Yehova Sadzachedwa
“Akachedwa [masomphenyawo] uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.”—HABAKUKU 2:3.
1. Kodi ndi kutsimikiza mtima kotani komwe anthu a Yehova asonyeza, ndipo kodi zimenezi zaŵasonkhezera kuchitanji?
“NDIDZAIMA pa dindiro langa.” Kumeneku kunali kutsimikiza mtima kwa mneneri wa Mulungu, Habakuku. (Habakuku 2:1) Anthu a Yehova a m’zaka za zana la 20 asonyezanso kutsimikiza mtima kofananako. Chotero, iwo amvera mofunitsitsa chiitano ichi chomwe chinaperekedwa pamsonkhano womwe unasintha zinthu mu September 1922 chakuti: “Lino ndilo tsiku la masiku onse. Taonani, Mfumu ikulamulira! Inu ndinu oimira ake olengeza. Chifukwa chake lengezani, lengezani, lengezani, Mfumu ndi ufumu wake.”
2. Atabwezeretsedwa kuntchito yachamuna, nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, kodi Akristu odzozedwa anali okhoza kulengeza kuti chiyani?
2 Nkhondo yoyamba yapadziko lonse itatha, Yehova anabwezeretsa otsalira odzozedwa okhulupirikawo kuntchito yachamuna. Kenako, monga Habakuku, aliyense wa iwo anali wokhoza kulengeza kuti: “Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang’anira ndione ngati adzanenanji mwa ine.” Mawu a Chihebri otanthauza “yang’anira” ndi “lindira” abwerezedwa m’maulosi ochuluka.
‘Sadzazengereza’
3. Kodi n’chifukwa chiyani tifunikira kukhalabe odikira?
3 Pamene Mboni za Yehova zikupereka chenjezo la Mulungu lerolino, zifunika kukhala zogalamuka nthaŵi zonse kuti zizilabadira mawu othera a ulosi waukulu wa Yesu akuti: “Chifukwa chake dikirani; pakuti simudziŵa inu nthaŵi yake yakubwera mwininyumba, kapena madzulo, kapena pakati pausiku, kapena pakulira tambala, kapena mamaŵa; kuti angabwere balamanthu nakakupezani muli m’tulo. Ndipo chimene ndinena ndi inu ndinena kwa onse, Dikirani.” (Marko 13:35-37) Mofanana ndi Habakuku, komanso mogwirizana ndi mawu a Yesu, tiyenera kudikira!
4. Kodi mkhalidwe wa zinthu lerolino ukufanana motani ndi wa m’nthaŵi ya Habakuku cha m’chaka cha 628 B.C.E.?
4 Habakuku ayenera kuti anamaliza kulemba buku lakelo cha m’chaka cha 628 B.C.E., Babulo asanakhale n’komwe ufumu wamphamvu padziko lonse. Kwazaka zambiri, chiweruzo cha Yehova pa Yerusalemu wampatukoyo chinali kulengezedwa. Komatu, sizinali kudziŵika bwinobwino kuti chiweruzocho chidzaperekedwa liti. Ndani amene akanakhulupirira kuti chinali kudzaperekedwa patangotha zaka 21, ndikuti Babulo ndiye amene adzakhale wakupha wa Yehova? N’zofanana ndi lerolino, sitikudziŵa ‘tsiku ndi nthaŵi’ pamene mapeto a dongosolo lino adzafika, koma Yesu watichenjezeratu kuti: “Khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.”—Mateyu 24:36, 44.
5. Kodi n’chiyani chomwe chili cholimbikitsa kwenikweni ponena za Mawu a Mulungu olembedwa pa Habakuku 2:2, 3?
5 Pachifukwa chabwino zedi, Yehova anapatsa Habakuku ntchito yosangalatsa imeneyi akumati: “Lembera masomphenyawo, nuwachenutse pamagome, kuti awaŵerenge mofulumira. Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:2, 3) Lerolino, kuipa ndi chiwawa zikuchuluka kwambiri padziko lonse, kusonyeza kuti taimadi pakhomo penipeni pa “tsiku la Yehova lalikulu loopsa.” (Yoweli 2:31) Mawu a Yehova mwiniyo otitsimikizira akuti ‘sazengereza,’ alidi olimbikitsa kwambiri!
6. Kodi tingapulumuke bwanji tsiku lachiweruzo chakupha lomwe likubweralo?
6 Pamenepa, kodi tingapulumuke bwanji tsiku lachiweruzo chakupha limene likubweralo? Yehova akuyankha mwa kusiyanitsa pakati pa olungama ndi osalungama motere: “Taonani, moyo wake udzikuza, wosawongoka m’kati mwake; koma wolungama adzakhala ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.” (Habakuku 2:4) Atsogoleri ndi anthu onyada ndiponso adyera aipitsa mbiri ya anthu yamakono ndi magazi a mamiliyoni a anthu osalakwa, makamaka m’nkhondo ziŵiri zapadziko lonse ndi m’nkhondo zamafuko. Koma anthu okonda mtendere, odzozedwa a Mulungu apirira m’chikhulupiriro. Iwo ali “mtundu wolungama, umene uchita zoonadi.” Mtundu umenewu, limodzi ndi anzawo, “nkhosa zina” amamvera langizo lakuti: “Khulupirirani Yehova nthaŵi zamuyaya, pakuti mwa Ambuye Yehova muli thanthwe lachikhalire.”—Yesaya 26:2-4; Yohane 10:16.
7. Mogwirizana ndi mmene Paulo anagwiritsira ntchito Habakuku 2:4, kodi tiyenera kuchita chiyani?
7 Polembera Akristu achihebri, mtumwi Paulo anagwira mawu Habakuku 2:4 pouza anthu a Yehova kuti: “Pakuti chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano. Pakuti katsala kanthaŵi kakang’onong’ono. Ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa. Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m’chikhulupiriro: Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.” (Ahebri 10:36-38) M’tsiku lathu lino si nthaŵi yokhala manja lende kapena yokodwa mumsampha wa dziko la Satana lokonda zinthu zakuthupi ndi zosangalatsa. Kodi tiyenera kuchitanji kufikira “kanthaŵi kakang’onong’ono” kameneka katatha? Monga Paulo, ife a mtundu woyera wa Yehova, tiyenera ‘kutambalitsira zam’tsogolo, kulondetsa kutsatira mfupo’ ya moyo wosatha. (Afilipi 3:13, 14) Komanso monga Yesu, tiyenera ‘kupirira chifukwa cha chimwemwe choikidwa pamaso pathu.’—Ahebri 12:2.
8. Kodi ndani yemwe ali “munthu” wotchulidwa pa Habakuku 2:5, ndipo n’chifukwa chiyani iye sadzapambana?
8 Habakuku 2:5 akulongosola za “munthu wodzikuza” amene, mosiyana ndi atumiki a Yehova, akulephera kukwaniritsa cholinga chake, ngakhale kuti “wakulitsa chikhumbo chake ngati kunsi kwa manda.” Kodi munthu yemwe ‘sangakhuteyu’ ndani? Ndi kususuka kofanana ndi kuja kwa Babulo wa m’nthaŵi ya Habakuku, “munthu” wachiungwe ameneyu, wopangidwa ndi maulamuliro andale amphamvu zedi, kaya ndi achifasisiti, Nazi, Chikomyunizimu, ngakhalenso otchedwa a demokalase, amachita nkhondo kuti afutukule mayiko ake. Akudzazanso manda ndi anthu osalakwa. Koma “munthu” wachiungwe wonyengayu wadziko la Satana, wodziona kukhala wofunika kwambiri, akulephera ‘kudzisonkhanitsira amitundu onse ndi kudzimemezera mitundu yonse ya anthu.’ Ndi Yehova Mulungu yekha amene angagwirizanitse anthu onse, ndipo adzaterodi kupyolera mu Ufumu Waumesiya.—Mateyu 6:9,10.
Loyamba mwa Masoka Asanu Ochititsa Mantha
9, 10. (a) Kodi Yehova akupitiriza kulengeza chiyani kupyolera mwa Habakuku? (b) Polingalira za kupeza phindu m’njira zosalungama, kodi zinthu zili bwanji lerolino?
9 Kupyolera mwa mneneri wake Habakuku, Yehova akupitiriza kulengeza masoka asanu otsatizana, ziweruzo zimene ziyenera kuperekedwa pokonza dziko kuti olambira a Mulungu okhulupirika akhalemo. Anthu a mitima yolungamawo ‘adzanenera fanizo’ limene Yehova akupereka. Timaŵerenga pa Habakuku 2:6 kuti: “Tsoka iye wochulukitsa zimene sizili zake! Mpaka liti? Iye wodzisenzera zigwiriro.”
10 Pano akugogomezera kupeza phindu m’njira zosalungama. M’dzikoli, olemera amamka nalemerabe pamene osauka amamka nasaukabe. Ogulitsa mankhwala osokoneza bongo ndi ochita katangale amapeza chuma chochuluka, pamene anthu wamba amafa ndi njala. Gawo limodzi la anthu mwa magawo anayi padziko lonse akuti ndi osauka kwambiri. Mikhalidwe ndi yoipa kwambiri m’mayiko ochuluka. Awo amene amafuna chilungamo padziko lapansi amafuula kuti: Kuipaku kuwonjezerekabe “mpaka liti!” Komatu, mapeto ali pafupi! Ndithudi, masomphenyawo ‘sadzazengereza.’
11. Kodi Habakuku akunenanji pa kukhetsedwa kwa magazi a anthu, ndipo n’chifukwa chiyani ifeyo tinganene kuti padziko lapansi lerolino pali liwongo lalikulu la mwazi?
11 Mneneriyu akuuza wochita zoipa kuti: “Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mudzi, ndi onse okhalamo.” (Habakuku 2:8) Kuphana kwachulukadi padziko lerolino! Yesu ananena momveka bwino kuti: “Onse akugwira lupanga adzawonongeka ndi lupanga.” (Mateyu 26:52) Komatu, m’zaka za zana la 20 zokha, mayiko ndi mafuko amene ali ndi liwongo la mwazi, achirikiza kuphedwa kwa anthu oposa mamiliyoni zana limodzi. Tsoka kwa onse omwe akuchita nawo kupha kumeneku!
Tsoka Lachiŵiri
12. Ndi tsoka lachiŵiri liti lomwe Habakuku analemba, ndipo kodi tingakhale otsimikiza motani kuti kupeza chuma mosaona mtima sikudzapindula kalikonse?
12 Tsoka lachiŵiri, lolembedwa pa Habakuku 2:9-11, likugwera “iye wakupindulitsira nyumba yake phindu loipa, kuti aike chisanja chake ponyamuka, kuti alanditsidwe m’dzanja la choipa!” Kupeza phindu mosaona mtima sikudzapindula kalikonse, monga mmene wamasalmo akumveketsera bwino kuti: “Usaope polemezedwa munthu, pochuluka ulemu wa nyumba yake; pakuti pomwalira iye sadzamuka nako kanthu kalikonse; ulemu wake sutsika naye kumutsata m’mbuyo.” (Salmo 49:16, 17) Chotero, malangizo anzeru a Paulo n’ngochititsa chidwi zedi, iye anati: “Lamulira iwo achuma m’nthaŵi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziŵika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo.”—1 Timoteo 6:17.
13. N’chifukwa chiyani tiyenera kupitirizabe kupereka chenjezo la Mulungu?
13 N’kofunikadi kwambiri kuti mauthenga a Mulungu a chiweruzo aperekedwe lerolino! Pamene Afarisi anatsutsa makamu kutchula Yesu kuti ‘Mfumu yomwe ikudza m’dzina la Ambuye’ iye anati: “Ndinena ndi inu, ngati aŵa akhala chete miyala idzafuula.” (Luka 19:38, 40) Mofananamo, ngati anthu a Mulungu lerolino anakalephera kuvumbula kuipa komwe kuli m’dzikoli, ‘mwala wa m’khoma ukadafuula.’ (Habakuku 2:11) Choncho tipitirizetu kupereka chenjezo la Mulungu molimba mtima!
Tsoka Lachitatu Komanso Nkhani ya Liwongo la Mwazi
14. Kodi zipembedzo zadziko zili ndi liwongo la mwazi lotani?
14 Tsoka lachitatu, lolengezedwa kudzera mwa Habakuku likunena za liwongo la mwazi. Habakuku 2:12 amati: “Tsoka iye wakumanga mudzi ndi mwazi, nakhazikitsa mudzi ndi chisalungamo!” M’dongosolo lino la zinthu, chisalungamo ndi kupha kaŵirikaŵiri zimayendera pamodzi. Mokulira, zipembedzo zadziko zachititsa kuphedwa kwa anthu koipitsitsa m’mbiri ya anthu. Tingangotchulako za Nkhondo za Mtanda, zimene zinamenyanitsa amene ankati ndi Akristu ndi Asilamu; Bwalo la Inquisition lachikatolika ku Spain ndi ku Latin America; Nkhondo ya Zaka Makumi Atatu ya ku Ulaya, yomenyedwa pakati pa Apolotesitanti ndi Akatolika; ndipo zoipitsitsa pa zonse, nkhondo ziŵiri zadziko za m’zana lathu, zimene zonse ziŵiri zinayambira m’Gawo la Matchalitchi Achikristu.
15. (a) Mochirikizidwa kapena kuvomerezedwa ndi tchalitchi, kodi mayiko akupitirizabe kuchita chiyani? (b) Kodi United Nations ingathetse kukhala ndi zida zankhondo m’dzikoli?
15 Chimodzi cha zinthu zoipitsitsa kwambiri m’nkhondo yadziko yachiŵiri chinali Chipululutso cha Nazi chimene chinawononga mamiliyoni ochuluka a Ayuda ndi anthu ena osalakwa ku Ulaya. Akuluakulu a Roma Katolika ku France avomera posachedwapa kuti analephera kutsutsa kutumizidwa kwa anthu zikwi mazanamazana kumisasa ya Nazi yopherako anthu. Komabe, mayiko akupitirizabe kukonzekera kukhetsa magazi, mochirikizidwa kapena movomerezedwa ndi tchalitchi. Ponena za Tchalitchi cha Russian Orthodox, magazini ya Time, (kope lofalitsidwa padziko lonse) posachedwapa inati: “Tchalitchi choyambitsidwanso chimenechi chilinso ndi chisonkhezero chachikulu pa nkhani yomwe sinkalingaliridwa n’kalelonse: dongosolo la zankhondo la ku Russia. . . . Changokhala chizoloŵezi kwa atsogoleri a chipembedzo cha Russian Orthodox kudalitsa omenya nkhondo ya mu mlengalenga ndiponso m’malo omwe asilikali amakhala. Mu November, kunyumba ya amonke ya Danilovsky ku Moscow, kumene kumakhala akuluakulu a Russian Patriarchate, tchalitchi chimenechi chinafikira pa kudalitsa ngakhale nkhokwe ya zida za nyukiliya ya ku Russia.” Kodi United Nations ingaletse dzikoli kuti lisakhalenso ndi zida zankhondo zauchiŵandazo? Kutalitali! Yemwe anapatapo mphotho ya Nobel Peace Prize anatsirira ndemanga mu nyuzipepala ya The Guardian ya ku London, England, motere: “Chimene chilidi chosokoneza maganizo ndi chakuti mamembala achikhalire asanu a Bungwe Lachitetezo la United Nations ndiwonso mayiko asanu akuluakulu padziko lonse ogulitsa zida zankhondo.”
16. Kodi Yehova adzachitanji ku mayiko okonda nkhondoŵa?
16 Kodi Yehova adzapereka chiweruzo pa mayiko okonda nkhondoŵa? Habakuku 2:13 amati: “Taonani, sichichokera kwa Yehova wa makamu kodi kuti mitundu ya anthu ingogwirira moto ntchito, ndi anthu angodzilemetsa pa zopanda pake?” “Yehova wa makamu”! Inde, Yehova ali ndi makamu a angelo kumwamba, amene adzaŵagwiritsa ntchito pa kuwononga anthu ndi mayiko okonda nkhondo!
17. Kodi chidziŵitso cha Yehova chidzadzaza dziko mpaka pati pambuyo popereka chiweruzo chake ku mitundu yachiwawa?
17 Kodi n’chiyani chimene chidzatsatira kuperekedwa kwa chiweruzo cha Yehova pa mitundu yachiwawa imeneyo? Habakuku 2:14 akutipatsa yankho lakuti: “Pakuti dziko lapansi lidzadzazidwa ndi chidziŵitso cha ulemerero wa Yehova, monga madzi aphimba pansi pa nyanja.” Ndi chiyembekezo chosangalatsa bwanji! Pa Armagedo, uchifumu wa Yehova udzatsimikiziridwa kosatha. (Chivumbulutso 16:16) Iye akutitsimikizira kuti ‘adzachititsa malo a mapazi ake ulemerero.’ Maloŵa ndi dziko lapansi tikukhalamo lino. (Yesaya 60:13) Mtundu wonse wa anthu udzaphunzitsidwa m’njira ya moyo ya Mulungu, kotero kuti chidziŵitso cha zifuno za ulemerero za Yehova chidzadzaza dziko lapansi monga momwe madzi amadzazira nyanja.
Tsoka Lachinayi ndi Lachisanu
18. Ndi tsoka lachinayi liti limene likulengezedwa kupyolera mwa Habakuku, ndipo kodi likusonyezedwa motani m’mikhalidwe yadziko lerolino?
18 Tsoka lachinayi likulongosoledwa pa Habakuku 2:15 m’mawu aŵa: “Tsoka wakuninkha mnzake chakumwa, ndi kuwonjezako mankhwala ako, ndi kumuledzeretsa, kuti upenyerere manyazi awo!” Izi zikutipangitsa kuganiza za mkhalidwe wolekerera, wopulupudza wadziko lamakonoli. Khalidwe lake loipa, lomwe limachirikizidwa ngakhale ndi magulu achipembedzo olekerera, lafika poipitsitsa zedi. Miliri, monga ngati AIDS ndiponso matenda ena opatsirana mwakugonana, akufalikira kwambiri padziko lonse. M’malo mosonyeza “ulemerero wa Yehova,” mbadwo wadyera wa lerolino ukuloŵererabe m’zoipa ndipo ukulunjikabe ku chiweruzo choperekedwa ndi Mulungu. ‘Podzazidwa nawo manyazi m’malo mwa ulemerero,’ dziko lopulupudzali lili pafupi kumwera chikho cha mkwiyo wa Yehova, chimene chikuimira chifuno chake ku dzikoli. ‘Kusanza kwa manyazi kudzakhala pa ulemerero wake.’—Habakuku 2:16.
19. Mawu oyambirira onena za tsoka lachisanu lomwe Habakuku akulengeza akukhudzana ndi chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani mawuwo ali ofunika kwambiri m’dziko lamakono lino?
19 Mawu oyambirira onena za tsoka lachisanu akuchenjeza mwamphamvu za kulambira mafano. Yehova akuchititsa mneneriyu kulengeza mawu amphamvuŵa kuti: “Tsoka iye wakunena kwa mtengo, Galamuka; ndi kwa mwala wosalankhula, Nyamuka! Kodi ichi chiphunzitsa? Taona chakutidwa ndi golidi ndi siliva, ndi m’kati mwake mulibe mpweya konse.” (Habakuku 2:19) Kufikira lerolino, mbali zonse ziŵiri, Matchalitchi Achikristu ndi lotchedwa dziko lachikunja, zimagwadira mitanda, mafano a Mariya, zithunzithunzi, ndi mafano ena a zifanizo za anthu ndi nyama. Palibe chilichonse cha zimenezi chimene chingadzuke kuti chipulumutse olambira ake pamene Yehova akubwera kudzapereka chiweruzo. Kukutidwa kwawo ndi golide ndi siliva n’kosanunkha kanthu poyerekezera ndi ulemerero wa Mulungu yemwe akukhalako kosatha, Yehova, ndiponso ulemerero wa chilengedwe chake chamoyo. Tilemekezetu dzina lake losayerekezekalo kosatha!
20. Ndi m’makonzedwe a kachisi ati momwe ifeyo tili amwayi kutumikiramo mwachimwemwe?
20 Inde, Mulungu wathu, Yehova, ndiye woyenera kulemekezedwa kwambiri. Ndi ulemu waukulu kwa iye, tiyeni timvere chenjezo lamphamvuli pa kulambira mafano. Koma tamverani! Yehova akulankhulabe kuti: “Yehova ali m’Kachisi wake wopatulika; dziko lonse lapansi likhale chete pamaso pake.” (Habakuku 2:20) Mosakayikira mneneriyu anali kuganiza za kachisi wa ku Yerusalemu. Komabe, ife lerolino tili ndi mwayi wa kulambira m’makonzedwe a kachisi wauzimu wokwezeka kwambiri, mmene Ambuye wathu Yesu Kristu waikidwa monga Mkulu wa Ansembe. Pano, m’bwalo lapadziko lapansi la kachisi ameneyo, timasonkhana, kutumikira, ndi kupemphera, kupereka kwa Yehova ulemu umene umayenerera dzina lake la ulemererolo. Ndipotu tili ndi chimwemwe chosaneneka pamene tikupereka kulambira kwathu kochokera pansi pa mtima kwa Atate wathu wachikondi wakumwamba!
Kodi Mukukumbukira?
• Kodi m’mawaona motani mawu a Yehova akuti: ‘Sadzazengereza’?
• Kodi tanthauzo lamakono la masoka olengezedwa kudzera mwa Habakuku n’lotani?
• N’chifukwa chiyani tikufunikira kupitirizabe kupereka chenjezo la Yehova?
• Kodi tili amwayi kutumikira m’bwalo la kachisi wotani?
[Zithunzi patsamba 15]
Mofanana ndi Habakuku, atumiki a Mulungu amakono akudziŵa kuti Yehova sadzachedwa
[Zithunzi patsamba 18]
Kodi mumayamikira mwayi wolambira Yehova m’bwalo la kachisi wake wauzimu?
[Mawu a Chithunzi patsamba 16]
Chithunzi cha U.S. Army