“Mundilindire”
“Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova.”—ZEFANIYA 3:8.
1. Kodi ndi chenjezo lotani limene linaperekedwa ndi mneneri Zefaniya, ndipo nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika kwa anthu alerolino?
“TSIKU lalikulu la Yehova lili pafupi.” Mfuu imeneyi yochenjeza inaperekedwa ndi mneneri Zefaniya pakati pa zaka za zana lachisanu ndi chiŵiri B.C.E. (Zefaniya 1:14) Pazaka 40 kapena 50, ulosiwo unakwaniritsidwa pamene tsiku la kupereka ziweruzo za Yehova linafika pa Yerusalemu ndi pa mitundu ija imene inanyoza uchifumu wa Yehova mwa kusautsa anthu ake. Kodi nchifukwa ninji zimenezi zili zofunika kwambiri kwa anthu okhala kumapeto kwa zaka za zana la 20? Tikukhala panthaŵi imene “tsiku lalikulu” lomaliza la Yehova likuyandikira mofulumira. Monga momwe zinalili m’nthaŵi ya Zefaniya, “mkwiyo . . . waukali” wa Yehova uli pafupi kuyakira Dziko Lachikristu—lofanana ndi Yerusalemu m’nthaŵi zamakono—ndi mitundu yonse imene imasautsa anthu a Yehova ndi kunyoza uchifumu wake wachilengedwe chonse.—Zefaniya 1:4; 2:4, 8, 12, 13; 3:8; 2 Petro 3:12, 13.
Zefaniya—Mboni Yolimba Mtima
2, 3. (a) Kodi nchiyani chimene tikudziŵa ponena za Zefaniya, ndipo nchiyani chikusonyeza kuti anali mboni ya Yehova yolimba mtima? (b) Kodi ndi maumboni otani amene akutithandiza kudziŵa nthaŵi ndi malo kumene Zefaniya analoserako?
2 Tikudziŵa zochepa ponena za mneneri Zefaniya, amene dzina lake (m’Chihebri, Tsephan·yahʹ) limatanthauza “Yehova Wabisa (Wakundika).” Komabe, mosiyana ndi aneneri ena, Zefaniya analongosola mzera wake wobadwira kufikira ku mbadwo wachinayi, kwa “Hezekiya.” (Zefaniya 1:1; yerekezerani ndi Yesaya 1:1; Yeremiya 1:1; Ezekieli 1:3.) Zimenezi nzachilendo kwambiri kwakuti othirira ndemanga ambiri amati agogo ŵa agogo ake anali Mfumu Hezekiya yokhulupirikayo. Ngati anali ameneyo, ndiye kuti Zefaniya anali wapabanja lachifumu, ndipo zimenezi zingakhale zitawonjezera mphamvu ya zilengezo zake zoŵaŵa zotsutsa akalonga a Yuda ndipo zingakhale zitasonyeza kuti iye anali mboni ndi mneneri wa Yehova wolimba mtima. Kudziŵa kwake mwakuya malo a Yerusalemu ndi zimene zinali kuchitika m’bwalo la mfumu kumasonyeza kuti iye angakhale atalengeza ziweruzo za Yehova m’malikuluwo.—Onani Zefaniya 1:8-11, NW, mawu amtsinde.
3 Chapadera ndi choonadi chakuti, pamene Zefaniya analengeza ziweruzo zaumulungu kwa “akalonga” aboma la Yuda (anthu apamwamba, kapena makosana) ndi “ana a mfumu,” iye sanaitchule konse mfumuyo m’ziweruzo zake.a (Zefaniya 1:8; 3:3) Zimenezi zikusonyeza kuti Mfumu Yosiya wachichepere anali atasonyeza kale chikondi chake pa kulambira koyera, ngakhale kuti, chifukwa cha mkhalidwe umene Zefaniya anatsutsa, iye mwachionekere anali asanayambe masinthidwe ake achipembedzo. Zonsezi zikusonyeza kuti Zefaniya analosera m’Yuda m’zaka zoyambirira za Yosiya, amene analamulira kuyambira mu 659 mpaka 629 B.C.E. Kulosera kwamphamvu kwa Zefaniya mosakayika kunachititsa Yosiya wachichepereyo kuzindikira kwambiri kupembedza mafano, chiwawa, ndi kuipa zimene zinafala m’Yuda panthaŵiyo ndi kumlimbikitsa pambuyo pake kuchita mkupiti wochotsa kupembedza mafano.—2 Mbiri 34:1-3.
Zifukwa za Mkwiyo Waukali wa Yehova
4. Kodi Yehova anasonyeza mkwiyo wake pa Yuda ndi Yerusalemu mwa mawu otani?
4 Yehova anali ndi chifukwa chabwino chokwiyira atsogoleri ndi okhala m’Yuda ndi malikulu ake m’Yerusalemu. Mwa mneneri wake Zefaniya, iye anati: “Ndidzatambasulira dzanja langa pa Yuda, ndi pa onse okhala m’Yerusalemu; ndipo ndidzawononga otsala a Baala kuwachotsa m’malo muno, ndi dzina la [ansembe a milungu yakunja, NW] pamodzi ndi ansembe; ndi iwo akulambira khamu la kumwamba pamwamba pa matsindwi; ndi iwo akulambira, akulumbira pali Yehova, nalumbiranso pali [Malikamu, NW].”—Zefaniya 1:4, 5.
5, 6. (a) Kodi mkhalidwe wachipembedzo m’Yuda panthaŵi ya Zefaniya unali wotani? (b) Kodi mkhalidwe wa atsogoleri aboma la Yuda ndi anthu awo unali wotani?
5 Yuda anaipitsidwa ndi madzoma onyansa a kubala a kulambira Baala, kupenda nyenyezi kwauchiŵanda, ndi kulambira mulungu wachikunja Malikamu. Ngati Malikamu ndiyenso Moleki, malinga ndi mmene ena amanenera, ndiye kuti kulambira konyenga kwa Yuda kunaphatikizapo kupereka ana nsembe konyansa. Miyambo yachipembedzo yotero inali yonyansa pamaso pa Yehova. (1 Mafumu 11:5, 7; 14:23, 24; 2 Mafumu 17:16, 17) Iwo anaputa mkwiyo wake kwambiri popeza opembedza mafanowo analumbirabe m’dzina la Yehova. Iye sakanatha kulekerera chidetso chotero chachipembedzo ndipo anati adzadula ansembe achikunja ndi ampatuko omwe.
6 Ndiponso, atsogoleri aboma la Yuda anali oipa. Akalonga ake anali ngati “mikango yobangula” yolusa, ndipo oweruza ake anali ngati “mimbulu” yolusa. (Zefaniya 3:3) Anthu awo anaimbidwa mlandu wa ‘kudzaza nyumba ya ambuye wawo ndi chiwawa ndi chinyengo.’ (Zefaniya 1:9) Kukondetsa zinthu zakuthupi kunali kofala. Ambiri anali kudyerera mkhalidwewo kuti akundike chuma.—Zefaniya 1:13.
Zikayikiro Ponena za Tsiku la Yehova
7. Kodi Zefaniya analosera kwa nthaŵi yaitali motani lisanadze “tsiku lalikulu la Yehova,” ndipo mkhalidwe wauzimu wa Ayuda ambiri unali wotani?
7 Monga momwe taonera kale, mkhalidwe woipa wachipembedzo umene unaliko m’tsiku la Zefaniya umasonyeza kuti iye anachita ntchito yake monga mboni ndi mneneri Mfumu Yosiya isanayambe mkupiti wake wochotsa kupembedza mafano, pafupifupi 648 B.C.E. (2 Mbiri 34:4, 5) Pamenepa, nkwachionekere kuti Zefaniya analosera zaka zosachepera 40 “tsiku lalikulu la Yehova” lisanafike pa ufumu wa Yuda. Tsikulo lisanafike, Ayuda ambiri anali ndi zikayikiro ndipo ‘anabwerera’ kusiya kutumikira Yehova, nakhala amphwayi. Zefaniya akulankhula za aja “osamfuna Yehova, kapena kufunsira kwa iye.” (Zefaniya 1:6) Mwachionekere, anthu m’Yuda anali amphwayi, osafuna kudzivuta ndi za Mulungu.
8, 9. (a) Kodi nchifukwa ninji Yehova anafuna kusanthula “amunawo okhala ndi nsenga”? (b) Kodi ndi motani mmene Yehova anali kudzalunjikitsira nkhope yake kwa okhala m’Yuda ndi atsogoleri awo aboma ndi achipembedzo?
8 Yehova anadziŵikitsa chifuno chake cha kusanthula aja omwe anati ndi anthu ake. Pakati pa amene anati ndi olambira ake, iye anali kudzafunafuna aja amene mitima yawo inali ndi zikayikiro ponena za kukhoza kwake ndi cholinga chake cha kuloŵererapo pa zochita zaumunthu. Iye anati: “Kudzachitika nthaŵi yomweyi kuti ndidzasanthula Yerusalemu ndi nyali, ndipo ndidzalanga amunawo okhala ndi nsenga, onena m’mtima mwawo, Yehova sachita chokoma, kapena kuchita choipa.” (Zefaniya 1:12) Mawuwo “amunawo okhala ndi nsenga” (okhudza kupanga vinyo) amanena za aja amene akhazikika pansi, monga nsenga pansi pa mbiya, ndipo safuna kuwasokoneza ndi chilengezo chilichonse cha kuloŵererapo kwa Mulungu komayandikirako pa zochita za anthu.
9 Yehova anali kudzalunjika nkhope yake kwa okhala m’Yuda ndi Yerusalemu ndi ansembe awo amene anasanganiza kulambira kwake ndi chikunja. Ngati iwo anamva kukhala otetezereka, monga ngati mumdima wa usiku mkati mwa makoma a Yerusalemu, iye anali kudzawafunafuna monga ngati anali ndi nyali zoŵala zimene zikanaloŵa mumdima wauzimu umene anabisalamo. Iye anali kudzawagubuduza kuwatulutsa mu mphwayi yawo yachipembedzo, choyamba mwa mauthenga owopsa achiweruzo, ndiyeno mwa kupereka ziweruzo zimenezo.
“Tsiku Lalikulu la Yehova Lili Pafupi”
10. Kodi Zefaniya analifotokoza motani “tsiku lalikulu la Yehova”?
10 Yehova anauzira Zefaniya kulengeza kuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi, lili pafupi lifulumira kudza, mawu a tsiku la Yehova [ali oŵaŵa, NW].” (Zefaniya 1:14) Inde masiku oŵaŵa anali kuyembekezera aliyense—ansembe, akalonga, ndi anthu—amene anakana kulabadira chenjezo ndi kuyambiranso kulambira koyera. Pofotokoza tsikulo la kupereka chiweruzo, ulosiwo ukupitiriza kuti: “Tsikulo ndi tsiku lamkwiyo, tsiku lamasauko ndi lopsinja[,] tsiku labwinja, ndi chipasuko, tsiku lamdima ndi lachisirira, tsiku lamitambo ndi lakuda bii; tsiku la lipenga ndi lakufuulira midzi yamalinga, ndi nsanja zazitali za kungondya.”—Zefaniya 1:15, 16.
11, 12. (a) Kodi ndi uthenga wachiweruzo wotani umene unalengezedwa pa Yerusalemu? (b) Kodi chuma chakuthupi chikanawapulumutsa Ayuda?
11 Pazaka makumi angapo, magulu a nkhondo a Babulo anali kudzaukira Yuda. Yerusalemu sanayembekezere kudzapulumuka. Zigawo zake zokhalako anthu ndi zamalonda zinali kudzasakazidwa. “Ndipo tsiku ilo, ati Yehova, kudzakhala phokoso lakulira lochokera kuchipata chansomba, ndi kuchema kochokera kudera lachiŵiri, ndi kugamuka kwakukulu kochokera kuzitunda. Chemani okhala m’chigwa [“Makiteshi,” NW] [chigawo cha Yerusalemu], pakuti amalonda onse atayika, onsewo osenza siliva awonongeka.”—Zefaniya 1:10, 11.
12 Pokhala sanafune kukhulupirira kuti tsiku la Yehova linali pafupi, Ayuda ambiri anatanganidwa kwambiri ndi malonda aphindu. Koma kupyolera mwa mneneri wake wokhulupirika Zefaniya, Yehova ananeneratu kuti chuma chawo chidzakhala ‘chakufunkhidwa; ndi nyumba zawo zabwinja.’ Sadzamwa vinyo amene anapanga, ndipo “ngakhale siliva wawo, ngakhale golidi wawo sizidzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova.”—Zefaniya 1:13, 18.
Mitundu Ina Iweruzidwa
13. Kodi ndi uthenga wachiweruzo wotani umene Zefaniya analengeza kwa Moabu, Amoni, ndi Asuri?
13 Kupyolera mwa mneneri wake Zefaniya, Yehova anasonyeza mkwiyo wake pa mitundu imene inali itasautsa anthu ake. Iye anati: “Ndinamva kutonza kwa Moabu ndi matukwano a ana a Amoni, zimene anatonza nazo anthu anga, ndi kudzikuza pa malire awo. Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, Zedi Moabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha. . . . Ndipo adzatambasulira dzanja lake kumpoto nadzawononga Asuri, nadzasanduliza Nineve akhale bwinja, wouma ngati chipululu.”—Zefaniya 2:8, 9, 13.
14. Kodi pali umboni wotani wakuti mitundu yakunja ‘inadzikuza’ pa Aisrayeli ndi Mulungu wawo, Yehova?
14 Moabu ndi Amoni anali adani akalekale a Israyeli. (Yerekezerani ndi Oweruza 3:12-14.) Mwala wa Moabu, umene uli mu Louvre Museum ku Paris, umasonyeza mawu olembedwa a kudzitama kwa Mfumu ya Moabu Mesa. Iye modzikweza akusimba za kulanda kwake mizinda ingapo ya Israyeli mothandizidwa ndi mulungu wake Kemosi. (2 Mafumu 1:1) Yeremiya, wokhalako nthaŵi imodzimodzi ndi Zefaniya, analankhula zakuti Aamoni anakhala m’dera la Gadi la Israyeli m’dzina la mulungu wawo Malikamu. (Yeremiya 49:1, NW) Ponena za Asuri, Mfumu Salimanezere V anali atazinga ndi kulanda Samariya zaka ngati zana limodzi lisanafike tsiku la Zefaniya. (2 Mafumu 17:1-6) Patapita nthaŵi pang’ono, Mfumu Sanakeribu anaukira Yuda, kulanda mizinda yake yambiri yamalinga, ndipo ngakhale kuwopseza Yerusalemu. (Yesaya 36:1, 2) Nthumwi ya mfumu ya Asuri inadzikuzadi pamaso pa Yehova pamene inali kukakamiza Yerusalemu kugonja.—Yesaya 36:4-20.
15. Kodi Yehova anali kudzaitsitsa motani milungu ya amitundu imene inadzikuza pa anthu ake?
15 Salmo 83 limatchula mitundu ingapo, kuphatikizapo Moabu, Amoni, ndi Asuri, imene inadzikuza pa Israyeli, niiti modzitama: “Tiyeni tiwawononge asakhalenso mtundu wa anthu; ndipo dzina la Israyeli lisakumbukikenso.” (Salmo 83:4) Mneneri Zefaniya analengeza molimba mtima kuti mitundu yonseyi yodzitukumula ndi milungu yawo idzatsitsidwa ndi Yehova wa makamu. “Ichi adzakhala nacho m’malo mwa kudzikuza kwawo, chifukwa anatonza, nadzikuza pa anthu a Yehova wa makamu. Yehova adzawakhalira wowopsa; pakuti adzaondetsa milungu yonse ya padziko lapansi; ndipo adzamlambira iye, yense pamalo pake, a m’zisumbu zonse za amitundu.”—Zefaniya 2:10, 11.
‘Mulindire’
16. (a) Kodi ndani amene kuyandikira kwa tsiku la Yehova kunapatsa chimwemwe, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi ndi chiitano chosonkhezera chotani chimene chinaperekedwa kwa otsalira okhulupirika ameneŵa?
16 Pamene kuwodzera kwauzimu, kukayikira, kupembedza mafano, chinyengo, ndi kukondetsa zinthu zakuthupi zinali zofala pakati pa atsogoleri ndi ambiri okhala m’Yuda ndi Yerusalemu, mwachionekere Ayuda ena okhulupirika anamvetsera maulosi ochenjeza a Zefaniya. Anachita chisoni ndi machitachita onyansa a akalonga, oweruza, ndi ansembe a Yuda. Zilengezo za Zefaniya zinawatonthoza okhulupirika ameneŵa. M’malo mowasautsa, kuyandikira kwa tsiku la Yehova kunawapatsa chimwemwe, chifukwa linali kudzathetsa machitachita oipa amenewo. Otsalira okhulupirika ameneŵa anayankha chiitano chosonkhezera cha Yehova chakuti: “Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali.”—Zefaniya 3:8.
17. Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene mauthenga achiweruzo a Zefaniya anayamba kukwaniritsidwa pa mitundu?
17 Aja amene anamva chenjezolo sanadabwe ndi zimenezo. Ambiri anaonako pamene ulosi wa Zefaniya unakwaniritsidwa. Mu 632 B.C.E., Nineve analandidwa ndi kuwonongedwa ndi mgwirizano wa Ababulo, Amedi, ndi makamu ochokera kumpoto, mwinamwake Asikuti. Wolemba mbiri Will Durant akusimba kuti: “Gulu la nkhondo la Ababulo lotsogozedwa ndi Nabopolassar linagwirizana ndi gulu la nkhondo la Amedi lotsogozedwa ndi Cyaxares ndi khamu la Asikuti ochokera ku Caucasus, ndipo mosavutika konse ndi mofulumira kwenikweni analanda mphala zakumpoto. . . . Pakuukira kumodzi Asuri anazimiririka m’mbiri.” Izi nzimenedi Zefaniya analosera.—Zefaniya 2:13-15.
18. (a) Kodi chiweruzo chaumulungu chinaperekedwa motani pa Yerusalemu, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi ulosi wa Zefaniya wonena za Moabu ndi Amoni unakwaniritsidwa motani?
18 Ayuda ambiri amene analindira Yehova anaonakonso pamene ziweruzo zake zinaperekedwa pa Yuda ndi Yerusalemu. Ponena za Yerusalemu, Zefaniya anali atalosera kuti: “Tsoka uyo wopanduka, ndi wodetsedwa, ndiye mudzi wozunza! Sanamvera mawu, sanalola kulangizidwa; sanakhulupirira Yehova, sanayandikira kwa Mulungu wake.” (Zefaniya 3:1, 2) Chifukwa cha kusakhulupirika kwake, Yerusalemu anazingidwa kaŵiri ndi Ababulo ndipo pomaliza anamlanda ndi kumuwononga mu 607 B.C.E. (2 Mbiri 36:5, 6, 11-21) Ponena za Moabu ndi Amoni, malinga ndi wolemba mbiri wachiyuda Josephus, chaka chachisanu pambuyo pa kugwa kwa Yerusalemu, Ababulo anathira nkhondo pa iwo ndi kuwagonjetsa. M’kupita kwa nthaŵi iwo sanakhalekonso, monga mwa ulosiwo.
19, 20. (a) Kodi Yehova anawafupa motani aja amene anamlindira iye? (b) Kodi nchifukwa ninji zochitika zimenezi zikutikhudza, ndipo tidzapenda chiyani m’nkhani yotsatira?
19 Kukwaniritsidwa kwa mbali zimenezi ndi zina za ulosi wa Zefaniya kunalimbitsa chikhulupiriro cha Ayuda ndi osakhala Ayuda amene analindira Yehova. Ena amene anapulumuka chiwonongeko chimene chinagwera Yuda ndi Yerusalemu ndiwo Yeremiya, Ebedi-Meleki Mkusi, ndi nyumba ya Yonadabu, Mrekabu. (Yeremiya 35:18, 19; 39:11, 12, 16-18) Ayuda okhulupirika okhala mu ukapolo ndi mbadwa zawo, amene anapitiriza kuyembekeza Yehova, anakhala mbali ya otsalira okondwera amene analanditsidwa ku Babulo mu 537 B.C.E. nabwerera ku Yuda kukakhazikitsanso kulambira koyera.—Ezara 2:1; Zefaniya 3:14, 15, 20.
20 Kodi zonsezi zikutanthauzanji m’nthaŵi yathu? M’njira zambiri mkhalidwe wa m’tsiku la Zefaniya ngwofanana ndi zinthu zonyansa zimene zikuchitikira m’Dziko Lachikristu lerolino. Ndiponso, maganizo osiyanasiyana a Ayuda panthaŵiyo amafanana ndi maganizo amene amapezeka lerolino, nthaŵi zina ngakhale pakati pa anthu a Yehova. Imeneyi ndiyo nkhani imene idzafotokozedwa m’mutu wotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Zikuchita ngati kuti mawuwo “ana a mfumu” akunena za akalonga onse apabanja la mfumu, pakuti ana ake a Yosiya anali aang’ono kwambiri panthaŵiyo.
Kubwereza
◻ Kodi mkhalidwe wachipembedzo unali wotani m’Yuda m’tsiku la Zefaniya?
◻ Kodi ndi mikhalidwe yotani imene inali pakati pa atsogoleri aboma, ndipo maganizo a anthu ambiri anali otani?
◻ Kodi ndi motani mmene mitundu inadzikuzira pa anthu a Yehova?
◻ Kodi ndi chenjezo lotani limene Zefaniya anapereka kwa Yuda ndi mitundu ina?
◻ Kodi aja amene analindira Yehova anafupidwa motani?
[Chithunzi patsamba 9]
Mwala wa Moabu umatsimikizira kuti Mfumu Mesa ya Moabu inalankhula mawu otonza Israyeli wakale
[Mawu a Chithunzi]
Mwala wa Moabu: Musée du Louvre, Paris
[Chithunzi patsamba 10]
Kuchirikiza ulosi wa Zefaniya, mwala uwu wozokota wa Mbiri ya Babulo umasimba za chiwonongeko cha Nineve chochitidwa ndi mgwirizano wa magulu a nkhondo
[Mawu a Chithunzi]
Mwala wozokota: Mwachilolezo cha The British Museum