Zefaniya
1 Mʼmasiku a Yosiya+ mwana wa Amoni+ mfumu ya Yuda, Yehova analankhula kudzera mwa Zefaniya* mwana wa Kusa, mwana wa Gedaliya, mwana wa Amariya, mwana wa Hezekiya. Iye anati:
2 “Ine ndidzasesa chilichonse chimene chili panthaka,” watero Yehova.+
3 “Ndidzasesa anthu ndi nyama.
Ndidzasesa mbalame zamumlengalenga ndiponso nsomba zamʼnyanja.+
Ndidzasesanso zopunthwitsa*+ pamodzi ndi anthu oipa,
Ndipo ndidzawononga anthu onse padziko,” watero Yehova.
4 “Ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwononga Yuda,
Ndiponso anthu onse okhala mu Yerusalemu.
Ndidzawononga chilichonse chokhudza Baala+ pamalowa.
Ndidzawononganso ansembe komanso dzina la ansembe a mulungu wachilendo.+
5 Ndidzawononga anthu amene amakwera padenga nʼkumagwadira magulu a zinthu zakumwamba.*+
Komanso amene amagwada ndiponso kulumbira kuti adzakhala okhulupirika kwa Yehova+
Koma nʼkumalumbiranso kuti adzakhala okhulupirika kwa Malikamu.+
6 Ndidzawononga amene asiya kutsatira Yehova,+
Komanso amene sanafunefune Yehova kapena kufunsa malangizo kwa iye.”+
7 Khalani chete pamaso pa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi,+
Yehova wakonza nsembe ndipo wayeretsa anthu amene wawaitana.
8 “Pa tsiku limene Yehova adzapereke nsembe, ine ndidzaweruza akalonga,
Ana a mfumu+ ndi onse ovala zovala zachilendo.
9 Pa tsiku limenelo ndidzaweruza aliyense amene amakwera pamalo omwe pamakhala mpando wachifumu,
Anthu amene adzaza nyumba ya ambuye awo ndi chiwawa ndiponso chinyengo.”
10 Yehova wanena kuti: “Patsiku limenelo,
Ku Geti la Nsomba+ kudzamveka phokoso la anthu,
Ndipo Kumbali Yatsopano ya mzinda kudzamveka kulira mokweza.+
Kumapiri kudzamveka phokoso la chiwonongeko.
11 Lirani mofuula inu anthu okhala ku Makitesi,*
Chifukwa amalonda onse awonongedwa.
Ndipo onse amene amayeza siliva pasikelo aphedwa.*
12 Pa nthawi imeneyo ndidzafufuza ndi nyale mosamala kwambiri mu Yerusalemu,
Ndipo ndidzaweruza anthu amene akukhala mosatekeseka* nʼkumaganiza kuti,
‘Yehova sadzachita zabwino kapena zoipa.’+
13 Chuma chawo chidzatengedwa ndipo nyumba zawo zidzawonongedwa.+
Iwo adzamanga nyumba, koma sadzakhalamo.
Iwo adzalima minda ya mpesa koma sadzamwa vinyo wake.+
14 Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi.+
Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.+
Mkokomo wa tsiku la Yehova ukubwera ndi zowawa.+
Pa tsiku limenelo msilikali adzalira.+
15 Tsiku limenelo ndi tsiku la mkwiyo,+
Tsiku la masautso ndi zowawa,+
Tsiku lowononga ndi la mphepo yamkuntho,
Tsiku la mdima wochititsa mantha,+
Tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani,+
16 Tsiku loliza lipenga ndiponso la mfuu yankhondo,+
Pochenjeza mizinda ya mipanda yolimba komanso nsanja zazitali zamʼmakona.+
Magazi awo adzakhuthulidwa pansi ngati fumbi,
Ndipo matumbo awo adzakhuthulidwa pansi ngati ndowe.+