Phiri Limene “Limayenda”
KUMADZULO kwa Ireland, phiri lokongola mochititsa chidwi la Croagh Patrick limaonekera pamwamba pa mapiri ena olizinga. Chaka chilichonse, pa Sande yomaliza ya July, nsonga ya phirilo imaoneka ngati ikuyenda pamene anthu ngati 30,000, achichepere ndi achikulire omwe, akwera kupita pamwambapo (mamita 765) paulendo wopatulika wa pachaka.
Tsikulo, apaulendowo amakwera ndi kutsika pakanjira kopapatiza, kamakolokoto, ndi kowopsa m’malo ena. Ndipotu, mbali yomaliza pokwera (ya mamita ngati 300) ili yocholima kwambiri ndipo miyala yake yambiri njosagwira, ikumachititsa ngozi ndi kutopetsa pokwera.
Ena amakwera alibe nsapato, ndipo oŵerengeka amakwera mbali zina chokwaŵa. Kale, ulendowo unali kuyamba usiku.
Kodi nchifukwa ninji ambiri amaona kukwera phiri la Croagh Patrick kukhala chinthu chofunika kwambiri?
Malo Opatulika Akalekale
Kuchiyambi kwa zaka za zana lachisanu C.E., Tchalitchi cha Roma Katolika chinatuma Patrick kukhala bishopu wachimishonale ku Ireland. Cholinga chake chachikulu chinali kutembenuza Aairishi kukhala Akristu, ndipo m’zaka za kulalikira kwake ndi kugwira ntchito pakati pa anthuwo, Patrick akunenedwa kuti anayala maziko a Tchalitchi cha Katolika komweko.
Ntchito yake inamfikitsa kumalo osiyanasiyana m’dzikolo. Ena a malowo anali kumadzulo kwa Ireland, kumene malinga ndi kunena kwa ena, anakhala masiku 40 usana ndi usiku pamwamba pa phiri limene linadzatchedwa ndi dzina lake—Croagh Patrick (kutanthauza “Phiri la Patrick”). Ali pompo iye anasala kudya napempherera kukwaniritsika kwa ntchito yake.
M’kupita kwa zaka pakhala nthano zambiri ponena za zochita zake. Ina yotchuka koposa njakuti pamene Patrick anali paphiripo, anapitikitsa njoka zonse m’Ireland.
Anthu amakhulupirira kuti iye anamanga katchalitchi pansonga ya phirilo. Ngakhale kuti chimangocho pakhala palibe kwa nthaŵi yaitali, maziko ake oyamba adakalipo, ndipo malowo limodzi ndi phirilo akhala malo opitako opatulika zaka zonsezi.
Mbali za Ulendo Wopatulika
Kwa munthu wokalamba kapena amene sanazoloŵere kukwera mapiri, kungomaliza ulendo wokwera phirilo wa makilomita asanu ndi kutsika bwinobwino kulidi kuchita zazikulu.
M’malo owopsa a m’kanjiramo, m’makhala timagulu ta anthu okonzekera kusamalira anthu ovulala mosiyanasiyana.
Pali malo atatu, kapena moima, m’kanjiramo pamene apaulendowo amachita madzoma osiyanasiyana osonyeza kulapa. Zimenezo nzofotokozedwa bwino lomwe panotisibodi imene ili poyambira kukwera.—Onani bokosi.
Kodi Amalikwereranji?
Kodi nchifukwa ninji ambiri amapita paulendo wopatulika wotopetsa umenewu? Kodi nchifukwa ninji ena amadzivutitsa kwambiri motero pokwera?
Eya, ena amakhulupirira kuti mwa kupemphera pamene ali paulendowo, kuthekera kwakuti mapindu aumwini omwe amapempha adzamvedwa kumakula kwambiri. Ena amachita zimenezo kuti akhululukidwe zolakwa zawo zakutizakuti. Ena, ndi mmene amasonyezera chiyamikiro. Inde, ambiri amangokonda kucheza kumene kumakhalako. Mkulu wina wa boma ananena kuti ndiko ‘njira yosonyezera mzimu wa kugwirizana kwa anthu ndi kukondana kwawo.’ Ananenanso kuti kukwera phiri la Croagh Patrick “ndiko njira yawo yotsatira m’mapazi a St. Patrick ndi yosonyezera kudzimva kwawo a mangawa kwa iye kaamba ka chikhulupiriro chawo.” Anawonjezera kuti, makamaka, kukwera phiriko kuli “kudzilanga kwa mtundu wina chifukwa chakuti kutopa kumene kumakhalapo kulidi mchitidwe wosonyeza kulapa. Kukwera pang’onopang’ono kukafika pamwamba ndiko kusonyeza chisoni kwa nthaŵi yaitali.”
Mwamuna wina monyada ananena kuti anakwera phirilo nthaŵi 25! Iye anati anachita zimenezo “kuti adzilange pang’ono!” Mwamuna wina anangoti, “Ngati suvutikapo sungapeze zabwino!”
Ngakhale kuti si lamulo kukwera phiri popanda nsapato, ambiri amatero. Chifukwa ninji? Choyamba, amayesa nthakayo kukhala “yopatulika” choncho amavula nsapato zawozo. Chachiŵiri, zimenezo zimagwirizana ndi cholinga chawo cha ‘kudzilanga pang’ono.’ Nchifukwa chakenso ena amachita madzoma pamalo oimapo atagwada.
Tisonkhezereka Kuyamikira Mlengi
Nanga bwanji ngati wina sali ndi zikhulupiriro zofanana ndi za apaulendowo amene amakwera phirilo patsiku lapadera? Ngati kunja kwacha bwino ndipo muli ndi nsapato zolimba, phirilo mungalikwere panthaŵi ina iliyonse. Ife tinalikwera panthaŵi ina osati patsiku limene khamu lomayenda la apaulendo wopatulika linali kukwera. Pa kupuma kumene tinachita kaŵirikaŵiri, tinasinkhasinkha kukwerako ndi zimene kunachititsa anthu ambiri. Polingalira za apaulendo wopatulika zikwizikwi amene amakwera phiri lotopetsa limeneli ndi kuchita madzoma osiyanasiyana osonyeza kulapa, tinakakamizika kuganiza kuti, ‘Kodi izi nzimene Mulungu amafuna? Kodi dzoma la kukwera phiri kapena kuzungulira zifanizo zina pamene munthu akupemphera mobwerezabwereza kumamyandikitsadi kwa Mulungu?’ Bwanji nanga za uphungu wa Yesu ponena za mapemphero obwerezabwereza pa Mateyu 6:6, 7?
Inde, kukwera kwathu phirilo sikunali chifukwa cha chipembedzo. Chikhalirechobe, tinamva kukhala pafupi kwambiri ndi Mlengi wathu chifukwa chakuti tinakhoza kumvetsetsa chilengedwe chake, pakuti mapiri alionse ali mbali ya zodabwitsa za pa dziko lapansi. Tili pansonga pa phirilo tinakhoza kuona bwino lomwe malo okongolawo, ngakhale kuona gombe la Atlantic Ocean. Tizisumbu tobiriŵira m’chigwegwe chapansipo kumbali inayo tinaoneka tosiyana kwambiri ndi dera la mapiri amiyala ndi osamela kanthu kumbali inayo.
Tinalingalira za malo atatu oimapo. Tinakumbukira mawu a Yesu mwiniyo, pamene anauza otsatira ake enieni: “Popemphera musabwerezebwereze chabe iyayi, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhulalankhula kwawo.”—Mateyu 6:7.
Tinaona kuti phirilo linakhala mbali ya mwambo umene wamanga anthu zikwizikwi m’dzoma losautsa. Tinalingalira mmene zimenezo zilili zosiyana ndi ufulu wotchulidwa ndi mtumwi Yohane pamene anati: “Tisunge malamulo [a Mulungu]: ndipo malamulo ake sali olemetsa.”—1 Yohane 5:3.
Tinakondwa ndi kucheza kwathu, kuphatikizapo kukwera phiri la Croagh Patrick. Kunatisonkhezera kuyang’ana kutsogolo ku nthaŵi pamene anthu onse adzamasuka ku miyambo yotsutsa Baibulo ndi kulambira Mlengi wachikondi wa dziko lapansi “mumzimu ndi m’choonadi.”—Yohane 4:24.
[Bokosi patsamba 27]
Mbali Zazikulu za Ulendo Wopatulika
Wapaulendo wopatulika aliyense amene akwera phirilo pa St. Patrick’s Day kapena m’masiku asanu ndi atatu a chochitikacho, kapena panthaŵi ina iliyonse m’mwezi wa June, July, August ndi September, ndi KUPEMPHERERA dalitso la Papa M’TCHALITCHI KAPENA CHAPAFUPIPO angapeze chikhululukiro malinga ngati apita Kukaulula Machimo ndi kupita Kumisa pansonga ya phiri kapena mkati mwa mlungu.
MALO OIMAPO AMWAMBO
Pali “malo oimapo” atatu (1) Mmunsi mwa phirilo kapena Leacht Benain, (2) Pansonga ya phiri, (3) Roilig Muire, cha ku mbali ya ku Lecanvey [tauni] ya phirilo.
Malo Oimapo Oyamba - LEACHT BENAIN
Wapaulendo amazungulira mulu wa miyala kasanu ndi kaŵiri akumapereka mapemphero 7 a Atate Wathu, 7 a Tikuoneni Mariya ndi Mawu a Atumwi kamodzi.
Malo Oimapo Achiŵiri - PANSONGA YA PHIRI
(a) Wapaulendoyo amagwada ndi kupereka mapemphero 7 a Atate Wathu, 7 a Tikuoneni Mariya ndi limodzi la Mawu a Atumwi
(b) Wapaulendoyo amapemphera pafupi ndi Tchalitchi kupempherera dalitso la Papa
(c) Wapaulendoyo amazungulira Tchalitchi nthaŵi 15 akumapereka mapemphero 15 a Atate Wathu, 15 a Tikuoneni Mariya ndi limodzi la Mawu a Atumwi
(d) Wapaulendoyo amazungulira Leaba Phadraig [Kama wa Patrick] nthaŵi 7 akumapereka mapemphero 7 a Atate Wathu, 7 a Tikuoneni Mariya ndi limodzi la Mawu a Atumwi
Malo Oimapo Achitatu - ROILIG MUIRE
Wapaulendoyo amazungulira mulu uliwonse wa miyala nthaŵi 7 akumapereka mapemphero 7 a Atate Wathu, 7 a Tikuoneni Mariya ndi limodzi la Mawu a Atumwi [pali miyulu itatu] ndipo pomaliza amazungulira mpanda wonse wa Roilig Muire nthaŵi 7 akumapemphera.