2 Mafumu
9 Mneneri Elisa anaitana mmodzi wa ana a aneneri nʼkumuuza kuti: “Manga zovala zako mʼchiuno, nyamula botolo ladothi la mafutali ndipo upite mwamsanga ku Ramoti-giliyadi.+ 2 Ukakafika mumzindawo, ukafufuze Yehu+ mwana wa Yehosafati mwana wa Nimusi. Ukamupeza ali ndi abale ake ndipo ukamutenge nʼkulowa naye mʼchipinda chamkati. 3 Ndiyeno ukatenge botolo ladothi la mafutali nʼkumuthira pamutu ndipo ukanene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndikukudzoza kuti ukhale mfumu ya Isiraeli.”’+ Ukakatero, ukatsegule chitseko nʼkuthawa, usakachedwe.”
4 Choncho mtumiki wa mneneriyo ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi. 5 Atafika mumzindawo, anapeza akuluakulu a asilikali atakhalakhala. Kenako iye anati: “Ndabwera ndi uthenga wanu inu mkulu wa asilikali.” Ndiyeno Yehu anati: “Ndani kwenikweni pakati pathupa?” Iye anayankha kuti: “Inuyo mkulu wa asilikali.” 6 Choncho Yehu ananyamuka nʼkulowa mʼnyumba. Ndiyeno mtumiki wa mneneri uja anatenga mafuta aja nʼkumuthira pamutu. Kenako anamuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ndikukudzoza kuti ukhale mfumu ya anthu a Yehova, Aisiraeli.+ 7 Ukaphe anthu a mʼbanja la mbuye wako Ahabu ndipo ine ndidzabwezera magazi a atumiki anga aneneri ndiponso magazi a atumiki onse a Yehova amene Yezebeli anawapha.+ 8 Anthu onse a mʼnyumba ya Ahabu adzaphedwa ndipo ndidzapha mwamuna aliyense* wa mʼbanja la Ahabu, ngakhale anthu ooneka onyozeka ndi ofooka mu Isiraeli.+ 9 Ndidzachititsa nyumba ya Ahabu kukhala ngati nyumba ya Yerobowamu+ mwana wa Nebati ndiponso ngati nyumba ya Basa+ mwana wa Ahiya. 10 Yezebeli adzadyedwa ndi agalu mʼmunda wa ku Yezereeli+ ndipo palibe amene adzamuike mʼmanda.’” Mtumikiyo atamaliza kunena zimenezi, anatsegula chitseko nʼkuthawa.+
11 Yehu atabwerera kwa atumiki a mbuye wake, atumikiwo anamufunsa kuti: “Zili bwino kodi? Nanga munthu wamisalayu amadzatani?” Iye anawayankha kuti: “Inu mukumudziwa munthuyu ndiponso zonena zake.” 12 Koma iwo anati: “Ayi ukunama! Tiuze zoona.” Ndiyeno Yehu anati: “Wandiuza zakutizakuti kenako ananena kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ndikukudzoza kuti ukhale mfumu ya Isiraeli.”’”+ 13 Anthuwo atamva zimenezi, nthawi yomweyo aliyense anavula malaya ake nʼkumuyalira pamasitepe popanda kanthu.+ Kenako analiza malipenga nʼkunena kuti: “Tsopano Yehu ndi mfumu!”+ 14 Ndiyeno Yehu+ mwana wa Yehosafati mwana wa Nimusi, anakonzera Yehoramu chiwembu.
Yehoramu ankalondera Ramoti-giliyadi+ pamodzi ndi Aisiraeli onse, chifukwa cha Hazaeli+ mfumu ya Siriya. 15 Kenako Mfumu Yehoramu anabwerera ku Yezereeli+ kuti akachire mabala amene Asiriya anamuvulaza pamene ankamenyana ndi Hazaeli mfumu ya Siriya.+
Ndiyeno Yehu anati: “Ngati mukugwirizana nazo, musalole aliyense kutuluka mumzinda uno nʼkukanena zimenezi ku Yezereeli.” 16 Kenako Yehu anakwera galeta lake nʼkunyamuka ulendo wa ku Yezereeli popeza Yehoramu anali chigonere kumeneko chifukwa chovulala. Ahaziya mfumu ya Yuda anali atapita ku Yezereeli komweko kukaona Yehoramu. 17 Ku Yezereeliko, mlonda amene anaima pansanja anaona gulu lankhondo la Yehu likubwera. Nthawi yomweyo mlondayo anati: “Ndikuona gulu la anthu likubwera.” Yehoramu anati: “Uza munthu wokwera hatchi kuti apite kukakumana nawo. Akawafunse kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’” 18 Munthu wokwera pahatchiyo anapitadi kukakumana ndi Yehu, nʼkunena kuti, “Mfumu yanena kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’” Koma Yehu anati: “Ukudziwa chiyani zokhudza ‘mtendereʼ iweyo? Tiye zinditsatira!”
Ndiyeno mlonda wa pansanja uja anati: “Munthu tinamutuma uja wakumana nawo koma sakubwerera.” 19 Choncho anatumizanso munthu wina wokwera pahatchi. Nayenso atafika anati: “Mfumu yanena kuti, ‘Kodi mukubwerera zamtendere?’” Koma Yehu anati: “Ukudziwa chiyani zokhudza ‘mtendereʼ iweyo? Tiye zinditsatira!”
20 Ndiyeno mlonda uja ananena kuti: “Munthu tamutuma uja wakumana nawo, koma nayenso sakubwerera. Ndipo mmene anthuwo akuthamangira, akuthamanga ngati Yehu mdzukulu wa Nimusi, chifukwa iye amathamangitsa galeta ngati wamisala.” 21 Yehoramu atamva zimenezi, anati: “Mangirirani mahatchi kugaleta!” Choncho anamangiriradi mahatchi kugaleta lake lankhondo. Ndiyeno Yehoramu mfumu ya Isiraeli ndi Ahaziya+ mfumu ya Yuda, ananyamuka aliyense pagaleta lake lankhondo, kupita kukakumana ndi Yehu ndipo anakumana naye pamunda wa Naboti+ wa ku Yezereeli.
22 Yehoramu atangoona Yehu, anamʼfunsa kuti: “Kodi ukubwerera zamtendere Yehu?” Koma Yehu anayankha kuti: “Mtendere ungakhalepo bwanji pali uhule wa Yezebeli+ mayi ako ndi zamatsenga zake zambirimbiri?”+ 23 Ndiyeno Yehoramu anatembenuza galeta lake kuti azithawa ndipo anauza Ahaziya kuti: “Ahaziya, anthuwa atikonzera chiwembu!” 24 Zitatero Yehu anakoka uta wake nʼkubaya Yehoramu kumsana pakati pamapewa mpaka muviwo unatulukira pamtima pake ndipo Yehoramu anagwa mʼgaleta lake lankhondo. 25 Kenako Yehu anauza Bidikara msilikali wake womuthandiza, kuti: “Munyamule umuponye mʼmunda wa Naboti wa ku Yezereeli.+ Kumbukira kuti iwe ndi ine tinkabwera pambuyo pa Ahabu bambo ake, aliyense atakwera pagaleta lake la mahatchi awiri, pa nthawi imene Yehova anamutemberera kuti:+ 26 ‘Yehova wanena kuti: “Ndithu magazi a Naboti+ ndi magazi a ana ake amene ndawaona dzulo, ndidzawabwezera+ pa iwe mʼmunda uwu,” watero Yehova.’ Choncho munyamule umuponye mʼmundamo mogwirizana ndi mawu a Yehova.”+
27 Ahaziya+ mfumu ya Yuda ataona zimenezi, anayamba kuthawa kudzera njira yakumunda.* (Kenako Yehu anayamba kumʼtsatira ndipo anati: “Ameneyonso mʼbayeni!” Choncho anamʼbayadi ali mʼgaleta lake pamene ankathawira ku Guru kufupi ndi ku Ibuleamu.+ Koma anapitirizabe kuthawa mpaka ku Megido kumene anakafera. 28 Kenako atumiki ake anamunyamula mʼgaleta nʼkupita naye ku Yerusalemu ndipo anakamuika mʼmanda ake mu Mzinda wa Davide+ pamalo amene panagona makolo ake. 29 Ahaziya+ anakhala mfumu ya Yuda mʼchaka cha 11 cha Yehoramu mwana wa Ahabu.)
30 Yehu atafika ku Yezereeli,+ Yezebeli+ anamva zimenezo. Choncho Yezebeliyo anapaka zodzikongoletsera zakuda mʼzikope zake komanso anakonza tsitsi lake. Atatero anakaima pawindo nʼkumayangʼana kunja. 31 Ndiyeno Yehu atalowa pageti, Yezebeli anati: “Kodi Zimiri amene anapha mbuye wake, zinthu zinamuyendera bwino?”+ 32 Yehu anakweza maso kuyangʼana pawindopo nʼkufunsa kuti: “Ndani ali kumbali yanga? Ndani?”+ Nthawi yomweyo nduna ziwiri kapena zitatu za panyumba ya mfumu zinasuzumira pawindo kuyangʼana Yehu. 33 Ndiyeno Yehu anati: “Mʼponyeni pansi Yezebeliyo!” Iwo anamʼponyadi pansi ndipo magazi ake ena anagwera pakhoma ndi pamahatchi. Kenako Yehu anamʼpondaponda ndi mahatchi ake. 34 Atatero, analowa mʼnyumba ndipo anayamba kudya ndi kumwa, kenako anati: “Mutengeni mayi wotembereredwayu mukamuike mʼmanda, paja ndi mwana wa mfumu.”+ 35 Koma atapita kuti akamuike mʼmanda, anangopezapo mutu, mapazi ndi manja.+ 36 Anthuwo atabwerera kwa Yehu kukamuuza, iye anati: “Zimenezi zakwaniritsa mawu a Yehova+ amene ananena kudzera mwa mtumiki wake Eliya wa ku Tisibe, akuti: ‘Mʼmunda wa ku Yezereeli, agalu adzadya thupi la Yezebeli.+ 37 Ndipo mtembo wa Yezebeli udzasanduka manyowa mʼmunda wa ku Yezereeli kuti anthu asadzanene kuti: “Uyu ndi Yezebeli.”’”