‘Palibe Mtendere kwa Oipa’
“‘Palibe mtendere,’ ati Mulungu wanga, ‘kwa oipa.’”—YESAYA 57:21.
1, 2. (a ) Kodi ndimotani mmene anthu ambiri amamverera ponena za mtsogolo mwa mtundu wa anthu? (b) Kodi nchiyani chimene chakhala chotulukapo cha zoyesayesa za anthu za kupanga mtendere?
“NDIRI mokhazikika wozindikira kuti mphindi iriyonse dziko lingaphulikire kumaso kwanga.” Mawu ochititsa mantha amenewa, ogwidwa mawu mu magazini ya Psychology Today, anapangidwa ndi wophunzira pa sukulu yapamwamba ku North America. Nthawi ina yake posachedwa, wophunzirayo anawopa, nkhondo ya nyukiliya mwachiwonekere ingawononge mtundu onse wa anthu. Msungwana wa sukulu wa chiRussia akulongosola zotulukapo za nkhondo ya nyukiliya: “Zinthu zonse za moyo zidzatha psyiti—popanda udzu, mitengo, kubiriwira.” Ndi chiyembekezo chochititsa mantha chotani nanga! Komabe, anthu amamva kuti ichi chikachitikadi. Mu kufufuza kwaposachedwa 40 peresenti ya akulu ofunsidwa anamva kuti panali “mwawi wokulira” wa nkhondo ya nyukiliya chisanafike chaka cha 2000.—Onani Luka 21:26.
2 Atsogoleri adziko nawonso amawona ngozi. Pamapeto pa nkhondo ya dziko yomalizira, iwo anakhazikitsa gulu la Mitundu Yogwirizana kuyesera kubweretsa mtendere ndi chisungiko kwa mtundu wa anthu—koma mopanda phindu. M’malo mwake, zaka za pamapeto pa nkhondo zawona kukula kwamphamvu kwa udani pakati pa maulamuliro aakulu amphamvu awiri a zida za nyukiliya. Kwanthawi ndi nthawi, atsogoleri amphamvu zimenezi amakumana kuyesa kuthetsa chidani chadziko lonse, ndi zotulukapo zochepa. Mosasamala kanthu za chenicheni chakuti atsogoleri achipembedzo akupemphera kaamba ka mtendere, mikhalidwe iri yofananandi monga mmene yalongosoledwera pa Yesaya: “Olimba mtima awo angofuula kunja, mithenga ya mtendere ilira kowawa.”—Yesaya 33:7.
3. Nchifukwa ninji palibe kuthekera kwakuti anthu adzapambana mu zoyesayesa zawo zopanga mtendere?
3 Akristu odziwitsidwa bwino amadziwa nchifukwa ninji andale sangabweretse nkomwe mtendere wosatha. Iwo amazindikira kuti kufikira ku utali kumene anthu ali odzaza ndi kudzikonda, chidani, umbombo, kunyada, ndi kudzitukumula, sipadzakhala mtendere. (Yerekezani ndi Yakobo 4:1. ) Pambali pa icho, zochita za anthu sizilamuliridwa kotheratu ndi anthu. M’malo mwake, Baibulo limatiuza ife: “Dziko lonse ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19; 2 Akorinto 4:4) Mkhalidwe wa mtundu wa anthu pansi pa wolamulira ameneyu ukulongosoledwa bwino ndi Yesaya: “Koma oipa ali ofanana ndi nyanja yowinduka; pakuti sungaipume, . . . ‘palibe mtendere’, ati Mulungu wanga, ‘kwa oipa.’”—Yesaya 57:20, 21.
“Mulungu wa Mtendere“
4. Kodi ndani yekha amene ali ndi mphamvu ya kubweretsa mtendere padziko lapansi?
4 Ichi sichimatanthauza kuti mtundu wa anthu sungathe kupulumuka chiwonongeko chamtsogolo cha nkhondo ya nyukiliya. Icho chingotanthauza kokha kuti ngati tikayenera kuwona mtendere, uyenera kuchokera ku magwero akunja. Mwachimwemwe, magwero amenewo alipo mu munthu wa Yehova Mulungu, “Mulungu wa mtendere.” (Aroma 16:20) lye ali ndi mphamvu ya kulimbana ndi zisonkhezero za Satana ndipo wakonzekera “kudalitsa anthu ake ndi mtendere.” (Masalmo 29:11) Mkuwonjezerapo, iye wapanga lonjezo losangalatsa: “Ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Masalmo 37:11.
5. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova anagwiritsira ntchito Danieli kutipatsa ife chidziWitso ponena za chifuno chake chakubweretsa mtendere? (b) Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala okhudzidwa ndi ulosi umenewu wolembedwa ndi Danieli?
5 Zaka zambiri zapita, Yehova anavumbulutsa kukula kwa mbiri yakale ya zinthu zomwe zidzatsogolera kukubweretsa kwake mtendere padziko lapansi. Kupyolera mwa m’ngelo iye analankhula kwa mneneri wake wokhulupirika Danieli ponena za “masiku amapeto,” nthawi yathu. (Danieli 10:14) Iye ananeneratu ponena za chidani cha mphamvu zazikulu za lerolino ndipo anasonyeza kuti posachedwa idzatha m’njira imene iriyonse yamphamvuzo siyembekezera. Ndipo iye analonjeza kuti zochitika zosayembekezereka zimenezi zidzabweretsa mtendere weniweni. Kwa Akristu ulosi umenewu uli wachikondwerero chachikulu. Umapereka kayang’anidwe kowonekera ka pamene tiri mu nthawi ya nyengo ndi kulimbikitsa kulimba mtimakwathu kukhalabe a uchete ku udani wa dziko lonse pamene tikudikirira moleza mtima kaamba ka Mulungu kuchitapo kanthu m’malo mwathu.—Masalmo 146:3, 5.
Udani Uyambika
6. Longosolani chiyambi cha mbiri ya udani wamphamvu zazikulu za lerolino.
6 Chowonadi chiri chakuti, udani wamphamvu zazikulu za lerolino siuli chinthu chatsopano pa chochitika chadziko. Iwo, m’malo mwake, uli kupitirizika kwa chinthu chinachake chomwe chinayamba nthawi yakale. Pambuyo pa kugwa kwa ulamuliro wa Alexander the Great cha kumapeto kwa chaka cha zana lachinayi B. C.E., awiri a atsogoleri ake a nkhondo anatenga mphamvu ya Syria ndi Igupto. Udani wosatha umene mokulira unatsogolera ku mpikisano wa mphamvu zazikulu unabuka pakati pawo ndipo mlowa m’malo wawo—wolankhulidwa monga mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera chifukwa chakuti iwo ali kumpoto ndi kum’mwera kwa dziko la anthu a Mulungu. Kukula kwambiri kwa udani umenewo kunavumbulidwa pasadakhale kwa mneneri Danieli kupyolera mwa m’ngelo.
7. (a) Kodi timadziwa motani kuti pali mbali yosawoneka, ya mzimu ku zochitika za anthu? (b) Ndi ndani poyambirira, amene anali mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera, ndipo ndimotani mmene udani wawo unayambira?
7 M’ngeloyo choyamba analongosola ndimotani mmene iye, mochirikizidwa ndi Mikaeli, anakhala akumenya molimbana ndi ‘akalonga’ a mizimu ya Perisiya ndi Girisi. (Danieli 10:13, 20-11:1) Kusunzumira kumeneku m’malo a mizimu kumatsimikizira kuti kulimbana kwa utundu kumaphatikiza zoposa anthu wamba. Pali mphamvu za ziwanda kapena “akalonga,” kumbuyo kwa atsogoleri a anthu owoneka ndi maso. Koma kuchokera kunthawi za makedzana anthu a Mulungu akhala ali ndi “kalonga,” Mikaeli, kuwalimbikitsa iwo motsutsana ndi mphamvu za uchiwanda zimenezi. (Aefeso 6:12) Kenaka m’ngeloyo akulunjikitsa chidwi chathu pa udani pakati pa Syria ndi Igupto. Iye akuyamba: “Ndipo mfumu ya kum’mwera, ndiye wina wa akalonga wake.” (Danieli 11:5a) Mfumu ya kum’mwera pano inali Ptolemy I, wolamulira wa Igupto, yemwe analanda Yerusalemu chifupifupi 312 B.C.E. M’ngeloyo kenaka akulozera kwa mfumu ina yomwe “idzamposa mphamvu, nidzakhala nawo ulamuliro; ulamuliro wake ndi ulamuliro waukulu.” (Danieli 11:5b) Iyi ndi mfumu ya kumpoto mwaSeleucus I Nicator, amene ufumu wake, Syria, unakhala wamphamvu kuposa Igupto.
8. Kodi nchiyani chimene kulongosola kodziwikiratu kwa mbali yoyambirira ya ulosi wa m’ngelo ponena za mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera kumatanthauza kwa Akristu lerolino?
8 M’ngeloyo akupitiriza kulosera tsatanetsatane wa zochuluka ponena za kupitiriza kwa udani pakati pa olamulira opambana a Syria ndi Igupto. (Danieli 11:6-19) Maulosi amenewa anali olongosoka kotero kuti ena amadzimva kuti bukhu la Danieli lingakhale linalembedwa pambuyo pachochitika chenicheni.a Kwa Akristu, ngakhale kuli tero, kulongosoka kotsimikizirika kwa maulosi kumeneku kumalimbikitsa chikhulupiriro chawo mu mbali zimenezo za ulosi zomwe zidzakwaniritsidwa mkati mwa “masiku amapeto.”
Kalonga wa Pangano
9. Kodi ndimotani mmene kachitidwe ka mfumu ya kumpoto kanatsogolera ku kubadwira kwa Yesu ku Betelehemu?
9 Sichiyenera kuyembekezeredwa kuti m’ngeloyo adzatetezera wolamulira aliyense kuchokera kwa Ptolemy kufikira ku “nthawi ya mapeto.” M’malo mwake, tikumvetsetsa kuti pambuyo pa versi 19 ulosiwo ukulumpha ku zaka zotsatizana mwamsanga mu Nyengo Yathu, pamene tiwerenga: “Ndipo m’malo mwake [mwa mfumu ya kumpoto] adzauka wina wakupititsa wamsonkho pa ulemerero wa ufumuwo.” (Danieli 11:20) Kufikira tsopano, Syria ali gawo la Roma, ndipo mfumu ya kumpoto ikuimiridwa ndi wolamulira wa Chiroma Augustus. Iye anali amene analamulira kulembetsa komwe kunatulukapo m’kubadwira kwa Yesu ku Betelehemu m’malo mwa ku Nazarete.—Luka 2:1-7; Mika 5:2.
10. Kodi ndi kuchigwirizano china chotani pakati pa mfumu ya kumpoto ndi Mesiya ku chimene m’ngelo anakokera chidwi chathu?
10 Pambuyo pa Augustus kunabwera Tiberius, munthu wonyansa wolongosoledwa ndi m’ngelo monga “munthu woluluka.” (Danieli 11:21) Mkati mwa ulamuliro wake, chiwembu chowopsya ku malire a kumpoto kwa Ufumu wa Roma chinaletsedwa ndipo malirewo anathunzitsidwa mtima, kukwaniritsa mawu a ulosi: “Ndipo mwa mayendedwe ake a chigumula adzakokololedwa pamaso pake, nadzathyoledwa.” Mkuwonjezerapo, mkati mwa ulamuliro wake Yesu anaphedwa ndi asirikari a Chiroma mkukwaniritsa ulosi wa m’ngelo kuti “Mtsogoleri wapangano” adzathyoledwa.—Danieli 11:22; 9:27.
Pa “Nthawi Yoikidwiratu”
11. (a) Mu 1914, kodi nchiyani chomwe chinali chizindikiro cha mfumu ya kumpoto ndi ya kum’mwera? (b) Kodi ndi ulosi uti umene unakwaniritsidwa pa nthawi zoikidwiratu”?
11 Kenaka, ulosiwo ukutibweretsa ife kufika ku “nthawi yoikidwiratu,” mu 1914. (Danieli 11:27; Luka 21:24) Kufikira tsopano, pakhala kusintha mu kuzindikirika kwa anthu a Mulungu. Popeza Israyeli wakuthupi anakana Mesiya, anthu osankhidwa a Yehova anakhala Israyeli wauzimu, mpingo wa Akristu odzozedwa. (1 Petro 2:9, 10) Chizindikiritso cha mafumu awiri chasinthanso. Britain, ndi mnzake wandale United States of America, mwachiwonekere akhala mfumu ya kum’mwera, pamene mfumu ya kumpoto tsopano iri Germany. Nkhondo ya Dziko I inanenedweratu mu mawu awa: “Pa nthawi yoikika adzabwerera [mfumu ya kumpoto] nadzalowa kum’mwera; koma siidzakhala monga nthawi yoyamba ija, kapena yotsirizayi.” (Danieli ll: 29) Mfumu ya kum’mwera inapambana nkhondo. Mkhalidwe chotero unali wosiyana ndi chimene chinali chowona “poyamba, kunena kuti, pamene Roma yemwe anali kupambana anali mfumu ya kumpoto.
12. Longosolani mbali za zochitika za dziko kuyambira 1914 zomwe zinanenedweratu ndi m’ngelo mu mawu a ulosi kwa Danieli.
12 M’ngeloyo akupitiriza kunena za kupikisana pakati pa mafumu awiri kuyambira 1914 ndi, makamaka, m’njira imene onse awiri adzatsutsana ndi anthu a Yehova. Iye analoseranso za kuwoneka kwa “chonyansa cha kupululutsa,” chomwe chikukhalapo lerolino monga gulu la Mitundu Yogwirizana. (Danieli 11:31) Kukhazikitsidwa kwa UN kunali kuyesayesa kwa ndale mu kumene mafumu onse awiri anagwirizana kubweretsa mtendere. Koma chiri chotsimikizirika kulephera chifukwa chiri motsutsana ndi Ufumu wa Mulungu.b (Mateyu 24:15; Chivumbulutso 17:3, 8) Potsinzira, m’ngeloyo akulunjikitsa chidwi chathu ku “nthawi ya mapeto.”—Danieli 11:40.
Nthawi Yotsiriza”
13. (a) Mu 1914, kodi nchiyani chomwe chinali chizindikiro cha mfumu ya kumpoto ndi ya kum’mwera? (b) Kodi ndi ulosi uti umene unakwaniritsidwa pa nthawi zoikidwiratu”?
13 Kodi nthawi imeneyi nchiyani? Nthawi zina mawu akuti “nthawi yotsiriza” amalozera ku nthawi ya mapeto a dongosolo la kachitidwe kazinthu ili kuyambira 1914 kufika ku Armagedo. (Danieli 8:17, 19; 12:4) Koma zochitika mu chaka cha 1914, “nthawi yoikidwiratu,” zinanenedweratu kale mu versi 29, ndipo ulosi wa m’ngelo wabweretsedwa kwa ife kupyola pamenepo.c Chotero, “nthawi yotsirizira” pano mu versi 40 iyenera kulozera ku masiteji omalizira a zaka 2, 300 zazitali za kulimbana pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera. Timawerenganso, kenaka, ndi chikondwerero chachikulu, popeza tikuphunzira zochitika zomwe zidzachitika mtsogolo posachedwapa. Kufikira tsopano, kusinthana mu mphamvu pa chochitika cha tsiku kwatsogolera ku zochitika zowonjezereka mkuzindikiritsa mafumu awiriwo. Kuyambira pa kugwetsedwa kwamphamvu ya Nazi-Fascist kumapeto kwa Nkhondo ya Dziko II, tachitira umboni udani pakati pa mphamvu ziŵriri zazikulu, imodzi yoimiridwa ndi mfumu ya kumpoto, yolamulira makamaka mbali ya mitundu ya chisosholizimu, ndipo ina yoimiridwa ndi mfumu ya kum’mwera, yolamulira mokulira mbali ya chikapitalizimu.
14. Longosolani mbali za zochitika za dziko kuyambira 1914 zomwe zinanenedweratu ndi m’ngelo mu mawu a ulosi kwa Danieli.
14 Mkhalidwe wa Mfumu yomalizira ya kumpoto walongosoledwa bwino mu maversi 37, 38: “Ndipo sidzasamalira milungu ya makolo ake, . . . koma m’malo mwake idzachitira ulemu mulungu wa malinga, ndi mulungu amene makolo ake sanamudziwa, adzamulemekeza ndi golidi, ndi siliva, ndi miyala ya mtengo wake, ndi zinthu zofunika.” Kodi aliyense angalephere kuzindikira kulongosola kumeneku? Mfumu ya kumpoto ya lerolino mwalamulo imapititsa patsogolo kusakhulupirira kukhalako kwa Mulungu, kukana milungu ya chipembedzo ya mafumu a kumbuyoko a kumpoto. Iye amakonda kudalira mu zida za nkhondo, “mulungu wa malinga.” Ichi chaperekako ku mpikisano wochititsa mantha wa zida za nkhondo kaamba ka umene mafumu awiri ayenera kugawana thayo. Ndalama zowonongedwa za chitetezero za chaka ndi chaka za mfumu ya kumpoto yokha zinafika chifupifupi madola mabiliyoni 300 mu 1985. Ndi nsembe yokulira chotani nanga ya ‘golidi ndi siliva ndi miyala ya mtengo ndi zinthu zofunika’ kwa mulungu wosafunika wa zida za nkhondo!
15, 16. (a) Kodi ndimotani mmene zinthu zidzachitikira pakati pa mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera? (b) Kodi nchiyani chimene icho chidzatanthauza kwa anthu a Mulungu?
15 Chotero, kodi nchiyani chimene pomalizira chikuchitika pakati pa mafumu awiri amenewa? M’ngeloyo akunena: “Ndipo nthawi yotsirizira [mapeto a mbiri ya mafumu awiri] mfumu ya kum’mwera idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kabvulumvulu, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m’maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.” (Danieli 11:40; Mateyu 24:3) Mwachiwonekere, misonkhano siiri yankho ku udani wamphamvu zazikulu. Kukwinjika kopangidwa ndi ‘kukankha’ kwa mfumu ya kum’mwera ndi kufutukuka kwa mfumu ya kumpoto kungapite kupyolera mu magawo amphamvu ochuluka kapena ochepera koma kenaka, m’njira ina yake, mfumu ya kumpoto idzaputidwa mu kuchititsa mchitidwe wachiwawa chowopsya wolongosoledwa ndi Danieli.d
16 Masiku otsiriza amenewa ali ovuta mwapadera kwa anthu a Mulungu, amene mkati mwa zana lino akhala akuzunzidwa ndi mafumu onse awiri. M’ngeloyo anachenjeza kuti mfumu ya kumpoto “idzalowa m’dziko Lokometsetsa ndipo kudzakhala maiko ambiri amene adzakhumudwa nalo.” “Dziko Lokometsetsa” limenelo limaimira dziko la anthu a Mulungu. Ndiye kuti, mawu a m’ngelo ayenera kutanthauza kuti, limodzi ndi kugonjetsa mitundu yambiri, mfumu ya kumpoto idzaukira mkhalidwe wauzimu wa anthu a Yehova. (Danieli 8:9; 11:41-44; Ezekieli 20:6) Mu versi 45, ulosiwo ukuwonjezera: “Ndipo adzamanga mahema a nyumba yachifumu yake pakati pa nyanja yamchere ndi phiri lopatulika lofunika.” M’mawu ena, iye akudzikhazikitsa iyemwini kuti apange kuukira komalizira motsutsana ndi paradaiso wawo wauzimu.
“Adzafikira Chimaliziro Chake”
17. Kodi ndi chochitika chosayembekezereka chotani chimene chidzakwiyitsa mfumu ya kumpoto?
17 Koma pofika nthawi imeneyo chinachake chidzakhala chitachitika kale chimene mfumu ya kumpoto osatinso mfumu ya kum’mwera inawoneratu. M’ngelo analosera: “Koma mbiri yochokera kum’mawa ndi kumpoto idzamvuta [mfumu ya kumpoto]; nadzatuluka iye ndi ukali waukulu kupha ndi kuwononga konse ambiri.’’—Danieli 11:44.
18. (a) Kodi ndi ati omwe ali magwero a “mbiri” zonenedweratu ndi m’ngelo? (b) Kodi nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo chomalizira kwa mfumu ya kumpoto?
18 “Kodi nchiyani chimene mbiri imeneyi idzakhala? M’ngeloyo sakulankhula mwachindunji, koma iye akuvumbula magwero ake. Izo zidzachokera “kum’mawa,” ndipo Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu akuyerekezeredwa kukhala “mafumu ochokera kotuluka dzuwa.” (Chivumbulutso 16:12) Mbiri imeneyi ikubweranso “kuchokera kumpoto,” ndipo Baibulo limalankhula mophiphiritsira za Phiri la Ziyoni, mudzi wa Mfumu yaikulu Yehova, kukhala “kumbali zake za kumpoto.” (Masalmo 48:2) Chotero, iri “mbiri” yochokera kwa Yehova ndi Yesu Kristu yomwe idzatumiza mfumu ya kumpoto pa ndawala yake yomalizira yaikulu. Koma zotulukapo zake zidzakhala zosakaza kwa iye. Kothera kwa versi 45 kukutiuza ife: “Koma adzafikira chimaliziro chake wopanda wina wakumthandiza.”
19. (a) Kodi ndi ziti zomwe zidzakhala zotulukapo zosiyana kaamba ka dziko iri ndi kaamba ka “olungama”? (b) Kodi ndi mafunso otani amene atsala kuti ayankhidwe?
19 Indedi, sipadzakhala “mtendere . . . kwa oipa.” (Yesaya 57:21) M’malo mwake, mbiri ya mfumu ya kumpoto idzakhala yozindikiridwa ndi nkhondo kufikira kumapeto. Koma kwa atumiki Ake okhulupirika, Yehova akulonjeza: “Pakuti owongoka mtima adzakhala m’dziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzazulidwamo.” (Miyambo 2:21, 22) Ngakhale kuli tero, nchiyani, chimene chidzachitika kwa mfumu ya kum’mwera pamene mfumu ya kumpoto ‘idzafikira chimaliziro chake’? Nchiyani chimene chidzachitika kwa Akristu pamene mfumu ya kumpoto ‘idzamanga mahema ake’ m’mkhalidwe wowopsya motsutsana ndi iwo? (Danieli 11:45) Kodi ndimotani mmene potsirizira mtendere udzafikira padziko lapansi? Yehova, kupyolera mwa m’ngelo wake, wayankha mafunso amenewo, monga mmene tidzawonera mu nkhani zotsatira.
Mawu a M’munsi
a Kaamba ka tsatanetsatane wochuluka, onani mu bukhu la “Your Will Be Done on Earth,“ mutu 10, lofalitsidwa mu 1958, ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka pa gawo ili laulosi, onani “Your Will Be Done on Earth.” mutu 11.
c Zindikirani, kachiŵririnso, kuti mu versi 35 “nthaŵi yotsiriza,” ikunenedwa kukhala idakali kutsogolo.
d Onani “Your Will Be Done on Earth,” masamba 298-303.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi ndi mbali ziti za mzimu zomwe zaphatikizidwa mu zochitika za ndale za anthu?
◻ Kodi ndi ndani amene anali mfumu a kumpoto ndi mfumu ya um’mwera mu 1914?
◻ Kodi ndimotani mmene mfumu ya kumpoto ya lerolino imalambirira mulungu wa malinga?
◻ Kodi ndi chitsenderezo chotani chimene chidzabweretsedwa pa anthu a Mulungu ndi mfumu ya kumpoto?
◻ Kodi nchiyani chimene pomalizira chidzachitika kwa mfumu ya
[Mapu/Chithunzi patsamba 12]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
The Great Sea
Syria
Judea
Egypt
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
U.S. National Archives