A1
Mfundo Zimene Anatsatira Pomasulira Baibulo
Poyamba Baibulo linalembedwa mʼChiheberi chakale, Chiaramu ndi Chigiriki. Masiku ano, Baibulo lonse kapena mbali yake chabe likupezeka mʼzilankhulo zoposa 3,000. Anthu ambiri amene amawerenga Baibulo sangamve zilankhulo zoyambirirazo. Nʼchifukwa chake Baibulo linafunika kumasuliridwa. Kodi omasulira Baibulo amafunika kutsatira mfundo ziti, nanga mfundo zimenezi zinathandiza bwanji pomasulira Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika?
Ena angaganize kuti kumasulira Baibulo liwu ndi liwu kungathandize kuti munthu amene akuwerenga amvetse mosavuta zimene zinafotokozedwa mʼzilankhulo zoyambirirazo. Koma si mmene zimakhalira nthawi zonse. Tiyeni tione zifukwa zingapo:
Malamulo a chilankhulo, kalembedwe ka mawu komanso kasanjidwe ka ziganizo zimasiyana mʼzilankhulo zosiyanasiyananso. Katswiri wina wachilakhulo cha Chiheberi, S. R. Driver, analemba kuti zilankhulo “zimasiyana malamulo a kalembedwe ndiponso mawu ake, komanso . . . njira imene mfundo zimasanjidwira mʼchiganizo.” Anthu amene amalankhula zilankhulo zosiyana amaganizanso mosiyana. S. R. Driver ananenanso kuti “nʼchifukwa chake kapangidwe ka ziganizo mʼzilankhulo zosiyana kamasiyananso.”
Palibe chilankhulo chimene mawu ndiponso malamulo ake a kalembedwe ndi ofanana ndendende ndi a Chiheberi, Chiaramu ndiponso Chigiriki chimene anagwiritsira ntchito polemba Baibulo. Choncho Baibulo lomasuliridwa liwu ndi liwu lingakhale lovuta kumva ndipo nthawi zina lingapereke tanthauzo lolakwika.
Tanthauzo la mawu likhoza kusintha potengera mmene awagwiritsira ntchito mʼchiganizo.
Mʼziganizo zina, omasulira angathe kugwiritsa ntchito mawu a chilankhulo choyambirira, koma ayenera kusamala kwambiri pochita zimenezi.
Tiyeni tione zitsanzo zimene zikusonyeza kuti kumasulira liwu ndi liwu kungapangitse kuti munthu amve zolakwika:
Malemba amagwiritsa ntchito mawu akuti “tulo” komanso “kugona” akamanena za tulo teniteni komanso imfa. (Mateyu 28:13; Machitidwe 7:60, mawu amʼmunsi) Mawu amenewa akagwiritsidwa ntchito ponena za imfa, omasulira Baibulo angagwiritse ntchito mawu akuti “kugona mu imfa” kapena akuti “kumwalira” kuti amene akuwerenga asasokonezeke.—1 Akorinto 7:39; 1 Atesalonika 4:13; 2 Petulo 3:4.
Mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mawu amene akupezeka pa Aefeso 4:14 omwe kuwamasulira liwu ndi liwu angamveke kuti “pochita maere a anthu ndi kampira.” Mawu okuluwika amenewa ankanena za kuchitira ena chinyengo pogwiritsira ntchito kampira kochitira maere. Komatu mʼzilankhulo zambiri, mawu amenewa akamasuliridwa liwu ndi liwu amakhala osamveka. Tanthauzo lake limamveka bwino akamasuliridwa kuti “zinthu zachinyengo zimene anthu amaphunzitsa.”
Pa Aroma 12:11 anagwiritsira ntchito mawu a Chigiriki amene akamasuliridwa liwu ndi liwu amati “mpaka kuwira mzimu.” MʼChichewa, mawu amenewa sakubweretsa tanthauzo limene likufunika palembali. Choncho mʼBaibuloli anamasuliridwa kuti “yakani ndi mzimu.”
Pa ulaliki wake wotchuka kwambiri wapaphiri, Yesu anagwiritsa ntchito mawu omwe nthawi zambiri amamasuliridwa kuti: “Odala ali osauka mumzimu.” (Mateyu 5:3, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu) Komatu mʼzilankhulo zambiri mawu amenewa akawamasulira liwu ndi liwu samveka bwino. Nthawi zina kungomasulira mawuwa liwu ndi liwu kumapereka tanthauzo loti ‘osauka mumzimuwoʼ mitu yawo siigwira kapena ndi opanda mphamvu ndiponso okayikakayika pochita zinthu. Koma apa Yesu ankaphunzitsa anthu mfundo yoti angakhale osangalala, osati chifukwa choti apeza zinthu zimene amafuna, koma chifukwa chozindikira kuti akufunika kutsogoleredwa ndi Mulungu. (Luka 6:20) Choncho tanthauzo lake lenileni limamveka bwino akamasuliridwa kuti, “anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu,” kapena “anthu amene akuzindikira kuti akufunikira Mulungu.”—Mateyu 5:3, The New Testament in Modern English.
Mʼmalo ambiri, mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “nsanje” ali ndi tanthauzo lofanana ndi la mawu a Chichewa. Mawuwa amatanthauza kukwiya chifukwa choti zikuoneka kuti mnzathu akuchita zinthu zosakhulupirika kapena kuipidwa ndi anthu ena chifukwa cha zinthu zimene ali nazo. (Miyambo 6:34; Yesaya 11:13) Koma mawu a Chiheberi omwewo amatanthauzanso zinthu zabwino. Mwachitsanzo, angagwiritsidwe ntchito ponena za “khama” kapena mtima umene Yehova ali nawo wofunitsitsa kuteteza anthu ake kapenanso ‘wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.’ (Ekisodo 34:14; 2 Mafumu 19:31; Ezekieli 5:13; Zekariya 8:2) Angagwiritsidwenso ntchito ponena za “khama” limene atumiki ake okhulupirika ali nalo potumikira kapena kulambira Mulungu kapenanso mtima wawo ‘wosalekerera kuti anthu azipikisanaʼ ndi Mulungu.—Salimo 69:9; 119:139; Numeri 25:11.
Mawu a Chiheberi amene nthawi zambiri amanena za dzanja la munthu, ali ndi matanthauzo osiyanasiyana. Potengera mmene awagwiritsira ntchito, mawuwa angatanthauze “ulamuliro,” “kuwolowa manja” kapena “mphamvu.” (2 Samueli 8:3; 1 Mafumu 10:13; Miyambo 18:21) Ndipotu mawu amenewa anamasuliridwa mʼnjira zosiyanasiyana zoposa 40 mu Baibulo la Dziko Latsopano la Chingelezi.
Tikaganizira mfundo zimenezi, nʼzoonekeratu kuti kumasulira Baibulo si ntchito yongomasulira mofanana mawu a chilankhulo choyambirira paliponse pamene akupezeka. Womasulira ayenera kuganiza mozama kuti asankhe bwino mawu amene ali ndi tanthauzo lolondola la mawu a chilankhulo choyambiriracho. Komanso kuti ziganizo zikhale zosavuta kuwerenga, ayenera kuzilemba mogwirizana ndi malamulo a kalembedwe ka chilankhulo chake.
Koma pochita zimenezi, ayenera kupewa kufotokozera kwambiri mawu. Womasulira amene amangofotokozera mawu a mʼBaibulo mogwirizana ndi zimene iyeyo akumva palembalo angathe kusokoneza tanthauzo lenileni la mawuwo. Kodi angachite bwanji zimenezi? Womasulira angalakwitse powonjezeramo maganizo ake nʼkumaganiza kuti ndi zimene malembawo akutanthauza kapena akhoza kuchotsa mfundo zina zofunika zimene zinali mʼmawu a zilankhulo zoyambirira. Ngakhale kuti Mabaibulo amene anafotokozera kwambiri zinthu pomasulira savuta kuwerenga, nthawi zina zimenezi zimalepheretsa anthu kumva uthenga weniweni umene unali mʼmalembawo.
Zinthu zimene omasulira amakhulupirira zikhozanso kukhudza mawu amene angagwiritse ntchito pomasulira. Mwachitsanzo, lemba la Mateyu 7:13 limanena kuti: “Msewu umene ukupita kuchiwonongeko ndi wotakasuka.” Omasulira ena anagwiritsa ntchito mawu akuti “kuhelo” mʼmalo mwa mawu akuti “kuchiwonongeko” amene akugwirizana ndi tanthauzo la mawu a Chigiriki amene ali palembali. Iwo anachita zimenezi kuti zigwirizane ndi zimene zipembedzo zawo zimakhulupirira.
Womasulira Baibulo ayeneranso kuganizira mfundo yoti polemba Baibulo anagwiritsira ntchito mawu osavuta, omwe anthu wamba monga alimi, abusa ndiponso asodzi, ankagwiritsa ntchito tsiku ndi tsiku. (Nehemiya 8:8, 12; Machitidwe 4:13) Choncho Baibulo lomasuliridwa bwino limafotokoza uthenga wake mosavuta ndipo anthu oona mtima amatha kuumvetsa mosaganizira chikhalidwe kapena dera lomwe akukhala. Ndiye womasulira ayenera kugwiritsa ntchito mawu omveka bwino, odziwika komanso omwe anthu osaphunzira kwambiri angathe kuwamva mosavuta, mʼmalo mogwiritsa ntchito mawu omwe anthu sakonda kuwagwiritsa ntchito.
Popanda zifukwa zomveka, omasulira Baibulo ambiri achotsa dzina la Mulungu lakuti Yehova mʼMabaibulo amene akumasulira masiku ano. Iwo achita zimenezi ngakhale kuti dzinali likupezeka mʼmipukutu yakale ya Baibulo. (Onani Zakumapeto A4.) MʼMabaibulo ambiri anachotsa dzinali nʼkuikamo dzina laudindo ngati “Ambuye,” ndipo ena amachititsa kuti anthu asadziwe zoti Mulungu ali ndi dzina lenileni. Mwachitsanzo, pemphero la Yesu limene lili pa Yohane 17:26 analimasulira kuti: “Ndachititsa kuti iwo akudziweni,” ndipo pa Yohane 17:6 anati, “Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa.” Koma Baibulo limene linamasulira pemphero la Yesuli molondola limati: “Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu,” komanso kuti “anthu amene munawatenga mʼdziko nʼkundipatsa, ine ndawadziwitsa dzina lanu.”
Mogwirizana ndi zimene Baibulo la Dziko Latsopano la Chingelezi loyambirira linanena mʼmawu oyamba, “Ife sitinafotokozere Malemba. Pamene zinali zotheka kugwiritsira ntchito mawu amakono a Chingelezi pomasulira liwu ndi liwu, ndiponso pamene tinaona kuti kuchita zimenezi sikusintha tanthauzo lenileni la mawuwo kapena kulipangitsa kuti lisamveke bwino, tayesetsa kumasulira liwu ndi liwu.” Choncho Komiti Yomasulira Baibulo la Dziko Latsopano yayesetsa kugwiritsa ntchito mawu komanso kuwalemba mofanana ndi mmene analembedwera mʼchilankhulo choyambirira. Komabe, yaonetsetsa kuti asagwiritse ntchito mawu ovuta kuwerenga komanso amene angapangitse kuti anthu asamve tanthauzo lake. Izi zachititsa kuti Baibuloli likhale losavuta kuwerenga ndipo amene akuwerenga sangakayikire ngakhale pangʼono kuti uthenga wake wouziridwa unamasuliridwa molondola.—1 Atesalonika 2:13.