MUTU 9
Muzichitira Ena Zimene Mulungu Amafuna
1-3. (a) Kodi Akhristu ena amaganiza chiyani akamva za mzinda wa Turo wakale? (b) Kodi panali ubwenzi wotani pakati pa Mfumu Hiramu ndi mtundu wa Isiraeli? (c) Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene anthu a ku Turo anachita?
KODI mumaganiza chiyani mukamva za mzinda wakale wa Turo? Akhristu ena angaganize za kukwaniritsidwa kwa ulosi winawake wonena za kuwonongedwa kwa mzindawo. Ulosiwo unakwaniritsidwa pamene Alekizanda Wamkulu anafukula miyala m’mabwinja a mzinda wa Turo wakale n’kumangira msewu umene unakafika pamzinda wa Turo watsopano womwe unali pachilumba. Kenako iye anadutsa mumsewu umenewu popita kukawononga mzinda wa Turo wa pachilumbawo. (Ezekieli 26:4, 12; Zekariya 9:3, 4) Komabe, mukamva za mzindawu muziganiziranso zimene muyenera kuchitira anthu ena kapena Akhristu anzanu, ndiponso zimene simuyenera kuwachitira.
2 Ndiyeno ganizirani chifukwa chake mzindawu unawonongedwa. Yehova ananena kuti: “Popeza kuti Turo anapanduka mobwerezabwereza, . . . chifukwa chakuti anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo, ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pa ubale. Ndidzatumiza moto pakhoma la Turo.” (Amosi 1:9, 10) Poyamba, Mfumu Hiramu wa ku Turo anasonyeza kuti anali wokoma mtima kwa Davide moti anapereka zipangizo zomangira kachisi wa Solomo. Komanso Solomo anachita pangano ndi mfumuyi ndipo anaipatsa mizinda ina ya ku Galileya. M’pake kuti Mfumu Hiramu anatchula Solomo kuti “m’bale wanga.” (1 Mafumu 5:1-18; 9:10-13, 26-28; 2 Samueli 5:11) Patapita nthawi, anthu a ku Turo “sanakumbukire pangano la pa ubale” limeneli ndipo anagulitsa anthu ena a Mulungu kuti akhale akapolo. Koma Yehova sanasangalale ndi zimenezi.
3 Choncho Mulungu anaweruza Akanani a ku Turo amenewo chifukwa chochitira nkhanza anthu ake. Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Mfundo yaikulu imene tikuphunzira ndi yokhudza mmene tiyenera kuchitira zinthu ndi Akhristu anzathu. M’mitu ina ya m’mbuyomu, tinaphunzira malangizo a aneneri 12 a mmene tingachitire zinthu ndi ena. Mwachitsanzo, tinaona mmene tingachitire zinthu mwachilungamo pa nkhani ya bizinezi komanso mmene tingakhalire ndi makhalidwe abwino. Komabe, m’mabuku 12 amenewa mulinso zina zimene Mulungu akufuna kuti tizichitira anthu ena.
MUSAMASANGALALE WINA AKAMAVUTIKA
4. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Aedomu anali “abale” enieni a Aisiraeli, nanga kodi Aedomuwo anachitira chiyani abale awowo?
4 Zimene Mulungu ananena podzudzula anthu a ku Edomu, mzinda womwe unali pafupi ndi dziko la Isiraeli, zikutiphunzitsa mfundo inayake. Iye anati: “Iwe sunayenera kumangoonerera mosangalala pa tsiku limene m’bale wako anakumana ndi tsoka. Sunayenera kusangalala pa tsiku limene ana a Yuda anali kuwonongedwa.” (Obadiya 12) Anthu a ku Turo anali “pa ubale” ndi Aisiraeli ndipo n’kutheka kuti ubale umenewu unayamba chifukwa cha nkhani zamalonda. Koma Aedomu anali abale enieni a Aisiraeli chifukwa iwo anali mbadwa za Esau, mchimwene wa Yakobo. Ndipotu Yehova anatchula Aedomu kuti ndi “abale” awo a Aisiraeli. (Deuteronomo 2:1-4) Choncho Aedomu anasonyeza kuti anali ndi nkhanza zoopsa chifukwa anasangalala pamene Ababulo anaukira Ayuda.——Ezekieli 25:12-14.
5. Kodi n’chiyani chingachititse kuti nthawi zina munthu asonyeze mtima ngati wa Aedomu?
5 N’zoonekeratu kuti Mulungu sanasangalale ndi zimene Aedomu anachitira Ayuda omwe anali abale awo. Choncho, ifeyo masiku ano tingachite bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi Mulungu amaona bwanji zimene ndimachitira abale anga?’ Mbali imodzi imene tiyenera kuiganizira ndi yokhudza zimene timachitira m’bale wathu ngati zinthu zina sizinayende bwino. Mwachitsanzo, tiyerekeze kuti Mkhristu wina wakukhumudwitsani kapena wasemphana maganizo ndi wachibale wanu. Ngati muli ndi “chifukwa chodandaulira” za mnzanuyo, kodi mudzamusungira chakukhosi osamukhululukira, kapena osayesa n’komwe kuthetsa vutolo? (Akolose 3:13; Yoswa 22:9-30; Mateyu 5:23, 24) Kuchita zimenezi kungakhudze mmene mungamachitire zinthu ndi m’bale wanuyo. Mwachitsanzo, zingachititse kuti musamamusangalalire, muzimupewa kapenanso muzinena zinthu zoipa zokhudza iyeyo. Komanso tiyerekezere kuti m’bale ameneyu nthawi ina, walakwitsa chinachake ndipo mwina akufunikira kupatsidwa uphungu ndi akulu mumpingo. (Agalatiya 6:1) Kodi inuyo mudzasangalala ngati mmene Aedomu anachitira? Kodi pamenepa Mulungu angafune kuti muchite chiyani?
6. Kodi lemba la Mika 7:18 likutilimbikitsa kuti tizichita chiyani kuwonjezera pa zimene zili pa Zekariya 7:10?
6 Yehova anauza Zekariya zimene akufuna kuti tisamachite. Iye anati: “Musamakonzerane ziwembu mumtima mwanu.” (Zekariya 7:9, 10; 8:17) Malangizo amenewa ndi othandiza ngati tikuona kuti Mkhristu wina watikhumudwitsa kapena wasemphana maganizo ndi wachibale wathu. Zikatere, zimakhala zosavuta ‘kumukonzera ziwembu mumtima mwathu’ ndipo zochita zathu zimasonyeza zimenezi. Koma kumbukirani kuti Mulungu amafuna kuti tizimutsanzira. Mika analemba kuti Yehova “amakhululukira zolakwa ndi machimo.”a (Mika 7:18) Ndiyeno kodi tingatani kuti nafenso tizikhululukira ena?
7. N’chifukwa chiyani ndi bwino kungoiwala zimene wina watilakwira?
7 N’zoona kuti zimene Mkhristu wina anakuchitirani kapena zimene anachitira wachibale wanu zingakupwetekeni. Komabe kodi nkhaniyo ndi yaikulu moti simungathe kungoiiwala? Baibulo limafotokoza zimene mungachite kuti mugwirizanenso ndi Mkhristu amene mwasemphana naye maganizo pa nkhani yaing’ono ngakhalenso yaikulu. Koma nthawi zambiri ndi bwino kungoiwala nkhaniyo kapena kuti ‘kungokhululuka.’ Choncho muzidzifunsa kuti: ‘Kodi umenewu si mwayi woti nditsatire zimene Yesu ananena zoti ndiyenera kukhululukira m’bale wanga mpaka nthawi 77? Kodi nkhaniyi sindingathe kungoiiwala?’ (Mateyu 18:15-17, 21, 22) N’zoona kuti nkhaniyo ingaoneke yaikulu panopa, koma kodi pakadutsa zaka 1,000, mudzaikumbukirabe? Mawu amene ali palemba la Mlaliki 5:20, onena za munthu amene akusangalala ndi zakudya komanso zakumwa chifukwa cha ntchito imene anagwira, angatiphunzitse kanthu kena. Lembali limati: “Zowawa za pamoyo wake waufupi sazizikumbukira kawirikawiri, chifukwa Mulungu woona akuchititsa kuti mtima wake uzisangalala.” Chifukwa chakuti munthuyo akungoganizira zinthu zosangalatsa zimene akuchitazo, sakukumbukiranso mavuto a pa moyo wake. Ifenso tiyenera kuchita zimenezi. Tikamaganizira madalitso amene timapeza chifukwa cha ubale wathu wachikhristu, zingatithandize kuti tiziiwala nkhani zosafunikira kwenikweni zomwe sitidzazikumbukira n’komwe m’dziko latsopano. Ndi bwino kuchita zimenezi kusiyana ndi kusangalala wina akakumana ndi mavuto, kapena kumakumbukirabe zimene ena atilakwira.
MUZINENA ZOONA ZOKHAZOKHA
8. Kodi tingakumane ndi vuto liti tikamakambirana nkhani zosiyanasiyana?
8 Mabuku 12 a aneneri amatchulanso zoti Mulungu amafuna kuti tizichita zinthu moona mtima komanso tizinena zoona nthawi zonse. N’zoona kuti timayesetsa kuchita zimenezi pouza ena “choonadi cha uthenga wabwino.” (Akolose 1:5; 2 Akorinto 4:2; 1 Timoteyo 2:4, 7) Komabe zingakhale zovuta kunena zoona zokhazokha pamene tikukambirana nkhani zosiyanasiyana ndi anthu a m’banja mwathu kapena Akhristu anzathu. N’chifukwa chiyani zili choncho?
9. Kodi n’chiyani chingachititse kuti munthu asanene zoona, ndipo tiyenera kudzifunsa mafunso otani?
9 Kodi alipo amene sanauzidwepo kuti walankhula kapena kuchita zinthu mosaganizira anzake? N’kutheka kuti munthu atakuuzani zimene munalakwitsazo munachita manyazi kapena munadziimba mlandu. Zimenezi zingachititse munthu kuti akane zimene analakwitsazo kapena ayambe kunama podziikira kumbuyo n’cholinga choti aoneke ngati sanalakwitse. Kapena ngati munthuyo akuchita manyazi chifukwa cha zimene wachitazo, angasankhe kunena zinthu zina n’kusiya zina kuti aoneke ngati sanalakwe. Choncho zimene iye anganenezo zingakhale zoona ndithu, koma kungoti sananene zonse ndipo anthu angakhale ndi chithunzi cholakwika cha zimene zinachitikadi. Mwina munthuyo angaganize kuti sananene bodza lankunkhuniza ngati limene anthu ambiri amanena masiku ano. Komabe, kodi tingati munthu amene sanafotokoze nkhani yonse ‘akulankhula zoona’ kwa ena kapena kwa Akhristu anzake? (Aefeso 4:15, 25; 1 Timoteyo 4:1, 2) Kodi mukuganiza kuti Mulungu amamva bwanji Mkhristu akamafotokoza nkhani m’njira yoti anzake asadziwe zoona zenizeni, kapena azikhulupirira zinthu zimene si zolondola?
10. Kodi aneneri anafotokoza bwanji zimene anthu ambiri ankachita ku Isiraeli ndi ku Yuda?
10 Aneneri ankaonanso kuti ngakhale amuna ndi akazi odzipereka kwa Yehova nthawi zina sankachita zimene iye amafuna. Hoseya ananena mmene zochita za anthu ena m’nthawi yake zinakhudzira Mulungu. Iye anati: “Adzawonongedwa chifukwa chakuti aphwanya malamulo anga. Ine ndinali kufuna kuwawombola, koma iwo alankhula mabodza otsutsana nane.” Kuwonjezera pa kunena mabodza oonekeratu potsutsana ndi Yehova, ena anayamba kuchita “malumbiro abodza” ndiponso “kuchita zachinyengo.” Mwina ankachita zimenezi pofuna kupotoza nkhani kuti ena asadziwe zoona zenizeni. (Hoseya 4:1, 2; 7:1-3, 13; 10:4; 12:1) Hoseya analemba mawu amenewa ali ku Samariya, mzinda womwe unali mu ufumu wa kumpoto. Nanga pa nthawiyi zinthu zinali bwanji ku Yuda? Mika akutiuza kuti: “Anthu olemera a mumzindawo amakonda kuchita zachiwawa. Anthu okhalamo akulankhula zonama ndipo lilime la m’kamwa mwawo ndi lachinyengo.” (Mika 6:12) Ndi bwino kudziwa mmene aneneriwo anadzudzulira anthu ‘ochita zachinyengo’ komanso omwe “lilime la m’kamwa mwawo ndi lachinyengo.” Choncho ngakhale Akhristu amene sanena mabodza ankunkhuniza, angadzifunse kuti: ‘Kodi nthawi zina ndimachita zachinyengo kapena lilime la m’kamwa mwanga limakhala lachinyengo? Kodi Mulungu akufuna kuti ndizichita chiyani pa nkhani imeneyi?’
11. Kodi aneneri ananena kuti Mulungu amafuna tizipewa chiyani tikamalankhula?
11 N’zosangalatsa kuti Mulungu anagwiritsira ntchito aneneri pofotokoza momveka bwino zimene iye akufuna kuti tizichita. Mwachitsanzo lemba la Zekariya 8:16 limanena kuti: “Anthu inu muzichita zinthu izi: Muzilankhulana zoona zokhazokha. Poweruza milandu m’zipata za mizinda yanu, muziweruza mogwirizana ndi choonadi komanso molimbikitsa mtendere.” M’nthawi ya Zekariya, akulu ankaweruza milandu pazipata za mizinda. (Rute 4:1; Nehemiya 8:1) Komabe, Zekariya sananene kuti anthu azilankhula zoona pa nthawi ya milandu pokha. N’zoona kuti tikufunika kulankhula zoona tikakhala pa gulu, koma tikulimbikitsidwanso kuti: “Muzilankhulana zoona zokhazokha.” Izi zikutanthauza kuti tizinena zoona tikamalankhula ndi achibale athu komanso mwamuna kapena mkazi wathu. Tizichitanso chimodzimodzi polankhula ndi Akhristu anzathu pamasom’pamaso, m’makalata, kapena pa foni. Popeza achibale athu, anzathu komanso Akhristu anzathu amatikhulupirira kwambiri, nthawi zonse amaona kuti zimene tikulankhula n’zoona. Nawonso makolo achikhristu ayenera kuphunzitsa ana awo kuipa kwa bodza. Zimenezi zidzathandiza kuti anawo azidziwa kuti Mulungu safuna kuti iwo akhale ndi lilime lachinyengo ndipo amafuna kuti nthawi zonse azinena zoona zokhazokha.—Zefaniya 3:13.
12. Kodi ndi mfundo zofunika ziti zimene tingaphunzire m’mabuku a aneneri?
12 Munthu aliyense, wachinyamata kapena wachikulire, amene amayesetsa kutsatira mfundo za choonadi amachita zimene Zekariya anatilimbikitsa kuti tizichita. Iye anati: “Muzikonda choonadi ndi kulimbikitsa mtendere.” (Zekariya 8:19) Malaki anafotokoza zimene Yehova anaona mwa Mwana Wake, zomwe ndi chitsanzo chabwino kwa ife. Iye anati: “Lamulo la choonadi linali m’kamwa mwake ndipo pamilomo pake panalibe zosalungama. Anali kuyenda ndi ine mwamtendere komanso mowongoka mtima.” (Malaki 2:6) Yehova akufuna kuti ifenso tizichita zimenezi. Kumbukirani kuti tili ndi Baibulo lonse mmene mulinso mabuku 12 a aneneri, ndipo tingaphunzire zambiri m’mabuku amenewa.
PEWANI KUCHITA ZACHIWAWA
13. Kodi lemba la Mika 6:12 limatchula zoti anthu a Mulungu anali ndi vuto liti?
13 Lemba la Mika 6:12 limatchula njira ina imene anthu a Mulungu ankachitira anthu ena zoipa. Lembali limati iwo ‘ankalankhula zonama ndiponso ankanena zachinyengo ndi lilime la m’kamwa mwawo.’ Koma lembali likutchulanso vuto lina lalikulu. Vuto lake ndi lakuti ‘anthu olemera a mumzindawo ankakonda kuchita zachiwawa.’ Kodi ankachita bwanji zimenezi, nanga ifeyo tiyenera kuchita chiyani?
14, 15. Kodi mitundu yoyandikana ndi anthu a Mulungu inali ndi mbiri yotani pa nkhani ya chiwawa?
14 Taganizirani zinthu zachiwawa zimene mitundu ina ya anthu yomwe inali pafupi ndi anthu a Mulungu inkachita. Kumpoto chakum’mawa kunali dziko la Asuri lomwe likulu lake linali Nineve. Ponena za mzinda umenewu Nahumu analemba kuti: “Tsoka mzinda wokhetsa magazi. Mzindawo wadzaza ndi chinyengo ndi chifwamba, moti nthawi zonse umafunkha zinthu za anthu ena.” (Nahumu 3:1) Anthu a ku Asuri anali ndi mbiri yochita nkhanza pa nthawi ya nkhondo komanso yochitira nkhanza akaidi ogwidwa pa nkhondo. Mwachitsanzo, akaidi ena ankawatentha kapena kuwasenda khungu lawo ali moyo, ndipo ena ankawathudzula maso kapena kuwadula mphuno, makutu ndi zala. Buku lina linanena kuti: “Anthu akamva dzina lakuti Nineve ankangoganizira za kuphana, kulanda katundu wa ena, kuponderezana ndiponso kuzunza anthu opanda mphamvu. Zinthu zimenezi zinkachitika nthawi zosiyanasiyana komanso pa nkhondo.” (Gods, Graves, and Scholars) M’buku la Yona muli mawu a mfumu ya ku Nineve imene inaona (kapena kuchita nawo) zachiwawazo. Mfumuyi itamva uthenga wa Yona wonena zimene zidzachitikire anthu mumzindawo, inanena kuti: “Munthu aliyense komanso ziweto zivale chiguduli. Afuulire Mulungu ndi mphamvu zawo zonse, ndipo aliyense asiye njira zake zoipa ndi zinthu zonse zachiwawa zimene amachita.”—Yona 3:6-8.b
15 Nkhanza zoopsazi sizinkachitika ku Asuri kokha. Mulungu anadzudzulanso mzinda wa Edomu womwe unali kum’mwera chakum’mawa kwa Yuda. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi? Baibulo limati: “Edomu adzasanduka chipululu chopanda kanthu chifukwa cha chiwawa chimene anachitira ana a Yuda, ndiponso chifukwa chokhetsa magazi osalakwa m’dziko la Yudalo.” (Yoweli 3:19) Kodi Aedomu anamvera chenjezo limenelo n’kusiya zachiwawa zimene ankachitazo? Patapita zaka pafupifupi 200, Obadiya analemba kuti: “Iwe Temani, [mzinda wa ku Edomu] anthu ako amphamvu adzachita mantha. . . . Chifukwa chakuti m’bale wako Yakobo unam’chitira zachiwawa, . . . udzawonongedwa ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.” (Obadiya 9, 10) Nanga bwanji anthu a Mulungu? Kodi nawonso ankachita nawo zachiwawazo?
16. Kodi Amosi ndi Habakuku akutithandiza kuona vuto liti limene linalipo m’nthawi yawo?
16 Amosi anafotokoza mmene zinthu zinalili ku Samariya, likulu la ufumu wa kumpoto. Iye anati: “‘Onani zinthu zambiri zachisokonezo ndi zachinyengo zimene zikuchitika mumzinda umenewo. Anthuwo sadziwa kuchita zolungama, ndipo asonkhanitsa munsanja zawo zokhalamo zinthu zimene anafunkha mwachiwawa,’ watero Yehova.” (Amosi 3:9, 10) Mwina mungaganize kuti zinthu sizinali choncho ku Yuda kumene kunali kachisi wa Yehova. Koma Habakuku yemwe ankakhala ku Yudako anafunsa Mulungu kuti: “Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku chiwawa koma inu osandimva kufikira liti? N’chifukwa chiyani mukundichititsa kuona zinthu zopweteka? N’chifukwa chiyani mukupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa? N’chifukwa chiyani kufunkha ndi chiwawa zikuchitika pamaso panga?”—Habakuku 1:2, 3; 2:12.
17. Kodi n’kutheka kuti anthu a Mulungu anayamba kuchita chiwawa chifukwa chiyani?
17 Kodi n’kutheka kuti anthu a Mulunguwa anayamba kuchita chiwawa potengera zimene anthu a mitundu ina ankachita, monga a ku Edomu ndi ku Asuri? Solomo anali atachenjeza kuti zimenezi zingathe kuchitika. Iye anati: “Usasirire munthu wachiwawa, kapena kusankha njira zake.” (Miyambo 3:31; 24:1) Patapita nthawi, Yeremiya ananena mosapita m’mbali kuti: “Yehova wanena kuti: ‘Musaphunzire njira za anthu a mitundu ina ngakhale pang’ono.’”—Yeremiya 10:2; Deuteronomo 18:9.
18, 19. (a) Ngati Habakuku akanakhala ndi moyo m’nthawi yathu ino, kodi akanamva bwanji poona zachiwawa zimene zikuchitikazi? (b) Kodi inuyo mumamva bwanji ndi zachiwawa zimene zikuchitika masiku ano?
18 N’zodziwikiratu kuti ngati Habakuku akanakhala ndi moyo m’nthawi yathu ino, akanaipidwa ndi zachiwawa zimene zikuchitikazi. Anthu ambiri amaonerera zachiwawa kuyambira ali ana chifukwa mavidiyo ambiri a ana amakhala achiwawa. Mwachitsanzo, mavidiyowa amasonyeza anthu akuvulazana, kuwomberana kapena kuphulitsana ndi mabomba. Anawo akamakula, amayamba kuchita masewera achiwawa a pakompyuta. Kuti apambane pa masewerawa, amawombera kapena kuphulitsa ndi mabomba zithunzi za anthu zimene zimaoneka pakompyutayo. Koma mwina ena anganene kuti, “Zimenezi zilibe vuto chifukwa zimakhala zongoyerekezera.” Komabe munthu akamakonda kuchita masewera achiwawa pakompyuta, maganizo ndi zochita zake zimakhalanso zachiwawa. Izi zikugwirizana ndi mfundo youziridwa yakuti: “Munthu wachiwawa amakopa mnzake, ndipo amam’chititsa kuti ayende m’njira yoipa.”—Miyambo 16:29.
19 Habakuku ankamva chisoni kwambiri chifukwa sakanapewa ‘kupitiriza kuyang’ana khalidwe loipa’ komanso “chiwawa” chimene ‘chinkachitika pamaso’ pake. Choncho inuyo mungachite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi iye akanasangalala ngati tikanaonera limodzi mapulogalamu a pa TV amene ine ndimakonda kuonera? Kodi iye akanapita kukaonera masewera achiwawa amene amafuna kuti osewerawo avale zinthu zodzitetezera ngati mmene ankachitira anthu akale omwe ankachita masewera omenyana pogwiritsa ntchito zida zoopsa?’ Masiku ano, anthu ambiri amasangalala kwambiri akamaona anthu akumenyana m’bwalo la masewera kapena anthu ochemerera akumenyana. Komanso anthu ambiri a zikhalidwe zina amaonerera mafilimu ankhondo kapena akarati. Mwina iwo anganene kuti amachita zimenezi chifukwa ndi zimene makolo awo ankachita kapena ndi chikhalidwe chawo. Koma kodi zifukwa zimenezi zimachititsa kuti zachiwawazo zikhale zovomerezeka?—Miyambo 4:17.
20. Kodi Malaki anasonyeza kuti Yehova amadana ndi mtundu wina uti wa chiwawa?
20 Malaki anatchulanso nkhani ina yofanana ndi imeneyi pofotokoza mmene Yehova anaonera zachinyengo zimene Ayuda ena ankachitira akazi awo. Iye anati: “‘Ine ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja,’ watero Yehova Mulungu wa Isiraeli. ‘Ndimadana ndi munthu amene zochita zake zankhanza zili ngati chovala chauve chimene wavala.’” (Malaki 2:16) Anthu amatanthauzira m’njira zosiyanasiyana mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “zochita zake zankhanza zili ngati chovala chauve chimene wavala.” Akatswiri ena a Baibulo amaganiza kuti mawuwa amatanthauza kuti magazi agwera pachovala cha munthu amene akumenya mnzake. Kaya mawuwa amatanthauzadi zimenezi kapena ayi, koma mfundo ndi yakuti Malaki ankadzudzula mwamphamvu amuna amene ankazunza akazi awo. Apa Malaki ankanena za chiwawa chimene chimachitika m’banja ndipo anasonyeza kuti Mulungu sasangalala ndi aliyense wochita zimenezi.
21. Kodi Mkhristu ayenera kupewa chiwawa chotani m’banja? Fotokozani.
21 Mulungu amadana ndi chiwawa chilichonse chimene chachitika m’nyumba mwa Mkhristu kapena kwina kulikonse, kaya chiwawacho chikhale kumenya kapena kulalata. (Mlaliki 5:8) Ngakhale kuti Malaki ananena za chiwawa chimene mwamuna angachitire mkazi wake, Baibulo silisonyeza kuti palibe vuto ngati atachitira chiwawacho ana ake kapena makolo ake okalamba. Komanso Mulungu sasangalala ngati mkazi atachitira chiwawa mwamuna wake, ana ake kapena makolo ake. N’zoona kuti nthawi zina m’banja anthu angasemphane maganizo chifukwa ndi opanda ungwiro ndipo zimenezi zingachititse kuti ena m’banjamo akhumudwe kapena akwiye. Komabe Baibulo limatilangiza kuti: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.”—Aefeso 4:26; 6:4; Salimo 4:4; Akolose 3:19.
22. Kodi tikudziwa bwanji kuti n’zotheka kupewa chiwawa ngakhale kuti anthu ambiri ndi achiwawa?
22 Ena anganene kuti amachita zachiwawa chifukwa chakuti anakulira m’banja la anthu achiwawa kapena anthu a m’dera lawo, mwinanso a chikhalidwe chawo, ndi okonda zachiwawa. Koma pamene Mika ankadzudzula ‘anthu olemera okonda kuchita zachiwawa,’ sanasonyeze kuti anthuwo sangathe kusiya zachiwawazo chifukwa anakulira pakati pa anthu okonda zachiwawa. (Mika 6:12) Taganizirani chitsanzo cha Nowa. Iye anakhala pa nthawi imene ‘dziko lapansi linadzaza ndi chiwawa’ ndipo ana ake anakulira pakati pa anthu achiwawawo. Kodi iwo anatengera khalidwe lachiwawa la anthuwo? Ayi, sanatengere. “Nowa anayanjidwa ndi Yehova” ndipo ana ake anatengera chitsanzo chake chabwino moti anapulumuka pa nthawi ya Chigumula.—Genesis 6:8, 11-13; Salimo 11:5.
23, 24. (a) N’chiyani chimatithandiza kuti tizidziwika kuti ndife anthu odana ndi chiwawa? (b) Kodi Yehova amaona bwanji anthu amene amachitira ena zinthu zimene iye amafuna?
23 Padziko lonse, a Mboni za Yehova amadziwika kuti ndi anthu okonda mtendere osati chiwawa. Iwo amalemekeza komanso kutsatira malamulo a Kaisara oletsa zachiwawa. (Aroma 13:1-4) Anthu a Mboni ‘asula malupanga awo kukhala makasu a pulawo,’ ndipo amayesetsa kukhala mwamtendere ndi wina aliyense. (Yesaya 2:4) Iwo amayesetsa “kuvala umunthu watsopano,” umene umawathandiza kupewa zachiwawa. (Aefeso 4:22-26) Komanso amatengera chitsanzo chabwino cha akulu achikhristu amene sachita ‘ndewu’ yeniyeni kapena ya mawu.—1 Timoteyo 3:3; Tito 1:7.
24 Zoonadi, tingakwanitse kuchitira ena zimene Mulungu amafuna, ndipo tiyenera kuchita zimenezi. Hoseya anati: “Ndani ali ndi nzeru kuti amvetse zinthu zimenezi? Wochenjera ndani kuti adziwe zimenezi? Pakuti njira za Yehova ndi zowongoka ndipo anthu olungama ndi amene adzayendamo.”—Hoseya 14:9.
a Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti “amakhululukira machimo,” amatanthauza “kulambalala machimo.” Katswiri wina wa Baibulo anafotokoza kuti mawu amenewa “anachokera ku zimene munthu wapaulendo amachita pongolambalala chinthu chomwe alibe nacho chidwi. Choncho Mulungu amaona ndithu machimo athu koma nthawi zina sawalabadira n’komwe. Iye amachita zimenezi popeza amakhululuka.”
b Pa mtunda wa makilomita pafupifupi 35 kum’mwera chakum’mawa kwa mzinda wa Nineve, panali mzinda wotchedwa Kala, umene Ashurnasirpal anaumanganso. Masiku ano mzindawu umatchedwa Nimrud. M’nyumba ina yosungiramo zinthu zakale ya ku Britain muli makoma a mzinda wa Kala. Pofotokoza za makoma amenewa, buku lina linati: “Ashurnasirpal anasonyeza bwino nkhanza zimene ankachita pomenya nkhondo. Akaidi ankapachikidwa pamitengo pafupi ndi mpanda wa mzinda umene wagonjetsedwa . . .; Amuna ndi akazi achinyamata ankawasenda khungu lawo ali moyo.”—Archaeology of the Bible.