Mawu a Yehova Ndi Amoyo
Mfundo Zazikulu za M’mabuku a Hagai ndi Zekariya
CHINALI chaka cha 520 B.C.E., patatha zaka 16 kuchokera pamene Ayuda amene anachoka ku ukapolo ku Babulo anamanga maziko a kachisi wa Yehova ku Yerusalemu. Kachisiyu anali asanamalizidwe, ndipo ntchito yomanga kachisiyo inali italetsedwa. Yehova anatumiza mneneri Hagai kuti akauze anthuwa mawu Ake. Patatha miyezi iwiri anatumizanso mneneri Zekariya.
Hagai ndi Zekariya anali ndi cholinga chimodzi. Cholinga chawo chinali choti akalimbikitse anthuwa kuti ayambirenso ntchito yomanga kachisiyo. Aneneriwa anakwaniritsa cholinga chawocho, motero patatha zaka zisanu, kachisiyo anamalizidwa. Zimene Hagai ndi Zekariya ananena zinalembedwa m’mabuku a Baibulo amene ali ndi mayina awowa. Buku la Hagai linamalizidwa mu 520 B.C.E. ndipo la Zekariya linamalizidwa mu 518 B.C.E. Monga aneneri amenewa ifenso tili ndi ntchito imene Mulungu anatipatsa, imene tiyenera kuimaliza dongosolo la zinthu lino lisanathe. Ntchito yake ndi yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira. Tiyeni tione kuti tingalimbikitsidwe bwanji ndi mabuku a Hagai ndi Zekariya.
“MTIMA WANU USAMALIRE NJIRA ZANU”
Hagai anapereka mauthenga anayi olimbikitsa kwambiri m’masiku 112. Uthenga woyamba unali wakuti: “Mtima wanu usamalire njira zanu. Kwerani kudziko lamapiri, ndi kukwera nayo mitengo, nimumange nyumbayi; ndipo kudzandikomera, ndipo ndidzalemekezedwa, ati Yehova.” (Hagai 1:7, 8) Anthuwo anachita zimenezi. Uthenga wachiwiri unali ndi lonjezo lakuti: “[Ine Yehova] ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero.”—Hagai 2:7.
Malinga ndi uthenga wachitatu, ‘anthuwo komanso ntchito yonse ya manja awo’ inali yodetsedwa pamaso pa Yehova chifukwa choti ananyalanyaza ntchito yomanganso kachisiyo. Komabe kuchokera pa tsiku limene anayambanso kumanga kachisiyo, Yehova ‘anawadalitsa.’ Uthenga wachinayi unali wakuti Yehova ‘adzawononga mphamvu ya maufumu a amitundu’ n’kukhazikitsa Kazembe Zerubabele kuti akhale ngati “mphete yosindikizira.”—Hagai 2:14, 19, 22, 23.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
1:6—Kodi mawu akuti “mukumwa, koma osakoledwa” akutanthauza chiyani? Mawu amenewa akungonena za kusowa kwa vinyo. Chifukwa choti Yehova sanadalitse anthuwa, sankapeza vinyo wambiri, kusonyeza kuti anali wochepa zedi moti sakanatha n’komwe kuwakola.
2:6, 7, 21, 22—Kodi ndani kapena n’chiyani chimene chikugwedeza zinthuzi, ndipo kugwedeza kumeneko kukuchititsa chiyani? Yehova ndiye ‘akugwedeza amitundu onse’ kudzera m’ntchito ya padziko lonse yolalikira uthenga wa Ufumu. Ndipo ntchito yolalikirayo ikuchititsa kuti “zofunika za amitundu onse” zifike m’nyumba ya Yehova, ndi kuidzaza ndi ulemerero. M’kupita kwa nthawi, “Yehova wa makamu” ‘adzagwedeza miyamba ndi dziko lapansi, ndi nyanja, ndi mtunda womwe,’ pochotseratu dongosolo lonse la zinthu lomwe lilipoli.—Aheberi 12:26, 27.
2:9—Kodi ‘ulemerero wotsiriza wa nyumbayo unaposa woyambawo’ m’njira zotani? Zimenezi zinachitika m’njira zosachepera zitatu: Zaka zimene kachisiyu anakhala, amene anaphunzitsa pa kachisiyu, ndiponso khamu la anthu amene anapita kumeneku kukalambira Yehova. Ngakhale kuti kachisi waulemerero amene Solomo anamanga anakhala kwa zaka 420, kuchokera mu 1027 B.C.E. mpaka mu 607 B.C.E., nyumba yachiwiriyi inagwiritsidwa ntchito kwa zaka 580, kuyambira panthawi imene inamalizidwa mu 515 B.C.E. kufika panthawi imene inawonongedwa mu 70 C.E. Komanso Mesiya, Yesu Khristu anaphunzitsa m’nyumba yachiwiriyi, ndipo munafika anthu ambiri odzalambira Mulungu kuposa yakale ija.—Machitidwe 2:1-11.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:2-4. Tikamaletsedwa kuchita ntchito yathu yolalikira tisamasiye ‘kupitiriza kufuna ufumu choyamba’ n’cholinga choti tiyambe tachita kaye zofuna zathu.—Mateyo 6:33.
1:5, 7. Ndi bwino kuti ‘mtima wathu uzisamalira njira zathu’ n’kuganizira mmene zochita zathu zikukhudzira ubwenzi wathu ndi Mulungu.
1:6, 9-11; 2:14-17. Ayuda m’nthawi ya Hagai ankalimbikira kwambiri ntchito zawo koma sankadyerera thukuta lawolo. Iwo ankanyalanyaza kachisi, motero Mulungu sanawadalitse. Ifenso tiziika patsogolo zolinga zauzimu n’kumatumikira Mulungu ndi mtima wonse, ndipo tizikumbukira kuti kaya tili ndi zinthu zakuthupi zochepa kapena zambiri, ‘madalitso a Yehova ndiwo amalemeretsa.’—Miyambo 10:22.
2:15, 18. Yehova analimbikitsa Ayudawo kuti kuyambira tsiku limenelo aziganizira kwambiri m’mitima yawo za ntchito yomanganso kachisi, osati za zomwe anachita m’mbuyomo zonyalanyaza kachisiyo. Nafenso tiziyesetsa kuyang’ana m’tsogolo polambira Mulungu.
“NDI MPHAMVU AYI, KOMA NDI MZIMU WANGA”
Zekariya anayamba ntchito yake yauneneri polimbikitsa Ayuda kuti ‘abwerere kwa Yehova.’ (Zekariya 1:3) Masomphenya 8 amene iye anaona atanena zimenezi anatsimikizira kuti Mulungu anali nawo pantchito yomanganso kachisi. (Onani bokosi lakuti “Masomphenya 8 a Zekariya.”) Ntchito yomanganso kachisiyo sinafike pomalizidwa bwinobwino chifukwa cha ‘khamu la nkhondo kapena mphamvu, koma chinali chifukwa cha Mzimu wa Yehova.’ (Zekariya 4:6) Munthu wotchedwa Mphukira ndiye ‘adzamange Kachisi wa Yehova’ ndipo ‘adzakhala wansembe pampando wachifumu wake.’—Zekariya 6:12, 13.
Anthu a ku mzinda wa Beteli anatumiza anthu kuti akafunse ansembe nkhani ya miyambo ya kusala kudya pokumbukira kuwonongedwa kwa Yerusalemu. Yehova anauza Zekariya kuti kulira kumene kunachitika ku Yerusalemu pa miyambo inayi yotereyi kudzasanduka “chimwemwe ndi chikondwerero ndi nyengo zoikika zosekerera.” (Zekariya 7:2; 8:19) Mauthenga awiri amene akupereka pambuyo pa zimenezi ndi onena za chiweruzo kwa amitundu ndi aneneri onyenga, za maulosi okhudza Mesiya, ndiponso za kubwezeretsedwa kwa anthu a Mulungu.—Zekariya 9:1; 12:1.
Kuyankha Mafunso a M’Malemba:
2:1—N’chifukwa chiyani munthu anayeza Yerusalemu ndi chingwe? Zikuoneka kuti kuyeza kumeneku kukuimira kumangidwa kwa khoma loteteza mzindawo. Mngelo anauza munthuyo kuti mzinda wa Yerusalemu udzakula ndipo udzakhala wotetezedwa ndi Yehova.—Zekariya 2:3-5.
6:11-13—Kodi kuvekedwa ufumu kwa Mkulu wa Ansembe Yoswa, kunam’chititsa kukhala wansembe wachifumu? Ayi, Yoswa sanabadwire mumzera wachifumu wa Davide. Komabe, kuvekedwa kwake ufumu kunachitira chithunzi Mesiya. (Aheberi 6:20) Ulosi wonena za “Mphukira” unakwaniritsidwa mwa Wansembe wachifumu kumwamba Yesu Khristu. (Yeremiya 23:5) Monga mmene mkulu wa ansembe Yoswa anathandizira Ayuda amene anabwerera kwawo pantchito yomanga kachisi, Yesu Khristu nayenso ndi Mkulu wa Ansembe pa kulambira koona m’kachisi wauzimu wa Yehova.
8:1-23—Kodi mauthenga khumi amene atchulidwa m’mavesi amenewa anakwaniritsidwa liti? Uthenga uliwonse ukuyamba ndi mawu akuti: “Atero Yehova wa makamu” ndipo ndi lonjezo la mtendere limene Mulungu akuuza anthu ake. Ena mwa mauthenga amenewa anakwaniritsidwa m’zaka za m’ma 500 B.C.E., ndipo ena akhala akukwaniritsidwa kuyambira mu 1919 C.E., pomwe ena akukwaniritsidwa panopo.a
8:3—N’chifukwa chiyani Yerusalemu akutchedwa “mudzi wa choonadi”? Mzinda wa Yerusalemu usanawonongedwe mu 607 B.C.E., unali “mudzi wozunza,” wodzaza ndi aneneri ndiponso ansembe achinyengo komanso anthu osakhulupirika. (Zefaniya 3:1; Yeremiya 6:13; 7:29-34) Komano, kachisi atamangidwanso anthu n’kuyambanso kulambira Yehova mokhulupirika, m’kachisimo munayambanso kunenedwa mawu a choonadi okhudza kulambira koona, ndipo Yerusalemu anayamba kutchedwa “mudzi wa choonadi.”
11:7-14—Kodi n’chiyani chimene Zekariya anali kufanizira podula ndodo yotchedwa “Chisomo” ndi inanso yotchedwa “Chomanganitsa”? Pamenepa Zekariya anali kusonyezedwa monga munthu amene watumidwa ‘kukadyetsa zoweta zokaphedwa,’ kutanthauza anthu angati nkhosa amene anali kudyeredwa masuku pamutu ndi atsogoleri awo. Pantchito yake monga mbusa, Zekariya anali kuphiphiritsira Yesu Khristu, amene anatumizidwa kwa anthu amene Mulungu anachita nawo pangano koma anthuwo anamukana. Kudulidwa kwa ndodo yotchedwa “Chisomo” ija kunali kuphiphiritsira mfundo yakuti Mulungu adzathetsa pangano la Chilamulo lomwe anali nalo ndi Ayuda ndipo adzasiya kuchita nawo zinthu m’njira yowakomera. Kudulidwa kwa ndodo yotchedwa “Chomanganitsa” kunali kutanthauza kuthetsedwa kwa ubale wauzimu wa pakati pa Yuda ndi Isiraeli.
12:11—Kodi mawu akuti “maliro a Hadadirimoni m’chigwa cha Megidoni” akutanthauza chiyani? Mfumu Yosiya ya Yuda anaphedwa pankhondo yomwe ankamenyana ndi Farao Neko wa ku Iguputo “m’chigwa cha Megidoni” ndipo anamulira ‘m’nyimbo za maliro’ kwa zaka zambiri. (2 Mbiri 35:25) Motero, “maliro a Hadadirimoni” ayenera kuti akutanthauza kulira maliro a Yosiya.
Zimene Tikuphunzirapo:
1:2-6; 7:11-14. Yehova amasangalala ndipo amayanjanso anthu amene amalapa, kuvomereza chidzudzulo n’kubwerera kwa iye poyambanso kumutumikira ndi moyo wawo wonse. Komano, iye samvera zopempha za anthu amene ‘amakana kumvera, nakaniza phewa lawo, natseka makutu awo, kuti asamve’ uthenga wake.
4:6, 7. Palibe vuto lililonse limene mzimu wa Yehova unalephera kulithetsa pantchito yomanga kachisi kuti amalizidwe bwinobwino. Ifenso ngakhale titakumana ndi mavuto otani potumikira Mulungu tingathe kuwathetsa posonyeza chikhulupiriro mwa Yehova.—Mateyo 17:20.
4:10. Moyang’aniridwa ndi Yehova, Zerubabele ndi anthu ake anamaliza kumanga kachisi mogwirizana ndi miyezo yapamwamba ya Mulungu. Zimenezi zikusonyeza kuti si zovuta kwambiri kwa anthu opanda ungwiro kuchita zimene Yehova amafuna.
7:8-10; 8:16, 17. Kuti tiziyanjidwa ndi Yehova, tiyenera kuchita zinthu mwachilungamo, mwachikondi ndi mwachifundo ndiponso tiziuzana zoona.
8:9-13. Yehova amatidalitsa ‘manja athu akalimbika’ kuchita ntchito imene watipatsa. Madalitso amenewa ndi zinthu monga mtendere, kusatekeseka, ndiponso kupita patsogolo mwauzimu.
12:6. Anthu amene ali ndi maudindo pakati pa anthu a Yehova azikhala ngati “muuni wamoto” kutanthauza kuti azikhala achangu choonekera kwambiri.
13:3. Tizikhulupirika kwambiri kwa Mulungu ndi gulu lake kuposa mmene tingakhulupirikire kwa munthu wina aliyense, ngakhale titagwirizana naye motani.
13:8, 9. Anthu opanduka amene Yehova anasiya kuwayanja anali ambiri ndithu, anali magawo awiri pa magawo atatu a dziko lonselo. Ndi gawo limodzi lokha limene tingati linayengedwa ndi moto. Masiku ano, Matchalitchi Achikhristu, omwe ali ndi anthu ambiri amene amati ndi Akhristu, sayanjidwa ndi Yehova. Ndi Akhristu odzozedwa ochepa chabe, amene ‘aitana dzina la Yehova’ n’kulola kuti ayengedwe. Iwowa ndiponso okhulupirira anzawo aonetsa kuti si Mboni za Yehova m’dzina lokha ayi, koma ngakhalenso m’zochita.
Zitilimbikitse Kuchita Zinthu Mwachangu
Kodi uthenga wa Hagai ndi Zekariya uyenera kutikhudza bwanji masiku ano? Tikaganizira za mmene uthenga umenewu unalimbikitsira Ayuda kuti ayambe kuganizira kwambiri ntchito yomanganso kachisi, kodi sitilimbikitsidwa kuchita nawo mwachangu ntchito yolalikira za Ufumu ndi kupanga ophunzira?
Zekariya analosera kuti Mesiya adzabwera ‘atakwera pa bulu,’ ndiponso kuti adzaperekedwa ndi “ndalama zasiliva makumi atatu,” ndi kutinso adzakwapulidwa, ndiponso kuti “nkhosa zidzabalalika.” (Zekariya 9:9; 11:12; 13:7) Chikhulupiriro chathu chimalimba tikaganizira za kukwaniritsidwa kwa maulosi a Zekariya onena za Mesiya. (Mateyo 21:1-9; 26:31, 56; 27:3-10 ) Zimenezi zimatithandizanso kuti tizidalira kwambiri Mawu a Yehova ndiponso zimene watikonzera kuti tidzapulumuke.—Aheberi 4:12.
[Mawu a M’munsi]
[Bokosi patsamba 11]
MASOMPHENYA 8 A ZEKARIYA
1:8-17: Akutsimikizira kuti kachisi adzamalizidwa ndipo akusonyeza kuti Yerusalemu ndi mizinda ina mu Yuda idzadalitsidwa.
1:18-21: Akulonjeza kutha kwa ‘nyanga zinayi zimene zinabalalitsa Yuda,’ kutanthauza maboma onse amene anatsutsa kulambira Yehova.
2:1-13: Akusonyeza kuti mzinda wa Yerusalemu udzakula ndiponso kuti Yehova ‘adzakhala kwa iye linga la moto pozungulira pake’ kutanthauza kuti adzauteteza.
3:1-10: Akusonyeza kuti Satana ndiye anali kusonkhezera zoletsa ntchito yomanga kachisi ndipo akusonyezanso kuti Mkulu wa Ansembe, Yoswa analanditsidwa ndiponso kuyeretsedwa.
4:1-14: Akutsimikizira kuti mavuto aakulu ngati phiri adzasalazidwa ndiponso kuti Kazembe Zerubabele ndiye adzamalizitse ntchito yomanga kachisi.
5:1-4: Akutemberera anthu oipa amene sanalangidwe.
5:5-11: Akulosera mapeto a zoipa.
6:1-8: Akulonjeza kuti angelo amayang’anira ndi kuteteza.
[Chithunzi patsamba 8]
Kodi cholinga cha uthenga wa Hagai ndi Zekariya chinali chiyani?
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi anthu amene ali m’maudindo oyang’anira ali ngati “muuni wamoto” m’njira yotani?