“Kachisi” ndi “Kalonga” Lerolino
“Kalongayo . . . poloŵa iwo aloŵe pakati pawo, ndipo potuluka iwo atulukire pamodzi.”—EZEKIELI 46:10.
1, 2. Kodi ndi choonadi chofunika chiti chimene chikutithandiza kudziŵa mbali yokulira ya tanthauzo la masomphenya a Ezekieli a kachisi?
ARABI ena akale sanakhutire nalo buku la Ezekieli. Malinga n’kunena kwa Talmud, ena a iwo anafika polingalira zolichotsa pamabuku ovomerezedwa a Malemba Oyera. Masomphenya a kachisi anawavuta kwambiri kumasulira ndipo anati anthu sangathe kuwamvetsa. Akatswiri ena a zamaphunziro a Baibulo azizwa ndi masomphenya a Ezekieli a kachisi wa Yehova. Nanga bwanji ifeyo?
2 Kuyambira pamene kulambira koyera kunabwezeretsedwa, Yehova wadalitsa anthu ake mwa kuwapatsa mauniko ochuluka a chidziŵitso chauzimu, kuphatikizapo kuzindikira kachisi wauzimu wa Mulungu—makonzedwe a Yehova onga kachisi a kulambira koyera.a Choonadi chofunika chimenechi chimatithandiza kudziŵa mbali yokulira ya tanthauzo la masomphenya a Ezekieli onena za kachisi. Tiyeni tipende mosamalitsa mbali zinayizo za masomphenya ameneŵa—kachisi, ansembe, kalonga, ndi dziko. Kodi zimenezi zikutanthauzanji lerolino?
Kachisi ndi Inu
3. Kodi tsindwi lam’mwambalo ndi mitengo ya kanjedza yozokotedwa m’makoma a njira zoloŵera m’kachisi zikutiphunzitsanji?
3 Tayerekezerani kuti tikuyendera kachisi wa m’masomphenya ameneyu. Tikukwera masitepe asanu ndi aŵiri kupita kuchipata china chachikulu. Titaloŵa pakhomopo, tikuyang’ana m’mwamba ndi kudabwa. Tsindwi lake lili mamita oposa 30 m’mwamba! Zimenezo zikutikumbutsa kuti zofunika zoloŵera m’makonzedwe a Yehova a kulambira n’zapamwamba. Kuŵala koloŵera m’mazenera kukuunika mitengo yakanjedza yozokotedwa kumakoma, imene Malemba amagwiritsa ntchito kuimira chilungamo. (Salmo 92:12; Ezekieli 40:14, 16, 22) Malo opatulika ameneŵa ndi a anthu olungama m’makhalidwe ndi mwauzimu. Pogwirizana ndi zimenezo, ifenso tikhale olungama kuti Yehova avomereze kulambira kwathu.—Salmo 11:7.
4. Kodi ndani amene sakuloledwa kuloŵa m’kachisi, ndipo zimenezi zikutiphunzitsanji?
4 Kutsidya lililonse la njira kuli zipinda zitatu za alonda. Kodi alondawo adzatilola kuloŵa m’kachisimo? Yehova akuuza Ezekieli kuti mlendo “wosadulidwa m’mtima” asaloŵe. (Ezekieli 40:10; 44:9) Kodi zimenezo zikutanthauzanji? Zikutanthauza kuti Mulungu amavomereza kokha aja okonda malamulo ake ndi kuwatsata kuti akhale olambira ake. (Yeremiya 4:4; Aroma 2:29) Amalola oterowo kuloŵa m’hema wake wauzimu, nyumba yake yolambiriramo. (Salmo 15:1-5) Kuyambira pamene kulambira koyera kunabwezeretsedwa mu 1919, gulu la Yehova la padziko lapansi lamveketsa pang’onopang’ono ndi kutsata malamulo ake a makhalidwe. Amene amakana dala kuwamvera saloledwanso kuyanjana ndi anthu ake. Lerolino, mchitidwe wa m’Baibulo wochotsa anthu olakwa osalapa wapangitsa kuti kulambira kwathu kukhale kosadetsedwa ndi koyera.—1 Akorinto 5:13.
5. (a) Kodi masomphenya a Ezekieli ndi masomphenya a Yohane olembedwa pa Chivumbulutso 7:9-15 akufanana motani? (b) M’masomphenya a Ezekieli, kodi mafuko 12 amene akulambira kubwalo lakunja akuimira ayani?
5 Njirayo ikutulukira kubwalo lakunja, kumene anthu akulambira ndi kutamanda Yehova. Zimenezi zikutikumbutsa za masomphenya a mtumwi Yohane a “khamu lalikulu” lolambira Yehova “usana ndi usiku m’Kachisi mwake.” Mitengo yakanjedza ikusonyezedwa m’masomphenya aŵiriwo. M’masomphenya a Ezekieli, ikukometsera makoma a njira yoloŵera. M’masomphenya a Yohane, olambira ali ndi makhwata a kanjedza m’manja mwawo, kuimira chimwemwe chawo potamanda Yehova ndi pochingamira Yesu monga Mfumu. (Chivumbulutso 7:9-15) M’nkhani ya masomphenya a Ezekieli, mafuko 12 a Israyeli akuimira “nkhosa zina.” (Yohane 10:16; yerekezerani ndi Luka 22:28-30.) Kodi ndinu mmodzi wa awo amene akupeza chimwemwe potamanda Yehova mwa kulengeza Ufumu wake?
6. Kodi cholinga cha zipinda zodyera kubwalo lakunja chinali chiyani, ndipo kodi zimenezi zingawakumbutse mwayi wotani a nkhosa zina?
6 Pamene tikuyendera bwalo lakunja, tikuona zipinda 30 zodyeramo kumene anthu akudyera zopereka zawo zaufulu. (Ezekieli 40:17) Lerolino, a nkhosa zina sapereka nsembe za nyama, koma sabwera opanda kanthu ku kachisi wauzimu. (Yerekezerani ndi Eksodo 23:15.) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Potero mwa Iye [Yesu] tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake. Koma musaiŵale kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena; pakuti nsembe zotere Mulungu akondwera nazo.” (Ahebri 13:15, 16; Hoseya 14:2) Ndi mwayi waukulu kwambiri kupereka nsembe zotero kwa Yehova.—Miyambo 3:9, 27.
7. Kodi kupima kachisi kukutitsimikizira za chiyani?
7 Ezekieli akuona pamene mngelo akupima kachisi wa m’masomphenyawo. (Ezekieli 40:3) Mofananamo, mtumwi Yohane anauzidwa kuti: “Tanyamuka, nuyese Kachisi wa Mulungu, ndi guwa la nsembe, ndi iwo akulambiramo.” (Chivumbulutso 11:1) Kodi kupima kumeneku kukutanthauzanji? Malinga ndi umboni, zimenezo m’nkhani zonse ziŵiri zinali chitsimikizo chakuti palibe chimene chingaletse Yehova kukwaniritsa zolinga zake zokhudza kulambira koyera. Momwemonso lerolino, tikutsimikiza kuti palibe chilichonse—ngakhale chitsutso choopsa cha maboma amphamvu—chimene chingaletse kubwezeretsa kulambira koyera.
8. Kodi ndani akuloŵa pazipata zoloŵera kubwalo lamkati, ndipo kodi zipatazi zikutikumbutsa chiyani?
8 Pamene tikudutsa bwalo lakunja, tikuona zipata zitatu zoloŵera kubwalo lamkati; zipata zamkati zikutsatizana ndi zipata zakunja ndipo ukulu wake n’chimodzimodzi. (Ezekieli 40:6, 20, 23, 24, 27) Ansembe okha ndi amene ayenera kuloŵa m’bwalo lamkati. Zipata zamkati zikutikumbutsa kuti odzozedwa ayenera kukwanitsa miyezo yaumulungu ndi malamulo ake, koma miyezo ndi malamulo amodzimodziwo amatsogoza Akristu onse oona. Nanga kodi ansembe akuchita ntchito yotani, ndipo ili ndi tanthauzo lanji lero?
Ansembe Okhulupirika
9, 10. Kodi “ansembe achifumu,” monga momwe anachitiridwa chithunzi ndi ansembe m’masomphenya a Ezekieli, apereka motani malangizo auzimu?
9 Chikristu chisanakhaleko, ansembe ankachita ntchito yolimba pakachisi. Ntchito yopha nyama za nsembe, kuzipereka paguwa la nsembe, ndi kutumikira ansembe anzawo ndi anthu ena, inali ntchito yovuta kwambiri. Komanso anali ndi ntchito ina yofunika. Yehova analamula ponena za ansembe kuti: “Aziphunzitsa anthu anga asiyanitse pakati pa zopatulika ndi zinthu wamba, ndi kuwazindikiritsa pakati pa zodetsa ndi zoyera.”—Ezekieli 44:23; Malaki 2:7.
10 Kodi mukuyamikira ntchito yaikulu ndi utumiki wodzichepetsa umene odzozedwa monga gulu, “ansembe achifumu,” achita kuchirikiza kulambira koyera? (1 Petro 2:9) Monga ansembe achilevi akale aja, iwo atsogolera pakupereka malangizo auzimu, kuthandiza anthu kuzindikira choyera ndi chovomerezeka pamaso pa Mulungu ndiponso chodetsa ndi chosavomerezeka. (Mateyu 24:45) Malangizo otero, operekedwa kudzera m’zofalitsa zozikidwa pa Baibulo ndi misonkhano yachikristu yaing’ono ndi yaikulu, athandiza anthu mamiliyoni ambiri kuyanjanitsidwa ndi Mulungu.—2 Akorinto 5:20.
11. (a) Kodi masomphenya a Ezekieli anagogomezera motani kufunika kwa chiyero cha ansembe? (b) M’masiku otsiriza, kodi odzozedwa ayeretsedwa motani m’lingaliro lauzimu?
11 Komabe, ansembe ayenera kuchita zambiri osati chabe kuphunzitsa ena kukhala oyera; iwo eniwo ayenera kukhala oyera. Chotero, Ezekieli anaoneratu kuyeretsedwa kwa ansembe a Israyeli. (Ezekieli 44:10-16) Mofananamo, mu 1918, Yehova anakhala pansi monga ‘woyenga’ m’kachisi wake wauzimu, kupenda kagulu ka ansembe odzozedwa. (Malaki 3:1-5) Aja amene anapezeka oyera mwauzimu pokhala atalapa pa kupembedza kwawo mafano kwakale analoledwa kupitiriza ndi udindo wotumikira m’kachisi wake wauzimu. Komabe, monga wina aliyense, munthu aliyense wodzozedwa angakhale wodetsedwa—mwauzimu kapena mwamakhalidwe. (Ezekieli 44:22, 25-27) Iwo akhala akuyesetsa zedi kukhalabe “osachitidwa maŵanga ndi dziko lapansi.”—Yakobo 1:27; yerekezerani ndi Marko 7:20-23.
12. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira ntchito ya odzozedwa?
12 Aliyense wa ife angafunse kuti, ‘Kodi ndimayamikira chitsanzo chimene odzozedwa apereka pazaka zambiri zautumiki wawo wokhulupirika? Kodi ndikutsanzira chikhulupiriro chawo?’ Ndi bwino kuti a khamu lalikulu azikumbukira kuti sadzakhala ndi odzozedwa nthaŵi zonse pano padziko lapansi. Ponena za ansembe m’masomphenya a Ezekieli, Yehova anati: “Musawapatsa cholandira chawo [cha malo] m’Israyeli; Ine ndine cholandira chawo.” (Ezekieli 44:28) Mofananamo, odzozedwa sadzakhala kosatha padziko lapansi. Iwo ali ndi choloŵa chakumwamba, ndipo a khamu lalikulu amaona kuti ali ndi mwayi kuwachirikiza ndi kuwalimbikitsa pamene adakali pano padziko lapansi.—Mateyu 25:34-40; 1 Petro 1:3, 4.
Kalonga—Kodi Iye Ndani?
13, 14. (a) Kodi n’chifukwa chiyani kalonga ayenera kukhala wapakati pa nkhosa zina? (b) Kodi kalonga akuimira yani?
13 Tsopano pakubuka funso lodzutsa chidwi. Kodi kalonga akuimira yani? Popeza akufotokozedwa monga munthu mmodzi ndiponso monga kagulu, tinganene kuti akuimira kagulu kena ka anthu. (Ezekieli 44:3; 45:8, 9) Anthu ati? Osati odzozedwa ayi. M’masomphenyawo, iye akugwira ntchito mogwirizana kwambiri ndi ansembe, koma sali mmodzi wa iwo. Kusiyana ndi kagulu ka ansembe, iye akupatsidwa choloŵa m’dzikolo ndipo tsogolo lake lili pano padziko lapansi, osati kumwamba. (Ezekieli 48:21) Ndiponso, Ezekieli 46:10 amati: “Kalongayo tsono, poloŵa iwo [mafuko osakhala ansembe m’bwalo lakunja la kachisi] aloŵe pakati pawo, ndipo potuluka iwo atulukire pamodzi.” Saloŵa m’bwalo lamkati koma alambirira m’bwalo lakunja, kuloŵa ndi kutuluka m’kachisi pamodzi ndi anthu. Mbali zimenezi mosakayikira zikuonetsa kuti kalonga ali pakati pa khamu lalikulu la nkhosa zina.
14 Mwachionekere, kalongayo ali ndi udindo pakati pa anthu a Mulungu. M’bwalo lakunja, iye akukhala m’khonde la Chipata Chakummaŵa. (Ezekieli 44:2, 3) Zimenezi zikusonyeza malo a uyang’aniro, ofanana ndi amuna akulu m’Israyeli, amene ankakhala pachipata cha mudzi ndi kuweruza milandu. (Rute 4:1-12; Miyambo 22:22) Kodi ndani pakati pa nkhosa zina amene ali ndi udindo woyang’anira lerolino? Akulu oyembekezera kukhala padziko lapansi oikidwa ndi mzimu woyera. (Machitidwe 20:28) Chotero kagulu ka kalonga kakukonzekeretsedwa tsopano kuti pambuyo pake kadzakhale ndi udindo woyang’anira m’dziko latsopano.
15. (a) Kodi masomphenya a Ezekieli akusonyeza motani unansi umene uli pakati pa akulu a m’khamu lalikulu ndi kagulu ka ansembe odzozedwa? (b) Kodi akulu odzozedwa atsogolera motani m’gulu la Mulungu la padziko lapansi?
15 Nanga kodi pali unansi wotani pakati pa kagulu ka ansembe odzozedwa ndi amuna akulu amenewo amene, pokhala a m’khamu lalikulu, akutumikira pamaudindo auyang’aniro? Masomphenya a Ezekieli akusonyeza kuti akulu amene ali a khamu lalikulu ali ndi ntchito yochirikiza ndiponso yaing’ono, pamene odzozedwa akutsogolera pa zauzimu. Motani? Kumbukirani kuti m’masomphenyawo ansembe anapatsidwa udindo wophunzitsa anthu zinthu zauzimu. Anauzidwanso kukhala oweruza milandu. Ndiponso, Alevi anapatsidwa ‘malo akuyang’anira’ kuzipata. (Ezekieli 44:11, 23, 24) Mwachionekere, kalonga anafunikira kugonjera modzichepetsa pamautumiki auzimu ndi utsogoleri wa ansembe. Pamenepa, n’koyenera kuti lerolino odzozedwa akutsogolera pakulambira koyera. Mwachitsanzo, mamembala a Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova asankhidwa mwa iwo. Akulu amenewo odzozedwa ndiponso okhulupirika akhala akuphunzitsa kagulu komakula ka kalonga kwa zaka zambiri, kukonzekeretsa amene adzakhala mamembala a kagulu kameneka kaamba ka tsiku pamene adzapatsidwa ulamuliro wonse m’dziko latsopano la Mulungu likudzalo.
16. Malinga ndi Yesaya 32:1, 2, kodi akulu onse ayenera kuchitanji?
16 Kodi ameneŵa amene adzakhala mamembala ndiponso odikirira maudindo okulirapo monga kagulu ka kalonga, ali oyang’anira amtundu wanji? Ulosi wopezeka pa Yesaya 32:1, 2 umati: “Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo. Ndipo munthu adzakhala monga pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo; monga mitsinje yamadzi m’malo ouma, monga mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko lotopetsa.” Ulosi umenewu ukukwaniritsidwa lero, pamene akulu achikristu—odzozedwa ndi a nkhosa zina—akugwira ntchito kuteteza nkhosa ku “chimphepo” cha chizunzo ndi kugwa mphwayi.
17. Kodi abusa achikristu ayenera kudziona motani, ndipo nkhosa ziyenera kuwaona motani?
17 Liwu lakuti “kalonga” silikugwiritsidwa ntchito monga dzina laulemu lokweza nalo anthu. M’malo mwake, likufotokoza udindo umene amuna ameneŵa akusenza posamalira nkhosa za Mulungu. Yehova akuchenjeza mwamphamvu kuti: “Likufikireni akalonga a Israyeli inu, lekani kuchita chiwawa, ndi kulanda za eni ake; muchite chiweruzo ndi chilungamo.” (Ezekieli 45:9) Ndi bwino kuti akulu onse alabadire uphungu umenewo lerolino. (1 Petro 5:2, 3) Nkhosanso zikuzindikira kuti Yesu wapereka abusa monga “mphatso mwa amuna.” (Aefeso 4:8, NW) Ziyeneretso zawo zafotokozedwa m’Mawu ouziridwa a Mulungu. (1 Timoteo 3:1-7; Tito 1:5-9) Chotero Akristu amatsata chitsogozo cha akulu.—Ahebri 13:7.
18. Kodi lerolino ena mwa maudindo a amene adzakhala a kagulu ka kalonga ndi otani, ndipo kodi kadzakhala ndi udindo wotani m’tsogolo?
18 M’nthaŵi za Baibulo akalonga ena anali ndi ulamuliro waukulu, ena anali ndi wochepa. Lerolino, akulu a khamu lalikulu ali ndi maudindo osiyanasiyana kwambiri. Ena amatumikira mumpingo umodzi; ena amatumikira mipingo yambiri monga oyang’anira oyendayenda; ena amatumikira mayiko athunthu monga mamembala a Komiti ya Nthambi; enanso amathandizira mwachindunji m’makomiti osiyanasiyana a Bungwe Lolamulira. M’dziko latsopano, Yesu adzaika “mafumu [“akalonga,” NW] m’dziko lonse lapansi” kuti atsogolere olambira a Yehova padziko lapansi. (Salmo 45:16) Mosakayikira Yesu adzasankha ambiri a ameneŵa mwa akulu okhulupirika lerolino. Popeza amuna ameneŵa akuonetsa umboni wotsimikiza panopo, iye adzasankha zoikiza ambiri ndi maudindo okulirapo m’tsogolo pamene adzasonyeza ntchito ya kagulu ka kalonga m’dziko lapansi latsopano.
Dziko la Anthu a Mulungu Lerolino
19. Kodi dziko la m’masomphenya a Ezekieli limaimira chiyani?
19 Masomphenya a Ezekieli amasonyezanso dziko lobwezeretsedwa la Israyeli. Kodi mbali imeneyi ya masomphenya ikuimira chiyani? Maulosi ena onena za kubwezeretsa analosera kuti dziko limenelo, Israyeli, lidzakhala paradaiso ngati Edene. (Ezekieli 36:34, 35) Lerolino, tikusangalala ndi “dziko” lobwezeretsedwa, ndipo ilonso lili ngati Edene m’lingaliro lina. Mofananamo, nthaŵi zambiri timalankhula za paradaiso wathu wauzimu. Nsanja ya Olonda yafotokoza kuti “dziko” lathu ndilo “dera la ntchito” la anthu a Mulungu osankhidwa.b Kulikonse kumene mtumiki wa Yehova angakhale, ali m’dziko limenelo lobwezeretsedwa malinga ngati akuyesetsa kuchirikiza kulambira koona mwa kuyenda m’mapazi a Kristu Yesu.—1 Petro 2:21.
20. Kodi tingaphunzirepo pulinsipulo lotani pa “chopereka chopatulika” cha m’masomphenya a Ezekieli, ndipo pulinsipuloli tingaligwiritse ntchito motani?
20 Bwanji nanga za gawo la dzikolo lotchedwa “chopereka chopatulika”? Anthu analipereka kuthandiza ansembe ndi mudzi wawo. Mofananamo, “anthu onse a m’dziko” anayenera kupereka gawo la dzikolo kwa kalonga. Kodi zimenezi zikutanthauzanji lerolino? Osati kuti anthu a Mulungu azisenza mtolo wosamalira kagulu ka atsogoleri achipembedzo olipiridwa. (2 Atesalonika 3:8) M’malo mwake, chichirikizo chimene akulu lerolino amalandira n’chauzimu makamaka. Chikuphatikizapo kuthandiza pantchito imene ikuchitika ndi kuonetsa mzimu wa kugwirizana ndi kugonjera. Komabe, monga m’tsiku la Ezekieli, chopereka chimenechi chimapatsidwa “kwa Yehova,” osati kwa munthu aliyense.—Ezekieli 45:1, 7, 16.
21. Kodi kugaŵa dziko kwa m’masomphenya a Ezekieli kungatiphunzitsenji?
21 Si kalonga ndi ansembe okha omwe agaŵiridwa malo m’dziko limeneli lobwezeretsedwa. Kugaŵidwa kwa dzikolo kukusonyeza kuti lililonse la mafuko 12 lili ndi choloŵa chotetezeka. (Ezekieli 47:13, 22, 23) Chotero a khamu lalikulu sali chabe ndi malo m’paradaiso wauzimu lerolino komanso adzapatsidwa gawo pamene adzalandira malo padziko lapansi mu Ufumu wa Mulungu.
22. (a) Kodi mudzi wa m’masomphenya a Ezekieli ukuimira chiyani? (b) Kodi mfundo yakuti mudziwo uli ndi zipata kumbali zonse ikutiphunzitsanji?
22 Pomaliza, kodi mudzi wa m’masomphenyawo ukuimira chiyani? Suli mudzi wakumwamba, pakuti uli pakati pa dziko “wamba” (losapatulika). (Ezekieli 48:15-17) Chotero uyenera kukhala wa padziko lapansi. Chabwino, kodi mudzi n’chiyani? Kodi liwulo silikupereka lingaliro la anthu okhala pamodzi monga gulu amene ali olinganizidwa? Inde. Choncho, mudziwo ukuoneka kuti ukuimira uyang’aniro wa padziko lapansi umene udzapindulitsa onse amene adzapanga mtundu wolungama wapadziko lapansi. Udzagwira ntchito mwachikwanekwane mu “dziko latsopano” likudzalo. (2 Petro 3:13) Zipata za mudziwo kumbali zake zonse, chimodzi pa mtundu umodzi, zikusonyeza bwino lomwe kuti mudziwo n’ngwotseguka. Lerolino, anthu a Mulungu sakuyang’aniridwa ndi anthu ena osadziŵika bwino, ochita zinthu mobisala. Abale okhala ndi udindo ayenera kukhala ofikirika; mapulinsipulo amene amawatsogoza n’ngodziŵika bwino kwa onse. Mfundo yakuti anthu ochokera m’mafuko onse akulima munda wochirikiza mudziwo ikutikumbutsa kuti a nkhosa zina, ngakhale mwa kupereka chuma chakuthupi, akuchirikiza makonzedwe auyang’aniro opangidwira anthu a Mulungu padziko lonse.—Ezekieli 48:19, 30-34.
23. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?
23 Bwanji nanga za mtsinje wochokera m’malo opatulika a kachisi? Zimene umaimira lerolino ndi m’tsogolo n’zimene tidzakambirana m’nkhani yachitatu ndi yomaliza ya nkhani zotsatizanazi.
[Mawu a M’munsi]
a Onani buku la Revelation—Its Grand Climax At Hand!, tsamba 64, ndime 22, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Mfundo Zopenda
◻ Kodi kachisi wa m’masomphenya a Ezekieli akuimira chiyani?
◻ Kodi ansembe amene akutumikira pakachisi akuimira yani?
◻ Kodi kagulu la kalonga n’chiyani, ndipo ena mwa maudindo ake ndi otani?
◻ Kodi dziko la m’masomphenya a Ezekieli n’chiyani, ndipo n’logaŵidwa kwa mafuko 12 m’lingaliro lotani?
◻ Kodi mudzi ukuimira chiyani?
[Chithunzi/Mapu patsamba 15]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Kugaŵidwa kwa dziko kolongosoledwa m’masomphenya a Ezekieli
MAFUKO KHUMI NDI AŴIRI
Nyanja Yaikulu
Nyanja ya Galileya
Mtsinje wa Yordano
Nyanja ya Mchere
DANI
ASERI
NAFITALI
MANASE
EFRAIMU
RUBENI
YUDA
KALONGA
BENJAMINI
SIMEONI
ISAKARA
ZEBULONI
GADI
[Chithunzi]
CHITHUNZI CHACHIKULU CHA CHOPEREKA CHOPATULIKA
A. “Yehova Ali Pomwepo” (Yehova-Sama); B. Minda ya mudzi
Gawo la Alevi
Malo Opatulika a Yehova
Gawo la Ansembe
B A B