“Manja Anu Asakhale Olefuka”
“Manja anu asakhale olefuka. Yehova Mulungu wako ali pakati pako, [pokhala Wamphamvu, iye adzapulumutsa, NW].”—ZEFANIYA 3:16, 17.
1. Kodi katswiri wina wa Baibulo ananena chiyani pa ulosi wa Zefaniya?
ULOSI wa Zefaniya unapyola pa kukwaniritsidwa kwake koyamba m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri ndi lachisanu ndi chimodzi B.C.E. M’buku lake la ndemanga ponena za Zefaniya, Profesa C. F. Keil analemba kuti: “Ulosi wa Zefaniya . . . sumangoyamba ndi chilengezo cha chiweruzo cha onse padziko lonse, chimene chikunena za chiweruzo chimene chidzagwera Yuda chifukwa cha machimo ake, ndi dziko la mitundu chifukwa cha udani wake kulinga kwa anthu a Yehova; komanso umafotokoza mwatsatanetsatane za tsiku lalikulu ndi lowopsa la Yehova.”
2. Kodi pali kufanana kotani pakati pa mikhalidwe m’tsiku la Zefaniya ndi mkhalidwe umene uli m’Dziko Lachikristu lerolino?
2 Lerolino, chigamulo chachiweruzo cha Yehova nchakuti asonkhanitse amitundu kuwawononga pamlingo waukulu kuposa m’tsiku la Zefaniya. (Zefaniya 3:8) Mitundu ija imene imati ndi yachikristu ili ndi mlandu waukulu kwambiri pamaso pa Mulungu. Monga momwedi Yerusalemu anatuta zowopsa chifukwa cha kusakhulupirika kwake kwa Yehova, Dziko Lachikristu lilinso ndi mlandu kwa Mulungu chifukwa cha njira zake zosadziletsa. Ziweruzo zaumulungu zoperekedwa pa Yuda ndi Yerusalemu m’tsiku la Zefaniya zikugwira ntchito mwamphamvu kwambiri pa matchalitchi ndi timagulu ta mpatuko ta Dziko Lachikristu. Iwo aipitsanso kulambira koyera ndi ziphunzitso zawo zonyoza Mulungu, zambiri zachikunja. Iwo apereka nsembe mamiliyoni a ana awo aamuna athanzi pa guwa la nsembe lamakono la nkhondo. Ndiponso, okhala m’Yerusalemu wophiphiritsirayu amasanganiza chotchedwa Chikristu ndi kupenda nyenyezi, zamizimu, ndi chisembwere choluluzika, zimene zimakumbutsa za kulambira Baala.—Zefaniya 1:4, 5.
3. Kodi chinganenedwe nchiyani pa atsogoleri adziko ndi maboma andale lerolino, ndipo Zefaniya analosera chiyani?
3 Atsogoleri andale ambiri a Dziko Lachikristu amakonda kuonekera m’tchalitchi. Koma monga “akalonga” a Yuda, ambiri a iwo amalima anthu pamsana monga “mikango yobangula” ndi “mimbulu” yolusa. (Zefaniya 3:1-3) Akapolo awo andale amene kwawo ndi kugonjera basi ‘amadzaza nyumba ya mbuye wawo ndi chiwawa ndi chinyengo.’ (Zefaniya 1:9) Ziphuphu ndi kusaona mtima zili zofala. Ponena za maboma andale mkati ndi kunja kwa Dziko Lachikristu, ambiri a iwo ‘amadzikuza’ pa anthu a Yehova wa makamu, Mboni zake, akumawayesa “mpatuko” wonyozeka. (Zefaniya 2:8; Machitidwe 24:5, 14) Ponena za atsogoleri onse otero andale ndi otsatira awo, Zefaniya analosera kuti: “Ngakhale siliva wawo, ngakhale golidi wawo sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova; koma dziko lonse lidzatha ndi moto wa nsanje yake; pakuti adzachita chakutsiriza, mofulumira, onse okhala m’dziko.”—Zefaniya 1:18.
‘Kubisika Tsiku la Mkwiyo wa Yehova’
4. Kodi nchiyani chikusonyeza kuti padzakhala opulumuka tsiku lalikulu la Yehova, koma kodi ayenera kuchitanji?
4 Si onse okhala m’Yuda amene anawonongeka m’zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E. Choteronso, padzakhala opulumuka tsiku lalikulu la Yehova. Kwa otero Yehova anati kupyolera mwa mneneri wake Zefaniya: “Lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova. Funani Yehova, ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.”—Zefaniya 2:2, 3.
5. M’nthaŵi ino yamapeto, kodi ndani amene anali oyamba kulabadira chenjezo la Zefaniya, ndipo kodi Yehova wawagwiritsira ntchito motani?
5 M’nthaŵi ya mapeto a dziko lino, oyamba kuyankha chiitano chaulosi anali otsalira a Aisrayeli auzimu, Akristu odzozedwa. (Aroma 2:28, 29; 9:6; Agalatiya 6:16) Pokhala atafuna chilungamo ndi chifatso ndi pokhala atalemekeza zigamulo zachiweruzo za Yehova, analanditsidwa kwa Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, napezanso chiyanjo cha Mulungu mu 1919. Kuyambira pamenepo, ndipo makamaka chiyambire 1922, otsalira okhulupirika ameneŵa akhala akulengeza mopanda mantha ziweruzo za Yehova pa matchalitchi ndi timagulu ta mpatuko ta Dziko Lachikristu ndi pa mitundu yandale.
6. (a) Kodi Zefaniya analosera chiyani ponena za otsalira okhulupirika? (b) Kodi Ulosi umenewu wakwaniritsidwa motani?
6 Ponena za otsalira okhulupirika ameneŵa, Zefaniya analosera kuti: “Ndidzasiya pakati pako anthu [odzichepetsa ndi ofatsa, NW], ndipo iwo [adzathaŵiradi m’dzina la, NW] Yehova. Otsala a Israyeli sadzachita chosalungama, kapena kunena mabodza; ndi m’kamwa mwawo simudzapezeka lilime lonyenga; pakuti adzadya nadzagona pansi, ndi palibe wakuwawopsa.” (Zefaniya 3:12, 13) Akristu odzozedwa ameneŵa adziŵikitsa dzina la Yehova nthaŵi zonse, koma makamaka chiyambire 1931, pamene analandira dzina lakuti Mboni za Yehova. (Yesaya 43:10-12) Mwa kusonyeza nkhani ya uchifumu wa Yehova, iwo alemekeza dzina la Mulungu, ndipo ilo lakhala pothaŵira pawo. (Miyambo 18:10) Yehova wawadyetsa mwauzimu kochuluka, ndipo akukhala m’paradaiso wauzimu popanda mantha.—Zefaniya 3:16, 17.
“Dzina, ndi Chilemekezo mwa Mitundu Yonse ya Anthu”
7, 8. (a) Kodi ndi ulosi wina uti umene wakwaniritsidwa pa otsalira a Israyeli wauzimu? (b) Kodi anthu mamiliyoni afika pozindikira chiyani, nanga inu mwini mumaganiza bwanji pa zimenezi?
7 Chikondi chakuya cha otsalira pa dzina la Yehova ndi pa mapulinsipulo olungama a Mawu ake chaonekera. Anthu oona mtima aona kusiyana pakati pa khalidwe la otsalira ndi kuipa ndi chinyengo cha atsogoleri a dzikoli andale ndi achipembedzo. Yehova wadalitsa “otsala a Israyeli” wauzimu. Wawalemekeza mwa kuwapatsa thayo la kunyamula dzina lake, ndipo wawachititsa kukhala ndi mbiri yabwino pakati pa mitundu yapadziko lapansi. Zimenezi zikugwirizana ndi zimene Zefaniya analosera kuti: “Nthaŵi yomweyo ndidzakuloŵetsani, ndi nthaŵi yomweyo ndidzakusonkhanitsani; pakuti ndidzakuikani mukhale dzina, ndi chilemekezo mwa mitundu yonse ya anthu apadziko lapansi, pamene ndibweza undende wanu pamaso panu, ati Yehova.”—Zefaniya 3:20.
8 Chiyambire 1935, anthu mamiliyoni enieni azindikira kuti dalitso la Yehova lili ndi otsalira. Iwo mokondwa amatsatira Ayuda kapena Aisrayeli auzimu ameneŵa, akumati: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) “Nkhosa zina” zimenezi zimazindikira kuti otsalira odzozedwa ndiwo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” woikidwa ndi Kristu ‘kuyang’anira zinthu zake zonse [zapadziko lapansi].’ Iwo amadya moyamikira chakudya chauzimu chokonzedwa ndi kagulu ka kapolo “panthaŵi yake.”—Yohane 10:16; Mateyu 24:45-47.
9. Kodi ndi “chinenero” chotani chimene anthu mamiliyoni aphunzira kulankhula, ndipo ndi ntchito iti yaikulu imene a nkhosa zina akuchita “pheŵa ndi pheŵa” ndi otsalira odzozedwa?
9 Limodzi ndi otsalira, mamiliyoni ameneŵa a nkhosa zina akuphunzira kuchita ndi kulankhula mogwirizana ndi “chinenero choyera.”a Yehova analosera kupyolera mwa Zefaniya kuti: “Pamenepo ndidzasintha anthu kuti alankhule chinenero choyera, kuti iwo onse aitanire pa dzina la Yehova, kuti amtumikire pheŵa ndi pheŵa.” (Zefaniya 3:9, NW) Inde, nkhosa zina zimatumikira Yehova “pheŵa ndi pheŵa” mogwirizana ndi otsalira a “kagulu ka nkhosa” pantchito yolalikira “uthenga uwu wabwino wa ufumu . . . ukhale mboni kwa anthu a mitundu yonse.”—Luka 12:32; Mateyu 24:14.
‘Tsiku la Yehova Lidzadza’
10. Kodi otsalira odzozedwa nthaŵi zonse akhala otsimikiza za chiyani, ndipo monga kagulu, adzaonako chiyani?
10 Otsalira odzozedwa nthaŵi zonse akhala akukumbukira mawu ouziridwa a mtumwi Petro akuti: “[Yehova, NW] sazengereza nalo lonjezano, monga ena achiyesa chizengerezo; komatu aleza mtima kwa inu, wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa. Koma tsiku la [Yehova, NW] lidzadza ngati mbala.” (2 Petro 3:9, 10) Akagulu ka kapolo wokhulupirika sanakhalepo ndi zikayikiro zilizonse ponena za kudza kwake kwa tsiku la Yehova m’nthaŵi yathu. Tsiku lalikulu limenelo lidzayamba ndi kuperekedwa kwa ziweruzo za Mulungu pa Dziko Lachikristu, Yerusalemu wophiphiritsira, ndi pa mbali yotsala ya Babulo Wamkulu.—Zefaniya 1:2-4; Chivumbulutso 17:1, 5; 19:1, 2.
11, 12. (a) Kodi ndi mbali ina iti ya ulosi wa Zefaniya imene yakwaniritsidwa pa otsalira? (b) Kodi otsalira odzozedwa alabadira motani chiitano chakuti, “Manja anu asakhale olefuka”?
11 Otsalira odzozedwa ali achimwemwe pokhala atalanditsidwa mu 1919 ku ukapolo wauzimu wa Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Iwo aona kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Zefaniya wakuti: ‘Imba, mwana wamkazi wa Ziyoni; fuula, Israyeli; kondwera nusekerere ndi mtima wonse, mwana wamkazi wa Yerusalemu. Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israyeli, Yehova, ali pakati pako, sudzawopanso choipa. Tsiku lomwelo adzati kwa Yerusalemu, Usawopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka. Yehova Mulungu wako ali pakati pako, pokhala Wamphamvu, iye adzapulumutsa.’—Zefaniya 3:14-17.
12 Ali ndi chikhulupiriro ndi umboni wochuluka wakuti Yehova ali pakati pawo, otsalira odzozedwa apitabe patsogolo mopanda mantha kuchita ntchito yawo imene Mulungu anawapatsa. Iwo alalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndipo adziŵikitsa ziweruzo za Yehova pa Dziko Lachikristu, mbali yotsala ya Babulo Wamkulu, ndi pa dongosolo lonse la zinthu loipa la Satana. M’nthaŵi zonse zovuta, pazaka makumi ambiri chiyambire 1919, iwo amvera lamulo la Mulungu lakuti: “Usawopa Ziyoni, manja anu asakhale olefuka.” Sanachite ulesi ndi manja awo pogaŵira matrakiti, magazini, mabuku, ndi timabuku mabiliyoni ambiri olengeza Ufumu wa Yehova. Akhala chitsanzo chosonkhezera chikhulupiriro mwa nkhosa zina zimene, chiyambire 1935, zabwera kudzawachirikiza.
“Manja Anu Asakhale Olefuka”
13, 14. (a) Kodi nchifukwa ninji Ayuda ena anasiya kutumikira Yehova, ndipo zimenezi zinaonekera motani? (b) Kodi chimene chingakhale chopanda nzeru kwa ife kuchita nchiyani, ndipo kodi ndi pantchito yotani imene sitiyenera kulola manja athu kulefuka?
13 Pamene ‘tikulindira’ tsiku lalikulu la Yehova, kodi tingapindule motani ndi ulosi wa Zefaniya? Choyamba, tiyenera kusamala kuti tisakhale ngati Ayuda a m’tsiku la Zefaniya amene analeka kutsatira Yehova chifukwa anali ndi zikayikiro ponena za kuyandikira kwa tsiku la Yehova. Kwenikweni Ayudawo sanasonyeze zikayikiro zawo poyera, koma zochita zawo zinasonyeza kuti iwo sanakhulupiriredi kuti tsiku lalikulu la Yehova linali pafupi. Analimbikira kukundika chuma m’malo molindira Yehova.—Zefaniya 1:12, 13; 3:8.
14 Ino si nthaŵi yakulola zikayikiro kuzika mizu m’mitima mwathu. Kungakhale kupandiratu nzeru ngati m’maganizo kapena mumtima mwathu tikankhira kutsogolo tsiku la Yehova likudzalo. (2 Petro 3:1-4, 10) Tiyenera kusasiya kutsatira Yehova kapena ‘kusalola manja athu kulefuka’ mu utumiki wake. Zimenezi zikuphatikizapo ‘kusachita ndi dzanja laulesi’ polalikira ife “uthenga wabwino.”—Miyambo 10:4; Marko 13:10.
Kulimbana ndi Mphwayi
15. Kodi nchiyani chimene chingatichititse kukhala ndi dzanja laulesi mu utumiki wa Yehova, ndipo vuto limeneli linanenedweratu motani mu ulosi wa Zefaniya?
15 Chachiŵiri, tiyenera kukhala maso ndi zotulukapo zowononga za mphwayi. M’maiko ambiri Akumadzulo, kusasamala za zinthu zauzimu kungakhale kolefula kwa alaliki ena a uthenga wabwino. Mphwayi yotero inaliko m’tsiku la Zefaniya. Yehova anati mwa mneneri wake: “Ndidzalanga amunawo . . . onena m’mtima mwawo, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.” (Zefaniya 1:12) Polemba za vesi limeneli mu Cambridge Bible for Schools and Colleges, A. B. Davidson anati ilo limanena za anthu amene “analoŵereredwa ndi mphwayi kwakuti mtima wawo unakhala wosakhudzika kapena ngakhale okayikira za kuloŵererapo kwa mphamvu ina yapamwamba pa zochita za anthu.”
16. Kodi ndi maganizo otani amene ambiri ali nawo m’matchalitchi a Dziko Lachikristu, koma kodi ndi chilimbikitso chotani chimene Yehova akutipatsa?
16 Mphwayi ndi mzimu wofala lerolino kumadera ambiri a dziko lapansi, makamaka m’maiko okhupuka kwambiri. Ngakhale anthu a m’matchalitchi a Dziko Lachikristu sakhulupirira konse kuti Yehova Mulungu adzaloŵererapo pa zochita za anthu m’tsiku lathu. Iwo amakana pamene tiyesayesa kuwafika ndi uthenga wabwino wa Ufumu mwina mwa kuseka kosuliza kapena ndi yankho lalifupi lakuti “Ndilibe nthaŵi!” M’mikhalidwe imeneyi, kulimbikira kuchitira umboni kumakhala kovuta kwambiri. Kumayesa chipiriro chathu. Koma kupyolera mwa ulosi wa Zefaniya, Yehova amapatsa mphamvu anthu ake okhulupirika, akumati: “Manja anu asakhale olefuka. Yehova Mulungu wako ali pakati pako, [pokhala Wamphamvu, iye adzapulumutsa]; adzakondwera nawe ndi chimwemwe, adzakhala [chete, NW] m’chikondi chake; adzasekerera nawe ndi kuimbirapo.”—Zefaniya 3:16, 17.
17. Kodi ndi chitsanzo chabwino chiti chimene atsopano pakati pa nkhosa zina ayenera kutsanzira, ndipo motani?
17 Zili zoona m’mbiri yamakono ya anthu a Yehova kuti otsalira, limodzinso ndi achikulire okhala pakati pa nkhosa zina, achita ntchito yaikulu yakututa m’masiku ano otsiriza. Akristu onsewa okhulupirika asonyeza chipiriro pazaka makumi ambiri. Sanalole mphwayi ya unyinji wa anthu m’Dziko Lachikristu kuwalefula. Chotero atsopano okhala pakati pa nkhosa zina asagwetsedwe ulesi ndi mphwayi ya zinthu zauzimu yofala lerolino m’maiko ambiri. Asaloletu ‘manja awo kukhala olefuka,’ kapena kuliphitika. Agwiritsire ntchito mpata uliwonse kugaŵira Nsanja ya Olonda, Galamukani!, ndi zofalitsa zina zabwino zokonzedwa makamaka kuthandiza anthu onga nkhosa kuphunzira choonadi cha tsiku la Yehova ndi madalitso otsatirapo.
Tisatope Pamene Tikuyembekezera Tsiku Lalikulu!
18, 19. (a) Kodi ndi chilimbikitso chotani cha kupirira chimene timapeza pa Mateyu 24:13 ndi Yesaya 35:3, 4? (b) Kodi tidzadalitsidwa motani ngati mogwirizana tipitiriza mu utumiki wa Yehova?
18 Yesu anati: “Iye wakulimbikira chilimbikire kufikira kuchimaliziro, yemweyo adzapulumuka.” (Mateyu 24:13) Choncho, tisakhale ndi “manja opanda mphamvu” kapena “maondo agwedwegwede” pamene tikuyembekezera tsiku lalikulu la Yehova! (Yesaya 35:3, 4) Ulosi wa Zefaniya umanena molimbikitsa ponena za Yehova kuti: “Pokhala Wamphamvu, iye adzapulumutsa.” (Zefaniya 3:17) Inde, Yehova adzapulumutsa “khamu lalikulu” kupyola mbali yomaliza ya “chisautso chachikulu,” pamene adzalamula Mwana wake kuswa mitundu yandale imene imapitirizabe “kudzikuza” pa anthu ake.—Chivumbulutso 7:9, 14; Zefaniya 2:10, 11; Salmo 2:7-9.
19 Pamene tsiku lalikulu la Yehova likufika, tiyeni tipite patsogolo mwachangu, tikumamtumikira “pheŵa ndi pheŵa”! (Zefaniya 3:9) Mwakutero, ifeyo ndi ena osa-ŵerengeka tidzaikidwa pakati pa amene ‘adzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova’ ndi kuona kuyeretsedwa kwa dzina lake loyera.—Zefaniya 2:3.
[Mawu a M’munsi]
a Ngati mufuna malongosoledwe atsatanetsatane a “chinenero choyera,” onani Nsanja ya Olonda ya April 1, 1991, masamba 20-5, ndi May 1, 1991, masamba 10-20.
Kubwereza
◻ Kodi ndi pambali ziti zimene mkhalidwe wachipembedzo m’Dziko Lachikristu ulili wofanana ndi uja wa m’tsiku la Zefaniya?
◻ Kodi atsogoleri andale ambiri lerolino amafanana motani ndi “akalonga” aboma m’nthaŵi ya Zefaniya?
◻ Kodi ndi malonjezo ati m’buku la Zefaniya amene akwaniritsidwa pa otsalira?
◻ Kodi anthu mamiliyoni afika pakuzindikira chiyani?
◻ Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kulola manja athu kulefuka mu utumiki wa Yehova?
[Zithunzi patsamba 15]
Monga Zefaniya, otsalira a Akristu odzozedwa okhulupirika akhala akulengeza ziweruzo za Yehova mopanda mantha
[Zithunzi patsamba 18]
“Nkhosa zina” sizinalole mphwayi ya anthu kuwalefula