Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’mabuku a Yoweli ndi Amosi
YOWELI sanalembe zambiri za moyo wake kusiyapo kunena kuti iye ndi “Yoweli mwana wa Petueli.” (Yoweli 1:1) M’buku lake, Yoweli sananene zinthu zambiri koma anangonena za uthenga wake moti ngakhale nthawi imene analemba ulosi wake sikudziwika bwinobwino. Koma zikuoneka kuti analemba buku lakelo cha mu 820 B.C.E., zaka 9 Uziya atakhala mfumu ya Yuda. Kodi n’chifukwa chiyani Yoweli sanalembe zambiri za moyo wake? Ayenera kuti sanafune kunena zambiri za iye monga wopereka uthenga n’cholinga choti atsindike kwambiri za uthenga wake.
M’nthawi ya Uziya, Amosi yemwe ankakhala ku Yuda ndipo anali “woweta ng’ombe, ndi wakutchera nkhuyu” nayenso anapatsidwa ntchito yauneneri. (Amosi 7:14) Yoweli anali mneneri ku Yuda koma Amosi anatumidwa kukalosera kumpoto, ku ufumu wa Isiraeli wa mafuko khumi. Amosi anamaliza kulemba buku lake cha mu 804 B.C.E. atabwerera ku Yuda, ndipo analilemba mosavuta kumva ndiponso m’njira yoti munthu ukamawerenga uziona ngati zimene zikunenedwazo zikuchitika.
N’CHIFUKWA CHIYANI YOWELI ANATI “KALANGA INE, TSIKULI!”?
Yoweli anaona m’masomphenya mliri wa ‘chimbalanga, dzombe, chilimamine, ndi anoni.’ Tizilomboti tikutchedwa “mtundu waukulu ndi wamphamvu.” (Yoweli 1:4; 2:2-7) Yoweli anati: “Kalanga ine, tsikuli! pakuti layandikira tsiku la Yehova, lidzafika ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.” (Yoweli 1:15) Yehova analangiza anthu a ku Ziyoni kuti: “Munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse.” Ngati iwo akanatero, Yehova ‘akanawachitira chifundo’ ndipo akanawateteza ku “nkhondo ya kumpoto,” kapena kuti ku mliri wa tizilombo. Tsiku lake lalikulu lisanafike, Yehova ‘adzatsanulira mzimu wake pa anthu onse’ ndipo ‘adzaonetsa zodabwiza kuthambo ndi pa dziko lapansi.’—Yoweli 2:12, 18-20, 28-31.
Amitundu anauzidwa kuti: “Sulani makasu anu akhale malupanga, ndi anangwape anu akhale nthungo” ndipo konzekerani nkhondo. Analamulidwa kuti “akwerere ku chigwa cha Yehosafati,” kumene adzaweruzidwa ndi kuwonongedwa. “Koma Yuda adzakhala chikhalire.”—Yoweli 3:10, 12, 20.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:15; 2:1, 11, 31; 3:14—Kodi “tsiku la Yehova” n’chiyani? Tsiku la Yehova ndi nthawi imene iye adzaweruza adani ake ndipo adzawawononga n’kupulumutsa olambira oona. Mwachitsanzo, tsiku lotere linafikira ufumu wakale wa Babulo mu 539 B.C.E., pamene Amedi ndi Aperisi anauwononga. (Yesaya 13:1, 6) “Tsiku la Yehova” linanso layandikira, pamene adzawononga “Babulo Wamkulu,” yemwe ndi ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga.—Chivumbulutso 18:1-4, 21.
2:1-10, 28—Kodi ulosi wonena za mliri wa tizilombo wakwaniritsidwa bwanji? Baibulo silinena chilichonse kuti ku Kanani kunagwa mliri wa tizilombo ngati wofotokozedwa m’buku la Yoweliwu. Choncho, zikuoneka kuti mliri umene Yoweli anafotokoza ndi ulosi wa zimene zinachitika mu 33 C.E., pamene Yehova anayamba kutsanulira mzimu wake pa otsatira a Khristu oyambirira ndipo iwo anayamba kulalikira uthenga womwe unavutitsa maganizo atsogoleri onyenga achipembedzo. (Machitidwe 2:1, 14-21; 5:27-33) Nafenso masiku ano, tili ndi mwayi wochita ntchito yofanana ndi imeneyi.
2:32—Kodi ‘kuitana pa dzina la Yehova’ kumatanthauza chiyani? Kuitana pa dzina la Mulungu kumatanthauza kudziwa bwino dzinali, kulilemekeza kwambiri, ndiponso kudalira ndi kukhulupirira mwini wake wa dzinalo.—Aroma 10:13, 14.
3:14—Kodi “chigwa chotsirizira mlandu” n’chiyani? Ndi malo ophiphiritsa kumene Mulungu amawonongerako adani ake. Mulungu anapulumutsa Ayuda ku mitundu yozungulira mwa kusokoneza magulu awo ankhondo m’nthawi ya Mfumu Yehosafati ya Yuda, amene dzina lake limatanthauza “Yehova Ndi Woweruza.” Choncho, malowo amatchedwanso kuti “chigwa cha Yehosafati.” (Yoweli 3:2, 12) Masiku ano, chigwachi chimaimira malo ophiphiritsa kumene mitundu idzaphwanyidwa ngati mmene amachitira poponda mphesa.—Chivumbulutso 19:15.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:13, 14. Kuti munthu apulumuke afunikira kulapa ndi mtima wonse ndi kuvomereza kuti Yehova ndi Mulungu woona.
2:12, 13. Kulapa kwenikweni kumachokera m’mtima. Kumafuna ‘kung’amba mtima’ osati ‘zovala ayi.’
2:28-32. Anthu okhawo amene “adzaitana pa dzina la Yehova adzapulumutsidwa” pa “tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.” Ndife oyamikira kuti Yehova amatsanulira mzimu wake pa anthu onse ndipo walola kuti ana ndi akulu omwe, amuna ndi akazi, agwire nawo ntchito yonenera, kapena kuti kulengeza “zinthu zazikulu za Mulungu.” (Machitidwe 2:11) Popeza tsiku la Yehova layandikira, tiyenera kukulitsa “khalidwe loyera” ndiponso kuchita ‘ntchito za kudzipereka kwa Mulungu.’—2 Petulo 3:10-12.
3:4-8, 19. Yoweli analosera kuti mitundu yoyandikana ndi Yuda idzaimbidwa mlandu wozunza anthu osankhidwa a Mulungu. Mawu amenewa analidi oona chifukwa mzinda wa Turo unawonongedwa ndi Mfumu Nebukadinezara ya Babulo. Kenako, pamene mzinda wa pachilumba wa Turo unagonjetsedwa ndi Alexander Wamkulu, asilikali ndi anthu odziwika zikwizikwi anaphedwa ndiponso anthu ena 30,000 anagulitsidwa ku ukapolo. Alexander ndiponso anthu amene anamulowa m’malo anazunza Afilisiti chimodzimodzi. Pofika m’zaka za m’ma 300 B.C.E., mzinda wa Edomu unali bwinja. (Malaki 1:3) Kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kumalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Yehova, yemwe ndi Wokwaniritsa malonjezo. Kumasonyezanso mmene Yehova adzachitira ndi mitundu imene imazunza olambira ake masiku ano.
3:16-21. “Thambo ndi dziko lapansi zidzagwedezeka,” ndipo mitundu idzawonongedwa ndi Yehova. “Koma Yehova adzakhala chopulumukirako anthu ake,” ndipo adzawapatsa moyo wabwino m’Paradaiso. Ndiyeno, kodi si koyenera kuti tiyesetse kukhala pafupi ndi iye pamene tsiku lake lowononga dziko loipali likuyandikira?
“DZIKONZERETU KUKUMANA NDI MULUNGU WAKO”
Amosi anali ndi uthenga wopita ku mitundu imene inkalimbana ndi Isiraeli komanso ku Yuda ndi Isiraeli. Suriya, Filistia, Turo, Edomu, ndi Moabu anali kudzawonongedwa chifukwa chochitira nkhanza anthu a Mulungu. Ayuda analinso kudzawonongedwa ‘popeza anakaniza chilamulo cha Yehova.’ (Amosi 2:4) Nanga bwanji ufumu wa Isiraeli wa mafuko khumi? Anthu mu ufumuwu ankapondereza aumphawi pofuna phindu, anali achiwerewere ndiponso ankanyoza aneneri a Mulungu. Amosi anachenjeza kuti Yehova ‘adzalanga maguwa a nsembe a ku Beteli’ ndiponso ‘adzakantha nyumba ya nyengo yachisanu, pamodzi ndi nyumba ya nyengo yadzuwa.’—Amosi 3:14, 15.
Ngakhale kuti Aisiraeli anali atalangidwapo kale anapitiriza kukhala ouma khosi. Amosi anawauza kuti: “Dzikonzeretu kukumana ndi Mulungu wako.” (Amosi 4:12) Kwa Aisiraeli, tsiku la Yehova linatanthauza ‘kumka kundende kutsogolo kwa Damasiko,’ kapena kuti kwa Asuri. (Amosi 5:27) Amosi anatsutsidwa ndi wansembe wa ku Beteli koma zimenezi sizinam’chititse mantha. Yehova anauza Amosi kuti: “Chitsiriziro chafikira anthu anga Isiraeli, sindidzawalekanso.” (Amosi 8:2) Manda kapena mapiri aatali sakanawateteza ku chiweruzo cha Mulungu. (Amosi 9:2, 3) Komabe, panali chiyembekezo. Yehova anati: “Ndidzabwezanso undende wa anthu anga Isiraeli, ndipo adzamanganso mabwinja, ndi kukhala mmenemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wake, nadzalima minda ndi kudya zipatso zake.”—Amosi 9:14.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
4:1—Kodi “ng’ombe zazikazi za ku Basana” zimaimira chiyani? Dera lokwera la Basana, lomwe linali kum’mawa kwa Nyanja ya Galileya, linali lodziwika chifukwa cha ziweto zake zabwino monga ng’ombe. Chinthu chimodzi chimene chinathandiza kuti kukhale ziweto zonenepa chinali msipu wabwino. Amosi anayerekezera akazi okonda moyo wapamwamba a ku Samariya ndi ng’ombe za ku Basana. Mosakayikira, akazi amenewa ankaumiriza “ambuyawo,” kapena kuti amuna awo, kusautsa aumphawi kuti akwaniritse zolinga zawo zokonda chuma.
4:6—Kodi mawu akuti “mano oyera” amatanthauza chiyani? Popeza kuti ananena mawuwa limodzi ndi mawu akuti “kusowa mkate,” mawuwa angatanthauze nthawi ya njala pamene mano amakhala oyera chifukwa chosowa chakudya.
5:5—Kodi Aisiraeli sanayenera ‘kufuna Beteli’ m’njira yotani? Yerobiamu anali ataimika fano la mwana wa ng’ombe ku Beteli. Kuyambira nthawi imeneyo, mzindawu unakhala chimake cha kulambira konyenga. Giligala ndi Beeriseba ayenera kuti analinso malo a kulambira kwampatuko. Kuti apulumuke tsoka limene linali kubwera, Aisiraeli anafunika kusiya kukalambira ku malo amenewa kenako n’kuyamba kufunafuna Yehova.
7:1—Kodi mawu oti ‘kusengera kwa mfumu’ amanena za chiyani? Ayenera kuti amanena za msonkho umene mfumu inakhazikitsa wothandizira amuna apakavalo ndi ziweto zake. Msonkhowu unkalipiridwa “poyamba kuphuka kwa maudzu a chibwereza.” Kenako, anthu ankayamba kukolola. Koma asanakolole, kunagwa mliri wa dzombe n’kudya mbewu zawo zonse.
8:1, 2—Kodi “mtanga wa zipatso zamalimwe” unkasonyeza chiyani? Unkasonyeza kuti tsiku la Yehova lili pafupi. Zipatso zamalimwe zimathyoledwa ku mapeto kwa nyengo yokolola, kapena kuti kumapeto a chaka chaulimi. Pamene Yehova anaonetsa Amosi “mtanga wa zipatso zamalimwe,” anasonyeza kuti mapeto a Isiraeli ayandikira. Choncho, Mulungu anauza Amosi kuti: “Chitsiriziro chafikira anthu anga Isiraeli, sindidzawalekanso.”
Zimene Tikuphunzirapo:
1:3, 6, 9, 11, 13; 2:1, 4, 6. Ponena za Isiraeli, Yuda, ndi mitundu 6 yowazungulira, Yehova anati: “Sindidzabweza kulanga kwake.” Palibe munthu amene angathawe chiweruzo cha Yehova.—Amosi 9:2-5.
2:12. Tisamafoole apainiya, oyang’anira oyendayenda, amishonale, ndi anthu a pa Beteli amene amagwira ntchito mwakhama powauza kuti asiye utumiki wawo n’kuyamba kuchita zinthu zina. Koma tiziwalimbikitsa kuti apitirize ntchito yawo yabwino.
3:8. Monga mmene anthu amaopera akamva mkango ukubangula, Amosi anafuna kulalikira pamene anamva Yehova akunena kuti: “Muka, nenera kwa anthu anga.” (Amosi 7:15) Kuopa Mulungu kuyenera kutilimbikitsa kulalikira uthenga wa Ufumu mwachangu.
3:13-15; 5:11. Mothandizidwa ndi Yehova, Amosi yemwe ankagwira ntchito yonyozeka yoweta ziweto, anatha ‘kuchitira umboni’ kwa anthu achuma amene sankamvetsera uthenga wake. Mofanana ndi Amosi, Yehova angatithandize kulengeza uthenga wa Ufumu ngakhale m’gawo lovuta kulalikira.
4:6-11; 5:4, 6, 14. Ngakhale kuti nthawi zambiri Aisiraeli analephera ‘kubwerera’ kwa Yehova, iwo analimbikitsidwa ‘kufuna Yehova kuti akhale ndi moyo.’ Malinga ngati Yehova apitirize kuleza mtima n’kulola dongosolo lazinthu loipali kupitirizabe, tiyenera kulimbikitsa anthu kubwerera kwa Mulungu.
5:18, 19. ‘Kufuna tsiku la Yehova’ usanalikonzekere ndi kupusa. N’zofanana ndi munthu amene wathawa mkango n’kukakumana ndi chimbalangondo, kenako pothawa chimbalangondocho n’kukangolumidwa ndi njoka. Tingachite bwino ‘kukhala maso’ mwauzimu n’kukhala okonzekera nthawi zonse.—Luka 21:36.
7:12-17. Tiyenera kulengeza uthenga wa Mulungu molimba mtima ndi mopanda mantha.
9:7-10. Mulungu sanayanje Aisiraeli osakhulupirika monga mmene sanayanjire Akusi, ngakhale kuti Aisiraeliwo anali ana a makolo okhulupirika ndiponso a anthu osankhidwa a Mulungu omwe anapulumutsidwa ku Iguputo. Kuyanjidwa ndi Mulungu wopanda tsankho, sikudalira banja lomwe tinachokera, koma kumadalira pa ‘kumuopa ndi kuchita chilungamo.’—Machitidwe 10:34, 35.
Zimene Tiyenera Kuchita
Tsiku limene Mulungu adzawononge dziko la Satana layandikira. Mulungu watsanulira mzimu wake pa omulambira n’kuwathandiza kuti achenjeze anthu za tsiku lake likubwerali. Kodi si bwino kuti tizichita zonse zimene tingathe kuthandiza anthu ena kudziwa Yehova ndi ‘kuitana pa dzina lake’?—Yoweli 2:31, 32.
Amosi analangiza kuti: “Danani nacho choipa, nimukonde chokoma; nimukhazikitse chiweruzo kuchipata.” (Amosi 5:15) Pamene tsiku la Yehova likuyandikira, tingachite bwino kuyandikira kwa Mulungu n’kulekana ndi dzikoli ndi zinthu zake zoipa. Mabuku a m’Baibulo a Yoweli ndi Amosi ali ndi malangizo a panthawi yake amene angatithandize kuchita zimenezi.—Aheberi 4:12.
[Chithunzi patsamba 12]
Yoweli analosera kuti: “Layandikira tsiku la Yehova.”
[Zithunzi patsamba 15]
Mofanana ndi Amosi, tiyenera kulengeza uthenga wa Mulungu molimba mtima ndi mopanda mantha