Wolembedwa ndi Luka
6 Tsiku lina pa tsiku la sabata, Yesu ankadutsa mʼmunda wa tirigu ndipo ophunzira ake ankabudula ngala za tirigu+ nʼkumazitikita mʼmanja mwawo kenako nʼkudya.+ 2 Afarisi ena ataona zimenezi anati: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita zinthu zimene ndi zosayenera kuchita pa Sabata?”+ 3 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala?+ 4 Kodi simunawerenge kuti analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,* imene iye ndi anthu omwe anali nawo aja sankayenera kudya malinga ndi malamulo, koma ansembe okha?”+ 5 Kenako anapitiriza kuwauza kuti: “Mwana wa munthu ndi Mbuye wa Sabata.”+
6 Tsiku linanso la sabata,+ iye analowa musunagoge nʼkuyamba kuphunzitsa. Mmenemo munali munthu amene dzanja lake lamanja linali lolumala.+ 7 Alembi ndi Afarisi ankamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthuyo pa Sabata nʼcholinga choti amuimbe mlandu. 8 Koma iye anadziwa zimene iwo ankaganiza.+ Choncho anauza munthu wolumala dzanjayo kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.” Munthuyo ananyamuka nʼkuima pamenepo. 9 Kenako Yesu anawafunsa kuti: “Kodi malamulo amalola kuchita chiyani pa Sabata, chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”+ 10 Atayangʼana uku ndi uku, anauza munthu uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhalanso labwinobwino. 11 Koma iwo anakwiya kwambiri ndipo anayamba kukambirana zoti amuchite Yesu.
12 Mʼmasiku amenewo, Yesu anapita kuphiri kukapemphera+ ndipo anachezera usiku wonse kupemphera kwa Mulungu.+ 13 Kutacha, anaitana ophunzira ake nʼkusankhapo 12, amenenso anawapatsa dzina lakuti atumwi.+ 14 Iye anasankha Simoni, amene ankatchulidwa kuti Petulo, ndi Andireya mchimwene wake. Anasankhanso Yakobo, Yohane, Filipo,+ Batolomeyo, 15 Mateyu, Tomasi,+ Yakobo mwana wa Alifeyo, ndi Simoni wotchedwa “wakhama.” 16 Komanso anasankha Yudasi mwana wa Yakobo ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anamupereka.
17 Kenako anatsika nawo nʼkukaima pamalo afulati. Pamenepo panali gulu lalikulu la ophunzira ake. Panalinso chigulu cha anthu ochokera ku Yudeya konse ndi ku Yerusalemu konse, komanso kumadera amʼmphepete mwa nyanja a ku Turo ndi ku Sidoni. Onsewo anabwera kuti adzamumvetsere komanso kuti adzawachiritse. 18 Ngakhalenso amene ankavutitsidwa ndi mizimu yonyansa anachiritsidwa. 19 Gulu lonse la anthulo linkayesetsa kuti limugwire, chifukwa mphamvu zinkatuluka mwa iye+ nʼkuchiritsa anthu onsewo.
20 Kenako anayangʼana ophunzira ake nʼkuyamba kuwauza kuti:
“Osaukanu ndinu osangalala, chifukwa Ufumu wa Mulungu ndi wanu.+
21 Osangalala ndinu amene mukumva njala, chifukwa mudzakhuta.+
Osangalala ndinu amene mukulira, chifukwa mudzaseka.+
22 Ndinu osangalala anthu akamadana nanu,+ kukusalani,+ kukunyozani komanso kukana* dzina lanu nʼkumanena kuti ndi loipa, chifukwa cha Mwana wa munthu. 23 Sangalalani pa tsiku limenelo ndipo mudumphedumphe mokondwera, chifukwa mphoto imene Mulungu adzakupatseni ndi yaikulu,* popeza zinthu zimenezo ndi zimenenso makolo awo akale anachitira aneneri.+
24 Koma tsoka kwa inu amene muli achuma,+ chifukwa mukulandiriratu zonse zokusangalatsani.+
25 Tsoka inu amene mukukhuta panopa, chifukwa mudzamva njala.
Tsoka inu amene mukuseka panopa, chifukwa mudzamva chisoni komanso kulira.+
26 Muli ndi tsoka anthu onse akamanena zabwino za inu,+ popeza zinthu zimenezo ndi zimenenso makolo awo akale anachitira aneneri abodza.
27 Koma inu amene mukumvetseranu, ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu ndi kuchitira zabwino amene akudana nanu.+ 28 Pitirizani kudalitsa anthu amene akukutembererani komanso kupempherera amene akukunyozani.+ 29 Amene wakumenya mbama patsaya ili, umupatsenso linalo. Amene wakulanda malaya ako akunja, usamuletse kutenga malaya ako amkati.+ 30 Aliyense amene wakupempha kanthu mupatse,+ ndipo amene wakulanda zinthu usamuumirize kuti abweze.
31 Komanso, zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.+
32 Kodi mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, mudzapindula chiyani? Chifukwa ngakhale ochimwa amakonda anthu okhawo amene amawakonda.+ 33 Ngati mumachitira zabwino okhawo amene amakuchitirani zabwino, mudzapindula chiyani? Chifukwa ngakhale ochimwa amachita zomwezo. 34 Komanso, ngati mumakongoza popanda chiwongoladzanja kwa okhawo amene mukuyembekezera kuti adzabweza ngongoleyo, mudzapindula chiyani?+ Ochimwanso amakongoza ochimwa anzawo popanda chiwongoladzanja, kuti adzawabwezere zomwezo. 35 Mosiyana ndi zimenezo, inu pitirizani kukonda adani anu. Pitirizani kuchita zabwino ndi kukongoza popanda chiwongoladzanja, osayembekezera kulandira kalikonse.+ Mukatero, mphoto yanu idzakhala yaikulu ndipo mudzakhala ana a Wamʼmwambamwamba, chifukwa iye ndi wokoma mtima kwa osayamika ndi kwa oipa.+ 36 Pitirizani kukhala achifundo, mofanana ndi Atate wanu amenenso ndi wachifundo.+
37 Komanso, siyani kuweruza ena, mukatero inunso simudzaweruzidwa.+ Siyani kutsutsa ena ndipo inunso simudzatsutsidwa. Pitirizani kukhululukira anthu machimo awo ndipo machimo anunso adzakhululukidwa.+ 38 Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.+ Adzakhuthulira mʼmatumba anu muyezo wabwino, wotsendereka, wokhutchumuka ndi wosefukira. Chifukwa muyezo umene mukuyezera ena, iwonso adzakuyezerani womwewo.”
39 Kenako anawauzanso fanizo lakuti: “Munthu wosaona sangatsogolere wosaona mnzake, angatero ngati? Ngati angatero onse awiri angagwere mʼdzenje, si choncho?+ 40 Wophunzira saposa mphunzitsi wake, koma aliyense amene waphunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake. 41 Nanga nʼchifukwa chiyani umayangʼana kachitsotso mʼdiso la mʼbale wako, koma osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lako?+ 42 Ungauze bwanji mʼbale wako kuti, ‘Mʼbale taima ndikuchotse kachitsotso kamene kali mʼdiso lako,’ pamene iwe ukulephera kuona mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lako? Wachinyengo iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lakowo. Ukatero udzatha kuona bwino, moti udzakwanitsa kuchotsa kachitsotso kamene kali mʼdiso la mʼbale wako.
43 Mtengo wabwino sungabereke chipatso chowola ndipo mtengo wowola sungabereke chipatso chabwino.+ 44 Chifukwa mtengo uliwonse umadziwika ndi chipatso chake.+ Mwachitsanzo, anthu sathyola nkhuyu mumtengo waminga, kapena kudula mphesa pachitsamba chaminga. 45 Munthu wabwino amatulutsa zabwino mʼchuma chabwino chamumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa mʼchuma choipa chamumtima mwake, chifukwa pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+
46 Nanga nʼchifukwa chiyani mumandiitana kuti ‘Ambuye! Ambuye!’ koma osachita zimene ndimanena?+ 47 Aliyense amene amabwera kwa ine kudzamva mawu anga, nʼkuchita zimene wamvazo, ndikuuzani amene amafanana naye:+ 48 Iyeyo ali ngati munthu amene pomanga nyumba, anakumba mozama kwambiri nʼkuyala maziko pathanthwe. Ndiye mtsinje utasefukira, madzi anawomba nyumbayo, koma sanathe kuigwedeza chifukwa anaimanga bwino.+ 49 Pamene munthu amene wamva koma osachita chilichonse,+ ali ngati munthu amene wamanga nyumba yopanda maziko padothi. Apanso mtsinje unasefukira nʼkuwomba nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo inagwa, moti kugwa kwake kunali kwakukulu.”