Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Hoseya 1:1–14:9
Yehova Mulungu Wathu Ali Wachifundo
YEHOVA ali “Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni, wolekereza, ndi wochuluka chifundo.” (Nehemiya 9:17) Iye amamamatira ku miyezo yake yolunjika koma amaitana ochita zolakwa kulapa ndi kusangalala ndi unansi wabwino ndi iye. Ndi mwaubwino chotani nanga mmene ichi chinachitidwira chitsanzo ndi chimene Mulungu ananena kwa Aisrayeli osokera kupyolera mwa mneneri wake Hoseya!
Bukhu la Baibulo lokhala ndi dzina la Hoseya linamalizidwa ndi mneneriyo m’boma la Samariya pamapeto pa utumiki wake wautali wa zaka 59 (kuyambira chifupifupi 804 B.C.E. kufikira itapita 745 B.C.E.). Hoseya analosera mu ufumu wa mafuko khumi wa Israyeli m’masiku a Mfumu Yerobiamu II ndi olamulira a Yuda Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya. (Hoseya 1:1) Chifukwa chakuti Israyeli ananyalanyaza ziitano kaamba ka kulapa, mtunduwo unagwetsedwa ndi Asuri, ndipo mzinda waukulu wake, Samariya, unawonongedwa mu 740 B.C.E. Ngakhale kuti ulosi wa Hoseya unalunjikitsidwa kwa anthu a mazana apita, iwo uli ndi maphunziro kaamba ka ife ponena za chifundo cha Mulungu wathu, Yehova.
Njira Yosokera ya Israyeli
Yehova amapereka chifundo pa maziko a kulapa kowona mtima kwa wochimwayo. (Salmo 51:17; Miyambo 28:13) Kufunitsitsa kwa Mulungu kwa kusonyeza chifundo kwa Israyeli kunachitiridwa chitsanzo ndi zochita za Hoseya ndi mkazi wake, Gomeri. Monga momwe analamulidwa, iye anatenga “mkazi wachigololo.” Pambuyo pa kubala mwana mmodzi kwa Hoseya, Gomeri mwachiwonekere anabala ana aŵiri m’chigololo. Komabe, mneneriyo mwachifundo anatenganso mkazi wakeyo. Mofananamo, Israyeli anali monga mkazi wosakhulupirika kwa Yehova, molakwika akumapereka madalitso kwa mulungu wonama Baala. Koma Yehova anali wofunitsitsa kuwasonyeza iwo chifundo ngati analapa za chigololo chawo chauzimu.—1:1-3:5.
Ochimwa okhumba chifundo chaumulungu ayenera kutembenuka kuchoka ku njira yawo yochimwa ndi kugwirizana ndi chidziŵitso cha Mulungu. (Salmo 119:59, 66, 67) Yehova anali ndi mlandu wa lamulo motsutsana ndi nzika za Israyeli chifukwa chowonadi, chifundo, ndi chidziŵitso cha Mulungu zinali kusoweka m’dziko lawo. Popeza kuti anakana chidziŵitso, Yehova akawakana iwo. Pakayenera kukhala kuŵerengera mlandu kaamba ka Israyeli ndi Yuda olambira mafano. Koma chinanenedweratu kuti iwo akafuna Mulungu pamene akadzipeza iwo eni “m’msauko.”—4:1-5:15.
Kukolola Kavumvulu!
Ntchito zoyenera kulapa ziri zofunikira ngati ochita zolakwa akayenera kukumana ndi chifundo cha Mulungu. (Machitidwe 26:20) “Tiyeni, tibwerere kunka kwa Yehova,” anachonderera tero Hoseya. Koma chifundo cha Israyeli (wotchedwa Efraimu kaamba ka mfumu yake ya fuko) ndi Yuda anali “ngati mame akuphwa mamawa.” Anthuwo analakwira pangano la Mulungu ndipo sanatulutse zipatso zoyenera kulapa. “Ngati nkhunda yopusa yopanda nzeru,” iwo anafuna thandizo kuchokera ku Ilgupto ndi Asuri. Koma maulamuliro a ndale zadziko amenewa sakawachitira iwo chabwino koposa “uta wosakhulupirika” wosakhoza kulasa mivi pa chonulirapo.—6:1-7:16.
Kuti atute chomwe chiri chabwino, awo ofuna chifundo cha Yehova ayenera kufesa chomwe chiri chabwino. (Agalatiya 6:7, 8) Chifukwa chakuti Aisrayeli anataya chokoma, iwo anatuta choipa. ‘Abzala mphepo, nadzakolola kavumvulu.’ Mulungu “adzakumbukira mphulupulu yawo,” ndipo akatuta osati chifundo chake koma chiŵeruzo chake chowopsya. Iwo akakhala “othaŵathaŵa mwa amitundu,” mwachidziŵikire kugonjetsa kwa Asuri kukuthandizirako ku mkhalidwewo.—8:1-9:17; Deuteronomo 28:64, 65; 2 Mafumu 15:29; 17:1-6, 22, 23; 18:9-12; 1 Mbiri 5:26.
Tidzapitiriza kupindula kuchokera ku chifundo cha Mulungu kokha ngati ife tipitiriza kuyamikira zinthu zopatulika. (Ahebri 12:14-16) Aisrayeliwo analibe chiyamikiro chimenecho. M’malo mwa kufesa mbewu m’chilunjiko ndi kututa mogwirizana ndi chifundo, iwo analima choipa natuta chosalunjika. Mulungu anaitana Israyeli kutuluka mu Igupto monga mwana, koma chikondi Chake chinabwezeredwa ndi chinyengo. “Utembenukire kwa Mulungu wako, sunga chifundo ndi [chilungamo, NW],” Yehova analangiza tero. Koma Efraimu anadziloŵetsa m’kuchita choipa kwakukulu ndipo anafunikira chidzudzulo m’malo mwa chifundo.—10:1-12:14.
Bwererani kwa Yehova
Ngakhale awo amene amalakwa mokulira angabwerere kwa Yehova ndi kusonyezedwa chifundo. (Salmo 145:8, 9) Hoseya kachiŵirinso analozera ku chisamaliro chachifundo cha Mulungu kwa Aisrayeli. Ngakhale kuti mtunduwo unatembenuka motsutsana ndi Yehova, iye analonjeza kubwezeretsedwanso, akumanena kuti: ‘Ndidzawawombola ku mphamvu ya [Sheol, NW]; ndidzawawombola kuimfa.’ Samariya (Israyeli) anakayenera kulipira mtengo kaamba ka kuwukira. Koma Aisrayeli anafulumizidwa kubwerera kwa Mulungu ndi mawu owona mtima, ‘milomo ya ng’ombe zazing’ono.’ Ulosiwo unamaliza ndi lingaliro lotonthoza lakuti anzeru ndi olunjika omwe amayenda m’njira zowongoka za Yehova adzasangalala ndi chifundo chake ndi chikondi.—13:1–14:9.
Maphunziro ofunikira kukumbukira: Yehova amapereka chifundo pa maziko a kulapa kowona mtima kwa wochita cholakwayo. Koma ochimwa okhumba chifundo chake ayenera kugwirizana ndi chidziŵitso cha Mulungu ndi kutulutsa ntchito zoyenera kulapa. Iwo afunikira kufesa chomwe chiri chabwino ndipo ayenera kupitiriza kuyamikira zinthu zopatulika. Ndipo chitonthozo chingatengedwe kuchokera ku chidziŵitso chakuti ngakhale awo olakwa moipitsitsa angabwerere kwa Wam’mwambamwamba ndi chiyembekezo, popeza kuti Yehova Mulungu wathu ali wachifundo.
[Bokosi patsamba 14]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
○ 2:21-23—Yezreeli amatanthauza “Mulungu Adzafesa Mbewu.’ Yehova akasonkhanitsa otsalira okhulupirika ndi kuwafesa iwo monga mbewu mu Yuda, kumene akakhala chimanga, vinyo wokoma, ndi mafuta. M’malo mwa otsalira osowawo, zinthu zabwino zimenezi zikapempha dziko kutulutsa zinthu zofunikira ku mapesi a chimanga, mitengo ya mpesa, ndi mitengo ya azitona. Dziko lapansi likachonderera kumwamba kaamba ka mvula, ndipo iwo akafunsa Mulungu kutulutsa mtambo womwe ukapereka kugwa kwa mvula kofunikako.
○ 5:1—Ansembe ndi mafumu ampatuko a Israyeli anakhala msampha ndi ukonde kwa anthu mwa kuwanyenga iwo kudzilowetsa m’kulambira konyenga. Mwachidziŵikire, Phiri la Tabora (kumadzulo kwa Yordano) ndi Mizipa (mzinda wa kum’mawa kwa mtsinjewo) anali maziko a kulambira konyenga. Mkati mwa Israyeli yense, anthu anali kuchita kulambira mafano chifukwa cha chitsanzo choipa cha atsogoleri awo, omwe akakumana ndi chiweruzo chowopsya cha Mulungu.
○ 7:4-8—Aisrayeli achigololo anayerekezedwa ndi mophikira mkate, kapena ng’anjo, mwachiwonekere chifukwa cha zikhumbo zoipa zomatentha mkati mwawo. Chifukwa cha kusakanizana ndi mitundu mwa kutsanzira njira zawo ndi kufunafuna chigwirizano ndi iwo, Efraimu (Israyeli) anayerekezedwanso ndi mkate wozungulira wophikidwa kokha mbali imodzi.
○ 9:10—Aisrayeli ‘anadzipereka iwo eni ku chinthu chochititsa manyazi’ pamene anakhala ogwirizana ndi Baala wa ku Peori pa chidikha cha Moabu. (Numeri 25:1-5) Hoseya anagwiritsira ntchito verebu la Chihebri lotanthauza “kudzichotsa iwo eni ku; kudziika iwo eni olekanitsidwa kaamba ka.” Aisrayeli anali odzipereka kwa Mulungu koma odzipatula iwo eni kwa Baala wa ku Peori. Chochitika chimenecho chingakhale chinatchulidwa chifukwa chakuti kulambira kwa Baala kunali chimo lokulira la ufumu wa mafuko khumi. (Hoseya 2:8, 13) Lolani kuti tilabadire chenjezoli ndipo tisaswe kudzipereka kwathu kwa Yehova.—1 Akorinto 10:8, 11).
○ 10:5—Betaveni (kutanthauza “Nyumba Yopanda Pake”) inagwiritsiridwa ntchito m’lingaliro lotonza kaamba ka Beteli, lomwe limatanthauza “Nyumba ya Mulungu.” Beteli inakhala nyumba ya Mulungu koma inadzakhala nyumba yopanda pake chifukwa cha kulambira ng’ombe komwe kunali kuchitidwa kumeneko. (1 Mafumu 12:28-30) Pamene fano la ng’ombe linatengedwa ku ndende, anthuwo akachititsidwa mantha kaamba ka ilo. Fano lopanda moyolo silikanadzichinjiriza ilo lokha, mochepera koposa awo olilambira ilo.—Salmo 115:4-8.
○ 13:14—Yehova sakanalekerera Aisrayeli osamverawo mwa kuwapulumutsa iwo pa nthaŵi imeneyo kuchoka ku mphamvu ya Sheol kapena kuwalanditsa iwo ku imfa. Iye sakasonyeza kumvera chifundo, popeza kuti iwo sanayenerere chifundo. Koma mtumwi Paulo anasonyeza kuti Mulungu potsirizira pake akameza imfa kotheratu ndi kuthetsa chilakiko chake. Yehova anasonyeza mphamvu yake ya kuchita tero mwa kuwukitsa Yesu Kristu kuchokera ku imfa ndi Sheol, mwakutero kupereka chitsimikiziro chakuti anthu m’chikumbukiro cha Mulungu adzawukitsidwa ndi Mwana wake pansi pa ulamuliro wa Ufumu.—Yohane 5:28, 29.