Maphunziro Kuchokera m’Malemba: Zekariya 1:1–14:21
Yehova Asonkhezera Mzimu wa Anthu Ake
MOCHEDWA mu 538 B.C.E. kapena kuchiyambi mu 537 B.C.E., mfumu ya ku Peresiya Koresi inapereka lamulo lakuti Ayuda akayenera kubwerera kuchoka ku Babulo kupita ku Yerusalemu “nakaimange nyumba ya Yehova.” (Ezara 1:3) Podzafika 520 B.C.E., ngakhale kuli tero, kachisiyo inali chikhalirebe yosamangidwa. Chotero, Yehova anadzutsa mneneri Zekariya kugwira ntchito limodzi ndi Hagai m’kusonkhezera mzimu wa anthuwo.
Mawu owuziridwa a Zekariya anapatsanso mphamvu Ayuda okhulupirika mwa kusonyeza kuti Yehova anali kuwachirikiza iwo ndipo akadalitsa ntchito yawo. Bukhu limeneli la Baibulo limatichititsa nthumanzi nafenso chifukwa liri ndi maulosi a Umesiya, limodzinso ndi maulosi ena omwe akukwaniritsidwa m’nthaŵi yathu.a Limatipatsanso maphunziro opindulitsa.
Yehova Adalitsa Anthu Ake
Yehova ali wodera nkhaŵa ponena za anthu ake. Pambuyo pa kuvomereza kwa Ayuda kuti kulangidwa kwawo ndi Mulungu kunali kolungama, Zekariya ali ndi masomphenya atatu amene asonyeza nkhaŵa Yake yopitiriza kaamba ka iwo. Mu oyamba, iye akuwona akavalo ndi okwerapo aungelo. Mngelo mmodzi akuvutitsidwa kotero kuti mitundu imene inachititsa tsoka la Ayuda “sikuvutika.” Mu achiŵiri, Yehova akugamulapo kugwetsa “nyanga zinayi”—mphamvu za boma zimene zinabalalitsa anthu ake. Ndipo masomphenya achitatu mowonekera bwino akulongosola chisamaliro chotetezera chachikondi cha Yehova, cha Yerusalemu.—1:1–2:13.
Palibe amene adzakhala wokhoza kutsekereza atumiki okhulupirika a Mulungu. M’masomphenya achinayi, Satana, wotsutsa wamkulu wa anthu a Yehova, akudzudzulidwa kotheratu. (Yerekezani ndi Chibvumbulutso 12:10.) Mu achisanu, Zekariya akuphunzira kuti anthu a Mulungu adzachita chifuniro Chake mosasamala kanthu za zokhumudwitsa zonga mapiri. Motani? “Ndi khamu lankhondo ayi, ndi mphamvu ayi, koma ndi mzimu wanga, ati Yehova wa makamu.”—3:1–4:14.
Atumiki a Mulungu “adana nacho choipa.” (Salmo 97:10, 11) M’masomphenya achisanu ndi chimodzi, Mulungu akulengeza temberero pa ochita zoipa amene motero apita osalangidwa. Ndipo mu achisanu ndi chiŵiri, choimira cha kuipa chikuchotsedwa kutengeredwa ku “dziko la Sinara,” malo a chipembedzo chonyenga cha Chibabulo. Malo abwino kaamba ka icho! Kuipa sikumakhala pakati pa anthu a Yehova, amene amakuda iko. Zekariya chotsatira akuwona magareta anayi okokedwa ndi akavalo—makamu auzimu aungelo olamulidwa kukachinjiriza anthu a Mulungu pa dziko lapansi.—5:1–6:8.
Zowonedweratu za Ulosi
Kukwaniritsidwa kwa mawu aulosi a Yehova kuli kochititsa nthumanzi ndi kolimbitsa chikhulupiriro. Chiri chowona chotani nanga ponena za zowonedweratu za ulosi wa Zekariya kaamba ka tsiku lathu! Akumagwiritsira ntchito siliva ndi golidi zoperekedwa ndi Ayuda andende, iye akufunikira kupanga korona wamkulu kaamba ka Mkulu Wansembe Yoswa. M’kuwonjezerapo, “iwo akukhala kutali [mu Babulo] adzafika, nadzamanga ku kachisi wa Yehova,” monga mmene ambiri anasiira Babulo Wamkulu kuthandiza mu ntchito ya kachisi pambuyo pa 1919. Kuwongolera kwa malingaliro olakwika ponena za kusala kudya kunatsogoza ku kalongosoledwe ka mkhalidwe wa chisangalalo ulinkudza wa Yerusalemu. Chinanenedweratu kuti ‘anthu khumi kuchokera m’mitundu yonse’ akagwirizana ndi Ayuda auzimu m’kulambira kowona. (Agalatiya 6:16; Chibvumbulutso 7:4-10) “Fuula, mwana wamkazi wa Yerusalemu,” atero Yehova. Mfumu yake ikubwera yokwera pa bulu ndipo “adzanena zamtendere kwa amitundu.”—6:9–9:11.
Mulungu ndi Abusawo
Oyang’anira ali ndi thayo lalikulu ndipo ayenera kutumikira ndi changu. Pambuyo pa kulonjeza kupulumutsa anthu ake, Yehova akusonyeza ukali wake motsutsana ndi abusa osakhulupirira. “Abusa atatu” akuipitsa nkhosa ku mlingo wokulira wakuti Mulungu akuswa pangano lake ndi anthu ake. Yerusalemu adzakhala “mwala wolemetsa.” Aliyense wowukira iye “adzazilasa nawo.” Koma “akalonga Ayuda”—awo okhala ndi uyang’aniro pakati pa anthu osankhidwa a Mulungu—ayenera kukhala “ngati muuni wa moto,” wachangu mwapadera.—9:12–12:14.
Yehova amada chinyengo. Mu mpingo wa Mulungu, aliyense wowumirira ‘kulankhula chinyengo’ amakhala ‘olasidwa,’ kukanidwa monga ampatuko. “Magawo aŵiri” m’dziko adzadulidwa, pamene kuli kwakuti gawo lachitatu lidzayengedwa m’moto. Chofanana ndi ichi, unyinji wokulira wa awo odzinenera kukhala Akristu—awo a Chikristu cha Dziko—adulidwa ndi Yehova. Kuchokera mu 1919 kupita mtsogolo, kokha ochepera a Akristu okhulupirika, odzozedwa aitanira pa dzina la Yehova ndi kugonjera ku njira yake ya kuyenga.—13:1-9.
Anthu a Yehova angakhulupirire mu chinjirizo lake. Pamene adani ayesera kuwononga olambira owona, Mulungu adzachinjiriza anthu ake ndi kuchotsapo khamu la Satana. Kugawika kwa Phiri la Azitona kutulukapo m’chigwa chophiphiritsira m’chimene odzozedwa akumana ndi chinjirizo pansi pa Ufumu wa Yehova wa chilengedwe cha ponseponse ndi boma la Umesiya la Mwana wake. Padzakhala kuwala kaamba ka atumiki okhulupirika a Mulungu ndi mdima kaamba ka mitundu. Mtundu wa anthu uyenera kusankha: Kaya kulambira Yehova limodzi ndi anthu ake kapena kuvutika ndi chiwonongeko chamuyaya.—14:1-21.
[Mawu a M’munsi]
a Kukambitsiridwa kwa vesi ndi vesi kwa ulosi wa Zekariya kumapezeka m’bukhu la Paradise Restored to Mankind—By Theocracy! lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
[Bokosi patsamba 31]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
○ 1:3—Ngakhale kuti Ayuda anabwerera kuchokera ku Babulo mu 537 B.C.E., iwo analimbikitsidwanso kubwerera kwa Mulungu mwachimvero cha moyo wonse ndi kulambira. Iwo akapereka umboni wowonekera wa kubwerera kumeneku mwa kudziloŵetsa mu ntchito yomanganso kufikira kachisi atamalizidwa.
○ 2:1-5—Mwachidziŵikire, mwamuna wachichepere anali kuyesa Yerusalemu kotero kuti amange linga la chitetezo mozungulira iyo. Koma mngelo wa Mulungu anasonyeza kuti kukula kwa mzindawo sikunayenera kuikidwira malire ndi linga. Palibe munthu akanakhoza kuletsa kukula kopitirizabe kwa Yerusalemu. Yehova akakhala chinjirizo lake, monga mmene iye lerolino akuchinjirizira otsalira odzozedwa omwe adzakhala mbali ya Yerusalemu Watsopano wakumwamba.—Chibvumbulutso 21:2.
○ 6:11-15—Kuvekedwa chisoti chaufumu kwa Mkulu Wansembe Yoswa sikunampange iye kukhala wansembe-mfumu, chifukwa chakuti sanali m’mzera wa ufumu wa Davide. M’malomwake, kunapanga Yoswa kukhala munthu wa ulosi wa Mesiya, mwa amene ulosi wonena za “Mphukira” ukuzindikiridwa mokwanira. (Zekariya 3:8; Yeremiya 23:5) Yoswa anathandizira kumaliza ntchito ya kumanganso kachisi pa Yerusalemu. Wansembe-Mfumu wakumwamba, Yesu Kristu, akubweretsa kumapeto ntchito pa kachisi wauzimu.
○ 11:4-11—Anthu onga nkhosa anali “nkhosa zokaphedwa” m’njira yakuti abusa a boma anali kuwadyerera. Ndi ndodo imodzi yotchedwa “Chisomo” ndi inayo “Chomanganitsa,” Zekariya anachita monga mbusa wonyamula ndodo kutsogoza nkhosa ndi chibonga choyingitsira zirombo. (Salmo 23:4) Iye anachitira chithunzi Yesu, yemwe anatumizidwa kukhala mbusa wauzimu koma anakanidwa ndi Ayuda. Pamene Zekariya anathyola ndodo ya Chisomo, Mulungu analeka kuchita mokomera Ayudawo, akumaswa pangano lake ndi iwo. Ndipo pamene Zekariya anathyola ndodo yotchedwa Chomanganitsa, kuchotsedwa kwa pangano la Chilamulocho kochitidwa ndi Mulungu kwa Israyeli kunasiya Ayuda opanda chomangira cha umodzi cha teokratiki. Kusagwirizana kwawo kwa chipembedzo kunatulukapo m’kukhala kwa ngozi kaamba ka iwo ndi chiwonongeko cha Yerusalemu chochitidwa ndi Aroma mu 70 C.E.
○ 12:11—“Maliro a Hadadrimoni” angalozere ku kuliridwa kwa imfa ya Mfumu Yosiya ya Yuda. Hadadrimoni mwachiwonekere anali malo m’chigwa cha Megido, kumene anaphedwa m’nkhondo ndi Farao Neko. Imfa ya Yosiya inaliridwa mwachisoni, Yeremiya akufuula ndi oyimba akumatchula mfumuyo m’nyimbo za maliro.—2 Mbiri 35:20-25.
[Chithunzi patsamba 31]
Monga mmene Zekariya ananeneratu, anthu a mitundu yonse akuyanjana ndi Israyeli wauzimu tsopano