Tsiku “Lotentha Ngati Ng’anjo”
“Taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo.”—MALAKI 4:1.
1. Kodi ndi mafunso ati amene akubuka mogwirizana ndi Malaki 4:1?
MKATI mwa masiku otsiriza ano, odala ali awo amene dzina lawo limasankhidwa ndi Yehova kulembedwa m’buku lake la chikumbutso. Komano bwanji za awo amene samayenerera mwaŵi umenewu? Kaya akhale olamulira kapena anthu wamba, kodi zinthu zidzawayendera motani ngati achitira mwachipongwe olengeza Ufumu wa Mulungu ndi uthenga wawo? Malaki amanena za tsiku la kuŵerengera mlandu. Pa chaputala 4, vesi 1, timaŵerenga kuti: “Pakuti taonani, likudza tsiku, lotentha ngati ng’anjo; ndipo onse akudzikuza ndi onse akuchita choipa adzakhala ngati chiputu; ndi tsiku lilinkudza lidzawayatsa, ati Yehova wa makamu, osawasiyira muzu kapena nthambi.”
2. Kodi ndi mafotokozedwe amphamvu otani onena za chiweruzo cha Yehova amene akuperekedwa ndi Ezekieli?
2 Nawonso aneneri ena amayerekezera kuweruza mitundu kwa Yehova ndi kutentha kwakukulu kwa ng’anjo. Ezekieli 22:19-22 amayenerera bwino lomwe chotani nanga ndi kuweruza kwa Mulungu timagulu ta Dziko Lachikristu lampatuko! Timaŵerenga kuti: “Atero Ambuye Yehova, Popeza mwasanduka mphala nonsenu, chifukwa chake taonani, ndidzakusonkhanitsani . . . Monga asonkhanitsa mtapo wa siliva, ndi mkuwa, ndi chitsulo, ndi mtovu, ndi seta, mkati mwa ng’anjo, kuzivukutira moto, kuzisungunula momwemo, ndidzakusonkhanitsani mu mkwiyo wanga ndi ukali wanga, ndi kukuikani komweko, ndi kukusungunulani. Inde ndidzakusonkhanitsani, ndi kukuvukutirani ndi moto wa kuzaza kwanga, ndipo mudzasungunuka pakati pake. Monga siliva asungunuka mkati mwa ng’anjo, momwemo inu mudzasungunuka mkati mwake; motero mudzadziŵa kuti ine Yehova ndakutsanulirani ukali wanga.”
3, 4. (a) Kodi ndi mawu achinyengo otani amene atsogoleri achipembedzo anena? (b) Kodi mbiri yonyansa ya chipembedzo njotani?
3 Fanizo lamphamvudi! Atsogoleri achipembedzo amene apeŵa kugwiritsira ntchito dzina la Yehova, akumachitiradi mwano dzina loyeralo, ayenera kuyang’anizana ndi tsiku limenelo la kuŵerengera mlandu. Monyada, amanena kuti iwo ndi mabwenzi awo andale adzakhazikitsa Ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi, kapena kupangitsa dziko lapansi kukhala malo oyenerera Ufumuwo.
4 Dziko Lachikristu lampatukolo lagwirizana ndi olamulira andale m’nkhondo zowopsa. Mbiri imafotokoza za Nkhondo Zamtanda za nyengo zapakati, kutembenuza anthu koumiriza kwa bwalo la Spanish Inquisition, Nkhondo za Zaka Makumi Atatu zimene zinapulula Ulaya m’zaka za zana la 17, ndi nkhondo yotchedwa Spanish Civil War ya m’ma 1930, yomenyedwa kupangitsa Spain kukhala malo otetezereka a Chikatolika. Kukhetsa mwazi kwakukulu koposa kunadza ndi nkhondo ziŵiri za dziko za m’zaka za zana lathu lino, pamene Akatolika ndi Aprotesitanti analoŵa m’kupha kwa onse ndi kosasankha kwa okhulupirira anzawo ndiponso a zipembedzo zina. Posachedwapa, pakhala kumenyana kophana pakati pa Akatolika ndi Aprotesitanti ku Ireland, pakati pa magulu achipembedzo ku India, ndi pakati pa magulu achipembedzo a yemwe kale anali Yugoslavia. Mbiri ya chipembedzo yadzazidwanso ndi mwazi wa ofera chikhulupiriro zikwizikwi a mboni zokhulupirika za Yehova.—Chivumbulutso 6:9, 10.
5. Kodi chipembedzo chonyenga chikuyembekezera kupatsidwa chiweruzo chotani?
5 Tingayamikiredi chilungamo cha chiweruzo cha Yehova choyandikiracho pa Babulo Wamkulu, ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, limodzi ndi ochirikiza ake. Chiweruzo chimenechi chikufotokozedwa pa Chivumbulutso 18:21, 24: “Mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babulo, mudzi waukulu, udzapasulidwa kolimba, ndipo sudzapezedwanso konse. Ndipo momwemo munapezedwa mwazi wa aneneri ndi oyera mtima, ndi onse amene anaphedwa padziko.”
6. (a) Kodi ndani amene ayenera kukhala ngati chiputu, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi pali chitsimikizo chotani kwa awo amene amawopa Yehova?
6 Pamene nthaŵi ifika, adani onse a chilungamo ndi awo amene amamamatirana nawo, “adzakhala ngati chiputu.” Tsiku la Yehova lidzayaka ngati ng’anjo pakati pawo. ‘Silidzawasiyira muzu kapena nthambi.’ Patsiku limenelo la kuŵerengera mlandu, ana aang’ono, kapena nthambi, adzalangidwa moyenerera malinga ndi mmene Yehova aonera mizu yawo, makolo awo, amene amayang’anira ana ameneŵa. Makolo oipa sadzakhala ndi mbadwa zopitiriza njira zawo zoipa. Koma awo amene amasonyeza chikhulupiriro m’malonjezo a Ufumu wa Mulungu sadzagwedezeka. Motero Ahebri 12:28, 29 amalimbikitsa kuti: “Tikhale nacho chisomo, chimene tikatumikire nacho Mulungu momkondweretsa, ndi kumchitira ulemu ndi mantha. Pakuti Mulungu wathu ndiye moto wonyeketsa.”
Kodi Yehova ndi Mulungu Wankhanza?
7. Kodi chikondi cha Yehova chimaloŵa motani m’chiweruzo chake?
7 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti Yehova ndi Mulungu wankhanza ndi wokonda kulipsira? Kutalitali! Pa 1 Yohane 4:8, mtumwiyo akunena mfundo ina yofunika: “Mulungu ndiye chikondi.” Ndiyeno, mu vesi 16 iye akugogomezera, akumati: “Mulungu ndiye chikondi, ndipo iye amene akhala m’chikondi akhala mwa Mulungu, ndipo Mulungu akhala mwa iye.” Chili chifukwa cha kukonda kwake anthu kuti Yehova akulinganiza za kuchotsa pa dziko lapansi kuipa konse. Mulungu wathu wachikondi ndi wachifundo akulengeza: “Pali Ine, . . . sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji?”—Ezekieli 33:11.
8. Kodi ndimotani mmene Yohane anagogomezera chikondi, komanso nadzisonyeza kukhala Mwana wa Bingu?
8 Yohane amatchula za a·gaʹpe, chikondi chosalolera, kaŵirikaŵiri kuposa olemba Mauthenga Abwino ena atatu ataikidwa pamodzi, komabe pa Marko 3:17, Yohane mwiniyo akufotokozedwa kukhala ‘Mwana wa Bingu.’ Kunali mwa chiuziro cha Yehova kuti Mwana wa Bingu ameneyu analemba mauthenga ovumbulutsa a buku lotsiriza la Baibulo, Chivumbulutso, limene limasonyeza Yehova monga Mulungu amene amapereka chiweruzo. Buku limeneli nlodzala ndi mawu achiweruzo, onga akuti “moponderamo mphesa mwamukulu mwa mkwiyo wa Mulungu,” “mbale zisanu ndi ziŵiri za mkwiyo wa Mulungu,” ndi “mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuyonse.”—Chivumbulutso 14:19; 16:1; 19:15.
9. Kodi Yesu ananena mawu otani ponena za ziweruzo za Yehova, ndipo kodi maulosi ake anakwaniritsidwa motani?
9 Ambuye wathu Yesu Kristu, amene ali “fanizo la Mulungu wosaonekayo,” analengeza molimba mtima ziweruzo za Yehova pamene anali pa dziko lapansi pano. (Akolose 1:15) Mwachitsanzo, pali masoka asanu ndi aŵiri a Mateyu chaputala 23 amene anawalengeza mosabisa pa achipembedzo onyenga a m’tsiku lake. Iye anatsiriza kunena chiweruzo chotsutsacho ndi mawu aŵa: “Ha, Yerusalemu, Yerusalemu, amene umapha aneneri, ndi kuwaponya miyala iwo otumidwa kwa iwe! Ine ndinafuna kangati kusonkhanitsa pamodzi ana ako, inde monga thadzi lisonkhanitsa anapiye ake m’mapiko ake, koma inu simunafuna ayi! Onani, nyumba yanu yasiyidwa kwa inu yabwinja.” Zaka 37 pambuyo pake, chiweruzo chinaperekedwa ndi gulu la nkhondo Lachiroma pansi pa Kazembe Titus. Linali tsiku lowopsa, lolosera zimene zidzachitika m’tsiku limene lidzakhaladi lochititsa mantha koposa m’kukhalapo konse kwa anthu—tsiku la Yehova, limene likudza posachedwa.
“Dzuŵa” Liŵala
10. Kodi “dzuŵa la chilungamo” limabweretsa motani chimwemwe kwa anthu a Mulungu?
10 Yehova akudziŵikitsa kuti padzakhala opulumuka patsiku lakelo. Pa Malaki 4:2 amanena kwa ameneŵa kuti: “Inu akuwopa dzina langa, dzuŵa la chilungamo lidzakutulukirani, muli kuchiritsa m’mapiko mwake.” Dzuŵa la chilungamo limenelo sililinso wina koma Yesu Kristu mwiniyo. Iye ndiye “kuunika kwa dziko lapansi” kwauzimu. (Yohane 8:12) Kodi amaŵala motani? Amaunikira mwa machiritso okhala m’mapiko mwake—choyamba machiritso auzimu, amene tili nawo ngakhale lerolino, ndiyeno, m’dziko latsopano limene likudzalo, kuchiritsa anthu a m’mitundu yonse kwakuthupi. (Mateyu 4:23; Chivumbulutso 22:1, 2) Mophiphiritsira, monga momwe Malaki ananenera, ochiritsidwawo ‘adzatuluka ndi kutumphatumpha ngati ana a ng’ombe onenepa’ otulutsidwa kumene m’khola. Ndi chimwemwe chotani nanga chimene chidzapezedwanso ndi oukitsidwa amene akuuka ali ndi chiyembekezo cha kupeza ungwiro waumunthu!
11, 12. (a) Kodi nchiyani chimene chikuyembekezera oipa? (b) Kodi ndimotani mmene anthu a Mulungu ‘adzaponderezera oipa’?
11 Komabe, bwanji ponena za oipa? Pa Malaki 4:3, timaŵerenga kuti: “Mudzapondereza oipa; pakuti adzakhala ngati mapulusa ku mapazi anu, tsiku ndidzaikalo, ati Yehova wa makamu.” Pamene kuli kwakuti adzatetezera awo amene amamkonda, Mulungu wathu Wankhondoyo adzakhala atachotseratu pa dziko lapansi adani ankhanzawo, kuwawononga. Satana ndi ziŵanda zake adzakhala atalandidwa mphamvu.—Salmo 145:20; Chivumbulutso 20:1-3.
12 Anthu a Mulungu sadzakhala ndi mbali m’kuwononga oipa. Nangano, kodi ndimotani mmene ‘adzaponderezera oipa’? Adzachita zimenezi mophiphiritsira mwa kukhala ndi phande m’chikondwerero chachipambano chachikulu. Eksodo 15:1-21 amafotokoza za chikondwerero chimenecho. Chinachitidwa pambuyo pa kuwonongedwa kwa Farao ndi magulu ake a nkhondo m’Nyanja Yofiira. Mokwaniritsa Yesaya 25:3-9, kuchotsedwa kwa “akuwopsa” kudzatsatiridwa ndi phwando lachipambano logwirizanitsidwa ndi lonjezo la Mulungu: “Iye wameza imfa ku nthaŵi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzapukuta misozi pa nkhope zonse; ndipo chitonzo cha anthu ake adzachichotsa pa dziko lonse lapansi; chifukwa Yehova wanena. Ndipo adzanena tsiku limenelo, Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu; . . . uyu ndiye Yehova, tamlindirira iye, tidzakondwa ndi kusekerera m’chipulumutso chake.” M’chikondwerero chimenechi mulibe mzimu wokonda kulipsira kapena wokondwera ndi tsoka la wina, koma chikondwerero cha kuona dzina la Yehova likuyeretsedwa ndipo dziko lapansi likuyeretsedwa kuti likhalidwe ndi anthu amtendere ndi ogwirizana.
Programu Yaikulu ya Maphunziro
13. Kodi ndi maphunziro otani amene adzachitika mu “dziko latsopano”?
13 Pa Malaki 4:4, Ayuda analangizidwa ‘kukumbukira chilamulo cha Mose.’ Chotero lerolino tifunikira kutsatira “chilamulo cha Kristu,” monga momwe chatchulidwira pa Agalatiya 6:2. Opulumuka Armagedo mosakayikira adzapatsidwa malangizo ena ozikidwa pa chilamulo chimenechi, ndipo ameneŵa angadzalembedwedi mu “mabuku” a Chivumbulutso 20:12 amene adzatsegulidwa panthaŵi ya chiukiriro. Lidzakhala tsiku laulemerero chotani nanga limenelo, pamene ouka kwa akufawo akuphunzitsidwa kutsatira moyo wa “dziko latsopano”!—Chivumbulutso 21:1.
14, 15. (a) Kodi Eliya wamakono akudziŵidwa motani? (b) Kodi ndi thayo lotani limene kagulu ka Eliya kakukwaniritsa?
14 Kumeneko kudzakhala kuwonjezeredwa kwa ntchito ya maphunziro yonenedwa ndi Yehova, monga momwe kwalembedwera pa Malaki 4:5: “Taonani, ndidzakutumizirani Eliya mneneri lisanadze tsiku lalikulu ndi lowopsa la Yehova.” Kodi ndani amene ali Eliya wamakono ameneyo? Monga momwe kwasonyezedwera pa Mateyu 16:27, 28, potchula za ‘kudza kwake mu ufumu wake’ Yesu anati: “Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake, pamodzi ndi angelo ake; ndipo pomwepo iye adzabwezera kwa anthu onse monga machitidwe awo.” Masiku asanu ndi limodzi pambuyo pake, ali paphiri ndi Petro, Yakobo, ndi Yohane, “iye anasandulika pamaso pawo; ndipo nkhope yake inaŵala monga dzuŵa, ndi zovala zake zinakhala zoyera mbuu monga kuŵala.” Kodi iye anali yekha m’masomphenya ameneŵa? Ayi, pakuti “onani, Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo, alinkulankhula ndi iye.”—Mateyu 17:2, 3.
15 Kodi zimenezi zinatanthauzanji? Zinasonyeza Yesu kukhala Mose Wamkulu woloseredwayo panthaŵi ya kudza kwake kudzapereka chiweruzo. (Deuteronomo 18:18, 19; Machitidwe 3:19-23) Pamenepo iye akagwirizana ndi Eliya wamakono kotero kuti amalize ntchito yofunika, ija ya kulalikira uthenga wabwino umenewu wa Ufumu pa dziko lonse lapansi tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova lisanakanthe. Pofotokoza ntchito ya “Eliya” ameneyu, Malaki 4:6 amati: “Adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate awo; kuti ndisafike ndi kukantha dziko liwonongeke konse.” Motero, “Eliya” ameneyu akudziŵika kukhala kagulu ka kapolo wokhulupirika ndi wanzeru ka Akristu odzozedwa ka pa dziko lapansi, kamene Mbuyeyo, Yesu, wakaikizira chuma Chake chonse. Chimenechi chimaphatikizapo kugaŵira banja la chikhulupiriro ‘chakudya chauzimu chofunikira panthaŵi yake.’—Mateyu 24:45, 46.
16. Kodi ndi zotukulapo zokondweretsa zotani zimene ntchito ya kagalu ka Eliya yatulutsa?
16 Lerolino padziko lonse, tikuona zotulukapo zokondweretsa za programu ya kudyetsa imeneyo. Magazini a Nsanja ya Olonda, amene amasindikizidwa 16,100,000 kope lililonse m’zinenero 120, ndipo 97 za zimenezi zikumatuluka pamodzi ndi Chingelezi, akudzaza dziko lonse lapansi ndi “uthenga uwu wabwino wa ufumu.” (Mateyu 24:14) Zofalitsidwa zina m’zinenero zambiri zikugwiritsiridwa ntchito m’mbali zosiyanasiyana za ntchito yolalikira ndi kuphunzitsa ya Mboni za Yehova. Kagulu ka Eliya, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, kali maso kuti kagaŵire mowoloŵa manja kwa onse amene “ali osauka mumzimu.” (Mateyu 5:3) Ndiponso, awo amene amalandira chiyembekezo cha Ufumu chimenechi ndi kuchitapo kanthu amaloŵa mu umodzi wolimba wabwino kwambiri wa padziko lonse. Umaphatikizapo khamu lalikulu ‘lochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ (Chivumbulutso 7:9) Pamene ntchito imeneyi ichitidwa kufikira pa mlingo umene Yehova akufuna, pamenepo mapeto adzafika patsiku lake lalikulu ndi lochititsa manthalo.
17. Kodi tsiku lochititsa mantha la Yehova limenelo lidzadza liti?
17 Kodi ndi liti kwenikweni pamene tsiku lochititsa mantha limenelo lidzadza mwadzidzidzi? Mtumwi Paulo akuyankha: “Tsiku la [Yehova, NW] lidzadza monga mbala usiku. Pamene angonena [mwinamwake m’njira yapadera], Mtendere ndi [chisungiko, NW], pamenepo chiwonongeko chobukapo chidzawagwera, monga zoŵaŵa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.”—1 Atesalonika 5:2, 3.
18, 19. (a) Kodi ndimotani mmene “mtendere ndi chisungiko” zikulengezedwera? (b) Kodi anthu a Yehova adzapeza mpumulo liti?
18 Kodi ndani amene “angonena” amenewo mu ulosi umenewu? Iwowo ndiwo atsogoleri andale amene amanena kuti angathe kumanga dongosolo latsopano logwirizana ndi mbali zoswekasweka za dziko lachiwawali. Magulu aakuluwo amene iwo apanga, League of Nations ndi United Nations, alephera kuchita zimenezi. Monga momwe mneneri wa Yehova analoserera, tsopano iwo ‘akunenadi kuti, Mtendere, mtendere; koma palibe mtendere.’—Yeremiya 6:14; 8:11; 14:13-16.
19 Pakali pano, anthu a Yehova amapirira ndi mavuto ndi zizunzo za dziko losapembedzali. Koma posachedwapa, monga momwe kwanenedwera pa 2 Atesalonika 1:7, 8, adzapeza mpumulo “pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera uthenga wabwino wa Ambuye wathu Yesu.”
20. (a) Kodi Zefaniya ndi Habakuku amaloseranji ponena za tsiku “lotentha ngati ng’anjo”? (b) Kodi ndi uphungu wotani ndi chilimbikitso chimene maulosi ameneŵa amapereka?
20 Kodi zimenezo zidzakhalako posachedwapa liti? Ambiri a ife takhala tikuyembekezera kwa nthaŵi yaitali. Pakali pano, ofatsa ambiri amene adzapulumuka akulabadira pempho lopezeka pa Zefaniya 2:2, 3: “Funani Yehova, . . . funani chilungumo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.” Ndiyeno, Zefaniya 3:8 ali ndi chilimbikitso ichi: “Chifukwa chake, mundilindire, ati Yehova, kufikira tsiku loukira ine zofunkha; pakuti ndatsimikiza mtima ine kusonkhanitsa amitundu, kuti ndimemeze maufumu kuwatsanulira kulunda kwanga, ndilo mkwiyo wanga wonse waukali; pakuti dziko lonse lapansi lidzathedwa ndi moto wa nsanje yanga.” Mapeto ali pafupi! Yehova akudziŵa za tsiku limenelo ndi ola ndipo sadzasintha nthaŵi yake. Tiyenitu tipirire modekha. “Pakuti masomphenyawo alindira nyengo yoikidwiratu, ndipo afulumira potsirizira pake, osanama; akachedwa uwalindirire; popeza afika ndithu, osazengereza.” (Habakuku 2:3) Tsiku lochititsa manthalo la Yehova likuyandikira mofulumira nthaŵi zonse. Kumbukirani kuti, tsikulo silidzachedwa!
Mwa Kubwereza:
◻ Kodi ndimotani mmene zinthu zidzayendera kwa olamulira ndi olamuliridwa pa tsiku lochititsa mantha la Yehova?
◻ Kodi Yehova ndi Mulungu wotani?
◻ Kodi ndi maphunziro otani a anthu a Mulungu amene akufotokozedwa?
◻ Kodi aneneri a Mulungu amatilimbikitsa motani polingalira za kuyandikira kwa mapeto?
[Chithunzi patsamba 21]
M’nthaŵi ya bwalo la Spanish Inquisition ambiri anaumirizidwa kutembenukira ku Chikatolika
[Mawu a Chithunzi]
The Complete Encyclopedia of Illustration/J. G. Heck