Deuteronomo
10 “Pa nthawi imeneyo Yehova anandiuza kuti, ‘Useme miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija+ komanso upange likasa lamatabwa. Ukatero ukwere mʼphiri muno kwa ine. 2 Pamiyalayo ndidzalembapo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija, imene unaiswa, ndipo udzaiike mʼlikasalo.’ 3 Choncho ndinapanga likasa la mtengo wa mthethe nʼkusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija. Kenako ndinakwera mʼphiri, miyala iwiriyo ili mʼmanja mwanga.+ 4 Ndiyeno analemba pamiyalayo mawu amene analemba poyamba aja,+ Malamulo Khumi,*+ amene Yehova anakuuzani paphiri kuchokera mʼmoto,+ pa tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Atatero, Yehova anandipatsa miyalayo. 5 Kenako ndinatembenuka nʼkutsika mʼphirimo+ ndipo ndinaika miyala iwiriyo mʼlikasa limene ndinapanga. Mpaka pano miyalayo idakali momwemo, mogwirizana ndi zimene Yehova anandilamula.
6 Zitatero Aisiraeli anachoka ku Beeroti Bene-yaakana kupita ku Mosera. Kumeneku nʼkumene Aroni anafera ndipo anamuikanso komweko.+ Mwana wake Eleazara anayamba kutumikira monga wansembe mʼmalo mwa Aroniyo.+ 7 Ndiyeno ananyamuka pamalo amenewo kupita ku Gudigoda. Anachokanso ku Gudigoda kupita ku Yotibata,+ dziko lokhala ndi mitsinje ya madzi.*
8 Pa nthawi imeneyo, Yehova anapatula fuko la Levi+ kuti lizinyamula likasa la pangano la Yehova,+ liziima pamaso pa Yehova nʼkumamutumikira komanso kuti lizidalitsa anthu mʼdzina lake+ ngati mmene akuchitira mpaka lero. 9 Nʼchifukwa chake fuko la Levi silinapatsidwe gawo kapena cholowa ngati abale awo. Cholowa chawo ndi Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anawauza.+ 10 Ine ndinakhala mʼphirimo kwa masiku 40, masana ndi usiku,+ ngati mmene ndinachitira poyamba paja. Pa nthawi imeneyinso Yehova anandimvetsera.+ Yehova sankafuna kukuwonongani. 11 Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Tsogolera anthuwa ndipo mukonzekere ulendo, kuti akalowe nʼkutenga dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndidzawapatsa.’+
12 Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani?+ Akufuna kuti muzichita izi: muziopa Yehova Mulungu wanu,+ muziyenda mʼnjira zake zonse,+ muzikonda ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse,+ 13 ndiponso kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, kuti zinthu zikuyendereni bwino.+ 14 Taonani, kumwamba ndi kwa Yehova Mulungu wanu, ngakhale kumwamba kwa kumwambako* komanso dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo zonsezo ndi zake.+ 15 Koma Yehova anayandikira kwa makolo anu okha nʼkuwasonyeza chikondi chake, ndipo wasankha inuyo mbadwa zawo+ pakati pa anthu onse, ngati mmene mulili lero. 16 Tsopano muyeretse* mitima yanu+ ndipo musakhalenso ankhutukumve.*+ 17 Chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye. Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera munthu aliyense+ ndipo salandira chiphuphu. 18 Iye amachitira chilungamo ana amasiye ndi akazi amasiye,+ ndipo amakonda mlendo+ moti amamupatsa chakudya ndi zovala. 19 Inunso muzikonda mlendo, chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+
20 Yehova Mulungu wanu muzimuopa, muzimutumikira,+ muzikhala naye pafupi kwambiri komanso muzilumbira pa dzina lake. 21 Iye ndi amene muyenera kumutamanda.+ Iyeyo ndi Mulungu wanu amene wakuchitirani zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha zonsezi, zimene mwaziona ndi maso anu.+ 22 Makolo anu anapita ku Iguputo ndi anthu 70,+ koma pano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.”+