Tidzayenda M’dzina la Yehova Mpaka Muyaya!
“Tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.” —MIKA 4:5.
1. Kodi ndi uthenga wotani umene wafotokozedwa m’machaputala 3 mpaka 5 a Mika?
YEHOVA anali ndi mawu oti auze anthu ake ndipo anagwiritsa ntchito Mika monga mneneri wake. Cholinga cha Mulungu chinali chakuti alange anthu oipa. Anafuna kulanga Israyeli chifukwa cha mpatuko wake. Komabe chosangalatsa n’chakuti Yehova adzadalitsa amene akuyenda m’dzina lake. Uthenga umenewu wafotokozedwa bwino m’machaputala 3 mpaka 5 a ulosi wa Mika.
2, 3. (a) Kodi atsogoleri a Israyeli anafunika kusonyeza khalidwe lotani, koma iwo anali kuchita chiyani? (b) Kodi mungafotokoze bwanji mafanizo opezeka pa Mika 3:2, 3?
2 Mneneri wa Mulunguyo analengeza kuti: “Imvanitu, inu akulu a Yakobo, ndi oweruza a nyumba ya Israyeli, simuyenera kodi kudziŵa chiweruzo?” Inde, zimenezi n’zimene anayenera kuchita, koma kodi iwo anali kuchita chiyani? Mika akuti: “Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lawo pathupi pawo, ndi mnofu wawo pa mafupa awo; inu amene mukudyanso mnofu wa anthu anga; ndi kusenda khungu lawo ndi kuthyola mafupa awo; inde awaduladula ngati nyama yoti aphike, ndi ngati nyama ya mumphika.”—Mika 3:1-3.
3 Tangoganizani! Atsogoleriwo anali kupondereza anthu amene anali osauka ndiponso opanda chitetezo. Anthu amene anali kumvera Mika anamvetsa mosavuta mafanizo amene anawagwiritsa ntchito pano. Akapha nkhosa, pofuna kuphika anali kuchotsa chikopa ndiyeno n’kuidula nthulinthuli. Nthaŵi zina mafupa anali kuwaswa kuti apeze mafuta a m’kati mwake. Anali kuphika minofu ndi mafupawo mumphika wonga umene Mika anatchula. (Ezekieli 24:3-5, 10) Limenelitu linali fanizo loyenerera losonyeza mmene atsogoleri oipawo anali kuzunzira anthu m’nthaŵi ya Mika!
Yehova Amafuna Kuti Tichite Chilungamo
4. Kodi pali kusiyana kotani pakati pa Yehova ndi atsogoleri a Israyeli?
4 Panali kusiyana kwakukulu pakati pa Mbusa wachikondi, Yehova, ndi atsogoleri a Israyeli. Chifukwa choti sanali kuchita chilungamo, analephera kugwira ntchito yawo yoteteza nkhosa. M’malo mwake, iwo anali kudyera masuku pamutu nkhosa zophiphiritsirazo, osazichitira chilungamo komanso amazichitira nkhanza mwa kukhetsa mwazi, monga mmene akunenera pa Mika 3:10. Kodi tingaphunzirepo chiyani pamenepa?
5. Kodi Yehova amafuna kuti amene akutsogolera anthu ake achite chiyani?
5 Mulungu amafuna kuti amene akutsogolera anthu ake azichita chilungamo. Izi n’zimene zikuchitika pakati pa atumiki a Yehova lerolino. Ndiponso zimenezi zikugwirizana ndi mawu amene ali pa Yesaya 32:1, akuti: “Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga adzalamulira m’chiweruzo.” Koma kodi n’chiyani chinali kuchitika m’nthaŵi ya Mika? ‘Odana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa’ anapitiriza kupotoza chilungamo.
Kodi Amayankha Mapemphero a Ndani?
6, 7. Kodi ndi mfundo yofunika iti imene ikupezeka pa Mika 3:4?
6 Kodi anthu oipa a m’nthaŵi ya Mika akanayembekezera Yehova kuwayanja? Ayi. Mika 3:4 akuti: “Adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira nkhope yake nthaŵi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe awo.” Zimenezi zikutsindika mfundo yofunika kwambiri.
7 Yehova sangayankhe mapemphero athu ngati tili ndi chozoloŵezi chochita tchimo. Zimenezo zingatero ngati moyo wathu uli wachinyengo, wobisa machimo athu kwina tikumadzionetsera ngati tikutumikira Mulungu mokhulupirika. Pa Salmo 26:4, Davide anaimba kuti: “Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nawo anthu otyasika.” Ndiye Yehova angayankhe bwanji mapemphero a anthu amene mwadala samvera Mawu ake?
Kupatsidwa Mphamvu ndi Mzimu wa Mulungu
8. Kodi aneneri onyenga a m’nthaŵi ya Mika, anawachenjeza chiyani?
8 Makhalidwe oipa anafala kwambiri pakati pa atsogoleri a Israyeli. Aneneri onyenga anasocheretsa mwauzimu anthu a Mulungu. Atsogoleri adyerawo anali kufuula kuti “Mtendere,” pomwe aliyense amene sanawapatse kanthu kuti adye anali kum’konzera nkhondo. Yehova anati: “Chifukwa chake kudzakhala ngati usiku kwa inu, wopanda masomphenya; ndipo kudzadera inu, wopanda kulosa; ndi dzuŵa lidzaloŵera aneneri, ndi usana udzawadera bii. Ndipo alauli adzachita manyazi, ndi olosa adzathedwa nzeru; ndipo onsewo adzasunama [“adzaphimba ndevu za pamlomo wapamwamba,” NW].”—Mika 3:5-7a.
9, 10. Kodi ‘kuphimba ndevu za pamlomo wapamwamba’ kunatanthauza chiyani ndipo n’chifukwa chiyani Mika sanachite zimenezi?
9 N’chifukwa chiyani “adzaphimba ndevu za pamlomo wapamwamba”? Anthu oipa a m’nthaŵi ya Mika anali kudzachita zimenezi chifukwa cha manyazi. Anthu oipawo anayeneradi kuchita manyazi. ‘Mulungu sanayankhe,’ iwo anaona choncho. (Mika 3:7b) Yehova samvera mapemphero a anthu onse oipa odzikuza.
10 Mika analibe chifukwa ‘chophimbira ndevu zake za pamlomo wapamwamba.’ Sanachite manyazi. Yehova anayankha mapemphero ake. Taonani pa Mika 3:8 pamene mneneri wokhulupirikayo anati: “Koma ine ndidzala nayo mphamvu mwa Mzimu wa Yehova, ndi chiweruzo, ndi chamuna.” Mika anayamikira kwambiri kuti nthaŵi yonse yaitali imene anatumikira mokhulupirika, ‘anadzala nayo mphamvu mwa mzimu wa Yehova.’ Zimenezi zinam’limbikitsa “kufotokozera Yakobo kulakwa kwake, ndi kwa Israyeli tchimo lake.”
11. Kodi anthu amapatsidwa bwanji mphamvu kuti alengeze uthenga wa Mulungu?
11 Mika anafunika mphamvu zoposa za chibadwa kuti alengeze uthenga wa chiweruzo choopsa cha Mulungu. Mzimu wa Yehova, kapena kuti mphamvu yogwira ntchito ndi yofunika. Nanga bwanji ifeyo? Ntchito yathu yolalikira tingaikwaniritse kokha ngati Yehova atilimbikitsa ndi mzimu wake woyera. Ngati tili ndi chizoloŵezi chochimwira dala, tidzalephera kotheratu ntchito yolalikira. Motero Mulungu sangayankhe mapemphero athu oti atipatse mphamvu kuti tichite ntchitoyi. Ndithudi, sitingalengeze uthenga wachiweruzo wa Atate wathu wakumwamba ngati “mzimu wa Yehova” suli pa ife. Tingathe kulankhula Mawu a Mulungu molimba mtima monga Mika ngati Iye amva mapemphero athu ndi kutithandiza mwa mzimu woyera.
12. Kodi n’chifukwa chiyani ophunzira oyambirira a Yesu anatha ‘kulankhula mawu a Mulungu molimbika mtima’?
12 Mwina mukukumbukira nkhani imene ili pa Machitidwe 4:23-31. Tayerekezerani kuti munali mmodzi mwa ophunzira a Yesu a m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino. Ozunza aliuma akufuna kuletsa otsatira a Kristu kulalikira. Koma anthu okhulupirikawo akupemphera kwa Ambuye Mfumu yawo, kuti: “Ambuye, penyani mawu awo akuopsa, ndipo patsani kwa akapolo anu alankhule mawu anu ndi kulimbika mtima konse.” Ndiyeno chinachitika n’chiyani? Mmene anapemphera iwo, panagwedezeka pamalo pamene anasonkhanirapo; ndipo anadzazidwa onse ndi mzimu woyera, nalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima. Tiyenitu nafenso tizipemphera kwa Yehova ndi kudalira thandizo lake la mzimu woyera pamene tikuchita utumiki wathu.
13. Kodi n’chiyani chimene chidzachitikira Yerusalemu ndi Samariya, ndipo chifukwa chake n’chiyani?
13 Taganiziraninso nthaŵi ya Mika. Pa Mika 3:9-12 akunena kuti olamulira omwe anali ndi mlandu wakupha anaweruza chifukwa chofuna mphoto, ansembe anali kuphunzitsa pofuna malipiro, ndipo aneneri onyenga analosera pofuna ndalama. N’zosadabwitsa kuti Mulungu analengeza kuti Yerusalemu, likulu la Yuda, ‘udzasanduka miunda.’ Chifukwa choti kulambira konyenga ndi makhalidwe oipa zinalinso ponseponse mu Israyeli, Mulungu anauza Mika kuti achenjeze kuti adzasandutsa Samariya “mulu wa miyala.” (Mika 1:6) Ndipotu, Mika anakhalabe ndi moyo mpaka anadzionera yekha pamene asilikali a Asuri anawononga Samariya mu 740 B.C.E. (2 Mafumu 17:5, 6; 25:1-21) N’zosakayikitsa kuti mauthenga a mphamvu ameneŵa otsutsa Yerusalemu ndi Samariya analengezedwa chifukwa cha mphamvu ya Yehova.
14. Kodi ulosi wopezeka pa Mika 3:12 unakwaniritsidwa bwanji, ndipo zimenezi ziyenera kutikhudza bwanji?
14 Ndithudi Yuda sangathaŵe chiŵeruzo choopsa cha Yehova. Pokwaniritsa ulosi umene uli pa Mika 3:12, Ziyoni anali woti “adzalimidwa ngati munda.” M’zaka zathu zino za m’ma 2000 tikudziŵa kuti zimenezi zinachitika pamene Ababulo anawononga Yuda ndi Yerusalemu mu 607 B.C.E. Zimenezi zinachitika patapita zaka zambiri kuchokera pamene Mika analosera, komabe iye anali kukhulupirira kuti zidzachitikadi. Ifenso tiyenera kukhulupirira chimodzimodzi kuti dongosolo la zinthu lamakonoli lidzatha pa “tsiku la Mulungu.”—2 Petro 3:11, 12.
Yehova Adzudzula
15. Kodi mungafotokoze bwanji m’mawu anuanu ulosi womwe ukupezeka pa Mika 4:1-4?
15 Tikayang’ana m’mbuyo tikuona kuti kenako Mika analengeza uthenga wosangalatsa wopatsa chiyembekezo. Timapeza mawu olimbikitsa kwambiri pa Mika 4:1-4. Mawu ena pamenepo akuti: “Kudzachitika masiku otsiriza, kuti phiri la nyumba ya Yehova lidzakhazikika pamwamba pa mapiri, nilidzakuzika pamwamba pa zitunda, ndi mitundu ya anthu idzayendako. . . . Ndipo Iye adzaweruza mwa mitundu yambiri ya anthu, nadzadzudzula amitundu amphamvu ali kutali; ndipo iwo adzasula malupanga awo akhale makasu, ndi mikondo yawo ikhale mazenga, mtundu wa anthu sudzasamulira mtundu unzake lupanga, kapena kuphunziranso nkhondo. Koma adzakhala munthu yense patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa; pakuti pakamwa pa Yehova wa makamu padanena.”
16, 17. Kodi Mika 4:1-4 akukwaniritsidwa bwanji lerolino?
16 Kodi “mitundu yambiri ya anthu” ndi “amitundu amphamvu” omwe akutchulidwa ndani? Si mitundu ndi maboma a dzikoli. M’malo mwake, ulosiwu ukutanthauza anthu ochokera m’mitundu yonse omwe tsopano ndi ogwirizana mu utumiki wopatulika mu phiri la Yehova la kulambira koona.
17 Posachedwapa, anthu padziko lonse lapansi adzalambira Yehova m’choonadi mokwanira pokwaniritsa ulosi wa Mika umenewu. Lerolino, anthu “ofuna moyo wosatha” akulangizidwa njira za Yehova. (Machitidwe 13:48, NW) Yehova ‘akuweruza ndi kudzudzula’ mwauzimu okhulupirira amene ali kumbali ya Ufumu. Ameneŵa adzapulumuka “chisautso chachikulu” monga a m’gulu la “khamu lalikulu.” (Chivumbulutso 7:9, 14) Ngakhale pakalipano, iwo akukhala mwamtendere ndi Mboni za Yehova zinzawo ndiponso anthu ena chifukwa chakuti asula malupanga awo kukhala makasu. N’zosangalatsatu kukhala m’gulu limeneli!
Kutsimikiza Kuyenda M’dzina la Yehova
18. Kodi ‘kukhala patsinde pa mpesa wake ndi patsinde pa mkuyu wake’ kukutanthauza chiyani?
18 Tikusangalala kuti ambiri akuphunzira njira za Yehova m’thaŵi yathu ino yomwe anthu padziko lonse lapansi ali ndi mantha adzaoneni. Tikulakalaka nthaŵi imene tsopano yatsala pang’ono kufika imene anthu onse okonda Mulungu sadzaphunzira nkhondo komanso adzakhala patsinde pa mpesa wawo ndi patsinde pa mkuyu wawo. Nthaŵi zambiri mikuyu amaidzala m’minda ya mpesa. (Luka 13:6) Kukhala patsinde pa mpesa wake ndi patsinde pa mkuyu wake, kukutanthauza kuti anthu adzakhala mwamtendere, osasoŵa kanthu, ndiponso otetezeka. Ngakhale pakalipano, ubwenzi wathu ndi Yehova umatipatsa mtendere wamaganizo ndipo umatiteteza mwauzimu. Ulamuliro wa Ufumu ukadzabweretsa zimenezi, sitidzakhala ndi mantha ndipo tidzatetezeka kotheratu.
19. Kodi kuyenda m’dzina la Yehova kumatanthauza chiyani?
19 Tiyenera kuyenda m’dzina la Yehova kuti iye atiyanje ndiponso kutidalitsa. Pa Mika 4:5 akufotokoza zimenezi mwamphamvu pamene mneneriyo akuti: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu ku nthaŵi yomka muyaya.” Kuyenda m’dzina la Yehova sikutanthauza kungonena kuti iye ndi Mulungu wathu. Sikutanthauza kungoyankhapo pamisonkhano yachikristu ndiponso kuchita ntchito yolalikira Ufumu, ngakhale kuti zimenezi ndi zofunikanso. Ngati tikuyenda m’dzina la Yehova ndiye kuti tadzipereka kwa iye ndipo tikuyesetsa kum’tumikira mokhulupirika chifukwa chom’konda ndi moyo wathu wonse. (Mateyu 22:37) Ndipo, monga olambira ake, tatsimikizadi mtima kuyenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka muyaya.
20. Kodi Mika 4:6-13 analosera chiyani?
20 Tsopano tiyeni tione mawu aulosi a pa Mika 4:6-13. “Mwana wamkazi wa Ziyoni” anafunika kupita ku ukapolo “ku Babulo.” Zimenezo zinachitikiradi anthu a mu Yerusalemu m’zaka za m’ma 600 B.C.E. Komabe, ulosi wa Mika unasonyeza kuti otsalira adzabwerera ku Yuda, ndipo Ziyoni akadzabwezeretsedwa Yehova adzaonetsetsa kuti adani a Ziyoni awonongedwa.
21, 22. Kodi Mika 5:2 anakwaniritsidwa bwanji?
21 Chaputala 5 cha Mika chikulosera zinthu zina zochititsa chidwi. Mwachitsanzo, taonani zimene akunena pa Mika 5:2-4. Mika analosera kuti Wolamulira woikidwa ndi Mulungu, amene “matulukiro ake ndiwo akale lomwe,” adzatulukira ku Betelehemu. Adzalamulira monga mbusa “mu mphamvu ya Yehova.” Ndiponso, Wolamulira ameneyo adzakhala wamkulu, osati mu Israyeli mokha, komanso “kufikira malekezero a dziko lapansi.” Dzikoli lingasokonezeke kuti ameneyu ndani, koma kwa ife nkhani imeneyi si chinsinsi.
22 Kodi ndani amene anabadwa ku Betelehemu yemwe anali wofunika kuposa wina aliyense? Ndipo ndani adzakhala “wamkulu kufikira malekezero a dziko lapansi”? Palibenso wina koma Mesiya, Yesu Kristu! Herode Wamkulu atafunsa ansembe aakulu ndi alembi kumene Mesiya anali kudzabadwira, iwo anayankha kuti “m’Betelehemu wa Yudeya.” Anagwiranso mawu a pa Mika 5:2. (Mateyu 2:3-6) Anthu wamba enanso anali kudziŵa zimenezi, chifukwa pa Yohane 7:42 pamati anthuwo ananena kuti: “Kodi sichinati chilembo kuti Kristu adza kutuluka mwa mbewu ya Davide, ndi kuchokera ku Betelehemu, kumudzi kumene kunali Davide?”
Mpumulo Weniweni kwa Anthu
23. Kodi n’chiyani chomwe chikuchitika lerolino pokwaniritsa Mika 5:7?
23 Pa Mika 5:5-15 akufotokoza kuti Asuri adzaloŵa m’dzikolo kwa kanthaŵi ndi kuti Mulungu adzabwezera chilango mitundu yosamvera. Mika 5:7 analonjeza kuti Ayuda otsala olapa adzawabwezera kudziko la kwawo, koma mawu ameneŵa amagwiranso ntchito lerolino. Mika anati: “Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu, ngati mame ochokera kwa Yehova, ngati mvula paudzu.” Mika anagwiritsa ntchito fanizo labwino limeneli kulosera kuti otsalira a Yakobo wauzimu, kapena kuti Israyeli, adzakhala dalitso la Mulungu kwa anthu. “Nkhosa zina” za Yesu zomwe zikuyembekezera kudzakhala padziko lapansi, n’zosangalala kutumikira mogwirizana ndi otsalira amakono a “Israyeli wa Mulungu,” kuthandiza ena kupeza mpumulo wauzimu. (Yohane 10:16; Agalatiya 6:16; Zefaniya 3:9) Pankhani imeneyi, pali mfundo yofunika kuiganizira. Tonsefe monga olengeza Ufumu tiyenera kunyadira mwayi umene tili nawo wothandiza anthu kupeza mpumulo weniweni.
24. Kodi ndi mfundo ziti za m’machaputala 3 mpaka 5 a Mika zomwe zakukhudzani mtima?
24 Kodi mwatolapo mfundo zotani pa machaputala 3 mpaka 5 a ulosi wa Mika? Muyenera kuti mwatolapo mfundo monga izi: (1) Mulungu amafuna kuti anthu amene akutsogolera anthu ake azichita chilungamo. (2) Yehova sangayankhe mapemphero athu ngati tili ndi chizoloŵezi chomwira dala. (3) Ntchito yathu yolalikira tingaikwaniritse kokha ngati Mulungu atilimbikitsa ndi mzimu wake woyera. (4) Tiyenera kuyenda m’dzina la Yehova kuti iye atiyanje. (5) Ife monga olengeza Ufumu, tiyenera kunyadira mwayi wathu wothandiza anthu kupeza mpumulo weniweni. Mwina pali mfundo zinanso zimene zakukhudzani mtima. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene tingaphunzire m’buku laulosi la m’Baibulo limeneli? Nkhani yotsatira itithandiza kupeza mfundo zothandiza pa machaputala aŵiri omaliza a ulosi wa Mika wolimbitsa chikhulupiriro.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Kodi Mulungu amafuna kuti anthu amene akutsogolera anthu ake azichita chiyani?
• N’chifukwa chiyani pemphero ndi mzimu woyera n’zofunika kwambiri potumikira Yehova?
• Kodi anthu ‘amayenda [bwanji] m’dzina la Yehova’?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mungafotokoze fanizo la Mika la mphika?
[Zithunzi patsamba 16]
Mofanana ndi Mika, timachita utumiki wathu molimba mtima