Danieli
11 “Mʼchaka choyamba cha Dariyo+ Mmedi, ine ndinkamulimbikitsa ndipo ndinali ngati mpanda wolimba kwambiri kwa iye. 2 Zimene ndikufotokozere panopa ndi zoona:
Mu ufumu wa Perisiya mudzakhala mafumu atatu amene adzalamulire, ndipo mfumu ya nambala 4 idzasonkhanitsa chuma chambiri kuposa ena onsewa. Ndipo ikadzangokhala yamphamvu chifukwa cha chuma chakecho, idzagwiritsa ntchito chilichonse pomenyana ndi ufumu wa Girisi.+
3 Ndiyeno mfumu yamphamvu idzayamba kulamulira ndi mphamvu zazikulu+ ndipo idzachita zofuna zake. 4 Koma mfumuyo ikadzayamba kulamulira, ufumu wake udzasweka ndipo udzagawanika nʼkutengedwa ndi mphepo 4 zakumwamba,+ koma sudzapita kwa mbadwa zake ndipo maufumuwo sadzafanana ndi ufumu wake. Zimenezi zidzachitika chifukwa ufumu wake udzazulidwa nʼkuperekedwa kwa ena.
5 Mfumu yakumʼmwera, imene ndi mmodzi mwa akalonga ake, idzakhala yamphamvu. Koma iye* adzaigonjetsa ndipo adzalamulira ndi mphamvu zazikulu kuposa za iyeyo.*
6 Pakadzatha zaka zingapo iwo adzapanga mgwirizano ndipo mwana wamkazi wa mfumu yakumʼmwera adzapita kwa mfumu yakumpoto kuti apange mgwirizano. Koma mwana wamkaziyo sadzakhalanso ndi mphamvu ndipo mphamvu za mfumuyo zidzathanso. Mwana wamkaziyo adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu ena pamodzi ndi amene anamubweretsa, amene anamubereka ndiponso amene ankamuchititsa kukhala wamphamvu masiku amenewo. 7 Kenako munthu wina wochokera ku mphukira ya mizu ya mwana wamkaziyo adzayamba kulamulira mʼmalo mwake* ndipo adzafika kwa gulu lankhondo nʼkupita kukaukira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri wa mfumu yakumpoto, moti munthuyo adzachita nayo nkhondo nʼkupambana. 8 Iye adzapita ku Iguputo ndi milungu yawo, zifaniziro zawo zachitsulo,* zinthu zawo zamtengo wapatali zasiliva ndi zagolide, pamodzi ndi anthu amene adzawagwire. Kwa zaka zingapo iye sadzalimbana ndi mfumu yakumpoto 9 imene idzapite kukaukira ufumu wa mfumu yakumʼmwera, kenako idzabwerera kudziko lakwawo.
10 Ana ake adzakonzekera nkhondo ndipo adzasonkhanitsa gulu lalikulu la asilikali. Iye adzafika mwamphamvu kwambiri nʼkudutsa mwachangu mʼdzikolo ngati madzi osefukira. Koma adzabwerera, ndipo adzachita nkhondo mpaka kumzinda wake wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.
11 Ndiyeno mfumu yakumʼmwera idzakwiya kwambiri ndipo idzapita kukamenyana ndi mfumu yakumpoto. Iye* adzakhala ndi gulu lalikulu, koma gululo lidzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu inayo. 12 Gululo lidzatengedwa ndipo iye* adzadzitukumula mumtima mwake moti adzachititsa kuti anthu masauzandemasauzande aphedwe. Iye adzakhala wamphamvu, koma sadzagwiritsa ntchito bwino mphamvu zakezo kuti zimuthandize.
13 Kenako mfumu yakumpoto idzabwerera kwawo nʼkusonkhanitsa gulu lalikulu kwambiri kuposa loyamba lija. Ndiyeno patapita nthawi yaitali, pambuyo pa zaka zingapo, mfumuyo idzabwera ndi gulu lalikulu la asilikali lokhala ndi zida zambiri. 14 Mʼmasiku amenewo anthu ambiri adzaukira mfumu yakumʼmwera.
Ndiyeno anthu achiwawa* pakati pa anthu a mtundu wako adzatengeka ndi zochitika zimenezi ndipo adzayesa kukwaniritsa masomphenya, koma adzapunthwa.
15 Kenako mfumu yakumpoto idzabwera ndipo idzamanga malo okwera omenyerapo nkhondo nʼkulanda mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Zida zankhondo zakumʼmwera* komanso asilikali ake osankhidwa mwapadera sadzatha kulimbana ndi mfumuyo. Iwo sadzakhala ndi mphamvu zoti alimbane nayo. 16 Mfumu imene idzabwere kudzamenyana nayo* idzachita zofuna zake ndipo palibe amene adzaime pamaso pake. Mfumuyo idzaimirira mʼDziko Lokongola+ ndipo idzakhala ndi mphamvu zoti nʼkupha anthu ambiri. 17 Mfumuyo idzatsimikiza mtima kuti ifike ndi gulu lonse la asilikali a ufumu wake ndipo adzachita nayo mgwirizano moti idzakwaniritsa zolinga zake. Iyo idzaloledwa kuti iwononge mwana wamkazi. Mwana wamkaziyo zinthu sizidzamuyendera bwino ndipo sadzapitiriza kukhala wokhulupirika kwa mfumuyo. 18 Idzatembenukira kumadera amʼmbali mwa nyanja ndipo idzalanda madera ambiri. Koma mtsogoleri wa asilikali adzathetsa khalidwe lake lonyoza, moti iye sadzanyozedwanso. Mtsogoleriyu adzachititsa kuti kunyozako kubwerere kwa mfumuyo. 19 Kenako idzabwerera* kumizinda yakwawo yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Kumeneko idzapunthwa nʼkugwa ndipo sidzakhalakonso.
20 Udindo wake udzatengedwa ndi wina amene adzachititse kuti wokhometsa msonkho* aziyendayenda mu ufumu waulemerero, koma mʼmasiku ochepa iye adzafa, osati chifukwa cha chiwawa kapena nkhondo.
21 Ndiyeno udindo wake udzatengedwa ndi munthu wonyozeka ndipo sadzamupatsa ulemerero waufumu. Iye adzabwera pa nthawi yamtendere* ndipo adzatenga ufumuwo mwachinyengo. 22 Iye adzagonjetsa magulu a asilikali okhala ngati madzi osefukira ndipo adzawonongedwa. Mtsogoleri+ wa pangano nayenso adzawonongedwa.+ 23 Ndipo chifukwa cha mgwirizano umene adzapange naye, iye adzachita zinthu mwachinyengo nʼkukhala ndi mphamvu pogwiritsa ntchito mtundu waungʼono. 24 Pa nthawi yamtendere,* iye adzalowa mʼmadera abwino kwambiri achigawocho ndipo adzachita zinthu zimene ngakhale makolo ake ndi makolo a makolo ake sanachitepo. Adzagawira anthu zinthu zimene zawonongedwa, zimene zalandidwa komanso katundu wosiyanasiyana. Adzakonzera ziwembu malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri, koma kwa kanthawi kochepa.
25 Iye adzasonkhanitsa mphamvu zake ndi kulimbitsa mtima wake kuti aukire mfumu yakumʼmwera ali ndi gulu lalikulu la asilikali. Mfumu yakumʼmwera nayonso idzakonzekera nkhondo ndipo idzasonkhanitsa gulu la asilikali lalikulu kwambiri komanso lamphamvu. Koma iye* sadzapambana chifukwa adzamukonzera chiwembu. 26 Anthu amene amadya zakudya zake zokoma ndi amene adzachititse kuti iye agonjetsedwe.
Gulu lake la asilikali lidzagonjetsedwa* ndipo anthu ambiri adzaphedwa.
27 Mafumu awiri amenewa adzakhala ndi mtima wofuna kuchita zoipa ndipo adzakhala patebulo limodzi nʼkumauzana zabodza. Koma zolinga zawo zonse sizidzatheka chifukwa mapeto adzafika pa nthawi yake.+
28 Choncho iye* adzabwerera kudziko lakwawo ali ndi katundu wochuluka ndipo adzakhala ndi mtima wofunitsitsa kuukira pangano lopatulika. Iye adzakwaniritsa zolinga zake nʼkubwerera kwawo.
29 Pa nthawi imene inaikidwiratu iye adzabweranso ndipo adzaukira mfumu yakumʼmwera. Koma sizidzakhala ngati mmene zinalili poyamba, 30 chifukwa sitima zapamadzi za ku Kitimu+ zidzabwera kudzamuukira ndipo adzachititsidwa manyazi.
Iye adzabwerera kwawo ndipo adzalankhula mawu amphamvu odzudzula* pangano lopatulika+ moti adzakwaniritsa zolinga zake. Adzabwerera kwawo ndithu ndipo adzayamba kuganizira za anthu amene akusiya pangano lopatulika. 31 Ndiyeno magulu a asilikali ake* adzachitapo kanthu* ndipo adzaipitsa malo opatulika,+ malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri komanso adzachotsa nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse.+
Iwo adzaika pamalowo chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko.+
32 Anthu amene amachita zinthu zoipa zotsutsana ndi pangano adzawachititsa kuti ayambe mpatuko pogwiritsa ntchito mawu achinyengo. Koma anthu amene amadziwa Mulungu wawo adzapambana ndipo adzakwaniritsa zolinga zawo. 33 Anthu ozindikira+ pakati pa anthuwo adzathandiza anthu ambiri kuti amvetse zinthu. Kwa masiku angapo iwo adzapunthwa chifukwa cha lupanga, malawi a moto, kutengedwa ukapolo komanso chifukwa cha kuwonongedwa kwa zinthu zawo. 34 Koma akadzapunthwa adzapatsidwa thandizo lochepa, ndipo anthu ambiri adzakhala kumbali yawo pogwiritsira ntchito mawu achinyengo. 35 Ena mwa anthu ozindikirawo adzapunthwa. Zidzakhala choncho kuti ntchito yoyenga ichitike chifukwa cha iwowo ndiponso kuti anthu ozindikira atsukidwe ndi kuyeretsedwa+ mpaka nthawi ya mapeto, chifukwa mapetowo adzafika pa nthawi yake.
36 Mfumuyo idzachita zofuna zake ndipo idzadzikweza ndi kudzikuza kuposa mulungu aliyense. Iyo idzalankhula zinthu zodabwitsa zotsutsana ndi Mulungu wa milungu.+ Mfumuyo idzapambana mpaka nthawi ya mkwiyo itatha, chifukwa zimene Mulungu wakonza ziyenera kuchitika. 37 Mfumu imeneyi sidzalemekeza Mulungu wa makolo ake. Sidzaganiziranso zofuna za akazi kapena za mulungu wina aliyense koma idzadzikweza pamwamba pa aliyense. 38 Idzapereka ulemu kwa mulungu amene amalemekezedwa mʼmalo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Idzapereka ulemu kwa mulungu amene makolo ake sanamudziwe. Idzachita zimenezi popereka kwa mulunguyo golide, siliva, miyala yamtengo wapatali ndi zinthu zamtengo wapatali. 39 Mfumuyo idzakwaniritsa zolinga zake polimbana ndi malo otetezeka kwambiri okhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo idzachita zimenezi pamodzi ndi* mulungu wachilendo. Onse amene ali kumbali yake idzawapatsa* ulemerero waukulu ndipo idzachititsa kuti anthu oterowo alamulire pakati pa anthu ambiri. Idzagawa malo kwa munthu aliyense amene adzalipire.
40 Mu nthawi yamapeto mfumu yakumʼmwera idzayamba kukankhana* ndi mfumu yakumpoto ndipo mfumu yakumpotoyo idzabwera mwamphamvu kudzamenyana nayo. Idzabwera ndi magaleta, asilikali okwera pamahatchi ndi sitima zambiri zapamadzi ndipo idzalowa mʼmayiko nʼkudutsamo mofulumira ngati madzi osefukira. 41 Idzalowanso mʼDziko Lokongola+ ndipo idzachititsa kuti mayiko ambiri apunthwe. Koma Edomu, Mowabu ndi mbali yaikulu ya Aamoni adzapulumuka mʼmanja mwake. 42 Mfumuyo idzapitiriza kutambasula dzanja lake kuti izilamulira mayiko ndipo dziko la Iguputo silidzapulumuka. 43 Idzalamulira chuma chobisika cha golide ndi siliva komanso zinthu zonse zamtengo wapatali za Iguputo. Anthu a ku Libiya ndi a ku Itiyopiya adzamutsatira.
44 Koma malipoti ochokera kumʼmawa* ndi kumpoto adzaisokoneza ndipo idzapita ndi mkwiyo waukulu kukafafaniza ndi kuwononga ambiri. 45 Ndipo mfumuyo idzamanga matenti achifumu pakati pa nyanja yaikulu ndi phiri lopatulika la Dziko Lokongola.+ Ndiyeno pamapeto pake mfumuyo idzawonongedwa ndipo sipadzapezeka woithandiza.”