Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’buku la Yeremiya
MASOKA omwe Yeremiya analengeza kwa anthu ake anali ochititsa mantha kwambiri. Kachisi wokongola mochititsa chidwi yemwe kwa zaka zoposa 300, anali likulu la kulambira, adzatenthedwa n’kukhala phulusa lokhalokha. Mzinda wa Yerusalemu ndiponso dziko la Yuda zidzawonongedweratu, ndipo anthu ake adzatengedwa ukapolo. Nkhani imeneyi komanso ziweruzo zina zinalembedwa m’buku la Yeremiya, lomwe ndi lachiwiri pa mabuku akuluakulu a m’Baibulo. Bukuli limafotokozanso zimene zinam’chitikira Yeremiya pamene ankatumikira mokhulupirika kwa zaka 67. Nkhani zomwe zili m’buku limeneli sizinalembedwe motsatira nthawi imene zinachitikira, koma mogwirizana ndi mitu yake.
N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi buku la m’Baibulo la Yeremiya? Maulosi ake omwe anakwaniritsidwa amathandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba choti Yehova adzakwaniritsa malonjezo ake a zam’tsogolo. (Yesaya 55:10, 11) Ntchito imene mneneri Yeremiya anachita ndiponso mmene anthu analabadirira uthenga wake, n’zofanana kwambiri ndi mmene zikuchitikira masiku ano. (1 Akorinto 10:11) Ndiponso, nkhani za mmene Yehova anachitira zinthu ndi anthu ake zimasonyeza makhalidwe ake ndipo ziyenera kutikhudza kwambiri.—Aheberi 4:12.
“ANTHU ANGA ANACHITA ZOIPA ZIWIRI”
Yeremiya anasankhidwa kukhala mneneri m’chaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya, mfumu ya Yuda, ndipo kunali kutatsala zaka 40 kuti Yerusalemu awonongedwe mu 607 B.C.E. (Yeremiya 1:1, 2) Zinthu zomwe analengeza makamaka kutatsala zaka 18 za ulamuliro wa Yosiya zinavumbula kuipa kwa Yuda ndipo zinasonyeza ziweruzo za Yehova zimene Yuda analandira. Yehova anati: “Ndidzayesa Yerusalemu miyulu . . . ndipo ndidzayesa midzi ya Yuda bwinja, lopanda wokhalamo.” (Yeremiya 9:11) N’chifukwa chiyani anadzachita zimenezi? Iye anati: “Pakuti anthu anga anachita zoipa ziwiri.”—Yeremiya 2:13.
Yeremiya anaperekanso uthenga wa kubwezeretsedwa kwa otsalira omwe analapa. (Yeremiya 3:14-18; 12:14, 15; 16:14-21) Koma anthu sanam’landire. “Kapitawo wamkulu m’nyumba ya Yehova” anamenya Yeremiya ndipo anamuika m’matangadza usiku wonse.—Yeremiya 20:1-3.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:11, 12—Kodi kudikira mawu ake kumene Yehova anachita kukugwirizana motani ndi “nthyole ya katungulume”? Mtengo wa katungulume ndi umodzi mwa mitengo imene imayambirira kuphuka m’nyengo ya masika [m’miyezi ya March mpaka May]. Mophiphiritsa, Yehova anali ‘kuuka mamawa ndi kutumiza aneneri’ kuti akachenjeze anthu ake za ziweruzo zake, ndipo iye ‘ankadikira’ kufikira zitakwaniritsidwa.—Yeremiya 7:25.
2:10, 11—N’chifukwa chiyani zochita za Aisiraeli osakhulupirika zinali zodabwitsa kwambiri? Mitundu imene sinkalambira Yehova yomwe inkakhala kumadzulo kwa dziko la Aisiraeli mpaka ku Kitimu ndi kum’mawa kwa dzikolo mpaka ku Kedara inkabweretsa milungu ya mitundu ina kuiphatikiza pa imene iwo anali nayo. Iwo sanaganizireko n’komwe zoti angasiye kulambira milungu yawoyo n’kumalambira yachilendo yokhayo basi. Koma Aisiraeli anasiyiratu Yehova ndi kuyamba kulambira mafano.
3:11-22; 11:10-12, 17—N’chifukwa chiyani Yeremiya anaphatikiza ufumu wa kumpoto wa mafuko khumi pa uthenga wake wa ziweruzo ngakhale kuti Samariya anali atawonongedwa kale mu 740 B.C.E.? Chifukwa chake n’chakuti kuwonongedwa kwa Yerusalemu mu 607 B.C.E. kunasonyeza chiweruzo cha Yehova pa mtundu wonse wa Isiraeli, osati pa Yuda yekha. (Ezekieli 9:9, 10) Ndipo mzindawu utawonongedwa, ufumu wa kumpoto wa mafuko khumi unkafunabe kuti Yerusalemu abwezeretsedwe. Izi zinali choncho chifukwa mauthenga a aneneri a Mulungu ankakhudzabe Aisiraeli.
4:3, 4—Kodi lamulo lomwe lili palembali likutanthauza chiyani? Ayuda osakhulupirika anafunikira kukonzekeretsa, kufewetsa, ndi kuyeretsa mitima yawo. Iwo anafunikira kuchotsa “khungu” la mitima yawo, kutanthauza kuchotsa maganizo ndi zolinga zawo zoipa. (Yeremiya 9:25, 26; Machitidwe 7:51) Zimenezi zinafuna kuti iwo asinthe moyo wawo, kusiya zoipa ndi kuyamba kuchita zomwe zikanawathandiza kuti Mulungu awadalitse.
4:10; 15:18—Kodi Yehova ananyenga motani anthu ake opanduka? M’nthawi ya Yeremiya, panali aneneri ena omwe ‘ankanenera monyenga.’ (Yeremiya 5:31; 20:6; 23:16, 17, 25-28, 32) Yehova sanawaletse kulengeza mauthenga achinyengo.
16:16—Kodi mawu oti Yehova ‘adzaitana akugwira nsomba ambiri’ ndi “osaka nyama ambiri,” amatanthauzanji? Izi zingatanthauze kutumiza adani kumene Yehova anadzachita kuti akafufuze Ayuda osakhulupirika omwe ankafuna kuwaweruza. Koma malinga ndi zomwe Yeremiya 16:15 amanena, vesili lingatanthauzenso kufufuza Aisiraeli omwe analapa.
20:7—Kodi Yehova anagwiritsa ntchito motani ‘mphamvu zake’ kuti akope Yeremiya? N’chifukwa choti anthu sankamvera uthenga wake, ankam’kana ndi kum’zunza pamene ankalengeza ziweruzo za Yehova, mwina Yeremiya anaona kuti analibe mphamvu zoti apitirize kuchita ntchitoyi. Koma Yehova anamuwonjezera mphamvu Yeremiya kuti athetse maganizo amenewa n’kupitiriza ntchito yake. Motero, Yehova anakopa mneneri Yeremiya mwa kum’gwiritsa ntchito kuti achite zimene iye ankaganiza kuti sangathe.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:8. Nthawi zina Yehova angalanditse anthu ake ku chizunzo mwina mwa kugwiritsa ntchito oweruza opanda tsankhu. Ndipo nthawi zina angalole kuti akulu aboma okakala mtima alowedwe m’malo ndi ena abwino, kapena angapatse olambira ake mphamvu zoti athe kupirira.—1 Akorinto 10:13.
2:13, 18. Aisiraeli osakhulupirika anachita zinthu ziwiri zoipa. Iwo anasiya Yehova yemwe akanathadi kuwadalitsa, kuwatsogolera ndi kuwateteza. Iwo anadzikumbira zitsime zophiphiritsa mwa kuchita mapangano othandizana pa nkhondo ndi Iguputo ndi Asuri. Masiku ano, ngati wina angasiye Mulungu n’kumatsatira mfundo za anthu ndiponso ndale, ndiye kuti wasinthitsa “kasupe wa madzi amoyo” ndi “zitsime zong’aluka.”
6:16. Yehova analimbikitsa anthu ake opanduka kuti aime kaye ndi kuonanso bwinobwino moyo wawo, n’cholinga choti abwerere ku “mayendedwe” a makolo awo okhulupirika akale. Kodi sizoona kuti tiyenera kudzipenda nthawi ndi nthawi kuti tione ngati tikuyendadi m’njira yomwe Yehova akufuna kuti tiyendemo?
7:1-15. Ngakhale kuti Ayuda ankadalira kachisi n’kumamuona ngati chithumwa chowateteza, kachisiyu sanawapulumutse. Tiyenera kuyenda mwa chikhulupiriro osati mwa zooneka ndi maso.—2 Akorinto 5:7.
15:16, 17. Mofanana ndi Yeremiya, ifenso tingathe kulimbana ndi zinthu zomwe zingatilefule. Tingachite zimenezi mwa kuphunzira Baibulo mwakhama patokha, kutamanda dzina la Yehova mu utumiki, ndiponso kupewa kucheza ndi anthu oipa.
17:1, 2. Yehova sanasangalale ndi nsembe za anthu a ku Yuda chifukwa cha machimo awo. Nsembe zathu zotamanda Mulungu sizingalandiridwe ngati tili ndi khalidwe loipa.
17:5-8. Tingachite bwino kudalira anthu ndi mabungwe awo pamene iwo akuchita zinthu zogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu ndiponso mfundo zake za m’Baibulo. Koma ponena za chipulumutso ndi mtendere weniweni, ndi bwino kuti tidzikhulupirira Yehova yekha basi.—Salmo 146:3.
20:8-11. Tisalole mphwayi, chitsutso, kapena chizunzo kuti zichepetse changu chathu pantchito yolalikira Ufumu.—Yakobe 5:10, 11.
“LONGANI MAKOSI ANU M’GOLI LA MFUMU YA KU BABULO”
Yeremiya analengeza ziweruzo kwa mafumu anayi omaliza a Yuda ndiponso kwa aneneri onama, abusa oipa, ndi ansembe achinyengo. Mwa kutchula anthu otsalira okhulupirika kuti ali ngati nkhuyu zabwino, Yehova anati: “Ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwachitire iwo bwino.” (Yeremiya 24:5, 6) Maulosi atatu omwe ali mu chaputala 25 afotokoza mwachidule ziweruzo zimene zafotokozedwa momveka bwino m’machaputala akutsogolo.
Ansembe ndi aneneri anakonza chiwembu choti aphe Yeremiya. Uthenga wa Yeremiya unali woti iwo adzatumikira mfumu ya ku Babulo. Yeremiya anauza Mfumu Zedekiya kuti: “Longani makosi anu m’goli la mfumu ya ku Babulo.” (Yeremiya 27:12) Komabe, “iye amene anabalalitsa Isiraeli adzasonkhanitsa [Isiraeli].” (Yeremiya 31:10) Pazifukwa zomveka, Arekabu analandira lonjezo. Yeremiya anaikidwa “m’bwalo la kaidi.” (Yeremiya 37:21) Yerusalemu anawonongedwa, ndipo anthu ake ambiri anatengeredwa ku ukapolo. Yeremiya ndi mlembi wake, Baruki, anali pakati pa anthu ochepa omwe anatsala. Ngakhale kuti Yeremiya anayesetsa kuwachenjeza kuti asachoke, anthu omwe ankachita mantha anathawira ku Iguputo. Machaputala 46 mpaka 51 amafotokoza uthenga umene Yeremiya analengeza wokhudza anthu a mitundu ina.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba
22:30—Kodi lamuloli likusonyeza kuti Yesu Khristu sanali woyenera kukhala pa mpando wachifumu wa Davide? (Mateyo 1:1, 11) Ayi. Lamuloli linaletsa mbadwa za Yehoyakimu “kukhala pa mpando wachifumu wa Davide . . . m’Yuda.” Yesu anali kudzalamulira ali kumwamba osati ali pampando wachifumu m’Yuda.
23:33—Kodi “katundu wa Yehova” n’chiyani? M’nthawi ya Yeremiya, uthenga wamphamvu umene mneneriyu analengeza wonena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu unali katundu kwa anthu omwe ankakhala nawo m’dzikolo. Ndipo anthu omwe sanalabadire uthengawu nawonso anali katundu kwa Yehova moti anawakana. Mofananamo, uthenga wa m’Malemba wonena za chiwonongeko cha Matchalitchi Achikhristu chomwe chikubwera uli katundu kwa iwo, ndipo anthu omwe salabadira uthengawu alinso katundu kwa Mulungu.
31:33—Kodi chilamulo cha Mulungu chimalembedwa motani m’mitima? Munthu akamakonda kwambiri chilamulo cha Mulungu moti amafuna kwambiri kuchita chifuniro cha Yehova, tinganene kuti chilamulo cha Mulungu chalembedwa m’mtima mwake.
32:10-15—Kodi cholinga chomwe analembera zikalata ziwiri zokhudza pangano limodzi n’chiyani? Chikalata chovundukuka chinali choti anthu ena azichiona. Koma chikalata chosindikizidwa chinkachitira umboni kuti chikalata chovundukukacho chinalidi choona. Yeremiya anatipatsa chitsanzo chabwino mwa kutsatira mfundo za malamulo, ngakhale pochita zinthu ndi wachibale kapena wokhulupirira mnzathu.
33:23, 24—Kodi “mabanja awiri” amene akunenedwa palembali ndi ati? Loyamba ndi banja lachifumu la m’mzera wa mafumu womwe Mfumu Davide anabadwira, ndipo linalo ndi banja la ansembe a mbadwa za Aroni. Koma pamene Yerusalemu ndi kachisi wa Yehova zinawonongedwa, zikuoneka kuti Yehova anakana mabanja awiriwa ndipo sanakhalenso ndi ufumu padziko lapansi kapena kuyambitsanso kulambira koyera.
46:22—N’chifukwa chiyani mawu a Iguputo anawafanizira ndi a njoka? Zimenezi zingatanthauze mkokomo wa njoka yothawa, kapena mmene Iguputo anachitira manyazi chifukwa cha kuwonongedwa kwake. Kufanizira kumeneku kunasonyezanso kuti zimene mafumu a ku Iguputo ankachita zinali zosathandiza. Ankavala nduwira kumutu zokhala ndi chizindikiro cha njoka chomwe ankachiona kuti n’chopatulika komanso kuti chinali kuwateteza. Chizindikirochi chinkaimira mulungu wawo wotchedwa Uatchit.
Zimene Tikuphunzirapo:
21:8, 9; 38:19. Ngakhale kuti nthawi inali itatha kale, Yehova anapereka mwayi woti anthu osalapa ndiponso oyenera kuphedwa a ku Yerusalemu alape. N’zoonadi, “zifundo zake n’zazikulu.”—2 Samueli 24:14; Salmo 119:156.
31:34. N’zolimbikitsatu kwabasi kudziwa kuti Yehova samakumbukiranso machimo a anthu omwe wawakhululukira ndiponso kuti m’tsogolo muno sangalange anthuwo chifukwa cha machimo amene iye anawakhululukira.
38:7-13; 39:15-18. Yehova samaiwala utumiki wathu umene timauchita mokhulupirika, womwe umaphatikizapo “kutumikira oyera.”—Aheberi 6:10.
45:4, 5. Mofanana ndi mmene zinthu zinalili m’masiku otsiriza a Yuda, “masiku otsiriza” a dongosolo lino la zinthu si nthawi yofuna “zinthu zazikulu” monga ndalama, kutchuka, kapenanso chuma.—2 Timoteyo 3:1; 1 Yohane 2:17.
YERUSALEMU ATENTHEDWA
Chaka cha 607 B.C.E., chinali chaka cha 11 mu ulamuliro wa mfumu Zedekiya. Ndipo mfumu ya ku Babulo, Nebukadinezara inali itazinga Yerusalemu kwa miyezi 18 tsopano. Patsiku la 7 la mwezi wachisanu, m’chaka cha 19 cha ulamuliro wa Nebukadinezara, mkulu wa asilikali oteteza mfumu dzina lake Nebuzaradani, “anadza,” kapena kuti anafika ku Yerusalemu. (2 Mafumu 25:8) Mwina Nebuzaradani ankachokera ku misasa imene anamanga kunja kwa mpanda wa Yerusalemu, n’kumakazonda mzindawo kuti adziwe mmene angaugonjetsere. Patangopita masiku atatu okha, patsiku la khumi la mweziwu, Nebuzaradani “anadza,” kapena kuti analowa mu Yerusalemu, ndipo anatentha mzindawu ndi moto.—Yeremiya 52:12, 13.
Yeremiya anafotokoza momveka bwino za kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Kufotokoza kumeneku kunachititsa kuti pakhale nyimbo za chisoni. Nyimbo zimenezi zinalembedwa m’buku la m’Baibulo lotchedwa Maliro.
[Chithunzi patsamba 8]
Mauthenga amene Yeremiya ankapereka okhudza ziweruzo za Yehova anaphatikizapo kuwonongedwa kwa Yerusalemu
[Chithunzi patsamba 9]
Kodi Yehova anagwiritsa ntchito motani ‘mphamvu zake’ kuti akope Yeremiya?
[Chithunzi patsamba 10]
“Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am’nsinga a Yuda.”—Yeremiya 24:5