MUTU 8
“Kodi Yehova Akufuna Chiyani kwa Iwe?”
1, 2. N’chifukwa chiyani tingalimbikitsidwe ndi zimene Yehova anachita pamene anthu ake ankachita makhalidwe oipa kwambiri?
TAYEREKEZERANI kuti mukuona mtsikana ali njenjenje chifukwa cha mantha atamva kugogoda mwamphamvu pachitseko cha nyumba yawo. Mtsikanayo akudziwa kuti amene akugogodayo ndi munthu wamalonda wokonda katangale amene akufuna ndalama zomwe makolo ake anakongola. Munthuyo wakhala akubera anthu ambiri pogwiritsa ntchito masikelo achinyengo komanso pochita katapila. Ndipo pofuna kuti asapatsidwe chilango, iye amapereka ziphuphu kwa oweruza n’cholinga choti asamathandize anthu oponderezedwawo. Mtsikanayo akuona kuti alibe womuthandiza chifukwa bambo ake anasiya mayi ake n’kukakwatira mkazi wachitsikana. Choncho, iye ndi mayi ake asowa mtengo wogwira moti akhoza kugulitsidwa n’kukhala akapolo.
2 Nkhani imeneyi ndi chitsanzo cha zinthu zoipa zomwe Ayuda ankachita kalelo ndipo aneneri 12 anadzudzula mwamphamvu Ayudawo. (Amosi 5:12; 8:4-6; Mika 6:10-12; Zefaniya 3:3; Malaki 2:13-16; 3:5) Kodi inuyo mukanakhalapo pa nthawiyo mukanatani chifukwa cha zoipa zomwe zinkachitikazo? Ngakhale kuti chitsanzochi chikusonyeza kuti anthuwo ankachita zinthu zoipa kwambiri, n’zolimbikitsa kuona kuti Yehova ankawachitirabe zinthu zabwino. Mukamawerenga mabuku 12 amenewa, mungaone kuti Mulungu ankalimbikitsa anthu ake kuti akhale ndi makhalidwe abwino. Mawu olimbikitsa amene Mulungu anauza anthu akewo angakuthandizeninso inuyo kuti mukhale ndi makhalidwe abwino, muzichita zabwino, ndiponso kuti muzimutamanda. Popeza tsiku la Yehova lachiweruzo latsala pang’ono kufika, mukamamvera uthenga wolimbikitsa umene uli m’mabukuwa mungadziwe zimene Mulungu akufuna kuti inuyo muzichita. Poyamba, tiyeni tione kaye zimene zinkachitika m’nthawi ya Mika, cha m’ma 700 B.C.E.
KODI YEHOVA AKUFUNA KUTI TIZICHITA CHIYANI?
3, 4. (a) M’buku la Mika, kodi Yehova akutichonderera kuti tizichita chiyani? (b) Kodi funso la pa Mika 6:8 likukukhudzani bwanji inuyo panokha?
3 Mukamawerenga buku la Mika, mwina poyamba mungaganize kuti m’bukuli mwangokhala uthenga wodzudzula wokhawokha wopita kwa Aisiraeli omwe anali osamvera. N’zoona kuti Yehova ankaona makhalidwe oipa kwambiri amene anthu ake ankachita, ndipo ananena kuti ena ‘ankadana ndi zinthu zabwino, n’kumakonda zinthu zoipa.’ (Mika 3:2; 6:12) Komabe ngakhale kuti m’bukuli muli uthenga wowadzudzula, mulinso uthenga wowachonderera kuti azichita zabwino. Ndipotu uthengawu uli m’gulu la mauthenga olimbikitsa kwambiri m’Baibulo lonse. Mika anathandiza anthuwo kuganizira za Mulungu, yemwe ndi wachilungamo, pamene anafunsa funso lofunika kuliganizira mozama. Iye anati: “Kodi Yehova akufuna chiyani kwa iwe? Iye akufuna kuti uzichita chilungamo, ukhale wokoma mtima ndiponso uziyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.”—Mika 6:8.
4 Kodi mukutha kuona zimene Mlengi wathu anachonderera kuti tizichita? Mwachikondi, iye anatichonderera kuti tizichita zinthu zabwino, ndipo tisatengeke ndi zinthu zoipa zomwe zachuluka m’dzikoli. Yehova amatikhulupirira chifukwa amadziwa kuti ndife anthu ake okhulupirika ndipo tikuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. Ndiyeno kodi inuyo mungayankhe bwanji mutafunsidwa kuti: ‘Kodi Yehova akufuna chiyani kwa inu?’ Kodi mukuona kuti kutsatira mfundo za Mulungu kwakuthandizani kusintha zinthu ziti pa moyo wanu? Nanga ndi zinthu zinanso ziti zimene muyenera kusintha? Mukamayesetsa kutsatira mfundo za Mulungu, moyo wanu udzakhala wabwino komanso ubwenzi wanu ndi Mulungu udzakhala wolimba kwambiri. Popeza kuti dziko lonse likhala paradaiso posachedwapa, tikulimbikitsidwa kuti: “Bzalani mbewu za chilungamo ndipo kololani zipatso za kukoma mtima kosatha. Limani munda panthaka yabwino pamene muli ndi nthawi yofunafuna Yehova, kufikira iye atabwera ndi kukupatsani malangizo onena za chilungamo.” (Hoseya 10:12) Tsopano tiyeni tikambirane mfundo zikuluzikulu zopezeka m’malangizo abwino kwambiri a pa Mika 6:8.
AKUFUNA KUTI TIKHALE ‘ODZICHEPETSA’
5. N’chifukwa chiyani ‘kudzichepetsa’ n’kofunika pamene tikuyenda ndi Mulungu?
5 N’zochititsa chidwi kuti Mika ananena kuti Yehova akufuna kuti ‘tiziyenda naye modzichepetsa.’ Ndipotu kukhala munthu wodzichepetsa n’kothandiza kwambiri chifukwa “nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.” (Miyambo 11:2) Munthu wodzichepetsa amazindikira kuti pali zinthu zina zomwe sangakwanitse kuchita chifukwa cha uchimo umene tinatengera kwa Adamu. Choncho kuvomereza kuti ndife opanda ungwiro ndi chinthu choyamba komanso chofunika kwambiri kuti tikwanitse kupewa kuchita machimo mwadala.—Aroma 7:24, 25.
6. Kodi kuzindikira mavuto amene angabwere chifukwa chochita tchimo kungatithandize bwanji?
6 N’chifukwa chiyani kudzichepetsa n’kofunika kwambiri kuti munthu athe kupewa kuchita tchimo mwadala? Kudzichepetsa kungathandize munthu kuzindikira kuti tchimo ndi lamphamvu kwambiri. (Salimo 51:3) Hoseya akutithandiza kumvetsa zoti tingathe kukopeka mosavuta ndi tchimo komanso kuti nthawi zonse zotsatira zake zimakhala zoopsa. Mwachitsanzo, Yehova anachenjeza Ayuda omwe anali osamvera kuti ‘adzawaimba mlandu.’ Zimenezi zikusonyezeratu kuti Yehova anali wokonzeka kupereka chilango kwa anthu ake omwe ankachimwa mwadalawo. Komabe mwina anthuwo ankaganiza kuti Mulungu sangawalange popeza kuti nthawi zambiri munthu yemwe akuchita tchimo amaganiza kuti palibe chomwe chingamuchitikire komanso tchimolo limalamulira zochita zonse za moyo wake. Komanso anthu omwe akuchita tchimo sakhala pa ubwenzi ndi Mulungu, ndipo akapanda kusintha, zinthu zimafika poipa kwambiri chifukwa ‘zochita zawo zimawalepheretsa kubwerera kwa Mulungu wawo.’ Munthu amene amakonda kuchita machimo mwadala, khalidwe lake limaipa kwambiri moti amafika ‘pochita zinthu zopweteka anzake’ nthawi zonse. Kuwonjezera pamenepa, munthu amene akuchita machimo, zinthu sizimamuyendera bwino pa moyo wake. N’zoona kuti kwakanthawi angaoneke ngati zinthu zikumuyendera bwino, koma Mulungu sangadalitse munthu wochimwa amene sakulapa.—Hoseya 1:4; 4:11-13; 5:4; 6:8.
7. Kodi anthu odzichepetsa amachita chiyani akamva malangizo a Yehova?
7 Anthu odzichepetsa amazindikiranso kuti amafunikira kutsogoleredwa ndi Mulungu n’cholinga choti apewe tchimo komanso mavuto amene angabwere chifukwa cha tchimolo. Mika analosera kuti m’nthawi yathu ino anthu ambirimbiri adzakhala ofunitsitsa ‘kuphunzitsidwa njira za Yehova’ ndiponso ‘kuyenda m’njira zakezo.’ Anthu amenewa, omwe ndi ofatsa, akufunafuna “malamulo” ndi “mawu a Yehova.” N’kutheka kuti inuyo mukusangalala kwambiri chifukwa muli m’gulu la anthu amene akuyesetsa ‘kuyenda m’dzina la Yehova,’ pochita zimene iye akufuna. Ngakhale zili choncho, mofanana ndi Mika, mwina inunso mungafune kudziwa zinthu zinanso zimene zingakuthandizeni kuti mukhalebe “woyera.” (Mika 4:1-5; 6:11) Ndipotu mukamayesetsa kukhala wodzichepetsa komanso mukamachita zimene Yehova akufuna, mudzakhalabe “woyera.”
AKUFUNA KUTI TIKHALE NDI MAKHALIDWE ABWINO
8. Kodi inuyo mumaona kuti makhalidwe a anthu masiku ano ndi otani?
8 Yehova akufuna kuti tikhale otetezeka mwauzimu komanso kuti tikhale ndi moyo wabwino. Choncho akutipempha kuti tikhale ndi makhalidwe abwino ngakhale kuti tikukhala m’dziko lomwe anthu ambiri ali ndi makhalidwe oipa. (Malaki 2:15) Masiku ano zinthu zolaula zili paliponse. Ndipo anthu ambiri amaona kuti palibe vuto lililonse kuonera mafilimu olaula, kuwerenga nkhani zokhudza kugonana, kuona zithunzi zolaula kapena kumvetsera nyimbo zolaula. Kuwonjezera pamenepa, pali anthu ena amene salemekeza akazi moti amangowaona ngati anthu ogonana nawo basi. Mwinanso ana a sukulu angamanene nthabwala zotukwana kapena mawu ena ophiphiritsira zogonana. Ndiyeno kodi mungatani kuti musatengere zimenezi?
9. M’nthawi ya aneneri 12, kodi anthu ambiri anasonyeza bwanji kuti sankatsatira mfundo za Yehova?
9 M’mabuku a aneneri 12 amene tikukambiranawa, muli malangizo ofunika kwambiri pa nkhaniyi. M’nthawi ya aneneri 12 amenewo, kunalibe nyumba zoonetsera mafilimu kapena mavidiyo. Komabe, pa nthawiyo kunali zithunzi ndi ziboliboli zosonyeza maliseche a mwamuna, anthu ankachita uhule womwe ankati ndi wopatulika komanso ankachita zachiwerewere mopanda manyazi. (1 Mafumu 14:24; Yesaya 57:3, 4; Habakuku 2:15) Zimene ena mwa aneneriwa analemba zikutithandiza kuona umboni wa zimenezi. Iwo analemba kuti: “Pakuti amuna akumatengana ndi mahule ndipo akumaperekera nsembe limodzi ndi mahule aakazi a pakachisi.” Komanso analemba kuti: “Mwana pamodzi ndi bambo ake akugona ndi mtsikana mmodzi ndi cholinga chofuna kuipitsa dzina langa loyera.” Ndipo amuna ena nthawi zonse ankapereka “malipiro a mahule” pochita miyambo yokhudzana ndi mphamvu zobereka.a Anthu ankachita chigololo mwachisawawa chifukwa ankasiya mabanja awo n’kupita kwa amuna kapena akazi ena omwe ‘ankawakonda kwambiri.’—Hoseya 2:13; 4:2, 13, 14; Amosi 2:7; Mika 1:7.
10. (a) Kodi khalidwe la chiwerewere limayamba bwanji? (b) Kodi anthu a Mulungu ankachita zinthu ziti polambira zomwe zinali ngati dama?
10 Mwina mukudziwa kuti khalidwe la chiwerewere limayambira mumtima. (Maliko 7:20-22) Choncho ponena za anthu ake omwe anali okonda chiwerewere, Yehova ananena kuti “mtima wadama,” kapena kuti mtima wokonda kugonana, “wawasocheretsa” komanso kuti “amangokhalira kuchita khalidwe lotayirira.”b (Hoseya 4:12; 6:9) Pofotokoza mmene zinthu zinalili pa nthawiyo, Zekariya ananena kuti m’dzikolo munali “mzimu wonyansa.” (Zekariya 13:2) Anthuwo ankachita khalidwe lotayirira komanso ankanyalanyaza kapena kunyoza mfundo za Yehova ndiponso ulamuliro wake. Choncho kuti munthu akhalenso ndi makhalidwe abwino, ankafunika kusintha kwambiri maganizo ndi mtima wake. Kuganizira zimenezi kungathandize Mkhristu kuti aziyamikira kwambiri malangizo ochokera kwa Mulungu, chifukwa angamuthandize kupewa chiwerewere komanso mavuto amene angabwere chifukwa cha khalidwe limeneli.
AKUFUNA KUTI TIKHALE OYERA
11. Kodi ndi mavuto ena ati amene amabwera chifukwa cha khalidwe lachiwerewere?
11 N’kutheka kuti mwaonapo kuti anthu amene ali ndi khalidwe lachiwerewere, mabanja awo sachedwa kutha ndiponso ana awo amasowa malangizo abwino ochokera kwa makolo. Komanso anthu akhalidweli amatha kutenga matenda oopsa ndipo ambiri amataya moyo wawo ndiponso wa ana osabadwa, pochotsa mimba. Anthu amene amanyalanyaza malangizo a Mlengi wathu pa nkhani yokhudza kugonana, kawirikawiri amakumana ndi mavuto. Mika analemba kuti: “Dzikoli liwonongedwa chifukwa chakuti ladetsedwa ndipo kuwonongedwako kukhala kopweteka.” (Mika 2:10) Mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambiri kwa anthu amene akufunitsitsa kulambira Mulungu woona kuti azipewa maganizo oipa omwe angaipitse mtima wawo.—Mateyu 12:34; 15:18.
12. Kodi timapeza madalitso otani tikamamvera malamulo a Yehova pa nkhani yokhudza kugonana?
12 Sikuti Akhristu amapewa chiwerewere chifukwa chongoopa matenda kapena kubereka ana apathengo. Koma iwo amachita zimenezi chifukwa amakonda malamulo a Mulungu okhudza kugonana, ndipo amawatsatira. Polenga anthu, Yehova anawapatsa chilakolako cha kugonana kuti ikhale njira imodzi yomwe anthu okwatirana angamasonyezerane chikondi. Choncho anthu okwatirana okha ndi amene ayenera kugonana. Zimenezi zimathandiza kuti mwamuna ndi mkazi wake azikondana kwambiri ndipo nthawi zina angabereke ana. Komabe, anthu osakwatirana akamagonana, zimabweretsa mavuto aakulu monga mmene aneneri 12 akusonyezera. Aneneriwa akusonyeza kuti Mulungu anasiya kukonda anthu amene ankachita chiwerewere. Kusiya kukondedwa ndi Mulungu kunali koopsa kwambiri pa nthawiyo, ndipo n’koopsanso kwambiri masiku ano.
13. Kodi tingatani kuti tipewe kapena ‘kusiya dama’?
13 Hoseya analimbikitsa anthu a m’nthawi yake kuti ‘asiye dama lawo.’ Kuti akwanitse kuchita zimenezi, anthuwo ankafunika kusintha makhalidwe awo n’kuyamba kuchita zinthu zabwino. (Hoseya 2:2) Masiku anonso tingachite bwino ngati titapewa zinthu zimene zingatichititse makhalidwe oipa. Mwachitsanzo, n’kutheka kuti mungamakumane ndi mayesero enaake mobwerezabwereza kusukulu kapena kudera limene mukukhala. Koma mwina simungathe kusintha sukulu kapena kusamukira kudera lina. Ngakhale zili choncho, pali zinthu zina zimene mungachite kuti musakumane ndi mayeserowo, ndipo mungapewe “dama.” Mwa zina, nthawi zonse muzidziwitsa anthu ena kuti ndinu Mkhristu wa Mboni za Yehova. Mwaulemu ndiponso momveka bwino, muziwauza mfundo zimene mumayendera komanso zimene mumakhulupirira. Muzionetsetsa kuti ena akudziwa zoti nthawi zonse mumatsatira mfundo zabwino za Yehova. (Amosi 5:15) Njira inanso imene ingakuthandizeni kupewa “dama,” ndiyo kupewa zinthu zolaula komanso zinthu zokayikitsa zimene anthu ena amaona kuti n’zosangalatsa. Kuti muchite zimenezi, nthawi zina mungafunike kutaya mabuku oipa. Kapena mungafunike kupeza anzanu atsopano amene amakonda Yehova ndiponso amene amakulimbikitsani kuti muzichita zimene Yehovayo akufuna. (Mika 7:5) Zoonadi, mothandizidwa ndi Yehova, mungapewe khalidwe lachiwerewere lomwe ndi lofala m’dzikoli.
AKUFUNA KUTI ‘TIKHALE OKOMA MTIMA’
14, 15. (a) Kodi ‘kukhala wokoma mtima’ kumatanthauza chiyani? (b) Kodi ‘kukhala wokoma mtima’ kungatithandize bwanji kuti tizichita zinthu mwachilungamo?
14 Mika ananenanso kuti Yehova akufuna kuti ‘tikhale okoma mtima.’ Munthu wokoma mtima amachita zinthu zabwino osati zoipa, komanso amakhala ndi khalidwe labwino. Kuti munthu akhaledi wokoma mtima amafunika kuti akhale woona mtima komanso wachilungamo m’zochita zake zonse. M’Mutu 6 wa buku lino tinakambirana mbali zina zofunika kwambiri pa moyo wathu, monga zokhudza bizinezi ndi ndalama, ndipo tinaona kuti kuchita zinthu mwachilungamo pa nkhani zimenezi n’kofunika kwambiri. Koma pali zinthu zinanso pa moyo wathu zimene tikufunikira kuchita mwachilungamo, moona mtima ndiponso mokoma mtima.
15 Anthu okoma mtima ndiponso amene amachitira ena zinthu zabwino amayesetsa kuchita zinthu mwachilungamo. Polankhula ndi Aisiraeli amene sankapereka chuma chawo kuti chithandizire pomulambira, Yehova anawauza kuti: “Inu mukundibera.” (Malaki 3:8) Kodi masiku ano munthu ‘angabere’ Mulungu m’njira ziti? Mwachitsanzo, Mkhristu wina angakhale ndi mwayi wosamalira ndalama zimene Akhristu ena apereka kuti zithandizire pa ntchito yolalikira. Kodi ndalama zimenezi mwiniwake ndi ndani? N’zodziwikiratu kuti mwiniwake ndi Yehova, chifukwa Akhristuwo anapereka kuti zithandizire pa ntchito yokhudzana ndi kumulambira. (2 Akorinto 9:7) Kodi munthu angabwereke ndalama zimenezi kuti agwiritse ntchito pa zinthu zina zadzidzidzi zimene zamuchitikira? Kapena kodi munthu angagwiritse ntchito ndalama zimenezi popanda chilolezo? Ayi, chifukwa kuchita zimenezi n’kubera Mulungu. Komanso munthu yemwe angachite zimenezi ndiye kuti sanachite zinthu mokoma mtima kapena mwachilungamo kwa anthu amene anapereka ndalamazo kuti zithandizire polambira Mulungu.—Miyambo 6:30, 31; Zekariya 5:3.
16, 17. (a) Kodi anthu ena anasonyeza bwanji kuti anali adyera m’nthawi ya Amosi ndiponso ya Mika? (b) Kodi Mulungu amaona bwanji anthu adyera?
16 Akhristu omwe ndi okoma mtima komanso a khalidwe labwino amapewanso dyera. M’nthawi ya Amosi, anthu ochuluka anali adyera kwambiri. Pofuna ‘kupeza siliva,’ anthu adyera amene anali ouma mtima ankagulitsa ‘anthu olungama,’ kapena kuti anthu amene ankalambira nawo limodzi Mulungu. (Amosi 2:6) Zimenezi zinkachitikanso m’nthawi ya Mika. Anthu olemera a ku Yuda ankalanda nyumba ndi minda ya anthu amene sakanatha kudziteteza, ndipo nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito mphamvu. (Mika 2:2; 3:10) Polanda minda ya anthu ena, anthu adyerawo ankaphwanya Chilamulo cha Yehova, monga lamulo lomaliza pa Malamulo Khumi komanso malamulo ena oletsa kugulitsa malo a makolo awo.—Ekisodo 20:13, 15, 17; Levitiko 25:23-28.
17 Masiku ano sizichitika kawirikawiri kuti anthu agulitse anzawo kuti akhale akapolo ngati mmene zinalili m’nthawi ya aneneri. Koma zikuoneka kuti anthu ambiri amadyera anzawo masuku pamutu pa nkhani zokhudza ndalama. Mkhristu yemwe ndi wokoma mtima amayesetsa kupewa kuchitira anzake zimenezi. Mwachitsanzo, iye amazindikira kuti sizoyenera komanso sangasonyeze kuti akuchita zinthu mokoma mtima ngati atayamba bizinezi yomwe akudalira kwambiri Akhristu anzake kuti azigula zinthu zakezo. Ngati atachita zimenezo angasonyeze kuti ali ndi dyera, chifukwa akufuna kupeza phindu podyera masuku pamutu Akhristu anzakewo. Ndipo Akhristufe timachenjezedwa kuti tiyenera kupewa khalidwe limeneli. (Aefeso 5:3; Akolose 3:5; Yakobo 4:1-5) Ndipotu munthu angasonyeze kuti ndi wadyera m’njira zambiri. Mwachitsanzo, iye angamakonde ndalama, angamafunitsitse kuti azilamulira ena kapena kupeza phindu, komanso angakhale wosusuka ndiponso wokonda kugonana. Mika anasonyeza kuti anthu adyera ‘sadzakhuta,’ ndipo zimenezi zikuchitikadi masiku ano.—Mika 6:14.
18, 19. (a) Kodi ena mwa aneneri 12 ananena chiyani pa nkhani ya mmene Yehova amasamalirira “mlendo”? (b) Kodi kuchitira ena zinthu mokoma mtima kungathandize bwanji kuti muzikhala bwino ndi anthu m’dera lanu?
18 Yehova analangiza anthu ake kuti ‘asamabere mwachinyengo mlendo.’ Komanso kudzera mwa Malaki, Mulungu anati: ‘Anthu inu ndidzakuyandikirani kuti ndikuweruzeni. Sindidzazengereza kupereka umboni wotsutsa anthu opondereza alendo.’ (Zekariya 7:10; Malaki 3:5) Kodi m’dera limene mukukhala mukufika anthu ambiri amitundu ina kapena ochokera kumayiko ena? Mwina anthuwo akudzafuna ntchito, kapena akuthawa mavuto osiyanasiyana kwawo. Kodi mumaona bwanji anthu amene moyo wawo komanso chinenero chawo n’chosiyana ndi chanu? Kodi nthawi zina mumachita zinthu zina zomwe zingasonyeze kuti muli ndi tsankho, lomwe ndi losiyana kwambiri ndi kukoma mtima?
19 Anthu amenewo akhoza kumvetsera uthenga wathu ngati mutasonyeza kuti nawonso ndi oyenera kuuzidwa uthenga wa m’Baibulo. Ngati muli wokoma mtima simungaone abale ochokera m’mayiko ena kuti akukusokonezani chifukwa akugwiritsira ntchito zinthu zina za gulu la Yehova, zimene inunso mumagwiritsa ntchito, monga Nyumba ya Ufumu. Mtumwi Paulo anakumbutsa Akhristu ena achiyuda a m’nthawi yake omwe ankasala anthu omwe sanali Ayuda, kuti palibe amene anali woyenerera kupulumuka. Koma chifukwa chakuti Mulungu anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu, aliyense angathe kudzapulumuka. (Aroma 3:9-12, 23, 24) Ngati tili okoma mtima, tidzasangalala kuona kuti Mulungu akukondanso anthu ambiri omwe poyamba analibe mwayi womva uthenga wabwino. (1 Timoteyo 2:4) Nthawi zambiri anthu ochokera kumayiko ena amakumana ndi mavuto osiyanasiyana, choncho tiyenera kuwakomera mtima ndi kuwaganizira. Tingachite zimenezi powalandira ndi kuwachitira zinthu “ngati mbadwa” kapena kuti nzika za m’dziko lathu.—Levitiko 19:34.
AKUFUNA KUTI TIZIYENDA NAYE, POPEZA IYE NDI MULUNGU WOONA
20. Kodi Aisiraeli ena anayamba kudalira chiyani?
20 Mika anatchulanso zoti tiziyenda ndi Mulungu. Zimenezi zikutanthauza kuti tizikhulupirira kuti iye ndi Mulungu woona, komanso tizilolera kuti azititsogolera. (Miyambo 3:5, 6; Hoseya 7:10) Ayuda atabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo, ena ankapita kwa anthu olosera zam’tsogolo, ndipo ena ankalambira milungu yonyenga. Mwina iwo ankaganiza kuti kuchita zimenezi pa nthawi ya mavuto monga chilala kungawathandize. Zimenezi zinkasonyeza kuti akudalira mizimu yoipa kuti iziwathandiza ngakhale kuti Yehova anali atanena momveka bwino kuti asamachite zimenezi. (Deuteronomo 18:9-14; Mika 3:6, 11; 5:12; Hagai 1:10, 11; Zekariya 10:1, 2) Pamenepatu Ayuda amenewo ankagwirizana ndi ziwanda zimene zimatsutsana ndi Mulungu woona.
21, 22. (a) Kodi anthu ambiri m’dera lanu amachita zinthu ziti zosonyeza kuti amakhulupirira mizimu? (b) N’chifukwa chiyani atumiki enieni a Yehova sayenera kuchita nawo zinthu zamizimu?
21 Masiku ano, anthu ambiri amaganiza kuti mizimu yoipa yotchulidwa m’Malemba si yeniyeni koma ndi maganizo oipa amene munthu amakhala nawo. Koma Baibulo limasonyeza kuti ziwanda zilipodi ndipo n’zimene zimatsogolera zaufiti, matsenga ndiponso anthu okhulupirira nyenyezi. (Machitidwe 16:16-18; 2 Petulo 2:4; Yuda 6) Choncho munthu angakumanedi ndi mavuto chifukwa chokhulupirira mizimu. Anthu azikhalidwe zosiyanasiyana amadalira asing’anga olankhula ndi mizimu ndiponso anthu anyanga. Komanso anthu ambiri amachita miyambo ndi zinthu zina pofuna kulankhula ndi mizimu ya anthu akufa. Ndipotu atsogoleri a mayiko ena amapita kwa anthu okhulupirira nyenyezi ndiponso asing’anga akafuna kuthandizidwa kusankha zochita pa nkhani zina. Koma zonsezi n’zotsutsana ndi malangizo opezeka m’buku la Mika akuti tiziyenda ndi Mulungu woona komanso kuti tizilolera kuti azititsogolera.
22 Komatu inuyo simuyenera kuchita nawo zimenezi chifukwa mumalambira Yehova, yemwe ndi Mulungu woona. Dziwani kuti Mulungu sagwiritsa ntchito matsenga pofuna kusonyeza mphamvu zake kapena pofuna kuuza anthu cholinga chake. Koma monga mmene lemba la Amosi 3:7 likusonyezera, Yehova akutitsimikizira kuti ‘amaulula chinsinsi chake kwa atumiki ake, aneneri.’ Komanso kuchita zinthu zamatsenga kungachititse munthu kuti azilamuliridwa ndi Satana, yemwe ndi mkulu wa ziwanda. Musaiwale kuti Satana ndi wabodza ndipo amachita zinthu zosiyanasiyana kuti asocheretse anthu. Iye pamodzi ndi gulu lake ndi ankhanza, ndipo cholinga chawo n’kuvulaza anthu kapena kuwapheratu. (Yobu 1:7-19; 2:7; Maliko 5:5) M’pake kuti Mika anatichenjeza kuti tisamagwirizane ndi olankhula ndi mizimu kapena asing’anga, koma anatilimbikitsa kuti tiziyenda ndi Mulungu woona.
23. Kodi tiyenera kupempha ndani kuti azititsogolera?
23 Munthu angakhale ndi makhalidwe abwino ngati akutsogoleredwa ndi Yehova komanso kumulambira m’njira imene iyeyo amavomereza. (Yohane 4:24) Mneneri Zekariya anatilimbikitsa ‘kupempha Yehova’ kuti azititsogolera. (Zekariya 10:1) Ngati ziwanda zikukuvutitsani kapena kukuyesani, kumbukirani kuti “aliyense woitana pa dzina la Yehova adzapulumuka.” (Yoweli 2:32) Mawu olimbikitsa amenewa ndi ofunika kuwaganizira mofatsa makamaka pamene tikuyembekezera tsiku lalikulu la Yehova.
24. Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera palemba la Mika 6:8?
24 Monga taonera, mawu a palemba la Mika 6:8 ndi othandiza kwambiri. Kuti tikhale ndi makhalidwe abwino tiyenera kukhala ndi maganizo abwino komanso tiyenera kuyesetsa kutsanzira makhalidwe amene Mulungu ali nawo. Hoseya ananena mawu olimbikitsa kwa ife amene tikukhala “m’masiku otsiriza.” Iye ananena kuti m’nthawi yathu ino, anthu oopa Yehova Mulungu adzafunafuna ubwino wake. (Hoseya 3:5) Nayenso Amosi ananena mawu osonyeza kuti Mulungu akufuna kuti tichite zimenezi. Iye anati: “Yesetsani kuchita zabwino . . . kuti mupitirize kukhala ndi moyo.” Ndipo anatilimbikitsanso kuti: “Muzikonda chabwino.” (Amosi 5:14, 15) Zimenezi zidzatithandiza kuti tizichita zimene Yehova akufuna ndipo tidzakhala osangalala.
a Aisiraeli anatengera makhalidwe oipa a Akanani. Ponena za makhalidwe oipa a Akananiwo, womasulira Baibulo wina dzina lake Joseph Rotherham analemba kuti: “Akanani ankachita zinthu zonyansa komanso zankhanza kwambiri pa kulambira kwawo. Akazi ankalolera kuchita zinthu zoipa pofuna kulemekeza milungu yawo. M’malo awo opatulika ankachitiramo zachiwerewere. Analinso ndi zizindikiro ndi ziboliboli zonyansa zomwe zinkaimira maliseche. Komanso anthuwo anali ndi mahule opatulika, aamuna ndi aakazi.”
b Anthu a Mulungu analinso ndi mlandu wolambira mafano, komwe kunali ngati kuchita dama. Iwo ananyalanyaza malamulo a Mulungu n’kuyamba kugwirizana ndi anthu a mitundu ina, zomwe zinachititsa kuti azilambira Yehova pamodzi ndi Baala.