“Tiuzeni, Zinthu izi Zidzachitika Liti?”
“Zatsopano Ine ndizitchula; zisanabuke ndidzakumvetsani.”—YESAYA 42:9.
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene atumwi a Yesu anafunsa ponena za mtsogolo? (b) Kodi yankho la Yesu lonena za chizindikiro chachiungwe lakwaniritsidwa motani?
CHIPHUNZITSO chaumulungu chimachokera kwa Yehova Mulungu, “Uyo amene amaneneratu zinthu kuyambira pachiyambi kufikira chimaliziro.” (Yesaya 46:10, NW) Monga momwe nkhani yapitayo inasonyezera, atumwi anafunafuna chiphunzitso chotero kwa Yesu, akumamfunsa kuti: “Tiuzeni, zinthu izi zidzachitika liti? Ndichotani chizindikiro chake chakuti zili pafupi pakumalizidwa zinthu izi zonse?”—Marko 13:4.
2 Poyankha, Yesu anafotokoza “chizindikiro” chachiungwe chokhala ndi umboni umene ukasonyeza kuti dongosolo Lachiyuda linali pafupi kutha. Chimenechi chinakwaniritsidwa pamene Yerusalemu anawonongedwa mu 70 C.E. Koma ulosi wa Yesu ukakwaniritsidwa mokulira m’zaka zambiri za mtsogolo. ‘Nthaŵi za akunja’ zitangotha mu 1914, chizindikirocho chikaonekera pamlingo waukulu, chikumasonyeza kuti posachedwa dongosolo loipa limene lilipoli likathera mu “chisautso chachikulu.”a (Luka 21:24) Mamiliyoni amene adakali ndi moyo lerolino angachitire umboni kuti chizindikiro chimenechi chakwaniritsidwa m’nkhondo zadziko ndi m’zochitika zina zatsoka za m’zaka za zana la 20. Zimenezi zimasonyezanso kukwaniritsidwa kwakukulu kwa ulosi wa Yesu, kukwaniritsidwa kwamakono kumeneku kukumaphiphiritsiridwa ndi zimene zinachitika kuyambira mu 33 mpaka mu 70 C.E.
3. Polankhula za chizindikiro china, kodi ndizochitika zotani zowonjezereka zimene Yesu ananeneratu?
3 Luka atatchula nthaŵi za akunja, zolembedwa zogwirizana mu Mateyu, Marko, ndi Luka zimafotokoza mpambo winanso wa zochitika zimene zimaphatikizapo chizindikiro chowonjezera pa ‘chizindikiro [chachiungwe] cha mapeto a dongosolo la zinthu.’ (Mateyu 24:3, NW) (Patsamba 15, mfundo imeneyi m’cholembedwacho yasonyezedwa ndi mizera iŵiri yodukizadukiza.) Mateyu akuti: “Koma pomwepo, atapita masauko a masiku awo, dzuŵa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzaonetsa kuŵala kwake, ndi nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndi mphamvu za kumwamba zidzagwedezeka: ndipo pomwepo padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu; ndipo [pomwepo, NW] mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pamitambo ya kumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Ndipo iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwakukulu kwa lipenga, ndipo iwo adzasonkhanitsa osankhidwa ake ku mphepo zinayi, kuyambira malekezero a thambo kufikira malekezero ake ena.”—Mateyu 24:29-31.
Chisautso ndi Zochitika za Kumiyamba
4. Kodi ndimafunso ati amene akubuka ponena za zochitika za kumiyamba zimene Yesu anatchula?
4 Kodi ndiliiti pamene zimenezi zikakwaniritsidwa? Zolembedwa za Mauthenga Abwino atatu onsewo zimatchula zimene tingatche zochitika za kumiyamba—kudetsedwa kwa dzuŵa ndi mwezi ndi kugwa kwa nyenyezi. Yesu ananena kuti zimenezi zikatsatira ‘chisautso.’ Kodi Yesu anali kulingalira za chisautso chimene chinachitika mu 70 C.E., kapena kodi anali kulankhula za chisautso chachikulu chimene chidakali mtsogolo m’nthaŵi zathu zino?—Mateyu 24:29; Marko 13:24.
5. Kodi ndilingaliro lotani limene panthaŵi ina linakhulupiriridwa ponena za chisautso cha m’nthaŵi zamakono?
5 Chiyambire pamene nthaŵi za akunja zinatha mu 1914, anthu a Mulungu akhala ofunitsitsa kudziŵa za “chisautso chachikulu.” (Chivumbulutso 7:14) Kwazaka zambiri iwo anaganiza kuti mbali yoyamba ya chisautso chachikulu chamakono inayamba panthaŵi imodzimodzi imene Nkhondo Yadziko I inayamba, ndiyeno nkuima, kenako nkuyamba mbali yake yothera, “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu, Wamphamvuyonse.” Ngati zinalidi choncho, kodi nchiyani chimene chikachitika mkati mwa zaka makumi ambiri za kuima kwake za “mapeto a dongosolo”?—Chivumbulutso 16:14; Mateyu 13:39; 24:3; 28:20.
6. Kodi chiyani chimene chinalingaliridwa kukhala kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yesu wonena za zochitika za kumiyamba?
6 Eya, kunalingaliridwa kuti mkati mwa nyengo ya kuima imeneyi chizindikiro chachiungwe chikaoneka, kuphatikizapo ntchito yolalikira yochitidwa ndi anthu osonkhanitsidwa a Mulungu. Kunalingaliridwanso kuti zochitika za kumiyamba zikayembekezeredwa mkati mwa nyengo ya kuimayo pambuyo pa mbali yoyamba ya mu 1914-18. (Mateyu 24:29; Marko 13:24, 25; Luka 21:25) Chisamaliro chinasumikidwa pa zinthu zenizeni za m’mwamba—masetelaiti, zombo za mumlengalenga, cheza cha cosmic kapena gamma rays, ndi madoko kapena mabwalo potera pamwezi.
7. Kodi nchidziŵitso chowongoleredwa chotani chimene chaperekedwa ponena za chisautso chachikulu?
7 Komabe, Nsanja ya Olonda ya July 15, 1970, inapendanso ulosi wa Yesu, makamaka chisautso chachikulu chilinkudza. Inasonyeza kuti polingalira zimene zinachitika m’zaka za zana loyamba, chisautso chamakono sichikanakhala ndi mbali yoyamba mu 1914-18, nyengo ya kuima ya zaka makumi ambiri, ndi kuyambanso pambuyo pake. Magazini imeneyo inanena kuti: “‘Masauko aakulu’ monga ngati amene sadzaonekanso konse akali mtsogolomu, pakuti amatanthauza kuwonongedwa kwa ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga (kuphatikizapo Dziko Lachikristu) otsatiridwa ndi ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ pa Armagedo.”
8. Ndi lingaliro lowongoleredwa la chisautso chamakono, kodi ndimotani mmene lemba la Mateyu 24:29 linafotokozedwera?
8 Koma pa Mateyu 24:29 pamanena kuti zochitika za kumiyambazo zichitika ‘pomwepo, chitapita chisautso.’ Kodi zingakhale choncho motani? Nsanja ya Olonda ya October 1, 1975, inapereka lingaliro lakuti panopa ‘chisautso’ chimatanthauza chija chimene chinachitika kalelo mu 70 C.E. Koma kodi ndim’lingaliro lotani limene kukananenedwera kuti zochitika za kumiyamba zimenezo za m’nthaŵi yathu zinali kuchitika “pomwepo” pambuyo pa chochitika mu 70 C.E.? Kunalingaliridwa kuti kwa Mulungu zaka mazana ambiri za pakati pake zikakhala zazifupi. (Aroma 16:20; 2 Petro 3:8) Komabe, kufufuza kozama kwambiri kwa ulosi umenewu, makamaka wa pa Mateyu 24:29-31, kumasonyeza mafotokozedwe osiyana kotheratu. Zimenezi zimasonyeza mmene kuunika kuŵalira “mowonjezerekawonjezereka kufikira usana woti ngwee.” (Miyambo 4:18, American Standard Version)b Tiyeni tipende chifukwa chimene mafotokozedwe atsopano, kapena owongoleredwa, alili oyenerera.
9. Kodi ndimotani mmene Malemba Achihebri amaperekera chidziŵitso chomveketsa mawu a Yesu onena za zochitika m’miyamba?
9 Kwa anayi a atumwi ake, Yesu anapereka ulosi wonena za ‘dzuŵa likumadetsedwa, mwezi ukamasiya kuonetsa kuŵala kwake, ndi nyenyezi zikumagwa.’ Pokhala Ayuda, iwo anazindikira kanenedwe kotero mwa Malemba awo Achihebri, amene mwachitsanzo anatchula nthaŵi ya Mulungu yachiweruzo kukhala “tsiku la bwinja, ndi chipasuko, tsiku la mdima ndi la chisisira, tsiku la mitambo ndi lakuda bii” pa Zefaniya 1:15. Aneneri Achihebri osiyanasiyana anafotokozanso za kudetsedwa kwa dzuŵa, kusaunikira kwa mwezi, ndi nyenyezi zikumaleka kuonetsa kuŵala kwawo. Mukhoza kupeza kanenedwe kotero m’mauthenga aumulungu otsutsa Babulo, Edomu, Igupto, ndi ufumu wakumpoto wa Israyeli.—Yesaya 13:9, 10; 34:4, 5; Yeremiya 4:28; Ezekieli 32:2, 6-8; Amosi 5:20; 8:2, 9.
10, 11. (a) Kodi nchiyani chimene Yoweli analosera ponena za zinthu za kumiyamba? (b) Kodi ndimbali ziti za ulosi wa Yoweli zimene zinakwaniritsidwa mu 33 C.E., ndipo nziti zimene sizinatero?
10 Pamene anamva zimene Yesu ananena, Petro ndi atatu enawo mosakayikira anakumbukira ulosi wa Yoweli wopezeka pa Yoweli 2:28-31 ndi 3:15 wakuti: “Ndidzatsanulira mzimu wanga pa anthu onse, ndi ana anu aamuna ndi aakazi adzanenera, . . . Ndipo ndidzaonetsa zodabwitsa kuthambo ndi padziko lapansi, mwazi, ndi moto, ndi utsi tolo. Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndi mwezi udzasanduka mwazi, lisanadze tsiku la Yehova lalikulu ndi lowopsa.” “Dzuŵa ndi mwezi zada, ndi nyenyezi zibweza kuŵala kwawo.”
11 Monga momwe kwasimbidwira pa Machitidwe 2:1-4 ndi 14-21, pa Pentekoste wa 33 C.E., Mulungu anatsanulira mzimu wake woyera pa ophunzira 120, amuna ndi akazi omwe. Mtumwi Petro anadziŵikitsa kuti zimenezi ndizo zimene Yoweli ananeneratu. Komabe, bwanji za mawu a Yoweli onena za ‘dzuŵa likumada ndipo mwezi ukumasanduka mwazi ndipo nyenyezi zikumabweza kuŵala kwawo’? Palibe umboni uliwonse wosonyeza kuti zimenezi zinakwaniritsidwa mu 33 C.E. kapena mkati mwa nyengo yaitali ya zaka zoposa 30 ya mapeto a dongosolo la zinthu Lachiyuda.
12, 13. Kodi zochitika za kumiyamba zimene Yoweli ananeneratu zinakwaniritsidwa motani?
12 Mwachionekere mbali yotsirizira imeneyo ya ulosi wa Yoweli inali yogwirizana kwambiri ndi ‘kudza kwa tsiku la Yehova lalikulu ndi lowopsa’—chiwonongeko cha Yerusalemu. Nsanja ya Olonda ya May 15, 1967, inati ponena za chisautso chimene chinagwera Yerusalemu mu 70 C.E.: “Limenelo linalidi ‘tsiku la Yehova’ ponena za Yerusalemu ndi ana ake. Ndipo mogwirizana ndi tsiku limenelo panali ‘mwazi wochuluka ndi moto ndi utsi tolo,’ dzuŵa likuleka kuunikira mkhalidwe wowopsa wa mzindawo masana, ndipo mwezi ukumakumbutsa kukhetsedwa kwa mwazi, osati kuŵala kwake kwamtendere usiku.”c
13 Inde, mofanana ndi maulosi ena amene taona, zochitika za kumiyamba zimene Yoweli ananeneratu zikakwaniritsidwa pamene Yehova akapereka chiweruzo. Mmalo mwa kuchitika m’nyengo yonseyo ya nthaŵi ya mapeto a dongosolo Lachiyuda, kudetsedwa kwa dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi kunachitika pamene magulu akupha anaukira Yerusalemu. Moyenerera, tingayembekezere kukwaniritsidwa kokulirapo kwa mbali imeneyo ya ulosi wa Yoweli pamene kuwonongedwa kwa dongosolo la zinthu lilipoli kochitidwa ndi Mulungu kuyambika.
Nchisautso Chiti Chimene Chidzachitika Zisanayambe Zochitika za Kumiyamba?
14, 15. Kodi ulosi wa Yoweli umayambukira motani kumvetsetsa kwathu Mateyu 24:29?
14 Kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yoweli (mogwirizana ndi maulosi ena ofotokoza zofanana) kumatithandiza kumvetsetsa mawu a pa Mateyu 24:29. Mwachionekere, zimene Yesu analankhula ponena za ‘kudetsedwa kwa dzuŵa, kusaunikira kwa mwezi, ndi kugwa kwa nyenyezi’ sizimatanthauza zinthu zochitika mkati mwa zaka makumi ambiri a mapeto a dongosolo lilipoli, zonga zombo za mumlengalenga, kutera pamwezi, ndi zina zotero. Ayi, anali kunena za zochitika zogwirizanitsidwa ndi “tsiku la Yehova lalikulu ndi lowopsa,” chiwonongeko chomwe chilinkudza.
15 Zimenezi zimatithandiza kumvetsetsa bwino kwambiri mmene zochitika za kumiyamba zikachitikira “pomwepo, atapita masauko.” Yesu sanali kunena za chisautso chimene chinathera mu 70 C.E. Mmalo mwake, anali kunena za kuyambika kwa chisautso chachikulu chimene chikagwera dongosolo la dziko mtsogolo, chikumatsiriza “kukhalapo” kwake kolonjezedwako. (Mateyu 24:3, NW) Chisautso chimenecho chidakali mtsogolo mwathu.
16. Kodi nchisautso chiti chimene lemba la Marko 13:24 linali kusonyako, ndipo chifukwa ninji?
16 Bwanji za mawu a pa Marko 13:24 akuti: “M’masiku [amenewo, NW], chitatha chisautso chimenecho, dzuŵa lidzadetsedwa, ndi mwezi sudzapatsa kuunika kwake”? Panopo, mawu onse aŵiriwo akuti “amenewo” ndi “chimenecho” ali mipangidwe ya liwu Lachigiriki lakuti e·keiʹnos, pronauni yosonyeza kanthu kena kokhala patali. E·keiʹnos angagwiritsiridwe ntchito kusonyeza kanthu kena kamene kanachitika kalekale (kapena kotchulidwapo kale) kapena kanthu kena kamtsogolo kwambiri. (Mateyu 3:1; 7:22; 10:19; 24:38; Marko 13:11, 17, 32; 14:25; Luka 10:12; 2 Atesalonika 1:10) Chotero, lemba la Marko 13:24 likutchula “chisautso chimenecho,” osati chisautso chimene chinadzetsedwa ndi Aroma, koma chochita champhamvu cha Yehova pamapeto a dongosolo lilipoli.
17, 18. Kodi nchidziŵitso chotani chimene buku la Chivumbulutso limapereka ponena za mmene chisautso chachikulu chidzachitikira?
17 Machaputala 17 mpaka 19 a Chivumbulutso amagwirizana bwino lomwe ndi kutsimikizira chidziŵitso chowongoleredwa chimenechi cha pa Mateyu 24:29-31, Marko 13:24-27, ndi Luka 21:25-28. Motani? Mauthenga Abwino amasonyeza kuti chisautso chachikulu chimenechi sichidzayamba ndi kutha kamodzi nkamodzi. Chitayamba, anthu ena osamvera adzakhalabe ali ndi moyo kuti aone “chizindikiro cha Mwana wa munthu” ndi kuchitapo kanthu—kulira ndipo, monga momwe kwanenedwera pa Luka 21:26, “kukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza ku dziko lapansi.” Mantha aakulu amenewo adzakhalapo chifukwa cha kuona kwawo “chizindikiro” chimene chidzasonyeza chiwonongeko chawo choyandikira.
18 Nkhani ya m’Chivumbulutso imasonyeza kuti chisautso chachikulu chamtsogolocho chidzayamba pamene “nyanga” zokonzekera nkhondo za “chilombo” cha padziko lonse zidzatembenukira “mkazi wachigololo,” Babulo Wamkulu.d (Chivumbulutso 17:1, 10-16) Koma anthu ambiri adzatsala, pakuti mafumu, amalonda, amalinyero, ndi anthu ena adzalira maliro a kutha kwa chipembedzo chonyenga. Mosakayikira ambiri adzazindikira kuti chiweruzo chawo ndicho chidzatsatira.—Chivumbulutso 18:9-19.
Kodi Nchiyani Chimene Chidzadza?
19. Kodi nchiyani chimene tingayembekezere pamene chisautso chachikulu chiyamba?
19 Zigawo za Mauthenga Abwino m’buku la Mateyu, Marko, ndi Luka zimagwirizana ndi Chivumbulutso machaputala 17-19 a Chivumbulutso kupereka chidziŵitso chachikulu cha zimene zidzachitika posachedwapa. Panthaŵi yoikidwiratu ya Mulungu, chisautso chachikulu chidzayamba ndi kuukiridwa kwa ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, (Babulo Wamkulu). Chiukirochi chidzakhala chachikulu makamaka pa Dziko Lachikristu, limene limafanana ndi Yerusalemu wosakhulupirikayo. ‘Pomwepo, itatha’ mbali imeneyi ya chisautso “kudzakhala zizindikiro pa dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi padziko lapansi chisauko [chopanda china chofanana nacho] cha mitundu ya anthu.”—Mateyu 24:29; Luka 21:25.
20. Kodi nzochitika za kumiyamba zotani zimene tingayembekezerebe?
20 Kodi ndim’lingaliro lotani limene ‘dzuŵa lidzadetsedwera, mwezi ukumaleka kuunika, nyenyezi zikumagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu za kumwamba zikumagwedezeka’? Mosakayikira, kuchiyambiyambi kwa chisautso chachikulu, zounikira zambiri—atsogoleri omveka a zipembedzo—adzakhala atavumbulidwa ndi kuchotsedwa ndi “nyanga khumi” zotchulidwa pa Chivumbulutso 17:16. Mosakayikira maulamuliro andale nawonso adzakhala atagwedezeka. Kodi pangadzakhalenso zochitika zowopsa kuthambo lenileni? Mwinamwake zidzaterodi, ndipo zowopsa kwambiri kuposa zija zofotokozedwa ndi Josephus kukhala zitachitika kumapeto kwa dongosolo Lachiyuda. Tidziŵa kuti kale, Mulungu anasonyeza mphamvu yake mwa kuchititsa masoka otero, ndipo akhoza kuteronso.—Eksodo 10:21-23; Yoswa 10:12-14; Oweruza 5:20; Luka 23:44, 45.
21. Kodi “chizindikiro” chamtsogolo chidzachitika motani?
21 Panopa olemba Mauthenga Abwino atatu onsewo akugwiritsira ntchito liwu lakuti toʹte (pomwepo) kufotokoza chochitika chotsatira. “Pomwepo padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu.” (Mateyu 24:30; Marko 13:26; Luka 21:27) Chiyambire Nkhondo Yadziko I, ophunzira owona a Yesu azindikira chizindikiro chachiungwe cha kukhalapo kwake kosaoneka, pamene kuli kwakuti anthu ochuluka sanachizindikire. Koma pa Mateyu 24:30 pakutchula “chizindikiro” china chodzaonekera mtsogolo, chija cha “Mwana wa munthu,” ndipo mitundu yonse idzaumirizika kuchiona. Pamene Yesu adza ndi mitambo mosaoneka, anthu otsutsa padziko lonse adzakakamizika kuzindikira ‘kudza’ kumeneko (Chigiriki er·khoʹme·non) chifukwa cha kusonyezedwa kodabwitsa kwa mphamvu zake zaufumu.—Chivumbulutso 1:7.
22. Kodi chiyambukiro cha kuona “chizindikiro” cha pa Mateyu 24:30 chidzakhala chotani?
22 Lemba la Mateyu 24:30 likugwiritsiranso ntchito toʹte kusonyeza chimene chikutsatira. Ndiyeno mitunduyo, pozindikira chotsatirapo cha mkhalidwe wawo, idzadziguguda pachifuŵa ndi kulira, mwinamwake ikumazindikira kuti chiwonongeko chawo chayandikira. Nzosiyana chotani nanga ndi ife atumiki a Mulungu, pakuti tidzakhoza kutukula mitu yathu, podziŵa kuti chiwomboledwe chayandikira! (Luka 21:28) Pa Chivumbulutso 19:1-6 pamasonyezanso olambira owona kumwamba ndi padziko lapansi akumakondwera chifukwa cha kuchotsedwa kwa mkazi wachigololo wamkuluyo.
23. (a) Kodi nchiyani chimene Yesu adzachita kulinga kwa osankhidwa? (b) Kodi nchiyani chimene chinganenedwe ponena za kutengeredwa kumwamba kwa otsalira?
23 Ulosi wa Yesu ukupitiriza pa Marko 13:27 kuti: “Pamenepo [toʹte] adzatuma angelo, nadzasonkhanitsa osankhidwa ake ochokera ku mphepo zinayi, kuyambira ku malekezero ake a dziko lapansi, ndi kufikira ku malekezero a thambo.” Panopo Yesu akunena za otsalira a 144,000 “osankhidwa” amene adakali ndi moyo padziko lapansi. Kuchiyambiyambi kwa mapeto a dongosolo la zinthu, ophunzira odzozedwa a Yesu ameneŵa analoŵetsedwa muumodzi wateokratiki. Komabe, malinga ndi tsatanetsatane wogwiritsiridwa ntchito, pa Marko 13:27 ndi Mateyu 24:31 pamafotokoza kanthu kena. “Ndi kulira kwakukulu kwa lipenga,” otsalira a “osankhidwa” amenewo adzasonkhanitsidwa kuyambira kumalekezero a dziko lapansi. Kodi adzasonkhanitsidwa motani? Mosakayikira, ‘adzasindikizidwa chizindikiro’ ndi kudziŵidwa bwino lomwe ndi Yehova monga mbali ya “oitanidwa, ndi osankhika ndi okhulupirika.” Ndipo panthaŵi yoikidwa ndi Mulungu, adzasonkhanitsidwira kumwamba kukakhala mafumu ndi ansembe.e Zimenezi zidzadzetsa chisangalalo kwa iwo ndi kwa atsamwali awo okhulupirika, a “khamu lalikulu,” amene iwo eniwo adzalembedwa chizindikiro cha “kutuluka m’chisautso chachikulu” kuti alandire madalitso padziko lapansi laparadaiso.—Mateyu 24:22; Chivumbulutso 7:3, 4, 9-17; 17:14; 20:6; Ezekieli 9:4, 6.
24. Kodi pa Mateyu 24:29-31 pamavumbula tsatanetsatane wotani wa zochitika zilinkudza?
24 Pamene atumwi ananena kuti, “Tiuzeni . . . ,” yankho la Yesu linaphatikizapo zambiri kuposa zimene anakhoza kumvetsetsa. Komabe, m’moyo wawo anakondwera kuona kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosi wake. Kupenda kwathu yankho la Yesu kwasumikidwa pa mbali ya ulosi wake imene idzakwaniritsidwa mtsogolomu posachedwa. (Mateyu 24:29-31; Marko 13:24-27; Luka 21:25-28) Taona kale kuti chiwomboledwe chathu chikuyandikira. Tingathe kuyang’anira mwachidwi chiyambi cha chisautso chachikulu, pomwepo chizindikiro cha Mwana wa munthu, ndipo pomwepo kusonkhanitsidwa kwa osankhidwa kochitidwa ndi Mulungu. Pomalizira pake, monga Wakupha wa Yehova pa Armagedo, Mfumu ndi Wankhondo wathu, Yesu wokhazikitsidwa pampando wachifumu, ‘adzamaliza kulaka kwake.’ (Chivumbulutso 6:2, NW) Tsiku la Yehova limenelo, pamene alipsira, lidzadza monga mbali yaikulu yomalizira ya mapeto a dongosolo la zinthu amene adziŵikitsa tsiku la Ambuye Yesu kuyambira 1914 kumkabe mtsogolo.
25. Kodi ndimotani mmene tingakhalire ndi phande m’kukwaniritsidwa kwamtsogolo kwa lemba la Luka 21:28?
25 Pitirizanibe kupindula inu mwini ndi chiphunzitso chaumulungu, kotero kuti mukachitepo kanthu pa kukwaniritsidwa kumene kudakali mtsogolo kwa mawu a Yesu akuti: “Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira.” (Luka 21:28) Ha, pali mtsogolo mwabwino chotani nanga kwa osankhidwawo ndi khamu lalikulu pamene Yehova ayeretsa dzina lake loyeralo!
[Mawu a M’munsi]
a Mboni za Yehova nzokondwa kupereka umboni wa zimenezi, zikumasonyeza mmene zochitika m’tsiku lathu zimakwaniritsira ulosi wa Baibulo.
b Mafotokozedwe owonjezereka anali pamasamba 296-323 m’buku lakuti God’s Kingdom of a Thousand Years Has Approached, lofalitsidwa mu 1973 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., ndi mu Nsanja ya Olonda ya March 15, 1983, pamasamba 18-24.
c Josephus analemba za zochitika pakati pa kuukira Yerusalemu koyamba kwa Aroma (66 C.E.) ndi chiwonongeko chake kuti: “Usikuwo kunaulika mkuntho wowononga; namondwe anawomba, mvula yamkokomo inagwa, mphezi zinang’anima mosalekeza, mabingu anagunda mochititsa mantha, dziko linanjenjemera ndi phokoso logonthetsa m’khutu. Tsoka la mtundu wa anthu linasonyezedweratu ndi kunyonyotsoka kwa mpangidwe wonse wa zinthu kumeneku, ndipo palibe aliyense amene anakayikira kuti zizindikirozi zinasonyeza tsoka lopanda lina lofanana nalo.”
d Chimene Yesu anatcha “masauko aakulu” ndi “chisautso” chinali kuwonongedwa kwa dongosolo Lachiyuda, monga tanthauzo lake loyamba. Koma m’mavesi amene ali ndi tanthauzo la m’tsiku lathu lokha, m’malemba oyambirira, anagwiritsira ntchito phatikizo lotsimikizira lakuti “cho,” akumati “chisautso chachikulucho.” (Mateyu 24:21, 29; Marko 13:19, 24) Lemba la Chivumbulutso 7:14 linatcha chochitika cha mtsogolo chimenechi “chisautso chachikulu,” kwenikweni “chisautso chachikulucho.”
e Onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1990.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi ndimotani mmene mbali za lemba la Yoweli 2:28-31 ndi Yoweli 3:15 zinakwaniritsidwira m’zaka za zana loyamba?
◻ Kodi nchisautso chiti chimene lemba la Mateyu 24:29 likunena, ndipo chifukwa ninji tikunena motero?
◻ Kodi nzochitika za kumiyamba ziti zimene lemba la Mateyu 24:29 likusonyako, ndipo kodi ndimotani mmene zingachitikire pomwepo chitatha chisautso?
◻ Kodi lemba la Luka 21:26, 28 lidzakwaniritsidwa motani mtsogolo?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Malo a kachisi
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.