuti nthawi ina wochimwayo nzeru zidzamubwerera ndipo adzabwereranso mumpingo.—Luka 15:17, 18.
18. Kodi akulu amakumbukira chiyani akamapereka malangizo ochokera m’Baibulo?
18 Kuti akulu achite zinthu mwachilungamo, nthawi zina amafunika kupereka malangizo a m’Baibulo. N’zoona kuti akulu sakhalira kufufuza zimene ena akulakwitsa. Komanso samangothamangira kupereka malangizo wina akalakwitsa. Koma nthawi zina Mkhristu ‘angayambe kulowera njira yolakwika mosazindikira.’ Zikatere, akulu amakumbukira kuti munthu amene amatsanzira chilungamo cha Yehova sachita zinthu mwankhaza komanso mopanda chifundo. Choncho amayesetsa “kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.” (Agalatiya 6:1) Ndipo akulu sangakalipire munthu wolakwa kapenanso kumulankhula mawu opweteka. M’malomwake, iwo amapereka malangizo mwachikondi ndipo zimenezi zimalimbikitsa munthuyo. Nthawi zina akulu amafunika kupereka malangizo osapita m’mbali ofotokoza mavuto amene angabwere ngati munthu atapitiriza kuchita zoipa. Komabe akamachita zimenezi amakumbukira kuti munthuyo ndi nkhosa ya Yehova.b (Luka 15:7) Ngati munthu wolakwa akuchita kuoneratu kuti akulu akumupatsa malangizo kapena uphungu mwachikondi komanso chifukwa chomufunira zabwino, zimakhala zosavuta kuti asinthe.
19. Kodi akulu amafunika kusankha zinthu ziti, ndipo ayenera kudalira chiyani?
19 Nthawi zambiri akulu amafunika kusankha zinthu zomwe zimakhudza Akhristu anzawo. Mwachitsanzo, amakumana kuti akambirane ngati abale ena mumpingo akuyenerera kukhala akulu kapena atumiki othandiza. Akulu amadziwa kuti sayenera kuchita zinthu mwatsankho. Posankha zochita, amatsatira mfundo za m’Baibulo zofotokoza zimene m’bale ayenera kuchita kuti akhale woyenera kuikidwa pa udindo, osangoti mmene iwowo akumuonera. Choncho amachita zinthu ‘mopanda tsankho kapena kukondera.’—1 Timoteyo 5:21.
20, 21. (a) Kodi akulu amayesetsa kuchita chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi akulu angatani kuti athandize “anthu amene ali ndi nkhawa”?
20 Akulu amasonyeza chilungamo m’njira zinanso. Atanena kuti akulu azidzachita zinthu “mwachilungamo,” Yesaya ananenanso kuti: “Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo, malo obisalirapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.” (Yesaya 32:2) Choncho akulu amayesetsa kuti azilimbikitsa Akhristu anzawo.
21 Popeza tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana omwe angatifooketse, anthu ambiri amafunika kulimbikitsidwa. Akulu, kodi mungatani kuti muthandize “anthu amene ali ndi nkhawa”? (1 Atesalonika 5:14) Muziwamvetsera mwachifundo. (Yakobo 1:19) Iwo angafune kufotokozera nkhawa zawo munthu amene amamudalira. (Miyambo 12:25) Muziwatsimikizira kuti Yehova komanso abale ndi alongo awo amawakonda kwambiri ndiponso amawaona kuti ndi ofunika. (1 Petulo 1:22; 5:6, 7) Mukhozanso kuwapempherera ndiponso kupemphera nawo limodzi. Zingawalimbikitse kwambiri kumva mkulu akuwapempherera mochokera pansi pamtima. (Yakobo 5:14, 15) Mulungu wathu wachilungamo amaona zonse zimene mumayesetsa kuchita pothandiza anthu amenewa.
Akulu amatsanzira chilungamo cha Yehova akamalimbikitsa anthu omwe ali ndi nkhawa
22. Kodi tingatsanzire Yehova pa nkhani yochita chilungamo m’njira ziti, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?
22 Kunena zoona, tikamatsanzira Yehova pa nkhani yochita zinthu mwachilungamo, timakhala naye pa ubwenzi wolimba. Tikamatsatira mfundo zake zolungama, tikamauza ena uthenga wabwino wothandiza kuti adzapulumuke ndiponso tikamaganizira kwambiri zabwino zimene ena amachita osati zimene amalakwitsa, timakhala kuti tikutsanzira Yehova pa nkhani yochita chilungamo. Akulu, mukamateteza mpingo kuti ukhalebe woyera, mukamapereka malangizo ochokera m’Baibulo, mukamasankha zinthu mosakondera komanso mukamalimbikitsa anthu omwe ali ndi nkhawa, mumakhala mukusonyeza kuti Mulungu ndi wachilungamo. Yehova ayenera kuti amasangalala kwambiri kumwambako akamaona kuti anthu ake akuyesetsa ‘kuchita chilungamo’ pamene akumutumikira.
a Mabaibulo ena amati, “musamaweruze ena” ndiponso “musamatsutse ena.” Koma mawu amenewa akhoza kungotanthauza kuti “musayambe kuweruza” ndiponso “musayambe kutsutsa.” Komabe m’mavesiwa, olemba Baibulo anagwiritsa ntchito mawu omuuza munthu kuti asiye zimene akuchita. Choncho zimene Yesu ananenazi anthu ankazichita pa nthawiyo ndipo ankafunika kuzisiya.
b Pa 2 Timoteyo 4:2, Baibulo limanena kuti nthawi zina akulu amayenera ‘kudzudzula, kutsutsa ndiponso kudandaulira.’ Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “dandaulira” (pa·ra·ka·leʹo) angatanthauzenso “kulimbikitsa.” Mawu enanso a Chigiriki ofanana nawo akuti pa·raʹkle·tos, amanena za loya amene amathandiza munthu wina m’khoti. Choncho ngakhale pamene akulu akupereka malangizo amphamvu, afunikanso kuthandiza munthu amene wafooka mwauzimuyo.