MUTU 24
Palibe Chimene ‘Chingatisiyanitse ndi Chikondi cha Mulungu’
1. Kodi ndi maganizo ofooketsa ati omwe anthu ambiri, ngakhalenso Akhristu ena oona, amavutika nawo?
KODI Yehova Mulungu amakukondani inuyo panokha? Ena amavomereza kuti Mulungu amakonda anthu onse mogwirizana ndi zimene lemba la Yohane 3:16 limanena. Komabe amaganiza kuti: ‘Mulungu sangandikonde ineyo pandekha.’ Ngakhalenso Akhristu oona nthawi zina amamva choncho. Bambo wina atakumana ndi mavuto anati: “Zikundivuta kwambiri kukhulupirira kuti ineyo Mulungu amandiganizira.” Kodi inunso mumaona choncho nthawi zina?
2, 3. Kodi ndi ndani amafuna kuti tizikhulupirira kuti Yehova amationa kuti ndife osafunika kapenanso sangatikonde, nanga tingathetse bwanji maganizo amenewa?
2 Satana amafunitsitsa kuti tizikhulupirira kuti Yehova Mulungu satikonda ndiponso sationa ngati ofunika. N’zoona kuti nthawi zambiri Satana amapusitsa anthu powachititsa kukhala odzikuza komanso onyada. (2 Akorinto 11:3) Komabe amasangalala kuchititsa anthu kuti azidziona kuti ndi osafunika. (Yohane 7:47-49; 8:13, 44) Satana amagwiritsa ntchito kwambiri bodza limeneli makamaka ‘m’masiku otsiriza’ ovuta ano. Anthu ambiri anakulira m’mabanja omwe anthu ake ‘sakonda achibale awo.’ Anthu ena tsiku lililonse amakumana ndi anthu oopsa, odzikonda komanso omva zawo zokha. (2 Timoteyo 3:1-5) Chifukwa choti kwa zaka zambiri ena akhala akuwachitira nkhanza, kuwasala komanso kudana nawo, anthu oterowo angafike pokhulupirira kuti ndi osafunika komanso palibe angawakonde.
3 Ngati nanunso nthawi zina mumavutika ndi maganizo oterewa, musataye mtima. Ambirife nthawi zina sitimadziona moyenera. Koma muzikumbukira kuti Mawu a Mulungu analembedwa kuti ‘azikonza zinthu’ komanso “kugwetsa zinthu zozikika molimba.” (2 Timoteyo 3:16; 2 Akorinto 10:4) Baibulo limati: “Tidzatsimikizira mitima yathu kuti Mulungu sakutiimba mlandu pa chilichonse chimene mitima yathu ingatitsutse, chifukwa Mulungu ndi wamkulu kuposa mitima yathu ndipo amadziwa zonse.” (1 Yohane 3:19, 20) Tiyeni tione zinthu 4 zimene Malemba amanena zomwe zimatithandiza ‘kutsimikizira mitima yathu’ kuti Yehova amatikonda.
Yehova Amakuonani Kuti Ndinu Wofunika
4, 5. Kodi fanizo la Yesu la mpheta limasonyeza bwanji kuti Yehova amationa kuti ndife ofunika kwambiri?
4 Choyamba, Baibulo limaphunzitsa kuti Mulungu amaona kuti mtumiki wake aliyense ndi wofunika. Mwachitsanzo, Yesu ananena kuti: “Mpheta ziwiri amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu, si choncho? Koma palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. Ndipotu ngakhale tsitsi lonse lam’mutu mwanu amaliwerenga. Choncho musachite mantha, ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.” (Mateyu 10:29-31) Kodi anthu omwe ankamvetsera mawu amenewa anamva bwanji?
5 Mwina mungadabwe kuti munthu ankagula mpheta chifukwa chiyani. N’chifukwa choti m’nthawi ya Yesu, mpheta inali mbalame yotchipa kwambiri yomwe anthu ankagula kuti akadye. Mutha kuona kuti munthu ankagula mpheta ziwiri ndi kakhobidi kamodzi. Koma pa nthawi ina Yesu anati munthu akapereka timakobidi tiwiri ankamupatsa mpheta 5 osati 4. Mbalame inayo ankangomupatsa ngati ya pulaizi. Mwina mbalamezi anthu ankaziona kuti ndi zosafunika kwenikweni, koma kodi Yehova ankaziona bwanji? Yesu anati: “Palibe ngakhale imodzi mwa mbalame zimenezi [ngakhalenso yapulaiziyo] imene Mulungu amaiiwala.” (Luka 12:6, 7) Tsopano tingayambe kumvetsa mfundo ya Yesu. Ngati Yehova amaona kuti mpheta ndi yofunika kwambiri, ndiye kuli bwanji munthu? Mogwirizana ndi zimene Yesu ananena, Yehova amadziwa chilichonse chokhudza ifeyo. Amadziwa ngakhalenso kuchuluka kwa tsitsi lam’mutu mwathu.
6. N’chifukwa chiyani sitikayikira kuti Yesu ankafotokoza zoona pomwe ananena kuti Mulungu amadziwa kuchuluka kwa tsitsi lathu?
6 Ena angakayikire kuti zimene Yesu ananena zoti Mulungu amadziwa kuchuluka kwa tsitsi lathu si zoona. Komabe, taganizirani za chiyembekezo chakuti akufa adzauka. Yehova ayenera kuti amatidziwa bwino kwambiri kuti adzathe kutilenganso. Amationa kuti ndife ofunika kwambiri moti amakumbukira chilichonse chokhudza ifeyo, kuphatikizapo malangizo omwe ali m’maselo a m’thupi mwathu, zonse zomwe timakumbukira komanso zimene zakhala zikutichitikira pa moyo wathu.a Choncho Yehova sizingamuvute kudziwa kuchuluka kwa tsitsi lathu, lomwe m’mitu ya anthu ambiri limangokwana pafupifupi 100,000.
N’chifukwa Chiyani Yehova Amationa Kuti Ndife Ofunika?
7, 8. (a) Kodi ndi makhalidwe ena ati amene Yehova amasangalala akawapeza pamene akufufuza mitima ya anthu? (b) Kodi ndi zinthu zina ziti zomwe timachita zimene Yehova amaona kuti ndi zamtengo wapatali?
7 Chachiwiri, Baibulo limatiuza chifukwa chake Yehova amaona kuti atumiki ake ndi ofunika. Mwachidule, iye amasangalala ndi makhalidwe athu abwino ndiponso khama lathu pomutumikira. Mfumu Davide anauza mwana wake Solomo kuti: “Yehova amafufuza mitima yonse ndipo amazindikira maganizo a munthu ndi zolinga zake zonse.” (1 Mbiri 28:9) Mulungu akamafufuza mitima ya anthu mabiliyoni m’dzikoli, lomwe anthu ambiri ndi achiwawa komanso amadana, ayenera kuti amasangalala kwambiri akapeza munthu wa mtima wokonda mtendere, choonadi ndiponso chilungamo. Kodi Mulungu amatani akapeza munthu amene amamukonda, yemwe akufuna kuphunzira za iye komanso kuuza ena zomwe akuphunzirazo? Yehova amatiuza kuti amachita chidwi ndi anthu omwe amauza ena zokhudza iyeyo. Moti ali ndi “buku la chikumbutso,” lonena za anthu onse ‘oopa Yehova ndiponso amene amaganizira za dzina lake.’ (Malaki 3:16) Iye amaona kuti zimene anthuwa amachita, ndi zamtengo wapatali.
8 Kodi zinthu zina zimene Yehova amaziona kuti ndi zamtengo wapatali ndi ziti? Zimene timachita poyesetsa kutsanzira Mwana wake Yesu Khristu. (1 Petulo 2:21) Mulungu amaonanso kuti ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wake ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Pa Aroma 10:15, timawerenga kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwambiri.” Nthawi zambiri sitiganiza zoti mapazi ndi okongola. Koma palembali akuimira khama limene atumiki a Yehova amachita polalikira uthenga wabwino. Yehova amaona kuti zonse zomwe atumiki ake amachitazi ndi zokongola komanso zamtengo wapatali.—Mateyu 24:14; 28:19, 20.
9, 10. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Yehova amayamikira tikamapirira pamene tikukumana ndi mavuto osiyanasiyana? (b) Kodi Yehova sachita chiyani akamafufuza mitima ya atumiki ake okhulupirika?
9 Yehova amayamikiranso tikamapirira. (Mateyu 24:13) Kumbukirani kuti Satana amafuna kuti tisiye kutumikira Yehova. Tsiku lililonse limene takhulupirika kwa Yehova, timakhala kuti tasonyeza nawo kuti Satana ndi wabodza. (Miyambo 27:11) Komatu nthawi zina kupirira kumakhala kovuta kwambiri. Tsiku lililonse tingamavutike ndi matenda, mavuto azachuma, nkhawa ndiponso mavuto ena. Tikhozanso kukhumudwa chifukwa choti zimene timayembekezera sizikuchitika. (Miyambo 13:12) Tikamapirira mavuto amenewa, Yehova amaona kuti ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. N’chifukwa chake Mfumu Davide anapempha Yehova kuti amusungire misozi yake ‘m’thumba lachikopa’ ndipo ankakhulupirira kuti Yehovayo analemba misoziyo “m’buku” lake. (Salimo 56:8) Choncho Yehova amaona kuti misozi yathu ndi yamtengo wapatali ndipo amaikumbukira. Amakumbukiranso tikamapirira mavuto kuti tikhalebe okhulupirika kwa iye. Misoziyo ndiponso kupirirako amaziona kuti ndi zamtengo wapatali.
Yehova amayamikira tikamapirira pamene tikukumana ndi mayesero
10 Koma mtima wathu ukhoza kumatsutsabe mfundo yakuti Mulungu amationa kuti ndife ofunika. Tikhoza kumaganiza kuti: ‘Pali anthu ambiri abwino kuposa ineyo. Yehova ayenera kuti amakhumudwa kwambiri akandiyerekezera ndi amenewo.’ Komatu Yehova satiyerekezera ndi ena ndiponso sayembekezera kuti tizichita zomwe sitingakwanitse. (Agalatiya 6:4) Amafufuza mosamala zimene zili m’mitima mwathu ndipo amayamikira zabwino zilizonse zimene wapeza, ngakhale zitakhala zochepa.
Yehova Amafufuza Zabwino pa Zoipa
11. Kodi nkhani ya Abiya ikutiphunzitsa chiyani za Yehova?
11 Chachitatu, Yehova amatifufuza mosamala kwambiri kuti apeze zabwino mwa ife. Mwachitsanzo, atalamula kuti anthu onse a m’banja la Mfumu Yerobowamu omwe anali ampatuko aphedwe, analamulanso kuti mwana mmodzi wa mfumuyo dzina lake Abiya aikidwe m’manda m’njira yolemekezeka. N’chifukwa chiyani anatero? Chifukwa chakuti ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli anapeza chinachake chabwino mwa yekhayu.’ (1 Mafumu 14:1, 10-13) Tinganene kuti Yehova anafufuza mosamala mumtima mwa mnyamatayo n’kupezamo “chinachake chabwino.” Kaya chabwinocho chinali chochepa bwanji, Yehova anaonabe kuti chinali choyenera kuchitchula m’Mawu ake. Ndiponso iye anapereka mphoto kwa Abiya pomusonyeza chifundo n’kulola kuti aikidwe m’manda mwaulemu.
12, 13. (a) Kodi nkhani ya Mfumu Yehosafati imasonyeza bwanji kuti Yehova amafufuza zabwino zimene timachita ngakhale pamene tachimwa? (b) Kodi Yehova amaona bwanji makhalidwe athu abwino komanso zabwino zimene timachita?
12 Chitsanzo chinanso chabwino kwambiri tingachione munkhani ya Yehosafati yemwe anali mfumu yabwino. Mfumuyi itachita zinthu zopanda nzeru, mneneri wa Yehova anaiuza kuti: “Chifukwa cha zimenezi Yehova wakukwiyirani.” Umenewutu unali uthenga wochititsa mantha. Komatu uthenga wa Yehovawu sunathere pomwepo. Mneneriyu ananenanso kuti: “Komabe, pali zinthu zabwino zimene zapezeka mwa inu.” (2 Mbiri 19:1-3) Ngakhale kuti Yehova anakwiyira Yehosafati, zimenezi sizinamulepheretse kuona zabwino zimene Yehosafatiyo anachita. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi zimene anthu omwe si angwirofe timachita. Anthu ena akatikhumudwitsa, tingalephere kuona zabwino zomwe amachita. Ndipo tikachita tchimo tingakhumudwe, kuchita manyazi ndiponso kudziimba mlandu moti tingalephere kuona zabwino zimene timachita. Komabe tizikumbukira kuti tikalapa machimo athu n’kuyesetsa kuti tisawabwerezenso, Yehova amatikhululukira.
13 Yehova akamatifufuza, amataya machimowo ngati mmene munthu wofufuza golide amatayira zinthu zosafunika n’kusunga miyala yagolide yokhayokha. Ndi mmenenso Yehova amaonera makhalidwe athu abwino komanso zabwino zimene timachita. Makolo ena amakonda kwambiri zithunzi zimene ana awo anajambula kapena zinthu zina zomwe ankapanga kusukulu moti amazisunga kwa zaka zambiri ngakhale anawo ataziiwala. Yehova ndi Kholo lachikondi kwambiri. Tikamapitiriza kukhala okhulupirika kwa iye, saiwala zabwino zomwe timachita ndiponso makhalidwe athu abwino. Kuchita zimenezi angakuone kuti n’kupanda chilungamo chifukwa iye ndi Mulungu wachilungamo. (Aheberi 6:10) Koma Yehova amatifufuzanso m’njira ina.
14, 15. (a) N’chifukwa chiyani zimene timalakwitsa sizilepheretsa Yehova kuona zinthu zabwino zimene timachita? Perekani chitsanzo. (b) Kodi Yehova amachita chiyani akaona kuti tili ndi makhalidwe abwino, nanga anthu ake okhulupirika amawaona bwanji?
14 Yehova amaona zambiri kuposa zimene timalakwitsa ndipo amadziwa kuti tikhoza kukhala anthu abwino kwambiri. Taganizirani izi: Anthu amene amakonda zojambulajambula amayesetsa ndi mtima wonse kukonza zithunzi zomwe zawonongeka kwambiri. Mwachitsanzo, munthu wina yemwe anali ndi mfuti anawononga chithunzi cha ndalama pafupifupi madola 30 miliyoni. Chithunzichi chinajambulidwa ndi Leonardo da Vinci, ndipo chinali m’nyumba yosungiramo zithunzi ku London. Komabe zimenezi zitachitika, palibe amene ananena kuti chithunzicho akangochitaya chifukwa chawonongedwa. Nthawi yomweyo ntchito yokonzanso chithunzi chojambulidwa mwalusochi, chomwe chakhalapo kwa zaka pafupifupi 500 inayambika. N’chifukwa chiyani sanangochitaya? Chifukwa chakuti anthu okonda zojambulajambula ankachiona kuti n’chamtengo wapatali. Komatu inuyo ndi wofunika kwambiri kuposa chithunzi chongojambula. Ndinu wamtengo wapatali kwa Mulungu, ngakhale kuti nthawi zina chifukwa cha uchimo womwe tonsefe timabadwa nawo, mungamadzione kuti ndinu wosafunika. (Salimo 72:12-14) Yehova Mulungu, yemwe analenga anthu mwaluso, adzachita zonse zofunika kuti athetse mavuto obwera chifukwa cha uchimo ndipo adzathandiza anthu onse amene amamukonda komanso kumumvera kuti akhale angwiro.—Machitidwe 3:21; Aroma 8:20-22.
15 Yehova amaona makhalidwe abwino amene tili nawo omwe ifeyo sitingawaone. Ndipo pamene tikumutumikira, amatithandiza kuti tizisonyeza kwambiri makhalidwewo mpaka pamene tidzakhale angwiro. Kaya dziko la Satanali latichitira zoipa zotani, Yehova amaona kuti atumiki ake okhulupirika ndi amtengo wapatali.—Hagai 2:7.
Yehova Amachita Zinthu Zosonyeza Kuti Amatikonda
16. Kodi umboni waukulu kwambiri wosonyeza kuti Yehova amatikonda ndi uti, nanga timadziwa bwanji kuti mphatso imeneyi inaperekedwa kwa aliyense payekha?
16 Cha 4, Yehova amachita zambiri posonyeza kuti amatikonda. Zimene anachita popereka Mwana wake kuti atifere ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Satana ndi wabodza akamanena kuti ndife anthu osafunika. Tisamaiwale kuti pamene Yesu anafa mozunzika pamtengo wozunzikirapo ndiponso pamene Yehova anapirira ululu waukulu kwambiri poona Mwana wake yemwe amamukonda akufa, ndi umboni wosonyeza kuti awiriwa amatikonda. N’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri amalephera kukhulupirira kuti mphatso imeneyi inaperekedwa kwa iwowo pawokha. Amadziona kuti ndi osayenera kupatsidwa mphatsoyi. Kumbukirani kuti mtumwi Paulo ankapha otsatira a Khristu. Komabe iye analemba kuti: “Mwana wa Mulungu . . . anandikonda n’kudzipereka yekha chifukwa cha ine.”—Agalatiya 1:13; 2:20.
17. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito chiyani kuti atikokere kwa iyeyo ndi Mwana wake?
17 Yehova amatitsimikizira kuti amatikonda pothandiza aliyense payekha kuti apindule ndi nsembe ya Khristu. Yesu anati: “Palibe munthu amene angabwere kwa ine pokhapokha Atate amene anandituma atamukoka.” (Yohane 6:44) Yehova ndi amene amatikokera kwa Mwana wake ndiponso kutipatsa chiyembekezo cha moyo wosatha. Kodi amachita bwanji zimenezi? Kudzera mu ntchito yolalikira, iye anaonetsetsa kuti taphunzira choonadi. Amagwiritsanso ntchito mzimu wake woyera potithandiza kumvetsa mfundo za m’Baibulo n’kumazigwiritsa ntchito ngakhale kuti si ife wangwiro. Choncho ponena za ife, Yehova akhoza kulankhulanso zomwe ananena zokhudza Aisiraeli kuti: “Ine ndakukonda ndipo ndidzakukonda mpaka kalekale. N’chifukwa chake ndakukokera kwa ine ndi chikondi chokhulupirika.”—Yeremiya 31:3.
18, 19. (a) Kodi njira yaikulu imene Yehova amatisonyezera chikondi ndi iti, ndipo n’chiyani chikusonyeza kuti udindo umenewu sanaupereke kwa aliyense? (b) Kodi Baibulo limatitsimikizira bwanji kuti Yehova amamvetsera ndipo amamva chisoni?
18 Yehova amatipatsa mwayi woti tizipemphera kwa iye ndipo mwina imeneyi ndi njira yaikulu imene amasonyezera chikondi kwa munthu aliyense payekha. Baibulo limauza aliyense payekhapayekha kuti ‘azipemphera’ kwa Mulungu nthawi zonse. (1 Atesalonika 5:17) Iye amamvetsera. Ndipotu amatchulidwa kuti “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Udindo umenewu sanaupereke kwa wina aliyense, ngakhalenso Mwana wake. Tangoganizani: Mlengi wa chilengedwe chonse amatilimbikitsa kuti tizilankhula naye momasuka m’pemphero. Ndiye tikamapemphera, kodi iye amangotimvetsera koma osakhudzika ndi zomwe zikutichitikira? Ayi ndithu.
19 Yehova amamva chisoni. Kodi kumvera munthu chisoni n’kutani? Mkhristu wina wachikulire ndiponso wokhulupirika anati: “Kumvera munthu chisoni kumatanthauza kumva ululu wake mumtima mwanga.” Kodi Yehova zimamukhudza tikamavutika? Taonani mmene anamvera pamene anthu ake Aisiraeli ankavutika. Baibulo limati: “Pa nthawi yonse imene iwo ankavutika, iye ankavutikanso.” (Yesaya 63:9) Yehova sankangoona anthuwo akuvutika koma ankawamveranso chisoni. Posonyeza kuti amamvera chisoni kwambiri atumiki ake, iye anati: “Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.”b (Zekariya 2:8) Zimenezitu zingakhale zopweteka kwambiri. Zoonadi, Yehova amatimvera chisoni. Tikamamva kuwawa, nayenso amamva kuwawa.
20. Kodi ndi maganizo olakwika ati amene tiyenera kupewa kuti tizitsatira malangizo apalemba la Aroma 12:3?
20 Palibe Mkhristu aliyense woganiza bwino amene angamadzikuze kapena kudziona kuti ndi wofunika kuposa ena chifukwa chodziwa kuti Mulungu amamukonda komanso amamuona kuti ndi wofunika. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anandisonyeza, ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira. Koma aliyense aziganiza mwanzeru n’kumadziweruza mogwirizana ndi chikhulupiriro chimene Mulungu wamupatsa. (Aroma 12:3) Baibulo lina limati: “Ndikuuza aliyense wa inu kuti asamadzione kuti ndi wofunika kwambiri kuposa mmene alili, koma azidziona moyenera.” (A Translation in the Language of the People, by Charles B. Williams) Choncho tikamasangalala kuti Atate wathu wakumwamba amatikonda, tiyeni tizikhala oganiza bwino n’kumakumbukira kuti sikuti Mulungu amatikonda ngati malipiro a zimene timachita koma chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.—Luka 17:10.
21. Kodi ndi mabodza a Satana ati amene tiyenera kuyesetsa kuti tisamawakhulupirire, nanga tizikhulupirira mfundo ya m’Baibulo iti imene Yehova amatiuza?
21 Tiyeni tizichita zonse zimene tingathe pokana kukhulupira mabodza a Satana, kuphatikizapo bodza lakuti ndife osafunika kapena palibe amene angatikonde. Ngati zimene mwakumana nazo pa moyo zachititsa kuti muzidziona kuti ndinu woipa kwambiri moti Mulungu sangakukondeni, kapena ngati mumaona kuti Mulungu saona zabwino zimene mumachita, kapenanso kuti munachita machimo oipa kwambiri moti ngakhale imfa ya Mwana wa Mulungu singawafafanize, dziwani kuti limeneli ndi bodza. Yesetsani kuti musamakhulupirire mabodza amenewa. Tiyeni tizitsimikizira mitima yathu mawu ouziridwa amene Paulo analemba akuti: “Ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera, mphamvu, msinkhu, kuzama kapena cholengedwa chilichonse, sizidzatha kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.”—Aroma 8:38, 39.
a Mobwerezabwereza Baibulo limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa chiyembekezo choti akufa adzauka ndi zimene Yehova amakumbukira. Munthu wokhulupirikayo Yobu anauza Yehova kuti: “Zikanakhala bwino mukanandiikira nthawi n’kudzandikumbukira.” (Yobu 14:13) Yesu anatchula za kuukitsidwa kwa “onse amene ali m’manda achikumbutso.” Izi zinali zoyenera chifukwa Yehova amawakumbukira bwino kwambiri akufa amene akufuna kudzawaukitsa.—Yohane 5:28, 29.
b Palembali, Mabaibulo ena anamasulira kuti munthu amene akukhudza anthu a Mulungu ndiye kuti akudzikhudza yekha diso lake kapena akukhudza diso la Aisiraeli, osati la Mulungu. Kulakwitsa kumeneku anakuyambitsa ndi anthu ena okopera Malemba amene ankaganiza kuti vesili likunyoza Mulungu. Koma maganizo awo olakwikawa anachititsa kuti mfundo yoti Yehova amachitira kwambiri chifundo anthu ake isaonekere.