Amosi
2 “Yehova wanena kuti,
‘“Popeza Mowabu anandigalukira mobwerezabwereza,*+ sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa anatentha mafupa a mfumu ya Edomu kuti apeze laimu.
2 Choncho ndidzatumiza moto ku Mowabu,
Ndipo udzawotcheratu nsanja zolimba za Kerioti.+
Mowabu adzafa pakati pa phokoso,
Pakati pa mfuu yankhondo ndiponso kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa.+
3 Ndidzachotsa wolamulira* pakati pake,
Komanso ndidzapha akalonga ake onse limodzi ndi iyeyo,”+ watero Yehova.’
4 Yehova wanena kuti,
‘Popeza Yuda anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa chakuti anakana malamulo* a Yehova,
Ndiponso chifukwa sanatsatire malangizo ake.+
Koma anasocheretsedwa ndi mabodza amene makolo awo ankatsatira.+
6 Yehova wanena kuti,
‘Popeza Isiraeli anandigalukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa chakuti anagulitsa munthu wolungama kuti apeze siliva,
Komanso munthu wosauka kuti apeze nsapato.+
Bambo ndi mwana wake wamwamuna akugona ndi mtsikana mmodzi,
Ndipo akuipitsa dzina langa loyera.
8 Zovala zimene alanda anthu ena monga chikole,+ amaziyala pafupi ndi guwa lililonse lansembe+ nʼkugonapo.
Ndipo vinyo amene amakamwera kunyumba* za milungu yawo, amagula ndi ndalama zimene alipiritsa anthu.’
9 ‘Koma ine ndi amene ndinapha Aamori iwo akuona.+
Aamoriwo anali aatali ngati mitengo ya mkungudza komanso amphamvu ngati mitengo ikuluikulu.
Ndinawononga zipatso zawo mʼmwamba ndiponso mizu yawo pansi.+
10 Ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo,+
Ndipo ndinakuyendetsani mʼchipululu zaka 40,+
Kuti mukatenge dziko la Aamori.
11 Ndinachititsa ana anu ena kukhala aneneri.+
Ndipo anyamata anu ena ndinawachititsa kukhala Anaziri.+
Si choncho kodi, inu Aisiraeli?’ watero Yehova.
13 Choncho ine ndidzakupondani pamalo anu,
Ngati mmene ngolo imene yanyamula mitolo ya tirigu imapondera zinthu.
14 Munthu waliwiro adzasowa kothawira,+
Palibe munthu wamphamvu amene adzalimbe,
Komanso palibe msilikali amene adzapulumuke.