MUTU 11
Kodi Mukufuna Kuti Anthu Adzapeze Moyo Wosatha Ngati Mmene Yehova Akufunira?
1, 2. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yona anachita Yehova atakhululukira anthu a ku Nineve? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira mozama chifundo chimene Mulungu ali nacho komanso mmene amaonera moyo?
PA NTHAWI inayake, Yona anakwiya kwambiri koma Yehova anali wosangalala. Kodi chinachitika n’chiyani? Mulungu anali atasonyeza chifundo kwa anthu ambirimbiri ndipo sanawawononge. Yona ankafuna kuti anthuwo awonongedwe. Koma Yehova anasankha kukhululukira anthuwo, omwe anali adani a anthu ake.
2 Monga mmene nkhani ya Yonayi ikusonyezera, nthawi zina anthufe zingativute kumvetsa chifundo chimene Mulungu ali nacho. Komanso zingativute kusonyeza mtima umene Mulungu ali nawo wofunitsitsa kuti anthu apulumuke. Yona ‘sanasangalale m’pang’ono pomwe ndipo anakwiya koopsa’ ndi zimene Yehova anachita posankha kukhululukira anthu a ku Nineve. Kodi kapena Yona ankaganizira kwambiri za iyeyo m’malo moganiza zochitira anthuwo chifundo ndi kuwathandiza kuti apulumuke? Mwina iye ankaganiza kuti anthu a ku Ninevewo akapanda kuwonongedwa, ndiye kuti iyeyo aoneka ngati wabodza. (Yona 4:1, 10, 11) Nanga bwanji m’nthawi yathu ino pamene tsiku la Yehova lachiweruzo lili pafupi kwambiri? Mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndingatani kuti ndizimvetsa bwino chifukwa chake Mulungu amakhululukira anthu komanso kuti ndizisangalala ndi zimenezi? Nanga ndingatani kuti ndithandize anthu ochimwa omwe alapa kuti nawonso apindule kwambiri ndi chifundo cha Mulungu? Komanso kodi ndingatani kuti nditsanzire mtima umene Mulungu ali nawo wofunitsitsa kuti anthu adzapeze moyo wosatha?’
MULUNGU AMASONYEZA CHILUNGAMO KOMANSO CHIFUNDO POFUNA KUPULUMUTSA ANTHU
3. Kodi Mulungu amagwiritsira ntchito bwanji makhalidwe ake awiri, omwe ndi chilungamo ndiponso chifundo?
3 Anthu ena amaganiza kuti nkhani zonse zimene zili m’mabuku a aneneri 12 n’zokhudza mkwiyo wa Mulungu komanso chiweruzo chimene iye amapereka kwa anthu. Chifukwa cha maganizo amenewa, mwina iwo angadzifunse kuti: ‘Kodi pamenepa tingati Yehova ndi wachifundo? Kodi tinganene kuti iye amafunadi kupulumutsa anthu?’ Koma zoona zake n’zakuti chilungamo cha Mulungu chimayendera limodzi ndi chifundo chake, ndipo iye amagwiritsa ntchito makhalidwe awiri onsewa pothandiza anthu kuti apulumuke. Ndipotu makhalidwe amenewa amathandiza Mulungu kuti azichita zinthu m’njira yoyenera. (Salimo 103:6; 112:4; 116:5) Mulungu akamakonza zinthu zimene anthu oipa awononga, amakhala akusonyeza chifundo kwa anthu amene amamumvera, ndipo zimenezi ndi umboni woti iye amasonyeza chilungamo mosalakwitsa. Komanso popeza Yehova ndi wachifundo, amakondabe anthu opanda ungwiro, ngakhale kuti iwo amalakwitsa zina ndi zina. Tinganene kuti iye amapereka chiweruzo pamene chikufunikira, komanso amachitira anthu chifundo ngati pakufunika kutero. M’mabuku a aneneriwa mungapezemo mfundo zambiri zotsimikizira kuti chilungamo cha Mulungu chimayendera limodzi ndi chifundo chake. Ndipo zimenezi ndi umboni wakuti iye amafuna kuti anthu apulumuke. Tsopano tiyeni tikambirane umboni wotsimikizira mfundo imeneyi, ndipo tikamachita zimenezi, tipeze mfundo zomwe tingazigwiritse ntchito pa moyo wathu.
4. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Mulungu amafuna kuti anthu apulumuke?
4 Pamene mneneri Yoweli ankalengeza uthenga wachiweruzo, anatsindikanso mfundo yakuti Mulungu “ndi wachisomo, wachifundo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.” (Yoweli 2:13) Patapita zaka pafupifupi 100, cha m’ma 700 B.C.E., nayenso Mika anatsindika mfundo yakuti anthufe tikufunikira kwambiri kukhululukidwa ndi Yehova. Pa nthawi ina Mika anafunsa kuti, “Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu?” Kenako iye ananena mawu otsatirawa pofotokoza za Yehova: “Inu simudzakhalabe wokwiya mpaka kalekale, pakuti kusonyeza kukoma mtima kosatha kumakusangalatsani. Inu mudzatichitiranso chifundo.” (Mika 7:18, 19) Komanso monga mmene taonera m’nkhani ya Yona ndi anthu a ku Nineve, Mulungu ndi wofunitsitsa kukhululukira anthu ochimwa. Iye ndi wokonzeka kuwakhululukira ngati anthuwo akumva chisoni ndi machimo awo ndipo akuchita zinthu zosonyeza kuti alapa.
5. Kodi ndi nkhani ziti zimene zimakulimbikitsani kwambiri, zosonyeza kuti Mulungu ndi wachifundo komanso amafunitsitsa kuti anthu adzapulumuke? (Onaninso bokosi lakuti “Anadzipereka Kuti Atumikire Mulungu.”)
5 N’zoona kuti ifeyo sitikukhala m’nthawi ya aneneri 12 amenewo. Koma kodi sitikuyamikira kwambiri Yehova chifukwa cha mmene amasonyezera anthu chifundo komanso mtima wofunitsitsa kuwakhululukira? Mukamayamikira Mulungu mwa njira imeneyi mudzayamba kumukonda kwambiri ndiponso mudzakhala ndi mtima wofunitsitsa kuthandiza anthu ena kuti adzapeze moyo. Ngakhale kuti anthu ambiri masiku ano amachita zinthu zoipa, inuyo mukudziwa kuti Mulungu “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Petulo 3:9) Ndipo zimene Hoseya ananena pamene ankatenganso Gomeri, mkazi wake wadama, zikuchitira chithunzi mfundo yakuti Yehova akufunitsitsa kuti anthu onse alape. Yehova ‘analankhula ndi anthu akewo mowafika pamtima.’ Mulungu anali ndi ufulu wosankha kusakhululukira anthuwo, komabe iye anawakhululukira ‘mwa kufuna kwake.’ (Hoseya 1:2; 2:13, 14; 3:1-5; 14:4) Kodi mukudziwa chifukwa chake mtima umene Mulungu amasonyeza pokhululukira anthu uli wofunika kwambiri? N’chifukwa chakuti nkhani yokhululuka imakhudza moyo wa anthu. Pali umboni winanso wosonyeza kuti Mulungu ndi wachifundo komanso akufunitsitsa kuti anthu adzapulumuke. Umboniwu mungaupeze mukaganizira za mpingo wachikhristu womwe ukugwira ntchito yofunika kwambiri, imene inunso mukugwira nawo.
THANDIZANI ANTHU KUTI ADZAPEZE MOYO WOSATHA
6. Kodi ndi njira yaikulu iti imene Mulungu akusonyezera kuti ndi wofunitsitsa kuti anthu adzapulumuke?
6 N’chifukwa chiyani mumagwira nawo ntchito yolalikira? Chimodzi mwa zifukwa zikuluzikulu n’chakuti mumafuna kuthandiza ena kuti adziwe Mulungu woona. Koma muyenera kudziwa mfundo yofunika kwambiri iyi yonena za Yehova: Iye amayamba wachenjeza anthu momveka bwino asanawapatse chilango. Zimenezi zikusonyeza kuti iye amachitira anthu chifundo ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo apulumuke osati awonongedwe. Ndipo aneneri 12 ankathandiza anthu ochimwa kudziwa kuti Mulungu anapatsa anthuwo mwayi woti akonzenso ubwenzi wawo ndi iye n’cholinga choti asadzawonongedwe pa tsiku lamkwiyo wake. Masiku ano ifenso tikugwira ntchito yofanana ndi imeneyi. Popeza inuyo ndinu Mkhristu, muli ndi mwayi wolengeza uthenga wochenjeza anthu za tsiku limene Mulungu adzapereke chilango kwa anthu osamvera. Mukamagwira ntchito imeneyi muzipewa mtima wofuna kuti anthu amene sakukumverani adzakhaule. Muzikumbukira kuti chifukwa china chachikulu chimene chikukuchititsani kulalikira, n’choti muthandize anthu ena kuti ayambe kuyenda mumsewu wopita ku moyo.—Yoweli 3:9-12; Zefaniya 2:3; Mateyu 7:13, 14.
7. (a) N’chifukwa chiyani kugwira nawo ntchito yolalikira n’kofunika kwambiri? (b) Kodi kuganizira mmene Yehova amaonera anthu kungatithandize bwanji tikamakumana ndi anthu amene sakulabadira uthenga wathu?
7 Nthawi ina iliyonse mukamalalikira choonadi cha m’Baibulo, kaya ndi kunyumba ndi nyumba, kusukulu, kuntchito kapena kwina kulikonse, mumakhala mukuthandiza munthu wina amene panopa akufunikira kuti Mulungu amuchitire chifundo komanso amukhululukire. (Hoseya 11:3, 4) Koma anthu ena sangasonyeze chidwi ndipo ena angakutsutseni. Komabe, mukamapirira mumatsanzira Mulungu wathu wachifundo yemwe analankhula ndi anthu ake osamvera kudzera mwa Zekariya kuti: “Chonde, siyani njira zanu zoipa ndi zochita zanu zoipa n’kubwerera kwa ine.” (Zekariya 1:4) Ndipotu simukudziwa kuti ndi anthu angati amene angalabadire mukamawauza za chifundo cha Mulungu ndiponso kuwathandiza kuti aziyenda mumsewu wopita ku moyo. Komanso muzikumbukira kuti inuyo mumalalikira chifukwa chakuti Yehova akufuna kuti anthu adzapeze moyo wosatha, ndipo ndi zimenenso inuyo mukufuna.
8. Kodi kukumbukira zimene anthu ena anachita Mulungu atawasonyeza chifundo n’kolimbikitsa bwanji?
8 Mungalimbikitsidwe kwambiri ngati mutakumbukira mfundo yotsatirayi: Nthawi zonse padzikoli pakhala pakupezeka anthu amene amalabadira uthenga wa Mulungu. N’chifukwa chake Hoseya ananena kuti anthu ena anazindikira kuti “njira za Yehova ndi zowongoka.” Kenako mneneriyu anawonjezera kuti: “Anthu olungama ndi amene adzayendamo.” (Hoseya 14:9) Kuyambira kale kwambiri, anthu ochuluka akhala akulabadira mawu a Mulungu akuti: “Bwererani kwa ine ndi mtima wanu wonse.” (Yoweli 2:12) Pa nthawiyo Yehova ankalankhula ndi anthu amene ankamudziwa kale. Koma mfundoyi ikusonyeza kuti iye akuitananso anthu omwe angoyamba kumene kuphunzira za iye. Zoonadi, Mulungu sanataye mtima ndi anthu ndipo akudziwa kuti ena angayambe kumva chisoni ndi machimo awo n’kulapa, ndipo angayambe kuchita zinthu zabwino. Ngati atachita zimenezo, anthuwo akhoza kudzapeza moyo wosatha.—1 Timoteyo 4:16.
9. Kodi zimene anthu a ku Nineve anachita zikusonyeza kuti munthu ayenera kuchita chiyani kuti akhululukidwe?
9 Tingaphunzirenso mfundo ina tikaganizira zimene Yehova anachita pokhululukira anthu a ku Nineve. Timawerenga kuti anthuwo analabadira atamva uthenga wachiweruzo wochokera kwa Mulungu, ndipo “anayamba kukhulupirira Mulungu.” (Yona 3:5) Kuti anthuwo apitirize kukhala ndi moyo, anafunika kukhala ndi chikhulupiriro chenicheni, osati kungoopa chiweruzo. Masiku anonso Yehova akufunitsitsa kuti anthu alape ndiponso kuti azichita zinthu zosonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro. Choncho iye watilola kuti tizilalikira n’kumathandiza anthu kuti asankhe kumumvera. Kodi zotsatira zake n’zotani? Zimene zikuchitika n’zofanana ndi zimene zinachitikira anthu a ku Nineve. Baibulo limati: “Mulungu woona anaona ntchito zawo. Anaona kuti alapa ndi kusiya njira zawo zoipa. Choncho, Mulungu woona anasintha maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti awabweretsera, moti sanawabweretsere.” (Yona 3:10) Yehova sangapusitsidwe ndi mawu chabe kapena zinthu zina zimene munthu angachite mwachiphamaso. Choncho zimene anthu a ku Nineve anachita posonyeza kuti alapa, zinali zochokeradi pansi pa mitima yawo. Ndipo Mulungu anaona kuti anthuwo asinthadi chifukwa anachita zinthu zosonyeza kuti alapa moona mtima komanso zosonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro.
10. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yehova amathandiza anthu kuti apulumuke.
10 Tisaganize kuti Yehova, yemwe amafunitsitsa kuti anthu onse adzapulumuke, anangothandiza anthu a ku Nineve okha kuti apulumuke. Mwachitsanzo, pamene Yerusalemu ankawonongedwa mu 607 B.C.E., Obadiya, Nahumu ndi Habakuku atamaliza utumiki wawo, Yehova anapulumutsa Yeremiya yemwe anali ndi mtima womvera, ndiponso gulu lina la atumiki ake okhulupirika. (Yeremiya 39:16-18) Aneneri a Mulungu analosera kuti Ayuda omwe analapa adzabwerera kwawo kuchokera ku ukapolo ku Babulo, kuti akayambirenso kulambira koona. (Mika 7:8-10; Zefaniya 3:10-20) Ndipo maulosi amenewo akukwaniritsidwa kwambiri masiku ano. Mwachitsanzo, nkhondo yoyamba ya padziko lonse itatha, ambiri mwa Akhristu odzozedwa anali atafooka mwauzimu. Koma iwo anathandizidwa kuti ayambirenso kutumikira Yehova mwakhama, zomwe zikanawathandiza kudzapeza moyo. Masiku anonso anthu ochokera ‘m’mitundu yambiri akudziphatika kwa Yehova.’ (Zekariya 2:11) Ndipo anthu amenewa ali ndi mwayi wodzapulumuka dzikoli likamadzawonongedwa. Choncho inuyo sikuti mumagwira ntchito yolalikira pongofuna kumvera lamulo lakuti Akhristu azigwira ntchitoyi. Komanso sikuti mumangogwira ntchitoyi n’cholinga choti mukwaniritse ulosi. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Koma mumagwira ntchito yolalikira n’cholinga choti muthandize anthu kudziwa za Yehova, kukhala ndi chikhulupiriro ndiponso kuti adzapeze moyo wosatha.
ANTHU AMENE AKUBWERERA KWA YEHOVA ADZAPEZA MOYO
11, 12. Kodi anthu amene poyamba ankalambira Mulungu angapindule bwanji ndi chifundo chimene Mulunguyo ali nacho?
11 Yehova amasangalala akaona anthu amene angoyamba kumene kumutumikira, ndipo amafunitsitsa kuti anthuwo adzapeze moyo. Komabe, sikuti iye amaiwala amene anayamba kalekale kumutumikira. Ifenso tiyenera kumachita chidwi ndi anthu amenewa ndipo tiziwathandiza kuti apitirize kuyenda mumsewu wopita ku moyo. Kodi tingawathandize m’njira ziti?
12 Mwina mukudziwa anthu ena omwe anaphunzira za Yehova ndi kumukhulupirira, ndipo ankamutumikira mwakhama koma panopa sakumutumikiranso. Mauthenga amene Yehova anatumiza kudzera mwa aneneri 12 akusonyeza kuti iye anali wofunitsitsa kuchitira chifundo anthu omwe poyamba anali m’gulu lake koma anasiya kumutumikira. N’chimodzimodzinso masiku ano. Yehova amafuna kuti anthu omwe asiya kumutumikira alape n’kubwerera kwa iye, kaya anthuwo anatengeka pang’onopang’ono ndi zinthu zina, kapena anachita tchimo. (Aheberi 2:1; 3:12) Ngakhale kuti anthuwo samakhala osangalala akasiya Yehova, zingawavute kwambiri kuti abwerere m’gulu lake. Koma Mulungu amachonderera anthu oterewa kuti abwerere kwa iye. Mwachitsanzo, mneneri Zekariya analemba kuti: “Yehova wa makamu wanena kuti: ‘Bwererani kwa ine,’ watero Yehova wa makamu, ‘ndipo ine ndidzabwerera kwa inu.’” (Zekariya 1:3) Nayenso Hoseya ananena mawu olimbikitsa kwambiri. Iye anati: “Iwe Isiraeli, bwerera kwa Yehova Mulungu wako pakuti wapunthwa mu zolakwa zako. Bwerera kwa Yehova ndi mawu osonyeza kulapa. Anthu nonsenu uzani Mulungu kuti, ‘Tikhululukireni zolakwa zathu. Landirani zinthu zabwino zochokera kwa ife.’” Zoonadi, Mulungu anali wofunitsitsa kwambiri kukhululukira ngakhale anthu amene anachita machimo akuluakulu koma kenako n’kulapa moona mtima ndi kubwerera kwa iye. (Hoseya 6:1; 14:1, 2; Salimo 103:8-10) Zimenezi zinkachitika m’nthawi ya aneneri, ndipo zikuchitikanso masiku ano.
13. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchitira chifundo anthu amene Mulungu wawakhululukira?
13 Kodi mfundo yakuti Yehova amakhululukira ndi kulandiranso anthu ochimwa amene alapa ingathandize bwanji Akhristu omwe akupitirizabe kuyenda mumsewu wopita ku moyo? Kodi tingasonyeze bwanji kuti timaona ena ngati mmene Yehova amawaonera? Yehova amafuna kuti tizichitira anthu ena chifundo, kaya anthuwo angoyamba kumene kumutumikira kapena anafooka n’kusiya kumutumikira. Kudzera mwa Hoseya, Mulungu ananena zimene akufuna kuti ifeyo tizichita. Iye anati: “Ndimakondwera ndi kukoma mtima kosatha, osati ndi nsembe.” Yesu Khristu nayenso ananena mfundo yogwirizana ndi mawu amenewa pamene anati: “Pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’” (Hoseya 6:6; Mateyu 9:13) Ndipo ifeyo tikamalephera kuchitira ena chifundo sitingakhale pa ubwenzi ndi Mulungu. Ndipotu mtumwi Paulo analemba mfundo yomwe ikusonyeza kuti kukhululukira ena n’kogwirizana kwambiri ndi kutsanzira Mulungu. Iye anati: “Khalani okomerana mtima, achifundo chachikulu, okhululukirana ndi mtima wonse, monga mmene inunso Mulungu anakukhululukirani ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu. Chotero muzitsanzira Mulungu, monga ana ake okondedwa, ndipo yendanibe m’chikondi.” (Aefeso 4:32–5:2) Kodi inuyo mukuchita zotani poyesetsa kutsanzira Mulungu pa nkhani imeneyi?
14, 15. Kodi nthawi zina tingayesedwe bwanji kuti tisonyeze ngati timatsanzira Yehova pa nkhani yokhululukira ena?
14 Nanga bwanji ngati m’bale amene anachita tchimo lalikulu sanalape ndipo anachotsedwa mumpingo? Zinthu ngati zimenezi zinkachitikanso m’nthawi ya atumwi, ndipo Akhristu osalapa ankachotsedwa mumpingo. Ngati zimenezi zinkachitika atumwi a Yesu alipo, sitiyenera kudabwa kuti nthawi zina masiku anonso zingachitike. Ndipo Akhristu okhulupirika amayesetsa kutsatira mfundo ya m’malemba yakuti asamacheze ndi wina aliyense wochotsedwa. Akhristu akamamvera lamulo la Yehovali mokhulupirika, amathandiza wolakwayo kuti azindikire kukula kwa tchimo lake, ndipo zimenezi zingamuchititse kuti alape. Mwachitsanzo, timawerenga m’Baibulo kuti munthu wina wa ku Korinto amene anachotsedwa, patapita nthawi analapa ndipo anabwezeretsedwa. (1 Akorinto 5:11-13; 2 Akorinto 2:5-8) Kodi inuyo mumamva bwanji zinthu zangati zimenezi zikachitika masiku ano? Nanga mungatani kuti musonyeze kuti mukufunitsitsa zoti anthu ena adzapeze moyo wosatha?
15 Nthawi zina munthu wochimwa yemwe walapa angamachite manyazi komanso sangadziwe zoyenera kuchita. Munthu wotere amafunikira kumutsimikizira kuti Mulungu komanso abale ake amamukonda ndipo iwo akufunitsitsa kuti iye adzapeze moyo wosatha. Taonani mmene Mulungu analimbikitsira anthu ake omwe anali ndi mtima wofunitsitsa kulapa. Iye anawauza mokoma mtima kuti: “Ndidzalonjeza kukukwatira mokhulupirika ndipo udzadziwadi Yehova.” (Hoseya 2:20) Choncho zochita zathu zizisonyeza kuti tikutsanzira Mulungu yemwe ‘amachitira ena chifundo’ ndipo amafunitsitsa kuti anthu ochimwa alape.—Zekariya 10:6.
16. Kodi tizimuona bwanji munthu amene wabwezeretsedwa mumpingo?
16 Popeza Mulungu amafuna kuti anthu adzapeze moyo, amasangalala munthu wochimwa akalapa kapena munthu amene anafooka akayambiranso kumutumikira mwakhama.a (Luka 5:32) Ponena za munthu wa ku Korinto, amene anabwezeretsedwa mumpingo, mtumwi Paulo analimbikitsa anthu a mumpingowo kuti amukhululukire ndiponso kuti azimulimbikitsa pomutsimikizira kuti amamukonda. Mtumwiyu analemba kuti: “Kudzudzulidwa ndi anthu ambiri chonchi n’kokwanira kwa munthu ameneyu. Chotero tsopano mukhululukireni ndi mtima wonse ndi kumutonthoza, kuopera kuti mwina wotereyu angamezedwe ndi chisoni chake chopitirira malire. Choncho ndikukudandaulirani kuti mumutsimikizire kuti mumamukonda.” (2 Akorinto 2:6-8) Komanso kumbukirani kuti Hoseya analemba mawu amene Yehova analankhula ponena za anthu ochimwa amene analapa. Iye anati: “Ndidzathetsa kusakhulupirika kwawo. Ndidzawakonda mwa kufuna kwanga.” (Hoseya 14:4) Kodi inuyo muyesetsa kutsanzira Yehova pothandiza anthu mosangalala kuti abwerere kwa iye, n’cholinga choti adzapeze moyo wosatha?
17, 18. Kodi tingatani kuti tithandize mwachikondi anthu amene abwerera kwa Yehova kapena anthu a m’banja limene wachibale wawo wachotsedwa?
17 Yehova ananena momveka bwino kuti amalandira ndi mtima wonse anthu ochimwa amene abwerera kwa iye, ndipo amawalemekeza komanso kuwakonda. Iye amachita zimenezi mofanana ndi mmene Hoseya anachitira ndi mkazi wake amene pa nthawi ina anali wosakhulupirika. Yehova akutiuza mmene anachitira zinthu ndi atumiki ake, kuti: “Ndinakhala ngati wochotsa goli m’khosi mwawo ndipo mwachikondi ndinali kubweretsera aliyense wa iwo chakudya.” (Hoseya 11:4) N’zolimbikitsa kwambiri tikaganizira za chikondi chimene Yehova amasonyeza anthu amene abwerera kwa iye. Ifenso tingamutsanzire tikamachita zinthu mwachikondi komanso mokoma mtima ndi anthu amene alapa moona mtima chifukwa chomva chisoni ndi tchimo limene anachita. Munthu yemwe walapa akabwezeretsedwa mumpingo, tisamadane naye kapena kumusungira chakukhosi chifukwa cha tchimo limene anachita. M’malomwake, tizimulimbikitsa nthawi ina iliyonse tikaona kuti akufunikira kulimbikitsidwa.—1 Atesalonika 5:14.
18 Kodi pali zinthu zina zimene mungachite kuti mutsanzire Yehova ngati munthu wina wachotsedwa mumpingo? Kodi mungathandize anthu okhulupirika a m’banja la munthuyo, mwina mkazi kapena mwamuna wake ndiponso ana? Mwina anthuwo akuvutika kuti azifika kumisonkhano nthawi zonse komanso kuti azilalikira. Inuyo mungachite bwino kuwathandiza mwapadera pa vuto limeneli. Mungawasonyeze chifundo polankhula nawo “mawu abwino ndiponso olimbikitsa” pamene mukucheza nawo. (Zekariya 1:13) Tingapeze mpata pa nthawi zosiyanasiyana kuti ticheze nawo n’kuwalimbikitsa, monga misonkhano isanayambe kapena itatha, tikayenda nawo mu utumiki, kapenanso pa nthawi zina. Nthawi zonse tizichita zinthu zimene zingawachititse kuona kuti sakusalidwa. Tizikumbukira kuti iwo ali mumpingo mwathu ndipo ndi Akhristu anzathu amene timawakonda kwambiri. Nthawi zina bambo kapena mayi akachotsedwa mumpingo, ana okha ndi amene amayesetsa kutumikira Yehova. Ifeyo timafunitsitsa kuti ana oterewa adzalandire moyo wosatha. Koma kodi tingatani kuti tisonyeze zimenezi?
MULUNGU ‘AMACHITIRA CHIFUNDO MWANA WAMASIYE’
19. Kodi Zefaniya anathandiza bwanji Yosiya, yemwe tinganene kuti anali “mwana wamasiye”?
19 Mungadziwe zoyenera kuchita pothandiza “mwana wamasiye” mukaona zimene Zefaniya, amene anatumikira m’zaka za m’ma 600 B.C.E., anachita. Zikuoneka kuti Zefaniya anali wochokera kubanja la chifumu ku Yuda, ndipo anali wachibale wa Mfumu Yosiya. Yosiya anayamba kulamulira ali ndi zaka 8 zokha, bambo ake omwe anali mfumu, ataphedwa. Iye anali ndi ntchito yovuta kwambiri chifukwa anthu ochuluka zedi mu ufumu wake ankalambira mafano ndiponso ankachita zinthu zina zoipa. (Zefaniya 3:1-7) Choncho Yosiya, yemwe anali mwana wamasiye, ankafunikira malangizo oyenerera kuti akwanitse kutsogolera mtundu wosamverawo. Monga mmene taonera m’Mutu 3 ndi 5 wa buku lino, Yehova anagwiritsa ntchito Yeremiya ndiponso Zefaniya popereka malangizo othandiza kwa Yosiya. Ndipo n’zochititsa chidwi kuti pamene Yehova ankadzudzula “akalonga” a ku Yuda kudzera mwa mneneri wake, sanadzudzule mfumuyi. (Zefaniya 1:8; 3:3) Zimenezi zikusonyeza kuti Mfumu Yosiya, yemwe anali mnyamata, anali atayamba kale kulambira Mulungu m’njira yoyenerera. Mosakayikira, malangizo amene mneneri Zefaniya ankapereka kwa Mfumu Yosiya, anathandiza kwambiri mfumuyi kuti iyambe ntchito yothetsa kulambira mafano ku Yuda.
20. Kodi Akhristu achikulire angathandize bwanji “ana amasiye” mumpingo, ndipo zotsatira zake zingakhale zotani?
20 Zimene Zefaniya anachita pothandiza Yosiya, zikusonyeza mmene Yehova amasamalirira ana amene akufunikira malangizo. Chitsanzo cha ana amenewa ndi omwe bambo kapena mayi awo anachotsedwa mumpingo. Hoseya ananena kuti: ‘Mulungu amachitira chifundo mwana wamasiye.’ (Hoseya 14:3) Kodi mukudziwa “mwana wamasiye” aliyense amene akufunikira malangizo omuthandiza kulambira Yehova komanso omuthandiza pa moyo wake watsiku ndi tsiku? Chitsanzo cha ana otere ndi ana omwe makolo awo si Mboni, ana omwe akuleredwa ndi mayi kapena bambo okha, kapenanso ana amene sakulimbikitsidwa mwauzimu ndi anthu a m’banja mwawo. Nthawi zambiri ana otere amayamba kutumikira Mulungu mwakhama ngati anthu ena achikulire mumpingo akuwasonyeza chidwi mwapadera n’kumawapatsa malangizo. “Ana amasiye” ochuluka amakhala Akhristu odalirika akakula chifukwa choti munthu wina wachikulire mumpingo ankawakonda komanso kuwasonyeza chidwi mwapadera.—Salimo 82:3.
21. Kodi Akhristu odziwa bwino malemba angathandize bwanji achinyamata?
21 Mwachitsanzo, Akhristu ena odziwa bwino malemba angathandize mayi amene akulera yekha ana ngati Akhristuwo atamasonyeza chidwi anawo. (Yakobo 1:27) Komanso akulu mumpingo pamodzi ndi anthu ena angathandize mwauzimu anthu ena ochokera m’mabanja omwe akufunikira kuwasonyeza chidwi komanso chikondi. Akuluwo angachite zimenezi molemekeza bambo, yemwe ndi mutu wa banjalo, komanso molemekeza anthu ena onse a m’banjamo. Mwina inunso pamodzi ndi banja lanu lonse mungapatule nthawi yoti muzicheza ndi ana amasiye. Kodi simungayesetse kuchita zinthu zosonyeza kuti mukuganizira achinyamata omwe akusowa munthu wowalimbikitsa? Iwo angafunikire munthu woti amvetsere nkhawa zawo kapena woti amuuze zakukhosi, ndipo angakhale ndi mpata wokuuzani zimenezi ngati mutayenda nawo mu utumiki. N’zoona kuti ndinu munthu wotanganidwa kwambiri, komabe mukamayesetsa kuthandiza wachinyamata wina mobwerezabwereza, zingaoneke kuti “chikondi chanu chilidi chenicheni.” (2 Akorinto 8:8) Mukamachita zimenezi mungasonyeze kuti mukufunitsitsa kuti anthu enanso adzapeze moyo wosatha.
22. Kodi mumamva bwanji mukaganizira mfundo yakuti Yehova akufuna kuti anthu adzapeze moyo wosatha?
22 N’zolimbikitsa kwambiri kudziwa kuti Mulungu akufuna kuti anthu adzapeze moyo wosatha. Iye angasangalale kwambiri kusonyeza chikondi chake kwa anthu amene amam’konda powapatsa moyo wosatha, m’malo mosonyeza mkwiyo wake kwa anthu amene sakufuna kusintha kuti adzalandire moyo wosatha. Pamene tikuyembekezera tsiku la Yehova, tiyeni tizimutsanzira pothandiza ena kuti aziyenda mumsewu wopita ku moyo wosatha.
a Pali mafanizo atatu osangalatsa kwambiri amene angatithandize kumvetsa mfundo yakuti Yehova amakondabe kwambiri anthu ake amene anasochera. Mafanizowa ndi a nkhosa yosochera, ndalama yotayika ndiponso mwana wolowerera.—Luka 15:2-32.