Mutu 39
Mfumu Yankhondo Idzapambana pa Aramagedo
Masomphenya 13—Chivumbulutso 19:11-21
Nkhani yake: Yesu adzatsogolera magulu ankhondo akumwamba powononga dziko la Satanali
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Babulo Wamkulu akadzawonongedwa
1. Kodi Aramagedo n’chiyani, ndipo idzayambika bwanji?
ANTHU ambiri amachita mantha akamva mawu akuti Aramagedo. Koma anthu okonda chilungamo akamva mawuwa amaganizira za tsiku limene akhala akuliyembekezera kwa nthawi yaitali, pamene Yehova adzapereke chiweruzo chomaliza ku mitundu yonse ya anthu. Nkhondo ya Aramagedo sidzakhala ya anthu koma idzakhala ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse,’ pamene iye adzalange olamulira a dziko lapansi. (Chivumbulutso 16:14, 16; Ezekieli 25:17) Kuwonongedwa kwa Babulo Wamkulu, kudzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu. Kenako polimbikitsidwa ndi Satana, chilombo chofiira kwambiri komanso nyanga zake 10 zija, zidzayamba kuukira kwambiri anthu a Yehova. Mdyerekezi, amene ndi wokwiya kwambiri ndi gulu la Mulungu lokhala ngati mkazi, adzagwiritsa ntchito anthu amene wakhala akuwapusitsa, kuti amenye nkhondo. Iye adzachita zimenezi n’cholinga choti awononge anthu amene ndi mbali ya mbewu ya mkazi amene adzakhale adakali padziko lapansi. (Chivumbulutso 12:17) Imeneyi idzakhala nthawi yomaliza yoti Satana aukire atumiki a Mulungu.
2. Kodi Gogi wa ku Magogi ndani, ndipo Yehova adzamuchititsa bwanji kuukira anthu ake?
2 Chaputala 38 cha buku la Ezekieli chimafotokoza momveka bwino mmene Mdyerekezi adzaukirire mwankhanza anthu a Mulungu. M’chaputalachi, Satana amene anaponyedwa kudziko lapansi, akutchedwa “Gogi wa kudziko la Magogi.” Pogwiritsa ntchito ngowe zophiphiritsa, Yehova adzakola chibwano cha Gogi ndipo adzamukoka pamodzi ndi asilikali ake ambirimbiri kuti aukire atumiki a Mulungu. Kodi Yehova adzachita bwanji zimenezi? Iye adzachititsa Gogi kuti aziona Mboni za Yehova ngati anthu osatetezeka amene “anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera ku mitundu ina, amene akusonkhanitsa chuma ndi katundu, komanso amene akukhala pakatikati pa dziko lapansi.” Anthu amenewa adzaonekera poyera kuti ndi anthu okhawo padziko lapansi amene anakana kulambira chilombo ndi chifaniziro chake. Ndipo Gogi adzakwiya kwambiri poona kuti anthu amenewa ndi olimba mwauzimu ndiponso zinthu zikuwayendera bwino. Choncho Gogi ndi asilikali ake ambirimbiri, pamodzi ndi chilombo chotuluka m’nyanja komanso nyanga zake 10, adzaukira atumiki a Mulungu n’cholinga choti awaphe. Koma mosiyana ndi Babulo Wamkulu, Mulungu adzateteza anthu ake oyera.—Ezekieli 38:1, 4, 11, 12, 15; Chivumbulutso 13:1.
3. Kodi Yehova adzawononga bwanji magulu ankhondo a Gogi?
3 Kodi Yehova adzawononga bwanji Gogi ndi gulu lake lonse? Baibulo limafotokoza kuti: “‘Ndidzamubweretsera lupanga m’madera anga onse a m’mapiri kuti limuwononge,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.’” Zida za nyukiliya kapena za mtundu wina uliwonse sizidzathandiza pa nkhondo imeneyi chifukwa Yehova ananena kuti: “Ine ndidzamuweruza ndi mliri ndiponso magazi. Ndidzamugwetsera mvula yamphamvu, matalala, moto ndi sulufule. Ndidzagwetsa zimenezi pa iyeyo, pagulu lake la asilikali ndi pa mitundu yambiri ya anthu amene adzakhale kumbali yake. Ndidzadzilemekeza, kudziyeretsa ndi kuchititsa kuti mitundu yambiri ya anthu indidziwe, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”—Ezekieli 38:21-23; 39:11; yerekezerani ndi Yoswa 10:8-14; Oweruza 7:19-22; 2 Mbiri 20:15, 22-24; Yobu 38:22, 23.
Iye Wotchedwa “Wokhulupirika ndi Woona”
4. Kodi Yohane ananena chiyani za Yesu Khristu amene ankaoneka kuti wakonzekera kumenya nkhondo?
4 Yehova adzabweretsa lupanga. Koma kodi ndani amene adzagwiritse ntchito lupanga limeneli? Tikabwerera m’buku la Chivumbulutso, tikupeza yankho la funso limeneli m’masomphenya ena ochititsa chidwi. Yohane anaona kumwamba kutatseguka ndipo anaona zinthu zina zochititsa mantha kwambiri. Iye anaona Yesu Khristu akuoneka kuti wakonzekera kumenya nkhondo. Yohane akutiuza kuti: “Ndipo nditayang’ana ndinaona kumwamba kutatseguka, kenako ndinaona hatchi yoyera. Wokwerapo wake dzina lake linali Wokhulupirika ndi Woona. Iyeyo anali kuweruza ndi kumenya nkhondo mwachilungamo. Maso ake anali ngati lawi la moto ndipo pamutu pake panali zisoti zachifumu zambiri.”—Chivumbulutso 19:11, 12a.
5, 6. Kodi zinthu zotsatirazi zikutanthauza chiyani? (a) “hatchi yoyera,” (b) dzina lakuti “Wokhulupirika ndi Woona,” (c) maso ooneka ngati “lawi la moto,” (d) “zisoti zachifumu zambiri.”
5 Mofanana ndi masomphenya a m’mbuyomu a okwera pamahatchi anayi aja, “hatchi yoyera” imeneyi ndi chizindikiro choyenerera cha nkhondo yolungama. (Chivumbulutso 6:2) Ndipo mwa ana onse a Mulungu, kodi palinso wina amene angakhale wolungama kwambiri kuposa Wankhondo wamphamvuyu? Popeza kuti dzina lake ndi “Wokhulupirika ndi Woona,” iye ayenera kuti ndi Yesu Khristu, yemwe ndi “mboni yokhulupirika ndi yoona.” (Chivumbulutso 3:14) Iye adzamenya nkhondoyi popereka chiweruzo cholungama cha Yehova. Choncho Yesu adzakwaniritsa udindo wake monga Woweruza woikidwa ndi Yehova, komanso monga “Mulungu Wamphamvu.” (Yesaya 9:6) Maso ake ooneka ngati “lawi la moto” ndi ochititsa mantha, ndipo akuyang’ana chiwonongeko cha adani ake choopsa ngati moto chimene chikubweracho.
6 Mfumu Yankhondoyi yavala zisoti zachifumu kumutu kwake. Chilombo chimene Yohane anaona chikutuluka m’nyanja chinalinso ndi zisoti 10 zachifumu. Zisoti zimenezi zinaimira mfundo yakuti chilombochi chili ndi ulamuliro padziko lapansi, womwe ndi wosakhalitsa. (Chivumbulutso 13:1) Koma Yesu ali ndi “zisoti zachifumu zambiri.” Palibe ulamuliro wina wofanana ndi ulamuliro wake waulemerero, chifukwa iye ndi “Mfumu ya olamulira monga mafumu ndi Mbuye wa olamulira monga ambuye.”—1 Timoteyo 6:15.
7. Kodi Yesu ali ndi dzina liti lolembedwa?
7 Yohane akupitiriza kufotokoza kuti: “Anali ndi dzina lolembedwa limene wina aliyense sanali kulidziwa, koma iye yekha.” (Chivumbulutso 19:12b) Baibulo limatchula Mwana wa Mulungu ndi mayina ena monga Yesu, Emanueli komanso Mikayeli. Koma zikuoneka kuti “dzina” losadziwikali likuimira udindo komanso utumiki umene Yesu ali nawo m’tsiku la Ambuye. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 2:17.) Pofotokoza udindo wa Yesu kuyambira mu 1914, Yesaya anati: “Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga Wamtendere.” (Yesaya 9:6) Mtumwi Paulo anagwirizanitsa dzina la Yesu ndi utumiki wake wapadera kwambiri pamene analemba kuti: “Mulungu anamukweza [Yesu] n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomera mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse. Anachita zimenezi kuti m’dzina la Yesu, onse . . . apinde mawondo awo.”—Afilipi 2:9, 10.
8. N’chifukwa chiyani ndi Yesu yekha amene angadziwe dzina lolembedwalo, ndipo wagawirako ndani ena mwa maudindo ake apadera?
8 Yesu ali ndi maudindo apadera kwambiri. Kupatulapo Yehova, ndi Yesu yekha amene amamvetsa tanthauzo la mwayi wapadera kwambiri umene ali nawo wokhala ndi maudindo amenewo. (Yerekezerani ndi Mateyu 11:27.) Choncho pa zinthu zonse zimene Mulungu analenga, ndi Yesu yekha amene angamvetse bwino tanthauzo la dzina limeneli. Komabe, Yesu wagawirako mkwatibwi wake ena mwa maudindo amenewo. Choncho iye analonjeza kuti: “Wopambana pa nkhondo . . . ndidzamulemba . . . dzina langa latsopano.”—Chivumbulutso 3:12.
9. (a) Kodi mfundo yakuti Yesu “anavala malaya akunja owazidwa magazi,” ikusonyeza chiyani? (b) Nanga n’chifukwa chiyani Yesu akutchedwa “Mawu a Mulungu”?
9 Yohane anapitiriza kuti: “Iye anavala malaya akunja owazidwa magazi, ndipo dzina limene anali kutchedwa nalo linali lakuti Mawu a Mulungu.” (Chivumbulutso 19:13) Kodi “magazi” amenewa ndi a ndani? Akhoza kukhala magazi opatsa moyo amene Yesu anakhetsa chifukwa cha anthu. (Chivumbulutso 1:5) Koma m’nkhaniyi zikuoneka kuti akunena za magazi a adani ake amene adzakhetsedwe ziweruzo za Yehova zikamadzaperekedwa. Zimenezi zatikumbutsa masomphenya ena amene taona m’mbuyomu onena za mpesa wa padziko lapansi. Mpesawu anaumweta ndi kuupondaponda m’choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu mpaka magazi anafika “m’zibwano za mahatchi,” kusonyeza kuti Mulungu adzagonjetseratu adani ake onse. (Chivumbulutso 14:18-20) Mofanana ndi zimenezi, magazi amene anawazidwa pazovala za Yesu akutsimikizira kuti iye adzapambana pa nkhondo n’kugonjetseratu adani ake onse. (Yerekezerani ndi Yesaya 63:1-6.) Tsopano palembali Yohane akunena kuti Yesu akutchulidwa dzina lina. Dzina limeneli ndi lodziwika bwino kwambiri lakuti “Mawu a Mulungu,” ndipo likusonyeza kuti Mfumu Yankhondoyi ndiye Womulankhulira Wamkulu wa Yehova komanso Wolimbikitsa choonadi.—Yohane 1:1; Chivumbulutso 1:1.
Ankhondo Anzake a Yesu
10, 11. (a) Kodi Yohane anasonyeza bwanji kuti Yesu sadzakhala yekha pomenya nkhondo? (b) Kodi mfundo yakuti pali mahatchi oyera, komanso kuti okwera pamahatchiwo anavala “zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee!” ikusonyeza chiyani? (c) Kodi ndani amene ali ‘m’magulu ankhondo’ akumwamba?
10 Yesu sakumenya yekha nkhondo imeneyi. Yohane akutiuza kuti: “Komanso magulu ankhondo amene anali kumwamba, anali kumutsatira pamahatchi oyera, atavala zovala zapamwamba, zoyera bwino, za mbee!” (Chivumbulutso 19:14) Mfundo yakuti mahatchiwo ndi “oyera” ikusonyeza kuti nkhondoyo ndi yolungama. M’pake kuti magulu ankhondo a Mfumu amene anakwera pamahatchiwo avale “zovala zapamwamba.” Ndipo zovalazo n’zonyezimira komanso zoyera, kusonyeza kuti Yehova amaona kuti okwera pamahatchiwo ndi oyera ndiponso olungama. Koma kodi ndani amene ali ‘m’magulu ankhondo’ amenewa? Mosakayikira, ena mwa amene ali m’maguluwa ndi angelo oyera. Kumayambiriro kwa tsiku la Ambuye, Mikayeli ndi angelo ake anachotsa Satana pamodzi ndi angelo ake kumwamba n’kuwaponya kudziko lapansi. (Chivumbulutso 12:7-9) Kenako Yesu amene wakhala pampando wachifumu waulemerero, akadzayamba kuweruza mitundu yonse ya anthu padziko lapansi, “angelo” onse adzayamba kumutumikira. (Mateyu 25:31, 32) N’zodziwikiratu kuti pa nkhondo yomaliza, Yesu adzakhala limodzi ndi angelo ake popereka chiweruzo cha Mulungu ndi kuwonongeratu adani ake.
11 Koma pali enanso amene adzamenye nawo nkhondoyi. Mu uthenga umene anatumiza kumpingo wa ku Tiyatira, Yesu analonjeza kuti: “Amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatira zochita zanga kufikira mapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu. Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo, ngati imenenso ine ndailandira kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi.” (Chivumbulutso 2:26, 27) Mosakayikira, nthawi ikadzafika, abale ake a Khristu amene apita kale kumwamba adzagwira nawo ntchito yokusa mitundu yonse ya anthu ndi ndodo yachitsulo imeneyo.
12. (a) Kodi atumiki a Mulungu padziko lapansi adzamenya nawo nkhondo ya Aramagedo? (b) Kodi anthu a Yehova padziko lapansi adzakhudzidwa bwanji ndi nkhondo ya Aramagedo?
12 Bwanji za atumiki a Mulungu amene ali padziko lapansi? Akhristu odzozedwa sadzamenya nawo nkhondo ya Aramagedo. Chimodzimodzinso a nkhosa zina amene akutumikira Mulungu mokhulupirika limodzi ndi odzozedwawo. A nkhosa zina ndiwo anthu amene akuchokera mwa anthu a mitundu yonse ndipo akhamukira m’nyumba yauzimu yolambiriramo Yehova. Anthu okonda mtenderewa anasula kale malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo. (Yesaya 2:2-4) Komabe, Akhristu odzozedwa pamodzi ndi a nkhosa zina adzakhudzidwa kwambiri ndi nkhondoyo. Monga mmene taonera kale, anthu a Yehova omwe amaoneka ngati osatetezeka, adzaukiridwa mwankhanza kwambiri ndi Gogi pamodzi ndi gulu lake lonse. Zimenezi zikadzachitika, Mfumu Yankhondo yoikidwa ndi Yehova pamodzi ndi magulu ankhondo akumwamba adzayamba kumenya nkhondo imene idzawonongeretu mitundu ya anthu imeneyi. (Ezekieli 39:6, 7, 11; yerekezerani ndi Danieli 11:44–12:1.) Anthu a Mulungu padziko lapansi, amene azidzangoonerera nkhondo ya Aramagedo, adzasangalala kwambiri chifukwa chakuti nkhondoyi idzawabweretsera chipulumutso. Iwo adzakhala ndi moyo kwamuyaya ndipo adzakhala mboni zimene zaona ndi maso nkhondo yaikulu ya Yehova yotsimikizira kuti iye ndiye woyenera kulamulira chilengedwe chonse.
13. Kodi tikudziwa bwanji kuti a Mboni za Yehova satsutsana ndi ulamuliro wonse wa maboma?
13 Kodi zimenezi zikusonyeza kuti anthu a Mboni za Yehova amatsutsana ndi ulamuliro wonse wa maboma? Ayi si choncho. Iwo amamvera malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu.” Iwo amadziwa kuti pa nthawi yonse imene dziko la Satanali likhalepo, Mulungu walola kuti “olamulira akuluakulu” amenewo akhalepo kuti azithandiza anthu kukhala mwabata. Choncho a Mboni za Yehova amakhoma misonkho, amamvera malamulo osiyanasiyana kuphatikizapo malamulo apamsewu, amakalembetsa kuboma zinthu zonse zofunikira, ndi zina zotero. (Aroma 13:1, 6, 7) Komanso potsatira mfundo za m’Baibulo, iwo amanena zoona, amachita zachilungamo, amakonda anthu ena, amakhala ndi mabanja olimba komanso amakhalidwe abwino, ndiponso amaphunzitsa ana awo kuti akhale nzika zabwino. Pochita zimenezi, sikuti iwo ‘amangopereka zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma amaperekanso za Mulungu kwa Mulungu.’ (Luka 20:25; 1 Petulo 2:13-17) Popeza Mawu a Mulungu amasonyeza kuti maboma a m’dzikoli ndi osakhalitsa, panopa anthu a Mboni za Yehova akukonzekera moyo weniweni, womwe ndi wosatha, umene adzasangalale nawo posachedwapa mu Ufumu wa Khristu. (1 Timoteyo 6:17-19) Ngakhale kuti a Mboni sadzamenya nawo nkhondo yowononga maulamuliro a m’dzikoli, iwo amakhudzidwa mtima kwambiri ndi zimene Baibulo Lopatulika, lomwe ndi Mawu a Mulungu ouziridwa, limanena za chiweruzo chimene Yehova watsala pang’ono kupereka pa nkhondo ya Aramagedo.—Yesaya 26:20, 21; Aheberi 12:28, 29.
Nkhondo Yomaliza
14. Kodi “lupanga lalitali lakuthwa” lotuluka m’kamwa mwa Yesu likuimira chiyani?
14 Kodi Yesu adzatenga kuti ulamuliro woti akagonjetse adani ake? Yohane akutiuza kuti: “M’kamwa mwake munali kutuluka lupanga lalitali lakuthwa, loti aphere mitundu ya anthu, ndipo adzawakusa ndi ndodo yachitsulo.” (Chivumbulutso 19:15a) “Lupanga lalitali lakuthwa” limeneli likuimira ulamuliro wa Yesu umene Mulungu anam’patsa kuti adzalamule kuti anthu onse okana kukhala kumbali ya Ufumu wa Mulungu aphedwe. (Chivumbulutso 1:16; 2:16) Mawu ophiphiritsawa akufanana ndi zimene Yesaya ananena kuti: “[Yehova] anachititsa m’kamwa mwanga kukhala ngati lupanga lakuthwa. Anandibisa mumthunzi wa dzanja lake. Anandisandutsa muvi wonola bwino.” (Yesaya 49:2) Palembali Yesaya ankaimira Yesu, amene adzalengeze ziweruzo za Mulungu ndipo adzapha anthu oipa ngati kuti wawapha ndi muvi wakuthwa kwambiri.
15. Pa nthawiyi, kodi ndani amene adzakhale ataululidwa ndi kuweruzidwa, ndipo zimenezi zidzakhala chiyambi cha chiyani?
15 Pa nthawiyi, Yesu adzakhala atakwaniritsa kale mawu a Paulo akuti: “Pamenepo, wosamvera malamuloyo adzaonekera ndithu, amene Ambuye Yesu adzamuthetsa ndi mzimu wa m’kamwa mwake, pomuwonongeratu pa nthawi imene kukhalapo kwa Yesuyo kudzaonekere.” Zoonadi, kukhalapo kwa Yesu (Chigiriki, pa·rou·siʹa) kwaonekera bwino kuyambira mu 1914 chifukwa cha kuululidwa ndiponso kuweruzidwa kwa munthu wosamvera malamulo, yemwe akuimira atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu. Kukhalapo kumeneku kudzaonekeranso mochititsa chidwi kwambiri, nyanga 10 za chilombo chofiira kwambiri zikadzawononga Matchalitchi Achikhristu, pamodzi ndi Babulo Wamkulu yense, mogwirizana ndi chiweruzo chimene anapatsidwa. (2 Atesalonika 2:1-3, 8) Chimenechi chidzakhala chiyambi cha chisautso chachikulu. Kenako Yesu adzathana ndi mbali yotsalira ya gulu la Satana, mogwirizana ndi ulosi wakuti: “Adzakwapula dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake, ndipo adzagwiritsa ntchito mzimu wa pakamwa pake kupha munthu woipa.”—Yesaya 11:4.
16. Kodi mabuku a Masalimo ndi Yeremiya anafotokoza bwanji zimene Mfumu Yankhondo yoikidwa ndi Yehova idzachite?
16 Mfumu Yankhondoyi, yomwe inaikidwa ndi Yehova, idzasiyanitsa anthu amene akuyenera kupulumuka ndi amene akuyenera kuphedwa. Yehova, polankhula mwaulosi kwa Mwana wa Mulungu ameneyu, anati: “Mitunduyo [kutanthauza olamulira a dzikoli] udzaiswa ndi ndodo yachifumu yachitsulo, udzaiphwanya ngati mbiya yadothi, n’kukhala zidutswazidutswa.” Ndipo Yeremiya analemba uthenga wopita kwa atsogoleri a boma achinyengo amenewa, pamodzi ndi anthu onse amene amangowamvera pa chilichonse, kuti: “Fuulani, ndipo lirani abusa inu! Gubuduzikani pafumbi inu anthu otchuka pakati pa gulu la nkhosa, chifukwa masiku a kuphedwa ndi kubalalitsidwa kwanu afika ndipo mudzagwa ndi kuphwanyika ngati chiwiya chosiririka!” Kaya dziko loipali linkaona kuti olamulira amenewa ndi osiririka bwanji, Mfumuyo ikadzangowamenya kamodzi kokha ndi ndodo yake yachitsulo, iwo adzaphwanyikiratu ngati mmene chingaphwanyikire chiwiya chosiririka. Zidzachitika monga mmene Davide analoserera ponena za Ambuye Yesu kuti: “Yehova adzatambasula ndodo yako yachifumu yamphamvu kuchokera m’Ziyoni ndi kunena kuti: ‘Pita ukagonjetse anthu pakati pa adani ako.’ Yehova amene ali kudzanja lako lamanja adzaphwanyaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wake. Adzapereka chiweruzo pakati pa anthu a mitundu ina. Adzachititsa mitembo ya anthu kupezeka paliponse.”—Salimo 2:9, 12; 83:17, 18; 110:1, 2, 5, 6; Yeremiya 25:34.
17. (a) Kodi Yohane ananena chiyani pofotokoza mmene Mfumu Yankhondo idzaphere adani ake? (b) Fotokozani maulosi ena amene akusonyeza kuti tsiku la mkwiyo wa Mulungu lidzakhala loopsa kwa mitundu ya anthu.
17 Mfumu Yankhondo yamphamvuyi inaonekeranso m’mbali yotsatira ya masomphenyawa. Yohane anati: “Iye anali kupondapondanso m’chopondera mphesa cha mkwiyo waukulu wa Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 19:15b) M’masomphenya ena amene takambirana kale, Yohane anaona ‘choponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu’ chikupondedwapondedwa. (Chivumbulutso 14:18-20) Yesaya nayenso anafotokoza za choponderamo mphesa chophera anthu, ndipo aneneri enanso anafotokoza kuti tsiku la mkwiyo wa Mulungu lidzakhala loopsa kwa mitundu yonse ya anthu.—Yesaya 24:1-6; 63:1-4; Yeremiya 25:30-33; Danieli 2:44; Zefaniya 3:8; Zekariya 14:3, 12, 13; Chivumbulutso 6:15-17.
18. Kodi mneneri Yoweli anaulula chiyani pofotokoza za chiweruzo cha Yehova pa mitundu yonse ya anthu?
18 Mneneri Yoweli anatchula choponderamo mphesa pofotokoza za kubwera kwa Yehova ‘kudzaweruza mitundu yonse ya anthu yokhala mozungulira.’ Ndipo mosakayikira, Yehova ndi amene analamula Woweruza mnzake, yemwe ndi Yesu, komanso magulu ankhondo akumwamba a Yesuyo, kuti: “Yambani kumweta ndi chikwakwa, pakuti zokolola zacha. Bwerani, tsikirani kuno, pakuti moponderamo mphesa mwadzaza. Malo ogweramo vinyo wake asefukira, pakuti zoipa za anthu a mitundu ina zachuluka kwambiri. Makamu ambirimbiri a anthu ali m’chigwa choweruzira mlandu, pakuti tsiku la Yehova layandikira m’chigwa choweruzira mlandu. Dzuwa ndi mwezi zidzachita mdima, ndipo nyenyezi zidzasiya kuwala. Yehova adzabangula ngati mkango kuchokera m’Ziyoni ndipo adzalankhula ali ku Yerusalemu. Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka koma Yehova adzakhala chitetezo kwa anthu ake, ndipo adzakhala malo a chitetezo champhamvu kwa ana a Isiraeli. Pamenepo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.”—Yoweli 3:12-17.
19. (a) Kodi funso limene lili pa 1 Petulo 4:17 lidzayankhidwa bwanji? (b) Kodi pamalaya akunja a Yesu palembedwa dzina lotani, ndipo n’chiyani chidzasonyeze kuti dzinali ndi loyenerera?
19 Tsiku limeneli lidzakhaladi loopsa kwa anthu ndi mitundu yosamvera, koma kwa anthu amene akuthawira kwa Yehova ndi Mfumu yake yankhondo, lidzakhala tsiku lobweretsa mpumulo. (2 Atesalonika 1:6-9) Chiweruzo chimene chinayambira pa nyumba ya Mulungu mu 1918 chidzakhala chitafika pachimake, ndipo zimenezi zidzayankha funso la pa 1 Petulo 4:17 lakuti: “Ndiye mapeto a anthu osamvera uthenga wabwino wa Mulungu adzakhala otani?” Wopambana pa nkhondo waulemereroyu adzakhala atapondaponda m’choponderamo mphesa mpaka kufika pamapeto. Zimenezi zidzasonyeza kuti iye ndi munthu wokwezeka amene Yohane anamufotokoza kuti: “Pamalaya ake akunja, ngakhale pantchafu yake, anali ndi dzina lolembedwa lakuti, Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.” (Chivumbulutso 19:16) Iye wasonyeza kuti ndi wamphamvu kwambiri kuposa wolamulira aliyense, mfumu iliyonse, kapena ambuye aliyense padziko lapansi. Ulemu ndi ulemerero wake ndi wapamwamba kwambiri. Iye adzakwera pahatchi potsatira “choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,” ndipo adzagonjetseratu adani ake onse mpaka kalekale. (Salimo 45:4) Pa zovala zake zowazidwa magazi panalembedwa dzina limene anapatsidwa ndi Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Ndipo Mfumu Yankhondoyi imachita zinthu zosonyeza kuti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse.
Phwando Lalikulu la Mulungu la Chakudya Chamadzulo
20. Kodi Yohane anafotokoza bwanji “phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo,” ndipo zimenezi zikutikumbutsa ulosi wina uti wofanana ndi umenewu?
20 M’masomphenya a Ezekieli, khamu la anthu amene anali kumbali ya Gogi atawonongedwa, mbalame ndi nyama zakutchire zinaitanidwa ku phwando. Mbalame ndi nyama zimenezi zinadya n’kumaliza mitembo yonse ya adani a Yehova ndipo sinapezekenso panthaka. (Ezekieli 39:11, 17-20) Mawu otsatira a Yohane akutikumbutsa ulosi umenewu. Iye anati: “Ndinaonanso mngelo ataimirira padzuwa. Iye anafuula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zouluka chapafupi m’mlengalenga, kuti: ‘Bwerani kuno, dzasonkhaneni ku phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo, kuti mudzadye minofu ya mafumu, ya akuluakulu a asilikali, ya amuna amphamvu, ya mahatchi ndi ya okwerapo ake, ndi minofu ya onse, ya mfulu ndi ya akapolo, ya olemekezeka ndi ya onyozeka.’”—Chivumbulutso 19:17, 18.
21. Kodi mfundo zotsatirazi zikutanthauza chiyani? (a) mngelo amene ‘waimirira padzuwa,’ (b) mfundo yakuti mitembo idzasiyidwa panthaka, (c) anthu osiyanasiyana amene mitembo yawo idzasiyidwe panthaka, (d) mawu akuti “phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo.”
21 Mngelo uja anali “ataimirira padzuwa,” kutanthauza kuti adzaima pamalo abwino pamene mbalame zidzathe kumuona ndi kumva mosavuta pamene akuziitana. Iye adzaitana mbalamezo kuti zikonzekere kudya minofu ya anthu amene adzaphedwe ndi Mfumu Yankhondo ija ndi magulu ake ankhondo akumwamba. Mfundo yakuti mitembo ya anthu ophedwawo idzasiyidwa panthaka ikusonyeza kuti imfa yawo idzakhala yochititsa manyazi. Mofanana ndi zimene zinachitikira Yezebeli m’mbuyomu, iwo sadzaikidwa m’manda mwaulemu. (2 Mafumu 9:36, 37) Baibulo likutiuza kuti mitembo ya anthu osiyanasiyana monga mafumu, akuluakulu a asilikali, amuna amphamvu, mfulu komanso akapolo, idzasiyidwa panthaka. Izi zikusonyeza kuti aliyense adzakhudzidwa. M’dzikoli simudzapezekanso aliyense wotsutsana ndi Yehova chifukwa adzakhala atawonongedwa. Zimenezi zikadzachitika, ndiye kuti sipadzakhalanso nyanja yamafunde ya anthu osokonezedwa maganizo. (Chivumbulutso 21:1) Limeneli lidzakhala “phwando lalikulu la Mulungu la chakudya chamadzulo,” chifukwa Yehova ndi amene adzaitane mbalame kuti zidzadye ku phwandoli.
22. Kodi Yohane anati chiyani pofotokoza mwachidule zimene zidzachitike pa nkhondo yomalizayi?
22 Kenako Yohane akufotokoza mwachidule zimene zidzachitike pa nkhondo yomalizayi. Iye akuti: “Ndipo ndinaona chilombo, mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahatchi uja ndi gulu lake lankhondo. Koma chilombocho chinagwidwa limodzi ndi mneneri wonyenga uja, amene anachita zizindikiro pamaso pa chilombocho. Zizindikiro zimenezi anasocheretsa nazo olandira chizindikiro cha chilombo ndi olambira chifaniziro chake. Adakali amoyo, onse awiri anaponyedwa m’nyanja ya moto yoyaka ndi sulufule. Koma ena onse anaphedwa ndi lupanga lalitali la wokwera pahatchi, limene linatuluka m’kamwa mwake lija. Ndipo mbalame zonse zinakhuta minofu yawo.”—Chivumbulutso 19:19-21.
23. (a) Kodi mfundo yakuti ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ idzachitikira ku “Aramagedo,” ikutanthauza chiyani? (b) Kodi “mafumu a dziko lapansi” alephera kumvera chenjezo liti, ndipo zotsatira zake zidzakhala zotani?
23 Mngelo atakhuthula mbale ya 6 ya mkwiyo wa Yehova, Yohane ananena kuti “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu,” anasonkhanitsidwa ndi mawu okopa a ziwanda “kunkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” Nkhondo imeneyi idzachitikira ku Aramagedo. Mawu akuti Aramagedo sakutanthauza malo enieni, koma ndi zinthu zimene zidzachitike padziko lonse lapansi zimene zidzachititse kuti Yehova apereke chiweruzo chake. (Chivumbulutso 16:12, 14, 16) Tsopano Yohane anaona anthu okonzekera kumenya nkhondo. Iye anaona “mafumu a dziko lapansi, ndi magulu awo ankhondo” atasonkhana pamodzi motsutsana ndi Mulungu. Modzikuza, iwo anakana kumvera Mfumu yoikidwa ndi Yehova. Komabe, Mfumuyi inawachenjeza mokoma mtima mu uthenga wake wouziridwa wakuti: “Psompsonani mwanayo kuopera kuti Mulungu angakwiye, ndipo mungawonongeke ndi kuchotsedwa panjirayo.” Iwo akuyenera kuphedwa chifukwa sanagonjere ulamuliro wa Khristu.—Salimo 2:12.
24. (a) Kodi chilombo ndi mneneri wonyenga adzalandira chiweruzo chotani, ndipo mfundo yakuti iwo adakali “amoyo” ikutanthauza chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti ‘nyanja ya moto’ ndi yophiphiritsa?
24 Chilombo cha mitu 7 ndi nyanga 10 chotuluka m’nyanja, chimene chikuimira maulamuliro andale amene Satana wakhazikitsa, chidzawonongedwa pamodzi ndi mneneri wonyenga, amene akuimira ulamuliro wa 7 wamphamvu kwambiri padziko lonse. (Chivumbulutso 13:1, 11-13; 16:13) Chilombochi komanso mneneri wonyengayu adzaponyedwa “m’nyanja ya moto” adakali “amoyo,” kapena kuti akuchitabe zinthu mogwirizana, potsutsana ndi anthu a Mulungu padziko lapansi. Kodi nyanja ya motoyi ndi nyanja yeniyeni? Ayi ndi yophiphiritsa, chifukwa chilombocho komanso mneneri wonyengayu n’zophiphiritsanso. Choncho nyanja ya moto ikuimira chiwonongeko chotheratu chomwenso ndi chomaliza, kutanthauza kuti owonongedwawo sadzakhalaponso mpaka kalekale. N’chifukwa chake pamapeto pake imfa ndi Manda, komanso Mdyerekezi weniweniyo adzaponyedwe m’nyanja imeneyi. (Chivumbulutso 20:10, 14) Choncho nyanja imeneyi si ng’anjo ya moto, kumene anthu ena amaganiza kuti anthu oipa amakazunzika kwamuyaya. Zili choncho chifukwa Yehova amanyansidwa ndi chiphunzitso chakuti anthu oipa amakazunzika kwamuyaya m’ng’anjo ya moto.—Yeremiya 19:5; 32:35; 1 Yohane 4:8, 16.
25. (a) Kodi ndani amene ‘adzaphedwe ndi lupanga lalitali la wokwera pahatchi’? (b) Kodi tiyembekezere kuti amene ‘adzaphedwewo’ adzaukitsidwa?
25 Ena onse amene sali m’gulu la olamulira andale, koma ali kumbali ya dziko loipa lomwe silingathe kusintha, nawonso ‘adzaphedwa ndi lupanga lalitali la wokwera pahatchi.’ Yesu adzawaweruza kuti ndi oyenera kuphedwa. Popeza kuti Baibulo silikunena kuti anthu amenewa adzaponyedwa m’nyanja ya moto, kodi tiyembekezere kuti adzaukitsidwa? Mawu a Mulungu sanena pena paliponse kuti anthu amene adzaphedwe pa nthawi imeneyo ndi Woweruza woikidwa ndi Yehova, adzaukitsidwa. Monga momwe Yesu ananenera, onse amene si “nkhosa” adzachoka kupita “kumoto wosatha wokolezedwera Mdyerekezi ndi angelo ake,” kutanthauza kuti adzapita ku “chiwonongeko chotheratu.” (Mateyu 25:33, 41, 46) Pa nthawiyi, ‘tsiku lachiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osaopa Mulungu’ lidzakhala litafika pachimake.—2 Petulo 3:7; Nahumu 1:2, 7-9; Malaki 4:1.
26. Fotokozani mwachidule mmene zinthu zidzakhalire pambuyo pa Aramagedo.
26 Umu ndi mmene mbali zonse zimene Satana wakhazikitsa padziko lapansi zidzathere. “Kumwamba kwakale,” kutanthauza olamulira andale, kudzakhala kutachotsedwa. “Dziko lapansi,” lomwe likuimira dongosolo looneka ngati lolimba limene Satana wakhazikitsa kwa zaka zambiri, lidzakhala litawonongedwa kotheratu. Ndiponso “nyanja,” yomwe ikuimira anthu oipa amene akutsutsana ndi Yehova, sidzakhalakonso. (Chivumbulutso 21:1; 2 Petulo 3:10) Koma kodi Yehova adzachita naye chiyani Satana? Yohane akupitiriza kutifotokozera.