Masiku aulosi a Danieli ndi Chikhulupiriro Chathu
“[Wachimwemwe, NW] iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.”—DANIELI 12:12.
1. Kodi nchifukwa ninji ambiri amalephera kupeza chimwemwe chenicheni, ndipo kodi chimwemwe chowona nchogwirizanitsidwa nchiyani?
ALIYENSE amafuna kukhala wachimwemwe. Komabe, lerolino, oŵerengeka kwambiri ndiwo ali achimwemwe. Chifukwa ninji? Chimodzi cha zifukwazo nchakuti ambiri amakafunafuna chimwemwe kumalo olakwika. Chimwemwe chimafunidwa m’zinthu zonga maphunziro, chuma, ntchito, kapena kufunafuna kukhala ndi mphamvu. Komabe, Yesu, poyamba Ulaliki wake wa pa Phiri, anagwirizanitsa chimwemwe ndi kudziŵa kwa munthu kusoŵa kwake kwauzimu, chifundo, kuyera mtima, ndi mikhalidwe ina yofanana nayo. (Mateyu 5:3-10) Mtundu wa chimwemwe umene Yesu analankhula ndiweniweni ndi wokhalitsa.
2. Malinga nkunena kwa ulosi, kodi nchiyani chimene chingachititse chimwemwe m’nthaŵi ya mapeto, ndipo kodi ndimafunso otani amene akubuka ponena za zimenezi?
2 Kwa otsalira odzozedwa m’nthaŵi ya mapeto, chimwemwe chagwirizanitsidwa ndi kanthu kenanso. M’buku la Danieli, timaŵerenga kuti: “Pita Danieli; pakuti mawuwo atsekedwa, nakhomeredwa chizindikiro mpaka nthaŵi ya [mapeto, NW]. Wachimwemwe iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.” (Danieli 12:9, 12) Kodi ndinyengo ya nthaŵi iti pamene masiku 1,335 ameneŵa anakhalako? Kodi nchifukwa ninji awo amene anakhala m’masikuwo anali achimwemwe? Kodi zimenezi zili ndi kanthu kena pachikhulupiriro chathu lerolino? Tingathandizidwe kuyankha mafunso ameneŵa ngati titembenukira kumbuyo panthaŵi imene Danieli analemba mawuwa, Israyeli atangomasulidwa kumene kuundende wa ku Babulo ndi m’chaka chachitatu cha Koresi mfumu ya Perisiya.—Danieli 10:1.
Kubwezeretsedwa Kudzetsa Chimwemwe
3. Kodi ndimchitidwe wotani wa Mfumu Koresi umene unadzetsa chimwemwe chachikulu kwa Ayuda okhulupirika mu 537 B.C.E., koma kodi ndimwaŵi uti umene Koresi sanapereke kwa Ayuda?
3 Kwa Ayuda, kumasulidwa ku Babulo kunali chochitika cha chikondwerero chenicheni. Ayudawo atapirira pafupifupi zaka 70 muukapolo, Koresi Wamkulu anawapempha kuti abwerere ku Yerusalemu kukamanganso kachisi wa Yehova. (Ezara 1:1, 2) Awo amene analabadira pempholo anayamba kuyenda ulendowo ali ndi ziyembekezo zazikulu, akumafika kudziko lakwawo mu 537 B.C.E. Komabe, Koresi sanawapemphe kubwezeretsa ufumu wa mbadwa ya Mfumu Davide.
4, 5. (a) Kodi ndiliti pamene ufumu wa Davide unagwetsedwa? Chifukwa ninji? (b) Kodi nchitsimikizo chotani chimene Yehova anapereka chakuti ufumu wa Davide ukabwezeretsedwanso?
4 Zimenezo zinali ndi tanthauzo lalikulu. Zaka mazana asanu poyambirirapo, Yehova anali atalonjeza Davide kuti: “Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhazikikadi kunthaŵi zonse pamaso pako; mpando wachifumu wako udzakhazikika kunthaŵi zonse.” (2 Samueli 7:16) Momvetsa chisoni, mbadwa zambiri za mzera wachifumu wa Davide zinapanduka, ndipo liŵongo la mwazi la mtunduwo linakhala lalikulu koposa kwakuti mu 607 B.C.E., Yehova analola ufumu wa Davide kugwetsedwa. Kusiyapo panyengo yaifupi ya Maccabees, Yerusalemu analamulidwa ndi ulamuliro wachilendo kuyambira pamenepo kufikira pachiwonongeko chake chachiŵiri mu 70 C.E. Motero, mu 537 B.C.E., “nthaŵi zawo za anthu akunja,” m’zimene panalibe mwana wa Davide amene akalamulira monga mfumu, zinayamba.—Luka 21:24.
5 Komabe, Yehova sanaiŵale lonjezo lake kwa Davide. Mwa mipambo ya masomphenya ndi maloto, iye anavumbula kupyolera mwa mneneri wake Danieli tsatanetsatane wa zochitika zadziko zamtsogolo zimene zikatenga nyengo ya zaka mazana ambiri kuyambira panthaŵi ya ulamuliro wa dziko wa Babulo kufikira panthaŵiyo pamene mfumu yokhala mumzera wa Davide ikalamuliranso muufumu wa anthu a Yehova. Maulosi ameneŵa, olembedwa m’buku la Danieli machaputala 2, 7, 8, ndi 10-12, anatsimikiziritsa Ayuda okhulupirika kuti, potsirizira pake, mpando wachifumu wa Davide ‘udzakhazikikadi kunthaŵi zonse.’ Ndithudi, chowonadi chovumbulidwacho chinadzetsa chimwemwe kwa Ayuda amenewo amene anabwerera kudziko lakwawo mu 537 B.C.E.!
6. Kodi timadziŵa motani kuti ena a maulosi a Danieli anafunikira kudzakwaniritsidwa m’nthaŵi yathu?
6 Othirira ndemanga a Baibulo ambiri amanena kuti maulosi a Danieli anakwaniritsidwa pafupifupi onse amene kubadwa kwa Yesu Kristu kusanachitike. Koma zimenezi sizili choncho konse. Pa Danieli 12:4, mngelo akuuza Danieli kuti: “Tsekera mawu awa, nukhomere chizindikiro buku, mpaka nthaŵi ya [mapeto, NW]; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziŵitso chidzachuluka.” Ngati buku la Danieli linafunikira kutsegulidwa—tanthauzo lake likumavumbulidwa mokwanira—m’nthaŵi ya mapeto yokha, ndithudi ena a maulosi ake ayenera kugwira ntchito m’nyengo imeneyo.—Onani Danieli 2:28; 8:17; 10:14.
7. (a) Kodi ndiliti pamene nthaŵi zoikidwiratu za amitundu zinatha, ndipo kodi ndifunso lofuna yankho lofulumira liti limene linayenera kuyankhidwa panthaŵiyo? (b) Kodi ndani amene sanali “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?
7 Mu 1914 nthaŵi zoikidwiratu za amitundu zinatha, ndipo nthaŵi ya mapeto a dzikoli inayamba. Ufumu wa Davide unabwezeretsedwa, osati ku Yerusalemu wa padziko lapansi, koma mosaoneka mu “mitambo ya kumwamba.” (Danieli 7:13, 14) Panthaŵiyo, chifukwa chakuti “namsongole” wa Chikristu chonyengezera anali kufalikira, mkhalidwe wa Chikristu chowona sunaonekere bwino—makamaka ndi maso aumunthu. Komabe, funso lofunika linayenera kuyankhidwa: “Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru?” (Mateyu 13:24-30; 24:45) Kodi ndani amene akaimira Ufumu wa Davide wobwezeretsedwansowo padziko lapansi? Osati abale akuthupi a Danieli, Ayuda. Iwo anali atakanidwa chifukwa chakuti anasoŵa chikhulupiriro nakhumudwa ndi Mesiya. (Aroma 9:31-33) Kapolo wokhulupirikayo sanapezeke konse pakati pa magulu a Dziko Lachikristu! Ntchito zawo zoipa zinatsimikizira kuti Yesu sanawadziŵe. (Mateyu 7:21-23) Nangano, kodi iye anali yani?
8. Kodi ndani amene atsimikizira kukhala “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” m’nthaŵi ya mapeto? Kodi tikudziŵa motani?
8 Mosakayikira konse, iye anali bungwe laling’ono la abale a Yesu odzozedwa amene mu 1914 anadziŵika kukhala Ophunzira Baibulo koma chiyambire 1931 adziŵidwa monga Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10) Ndiokhawo amene alengeza za Ufumu wobwezeretsedwanso mumzera wa Davide. (Mateyu 24:14) Ndiokhawo amene anadzilekanitsa ndi dziko ndi kulemekeza dzina la Yehova. (Yohane 17:6, 14) Ndipo nkwa okhawo kumene maulosi a Baibulo onena za anthu a Mulungu m’masiku omaliza akwaniritsidwapo. Pakati pa maulosi ameneŵa pali mpambo wa nyengo za ulosi wondandalikidwa m’buku la Danieli chaputala 12 zimene zimaphatikizapo masiku 1,335 amene akadzetsa chimwemwe.
Masiku 1,260
9, 10. Kodi ndizochitika zotani zimene zinasonyeza “nthaŵi imodzi ndi nthaŵi zina, ndi nthaŵi yanusu” ya pa Danieli 7:25, ndipo kodi ndimalemba ena ati amene amanena mogwirizana ndi nyengo ya nthaŵi yotchulidwayo?
9 Pa Danieli 12:7, timaŵerenga za nyengo yoyamba ya ulosiwo kuti: “Zidzachitika nthaŵi, ndi nthaŵi zina, ndi nusu; ndipo atatha kumwaza mphamvu ya anthu opatulikawo zidzatha izi zonse.”a Nyengo imodzimodziyi ikutchulidwa pa Chivumbulutso 11:3-6, pamene pamati mboni za Mulungu zikalalikira m’chiguduli kwazaka zitatu ndi theka ndiyeno zikaphedwa. Kachiŵirinso, pa Danieli 7:25, timaŵerenga kuti: “Nidzanena mawu akutsutsana ndi Wam’mwambamwamba, nidzalemetsa opatulika a Wam’mwambamwamba, nidzayesa kusintha nthaŵizo ndi chilamulo; ndipo adzaperekedwa m’dzanja lake mpaka nthaŵi imodzi ndi nthaŵi zina, ndi nthaŵi yanusu.”
10 Muulosi wotsirizirawu, ‘wodzanenayo’ ndiye ulamuliro wachisanu wa padziko lonse kuyambira pa Babulo. Umenewu ndiwo “nyanga ina, ndiyo yaing’ono,” umene ukakhalapo munthaŵi imene Mwana wa munthu akalandira “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu.” (Danieli 7:8, 14) Nyanga yophiphiritsira imeneyi, imene poyambirira inali ulamuliro wa Britain, inakula mkati mwa nkhondo yadziko yoyamba kukhala ulamuliro wadziko wa mbali ziŵiri wa Britain ndi America, tsopano wotsogozedwa ndi United States. Kwanthaŵi kapena zaka, zitatu ndi nusu, ulamuliro umenewu ukavutitsa oyera ndi kuyesa kusintha nthaŵi ndi lamulo. Potsirizira pake, oyerawo akaperekedwa m’dzanja lake.—Onaninso Chivumbulutso 13:5, 7.
11, 12. Kodi ndizochitika ziti zimene zinatsogolera kuchiyambi cha masiku aulosi 1,260?
11 Kodi maulosi oyendera limodzi ameneŵa anakwaniritsidwa motani? Kwazaka zambiri Nkhondo Yadziko I isanachitike, abale odzozedwa a Yesu anachenjeza poyera kuti 1914 akakhala mapeto a nthaŵi zoikidwiratu za amitundu. Pamene nkhondo inaulika, kunali kwachionekere kuti chenjezolo linali litanyalanyazidwa. Satana anagwiritsira ntchito “chilombo” chake, gulu la ndale la dziko panthaŵiyo lotsogozedwa ndi ulamuliro wa Britain, poyesayesa “kusintha nthaŵizo ndi chilamulo,” kuletsa nthaŵi imene Ufumu wa Mulungu ukalamulira. (Chivumbulutso 13:1, 2) Iye analephera. Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba, kosafikirika ndi munthu.—Chivumbulutso 12:1-3.
12 Kwa Ophunzira Baibulo, nkhondoyo inatanthauza nthaŵi ya mayeso. Kuyambira January 1914 iwo anali kusonyeza Photo-Drama of Creation, ulaliki wa m’Baibulo umene unasonkhezera chidwi pamaulosi a Danieli. M’chilimwe cha chaka chimenecho ku Northern Hemisphere, nkhondo inaulika. Mu October, nthaŵi zoikidwiratu zinatha. Podzafika kumapeto kwa chakacho, otsalira odzozedwa anali kuyembekezera chizunzo, monga momwe zikusonyezedwera m’chenicheni chakuti lemba la chaka cha 1915 linali funso la Yesu kwa ophunzira ake lakuti, “Kodi mukhoza kumwa chikho changa?” lotengedwa pa Mateyu 20:22, King James Version.
13. Kodi ndimotani mmene Ophunzira Baibulo analalikirira m’chiguduli m’masiku 1,260, ndipo nchiyani chimene chinachitika pamapeto a nyengo imeneyo?
13 Chifukwa chake, kuyambira mu December 1914, kagulu kakang’ono ka mboni kameneka ‘kanalalikira m’chiguduli,’ kakumapirira modzichepetsa pamene kanali kulengeza ziweruzo za Yehova. Chochititsa kakasi kwa ambiri chinali imfa ya C. T. Russell mu 1916, prezidenti woyamba wa Watch Tower Bible and Tract Society. Pamene mzimu wa nkhondo unafalikira, kaguluko kanakumana ndi chitsutso chomakulakula. Ena anaikidwa m’ndende. Ena, monga ngati Frank Platt ku England ndi Robert Clegg ku Canada, anazunzidwa ndi akuluakulu ankhalwe. Potsirizira pake, pa June 21, 1918, J. F. Rutherford, prezidenti watsopano, limodzi ndi akuluakulu a Watch Tower Bible and Tract Society, anapatsidwa chilango cha kukhala m’ndende kwa nthaŵi yaitali pazinenezo zonama. Motero, chakumapeto kwa nyengo yaulosiyo, “nyanga yaing’ono” imeneyo inapha ntchito yolinganizidwa ya kulalikira poyera.—Danieli 7:8, King James Version.
14. Kodi ndimotani mmene zinthu zinasinthira kwa otsalira odzozedwa mu 1919 ndi pambuyo pake?
14 Buku la Chivumbulutso limalosera zimene kenako zinachitika. Patapita nyengo yaifupi ya kusagwira ntchito—yonenedweratu kukhala masiku atatu ndi nusu mitembo yawo ili pakhwalala—otsalira odzozedwa anakhala ndi moyo nayambanso kugwira ntchito. (Chivumbulutso 11:11-13) Pa March 26, 1919, prezidentiyo ndi akuluakulu a Watch Tower Bible and Tract Society anamasulidwa, ndiyeno pambuyo pake anachotseredwa zinenezo zawo zonse zonama. Mwamsanga atamasulidwa, otsalira odzozedwa anayamba kukonzekera ntchito ina yowonjezereka. Motero, m’kukwaniritsa tsoka loyamba la m’buku la Chivumbulutso, iwo anatuluka m’dzenje la phompho la kusagwira ntchito monga dzombe lauzimu limodzi ndi utsi wochindikala, zikumasonyeza mtsogolo mopanda chiyembekezo mwa chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 9:1-11) M’zaka zotsatira zoŵerengeka, anadyetsedwa mwauzimu ndipo anali okonzekera za mtsogolo. Mu 1921 iwo anafalitsa buku latsopano lakuti, Zeze wa Mulungu, lolinganizidwira kuthandiza atsopano ndi ana kuphunzira chowonadi chamaziko cha Baibulo. (Chivumbulutso 12:6, 14) Zinthu zonsezi zinachitika m’nthaŵi ya nyengo ina yapadera.
Masiku 1,290
15. Kodi ndim’njira yotani mmene tingaŵerengerere chiyambi cha masiku 1,290? Kodi ndiliti pamene nyengo imeneyi inatha?
15 Mngelo anati kwa Danieli: “Kuyambira nthaŵi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire [“nsembe yopitirizabe,” NW, mawu amtsinde], nichidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana aŵiri kudza makumi asanu ndi anayi.” (Danieli 12:11) Pansi pa Chilamulo cha Mose, “nsembe yopitirizabe” inapserezedwa paguwa la nsembe pakachisi mu Yerusalemu. Akristu samapereka nsembe zopsereza, koma iwo amapereka nsembe yopitirizabe yauzimu. Paulo anatanthauza zimenezi pamene anati: “Tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.” (Ahebri 13:15; yerekezerani ndi Hoseya 14:2.) Nsembe yopitirizabe imeneyi inachotsedwa mu June 1918. Nangano nchiyani chimene chinali “chonyansa”—mbali yachiŵiri yofuna kupendedwa? Chinali gulu la Chigwirizano cha Mitundu, lochilikizidwa ndi maiko opambana pamapeto a Nkhondo Yadziko I.b Chinali chonyansa chifukwa chakuti atsogoleri a Dziko Lachikristu anachiika m’malo a Ufumu wa Mulungu, kuimira Chigwirizanocho monga chiyembekezo chokha cha mtendere cha anthu. Chigwirizanocho chinalinganizidwa mu January 1919. Ngati tiŵerenga masiku 1,290 (zaka zitatu, miyezi isanu ndi iŵiri) kuyambira panthaŵiyo, timafika mu September 1922.
16. Pamapeto a masiku 1,290, kodi ndimotani mmene kunaliri kwachionekere kuti otsalira odzozedwa anali okonzekera kuchitapo kanthu?
16 Nangano nchiyani chimene chinachitika? Eya, Ophunzira Baibulo tsopano anali otsitsimulidwa, omasuka ku Babulo Wamkulu, ndipo okonzeka kuchitapo kanthu. (Chivumbulutso 18:4) Pamsonkhano wochitidwa mu September 1922 pa Cedar Point, Ohio, U.S.A., iwo anayamba kulengeza mopanda mantha ziweruzo za Mulungu pa Dziko Lachikristu. (Chivumbulutso 8:7-12) Mbola za dzombe zinayambadi kupweteka! Chinthu chinanso nchakuti, tsoka lachiŵiri la m’Chivumbulutso linayamba. Unyinji wa ankhondo a pakavalo Achikristu—poyambirira wopangidwa ndi otsalira odzozedwa ndiyeno nuwonjezeka ndi khamu lalikulu—unakuta dziko lapansi. (Chivumbulutso 7:9; 9:13-19) Inde, mapeto a masiku 1,290 anadzetsa chisangalalo kwa anthu a Mulungu.c Koma panalinso zina.
Masiku 1,335
17. Kodi ndiliti pamene masiku 1,335 anayamba ndi kutha?
17 Pa Danieli 12:12 pamati: “Wachimwemwe iye amene ayembekeza, nafikira kumasiku chikwi chimodzi mphambu mazana atatu kudza makumi atatu ndi asanu.” Masiku 1,335 ameneŵa, kapena zaka zitatu, miyezi isanu ndi itatu ndi nusu, malinga ndi umboni anayamba pamapeto a nyengo imene inathayo. Pamene tiŵerenga kuyambira September 1922, zimenezi zimatifikitsa kumapeto a ngululu (ku Northern Hemisphere) ya 1926. Kodi nchiyani chimene chinachitika m’masiku 1,335 amenewo?
18. Kodi ndimaumboni ati amene amasonyeza kuti kalelo mu 1922 munafunikirabe masinthidwe oti achitidwe?
18 Mosasamala kanthu za kusintha kwa zinthu mu 1922, malinga ndi umboni ena analakalaka zakumbuyo. Mabuku a Studies in the Scriptures, olembedwa ndi C. T. Russell, anali kugwiritsidwabe ntchito kwambiri pophunzira. Ndiponso, kabuku kofalitsidwa kwambiri kakuti Millions Now Living Will Never Die kanapereka lingaliro lakuti mu 1925, zifuno za Mulungu ponena za kubwezeretsanso dziko lapansi ku Paradaiso ndi kuukitsidwa kwa anthu okhulupirika akale kukayamba kukwaniritsidwa. Chipiriro cha odzozedwa chinaonekera kukhala chikuyandikira mapeto ake. Chikhalirechobe, ena amene anayanjana ndi Ophunzira Baibulo sanadzimve kukhala okakamizika kuuza ena mbiri yabwino.
19, 20. (a) Kodi ndimotani mmene zinthu zambiri zinasinthira kwa anthu a Mulungu m’masiku 1,335? (b) Kodi nzochitika zotani zimene zinasonyeza mapeto a nyengo ya masiku 1,335, ndipo zinasonyezanji ponena za anthu a Yehova?
19 Pamene masiku 1,335 analinkupita, zonsezi zinasintha. Kuti abale alimbikitsidwe, panalinganizidwa timagulu tokhazikika ta maphunziro a The Watch Tower. Utumiki wakumunda unalimbikitsidwa. Kuyambira m’May 1923, aliyense anapemphedwa kuti akhale ndi phande muutumiki wakumunda patsiku Lachiŵiri loyamba la mwezi uliwonse, ndipo panapatulidwa nthaŵi pamisonkhano ya mpingo ya mkati mwa mlungu kuwalimbikitsa kugwira ntchito imeneyi. Mu August 1923, pamsonkhano wa mu Los Angeles, California, U.S.A., panasonyezedwa kuti fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi likakwaniritsidwa Ulamuliro wa Zaka Chikwi usanadze. (Mateyu 25:31-40) M’chaka cha 1924 munatsegulidwa nyumba ya wailesi yotchedwa WBBR, imene inagwiritsiridwa ntchito kuulutsira mbiri yabwino pawailesi. Nkhani yakuti “Kubadwa kwa Mtundu” m’kope la The Watch Tower la March 1, 1925, inawongolera tanthauzo la buku la Chivumbulutso chaputala 12. Potsirizira pake, Akristu okhulupirika anazindikira bwino tanthauzo la zochitika za chipwirikiti cha 1914-19.
20 Chaka cha 1925 chinafika pamapeto ake, komatu mapeto adziko anali asanadzebe! Chiyambire m’ma 1870, Ophunzira Baibulo anakhala akutumikira mokumbukira madetiwo—choyamba 1914, ndiyeno 1925. Tsopano, iwo anazindikira kuti ayenera kutumikira kwautali womwe Yehova akufuna. Kope la The Watch Tower la January 1, 1926, linali ndi nkhani yosintha zinthu yakuti “Kodi Ndani Adzalemekeza Yehova?” ikumafotokoza koposadi kalelonse kufunika kwa dzina la Mulungu. Ndipo potsirizira pake, m’May 1926 pamsonkhano wa ku London, England, panatengedwa chitsimikizo chotchedwa kuti “Umboni kwa Olamulira a Dziko.” Chimenechi chinalengeza molunjika chowonadi cha Ufumu wa Mulungu ndi kudza kwa chiwonongeko cha dziko la Satana. Pamsonkhano womwewo, buku lokhala ndi uthenga wamphamvu lotchedwa Deliverance linatulutsidwa, likumakhala buku loyamba mumpambo wake kuloŵa m’malo Studies in the Scriptures. Tsopano anthu a Mulungu anali kuyembekezera zochitika mtsogolo, osati kulakalaka za m’mbuyo. Masiku 1,335 anatha pamenepo.
21. Kodi kupirira m’nyengo ya masiku 1,335 kunatanthauzanji kwa anthu a Mulungu kalelo, ndipo kodi nchiyani chimene kukwaniritsidwa kwa ulosi wonena za nyengo ya nthaŵiyo kumatanthauza kwa ife?
21 Ena sanafune kusintha kuti agwirizane ndi zochitika zimenezi, koma awo amene anapirira analidi achimwemwe. Ndiponso, pamene tipenda za kukwaniritsidwa kwa nyengo za nthaŵi yaulosi zimenezi, nafenso timakhala achimwemwe chifukwa chakuti chidaliro chathu chimalimbikitsidwa chakuti kabungwe kakang’ono ka Akristu odzozedwa kamene kanapyola m’nthaŵi zimenezo kalidi kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. M’zaka zotsatira chiyambire nthaŵiyo, gulu la Yehova lafutukuka kwambiri, koma kapolo wokhulupirika ndi wanzeruyo akulitsogolerabe. Pamenepo, nkokondweretsa chotani nanga kudziŵa kuti pali chimwemwe chinanso chowonjezereka kwa odzozedwa ndi nkhosa zina! Tidzaona zimenezi pamene tipenda maulosi ena a Danieli.
[Mawu a M’munsi]
a Ponena za mmene munthu angaŵerengere nyengo zimenezi, onani buku lakuti Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu, mutu 8, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Onani kope la Nsanja ya Olonda la April 1, 1986, pamasamba 8-18.
c Onani kope la Nsanja ya Olonda la January 1, 1991, patsamba 12, ndi 1975 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, patsamba 132.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi ndimotani mmene timadziŵira kuti maulosi ena a m’buku la Danieli anafunikira kudzakwaniritsidwa m’nthaŵi yathu?
◻ Kodi nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro chakuti otsalira odzozedwa ndiwo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”?
◻ Kodi ndiliti pamene masiku 1,260 anayamba ndi kutha?
◻ Kodi ndikutsitsimula kotani ndi kubwezeretsedwanso kumene masiku 1,290 anadzetsa kwa otsalira odzozedwa?
◻ Kodi nchifukwa ninji awo amene anapirira kufikira mapeto a masiku 1,335 anali achimwemwe?
[Bokosi patsamba 11]
NYENGO ZA NTHAŴI ZA ULOSI WA DANIELI
Masiku 1,260:
December 1914 mpaka June 1918
Masiku 1,290:
January 1919 mpaka September 1922
Masiku 1,335:
September 1922 mpaka May 1926
[Chithunzi patsamba 8]
Kwakhala kwachionekere chiyambire 1919 kuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndiye kagulu ka otsalira odzozedwa
[Chithunzi patsamba 10]
Malikulu a Chigwirizano cha Mitundu mu Geneva, Switzerland
[Mawu a Chithunzi]
Chithunzi cha UN