Mikaeli Kalonga Wamkulu Aimirira
“Ndipo mkati mwa nthawi imeneyo Mikaeli adzaimirira, kalonga wamkulu amene akuimira ana a anthu a mtundu wako.’’—danieli 12:1, NW.
1. Kodi ndi njira ya mtsogolo ya zochitika za dziko yotani imene ikuwonedweratu mu Baibulo, ndipo kodi ndi funso lotani limene limabuka ponena za anthu a Mulungu chifukwa cha ichi?
YEHOVA wapereka chenjezo labwino: Sipadzakhala nkomwe mtendere padziko lapansi ngati mkangano pakati pa mfumu ya kumpoto ndi ya kum’mwera upitirira. Mphamvu ziwiri zimenezi nthawi zonse zidzakhala ndi zikondwerero zowombana. Ndiponso, pachimake pa udani wawo, mfumu ya kumpoto idzawopsyeza mkhalidwe wauzimu wa anthu a Mulungu ‘asanafike kumapeto ake.’ (Danieli 11: 44, 45) Kodi anthu a Mulungu adzapulumuka chiwopsyezocho? Ndipo nchiyani chimene chichitika kwa mfumu ya kum’mwera pamene mdani wake wamkulu afika ku mapeto ake?
2, 3. (a) Kodi ndi ulosi wotani umene tikuupeza mu bukhu la Ezekieli umene umatithandiza ife kumvetsetsa ulosi wonena za mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera? (b) Molingana ndi ulosi wa Ezekieli, kodi nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo cha kuukira kwakukulu komalizira pa anthu a Mulungu?
2 Ulosi wa mnzake wa Danieli Ezekieli umatithandiza ife kuyankha mafunso amenewa. Ezekieli nayenso, anauziridwa kulankhula ponena za “mbali ya mapeto ya masiku,” ndipo iye anachenjeza za kuukiridwa kwa ‘Gogi wa Magogi’ motsutsana ndi tsiku la anthu a Mulungu. (Ezekieli 38:2, 14-16; Danieli 10:14) Mu ulosi umenewo, Gogi akuimira Satana, ndipo khamu lake likuimira athenga onse a padziko lapansi a Satana omwe adzapanga kuyesera komalizira, kosaphula kanthu kwakutha psyiti anthu a Mulungu. Popeza kuukira kumeneku, monga kuja kwa mfumu ya kumpoto, kumachitika mu mbali ya mapeto a masiku, chiri chanzeru kumaliza kuti ‘kudzala kwa mahema a mfumu ya kumpoto pakati pa nyanja yaikulu ndi phiri loyera la chikometsero’ kuli m’kuchirikiza kuukira kwa Gogi. (Danieli 11:40, 45) Kodi kuukira kumeneku kudzapambana?
3 Ezekieli analosera: ‘“Ndipo kudzachitika tsiku ilo, tsiku loti Gogi adzadza kulimbana ndi dziko la Israyeli,’ ati Ambuye Yehova, ‘ukali wanga udzakwera m’mphuno mwanga. Ndipo ndidzalimbana naye ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mbvumbi waukulu, ndi matalala akulu, moto ndi sulfure.’” (Ezekieli 38:18, 22) Ayi, kuukira kumeneko sikudzapambana. Akristu owona adzapulumutsidwa, ndipo khamu la Gogi lidzawonongedwa.—Ezekieli 39:11.
4. Kodi mfumu ya kum’mwera idzapulumuka mapeto a mfumu ya kumpoto? Kodi ndi maulosi ena ati amene akuchirikiza yankho limeneli?
4 Mwachiwonekere, ndiyeno, nthawi yamapeto ya mfumu ya kumpoto iri nthawi ya mapeto ya Gogi ndi khamu lake, kuphatikizapo mfumu ya kum’mwera. Ichi chimagwirizana ndi maulosi ena onse a mu bukhu la Danieli. Mwachitsanzo, timawerenga kuti pambuyo pa kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu, iwo “udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse [kuphatikizapo ponse pawiri mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera], nudzakhala chikhalire.” (Danieli 2:44) Ndiponso, mu masomphenya a Danieli a nkhosa yamphongo ndi tonde, mphamvu ya ndale zadziko ya Anglo-America ikuimiridwa ndi nyanga yaing’ono. Nyanga yaing’ono imeneyi, “mu nthawi yotsiriza ya ufumu wawo,” ikuwonongedwa ndi mthenga wamphamvu yoposa ya munthu, osati ndi mfumu ya kumpoto: “Adzathyoledwa mopanda manja [a munthu].”—Danieli 7:24-27; 8:3-10, 20-25.
Mikaeli Kalonga Wamkulu
5. Kodi ndani amene adzakhala Mthenga Wamkulu wa Yehova kaamba ka chipulumutso cha anthu Ake, ndipo nchifukwa ninji ichi chiri choyenera?
5 M’ngeloyo kenaka akuvumbulutsa mthenga amene Yehova adzagwiritsira ntchito mkukwaniritsa mapeto a mphamvu zonsezo. Iye akuti: “Ndipo mkati mwa nthawi imeneyo Mikaeli adzaimirira, kalonga wamkulu amene akuimira ana a anthu a mtundu wako. Ndipo padzakhaladi nthawi ya chisautso imene sinachititsidwe kukhalako yotero kuyambira pamene kunakhala mtundu kufikira panthawi imeneyo. Ndipo mkati mwa nthawi imeneyo anthu a mtundu wako adzapulumuka, munthu aliyense amene akupezedwa atalembedwa mu bukhu.” (Danieli 12:1, NW) Kumayambiriro kwa ulosi wa m’ngelo, Mikaeli anasimbidwa monga akumenyera nkhondo a Israyeli motsutsana ndi kalonga wa Perisiya ndi Girisi. (Danieli 10:20, 21) Tsopano, pamene ulosiwo ukufika ku mapeto, Mikaeli mmodzimodziyo “akuimirira” kaamba ka anthu a Danieli. Kodi ndani ameneyo amene ali ngwazi ya anthu a Mulungu?
6, 7. (a) Malinga ndi ophunzira ena a Chipembedzo Chadziko, kodi ndani amene ali Mikaeli? (b) Ndi umboni wa Baibulo uti umene umatithandiza kupanga kuzindikiritsa koyenerera kwa Mikaeli?
6 Kubwerera kumayambiriro a 1800, wophunzira Baibulo Joseph Benson ananena kuti kulongosoledwa kwa Mikaeli kopezeka mu Baibulo “mwachiwonekere kumaloza ku Mesiya.” Lutheran wa mu zana la 19 E. W. Hengsten-berg anavomereza kuti “Mikaeli sali wina kuposa Kristu.” Mofananamo, wophunzira maphunziro a chipembedzo J. P. Lange, pamene anali kuchitira ndemanga pa Chivumbulutso 12:7, analemba: “Tikuchitenga icho kuti Mikaeli . . . ali, kuyambira pa chiyambi, Kristu mu mkhalidwe wonga wankhondo kutsutsana ndi Satana.” Kodi Baibulo limachirikiza chizindikiritso chimenecho? Inde, ilo limatero.a
7 Mwachitsanzo, molingana ndi m’ngelo, Mikaeli ayenera “kuimirira.” Mu ulosi wa m’ngeloyo, “kuimira” kapena “kuimirira” (Chihebri, ‛a·madhʹ) kungatanthauze “kupereka chirikizo.” (Danieli 11:1) Iko mwachiwonekere kungatanthauzenso “kupambana,” kuukira,” “kutsutsa,” kapena “kupirira.” (Danieli 11:6, 11, 14, 15, 16a, 17, 25) Koma kawirikawiri kumalozera kukachitidwe ka mfumu, kaya kutenga mphamvu yake ya ufumu kapena kuchita mokhutiritsa mkuthekera kwake monga mfumu. (Danieli 11:2-4, 7, 16b, 20, 21, 25) Ili ndi tanthauzo lomwe limayenera bwino mawu a m’ngelo mu Danieli 12:1. Ndipo mwachiwonekere limachirikiza chenicheni chakuti Mikaeli ali Yesu Kristu, popeza Yesu ali Mfumu yosankhidwa ya Yehova, yopatsidwa kuwononga mitundu yonse pa Armagedo. (Chivumbulutso 11:15; 16:14-16; 19:11-16) Chimagwirizananso ndi maulosi ena omwe amaloza kunthawi pamene Ufumu wa Mulungu, pansi pa Yesu Kristu, umachita motsutsana ndi mitundu yadziko iri.—Danieli 2:44; 7:13, 14, 26, 27.
8, 9. (a) Kodi ndi ndani amene poyambirira anali ‘anthu a Danieli’, ndipo kodi ndani amene ali atsopano? (b) Kodi ndimotani mmene chikondwerero chenicheni cha Mikaeli mwa ‘anthu a Danieli’ chasonyezedwera mkati mwa mibadwo?
8 Mikaeli kwanthawi yaitali wakhala wogwirizana ndi ‘anthu a Danieli,’ a Israyeli. Iye anali ndi iwo mu chipululu, ndipo iye anawachirikiza iwo motsutsana ndi mzimu wa “akalonga” a maulamuliro akale. (Danieli 10:13, 21; Eksodo 23:20, 21; Yuda 9) Ndipo iye anabadwa padziko lapansi monga munthu Yesu kukhala Mesiya woyembekezeredwa kwanthawi yaitali, “mbewu” yolonjezedwa kwa kholo la Danieli Abrahamu. (Genesis 22:16-18; Agalatiya 3:16; Machitidwe 2:36) Mwachisoni, Israyeli wachibadwa anamukana Yesu; chotero, Yehova anawakana iwo monga mtundu wapadera. (Mateyu 21:43; Yohane 1:11) Iye anakonzekera kuika dzina lake pa mtundu watsopano “Israyeli wa Mulungu” wopangidwa ponse pawiri ndi Ayuda achibadwa ndi omwe sanali Ayuda omwe anaika chikhulupiriro mwa Yesu.—Agalatiya 6:16; Machitidwe 15:14; 1 Petro 2:9, 10.
9 Mtundu watsopano umenewu, mpingo wodzozedwa Wachikristu, unayamba moyo mu 33 C.E., ndipo pambuyo pake unatumikira monga Israyeli wa Mulungu. Umenewu chotero ukakhala ‘anthu a Danieli.’ (Aroma 2:28, 29) Asanaukitsidwe kupita kumwamba mu 33 C.E. Yesu analonjeza chirikizo lowonjezereka kaamba ka ‘anthu a Danieli’ pamene iye ananena ponena za ziyembekezo za ziwalo za Israyeli watsopano ameneyo: “Onani! ine ndiri pamodzi ndi inu masiku onse, kufikira chimaliziro cha nthawi ya pansi pano.”—Mateyu 28:20; Aefeso 5:23, 25-27.
“Kuimira” Kaamba ka Anthu a Danieli
10. Malinga ndi mawu am’ngelo kwa Danieli, kodi ndimotani mmene Mikaeli akachitirapo kanthu mosankha, ndipo kodi ndi mafunso otani amene ichi chimadzutsa?
10 Koma tsopano m’ngeloyo akunena kuti Mikaeli akachitapo kanthu m’njira yapadera. Kugwiritsira ntchito liwu lakuti ‘kuimira’ kawiri, iye akuti: “Ndipo mkati mwa nthawi imeneyo Mikaeli adzaimira, kalonga wamkulu yemwe akuimira ana a anthu a mtundu wako.” (Danieli 12:1, NW) Kodi chimatanthauzanji kuti Yesu ‘akuimirira’? Ndipo kodi ndimotani mmene iye “akaimirira” ngati iye kale lomwe “akuimira anthu a [Danieli]”? Tisanayankhe mafunso amenewa, lingalirani chidziwitso china chapoyambirira
11. Ndimwanjira yotani mmene chingakhalire choyenera kunena kuti Yesuwakhala “akuimirira” kuyambira 1914?
11 Pambuyo pakuukitsidwa kwake mu 33 C.E.,Yesu anauza otsatira ake:“Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Yesu kwanthawi yaitali anakhala akusonyeza mphamvu yoteroyo pa atumiki ake odzozedwa padziko lapansi. (Akolose 1:13) Komabe, nthawi inali isanafike kaamba ka Yesu kusonyeza mphamvu monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. M’malo mwake, pambuyo pa kukwera kwake kumwamba iye ‘anakhala ku dzanja lamanja la Mulungu kumwamba’ kufikira nthawi ya kukhazikitsidwa kwa Ufumu umenewo. (Masalmo 110:1 , 2; Machitidwe 2:34, 35) Nthawi imeneyo inabwera mu 1914, “nthawi yoikika.” (Danieli 11:29) M’chaka chimenecho, Yesu anakhazikitsidwa monga Mfumu yolamulira ya Ufumu wa Mulungu ndipo mwamsanga, monga Mikaeli ndi m’ngelo wamkulu—anachotsa Satana kumwamba. (Chivumbulutso 11:15; 12:5-9)Chotero kuyambira 1914 Yesu wakhala “akuimirira” monga Mfumu.—Masalmo 2:6.
12, 13. Kodi ndi madalitso owonekera otani amene anthu a Mulungu asangalala nawo mkati mwa zaka kuyambira 1914, kusonyeza kuti Yesu wakhala ‘akuimira anthu a Danieli’?
12 “Kuimirira” kwa Yesu kwakhala dalitso lalikulu kwa ‘ana a anthu a Danieli.’ Kutenga kwake kwa mphamvu ya ufumu ndi kuchotsa Satana kupita kudziko lapansi kunayeretsa nyumba yawo ya mtsogolo ya kumwamba. (Yohane 14:2, 3) Pambuyo pake, awo amene anali atafa kale mu chikhulupiriro angaukitsidwe ku choloŵa chawo cha kumwamba. (1 Atesalonika 4:16, 17) Otsalira a iwo amene adakali padziko lapansi anavutika ndi kuzunzidwa koipa mkati mwa nkhondo yoyamba ya dziko, yomwe chifupifupi inaimitsa ntchito yawo yolalikira. Koma mu 1919 iwo anapatsidwanso mphamvu ndi kubweretsedwa pa chiwonekero chadziko monga mtundu watsopano.—Yesaya 66:7, 8; Chivumbulutso 9:14; 11:11, 12.
13 Pambuyo pachimenecho, Yesu anakwaniritsa lonjezo lake la “kusonkhanitsa pamodzi ndi kuchotsa mu ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusayeruzika.” (Mateyu 13:41) M’njira imeneyi, iye wasunga mpingo woyera wa Akristu odzozedwa omwe ‘adziwa Mulungu wawo, apita patsogolo, ndipo achita mokhutiritsa.’ Iwo alalikira mbiri yabwino ya Ufumu kuzungulira padziko lonse lapansi, chotero ‘kupereka kumvetsetsa kwa ambiri.’ (Danieli 11:32, 33; Mateyu 24:14) Kuyambira 1935 Yehova walumikiza ku mpingo umenewu chiwerengero chomakulakula cha “nkhosa zina,” zomwe zimasangalatsidwa ndi chiyembekezo cha padziko lapansi ndi zomwe mokhulupirika zakhala zikugawana mu ntchito ya kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Muhmgu.—Yohane 10:16; Chivumbulutso 7:9, 14, 15.
14. Kodi nchiyani chomwe chakhala chotuluka o cha ‘kuimirira kaamba ka anthu a Danieli’ wa Yesu kupyolera mu masiku omaliza?
14 Kukhalapo kwenikweni kwa gulu limeneli la Akristu lerolino kwakhala kotsimikizirika. Mu dziko logawanika mwa ndale, iwo asunga uchete weniweni monga nzika za Ufumu wa Mulungu. (Yohane 17:14) Monga chotulukapo chake, iwo avutika ndi kuzunzidwa pamanja a maufumu onse awiri. Chipembedzo chonyenga, nachonso, chapangana ndi kupanga chiwembu kuti iwo afafanizidwepo. M’malo mwa kuchitika chimenecho, iwo apita patsogolo ndipo lerolino akupezeka mu maiko oposa 200 ndi chiwerengero choposa mamiliyoni atatu cha anthu okhulupirika. Iwo amasangalala ndi paradaiso wauzimu pansi pa ulamuliro wa Kristu yemwe ali wosiyana kwambiri ndi mdima ndi kutsenderezedwa kwa dziko iri. (Yesaya 65:13, 14) Chotero, Yesu wakhala “akuimira ana a anthu [a Danieli]” mkati mwa masiku ano onse amapeto.—Danieli 12:1.
Mikaeli ‘Aimirira’
15. Kodi ndi m’njira yotani mmene Yesu “wa imirira” ndipo ndi liti pamene ichi chikuchitika?
15 Chotero, kodi ndimotani kuti Yesu, yemwe ‘‘akuimirira” kale, ‘aimirira’ panthaŵi imeneyo? (Danieli 12:1) M’chakuti ulamuliro wake uli wa mu gawo latsopano, monga mmene kunaliri. Iri nthaŵi kwa iye kuchitapo kanthu m’njira yowonekera kwambiri kupulumutsa ‘anthu a Danieli’ kuchokera ku kuwonongedwa ndi manja a maboma a anthu. (Ezekieli 38:18, 19) “Nthaŵi” yolozedwa pano iri mwachiwonekere “nthawi ya mapeto” a mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera, pamene mfumu ya kumpoto iwopsyeza mkhalidwe wauzimu wa anthu a Mulungu. (Danieli 11:40-45) Isanafike nthawi imeneyi, ulamuliro wa Yesu wakhala utatengedwa mosamalitsa kokha ndi nzika zokhulupirika za padziko lapansi. (Masalmo 2:2, 3) Tsopano, ngakhale kuli tero, iri nthaŵi ya “kuvumbulutsidwa kwa Ambuye Yesu,” pamene aliyense adzakakamizidwa kuzindikira ufumu wake. (2 Atesalonika 1:7, 8) Ichi chidzaphatikizapo kuwonongedwa kwa mphamvu zonse zotsutsa, kutsatiridwa ndi Zaka Zaulamuliro wa Zaka Chikwi wa Yesu ndi olamulira anzake, pamene Ufumuwo udzakhala boma limodzi lokha pa mtundu wa anthu.—Chivumbulutso 19:19-21; 20:4.
16. Kodi nchiyani chimene chiri chotulukapo cha ‘kuimirira’ kwa Yesu kwa anthu opanda umulungu?
16 M’chigwirizano ndi ichi, m’ngeloyo akunena kuti pamene Mikaeli adzaimirira, “padzakhaladi nthawi ya chisautso imene sinachititsidwe kukhalako yotero kuyambira pamene kunakhala mtundu kufikira panthaŵi imeneyo.” (Danieli 12:1; yerekezani ndi Mateyu 24: 21. ) Idzakhala nthawi ya chiwonongeko kwa oipa ndi chipulumuko kwa okhulupirika. (Miyambo 2:21, 22) Mvetserani ku chivomerezo cha kuchititsidwa mantha kwa mtundu wa anthu osakhulupirika pa nthawi imeneyo: “Nanena kwa mapiri ndi matanthwe: ‘Igwani pa ife, ndipo tibiseni ife ku nkhope ya iye amene akhala pa mpando wachifumu, ndi ku mkwiyo wa Mwanawankhosa, chifukwa lafika tsiku lalikulu la mkwiyo wawo, ndipo akhoza kuima ndani?’ ”—Chivumbulutso 6:16, 17.
17. Kodi nchiyani kenaka chimene chidzachitika ku magulu amphamvu a padziko lapansi a Satana, kuphatikizapo mfumu ya kumpoto ndi mfumu ya kum’mwera?
17 Chotulukapo cha “nthaŵi ya chisautso” imeneyi pa magulu a Satana a padziko lapansi chalongosoledwa mu ulosi wa Ezekieli motsutsana ndi Gogi wa Magogi: “Udzagwa pa mapiri a Israyeli, iwe ndi magulu ako onse, ndi mitundu ya antHu okhala ndi iwe; ndidzakupereka kwa mbalame zolusa za mitundu yonse, ndi kwa zirombo za kuthengo, akuyese chakudya.” (Ezekieli 39:4) Yeremiya, akulankhula ponena za nthaˆi imodzimodziyo ya nsautso, anati: “Ndipo akuphedwa a Yehova adzakhala tsiku lomwelo kuchokera ku malekezero ena a dziko lapansi kunka ku malekezero ena a dziko lapansi.” (Yeremiya 25:33) Idzakhaladi nthaŵi ya chisautso. Yesu adzamaliza mbiri yaitali ya nkhondo ya anthu pamene ‘adzaimirira’ kuchotsa mphamvu za anthu zomwe ziri ndi thayo.—Masalmo46:9; 1 Akorinto 15:25.
Opulumuka a “Nthawi ya Nsautso”
18. (a) Kodi nchiyani chimene chidzakhala chokumana nacho cha alambiri owona pamene Mikaeli ‘adzaimirira’? (b) Kodi nchiyani chimene chimatanthauza kukhala “olembedwa m’bukhu”?
18 Pamene kuli kwakuti anthu a Mulungu adamva zotulukapo za udani wa mdani, iyi idzakhala “nthawi ya nsautso” makamaka kwa oipa. (Masalmo 37:20) M’ngeloyo anauza Danieli: “Ndipo mkati mwanthaŵi imeneyo anthu a mtundu wako adzapulumuka, munthu aliyense wakupezedwa atalembedwa m’bukhu.” (Danieli 12:1) Ambiri a “ana a anthu a Danieli” adzakhala atafa ndi kulandira mphatso yawo ya kumwamba kufika nthawi imeneyo. Awa mosakaikira adzagawana ndi Mikaeli mu chipambano chachikulu cha nkhondo chimenechi. (Chivumbulutso 2:26, 27; Masalmo 2:8, 9) Awo amene atsalira padziko lapansi sadzagawana nawo mu kumenyana kumeneku; koma iwo adzakhala asungiliri aumphumphu, chotero adzakhala opulumuka. (Chivumbulutso 17:14; 19:7, 8) Oyanjana nawo awo a “khamu lalikulu,” nawonso adzakhala opulumuka. (Chivumbulutso 7:9, 14) Koma otsalira odzozedwa ndi “ankhosa zina” mwakutero adzatsimikizira kukhala “opezeka olembedwa m’bukhu,” kunena kuti mama awo adzakhala mu zolembera kukhala mu mzera wa kulandira moyo wosatha, kaya kumwamba kapena padziko lapansi.—Yohane 10:16; Eksodo 32:32, 33; Malaki 3: 16; Chivumbulutso 3:5.
19. (a) Kodi ndimotani mmene ‘kuimirira’ kwa Mikaeli kukabweretsera mtendere padziko lapansi? (b) Kodi ndi funso lotani limene latsala kuti liyankhidwe?
19 Awa adzapatsidwa mwaŵi wa kuwona kukhazikitsidwa kwa mtendere weniweni wa padziko lonse lapansi. Iwo adzachitira umboni kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova: “Pakuti ochita zoipa adzadulidwa, koma iwo akuyembekeza Yehova, iwowa adzalandira dziko lapansi.” (Masalmo 37:9) Chifukwa chakuti Ufumu wa Mulungu panthawiyo udzakhala boma lenileni pa dziko lapansi, munthu aliyense wa moyo adzakhala mtumiki wa Yehova. (Yesaya 11:9) Chotero, “panthaŵi ya mapeto”a mafumu awiri, Mikaeli “adzaimirira” kubweretsa mtendere kwa mtundu wa anthu. Palibe mphamvu yaikulu ya zida yomangidwa kapena machitidwe ena amene adzaimitsa kuchitika kumeneku. Kodi chimenecho chikutanthauza, ngakhale kuli tero, kuti tiyenera kudikira kufikira nthawi imeneyo kuti tikasangalale ndi mtendere? Ayi, pali mtendere umene Akristu akusangalala nawo ngakhale tsopano lino—ndithudi, mtendere wabwinopo woposa kusakhalapo kokha kwa nkhondo. Kodi nchiyani chimene chiri mtendere umenewu? Ulosi wa m’ngelo kwa Danieli ukupitiriza kuunikira pa ichi.
[Mawu a M’munsi]
a Popeza Mikaeli ali m’ngelo wamkulu, ena amadzimva kuti kumuzindikiritsa iye monga Yesu kumachotsa m’njira ina yake ulemu kapena thayo la Yesu. (Yuda 9) Komabe, chitsimikizo kaamba ka chizindikiritso chimenecho chinatsogoza ophunzira otchulidwa pamwambapo Achipembedzo Chadziko kuzindikira Mikaeli monga Yesu mosasamala kanthu za chenicheni chakuti iwo mwinamwake amakhulupirira mu Utatu.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Kodi ndi ndani amene ali Mikaeli Kalonga Wamkulu?
◻ Kodi ndi ndani amene ali anthu a Danieli lerolino?
◻ Kodi ndimotani mmene Mikaeli tsopano akuimira kaamba ka anthu a Danieli?
◻ Kodi ndimotani mmene Mikaeli posachedwapa adzaimirira m’njira yowonekera?
◻ Kodi ndi ndani amene adzapulumuka kuimirjra kwa Mikaeli?
[Chithunzi patsamba 16]
Kuyesera komalizira kwakuchotsa anthu a Mulungu kudzalephera—koma motani?
[Chithunzi patsamba 18]
Chipulumutso chidzabwera kwa anthu a Mulungu pamene Mikaeli ‘adzaimirira’ kuthetsa mkangano wa mafumu awiri