Zochitika kuchokera ku Dziko Lolonjezedwa
Mitundu Isonkhana pa Megido
“OFUFUZA amasinthasintha ponena za Armagedo ya dziko lonse,” inasimba tero nkhani ya sayansi pa kaya nkhondo ya nyukliya idzabweretsa “nyengo ya chisanu cha nyukliya” yozizira kapena “chirimwe cha nyukliya” chotentha.
Mwinamwake munawonapo ndemanga zoterozo zomwe zimagwirizanitsa “Armagedo” ndi nthaŵi zathu zovuta. Kodi “Armagedo” nchiyani? Mungafune kudziŵa, popeza kuti moyo wanu ukulowetsedwamo.
Yang’anani pamwamba pa kawonedwe ka mumlengalenga ka Megido. Awa anali malo a chandamale mu Israyeli wakale. Mtumwi Yohane anagwiritsira ntchito dzina lake pamene analemba za “malo otchedwa m’Chihebri Har–Magedo [Phiri la Megido],” kapena Armagedo. (Chibvumbulutso 16:16) Kudziŵa chiyambi cha Megido kumawunikira mawu amenewo.
Mungawone malo ake pa mapu yomwe yaikidwa muno. Iyo kotheratu inayang’anizana ndi misewu iŵiri yaikulu. Mapiri a Karimeli anatsekereza msewu wa N—S pakati pa Igupto kum’mwera ndi Damasiko kapena mizinda ina kulinga ku Firate kumpoto. Chotero magulu ankhondo ndi magulu a malonda oyenda pa akavalo anakakamizidwa kupyola m’kanjira ka kunsi m’mphepete mwa Megido, kanjira cha kulamanja kwa chithunzicho. Msewu wa N—S kupyola iwo unadutsa mu Chigwa cha Yesireeli ndi msewu wofunika koposa pakati pa Turo ndi Chigwa cha Yordano, kapena Samariya ndi Yerusalemu. Popeza anali pakati pa misewu imeneyi, Megido akanalamulira kotheratu opita mumsewu, ndipo chigwa kutsogolo kwa Megido chinakhala malo a nkhondo zosankha.
Mwachitsanzo, panali pano pamene Woŵeruza Baraki anagonjetsa Akanani pansi pa mkulu wankhondo Sisera, yemwe anali ndi magareta ankhondo achitsulo 900. (Oweruza 4:1-3, 12-16; 5:19) Pambuyo pake, Farao Neko anatsogoza gulu la asilikari amphamvu a Chiigupto ndi magareta kukwera ndi msewu wa m’gombe (mwakutero dzina lake, Via Maris, kapena Njira ya ku Nyanja) kukalimbikitsa Asuri pafupi ndi Firate. Kaamba ka chifukwa china, mfumu ya Chiyuda Yosiya anagamulapo za kulimbana kwa mitundu yonse ndi Neko. Koma kuti? Ngakhale kuti anali makilomita 90 kumpoto kwa Yerusalemu, Yosiya anasankha chigwa pafupi ndi Megido.—2 Mbiri 35:20-22; Yeremiya 46:2.
Iye anadziŵa kuti Aigupto anayenera kudutsa pamenepo, ndipo iye angakhale anadzimva kuti akakhala ndi mwaŵi, popeza kuti akakhala kufupi ndi malo ochinjiriza a Chiisrayeli. Monga mmene mungawonere, Tell (linga) ya Megido iri yaikulu ndithu. Mzinda wakalewo unali wowopsya. Solomo analimbitsa Megido, mwachidziŵikire akumamanga malinga a miyala ndi chipata chochinjirizira chachikulu.a (1 Mafumu 9:15) Kumbali ya kumanzere kwa lingalo, mungawone dzenje lalikulu, losongoka kutsogolo kwake, lomwe linali chipata cholowera ku dongosolo lopereka madzi locholowana. Makwerero ozolika anatsogoza pansi ku mtchera wautali wokumbidwa kupyolera m’thanthwe lapansi, kupatsa Aisrayeli mwaŵi ku madzi a pa kasupe pamene anali ochinjirizidwa ku kuwukiridwa. Akatswiri ofukula zofotseredwa pansi apezanso zotsalira za zakudya kaamba ka akavalo 450, mwinamwake kuchokera ku nthaŵi ya ulamuliro wa Ahabu.—Yerekezani ndi 1 Mafumu 9:19.
Mu nkhondo yosankha pafupi ndi Megido, Yosiya anavulazidwa mowopsya, ndipo iye anafa pa ulendo wobwerera ku Yerusalemu. (2 Mafumu 23:28-30) Ichi chingakhale chinali chochititsa cha ‘maliro m’chigwa cha Megido’ otchulidwa pa Zekariya 12:11. Pasanapite nthaŵi yaitali pambuyo pa kugonjetsedwa kwa Yosiya, Babulo anafutukula chisonkhezero chake cha nkhondo kulowa mu Yuda wofooketsedwa.—2 Mafumu 24:1, 2, 12-14; 2 Mbiri 36:1-6.
Ndi chidziŵitso cha kumbuyo choterocho, mungayamikire chifukwa chimene mu Chibvumbulutso choperekedwa kwa mtumwi Yohane, Megido anakhoza kutengedwa m’kunenera kusonkhanitsidwa kwa ‘mafumu a dziko lonse lokhalidwa ndi anthu’ ‘ku nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.’ Palibe malo amodzi aliwonse pa dziko lapansi, ndithudi osati chigwa chopanda kanthu cholamuliridwa ndi Tell Megido, chingakhale ndi mitundu yonse yotsutsana ndi Mulungu. Koma Har–Magedo, kapena Armagedo, moyenerera imaimira mkhalidwe kaamba ka nkhondo yosankha imeneyo.—Chibvumbulutso 16:14, 16; 19:11-21.
Chotero lolani andale zadziko ndi olemba nkhani molakwika alingalire za Armagedo monga nkhondo ya nyukliya yomwe idzasakaza chiwunda chathu. Ndi mbiri ya Megido m’maganizo, inu mungamvetsetse nkhaniyo molongosoka koposa. Mungayamikire kuti Armagedo iri mkhalidwe mu umene mitundu posachedwapa idzabweretsedwa kaamba ka nkhondo yaikulu pamene Mulungu adzachotsa dongosolo loipa liripoli, kutsegula njira kaamba ka dziko latsopano lolungama.—2 Petro 3:11-13.
[Mawu a M’munsi]
a Mungaŵerenge mu Nsanja ya Olonda ya August 15, 1988, masamba 24-6, mbiri yosangalatsa ya chipata cha Megido.
[Mapu patsamba 17]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Great Sea
To Damascus
To Tyre
Sea of Galilee
Acco
Caramel Range
Megiddo
Via Maris
Joppa
To Egypt
Beth-Shean
Dothan
Samaria
Shechem
To Jerusalem
Jordan River
Mi 0 10
Km 0 10 20
[Mawu a Chithunzi]
Based on a map copyrighted by Pictorial Archive (Near Eastern History) Est. and Survey of Israel
[Chithunzi patsamba 16]
Inu mudzapeza kawonedwe kokulira ka Megido mu Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1989. Zithunzi zake zisanu ndi chimodzi zidzakambitsiridwa chaka chino m’nkhani za Nsanja ya Olonda, zomwe mungafune kusunga limodzi ndi kalendayo kaamba ka kugwiritsira ntchito kwa mtsogolo.
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Chithunzi patsamba 17]
Chosemedwa cha Chiigupto ichi chingakuthandizeni inu kuchitira chithunzi m’maganizo kupita kodutsa Megido kwa Farao Neko, kumene iye anagonjetsa Mfumu Yosiya
[Mawu a Chithunzi]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.