Yeremiya—Mneneri Wachilendo wa Ziweruzo za Mulungu
Kuŵerenga Baibulo kwa mlungu ndi mlungu kuchokera m’bukhu la Yeremiya kwandandalitsidwa kaamba ka Sukulu ya Utumiki wa Teokratiki kuyambira mu April 17 mpaka August 21. Nkhani Zitatu zophunziridwazi zidzapereka mbiri yakale yabwino kaamba ka kumvetsetsa zolembedwa za mneneriyo
“Ndisanakulenge iwe m’mimba ndinakudziŵa . . . ndinakuika kuti ukhale mneneri wa mitundu ya anthu.”—YEREMIYA 1:5.
1. (a) Kubwerera ku nthaŵi zakale, ndimotani mmene ena anawonera Yeremiya? (b) Ndimotani mmene iye anadziwonera iyemwini?
“NGAKHALE pa gulu la aneneri, Yeremiya amawonekera wamkulu.” Ndemanga imeneyo ya wophunzira Baibulo imawonekera yotsutsana koposa ndi lingaliro la Yeremiya la iyemwini pamene iye choyamba analandira ntchito yake yochokera kwa Yehova kutumikira monga mneneri kwa Yuda ndi kwa amitundu. Yankho lake linali: “Ha, [Mfumu Ambuye Yehova! NW] Tawonani, sindithai kunena pakuti ndiri mwana.” Yeremiya mwachiwonekere anali wozindikira ponena za uchichepere wake, ndipo chitokoso choyang’anizana ndi mitundu yankhalwe chinawoneka chachikulu. Yehova analingalira mosiyanako.—Yeremiya 1:6.
2. Ndimotani mmene Yehova anaperekera chitsimikiziro mwa Yeremiya?
2 Kuchokera ku kukambitsirana kwa Yehova ndi Yeremiya wachichepere, chiri chowonekeratu kuti iye anali mmodzi wa anthu ochepa amene Yehova anali ndi thayo kaamba ka kubadwa kwawo. Ndipo nchifukwa ninji iye anapereka chikondwerero chachindunji mwa Yeremiya kuyambira pa kuwumbidwa kwake kunka mtsogolo? Chifukwa Yehova anali ndi ntchito yapadera m’malingaliro kaamba ka iye. Chotero, iye anakhoza kunena kuti: “Usanabadwe ndinakupatula iwe.” (Yeremiya 1:5) Kenaka iye analamula wachichepereyo: “Usati, ‘ndine mwana.’ Pakuti udzanka kwa yense amene ndidzakutumako iwe, nudzanena chonse chimene ndidzakuuza. Usawope nkhope zawo, chifukwa ‘ine ndiri ndi iwe kuti ndikulanditse iwe,’ ati Yehova.” Panalibe malo pano kaamba ka kufikira kosakhala kwa mtima wonse ku ntchito yake. M’malomwake, iyo inaitanira kaamba ka kulimba mtima ndi kukhulupirira mwa Yehova.—Yeremiya 1:7, 8.
3. Nchifukwa ninji ntchito ya Yeremiya inalidi ya chitokoso?
3 Anali wosangalatsidwa ndipo mwinamwake wochititsidwa mantha chotani nanga mwamuna wachichepere ameneyu pamene analandira ntchito yoteroyo mwachindunji kuchokera kwa Mulungu! Ndipo inali ntchito yovuta chotani nanga! “Penyatu, lero ndakuika ulamulire mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule, upasule, uwononge, ugwetse; umange, ubzyale.” Ndithudi, makhazikitsidwe a ndemanga zoterozo mu Yuda chifupifupi mkati mwa zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E. anapereka thayo lalikulu pa mneneri womakula ameneyu. Iye anayenera kuyang’anizana ndi mtundu wonyada, wodziyeneretsa womwe unadalira mu mzinda wake wopatulika, Yerusalemu, ndi kachisi wake, monga munthu wa matsenga. Pamene iye anatsiriza utumiki wake wa ulosi wa zaka 40 mu Yerusalemu, iye akayenera kupereka uthenga wake mkati mwa maulamuliro a mafumu osiyanasiyana asanu (Yosiya, Yehoahazi, Yehoyakimu, Yoyakini, ndi Zedekiya). Iye akayenera kulengeza ziweruzo zachilendo zotsutsa ku mitundu ya Chiyuda ndi ya Chibabulo.—Yeremiya 1:10; 51:41-64.
Nchifukwa Ninji Yeremiya Ayenera Kutikondweretsa Ife?
4, 5. (a) Nchifukwa ninji zochitika za m’tsiku la Yeremiya ziyenera kutidetsa ife nkhaŵa? (Aroma 15:4) (b) Ndi kugwira ntchito kwapadera kotani kumene kutisangalatsa ife?
4 Koma tingafunse, Nchiyani chimene zochitika zimenezo zakalelo ziyenera kuchita ndi ife, tsopano okhala pafupi ndi mapeto a zana la 20? Mtumwi Paulo akupereka yankho pamene akubwerera mu ina ya mbiri ya Israyeli m’kalata yake ku mpingo wa ku Korinto. Iye analemba: “Koma zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso iwowo analakalaka . . . ndipo zinalembedwa kutichenjeza ife, amene matsirizidwe a nthaŵi ya pansi pano adafika pa ife.”—1 Akorinto 10:6, 11.
5 Zochitika zomwe zinachitika mu Israyeli ndi Yuda zimatumikira monga zitsanzo zochenjeza ku mpingo wa Akristu owona m’nthaŵi ino ya mapeto. Tingawonenso kufanana ndi mitundu imene imapereka chiwunikiro cha pasadakhale ku zochitika zamtsogolo. (Yerekezani Yeremiya 51:6-8 ndi Chivumbulutso 18:2, 4.) Chotero, utumiki wa uneneri wa Yeremiya ndi zochitika zomwe zinagwera Yerusalemu ziri ndi kufunika kozama kaamba ka Mboni za Yehova lerolino, makamaka ponena za ntchito yawo m’mabwalo a Chikristu cha Dziko, monga mmene tidzawonera m’nkhani zotsatira.
Kulengeza Ziweruzo za Mulungu Kopanda Mantha kwa Yeremiya
6. Nchiyani chimene chinapangitsa ntchito ya Yeremiya kukhala yovuta kwambiri, komabe ndi chilimbikitso chotani chimene iye analandira?
6 Kuti alimbikitse Yeremiya kaamba ka thayo lake lowopsya, Yehova mowonjezereka anamutsimikizira iye kuti: “Nuwuke, nunene kwa iwo zonse zimene ndikuuza iwe; usawope nkhope zawo . . . Chifukwa tawona, ndakupanga iwe lero mudzi walinga . . . pa dziko lonse ndi pa mafumu a Yuda, ndi pa akulu ake, ndi pa ansembe ake, ndi pa anthu a m’dziko.” Mosakaikira ponena za icho, Yeremiya anayenera kukhala monga mudzi wa malinga ndi cholinga chofuna kuyang’anizana ndi olamulira ndi ansembe a Yuda. Ndipo kupereka uthenga wachilendo ndi wachitokoso kwa anthuwo sikunayenera kukhala ntchito yopepuka.—Yeremiya 1:17, 18.
7. Nchifukwa ninji atsogoleri a Chiyuda anatsutsa Yeremiya?
7 “Ndipo adzamenyana ndi iwe,” anachenjeza tero Yehova, “koma sadzakuposa.” (Yeremiya 1:19) Tsopano nchifukwa ninji Ayuda ndi olamulira awo anafuna kumenyana ndi mneneri ameneyu? Chifukwa uthenga wake unawukira kukhutiritsidwa kwawo ndi njira yawo ya chizoloŵezi cha kulambira. Yeremiya sanalefuke: “Tawona! mawu a Yehova awatonzetsa iwo, sakondwera nawo. Pakuti kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe [iwo enieniwo omwe anafunikira kukhala osungilira mapindu a makhalidwe abwino ndi auzimu] onse achita monyenga.”—Yeremiya 6:10, 13.
8. Ndimotani mmene ansembe ndi aneneri ankanyengera anthu?
8 Zowona, iwo anali kutsogolera mtunduwo m’kupereka nsembe. Iwo anali kutsatira njira za kulambira kowona, koma mitima yawo sinali pa izo. Mwambo unatanthauza zambiri kwa iwo kuposa mkhalidwe wabwino. Pa nthaŵi imodzimodziyo, atsogoleri a chipembedzo a Chiyuda anali kunamiza mtundu m’lingaliro lonyenga la chisungiko, akumanena kuti, “Mtendere! Mtendere!” pamene panalibe mtendere. (Yeremiya 6:14; 8:11) Inde, iwo anali kunamiza anthu m’kukhulupirira kuti iwo anali pa mtendere ndi Mulungu. Iwo anadzimva kuti panalibe chirichonse chodandaulitsa, popeza iwo anali anthu opulumutsidwa a Yehova, okhala ndi mzinda woyera ndi kachisi wake. Koma kodi mmenemo ndi mmene Yehova anawonera mkhalidwewo?
9. Ndi chenjezo lotani limene Yeremiya anapereka kwa alambiri ponena za kachisi wawo?
9 Yehova analamulira Yeremiya kutenga malo m’kawonedwe kapoyera kotheratu pa chipata cha kachisi ndi kupereka uthenga Wake kwa alambiri omwe analowa mmenemo. Iye anayenera kuwauza iwo kuti: “Musakhulupirire mawu onama, kuti ‘Kachisi wa Yehova, kachisi wa Yehova, kachisi wa Yehova ndi awa!’ . . . Sichidzapindulitsa.” Ayuda anali kuyenda ndi kuwona, osati ndi chikhulupiriro, pamene iwo anali kudzitukumula m’kachisi wawo. Iwo anali ataiwala kale mawu achenjezo a Yehova: “Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu, ndi dziko lapansi ndi choikapo mapazi anga. Mudzandimangira ine nyumba yotani?” Yehova, Mbuye Wolamulira wa chilengedwe chonse chachikulu ichi, ndithudi sanali woletsedwa ku zotsekeredwa za kachisi wawo, mosasamala kanthu kuti anali waulemerero chotani!—Yeremiya 7:1-8; Yesaya 66:1.
10, 11. Kodi ndi uti umene unali mkhalidwe wauzimu wa mtundu umene Yeremiya anaperekako uthenga wa chiweruzo ndipo kodi mkhalidwe m’Chikristu cha Dziko uli wabwinopo? (2 Timoteo 3:5)
10 Yeremiya anapitiriza ndi chidzudzulo chake choŵaŵa chapoyera: “Kodi mudzapha ndi kuba, ndi kuchita chigololo, ndi kulumbira zonama, ndi kupereka nsembe kwa Baala, ndi kutsata milungu yina imene simuidziŵa, . . . ndi kuti, ‘Talanditsidwa,’ kuti muchite zonyansa izi?” Ayuda, monga ‘anthu osankhidwa a Mulungu, anaganiza kuti iye akalekerera mtundu uliwonse wa mkhalidwe, malinga ngati iwo anali kubweretsa nsembe zawo ku kachisi. Ngakhale kuli tero, ngati iwo anamlingalira kukhala atate wa malingaliro womalekerera mwana yekha woipitsidwa, iwo anayenera kukumana ndi kugalamutsidwa koipa.—Yeremiya 7:9, 10; Eksodo 19:5, 6.
11 Kulambira kwa Yuda kunali kutatsika m’maso mwa Yehova chakuti funso lochititsa mantha linayenera kudzutsidwa: “Kodi nyumba ino, imene itchedwa dzina langa, ikhala phanga la okwatula pamaso panu?” Chifupifupi zaka 700 pambuyo pake mkhalidwewo sunali wabwino, pamene Yesu, mneneri wamkulu, kuposa Yeremiya, anagwiritsira ntchito mawu amodzimodziwo kutsutsa kudyerana masuku pamutu ndi kuchita malonda komwe kunali kuchitidwa pa kachisi womangidwanso m’nthaŵi yake. Ndipo mkhalidwe lerolino m’Chikristu cha Dziko suli wabwinopo.—Yeremiya 7:11; Mateyu 16:14; Marko 11:15-17.
Alonda Anyalanyazidwa, Tsoka Linenedweratu
12. Ndimotani mmene Ayuda anavomerezera kwa aneneri amene Yehova anatumiza kwa iwo?
12 Yeremiya sanali mneneri woyamba kugwiritsiridwa ntchito ndi Mulungu kuchenjeza Israyeli ndi Yuda za njira yawo yonyenga. Mkati mwa zaka zana kapena zochulukirapo zapita, aneneri Yesaya, Mika, Hoseya, ndi Obedi anali atatumizidwa monga alonda kukachenjeza mtunduwo. (Yesaya 1:1; Mika 1:1; Hoseya 1:1; 2 Mbiri 28:6-9) Ndimotani mmene ambiri anavomerezera? “Ndipo ndinaika alonda oyang’anira inu, ndi kuti, ‘Mverani mawu a lipenga!’ Koma anati, ‘Sitidzamvera.’” (Yeremiya 6:17; 7:13, 25, 26) Iwo anakana kupereka chisamaliro kwa Yeremiya. M’malomwake, iwo anamuzunza iye ndikuyesa kumletsa iye. Chotero Yehova anagamulapo kuti iwo anayenera kulipira kaamba ka kudzitukumula kwawo ndi kusakhulupirira.—Yeremiya 20:1, 2; 26:8, 11; 37:15; 38:6.
13. Nchiyani chimene chinali maziko kaamba ka chiweruzo cha Mulungu pa mtunduwo?
13 Monga chotulukapo ku kukana kwa mtunduwo kwa athenga ake, Yehova anapereka mawu, monga mmene kunaliri, ku mitundu ya padziko lapansi, akumanena kuti: “Tamva, dziko lapansi iwe; tawona, ine ndidzatengera choipa pa anthu awa, chipatso cha maganizo awo, pakuti sanamvera mawu anga, kapena chilamulo changa, koma achikana.” Nchifukwa ninji mtunduwo ukavutika ndi tsoka? Chifukwa cha kachitidwe kawo koipa kozikidwa pa malingaliro awo oipa. Iwo anakana mawu a Yehova ndi Lamulo ndi kutsatira zikhoterero zawo zadyera, za kuthupi.—Yeremiya 6:18, 19; Yesaya 55:8, 9; 59:7.
14. Ndi kuutali wotani kumene kulambira kwawo konyenga kunafika? (Yerekezani ndi 2 Mbiri 33:1-9.)
14 Ndipo nchiyani chimene iwo anali kuchita mu Yuda chimene chinaitanira tsoka la Yehova? Iwo anali kupanga mikate ya chopereka kwa “Mfumu yaikazi ya Kumwamba.” Iwo anali kupereka nsembe yothirira kwa milungu ina mwadala kuti akwiitse Yehova. Chotero, Yehova akufunsa: “Kodi ndine yemwe akukwiitsa? . . . Kodi iwo m’malomwake sakudzivulaza okha ku manyazi a nkhope zawo?” (Yeremiya 7:18, 19, New International Version) Komabe, zochita zawo zamwano zinafikira ngakhale ku mkhalidwe wotsika koposa—iwo anakhazikitsa mafano onyazitsa m’nyumba imene inali ndi dzina la Yehova. Iwo anamanga maguwa ansembe kunja kwa Yerusalemu, m’chigwa cha Hinomu, “kuti atenthe moto ana awo a amuna ndi a akazi.” Ndi mtengo wotani umene iwo anayenera kulipira kaamba ka kunyazitsa kwawo konse ku kulambira kowona?—Yeremiya 7:30, 31.
Yuda Apereka Malipiro
15. Ndi mbiri yoipa yotani imene Yeremiya anali nayo kaamba ka Yuda?
15 Pofika chifupifupi 632 B.C.E., Asuri anali atagonjera kwa Akasidi ndi Amedi, ndipo Igupto anachepetsedwa kukhala mphamvu yaing’ono kum’mwera kwa Yuda. Chiwopsyezo chenicheni kwa Yuda chikayenera kubwera kupyolera m’kulandidwa kwa kumpoto. Chotero, Yeremiya anayenera kupereka mbiri yoipa kwa Ayuda anzake! “Tawonani! mtundu wa anthu uchokera kumpoto . . . Ali ankhalwe, alibe chifundo. . . . Aguba monga anthu ofuna kumenyana nkhondo ndi iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni.” Mphamvu yadziko yomakwera kumeneyo panthaŵiyo anali Babulo. Iyi ikakhala chida cha Mulungu cha kulangila Yuda wosakhulupirira.—Yeremiya 6:22, 23; 25:8, 9.
16. Nchifukwa ninji panalibe chifukwa kwa Yeremiya m’kulowerera m’malo mwa mtunduwo?
16 Kodi panali nsonga iriyonse m’kuyesera kwa Yeremiya kulowerera m’malo mwa anthu a m’dziko lake? Kodi mwinamwake pakanakhala kugonjera ku kulambira kowona? Kodi Yehova mwinamwake akanalandira theka la miyezo yawo ndi kukhululukira anthu ake? Kaimidwe ka Yehova kanali kowonekera. Iye analamulira Yeremiya pa zochitika zitatu: “Usapempherere anthu awa, . . . pakuti ine sindidzakumvera iwe.” M’kukwaniritsidwa kofananako, chenjezo losalandirika lofananali likuperekedwa ku Chikristu cha Dziko.—Yeremiya 7:16; 11:14; 14:11.
17, 18. Ndimotani mmene chiweruzo cha Mulungu pomalizira chinaperekedwera motsutsana ndi Yuda?
17 Ndimotani mmene zinthu zinayendera kwa Yuda? Ndendende mongadi mmene Yehova anali ataneneratu kupyolera mwa Yeremiya. Mkati mwa kulamulira kwa Mfumu Yehoyakimu, Yuda anakhala mtundu wa ukapolo ku Babulo wamphamvu. Zaka zitatu pambuyo pake Yehoyakimu anaukira. Kachitidwe kopusa kameneka kanatsogolera ku kunyazitsidwa kokulira pamanja a Babulo, omwe analanda mzinda wa Yerusalemu. Pofika nthaŵi imeneyi Yehoyakimu anali atafa ndipo anali atalowedwa m’malo ndi mwana wake Yehoyakini. Kulanda kwa Ababulo kunabweretsa Yuda pansi, ndipo Yehoyakini ndi banja lake lachifumu, limodzi ndi nduna zazikulu za mu chitaganya cha Chiyuda, zinatengedwa m’ndende ku Babulo.—2 Mafumu 24:5-17.
18 Nchiyani chimene chinachitika ku kachisi wopatulika ndi zokongoletsa zake zonse za mtengo wapatali zopatulika? Izo ndithudi sizinatumikire monga chithumwa cha mwaŵi kwa Ayuda. Nebukadinezara “anatulutsa kuchotsa komweko chuma chonse cha nyumba ya Yehova ndi chuma cha nyumba ya mfumu naduladula zipangizo zonse zagolidi adazipanga Solomo mfumu ya Israyeli m’kachisi wa Yehova.” (2 Mafumu 24:13) Potsirizira pake, mfumu yoikidwa ya Chibabulo, Zedekiya, yemwe anasiidwa kumbuyo kuti alamulire zomwe zinatsalira mu Yerusalemu, anawukiranso motsutsana ndi ambuye ake. Chimenecho chinali chokhumudwitsa chomalizira kwa Nebukadinezara. Mzinda wa Yerusalemu unalaliridwanso, ndipo mu 607 B.C.E. unagwa kwa Nebuzaradani ndipo unasakazidwa kotheratu.—Yeremiya 34:1, 21, 22; 52:5-11.
19, 20. Ndi kusiyana kotani kumene kunalipo m’kawonedwe ka Yuda ndi Yeremiya kulinga ku tsoka lonenedweratulo ndipo ndi chotulukapo chotani?
19 Ndi kugonjetsedwa kwa tsoka chotani nanga kaamba ka ‘anthu osankhidwa’! Koma ndi mowonekera chotani nanga mmene zilengezo za chiweruzo za Yeremiya zinakwezedwera. Pamene kuli kwakuti Ayuda anali kukhala m’dziko la malingaliro osangalatsa, kumakhulupirira kuti panalibe tsoka lomwe likadza kwa iwo, “wofuula tsoka” Yeremiya m’chenicheni anali kunena zowonadi, osati wolota wogonjetsedwa. (Yeremiya 38:4; dziŵani kuti liwu lakuti “tsoka” limawoneka nthaŵi 64 m’bukhu la Yeremiya.) Ndi molongosoka chotani nanga mmene chiweruzo cha Yehova chinakhalira: “Ndipo udzati kwa iwo, ‘Umene ndi mtundu wosamvera mawu a Yehova Mulungu wawo, wosalola kulangizidwa, chowonadi chatha, chadulidwa pakamwa pawo.’ Ndipo ndidzaletsa m’midzi ya Yuda, ndi m’misewu ya Yerusalemu, mawu akukondwa ndi mawu akuseka, . . . pakuti dziko lidzasanduka bwinja”!—Yeremiya 7:28, 34.
20 M’njira yowopsya imeneyi, Ayuda onyada, odzidalira anayenera kuzindikira kuti kuputa kwawo mkwiyo wa Mulungu ndi kukhala kwawo ndi unansi wapadera ndi iye sunali chivomerezo chotsimikizirika cha chipulumutso chawo. Monga mmene ulosiwo unanenera: “Tinayang’anira mtendere, koma panalibe zabwino; ndi nthaŵi ya moyo, ndipo tawona kuwopsedwa! Masika apita, mphakasa yatha, ndipo ife sitinapulumutsidwe!” (Yeremiya 8:15, 20) Kwa Yuda inali tsopano nthaŵi ya kubwezera. Koma mneneri wopanda mantha Yeremiya anachinjirizidwa kupyola mkati mwa ntchito yake ndi kuloledwa kumaliza ntchito yake. Iye anamaliza masiku ake m’ndende, osati ku Babulo ndi mtundu wochititsidwa manyaziwo, koma mu Igupto. Kwa zaka zoposa 65, iye mopanda mantha ndipo mokhulupirika analengeza ziweruzo za Mulungu.
21. Ndi mafunso owonjezereka otani amene amatidetsa nkhaŵa ife?
21 Koma tsopano tiri osangalatsidwa m’kudziŵa ndi kugwira ntchito kotani kumene moyo ndi utumiki wa Yeremiya umenewu uli nawo ku nthaŵi zathu. Ndi ndani amene angakhale ofanana ndi Yeremiya m’zana lino la 20? Ndipo bwanji ponena za Yuda ndi Yerusalemu? Ndipo nchiyani chimene chikufanana ndi chiwopsyezo chomwe chikudza kuchokera kumpoto? Nkhani zathu zotsatira zidzasanthula mafunso amenewa.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Ndimotani mmene Yeremiya anavomerezera ku ntchito yake, ndipo nchiyani chimene chinali yankho la Yehova?
◻ Nchifukwa ninji tiri osangalatsidwa m’zochitika za tsiku la Yeremiya?
◻ Ndi mkhalidwe wotani wa Chikristu umene Yeremiya anatsutsa, ndipo ndi m’chiyani mmene Ayuda anaika chikhulupiriro?
◻ Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo chomalizira kwa Yerusalemu ndi Yuda?
[Mawu Otsindika patsamba 12]
Yeremiya mopanda mantha analalikira ziweruzo za Mulungu kwa atsogoleri a Chiyuda ndi kwa anthu
[Chithunzi patsamba 13]
Akazi anaphika mkate kwa “Mfumu yaikazi ya Kumwamba”