“Yesu Kristu Ndiye Ambuye”—Motani Ndipo Liti?
“AMBUYE anati kwa Ambuye wanga, Khalani kudzanja langa lamanja, kufikira ndipanga adani anu choikapo mapazi anu.” Ameneŵa ali matembenuzidwe a Salmo 110:1 a King James Version. Kodi panopa ndani yemwe ali “AMBUYE” ameneyo, ndipo kodi iye akulankhula kwa yani?
Matembenuzidwe olondola kwambiri a malembo Achihebri amayankha mwamsanga funso loyambalo. “Mawu a Yehova kwa Ambuye wanga n’ngakuti: . . . ” Motero, “AMBUYE” ameneyo m’zilembo zazikulu ndiye Mulungu wamphamvuyonse, Yehova mwiniyo. Ngakhale kuti King James Version imasonyeza dzina laumulungulo mwa kugwiritsira ntchito “AMBUYE” wosiyana ndi “Ambuye,” sindiyo inali yoyamba kusokoneza maina aulemuwa, popeza kuti Septuagint Yachigiriki yakale, yotembenuzidwa kuchokera m’Chihebri, inagwiritsira ntchito “Ambuye” kaamba ka Yehova m’makope ake apambuyo. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti dzina laulemulo “Ambuye” linaloŵa m’malo mwa dzina laumulungulo, Tetragrammaton (יהוה). Katswiri wina A. E. Garvie akuti: “Kugwiritsira ntchito dzina laulemu lakuti Ambuye [kyʹri·os] mwinamwake ndipo mosavuta kunachokera m’kugwiritsira ntchito dzina laulemu limenelo m’masunagoge Achiyuda mmalo mwa dzina la chipangano lakuti Yahveh [Yehova], pamene Malemba anali kuŵerengedwa.”
Baibulo limadziŵikitsa Yehova kukhala “Ambuye [Mfumu, NW].” (Genesis 15:2, 8; Machitidwe 4:24; Chivumbulutso 6:10) Iye amatchedwanso “Ambuye [woona, NW]” ndi “Ambuye wa dziko lonse.” (Eksodo 23:17; Yoswa 3:13; Chivumbulutso 11:4) Nangano, kodi ndani amene ali “Ambuye” winayo wa pa Salmo 110:1, ndipo kodi ndimotani mmene Yehova anafikira pakumzindikira monga “Ambuye”?
Yesu Kristu Monga “Ambuye”
Yesu akutchedwa “Ambuye” m’Mauthenga Abwino anayi, kaŵirikaŵiri ndi Luka ndi Yohane. M’zaka za zana loyamba C.E., dzinalo linali limodzi la maina aulemu, lofanana ndi lakuti “Bwana.” (Yohane 12:21; 20:15, Kingdom Interlinear) Mu Uthenga Wabwino wa Marko dzina lakuti “Mphunzitsi,” kapena Raboni, limagwiritsiridwa ntchito kaŵirikaŵiri potchula Yesu. (Yerekezerani ndi Marko 10:51 ndi Luka 18:41.) Ngakhale funso la Saulo panjira ya ku Damasiko lakuti “Ndinu yani Mbuye?” linali ndi lingaliro limodzimodzili la funso laulemu. (Machitidwe 9:5) Koma pamene ophunzira a Yesu anafikira pakudziŵa Mbuyawo, n’kwachionekere kuti kagwiritsiridwe ntchito kawo ka dzina laulemulo “Ambuye” kanatanthauza zinthu zambiri koposa kungochitira ulemu.
Pambuyo pa imfa yake ndi chiukiriro koma kukwera kwake kumwamba kusanachitike, Yesu anaonekera kwa ophunzira ake ndi kunena mawu odabwitsa aŵa: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi pa dziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Ndiyeno, patsiku la Pentekoste, mouziridwa ndi mzimu woyera wotsanulidwa, Petro anagwira mawu Salmo 110:1 ndipo anati: “Pamenepo lizindikiritse ndithu banja lililonse la Israyeli, kuti Mulungu anamuyesa Ambuye ndi Kristu, Yesu amene inu munampachika.” (Machitidwe 2:34-36) Chifukwa cha kukhulupirika kwake kufikira imfa yochititsa manyazi pamtengo wozunzirapo, Yesu anaukitsidwa ndi kupatsidwa mphotho yapamwamba kwambiri. Ndiyeno analoŵa mu mkhalidwe wake wa umbuye kumwamba.
Mtumwi Paulo anachitira umboni mawu a Petro pamene analemba kuti Mulungu “[a]namkhazikitsa [Kristu] pa dzanja lake lamanja m’zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m’nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza.” (Aefeso 1:20, 21) Umbuye wa Yesu Kristu uli wapamwamba pa maumbuye ena onse, ndipo udzapitirizabe mpaka kuloŵa m’dziko latsopano. (1 Timoteo 6:15) Iye “anamkwezetsa . . . nampatsa dzina limene liposa maina onse” kotero kuti aliyense avomereze “kuti Yesu Kristu ali Ambuye, kuchitira ulemu Mulungu Atate.” (Afilipi 2:9-11) Motero mbali yoyamba ya Salmo 110:1 inakwaniritsidwa, ndipo “angelo, ndi maulamuliro” anagonjera umbuye wa Yesu.—1 Petro 3:22; Ahebri 8:1.
M’Malemba Achihebri, mawu akuti “Mbuye wa ambuye” amagwira ntchito kwa Yehova yekha. (Deuteronomo 10:17; Salmo 136:2, 3) Koma Petro mouziridwa ananena za Kristu Yesu kuti: “Ndiye Ambuye wa onse [kapena, “Ambuye wa tonsefe,” Goodspeed],” (Machitidwe 10:36) Iye ndithudi ali “Ambuye wa akufa ndi wa amoyo.” (Aroma 14:8, 9) Akristu amavomereza Yesu Kristu mosavuta kukhala Ambuye wawo ndi Mwiniwawo ndi kumumvera mofunitsitsa monga omgonjera, ogulidwa ndi mwazi wake wamtengo wapatali. Ndipo Yesu Kristu walamulira monga Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye pampingo wake chiyambire pa Pentekoste wa 33 C.E. Koma tsopano, chiyambire 1914, iye wapatsidwa mphamvu yaufumu kulamulira ali m’malo otero ataika adani ake monga ‘chopondapo mapazi ake.’ Nthaŵi yake inali itakwana tsopano ya ‘kuchita ufumu pakati pawo,’ zonsezo mokwaniritsa Salmo 110:1, 2.—Ahebri 2:5-8; Chivumbulutso 17:14; 19:16.
Nangano, kodi ndimotani mmene mawu a Yesu akuti “zinthu zonse zinaperekedwa kwa ine ndi Atate wanga,” onenedwa imfa yake ndi chiukiriro zisanachitike, ayenera kumvedwera? (Mateyu 11:25-27; Luka 10:21, 22) Aŵa si mawu oloŵetsemo zonse monga amene tafotokoza kalewo. M’buku la Mateyu ndi Luka lomwe, mawu a m’nkhaniyo amasonyeza kuti Yesu anali kulankhula za chidziŵitso chobisika kwa anthu anzeru zaudziko koma ovumbulidwa kupyolera mwa iye chifukwa chakuti “adziŵa” Atate. Pamene anabatizidwa m’madzi ndi kubadwa monga Mwana wa Mulungu wauzimu, Yesu anakhoza kukumbukira kukhalapo kwake kumwamba asanakhale munthu ndi chidziŵitso chonse chimene anali nacho, koma zimenezi zinali kanthu kena kosiyana ndi mkhalidwe wake wapambuyo pake waumbuye.—Yohane 3:34, 35.
Kusiyanitsa Yesu Kristu Monga Ambuye
Mafotokozedwa ena a Malemba Achigiriki Achikristu amapereka vuto potembenuza mawu ogwidwa m’Malemba Achihebri amene mwachionekere amatchula za “AMBUYE,” Yehova Mulungu. Mwachitsanzo, yerekezerani Luka 4:19 ndi Yesaya 61:2 mu King James Version kapena The New Jerusalem Bible. Anthu ena amaumirira pakunena kuti Yesu anadzitengera dzina laulemulo “Ambuye” kwa Yehova ndi kuti Yesu m’thupi analidi Yehova, koma chimenechi n’chitsutso chimene chili chosachirikizidwa ndi Malemba. Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, nthaŵi zonse amasiyanitsidwa kwambiri m’Malemba. Yesu anadziŵikitsa dzina la Atate wake ndipo anamuimira.—Yohane 5:36, 37.
M’zitsanzo zotsatirazi, onani mawu ogwidwa m’Malemba Achihebri monga momwe amaonekera m’Malemba Achigiriki. Yehova Mulungu ndi Wodzozedwa Wake, kapena Mesiya, onsewo amatchulidwa pa Machitidwe 4:24-27, pamene pamagwira mawu a m’Salmo 2:1, 2. Mawu a nkhani yonse pa Aroma 11:33, 34 amanena za Mulungu momvekera bwino lomwe, Magwero a nzeru yonse ndi chidziŵitso, mwa kugwira mawu pa Yesaya 40:13, 14. Polembera mpingo wa Akorinto, Paulo akubwerezanso kugwira mawu kuti, “Wadziŵa ndani mtima wa [Yehova, NW]?” ndiyeno akuwonjezera kuti, “Koma ife tili nawo mtima wa Kristu.” Ambuye Yesu anavumbulira otsatira ake za mtima wa Yehova pankhani zambiri zofunika.—1 Akorinto 2:16.
Nthaŵi zina vesi la m’Malemba Achihebri limanena za Yehova, koma chifukwa cha kupereka Kwake mphamvu ndi ulamuliro, limakwaniritsidwa mwa Yesu Kristu. Mwachitsanzo, Salmo 34:8, limatipempha ‘kulawa, ndi kuona kuti Yehova ndiye wabwino.’ Koma Petro amagwiritsira ntchito mawu ameneŵa kwa Ambuye Yesu Kristu pamene akunena kuti: “Ngati mwalaŵa kuti Ambuye ali wokoma mtima.” (1 Petro 2:3) Petro amagwiritsira ntchito lamulolo ndi kusonyeza mmene zimenezi zililinso chimodzimodzi ndi Yesu Kristu. Mwa kuloŵetsa chidziŵitso cha Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu yemwe ndi kuchitapo kanthu, Akristu akhoza kulandira madalitso aakulu kuchokera kwa Atate ndi Mwana yemwe. (Yohane 17:3) Mafotokozedwe a Petro samapangitsa Ambuye Mfumu Yehova kukhala munthu mmodzimodziyo wotchedwa Ambuye Yesu Kristu.—Onani mawu amtsinde a 1 Petro 2:3, New World Translation With References.
Malo a unansi wa Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, afotokozedwa bwino kwambiri ndi mtumwi Paulo pamene amati: “Kwa ife kuli Mulungu mmodzi, Atate amene zinthu zonse zichokera kwa iye, ndi ife kufikira kwa iye; ndi Ambuye mmodzi Yesu Kristu, amene zinthu zonse zili mwa iye, ndi ife mwa iye.” (1 Akorinto 8:6; 12:5, 6) Polembera mpingo Wachikristu ku Efeso, Paulo anadziŵikitsa “Ambuye mmodzi,” Yesu Kristu, kukhala wosiyana kwambiri ndi “Mulungu mmodzi ndi Atate wa onse.”—Aefeso 4:5, 6.
Yehova Wapamwamba pa Onse
Chiyambire chaka cha 1914, mawu a pa Chivumbulutso 11:15 akhaladi oona: “Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova Mulungu], ndi wa Kristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthaŵi za nthaŵi.” The New International Dictionary of New Testament Theology (Voliyumu 2, tsamba 514) imati: “Pamene Kristu agonjetsa mphamvu zonse (1 Akor. 15:25), iye mwiniyo adzagonjera kwa Mulungu Atate. Chotero umbuye wa Yesu udzakhala utafika pachonulirapo chake ndipo Mulungu adzakhala zonse mu zonse (1 Akor. 15:28).” Pamapeto a Ulamuliro wake Wazaka Chikwi, Kristu Yesu adzabwezera kwa Atate wake, Mulungu Wamphamvuyonse, mphamvu ndi ulamuliro zimene anapatsidwa poyambapo. Chifukwa chake, ulemerero wonse ndi kulambira kudzaperekedwa moyenerera kwa Yehova, “Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Kristu.”—Aefeso 1:17.
Ngakhale kuti Yesu tsopano ndi Mbuye wa ambuye, iye samatchedwa konse Mulungu wa milungu. Yehova yekha ndiye wapamwamba pa onse. Mwanjira imeneyi, Yehova adzakhala “zonse mu zonse.” (1 Akorinto 15:28) Umbuye wa Yesu umampatsa malo ake oyenera monga Mutu wa mpingo Wachikrsitu. Ngakhale kuti tingaone “ambuye” amphamvu ambiri okhala m’malo apamwamba m’dziko lino, timakhala ndi chidaliro mwa uyo amene ali Mbuye wa ambuye. Komabe, Yesu Kristu, m’malo ake apamwambawo ndi okwezeka, n’ngwogonjerabe kwa Atate wake, “kuti Mulungu alamulire zonse.” (1 Akorinto 15:28, The Translator’s New Testament) Ndi chitsanzo chabwino kwambiri chotani nanga cha kudzichepetsa chimene Yesu anawaikira ophunzira ake kuti atsatire, ngakhale pamene amamvomereza kukhala Mbuye wawo!
[Bokosi patsamba 30]
“Pamene olemba Chipangano Chatsopano amanena za Mulungu iwo amatanthauza Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu. Pamene anena za Yesu Kristu, samanena za iye, kapena kuganiza za iye monga Mulungu. Iye ndiye Kristu wa Mulungu, Mwana wa Mulungu, Nzeru ya Mulungu, Mawu a Mulungu. Ngakhale Mawu Oyamba a St. John, amene amatsala pang’ono kufanana ndi Chiphunzitso cha ku Nicaea, ayenera kuŵerengedwa mogwirizana ndi mkhalidwe wogonjera wosonyezedwa bwino lomwe mu Uthenga Wabwino wonsewo; ndipo Mawu Oyambawo amamveka pang’ono m’Chigiriki chokhala ndi [the·osʹ] wa phatikizo koposa mmene alili m’Chingelezi.” —“The Divinity of Jesus Christ,” lolembedwa ndi John Martin Creed.