Zekariya
1 Mʼmwezi wa 8, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya*+ mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti: 2 “Yehova anakwiyira kwambiri makolo anu.+
3 Uwauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Bwererani kwa ine,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, “ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’”
4 “‘Musakhale ngati makolo anu amene aneneri akale anawauza kuti: “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndiponso zochita zanu zoipa.’”’+
‘Koma iwo sanamvere ndipo sanatsatire mawu anga,’+ watero Yehova.
5 ‘Kodi makolo anuwo ali kuti pano? Ndipo “kodi aneneriwo anakhalabe ndi moyo mpaka kalekale?” 6 Ndinauza makolo anu malamulo oti azitsatira ndipo ndinatumiza atumiki anga aneneri kuti akawachenjeze zimene zidzawachitikire ngati sangatsatire malamulowo. Kodi zonse zimene ndinanena kuti zidzawachitikirazo sizinawachitikire?’+ Choncho iwo anabwerera kwa ine nʼkunena kuti: ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba watichitira zimene anakonza mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+
7 Pa tsiku la 24 la mwezi wa 11 womwe ndi mwezi wa Sebati,* mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido. Anamuuza kuti anene kuti: 8 “Ndinaona masomphenya usiku. Ndinaona munthu atakwera pahatchi* yomwe inaima pakati pa mitengo ya mchisu imene inali mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali mahatchi ofiira kwambiri, ofiirira ndi oyera.”*
9 Choncho ndinafunsa kuti: “Kodi amenewa ndi ndani mbuyanga?”
Mngelo amene ankalankhula nane anandiyankha kuti: “Ndikuuza kuti amenewa ndi ndani.”
10 Kenako munthu amene anaima pakati pa mitengo ya mchisu uja anati: “Amenewa atumizidwa ndi Yehova kuti ayendeyende padziko lapansi.” 11 Ndiyeno iwo anauza mngelo wa Yehova amene anaima pakati pa mitengo ya mchisu uja kuti: “Ife tayendayenda padziko lonse lapansi ndipo taona kuti pali bata komanso palibe chosokoneza.”+
12 Choncho mngelo wa Yehova anati: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, kodi Yerusalemu ndiponso mizinda ya Yuda+ imene munaikwiyira kwa zaka 70 zimenezi,+ simuichitira chifundo mpaka liti?”
13 Yehova anayankha mngelo amene ankalankhula nane uja mokoma mtima komanso ndi mawu olimbikitsa. 14 Ndiyeno mngelo amene ankalankhula nane uja anandiuza kuti: “Fuula kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti nditeteze Yerusalemu ndi Ziyoni.+ 15 Ndakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene akukhala mosatekeseka.+ Ndawakwiyira chifukwa chakuti ine ndinangokwiyira anthu anga pangʼono,+ koma anthu amenewa anakulitsa kwambiri mavuto a anthu angawo.”’+
16 Choncho Yehova wanena kuti, ‘“Ndidzabwerera ku Yerusalemu nʼkuchitira chifundo mzinda umenewu+ ndipo nyumba yanga idzamangidwa mumzindawu.+ Chingwe choyezera chidzatambasulidwa pa Yerusalemu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’
17 Fuulanso kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Mizinda yanga idzasefukiranso ndi zinthu zabwino. Yehova adzalimbikitsanso Ziyoni+ ndipo adzasankhanso Yerusalemu.”’”+
18 Kenako nditakweza maso, ndinaona nyanga 4.+ 19 Choncho ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi nyangazi zikuimira chiyani?” Iye anandiyankha kuti: “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda,+ Isiraeli+ ndi Yerusalemu.”+
20 Kenako Yehova anandionetsa amisiri 4. 21 Ndiyeno ndinafunsa kuti: “Kodi awa abwera kudzatani?”
Mngeloyo anayankha kuti: “Zimenezi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda moti panalibe amene anatha kudzutsa mutu wake. Amisiriwa adzabwera kudzaopseza nyangazi ndipo adzawononga nyanga za mitundu ina ya anthu amene anakweza nyanga* zawo poukira dziko la Yuda kuti abalalitse anthu ake.”