MUTU 5
‘Funafunani Yehova’ Pomulambira M’njira Imene Amavomereza
1. Kodi mukupeza madalitso otani pokhala m’gulu la Mulungu?
INUTU muli ndi mwayi waukulu chifukwa chakuti mwadziwa Mulungu amene amakwaniritsa maulosi. Mukusangalala ndi madalitso ofanana ndi amene Aisiraeli ankasangalala nawo. Ponena za madalitso amenewo, mneneri Hoseya analemba kuti: “Ndidzalonjeza kukukwatira mokhulupirika ndipo udzadziwadi Yehova.” Apa Hoseya ankatanthauza kuti anthu a Mulungu akadzabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo ku Babulo, adzakhala otetezeka m’dziko lawo, ndipo adzakhala ngati ali m’paradaiso. Mofanana ndi zimenezi, anthu a Mulungu masiku ano akusangalala ndi madalitso auzimu ndipo zili ngati ali m’paradaiso. (Hoseya 2:18-20) Panopa mumadziwika ndi dzina la Mulungu chifukwa munadzipereka kwa Yehova ndipo ndinu Mboni yake. Choncho yesetsani kuti mupitirize kudziwika ndi dzina limeneli.—Yesaya 43:10, 12; Machitidwe 15:14.
2, 3. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa kuti Yehova ayambe kudana ndi mmene Aisiraeli ankamulambirira? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mozama uthenga umene aneneri ankalengeza?
2 Yehova anasankha Aisiraeli kuti akhale mtundu wake ndipo anawapatsa malamulo amene mitundu ina sinapatsidwe. (Deuteronomo 4:33-35) Koma pofika kumapeto kwa zaka za m’ma 800 B.C.E., Aisiraeli anasintha kwambiri moti Mulungu anauza mneneri Amosi kuti awauze kuti: “Ine ndimadana ndi zikondwerero zanu ndipo ndikuzikana, . . . Inu mukapereka nsembe zathunthu zopsereza, ine sindidzasangalala ndi nsembe zanuzo zoperekedwa ngati mphatso.” (Amosi 5:21, 22) N’zoona kuti Mulungu sakunena zimenezi ku mpingo wake wapadziko lonse masiku ano. Koma kodi mungamve bwanji Mulungu atakuuzani mawu amenewa posonyeza kuti sakusangalala ndi mmene mumamulambirira? Kodi tonsefe tingaphunzirepo chiyani?
3 Pa nthawi imeneyo, anthu a Mulungu ankanena kuti akumulambira m’njira yovomerezeka. Komabe, ambiri ankalambira milungu yachikunja monga mulungu wa Akanani wotchedwa Baala komanso zifaniziro za mwana wa ng’ombe, kapena ankapereka nsembe pamalo okwezeka. Iwo ankagwadira khamu lonse la zinthu zakuthambo monga dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, koma pa nthawi imodzimodziyo ankalambiranso Yehova. Choncho Mulungu woona anatumiza aneneri kuti akalimbikitse anthu kuti ayambirenso kulambira koona. (2 Mafumu 17:7-17; 21:3; Amosi 5:26) Pamenepa tikuona kuti ngakhale anthu amene anadzipereka kwa Mulungu kuti amutumikire, nthawi zina angafunike kuonanso zochita zawo kapena makhalidwe awo ngati akugwirizana ndi zimene Yehova amavomereza.
‘DZIWANI MULUNGU’
4. Kodi zinthu zinali bwanji pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Yerobowamu Wachiwiri?
4 Taganizirani mmene zinthu zinalili pa nthawi imene gulu loyambirira la aneneri 12 aja linayamba kulengeza uthenga wochokera kwa Mulungu. Aneneriwo ankalosera kuti ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 udzakumana ndi tsoka pa tsiku la Yehova. Komabe, zinthu zinkaoneka ngati zikuyenda bwino mu ufumu umenewu. Mogwirizana ndi zimene Yona analosera, Mfumu Yerobowamu Wachiwiri anabwezeretsa malire a Isiraeli kuyambira kumpoto, kufupi ndi Damasiko, mpaka kukafika ku Nyanja Yakufa. (2 Mafumu 14:24-27) Ngakhale kuti Yerobowamu ankachita zinthu zoipa, Yehova analeza mtima ndipo sankafuna kufafaniza Aisiraeli padziko lapansi. Yehova Mulungu anapereka mpata kwa Aisiraeli kuti alape ndi ‘kuyesetsa kumuyandikira kuti apitirize kukhala ndi moyo.’—Amosi 5:6.
5. Kodi n’chifukwa chiyani Yehova anakana Aisiraeli?
5 Aisiraeli amene ankaoneka ngati zinthu zikuwayendera bwino akanagwiritsa ntchito nthawi imeneyi kuti abwerere kwa Yehova. Iwo akanachita zimenezi poyesetsa kumudziwa bwino ndi kuchita zimene amafuna. M’malomwake, iwo ankadzidalira kwambiri ndipo ankaona kuti ‘tsoka silingawayandikire kapena kuwagwera.’ (Amosi 9:10) Mwina munganene kuti iwo anaiwala Yehova chifukwa ‘anakhuta ndipo mtima wawo unayamba kudzitukumula.’ (Hoseya 13:6) Tisaganize kuti imeneyi yangokhala mbiri yakale chabe ndipo ifeyo sizikutikhudza. Taonani chifukwa chake Yehova anayenera kuweruza Aisiraeliwo. Kudzera mwa Hoseya, iye ananena kuti: “Popeza iwo akana kundidziwa, inenso ndidzawakana kuti azinditumikira ngati wansembe wanga.” Mtundu wonse wa Isiraeli unali wodzipereka kwa Yehova. Komabe aliyense payekha, ‘sankadziwa Mulungu.’—Hoseya 4:1, 6.
6. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Aisiraeli sankadziwa kwenikweni Mulungu?
6 Sikuti Aisiraeliwo ankachita zimenezi chifukwa chakuti anali asanamvepo mawu a Mulungu. Izi zili choncho chifukwa chakuti panali lamulo loti makolo achiisiraeli aziphunzitsa ana awo mawu a Mulungu. N’kutheka kuti ambiri anali atamvapo nkhani za m’Baibulo kuchokera kwa makolo awo, kwa anthu ena, kapena pamisonkhano. (Ekisodo 20:4, 5; Deuteronomo 6:6-9; 31:11-13) Mwachitsanzo iwo anamva zimene zinachitika Aroni atapanga mwana wang’ombe wagolide pamene Mose anapita m’phiri la Sinai kukalandira Malamulo Khumi. (Ekisodo 31:18–32:9) Choncho Aisiraeli a m’nthawi ya aneneriwa ankadziwa ndithu Chilamulo ndipo anali atamva zimene zinachitikira makolo awo. Komabe, zimene ankadziwazo zinali zopanda phindu chifukwa chakuti sizinawalimbikitse kulambira Mulungu m’njira imene iye ankafuna.
7. (a) N’chifukwa chiyani Aisiraeli anakopeka mosavuta n’kuyamba kusamvera Mulungu? (b) Kodi Mkhristu angayambe bwanji ‘kuiwala amene anamupanga’?
7 Mwina mungadzifunse kuti, ‘N’chifukwa chiyani Aisiraeli anakopeka mosavuta n’kuyamba kusamvera Mulungu?’ Hoseya anafotokoza zimene zinawachititsa. Iye anati: “Isiraeli anaiwala amene anamupanga.” (Hoseya 8:14) Mawu achiheberi amene palembali anawamasulira kuti “anaiwala” angatanthauzenso kuti “anayamba kuiwala.” Izi sizikutanthauza kuti mwadzidzidzi Aisiraeli anaiwala zimene Yehova ankafuna kuti iwo azichita. Koma zikutanthauza kuti pang’onopang’ono iwo anayamba kuiwala kufunika komulambira m’njira imene iye amafuna. Kodi mukuganiza kuti zimenezi zingachitikenso kwa Mkhristu? Inde, zingachitike. Mwachitsanzo, ganizirani za mwamuna amene akuyesetsa kupezera banja lake zinthu zofunika pa moyo. (1 Timoteyo 5:8) M’pomveka kuti angaone kuti ntchito imene akugwira ndi yofunika kwambiri kuti akwanitse kuchita zimenezi. Ndiyeno zinazake zingachitike ndipo angaone kuti akufunika kuphonya misonkhano ina yachikhristu kuti akagwire ntchito. M’kupita kwa nthawi, angayambe kuona kuti palibe vuto kuphonya misonkhano ndipo angamachite zimenezi mobwerezabwereza. Pang’ono ndi pang’ono, ubwenzi wake ndi Mulungu ungayambe kuchepa, ndipo angayambe ‘kuiwala amene anamupanga.’ Zoterezi zingachitikirenso Mkhristu amene makolo ake kapena achibale ake ena ndi osakhulupirira. Iye angakumane ndi mavuto osiyanasiyana. Mwachitsanzo, angafunike kusankha kuti azicheza liti ndi achibale akewo komanso kwa nthawi yaitali bwanji. (Ekisodo 20:12; Mateyu 10:37) Angafunikenso kusankha kuti agwiritse ntchito nthawi yochuluka bwanji pochita zinthu zina monga kupita koyenda kapena kuchita zosangalatsa.
8. M’nthawi ya Amosi, kodi kukhala ndi “mano oyera” kunkatanthauza chiyani?
8 Timaphunzira Mawu a Mulungu ndipo timagwiritsa ntchito zimene taphunzirazo. Komabe, aliyense ayenera kuganizira mawu akuti “ndinakupatsani mano oyera,” amene ali m’mawu a m’munsi pa Amosi 4:6. Palembali, Mulungu anachenjeza anthu ake kudzera mwa Amosi kuti: “Ine ndinakupatsani [mano oyera] m’mizinda yanu yonse ndipo munali kusowa chakudya m’malo anu onse okhala.” Sikuti Mulungu ankatanthauza kuti manowo anali oyera chifukwa chowatsuka ayi. Koma chifukwa chosowa chakudya ndi madzi, kapena kuti chifukwa cha njala ndi ludzu. Komanso Mulungu anawabweretsera njala imeneyi powachenjeza za njala yauzimu. Iye anawachenjeza kuti “njala imeneyo siidzakhala ya chakudya kapenanso ludzu lofuna madzi ayi, koma idzakhala njala ndiponso ludzu lofuna kumva mawu a Yehova.”—Amosi 8:11
9, 10. (a) Kodi zingatheke bwanji kuti Mkhristu afe ndi njala yauzimu? (b) N’chifukwa chiyani tikufunika kukhala tcheru kuti tisafe ndi njala yauzimu?
9 Zimene Amosi anafotokoza zikukwaniritsidwa m’matchalitchi amene amati ndi achikhristu momwe muli njala yaikulu yauzimu. Mosiyana ndi matchalitchi amenewa, Mulungu watsegulira anthu ake padziko lonse “zipata za kumwamba” ndipo akuwapatsa chakudya chauzimu chamwanaalirenji. (Malaki 3:10; Yesaya 65:13, 14) Komabe, Mkhristu aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ineyo pandekha ndimadya chakudya chauzimu chimenechi mokwanira?’ Taganizirani izi: Akatswiri ena ofufuza zinthu ankasunga nyama zina zimene mbali ina ya ubongo wawo inawonongeka. Mbali imeneyi imathandiza nyamazo kudziwa kuti zili ndi njala. Iwo anaona kuti nyamazo zinalibe chilakolako choti zidye moti zikanatha kufa ndi njala ngakhale panali chakudya chambiri. Choncho zingatheke kuti Mkhristu akhale wopanda chilakolako cha chakudya chauzimu mpaka kufa ndi njala ngakhale kuti ali ndi chakudya chambiri chauzimu.
10 Pamene mukuganizira mmene zinthu zilili pa moyo wanu, kumbukirani kuti Yehova anapatsa Aisiraeli chakudya chambiri chauzimu. Iwo anali ndi Chilamulo chimene chikanawathandiza kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Mulungu, ndiponso ankafunika kumaphunzitsa ana awo nthawi zonse kuti adziwe Mulungu. Komanso anali ndi aneneri amene ankawathandiza kumvetsa chifuniro cha Mulungu. Komabe, iwo anayamba kuiwala Yehova, moti Baibulo limanena kuti m’masiku a Hoseya, iwo ‘anakhuta ndipo mtima wawo unayamba kudzitukumula.’ (Hoseya 13:6; Deuteronomo 8:11; 31:20) Tsiku lililonse tikufunika kukhala tcheru kuti tisalole zinthu zimene tili nazo kusokoneza ubwenzi wathu ndi Mulungu.—Zefaniya 2:3.
MUZIGANIZIRA ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI
11, 12. (a) Pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Uziya, n’chifukwa chiyani aneneri ankalimbikitsa anthu kuti abwerere kwa Yehova? (b) Kodi Yoweli analimbikitsa anthu kuti achite chiyani?
11 Pa nthawi imene Yerobowamu Wachiwiri ankalamulira ku Isiraeli, Uziya (amene ankadziwikanso kuti Azariya) ankalamulira ku Yuda. Uziya anawonjezera gawo limene ankalamulira komanso anamanga zinthu zina mumzinda wa Yerusalemu. Iye “anasonyeza mphamvu zochuluka zedi” chifukwa chakuti “Mulungu woona anapitiriza kumuthandiza.” Uziya “anapitiriza kuchita zoyenera pamaso pa Yehova” ndipo “anali kufunafuna Mulungu.” Komabe, anthu ambiri mu Yuda anapitiriza kupereka nsembe m’malo okwezeka.—2 Mbiri 26:4-9.
12 Ngakhale kuti anthu a ku Yuda komanso ku Isiraeli ankadziwika ndi dzina la Mulungu, kawirikawiri polambira Mulungu iwo ankachitanso zinthu zina zosamusangalatsa. Aneneri ankayesetsa kuwathandiza kuti aone kusiyana kwa kulambira kumene Mulungu amavomereza ndi kumene savomereza. Kudzera mwa Yoweli, Mulungu anachonderera anthuwo kuti: “Bwererani kwa ine ndi mtima wanu wonse. Salani kudya, lirani momvetsa chisoni ndiponso mokuwa.” (Yoweli 2:12) N’zoonekeratu kuti Mulungu ankafuna kuti anthu akewo abwerere kwa iye ‘ndi mtima wawo wonse.’ Izi zikusonyeza kuti iwo sankamulambira ndi mtima wawo wonse. (Deuteronomo 6:5) Tinganene kuti iwo ankalambira Yehova mwamwambo chabe. Choncho, mobwerezabwereza Mulungu ankauza anthuwo kudzera mwa aneneri ake kufunika kosonyeza makhalidwe amene amayambira mumtima, monga chilungamo, kukoma mtima kosatha komanso kufatsa.—Mateyu 23:23.
13. Kodi Ayuda amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo ku Babulo ankafunika kuchita chiyani?
13 Ndiyeno ganizirani zimene zinachitika Ayuda atabwerera kwawo kuchoka ku ukapolo. Ngakhale kuti Ayudawo anayambiranso kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka mogwirizana ndi Chilamulo, iwo sankatsatira malangizo onse a Mulungu. Mwachitsanzo, Ayuda anayamba kusala kudya pa masiku okumbukira kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu. Choncho Yehova anawafunsa kuti: “Kodi munalidi kusala kudya chifukwa cha ine?” Kuwonongedwa kwa mzinda wa Yerusalemu kunali chiweruzo cha Mulungu, ndipo panalibe chifukwa chodandaulira ndi zimene zinachitikazo. M’malo mokumbukira zakale n’kumasala kudya chifukwa chomva chisoni, Ayudawo ankafunika kumasangalala pa nthawi ya zikondwerero chifukwa cha madalitso amene ankapeza polambira Mulungu m’njira yovomerezeka. (Zekariya 7:3-7; 8:16, 19) Komanso panali zinthu zina zimene ankafunika kuchita. Kodi ankafunikira kuchita chiyani? Mulungu anawauza kuti: “Muzichita chilungamo chenicheni poweruza milandu. Muzisonyezana kukoma mtima kosatha ndi chifundo. . . . Musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu.” (Zekariya 7:9, 10) Choncho tonsefe tingapindule ndi mfundo zimene aneneriwo anaphunzitsa anthu a Mulungu zokhudza kulambira Mulungu ndi mtima wonse.
14. (a) Kodi Ayuda amene anabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo ankafunika kuchita zinthu zinanso ziti polambira Mulungu? (b) Kodi aneneri anatsindika bwanji zinthu zofunika kwambiri pa kulambira kovomerezeka?
14 Kodi munthu amene akufuna kulambira Mulungu ndi mtima wonse amafunika kuchita chiyani? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiganizire zimene anthu a Mulungu ankafunikira kuchita asanapite ku ukapolo komanso atabwerako. Iwo ankafunikira kutsatira mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino nthawi zonse. Komanso Chilamulo chinatchula mwachindunji zinthu zina zimene ankafunika kuchita, monga kusonkhana pamodzi kuti aphunzire kuchita chifuniro cha Mulungu. Kuwonjezera pamenepo, aneneri a Mulungu ankaphunzitsa anthuwo mobwerezabwereza kuti azisonyeza kukoma mtima kosatha, akhale achilungamo, ofatsa, achifundo komanso odzichepetsa. Potsindika makhalidwe amenewa, kudzera mwa Hoseya, Yehova anati: “Ndimakondwera ndi kukoma mtima kosatha, osati ndi nsembe. Ndimakondweranso ndi kudziwa Mulungu, osati ndi nsembe zopsereza zathunthu.” Ananenanso kuti: “Bzalani mbewu za chilungamo ndipo kololani zipatso za kukoma mtima kosatha.” (Hoseya 6:6; 10:12; 12:6) Nayenso Mika ananena kuti: “Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.” (Mika 6:6-8) Komanso mneneri Zefaniya analimbikitsa anthu a Mulungu kuti: “Bwerani kwa Yehova, inu nonse ofatsa a padziko lapansi, . . . Yesetsani kukhala olungama, yesetsani kukhala ofatsa.” (Zefaniya 2:3) Makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambiri kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka kwa Mulungu.
15. Mogwirizana ndi zimene aneneri ananena, kodi Akhristu akufunika kuchita chiyani polambira Mulungu?
15 Kodi makhalidwe amenewa ndi othandiza bwanji pa kulambira kwathu? Monga mukudziwira, ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndi yofunika kwambiri. (Mateyu 24:14; Machitidwe 1:8) Koma mwina mungadzifunse kuti: ‘Kodi ndimaona kuti kulalikira m’gawo lathu ndi ntchito yotopetsa ndiponso yosasangalatsa? Kapena kodi ndimaiona ngati mwayi wothandizira anthu ena amene akufuna kumva uthenga wa m’Baibulo, womwe ndi wopulumutsa moyo? Kodi anthu amenewo, ndimawasonyeza chifundo powalalikira?’ Zoonadi, tiyenera kukhala ofunitsitsa kuchenjeza anthu za tsiku la Yehova chifukwa chowamvera chifundo komanso pofuna kuwasonyeza kukoma mtima kosatha. Ndiponso tikamayesetsa kulengeza uthenga umenewu kwa anthu osiyanasiyana, timasonyeza chilungamo.—1 Timoteyo 2:4.
16, 17. N’chifukwa chiyani kufatsa ndi kudzichepetsa ali makhalidwe ofunika pa kulambira kwanu?
16 Ganiziraninso mfundo yoti timafunikira kupita kumisonkhano yachikhristu, imene mukudziwa kuti ndi yofunika kwambiri. (Aheberi 10:24, 25) Kodi munayamba mwaganizapo kuti munthu amafunika kukhala wofatsa komanso wodzichepetsa kuti apite kumisonkhano? Anthu ofatsa amakhala odzichepetsa ndipo amalandira malangizo mosavuta komanso amagwiritsa ntchito zimene aphunzira. Pochita zimenezi iwo amakhala akuchita zinthu mogwirizana ndi ziweruzo za Yehova. Munthu wodzichepetsa amadziwa kuti pali zinthu zina zimene sangathe kuchita. Chotero amadziwa kuti akufunika kulimbikitsidwa komanso kuphunzitsidwa kudzera m’misonkhano yachikhristu.
17 Mungaone kuti pa nkhani yolalikira ndiponso kupita kumisonkhano yachikhristu, tikuphunzira zambiri kuchokera pa zimene aneneri ankaphunzitsa. Komano mungatani ngati mwaona kuti mukufunika kusintha pena ndi pena pa nkhani zimenezi? Kapena kodi mungatani ngati nthawi ina munachita tchimo lalikulu, ndipo mumavutika maganizo mukakumbukira zimene munachitazo? Zimene aneneri 12 amenewa analemba zingakulimbikitseni komanso kukuthandizani kwambiri.
BWERERANI KWA YEHOVA
18. (a) Kodi ndani kwenikweni amene akulimbikitsidwa ndi uthenga wa aneneri 12? (b) Kodi mumamva bwanji mumtima mwanu mukaganizira mfundo yakuti Yehova amachonderera anthu kuti abwerere kwa iye?
18 Monga taonera, aneneri amene tikukambiranawa sankangolengeza uthenga wodzudzula ndi wachiweruzo wokhawokha. Uthenga wawo ukusonyeza kuti Yehova ankapempha anthu kuti abwerere kwa iye. Mwachitsanzo, ganizirani mmene Hoseya ankamvera pamene analimbikitsa anthu kuti: “Bwerani anthu inu. Tiyeni tibwerere kwa Yehova, pakuti iye watikhadzulakhadzula koma adzatichiritsa. Wakhala akutivulaza koma adzamanga zilonda zathu. . . . Ife tidzamudziwa Yehova ndipo tidzayesetsa kuti timudziwe bwino.” (Hoseya 6:1-3) Zoonadi, Yehova Mulungu anachita chilungamo poweruza dziko la Isiraeli komanso la Yuda. Komabe, anthu ake ankayenera kuona chilango chimenecho ngati njira yowathandiza kuti ayambirenso kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka. (Aheberi 12:7-13) Ngati anthu a Yehova olowererawo akanabwerera, iye ‘akanawachiritsa’ ndi ‘kumanga zilonda zawo.’ Ganizirani za munthu amene wagwada kuti amange bala la mnzake amene wavulala. Ndiyeno yerekezerani kuti mukuona Yehova akuchita zimenezi. Ndithudi Yehova ndi Mulungu wachifundo chifukwa amamanga mabala a anthu amene akufuna kubwerera kwa iye. Kodi zimenezi sizikutilimbikitsa kuti tikamuchimwira tizikhala ndi mtima wofunitsitsa kubwerera kwa iye?—Yoweli 2:13.
19. Kodi kudziwa bwino Yehova kumatanthauza chiyani?
19 Kodi munthu amafunikira kuchita zinthu zotani kuti abwerere kwa Mulungu? Hoseya analemba kuti kuwonjezera pa kudziwa Mulungu, munthu amafunika ‘kuyesetsa kuti amudziwe bwino.’ Ponena za lemba la Hoseya 6:3, buku lina laposachedwapa linanena kuti: “Kudziwa za Mulungu n’kosiyana kwambiri ndi kumudziwa bwino. Tingayerekezere zimenezi ndi mmene kungowerenga nkhani inayake yachikondi kumasiyanirana ndi kuyamba kukonda kwambiri munthu.” Timafunikira kudziwa zambiri zokhudza Yehova osati zochepa chabe. Mulungu ayenera kukhala weniweni kwa ife komanso Bwenzi lathu lapamtima lomwe tingamalankhule nalo nthawi iliyonse. (Yeremiya 3:4) Mukakhala pa ubwenzi woterewu ndi Mulungu mungamvetse mmene amamvera mukachita zinthu zinazake, ndipo zimenezi zingakuthandizeni kuti muziyesetsa kumulambira m’njira imene amavomereza.
20, 21. Kodi Mfumu Yosiya anachita chiyani chimene chinasonyeza kuti ankaona kuti kudziwa Mulungu n’chinthu chofunika kwambiri?
20 Mfumu Yosiya anali chitsanzo chabwino pa nkhani yokhudza kulambira Mulungu m’njira yovomerezeka. Tiyeni tipitirize kuona zimene iye anachita. Pa nthawi imene Yosiya anakhala mfumu, zinthu zinali zitaipa kwambiri m’dziko la Yuda. Izi zinali choncho chifukwa chakuti anthu ankalambira mafano komanso ankachita zachiwawa ndi zachinyengo. Zinthu zimenezi zinali zofala kwambiri mu ulamuliro wa Manase ndiponso wa Amoni. (2 Mafumu 21:1-6, 19-21) Yosiya ayenera kuti analimbikitsidwa kwambiri ndi mawu a Zefaniya akuti anthu ‘abwere kwa Yehova.’ Izi zili choncho chifukwa chakuti Mfumu Yosiya “anayamba kufunafuna Mulungu wa Davide.” Mfumuyi inayamba ntchito yothetsa kulambira mafano m’dziko la Yuda, ndipo ntchito imeneyi inafikanso m’madera amene kale anali mu ufumu wakumpoto.—Zefaniya 1:1, 14-18; 2:1-3; 3:1-4; 2 Mbiri 34:3-7.
21 Atamaliza ntchito imeneyi, Yosiya anapitiriza kufunafuna Yehova. Iye analamulanso kuti kachisi akonzedwe. Ntchito imeneyi ili mkati, “wansembe Hilikiya anapeza buku la chilamulo cha Yehova loperekedwa ndi dzanja la Mose.” Zikuoneka kuti bukuli linali mpukutu woyambirira weniweni wa Chilamulo. Kodi Yosiya anachita chiyani buku limeneli litawerengedwa? Malemba amati: “Mfumuyo itangomva mawu a chilamulowo, nthawi yomweyo inang’amba zovala zake.” Yosiya ‘anang’ambanso mtima wake’ ndipo nthawi yomweyo anayamba kuchita zimene zinawerengedwazo. Iye sanazengereze kutsatira chilamulocho poganiza kuti anali atachita kale zambiri pa ntchito yobwezeretsa kulambira koona. Kodi mukukumbukira zotsatira za ntchito yakeyi? Baibulo limanena kuti: “M’masiku ake onse, [ana a Isiraeli] sanasiye kutsatira Yehova Mulungu wa makolo awo.”—2 Mbiri 34:8, 14, 19, 21, 30-33; Yoweli 2:13.
22. Kodi tingapindule bwanji ndi chitsanzo cha Yosiya?
22 Mwina mungadzifunse kuti, ‘Kodi ineyo ndikanachita chiyani?’ Kodi mukanamvera mawu a aneneri n’kusintha zochita zanu komanso maganizo anu ngati mmene Yosiya anachitira? Ngakhale kuti sitikukhala m’nthawi ya Zefaniya ndi Yosiya, tikuona kuti masiku ano tikufunikiranso kumvera uthenga komanso malangizo ochokera kwa Mulungu. Choncho ngati Mkhristu akuona kuti akufunikira kusintha zina ndi zina pa moyo wake kapena zochita zake zokhudza kulambira Mulungu, kuphunzira zimene aneneri 12 analemba kungamulimbikitse kusintha mwamsanga.—Aheberi 2:1.
23. Kodi mungachite chiyani ngati mukuona kuti mukufunika kusintha zina n’zina pa moyo wanu?
23 Nthawi zina mungamamve ngati mmene Yona ankamvera pamene anali m’mimba mwa chinsomba. Iye anati: “Mwandipitikitsa pamaso panu! Kodi kachisi wanu woyera ndidzamuonanso?” (Yona 2:4) Komabe, mawu a Yehova opezeka pa Malaki 3:7 ndi olimbikitsa kwambiri kwa anthu opanda ungwirofe, amene timachimwa nthawi zonse. Palembali Yehova akutiuza kuti: “Bwererani kwa ine ndipo ine ndibwerera kwa inu.” Ngati mukuona kuti mukufunikira kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova, pemphani akulu a mumpingo wanu kuti akuthandizeni. Mwina mungafunike kuyamba kuchita pang’onopang’ono zinthu zina zauzimu. Ndiyeno mukazolowera, simudzavutika kuchita zinthu zinanso zimene zingakuthandizeni kupita patsogolo mwauzimu. Mosakayikira, Yehova adzakulandirani ndiponso kukuthandizani chifukwa iye ndi “wachisomo, wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.” (Yoweli 2:12-14) Zoonadi, uthenga umene aneneri 12 amenewa analemba ndi wolimbikitsa kwa aliyense amene akufuna kumalambira Mulungu m’njira imene iyeyo amavomereza.